Tikhaletu iwo Achikhulupiriro
“Ndife . . . a iwo a chikhulupiriro cha kuchipulumutso cha moyo.”—AHEBRI 10:39.
1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikhulupiriro cha mtumiki aliyense wokhulupirika wa Yehova n’chamtengo wapatali?
NTHAŴI ina mukadzakhalanso m’Nyumba ya Ufumu yodzaza ndi olambira Yehova, mukayang’ane kaye anthu onse okuzungulirani. Mukalingalire za njira zambiri zimene anthuwo amasonyezera chikhulupiriro. Mutha kudzaona achikulire amene atumikira Mulungu zaka zambirimbiri, achinyamata amene masiku onse amalimbana ndi chisonkhezero cha mabwenzi awo, ndi makolo amene akulimbikira kuphunzitsa ana awo kuopa Mulungu. Palinso akulu ndi atumiki otumikira, okhala ndi maudindo ambiri. Inde, mungadzaone abale ndi alongo auzimu a misinkhu yonse amene amagonjetsa zopinga zamitundumitundu kuti atumikire Yehova. Chikhulupiriro cha aliyense wa iwo n’chamtengo wapatali zedi!—1 Petro 1:7.
2. N’chifukwa chiyani uphungu wa Paulo m’machaputala 10 ndi 11 a Ahebri uli wopindulitsa kwa ife lerolino?
2 Ndi anthu opanda ungwiro ochepa okha, ngati alipo n’komwe, amene amaposa mtumwi Paulo pa kuzindikira kwawo kufunika kwa chikhulupiriro. Pauloyo ananenanso kuti chikhulupiriro chenicheni chimatsogolera ku “chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Koma Paulo anadziŵanso kuti chikhulupiriro chingawonongedwe ndi kufafanizidwa m’dziko lino lopanda chikhulupiriro. Anali kuwadera nkhaŵa kwambiri Akristu achihebri a ku Yerusalemu ndi ku Yudeya, amene anali kuyesetsa kuti asataye chikhulupiriro chawo. Pamene tipenda mbali zina za machaputala 10 ndi 11 a Ahebri, tiyeni tione njira zimene Paulo anagwiritsa ntchito pomangirira chikhulupiriro chawo. Pamene tikutero, tidzaona mmene tingamangire chikhulupiriro cholimba mwa ife eni ndiponso mwa anzathu.
Sonyezani Kuti Mumakhulupirirana
3. Kodi mawu a Paulo opezeka pa Ahebri 10:39 akusonyeza motani kuti iye anali ndi chikhulupiriro mwa abale ndi alongo ake a m’chikhulupiriro?
3 Chinthu choyamba chimene tingaone ndicho maganizo abwino a Paulo kwa anthu omwe ankawalembera kalatayo. Iye analemba kuti: “Koma ife si ndife a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko; koma a iwo achikhulupiriro cha kuchipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Paulo anali kuganiza zabwino, osati zoipa, ponena za Akristu anzake okhulupirikawo. Taonaninso kuti anagwiritsa ntchito mawu akuti “ife.” Paulo anali munthu wolungama. Komabe, sanayankhule modzitukumula kwa anthu omwe ankawalembera kalatayo, ngati kuti iyeyo ndiye anali wolungama kwambiri kuposa iwo. (Yerekezani ndi Mlaliki 7:16.) M’malo mwake, anadziphatika pagulu lawo. Anasonyeza chikhulupiriro chochokera pansi pa mtima chakuti iyeyo ndi Akristu okhulupirika omwe anaŵerenga kalata yake onse adzakumana ndi zopinga zothetsa nzeru zomwe zinali pafupi, kuti molimba mtima iwo adzakana kubwerera kuloŵa kuchitayiko, ndi kuti adzasonyeza kuti ali achikhulupiriro.
4. Kodi Paulo anali ndi chikhulupiriro mwa okhulupirira anzake pazifukwa ziti?
4 Chifukwa chiyani Paulo anali ndi chikhulupiriro chimenechi? Kodi sanali kuona zolakwa za Akristu achihebri? Iyayi. Anawapatsa uphungu wolunjika kuti awathandize kuthetsa zofooka zawo zauzimu. (Ahebri 3:12; 5:12-14; 6:4-6; 10:26, 27; 12:5) Komabe, Paulo anali ndi zifukwa zomveka ziŵiri zokhalira ndi chikhulupiriro mwa abale ake. (1) Monga wotsanzira Yehova, Paulo ankafuna kuona anthu a Mulungu monga momwe Yehova amawaonera. Sanali kungoona zolakwa zawo zokha koma mikhalidwe yawo yabwino ndi chiyembekezo chakuti iwo atha kusankha kuchita zabwino m’tsogolo. (Salmo 130:3; Aefeso 5:1) (2) Paulo anali kukhulupirira kwambiri mphamvu ya mzimu woyera. Anadziŵa kuti palibe zopinga, palibe zofooka zaumunthu, zimene zingaletse Yehova kuti asapereke “ukulu woposa wamphamvu” kwa Mkristu wina aliyense amene akufuna kutumikira Iye mokhulupirika. (2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13) Chotero chikhulupiriro cha Paulo mwa abale ndi alongo ake sichinali chophonyeka, chopanda pake, kapena chosaona zenizeni. Chinali chokhazikikadi ndiponso cha m’Malemba.
5. Kodi chikhulupiriro cha Paulo tingachitsanzire motani, ndipo pangatsatire chiyani?
5 Ndithudi, chikhulupiriro chimene Paulo anasonyeza chinasonkhezeranso ena. Pamene Paulo anayankhula molimbikitsa chotero ndi mipingo ku Yerusalemu ndi Yudeya, anthu a m’mipingomo ayenera kuti anakhudzidwa mtima kwambiri. Poyang’anizana ndi chitonzo choŵaŵa ndi kusoŵa chidwi kwa Ayuda odzitukumula omwe ankawatsutsa, mawu amenewo anathandiza Akristu achihebri kukhala otsimikizira m’mtima mwawo kuti akhale achikhulupiriro. Kodi lerolino tingachitenso chimodzimodzi kwa wina ndi mnzake? M’posavuta kungoona zolakwa zokhazokha ndi mikhalidwe yosasangalatsa mwa ena. (Mateyu 7:1-5) Komabe, tingathandizane kwambiri ngati tiyang’ana chikhulupiriro chapadera chimene aliyense ali nacho ndi kuchiyamikira kwambiri. Chikhulupirirotu chimakula ndi chilimbikitso choterechi.—Aroma 1:11, 12.
Kugwiritsa Ntchito Bwino Mawu a Mulungu
6. Kodi Paulo anali kutchula mawu ochokera kuti pamene analemba mawu opezeka pa Ahebri 10:38?
6 Paulo anamangiriranso chikhulupiriro mwa okhulupirira anzake pogwiritsa ntchito Malemba mwaluso. Mwachitsanzo, analemba kuti: “Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m’chikhulupiriro: ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.” (Ahebri 10:38) Paulo panopo anali kutchula mawu a m’buku la mneneri Habakuku.a Mawu ameneŵa ayenera kuti anali odziŵika kwa oŵerenga kalata ya Paulo, Akristu achihebri amene anali kuwadziŵa bwino kwambiri mabuku amaulosi. Poona cholinga chake, chomwe chinali kulimbitsa chikhulupiriro cha Akristu a m’Yerusalemu ndi m’madera oyandikana ndi mzindawo cha m’chaka cha 61 C.E., chitsanzo cha Habakuku chinali choyenerera zedi. Chifukwa chiyani?
7. Kodi Habakuku anaulemba liti ulosi wake, ndipo zinthu zinali motani m’dziko la Yuda panthaŵiyo?
7 Zikusonyeza kuti Habakuku analemba buku lake patangotsala zaka 20, kapena kuposapo pang’ono, kuti Yerusalemu awonongedwe mu 607 B.C.E. M’masomphenya, mneneriyo anaona Akasidi (kapena kuti, Ababulo), ‘mtundu woŵaŵa ndi waliŵiro,’ akukantha Yuda ndi kuwononga Yerusalemu, kumeza anthu ndi mitundu. (Habakuku 1:5-11) Koma tsoka limenelo linali litaloseredwa kuyambira m’tsiku la Yesaya, zaka zoposa zana limodzi m’mbuyo mwake. M’nthaŵi ya Habakuku, Yehoyakimu analoŵa m’malo Mfumu Yosiya yabwinoyo, ndipo kuipa kunachulukanso m’dziko la Yuda. Yehoyakimu anazunza ngakhalenso kupha anthu amene anali kuyankhula m’dzina la Yehova. (2 Mbiri 36:5; Yeremiya 22:17; 26:20-24) Ndiye chifukwa chaketu mneneri wachisoniyo Habakuku anafuula kuti: “Yehova, . . . mpaka liti?”—Habakuku 1:2.
8. N’chifukwa chiyani chitsanzo cha Habakuku chinathandiza Akristu m’zaka zana loyamba ndiponso lerolino?
8 Habakuku sanali kudziŵa kuti chiwonongeko cha Yerusalemu chinali pafupi motani. Mofananamo, Akristu a m’zaka zana loyamba sanali kudziŵa kuti dongosolo lazinthu lachiyuda lidzatha liti. Ifenso lerolino sitikudziŵa “tsiku ilo ndi nthaŵi yake” pamene chiweruzo cha Yehova chidzadza padongosolo loipa lino la zinthu. (Mateyu 24:36) Chotero tiyeni tione yankho la mbali ziŵiri la Yehova kwa Habakuku. Choyamba, iye anatsimikizira mneneriyo kuti mapeto adzadza panthaŵi yake. ‘Sadzazengereza,’ anatero Mulungu, ngakhale kuti kwa munthu, angaoneke ngati kuti akuchedwa. (Habakuku 2:3) Chachiŵiri, Yehova anakumbutsa Habakuku kuti: “Wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.” (Habakuku 2:4) Chimenechi ndi choonadi chosangalatsa ndiponso chosavuta kumva! Chofunika kwambiri si nthaŵi pamene mapetowo adzadza ayi, koma ngati tingapitirizebe kukhala moyo wachikhulupiriro.
9. Kodi atumiki omvera a Yehova anakhalabe motani ndi moyo mwa chikhulupiriro chawo (a) mu 607 B.C.E.? (b) pambuyo pa 66 C.E.? (c) N’chifukwa chiyani kulimbitsa chikhulupiriro chathu kuli kofunika zedi?
9 Yerusalemu atasakazidwa mu 607 B.C.E., Yeremiya, mlembi wake Baruki, Ebedi-Meleki, ndi Arekabu okhulupirikawo anaona choonadi cha lonjezo la Yehova kwa Habakuku. ‘Anakhalabe ndi moyo’ mwa kupulumuka chiwonongeko chowopsacho cha Yerusalemu. Chifukwa chiyani? Yehova anafupa kukhulupirika kwawo. (Yeremiya 35:1-19; 39:15-18; 43:4-7; 45:1-5) Mofananamo, Akristu achihebri a m’zaka zana loyamba ayenera kuti analabadira uphungu wa Paulo, popeza kuti pamene magulu ankhondo a Roma anazinga Yerusalemu mu 66 C.E. kenako n’kubwerera pachifukwa chosadziŵika bwino, Akristuwo anamvera mokhulupirika chenjezo la Yesu lakuti ayenera kuthaŵa. (Luka 21:20, 21) Anakhalabe ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Momwemonso, ifeyo tidzakhalabe ndi moyo ngati tikhalabe okhulupirika pamene mapeto afika. N’chifukwa chofunikatu zedi cholimbitsira chikhulupiriro chathu tsopano!
Kulongosola Bwino Lomwe Zitsanzo za Chikhulupiriro
10. Kodi Paulo anachilongosola motani chikhulupiriro cha Mose, ndipo kodi tingam’tsanzire motani Mose pambaliyi?
10 Paulo anamangiriranso chikhulupiriro mwa kugwiritsa ntchito zitsanzo. Poŵerenga Ahebri chaputala 11, onani mmene akulongosolera bwino lomwe zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, iye ananena kuti Mose ‘anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.’ (Ahebri 11:27) M’mawu ena, Yehova anali weniweni kwa Mose moti zinali ngati kuti akuona ndi maso Mulungu wosaonekayo. Kodi ena anganenenso chimodzimodzi za ife? M’posavuta kungoyankhula za unansi ndi Yehova, koma kumangirira ndi kulimbitsa unansiwo ndi ntchito ndithu. Imeneyo ndiyo ntchito imene tiyenera kuchita! Kodi timaona Yehova kukhala weniweni moti timaganiza za iye posankha zopanga, ngakhale zioneke ngati zazing’ono? Chikhulupiriro choterocho chidzatithandiza kupirira ngakhale chitsutso choŵaŵa.
11, 12. (a) Kodi chikhulupiriro cha Enoke chiyenera kuti chinayesedwa m’mikhalidwe yotani? (b) Kodi Enoke analandira mfupo yotani yolimbikitsa?
11 Lingaliraninso chikhulupiriro cha Enoke. N’kovuta kwa ife kuyerekeza chitsutso chimene anakumana nacho. Enoke anayenera kulengeza uthenga wopyoza mtima wachiweruzo pa anthu oipa omwe analiko m’nthaŵiyo. (Yuda 14, 15) Mwachionekere chizunzo chimene mwamuna wokhulupirikayu akanakumana nacho chinali choopsa kwambiri, chankhanza zedi, moti Yehova ‘anam’tenga,’ kum’samutsira kutulo ta imfa adani ake asanamuukire. Chotero Enoke kunalibe pamene ulosi umene ananena unakwaniritsidwa. Komabe, analandira mphatso imene, m’lingaliro lina, inali yabwino koposa.—Ahebri 11:5; Genesis 5:22-24.
12 Paulo anafotokoza kuti: “Asanam’tenge, [Enoke] anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu.” (Ahebri 11:5) Kodi mawuŵa anatanthauzanji? Asanagone tulo ta imfa, mwina Enoke anaona masomphenya ena ake, mwina anaona Paradaiso wapadziko lapansi mmene adzaukitsidwira tsiku lina posachedwapa. Mulimonse mmene zinalili, Yehova anadziŵitsa Enoke kuti Iye anakondwera ndi moyo wake wachikhulupiriro. Enoke anakondweretsa mtima wa Yehova. (Yerekezani ndi Miyambo 27:11.) Kuganiza za moyo wa Enoke n’kosangalatsa, kodi sitero? Kodi mungakonde kukhala ndi moyo wachikhulupiriro woterowo? Ndiyetu sinkhasinkhani pazitsanzo zimenezi; onani anthuwo monga kuti ali pambali panu. Khalani wotsimikizira mumtima kuti mudzasonyeza chikhulupiriro, tsiku ndi tsiku. Kumbukiraninso kuti iwo okhala ndi chikhulupiriro satumikira Yehova chifukwa chodziŵa tsiku kapena nthaŵi pamene Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake onse. M’malo mwake, tinasankha kutumikira Yehova kosatha! Kuchita zimenezi ndiko njira yabwino koposa ya moyo m’dongosolo la zinthu linolo komanso likudzalo.
Mmene Tingakhalire ndi Chikhulupiriro Cholimba
13, 14. (a) Kodi mawu a Paulo olembedwa pa Ahebri 10:24, 25 angatithandize motani kupanga misonkhano yathu kukhala chochitika chosangalatsa? (b) Kodi cholinga chachikulu cha misonkhano yachikristu n’chiyani?
13 Paulo anasonyeza Akristu achihebri njira zingapo mmene akanalimbitsira chikhulupiriro chawo. Tiyeni tikambirane ziŵiri zokha. Mwachionekere tikudziŵa chilimbikitso chake cha pa Ahebri 10:24, 25, chotilimbikitsa kusonkhana nthaŵi zonse pamisonkhano yathu yachikristu. Komano, kumbukirani kuti mawu ouziridwawo a Paulo sakunena kuti tiyenera kukhala pamisonkhano imeneyo n’kumangopenyerera. M’malo mwake, Paulo analongosola kuti misonkhanoyo ili mpata woti tidziŵane, tisonkhezerane kutumikira Mulungu mowonjezereka, ndi kuti tilimbikitsane. Timapezeka pamisonkhanoyo kuti tipatse, osati kungolandira. Zimenezo zimapangitsa misonkhano yathu kukhala zochitika zosangalatsa kwambiri.—Machitidwe 20:35.
14 Komabe, chachikulu kwambiri n’chakuti timafika pamisonkhano yachikristu kuti tilambire Yehova Mulungu. Timachita zimenezo mwa kugwirizana m’pemphero ndi kuimba nawo nyimbo, kumvetsera mosamala kwambiri, ndiponso mwa kupereka “chipatso cha milomo,” chimene chili mawu otamanda Yehova m’ndemanga zathu ndi m’nkhani zathu za pamisonkhanoyo. (Ahebri 13:15) Ngati tikhala ndi zolinga zimenezi m’maganizo mwathu ndi kuzichita pamsonkhano uliwonse, chikhulupiriro chathu chidzamangiriridwa nthaŵi zonse.
15. N’chifukwa chiyani Paulo anauza Akristu achihebri kuti agwiritse utumiki wawo, nanga n’chifukwa chiyani uphungu umodzimodziwo uli wofunikanso lerolino?
15 Njiranso ina yomangirira chikhulupiriro ndiyo mwa ntchito yolalikira. Paulo analemba kuti: “Tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika.” (Ahebri 10:23) Mumauza munthu kuti agwiritse chinachake chimene akuoneka kuti ali pafupi kuchileka. Ndithudi Satana anali kuvutitsa Akristu achihebri amenewo kuti asiye utumiki wawo, ndipo akuvutitsanso anthu a Mulungu lerolino. Poyang’anizana ndi mavuto ngati amenewo, kodi tiyenera kuchitanji? Talingalirani zimene Paulo anachita.
16, 17. (a) Kodi Paulo anakhala motani wolimba mtima muutumiki? (b) Kodi tiyenera kutani tikapeza kuti mbali inayake ya utumiki wathu wachikristu imatichititsa mantha?
16 Kwa Akristu a ku Tesalonika, Paulo analemba kuti: “Tingakhale tidamva zoŵaŵa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziŵa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa [“tinalimba mtima,” NW] mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.” (1 Atesalonika 2:2) Kodi Paulo ndi anzake ‘anachitiridwa chipongwe’ motani ku Filipi? Malinga n’kunena kwa akatswiri ena, mawu achigiriki amene Paulo anagwiritsa ntchito amatanthauza kutukwanidwa, kuselewulidwa, kapena kunyozedwa. Akuluakulu a ku Filipi anawakwapula ndi ndodo, kuwaponya m’ndende, ndi kuwamanga m’zigologolo. (Machitidwe 16:16-24) Kodi chokumana nacho choŵaŵa chimenecho chinam’khudza motani Paulo? Kodi anthu a mumzinda wotsatira, Tesalonika, omwe anawachezera paulendo wake waumishonalewo anaona kuti Paulo akuchita mantha? Iyayi, iye “analimba mtima.” Anagonjetsa mantha napitirizabe kulalikira molimba mtima.
17 Kodi kulimba mtima kwa Paulo kunachokera kuti? Mumtima mwake? Iyayi, ananena kuti analimba mtima “mwa Mulungu wathu.” Buku lina lothandiza otembenuza Baibulo linafotokoza kuti mawu ameneŵa angatembenuzidwenso kuti, “Mulungu anachotsa mantha m’mitima yathu.” Chotero ngati mumachita mantha muutumiki wanu, kapena ngati pali mbali ina yautumiki imene imakuchititsani mantha, bwanji osam’pempha Yehova kuti achitenso chimodzimodzi kwa inu? M’pempheni kuti achotse mantha mumtima mwanu. M’pempheni kuti akuthandizeni kulimba mtima kuti muchite ntchitoyo. Ndiponso, chitaninso zinthu zina zothandiza. Mwachitsanzo, linganizani kuti mukachite ntchitoyo ndi winawake waluso pamtundu wa umboni umene umakuchititsani manthawo. Mwina ndi ulaliki wa m’malo amalonda, umboni wa mu msewu, ulaliki wamwamwayi, kapena umboni wapatelefoni. Mwina mnzanuyo angalole kusonyeza chitsanzo kaye. Ngati zili motero, onani mmene akuchitira ndipo phunzirani. Komano kenako, limbani mtima kuti muyese kuchita zomwezo.
18. Kodi tingalandire madalitso otani ngati tilimba mtima muutumiki wathu?
18 Ngati mulimba mtima, lingalirani zimene zingatsatire. Mutalimbikira ndi kusalefuka, mungakhale ndi zokumana nazo zabwino pogaŵana choonadi ndi ena, zokumana nazo zimene mwina simukanakhala nazo. (Onani patsamba 25.) Mudzakhutira podziŵa kuti mwakondweretsa Yehova mwa kuchita chinthu chovuta kwa inu. Mudzalandira dalitso ndi thandizo lake pogonjetsa mantha anu. Chikhulupiriro chanu chidzalimba. Ndithudi, simungamangirire chikhulupiriro cha ena popanda kumangiriranso chanu panthaŵi imodzimodziyo.—Yuda 20, 21.
19. Kodi “iwo achikhulupiriro” adzalandira mfupo yotani yamtengo wapatali?
19 Pitirizanibe kulimbitsa chikhulupiriro chanu ndi chikhulupiriro cha anzanu. Mungachite zimenezi mwa kumangirira chikhulupiriro chanu ndi cha ena pogwiritsa ntchito mwaluso Mawu a Mulungu, kuphunzira zitsanzo za m’Baibulo za chikhulupiriro ndi kuziona ngati zikungochitika kumene, kukonzekera ndi kutengamo mbali m’misonkhano yachikristu, ndiponso mwa kugwiritsa mwayi wamtengo wapatali wa utumiki wapoyera. Pamene mukuchita zinthu zimenezi, dziŵani kuti ndinudi mmodzi wa “iwo achikhulupiriro.” Kumbukiraninso kuti anthu a m’gulu limeneli ali ndi mfupo yamtengo wapatali. Amenewo ndiwo “iwo achikhulupiriro cha kuchipulumutso cha moyo.”b Chikhulupiriro chanu chipitirizebe kukula, ndipo Yehova Mulungu akusungeni amoyo kosatha!
[Mawu a M’munsi]
a Paulo anatchula mawu a pa Habakuku 2:4 monga momwe alili mu Septuagint, imene ili ndi mawu akuti “ngati wina abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.” Mawu ameneŵa sakupezeka m’mipukutu yachihebri imene ilipo tsopano. Ena anena kuti Septuagint inazikidwa pa mipukutu yachihebri yakale kwambiri imene kulibenso lerolino. Mulimonse mmene zinalili, Paulo anawaphatikiza pano mawuwo mosonkhezeredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Chotero mawuwo ndi ouziridwa ndi Mulungu.
b Lemba la chaka la Mboni za Yehova m’chaka cha 2000 lidzakhala lakuti: “Ife si ndife a iwo akubwerera . . . koma a iwo a chikhulupiriro.”—Ahebri 10:39.
Kodi Mungayankhe Kuti Bwanji?
◻ Kodi Paulo anasonyeza motani chidaliro mwa Akristu achihebri, ndipo tingaphunzireponji pamenepa?
◻ N’chifukwa chiyani kunali koyenerera kuti Paulo atchule mawu a mneneri Habakuku?
◻ Kodi ndi zitsanzo za chikhulupiriro zotani za m’Malemba zimene Paulo anazilongosola bwino kwambiri?
◻ Kodi Paulo anayamikira njira yothandiza iti yomangira chikhulupiriro?
[Chithunzi patsamba 23]
Atakumana ndi mavuto aakulu ku Filipi, Paulo analimba mtima kuti apitirize kulalikira
[Zithunzi patsamba 24]
Kodi mungalimbe mtima kuti muyese njira zosiyanasiyana za ulaliki?