-
ChipembedzoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Aheb. 10:24, 25: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muwona tsiku lirikuyandika.” (Kuti lamulo Lamalemba limeneli likwaniritsidwe, payenera kukhala misonkhano Yachikristu imene tingafikepo pamlingo wanthaŵi zonse. Kakonzedwe kotero kamatilimbikitsa kusonyeza chikondi kwa ena, osati kokha kudera nkhaŵa ndi ife eni.)
-
-
ChipembedzoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Kodi ife tingakhale ndi unansi wabwino ndi Mulungu ngati tinaŵerengera malamulo ake kukhala osanunkha kanthu? Limodzi la ameneŵa nlakuti tiyenera kusonkhana nthaŵi zonse ndi okhulupirira anzathu.—Ahebri 10:24, 25.
-
-
ChipembedzoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Ndithudi, ngati munthu aŵerenga Baibulo koma sakuligwiritsira ntchito m’moyo wake, kumampindulitsa mochepekera. Ngati iye amalikhulupirira nachita mogwirizana nalo, iye adzagwirizana ndi atumiki a Mulungu m’misonkhano yanthaŵi yonse yampingo. (Aheb. 10:24, 25) Iye adzakhalanso ndi phande mkugaŵana “mbiri yabwino” ndi anthu ena.—1 Akor. 9:16; Marko 13:10; Mat. 28:19, 20.
-