Kodi Mudzapindula ndi Chisomo?
“PAMENE ndinaphunzira mowonjezereka miyezo ya Mulungu m’Baibulo, ndipamenenso ndinadziwona kukhala woyenerera chiyanjo chake ndi dalitso mocheperapo,” adatero Frank. Chikondwerero chake m’Baibulo chinadzutsidwa pamene adaali m’ndende chifukwa cha milandu yokhudza mankhwala ogodomalitsa. Anaŵerenga kope la bukhu la Choonadi Chimene Chimatsogolera ku Moyo Wamuyaya,a nakhala wotsimikizira kuti zimene linanena zinali chowonadi, ndipo, atamasulidwa m’ndende, anawonana ndi Mboni za Yehova kuti aphunzire zambiri ponena za Baibulo.
Kodi nchifukwa ninji kuphunzira Baibulo kunampangitsa kudziwona ali wopanda pake? Chifukwa chakuti njira yake ya moyo yapapitapo anali kuswa ambiri a malamulo amakhalidwe abwino a Mulungu. Kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, kuledzera, ndi zizoloŵezi zina zosiyanasiyana zoluluza zinamchititsa tondovi kwambiri kotero kuti panthaŵi ina wapolisi anamuuza kuti: “Kodi ungandiuze chonde keyala ya malo amene umakhala? Ndingofuna kudziŵa kumene tingatumize mtembo wako!”
Komabe, chimene kwenikweni pambuyo pake chinampangitsa kudziwona kukhala wopanda pake, chinali chakuti mosasamala kanthu za kuyesayesa kokulira kumene iye anachita, anakupeza kukhala kovuta kwambiri kulaka zizoloŵezi zonyansa zokhathamira zimenezi. Mwachitsanzo, kunonomela uchidakwa woluluzawo, kunatsala nenene kumlaka. “Ndinali nditalephera momvetsa chisoni mobwerezabwereza ndipo ndinali watondovi kwambiri,” iye anatero. “Panatsala nenene kuti ndileke, ndikumalingalira kuti ndinalidi wopanda pake.”
Ena angakhale analibe chiyambi chofanana ndi cha Frank. Komabe, iwo angakhale ndi malingaliro, onkitsa a kudziwona kukhala opereŵera. Ichi chingakhale chifukwa chakuti amadziikira miyezo yapamwamba mopambanitsa pamene akuyesayesa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi zimene iwo amaganizira kuti Mulungu amafuna. Pamene alephera, amadziwona kukhala aliwongo. “Liwongo lingakhale atulo oipa,” analongosola motero Dr. Claire Weekes m’bukhu lake lakuti Self-Help for Your Nerves, “makamaka kwa awo oyesa kudziikira miyezo yapamwamba.” Kodi nchiyani chimene Mkristu angachite atayambukiridwa ndi malingaliro motero a kukhala wopanda pake?
Yamikirani Chisomo
“Chinthu chimodzi chimene chinandithandiza kwambiri,” adatero Frank, “chidali kuzindikira zimene Baibulo limanena pa Ahebri 4:15, 16.” Pamenepo mtumwi Paulo akutikumbutsa kuti Yesu ndimthandizi wosamalira yemwe “amamva chifundo ndi zofooka zathu” ndi amene wakupanga kukhala kothekera kwa ife “kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza m’nthaŵi ya kusowa.”
Kodi mungafune mfungulo ya kulakira malingaliro a kupanda pake? Ndiiyi: Kumbukirani kuti Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu amadziŵa kuti ndife ofooka chifukwa cha kupanda ungwiro kobadwa nako. Iwo amazindikira kuti sitingayenerane ndendende ndi miyezo yolungama. (Salmo 51:5; Aroma 3:23; 5:12, 18; Yakobo 3:2) Chotero iwo samayembekezera zochuluka kwa ife koposa zimene tingachite. Iwo amayang’ana pa mikhalidwe yathu yabwino, osati pazofoka zathu. Wamasalmoyo anafunsa kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Inu mungazindikiredi kuti palibe aliyense wa ife akatero. Komabe, kupyolera m’dipo la nsembe ya Yesu Kristu, Yehova mwachifundo angatipatse kaimidwe koyera mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwathu. (1 Yohane 2:2; 4:9, 10) Tingapeze “kukhululukidwa kwa machimo athu”—ndipo chotero kuthandizidwa kulaka malingaliro aliwonse a kupanda pake—“monga mwa kulemera kwa chisomo chake.”—Aefeso 1:7.
Nkhaniyo njotere. Anthu amene amakonda kujambula zithunzi adzachita zothekera kukonzanso zithunzi zowonongedwa kapena zithunzi zina zojambulidwa mwaluso. Mwachitsanzo, pamene munthu wina wonyamula mfuti yachifefe anawononga chithunzithunzi choseketsa chotchedwa Leonardo da Vinci chamtengo wokwanira £20 miliyoni (chifupifupi $32 miliyoni, U.S.) mu National Gallery ku London, ku Mangalande, palibe aliyense anapereka lingaliro lakuti popeza kuti tsopano chithunzithunzi chojambulidwacho chinawonongedwa, chinayenera kutaidwa. Ntchito yokonza chithunzi chazaka 487 chokongolacho inayamba mofulumira. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chinali chamtengo wapatali kwa okonda zithunzithunzi zojambula.
Kodi inu simuli wamtengo wake kuposa chithunzithunzi chojambulidwa ndi choko ndi tsimbe? Inu mulidi wotero kwa Yehova—mosasamala kanthu za kuvulazika kumene inu mungakhale nako ndi tchimo lobadwa nalo. (Salmo 72:12-14; Mateyu 20:28) Yehova Mulungu, Mlengi woyambirira waluso wa banja la anthu, adzachita zimene ziri zoyenerera kubwezeretsa ziŵalo za banja limenelo kuungwiro zimene ziri zofunitsitsa kulabadira chisamaliro chake chachikondi.—Yerekezerani ndi Machitidwe 3:21; Aroma 8:20-22.
Labadirani Chisomo
Tsatirani chitsanzo cha mtumwi Paulo. Iye adayamikira kwambiri kukoma mtima kwa Mulungu amene mwachifundo anamkhululukira machimo ake apapitapo limodzinso ndi kumchirikiza mosalekeza m’nkhondo yake yogonjetsa zofoka zobwerezedwabwerezedwa. (Aroma 7:15-25; 1 Akorinto 15:9, 10) Paulo anawongolera njira yake ya moyo ndiponso ‘adapumphuntha thupi lake ndi kuliyesa kapolo’ kuti akhalebe panjira yoyanjidwa ndi Yehova. (1 Akorinto 9:27) Iye sanalole thupi lake, lokhala ndi zikhoterero zake zolakwa zakuthupi ndi zamaganizo, kumtsogolera iye monga kapolo.
Landirani chisomo cha Mulungu, ndipo chiloleni chikutsogolereni kukulapa. (Aroma 2:4; 2 Akorinto 6:1) Ngati zolakwa zakale zikali kukuvutitsani, ziwongolereni ndiyeno khulupirirani chitsimikiziro cha Yehova chakuti wakukhululukirani. (Yesaya 1:16-18; Machitidwe 2:38) Ngati zifooko zosalekeza zikukanthanibe, pitirizanibe kulimbana nazo. Pempherani mwaphamphu kaamba ka chithandizo cha Yehova kuzilaka pamene panthaŵi imodzimodziyo mukupindula ndi kukoma mtima kwake. (Salmo 55:22) Kuchokera pachokumana nacho cha iyemwini, Frank akulangiza kuti: “Pamene nthaŵi zina winawake alephera nkhondo yake yolimbana ndi chizoloŵezi choipa, iye sayenera kukuwona kukhala kulephera kotheratu, ndi kuti zathera pompo, koma mmalo mwake, kukhala chidodometso chakanthaŵi.” Ngati ena awonjezera mavuto anu mwa kufunsira zambiri kuchokera kwa inu koposa zimene mungachite, kumbukirani kuti ndiye Mulungu amene mukuyesayesa kukondweretsa, osati anthu.—Agalatiya 1:10.
M’nkhondo yanu ya kuchita chimene chiri chabwino, chenjerani ndi “machitachita amachenjera” a Satana, amene angatchedwe “zinyengo zauchiŵanda za Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11, New World Translation Reference Bible, mawu amtsinde; Today’s English Version) Lingalirani “zinyengo zauchiŵanda” ziŵiri zimene iye adzagwiritsira ntchito kuyesa kukulandani mapindu a chisomo.
“Zinyengo Zauchiŵanda” za Satana
Satana amagwiritsira ntchito malingaliro a kupanda pake kuyesa kukuchotsani kwa Mulungu. Satana ndiye magwero a tchimo limene lidakuvulazani poyambapo. Tsopano iye angakhale akuyesa kulimbikitsa lingaliro lakuti ndinu wopanda pake m’maso mwa Mulungu, monga momwe Bilidadi adayesera kuchita kwa Yobu. (Yobu 25:4-6; Yohane 8:44) Ndinkhondo zochuluka chotani nanga zomwe zagonjetsedwa chifukwa chakuti asilikali adaloŵa m’nkhondoyo atalefulidwa kale! Chotero, musalole Satana kukulefulani. (Aefeso 6:10-13) Kuchenjerera zolinganiza za Satana kuyenera kukusonkhezerani kumenyera nkhondo molimbika kwambiri kuchita zimene ziri zabwino.—2 Akorinto 2:11.
Ngati nthaŵi zina mumva chisoni ndi zolephera zosiyanasiyana, tsimikizirani kuti ‘simukumezedwa mwa kukhala wachisoni mopambanitsa.’ (2 Akorinto 2:7) Dr. Claire Weekes anathirira ndemanga pa chikhoterero cha ena cha kulola zolephera zapapitapo kuŵalaka: “Kulola liwongo lapapitapo kuwononga chochitika chatsopano kali kachitidwe kowononga.”—Wonani Machitidwe 3:19.
Ngati tingafikire ziyeneretso zonse za Mulungu mwachikwanekwane, iko kungakhale chisomo chotiyenerera kuti atipatse madalitso amene walonjeza. Koma Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu akutisonyeza ife chifundo chimene chiri “chachisomo.” A Greek-English Lexicon of the New Testament, lolembedwa ndi J. H. Thayer, likulongosola tanthauzo la liwu logwiritsiridwa ntchito ndi mtumwi Paulo kufotokoza mkhalidwe umenewu wa Mulungu kuti: “Liwulo [khaʹris] liri ndi lingaliro la kukoma mtima kumene kumabweretsa pa munthu chinthu chimene samachiyenerera.” Palibe ntchito yathu imene ingapeze dalitso la Mulungu. Kuli, monga mmene Paulo adanenera, chisomo. Ngati inu mowona mtima muchita zonse zimene mungathe m’kufoka kwanu kukwaniritsa mathayo anu kwa Mulungu, khalani achimwemwe pochita zimenezo. Yehova samafunsira zoposa zimenezo kwa inu.
Komabe, chenjerani ndi “zinyengo zauchiwanda” zina za Satana. Iye amasokeretsa ena kuganiza kuti angapindule ndi chisomo cha Mulungu, kuti angadyere masuku pamutu chifundo chake. Yehova mwachikondi amatikhululukira zofoka zathu, koma zimenezo sizimatanthauza kuti tileke kulimbana nazo kuti tizilake. Paulo akufotokoza ena amene “anapondereza mwana wa Mulungu, . . . nachitira chipongwe mzimu wa chisomo.” (Ahebri 10:29) Ameneŵa sanasonyeze ulemu kaamba ka malamulo amakhalidwe abwino olungama ndipo mwachipongwe anachitira mwano malamulo a Mulungu, akumadziika pamkhalidwe wosakhoza kukonzeka. Yuda mbale wa Yesu mwa bambo wina, amene anawona ngozi yochititsidwa ndi machenjera oterowo a Satana, analemba kuti: “Anthu ena anakwaŵira mtseri [mumpingo], . . . anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa.”—Yuda 4.
Satana angaputsitse oterowo kuganiza kuti kwakukulukulu iwo angaphatikizidwe m’kuchita zoipa dala kapena mochepera m’kuchita zoipa ndiyeno kupempha Mulungu kuŵakhululukira tchimo lawo. Komatu Yehova sadzakhululukira akuswa mwadala malamulo ake. Iye ‘Ndiwochuluka m’kukoma mtima’ kwa awo amene amayesayesa kumtumikira bwino kwambiri monga momwe angathere mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwawo. Iye “samamasula woparamula” pamene kutero kuli koyenerera.—Eksodo 34:6, 7.
Mungapindule ndi Chisomo
Kuli kotonthoza kudziŵa kuti Yehova samakuyang’anani kokha pamkhalidwe wanu wopanda ungwiro, mkhalidwe wopanda pake. Iye amadziŵa chimene inu mungakhale pamene mphamvu zochiritsa za dipo la nsembe ya Yesu zagwiritsiridwa ntchito mokwanira. Chotero, pempherani mwachidaliro kwa Yehova, monga mmene wamasalimo Davide anachitira. “Mundichitire ine chifundo, Mulungu,” adatero Davide, “monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga. Mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chiri pamaso panga chikhalire. Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse. . . . Inu Mulungu simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.”—Salmo 51:1-3, 9, 17.
Machimo anu ndi zophophonya zingakhale pamaso panu chikhalire. Nthaŵi zina mungalingalire mofanana ndi mwana woloŵerera wofotokozedwa ndi Yesu. Pamene mnyamata ameneyu anabwerera kunyumba pambuyo pa kuwawanya komvetsa chisoni choloŵa chake m’maiko achilendo, iye anadzuma kwa atate ŵake kuti: “Sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu”! (Luka 15:21) Komabe, mnyamata ameneyu adaali ndi kaimidwe kamaganizo kabwino. Iye sanakane kukoma mtima kwa atate ŵake kapena kuyesera kukudyera masuku pamutu. Chotero atate ŵake mwachikondi adamlandiranso m’banjamo. (Luka 15:20-24) Yehova ngwachimwemwe kuchitira zofananazo lerolino anthu ochimwa amene amayesayesa mwaphamphu kuchita chifuniro chake.—Salmo 103:8-14; Yesaya 55:7.
Frank sanalole malingaliro a kupanda pake kumlaka iye. Iye analabadira chisomo cha Mulungu, ndipo tsopano akutumikira monga mtumiki wotumikira mumpingo wa Mboni za Yehova. “Ndimadumpha ndi chisangalalo tsopano,” iye akutero, “pamene ndiganiza za zimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu atichitira ndipo adzatichitirabe!”
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.