Yehova Ndiye ‘Linga Lathu M’nyengo ya Nsautso’
“Chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yawo [“linga lawo,” NW] m’nyengo ya nsautso.”—SALMO 37:39.
1, 2. (a) Kodi Yesu anawapempherera chiyani ophunzira ake? (b) Kodi Mulungu ali n’cholinga chanji ndi anthu ake?
YEHOVA ndi wamphamvuyonse. Iye ali ndi mphamvu zoteteza anthu okhulupirika amene amamulambira ndipo angatero m’njira iliyonse yomwe angafune. Ndipotu angathe kuchotsa anthu ake padziko lapansi pano n’kukawaika kumalo ena otetezeka ndiponso amtendere. Koma ponena za ophunzira ake, Yesu anapemphera kwa Atate wake wakumwamba kuti: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.”—Yohane 17:15.
2 Yehova anasankha kuti asatichotse “m’dziko lapansi.” M’malo mwake, iye akufuna kuti tizikhala limodzi ndi anthu ena onse n’cholinga choti tiwalalikire ena uthenga wopatsa chiyembekezo ndi wolimbikitsa. (Aroma 10:13-15) Komabe monga momwe Yesu anasonyezera m’pemphero lake, pakuti tikukhala padziko lapansi lino, ndife osabisika kwa “woipayo.” Anthu akusautsika mtima kwambiri ndi anthu osamvera ndiponso mizimu yoipa, ndipo zimenezi zimachitikiranso Akristu.—1 Petro 5:9.
3. Kodi ndi zinthu zotani zimene zimachitikiranso ngakhale anthu okhulupirika olambira Yehova, koma kodi m’Mawu a Mulungu timapezamo mawu olimbikitsa ati?
3 Kutaya mtima mukakumana ndi mayesero ameneŵa sikodabwitsa. (Miyambo 24:10) M’Baibulo muli nkhani zambiri za anthu okhulupirika amene anakumana ndi masautso. Wamasalmo anati: “Masautso a wolungama mtima achuluka: Koma Yehova am’landitsa mwa onseŵa.” (Salmo 34:19) Inde, ngakhale munthu “wolungama” amakumananso ndi zoipa. Mofanana ndi wamasalmo Davide, nthaŵi zina tingafike mpaka ‘pofooka ndipo n’kuchinyizidwa.’ (Salmo 38:8) Koma n’zolimbikitsa kudziŵa kuti “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”—Salmo 34:18; 94:19.
4, 5. (a) Mogwirizana ndi Miyambo 18:10, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu atiteteze? (b) Kodi n’zinthu ziti zimene tingachite kuti Mulungu atithandize?
4 Mogwirizana ndi pemphero la Yesu, Yehova amatisungadi. Iye ndi ‘linga lathu m’nyengo ya nsautso.’ (Salmo 37:39) Buku la Miyambo limanenanso mawu ofanana ndi ameneŵa. Limati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” (Miyambo 18:10) Lemba limeneli limafotokoza mfundo yokhudza mmene Yehova amasamalilira mwachikondi zolengedwa zake. Mulungu amateteza makamaka anthu olungama amene amam’funafuna mwakhama, ngati kuti tikuthamanga kuti tikaloŵe mu linga lolimba ndi kubisalamo.
5 Tikakhala m’masautso, kodi tingathamangire motani kwa Yehova kuti atiteteze? Tiyeni tione zinthu zitatu zikuluzikulu zimene tingachite kuti Yehova atithandize. Choyamba, tiyenera kupemphera kwa Atate wathu wakumwambayu. Chachiŵiri, tiyenera kutsatira zimene mzimu wake woyera umafuna. Ndipo chachitatu n’chakuti tizicheza ndi Akristu anzathu amene angatichepetsere masautso, mogwirizana ndi zimene Yehova amatiuza.
Mphamvu Imene Pemphero Lili Nayo
6. Kodi Akristu oona amaliona motani pemphero?
6 Akatswiri ena a zaumoyo amati pemphero limathandiza kuthetsa kuvutika maganizo. Ngakhale kuti n’zoona kunena kuti maganizo amakhazikika munthu akakhala duu monga mmene amachitira popemphera, izi zingachitikenso pomvetsera zinthu zina zachilengedwe kapena kusisitidwa kumsana. Akristu oona sapeputsa pemphero poliona ngati mankhwala othandiza kuti maganizo akhale m’malo. Timaona kuti pemphero ndi njira yapamwamba kwambiri yolankhulira ndi Mlengi. Pemphero limafuna kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu ndiponso kuti tikhale ndi chikhulupiriro mwa iye. Inde, pemphero ndi mbali ya kulambira kwathu.
7. Kodi kupemphera mwachidaliro kumatanthauzanji, ndipo mapemphero otero amatithandiza motani kuti tithane ndi masautso?
7 Tiyenera kudalira Yehova pamene tikupemphera. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Uku ndi kulimbika mtima [“kum’dalira,” NW] kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera.” (1 Yohane 5:14) Yehova, yemwe ndi wapamwamba kwambiri, Mulungu yekhayo woona ndi wamphamvuyonse, amamvetsera mapemphero ochokera pansi pa mtima a anthu amene amamulambira. Kungodziŵa kokhako kuti Mulungu wathu wachikondi amamvetsera tikamam’fotokozera nkhaŵa ndiponso mavuto athu n’kolimbikitsa.—Afilipi 4:6.
8. N’chifukwa chiyani Akristu okhulupirika sayenera kuchita manyazi kapena kudziona kuti n’ngosayenera kupemphera kwa Yehova?
8 Akristu okhulupirika sayenera kuchita manyazi, kudziona kuti n’ngosayenera, kapena kukayikira akamapemphera kwa Yehova. N’zoona kuti tikadzikhumudwitsa kapena mavuto akatichulukira, sitingakhale ndi chizoloŵezi chokonda kupemphera kwa Yehova. Zinthu zikatero ndi bwino kukumbukira kuti Yehova ‘amachitira chifundo ovutidwa ake’ ndi kuti ‘amatonthoza odzichepetsa’ kapena kuti osautsidwa. (Yesaya 49:13; 2 Akorinto 7:6) Nthaŵi yomwe tathedwa nzeru ndiponso pamene tili mu nsautso m’pamene makamaka tiyenera kupemphera mwachidaliro kwa Atate wathu wakumwamba monga linga lathu.
9. Kodi chikhulupiriro chimagwira ntchito yanji pamene tikupemphera kwa Mulungu?
9 Kuti tipindule mokwanira ndi mwayi womatha kupemphera, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni. Baibulo limanena kuti “iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Kukhala ndi chikhulupiriro sikungokhulupirira chabe kuti Mulungu “alipo.” Munthu akakhala ndi chikhulupiro chenicheni amakhulupiriranso ndi mtima wonse kuti Mulungu ali ndi mphamvu yotipatsa mphoto chifukwa chokhala omvera ndiponso kuti iye akufunadi kuchita zimenezi. “Maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo.” (1 Petro 3:12) Kukumbukira nthaŵi zonse kuti Yehova amatidera nkhaŵa kumapangitsa kuti mapemphero athu azichokera pansi pa mtima.
10. Kodi mapemphero athu ayenera kukhala otani ngati tikufuna kuti Yehova atigwirizize mwauzimu?
10 Yehova amamvetsera mapemphero athu tikamapemphera ndi mtima wonse. Wamasalmo analemba kuti: “Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova.” (Salmo 119:145) Ife sitipemphera mosaikirapo mtima ngati mmene amachitira m’mapemphero a zipembedzo zambiri amene amangoperekedwa mwamwambo. Tikamapemphera kwa Yehova ndi ‘mtima wathu wonse,’ timatchula mfundo zomvekadi ndiponso zokhala ndi cholinga. Tikatha kupemphera mochokera pansi pa mtima choncho, timayamba kumva mpumulo womwe timapeza chifukwa chosenzetsa ‘Yehova nkhaŵa zathu.’ Mogwirizana ndi zimene Baibulo limalonjeza, ‘Iye adzatigwiriziza.’—Salmo 55:22; 1 Petro 5:6, 7.
Mzimu wa Mulungu Umatithandiza
11. Kodi ndi njira imodzi iti imene Yehova amatiyankhira ‘tikamapempha kosaleka’ thandizo lake?
11 Kuwonjezera pa kukhala Wakumva pemphero, Yehova alinso Woyankha pemphero. (Salmo 65:2) Davide analemba kuti: “Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu; popeza mudzandivomereza,” kapena kuti mudzandiyankha. (Salmo 86:7) Mogwirizana ndi mfundoyi, Yesu analimbikitsa ophunzira ake ‘kupempha [kosaleka, NW]’ thandizo la Yehova chifukwa chakuti ‘Atate wakumwambayu adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye.’ (Luka 11:9-13) Inde, mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu ndi mthandizi wolimbikitsa anthu ake.—Yohane 14:16.
12. Kodi mzimu wa Mulungu ungatithandize motani mavuto akatichulukira?
12 Ngakhale panthaŵi yomwe tili paziyeso, mzimu wa Mulungu ungatipatse “ukulu woposa wamphamvu.” (2 Akorinto 4:7) Mtumwi Paulo, amene anapirira masautso ambiri, ananena motsimikiza mtima kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) N’chimodzimodzinso ndi Akristu ambiri amasiku ano. Iwo apezanso mphamvu mwauzimu ndiponso mwamaganizo pambuyo popemphera. Nthaŵi zambiri tikalandira thandizo la mzimu wa Mulungu sitiona masautso ngati chinthu chofooketsa. Chifukwa cha mphamvu yochoka kwa Mulungu imeneyi, tinganene zangati zimene mtumwiyu ananena, kuti: “Ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osawonongeka.”—2 Akorinto 4:8, 9.
13, 14. (a) Kodi Yehova wakhala motani linga lathu kudzera m’Mawu ake olembedwa? (b) Kodi kugwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo kwakuthandizani motani inuyo panokha?
13 Komanso mzimu woyera unauzira ndi kusunga Mawu olembedwa a Mulungu kuti atithandize. Kodi Yehova wakhala motani linga lathu m’nyengo ya nsautso kudzera m’Mawu ake? Njira imodzi ndiyo mwa kutipatsa nzeru ndiponso luso la kuganiza. (Miyambo 3:21-24) Baibulo limaphunzitsa maganizo athu ndiponso kuwongolera ‘mphamvu zathu za kulingalira.’ (Aroma 12:1, NW) Tikamaŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, ndiponso kuwagwiritsira ntchito, tingapangitse ‘mphamvu zathu za kuzindikira kuzoloŵera kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ (Ahebri 5:14, NW) N’kutheka kuti inu mwaonapo mmene mfundo za m’Baibulo zinakuthandizirani kusankha mwanzeru zochita pamene munali pamavuto. Baibulo limatipatsa nzeru zimene zingatithandize kupeza njira zothetsera masautso.—Miyambo 1:4.
14 Mawu a Mulungu alinso ndi chinthu china chimene chimatipatsa mphamvu. Ali ndi chiyembekezo cha chipulumutso. (Aroma 15:4) Baibulo limatiuza kuti zinthu zoipa sizidzapitirira kuchitika mpaka kalekale. Mavuto onse amene timakumana nawo ndi a nthaŵi yochepa. (2 Akorinto 4:16-18) Tili ndi “chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthaŵi zosayamba.” (Tito 1:2) Tingapirire masautso ngati timakondwera ndi chiyembekezo chimenecho, komanso ngati nthaŵi zonse timaganizira za tsogolo labwino limene Yehova walonjeza.—Aroma 12:12; 1 Atesalonika 1:3.
Mpingo Ndi Umboni Wakuti Mulungu Amatikonda
15. Kodi Akristu angathandizane motani?
15 Njira ina imene Yehova angatithandizire panthaŵi ya masautso ndiyo anzathu amene timakhala nawo mu mpingo wachikristu. Baibulo limati: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) Mawu a Mulungu amalimbikitsa anthu onse mumpingo kuti azipatsana ulemu ndiponso kuti azikondana. (Aroma 12:10) “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake,” anatero mtumwi Paulo. (1 Akorinto 10:24) Kukhala ndi malingaliro ameneŵa kungatithandize kuganizira za mavuto a ena m’malo moganizira za mayesero athu okha. Tikamathandiza anthu ena, sikuti timangokhala tikuwathandiza koma timapezanso chimwemwe chimene chimapangitsa kuti mavuto athu apepuke.—Machitidwe 20:35.
16. Kodi Mkristu aliyense angatani kuti akhale wolimbikitsa?
16 Amuna ndi akazi okhwima mwauzimu angathandize kwambiri pankhani yolimbikitsa ena. Kuti achite zimenezi, amayesetsa kukhala ochezeka ndiponso okonzeka kukambirana zinthu ndi anzawo. (2 Akorinto 6:11-13) Mpingo umapindula kwambiri onse akamayesetsa kuyamikira ana, kulimbikitsa okhulupirira atsopano ndiponso ena omwe ali m’masautso. (Aroma 15:7) Kukonda abale athu kumatithandizanso kupeŵa mzimu wokayikirana. Tisamathamangire kunena kuti mavuto omwe anthu ali nawo ndi chizindikiro chakuti akufooka mwauzimu. Paulo anakhonza polimbikitsa Akristu kuti ‘azilimbikitsa otaya mtima.’ (1 Atesalonika 5:14, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Baibulo limasonyeza kuti ngakhale Akristu okhulupirika amakumana ndi nsautso.—Machitidwe 14:15.
17. Kodi tili ndi mipata yotani yomwe tingalimbitsire ubale wathu wachikristu?
17 Misonkhano yachikristu imatipatsa mwayi woti titonthozane ndi kulimbikitsana. (Ahebri 10:24, 25) Sikuti kulankhulana mwachikondi kumeneku kumangothera pamisonkhano ya mpingo. M’malo mwake, anthu a Mulungu amayesetsa kupeza mipata ina yochezerana. Motero, pakabuka zinthu zosautsa, sizingativute kuthandizana chifukwa chakuti pali kale mgwirizano wolimba. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Kusakhale chisiyano m’thupi; koma kuti ziwalo . . . zisamalane china ndi chinzake. Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.’—1 Akorinto 12:24-26.
18. Kodi tiyenera kupeŵa chizoloŵezi chotani panthaŵi imene tavutika maganizo kwambiri?
18 Nthaŵi zina, tingathe kuvutika maganizo kwambiri n’kumaona kuti sitingathe kucheza ndi Akristu anzathu. Tiyenera kupeŵa maganizo otero kuopa kuti tingataye mwayi woti tilimbikitsidwe ndiponso woti tithandizidwe ndi okhulupirira anzathu. Baibulo limatichenjeza kuti: “Wopanduka [“Wodzipatula,” NW] afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” (Miyambo 18:1) Zimene abale ndi alongo athu amatichitira ndi umboni wakuti Mulungu amatiganizira. Tingapeze mpumulo ku masautso athu tikamayamikira chikondi chimene Yehova anasonyeza potipatsa abale ndi alongo ameneŵa.
Khalani ndi Maganizo Olimbikitsa
19, 20. Kodi Malemba amatithandiza bwanji kupeŵa maganizo ofooketsa?
19 N’kosavuta kuti munthu akhale ndi maganizo ofooketsa ngati wataya mtima ndiponso ngati wakhumudwa. Mwachitsanzo, ena akakhala m’mavuto angathe kuyamba kukayikira za moyo wawo wauzimu, n’kumaganiza kuti kuvutika kwawoko ndi umboni wakuti Mulungu wasiya kuwayanja. Koma kumbukirani kuti Yehova sayesa aliyense ndi “zoipa.” (Yakobo 1:13) Baibulo limati Mulungu “samasautsa dala, ngakhale kumvetsa ana a anthu chisoni.” (Maliro 3:33) M’malo mwake, Yehova amamva chisoni kwambiri atumiki ake akamavutika.—Yesaya 63:8, 9; Zekariya 2:8.
20 Yehova ndi “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3) Iye amatisamalira, ndipo adzatikweza panthaŵi yake. (1 Petro 5:6, 7) Kukumbukira nthaŵi zonse kuti Mulungu amatikonda kungatithandize kukhalabe ndi maganizo olimbikitsa, ngakhalenso kukhala wosangalala kumene. Yakobo analemba kuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero amitundumitundu.” (Yakobo 1:2) Chifukwa chiyani? Iye anayankha kuti: “Pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akum’konda Iye.”—Yakobo 1:12.
21. Ngakhale kuti timakumana ndi mavuto, kodi Mulungu amawatsimikizira chiyani anthu amene ali okhulupirika kwa iye?
21 Mogwirizana ndi chenjezo la Yesu, m’dziko lino tizikhala ndi mavuto. (Yohane 16:33) Koma Baibulo limalonjeza kuti palibe ‘nsautso, kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zowopsa’ zimene zingatilekanitse ndi chikondi cha Yehova ndiponso chikondi cha Mwana wake. (Aroma 8:35, 39) N’zolimbikitsatu kwambiri kudziŵa kuti masautso onse amene timakumana nawoŵa n’ngakanthaŵi chabe. Pakalipano, pamene tikudikirira mapeto a mavuto a anthu, Yehova, yemwe ndi Atate wathu wachikondi, akutiyang’anira. Tikamam’funafuna kuti atiteteze, iye amakhala “msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m’nyengo za nsautso.”—Salmo 9:9.
Kodi Taphunzira Chiyani?
• Kodi Akristu ayenera kuyembekezera kuti chingachitike n’chiyani pamene ali m’dziko loipali?
• Kodi pemphero lochokera pansi pa mtima lingatilimbikitse motani pamene tili m’mayesero?
• Kodi mzimu wa Mulungu umatithandiza motani?
• Kodi tingatani kuti tithandizane?
[Chithunzi patsamba 18]
Tiyenera kufunafuna Yehova ngati kuti tikuthamanga kuti tikaloŵe mu linga lolimba
[Zithunzi patsamba 20]
Anthu okhwima mwauzimu amagwiritsira ntchito mpata uliwonse kuti ayamikire ndi kulimbikitsa ena