Yehova Ndi Malo Athu Okhalamo
“Inu Yehova, ndinudi malo athu okhalamo ku mibadwomibadwo.”—SAL. 90:1.
1, 2. Kodi atumiki a Yehova amamva bwanji akamakhala m’dzikoli? N’chifukwa chiyani tinganene kuti iwo ali ndi malo okhala?
KODI mumakhala momasuka bwinobwino m’dzikoli? Ngati si choncho, dziwani kuti si inu nokha? Kuyambira kalekale, anthu amene amakondadi Yehova amakhala ngati alendo m’dziko loipali. Mwachitsanzo, atumiki okhulupirika a Mulungu amene ankakhala moyo wosamukasamuka m’dziko la Kanani, “analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.”—Aheb. 11:13.
2 N’chimodzimodzinso ndi Akhristu odzozedwa omwe ndi “nzika zakumwamba.” Iwo amadziona kuti ndi “alendo ndiponso anthu osakhalitsa m’dzikoli.” (Afil. 3:20; 1 Pet. 2:11) Mofanana ndi Yesu, nazonso “nkhosa zina” sizili “mbali ya dzikoli.” (Yoh. 10:16; 17:16) Koma sikuti anthu a Mulungu alibe ‘malo okhala.’ Tili ndi malo okhala omwe ndi otetezeka komanso abwino kwambiri. Malo amenewa timawaona ndi maso achikhulupiriro. Mose anati: “Inu Yehova, ndinudi malo athu okhalamo ku mibadwomibadwo.”a (Sal. 90:1) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti iye anali malo okhalamo atumiki ake okhulupirika akale? Kodi iye amakhala bwanji malo okhalamo anthu odziwika ndi dzina lake masiku ano? Nanga adzakhala bwanji ‘malo okhalamo’ ndiponso otetezeka m’tsogolomu?
YEHOVA ANALIDI MALO OKHALAMO A ATUMIKI AKE AKALE
3. odi pa Salimo 90:1 Yehova akuyerekezeredwa ndi chiyani ndipo chifukwa chiyani?
3 Mofanana ndi mafanizo ambiri a m’Baibulo, mawu a pa Salimo 90:1 ali ndi mfundo yaikulu, chithunzi chake komanso kufanana kwake. Mfundo yaikulu kapena kuti mwininkhani ndi Yehova. Chithunzi chake ndi malo okhalamo. Yehova amafananadi ndi malo enieni okhalamo. Mwachitsanzo, Yehova amateteza anthu ake. Izi zikugwirizana ndi mfundo yakuti khalidwe lake lalikulu kwambiri ndi chikondi. (1 Yoh. 4:8) Iyenso ndi Mulungu wamtendere amene amathandiza anthu ake okhulupirika ‘kukhala otetezeka.’ (Sal. 4:8) Tiyeni tione mmene ankachitira zinthu ndi atumiki ake akale. Mwachitsanzo, tiyeni tiyambe kukambirana za Abulahamu.
4, 5. Kodi Mulungu anakhala bwanji malo okhalamo kwa Abulahamu?
4 Kodi mukuganiza kuti Abulahamu, yemwe pa nthawiyo ankadziwika ndi dzina loti Abulamu, anamva bwanji Yehova atamuuza kuti: “Tuluka m’dziko lako, pakati pa abale ako. . . . Upite kudziko limene ndidzakusonyeza”? Ngati Abulahamu ankada nkhawa ayenera kuti anasintha maganizo atamva mawu otsatira amene Yehova anamuuza. Anati: “Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa ndi kukuza dzina lako . . . Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo otemberera iwe ndidzawatemberera.”—Gen. 12:1-3.
5 Ponena mawu amenewa, Yehova anasonyeza kuti iye adzakhala malo achitetezo a Abulahamu ndiponso mbadwa zake. (Gen. 26:1-6) Yehova anachitadi zimene analonjezazo. Mwachitsanzo, Farao wa ku Iguputo komanso Abimeleki, mfumu ya ku Gerari, akanatha kuipitsa Sara n’kuphanso Abulahamu koma Yehova anawateteza. Anatetezanso Isaki ndi Rabeka pa zochitika za ngati zomwezi. (Gen. 12:14-20; 20:1-14; 26:6-11) Baibulo limati: “[Yehova] sanalole kuti munthu aliyense awachitire zachinyengo, koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo. Iye anati: ‘Anthu inu musakhudze odzozedwa anga, ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.’”—Sal. 105:14, 15.
6. Kodi Isaki anapereka malangizo otani kwa Yakobo ndipo mwina Yakobo ankamva bwanji?
6 Ena mwa aneneri amenewa anali Yakobo, yemwe anali chidzukulu cha Abulahamu. Itafika nthawi yoti Yakobo akwatire, Isaki anamuuza kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani. Nyamuka, pita ku Padana-ramu kunyumba ya Betuele bambo a mayi ako. Kumeneko ukatenge mkazi pakati pa ana a Labani.” (Gen. 28:1, 2) Yakobo anatsatira malangizo a Isaki. Iye ananyamuka kusiya achibale ake, amene pa nthawiyo ankakhala ku Kanani, n’kupita ku Harana. Ulendowu unali wautali kwambiri ndipo n’kutheka kuti anali yekha. (Gen. 28:10) Mwinatu ankadzifunsa kuti: ‘Kodi kumeneku ndikakhala nthawi yaitali bwanji? Kodi amalume angawo akandilandira bwino n’kundipatsadi mkazi woopa Mulungu?’ Ngati Yakobo ankadera nkhawa zimenezi ayenera kuti anasinthanso maganizo atafika pamalo otchedwa Luzi. Malowa anali pa mtunda wa makilomita 100 kuchokera ku Beere-seba. Kodi chinachitika n’chiyani ku Luzi?
7. Kodi Mulungu analimbikitsa bwanji Yakobo m’maloto?
7 Atafika ku Luzi, Yehova anaonekera kwa Yakobo m’maloto n’kumuuza kuti: “Ine ndili nawe ndipo ndikuyang’anira pa ulendo wako wonse, kufikira ndidzakubwezera kumalo ano. Sindidzakusiya kufikira nditachitadi zimene ndanena kwa iwe.” (Gen. 28:15) Mawu amenewatu ayenera kuti analimbikitsa Yakobo ndipo anamukhazika mtima pansi. Kodi mukuganiza kuti anayamba kuyenda bwanji atangomva mawu amenewa? Ayenera kuti ankafunitsitsa kuona mmene Mulungu angakwaniritsire mawu Akewo. Ngati munasamuka kwanu kukatumikira kudziko lina muyenera kuti mukumvetsa mmene Yakobo ankamvera mumtima mwake. Koma muyenera kuti mwaonanso Yehova akukusamalirani.
8, 9. Kodi Yehova anakhala bwanji malo okhalamo kwa Yakobo? Kodi tikuphunzirapo chiyani?
8 Yakobo atafika ku Harana, amalume ake a Labani anamulandira bwino ndipo kenako anamupatsa Leya ndi Rakele kuti akhale akazi ake. Koma Labani anayamba kupusitsa Yakobo n’kumusinthira malipiro ake maulendo 10. (Gen. 31:41, 42) Ngakhale zinali choncho, Yakobo anapirira zonsezi ndipo sankakayikira kuti Yehova apitiriza kumusamalira. Yehova anamusamaliradi. Pa nthawi imene Mulungu ankamuuza kuti abwerere ku Kanani, Yakobo anali ndi “ziweto zambiri, antchito aakazi ndi aamuna, ngamila ndi abulu.” (Gen. 30:43) Poyamikira Mulungu mochokera pansi pa mtima, Yakobo anapemphera kuti: “Ine ndine wosayenerera kukoma mtima kosatha ndi kukhulupirika konseku, kumene mwandionetsa ine mtumiki wanu. Ndinawoloka Yorodano ndilibe kanthu, koma ndodo yokha, ndipo tsopano ndili ndi magulu awiriwa.”—Gen. 32:10.
9 Zitsanzo zonsezi zikusonyeza kuti mawu a Mose anali oona. Paja iye anati: “Inu Yehova, ndinudi malo athu okhalamo ku mibadwomibadwo.” (Sal. 90:1) Umu ndi mmene Yehova alilinso kwa atumiki ake okhulupirika masiku ano. Iye akupitirizabe kukhala malo awo okhalamo abwino komanso otetezeka. Tisaiwale kuti iye “sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” (Yak. 1:17) Tiyeni tione mmene akuchitira zimenezi.
YEHOVA NDI MALO ATHU OKHALAMO MASIKU ANO
10. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yehova apitiriza kukhala malo okhalamo a atumiki ake?
10 Tiyerekeze kuti mwafika kukhoti kuti mupereke umboni pa mlandu wokhudza gulu lapadziko lonse la zigawenga zoopsa kwambiri. Mtsogoleri wa gululo ndi wochenjera kwambiri, wamphamvu, wabodza komanso wakupha. Kodi mungadzimve kuti ndinu wotetezeka potuluka m’khotilo pambuyo popereka umboni? Ayi ndithu, ndipo mungafune chitetezo champhamvu. Umu ndi mmene zilili ndi atumiki a Yehova. Iwo amaikira kumbuyo Yehova ndipo amapereka umboni wotsutsa Satana, yemwe ndi mdani wake wamkulu. (Werengani Chivumbulutso 12:17.) Koma kodi Satana wakwanitsa kulepheretsa anthu kutumikira Mulungu? Ayi. M’malomwake, timapitiriza kulalikira kwa anthu ambiri padziko lonse. Izi zikutheka chifukwa chakuti Yehova akupitiriza kutiteteza ndipo ndi “malo athu okhalamo” m’masiku otsiriza ano. (Werengani Yesaya 54:14, 17.) Koma kuti Yehova apitirize kukhala malo athu okhalamo, tisalole Satana kutipusitsa.
11. Kodi tikuphunzira chiyani kwa atumiki a Mulungu akale?
11 Tiyeni tionenso zimene tingaphunzire kwa atumiki akale. Ngakhale kuti ankakhala m’dziko la Kanani, iwo ankasiyana kwambiri ndi anthu a m’dzikolo ndipo ankadana ndi makhalidwe awo oipa. (Gen. 27:46) Sikuti ankafuna kuti pakhale lamulo pa nkhani iliyonse kuti azidziwa zoyenera ndi zosayenera. Zimene ankadziwa zokhudza Yehova komanso makhalidwe ake zinali zokwanira. Yehova anali malo awo okhalamo ndipo sankafuna kutengera ngakhale pang’ono makhalidwe a anthu oipa. Apatu anapereka chitsanzo chabwino kwa ife. Kodi mumatsanzira atumiki akalewa posankha anthu ocheza nawo komanso zosangalatsa? Chomvetsa chisoni n’chakuti Akhristu ena amaona kuti m’njira zina ndi omasuka m’dziko la Satanali. Ngati inuyo mumaona choncho ngakhale pang’ono, muyenera kuipempherera nkhaniyi. Musaiwale kuti dzikoli lili m’manja mwa Satana. Anthu ake amasonyeza mtima wa Satana wodzikonda komanso wosaganizira ena.—2 Akor. 4:4; Aef. 2:1, 2.
12. (a) Kodi Yehova wapereka zinthu ziti kwa atumiki ake? (b) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira zinthu zimene watipatsa?
12 Kuti Satana asatipusitse, tiyenera kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene Yehova amapereka kwa atumiki ake. Mwachitsanzo, iye amatithandiza pogwiritsa ntchito misonkhano, Kulambira kwa Pabanja ndiponso akulu amene amatilimbikitsa kuti tipirire mavuto athu. (Aef. 4:8-12) M’bale George Gangas, amene anali m’Bungwe Lolamulira kwa zaka zambiri, analemba kuti: “Ndikakhala ndi [anthu a Mulungu] ndimamasuka ngati kuti ndili ndi anthu a m’banja langa ndipo ndimaona kuti ndili m’paradaiso wauzimu.” Kodi inunso mumamva choncho?
13. Tchulani chinthu chofunika kwambiri chimene tikuphunzira pa Aheberi 11:13.
13 Atumiki akale sankaopa kukhala osiyana ndi anthu ena. Nafenso tiyenera kuwatsanzira pa nkhani imeneyi. Paja m’ndime yoyamba ija tanena kuti atumiki akalewa “analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.” (Aheb. 11:13) Kodi inunso mumafunitsitsa kukhala osiyana ndi anthu a m’dzikoli? N’zoona kuti kuchita zimenezi si kophweka. Koma mukhoza kukwanitsa mothandizidwa ndi Mulungu komanso Akhristu anzanu. Kumbukirani kuti simuli nokha. Anthu onse amene akufuna kutumikira Yehova ali pa nkhondo. (Aef. 6:12) Tikhoza kupambana nkhondoyi ngati tidalira Yehova n’kumaona kuti iye ndi malo athu okhalamo otetezeka kwambiri.
14. Kodi atumiki a Yehova ankayembekezera “mzinda” uti?
14 Tiyenera kutsanziranso Abulahamu pa nkhani yoyembekezera mphoto. (2 Akor. 4:18) Mtumwi Paulo analemba kuti Abulahamu “anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.” (Aheb. 11:10) “Mzinda” umenewu ndi Ufumu wa Mesiya. Abulahamu ankafunika kuyembekezera “mzinda”umenewu. Koma ife sitifunika kuuyembekezera chifukwa panopa wayamba kale kulamulira kumwamba. Komanso umboni woti posachedwapa uyamba kulamulira dziko lonse, ukuonekera. Kodi zimene mumachita pa moyo wanu zimasonyeza kuti mumakhulupirira Ufumuwu? Kodi mumaika Ufumuwu pa malo oyamba komanso kukhala osiyana ndi dziko?—Werengani 2 Petulo 3:11, 12.
YEHOVA AKHALABE MALO ATHU OKHALAMO PAMENE MAPETO AKUYANDIKIRA
15. Kodi anthu amene amakhulupirira dzikoli zidzawathera bwanji?
15 Pamene dziko la Satanali likupita kumapeto, mavuto okhala ngati “zowawa za pobereka” aziwonjezereka. (Mat. 24:7, 8) Zinthu zidzafika poipitsitsa pa chisautso chachikulu. Zinthu zambirimbiri zidzawonongedwa kapena kusokonekera ndipo anthu adzachita mantha kwambiri. (Hab. 3:16, 17) Chifukwa chosowa mtengo wogwira, iwo adzabisala “m’mapanga ndi m’matanthwe a m’mapiri.” (Chiv. 6:15-17) Koma mapanga enieni, kapena mabungwe andale ndi azachuma amene amakhala ngati mapiri, sadzawathandiza.
16. Kodi mpingo tiyenera kuuona bwanji ndipo n’chifukwa chiyani?
16 Koma Yehova Mulungu adzatiteteza pa chisautso chachikulu. Mofanana ndi mneneri Habakuku, ‘tidzakondwerabe mwa Yehova ndipo tidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso chathu.’ (Hab. 3:18) Kodi Yehova adzakhala bwanji malo athu okhalamo pa nthawi yovutayo? Panopa sitikudziwa koma zidzaoneka nthawi yomweyo. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti mofanana ndi Aisiraeli pa ulendo wawo wochoka ku Iguputo, “khamu lalikulu” lizidzachita zinthu mwadongosolo n’kumatsatira malangizo a Yehova. (Chiv. 7:9; werengani Ekisodo 13:18.) Zikuoneka kuti Yehova azidzapereka malangizo amenewa kudzera m’mipingo. Pa Yesaya 26:20 timamva za ‘zipinda zamkati’ mmene anthu a Mulungu angabisalemo kuti atetezeke. (Werengani Yesaya 26:20.) N’kutheka kuti zipinda zimenezi zikuimira mipingo masauzande ambiri imene ili padzikoli. Kodi inuyo mumakonda kupezeka pa misonkhano yampingo? Kodi mumatsatira mwamsanga malangizo amene Yehova amapereka kudzera mu mpingo?—Aheb. 13:17.
17. Kodi Yehova amakhala bwanji malo okhalamo a atumiki ake okhulupirika amene anamwalira?
17 Ngakhale anthu okhulupirika amene adzamwalire chisautso chachikulu chisanayambe, adzakhala otetezeka m’manja mwa Yehova yemwe ndi ‘malo awo okhalamo.’ N’chifukwa chiyani tikutero? Atumiki akale okhulupirika atamwalira, Yehova anauza Mose kuti: “Ndine Mulungu wa . . . Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.” (Eks. 3:6) Ndiyeno Yesu anagwira mawu amenewa n’kunena kuti: “Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:38) Izi zikusonyeza kuti pa maso pa Yehova, anthu okhulupirika amene anamwalira ndi amoyo chifukwa n’zosakayikitsa kuti adzawaukitsa.—Mlal. 7:1.
18. Kodi Yehova adzakhala bwanji malo okhalamo anthu ake m’dziko latsopano?
18 M’dziko latsopano limene layandikira, Yehova adzakhala malo okhala anthu ake m’njira inanso. Pa Chivumbulutso 21:3, timawerenga kuti: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo.” Poyamba, Yehova adzakhala ndi anthu ake padziko lapansi kudzera mwa Khristu Yesu. Pamapeto pa zaka 1,000, Yesu adzapereka Ufumu kwa Atate wake ndipo apa adzakhala atakwaniritsa chifuniro cha Mulungu padziko lapansi. (1 Akor. 15:28) Izi zikadzachitika, Yehova azidzalamulira anthu popanda mkhalapakati. Koma ndiye tikuyembekezera zinthu zabwino bwanji! Chofunika panopa n’kutsanzira atumiki okhulupirika akale amene ankaona kuti Yehova ndi ‘malo awo okhalamo.’
a Baibulo lina limamasulira lemba la Salimo 90:1 kuti: “Ambuye wathu, mwakhala nyumba yathu ku mibadwo yonse.”—Contemporary English Version.