MUTU 3
Tate wa Onse Okhala Ndi Chikhulupiriro
1, 2. Kodi zinthu zinasintha bwanji padziko lapansi kuyambira nthawi ya Nowa, nanga zimenezi zinkamukhudza bwanji Abulamu?
TSIKU lina Abulamu anayang’ana nsanja yaitali ya kachisi amene anali mumzinda wawo wa Uri.a Utsi unkakwera kuchokera m’kachisiyo ndipo munkamveka phokoso la ansembe omwe ankapereka nsembe kwa mulungu wa mwezi. Ndiyeno yerekezerani kuti mukumuona Abulamu akuyang’ana kumbali kwinaku akupukusa mutu wake komanso ataipitsa nkhope chifukwa cha zoipa zomwe zikuchitikazo. Pamene akubwerera kwawo n’kumadutsana ndi magulu a anthu, iye akuganizira za kulambira konyenga komwe anthu a mumzinda wa Uri ankachita. Pa nthawiyo, kulambira konyenga komwe kunayamba m’nthawi ya Nowa kunali kutafala kwambiri.
2 Nowa anamwalira kutangotsala zaka ziwiri kuti Abulamu abadwe. Nowa ndi banja lake atatuluka m’chingalawa pambuyo pa Chigumula, anapereka nsembe kwa Yehova Mulungu, yemwe kenako anachititsa kuti kuoneke utawaleza. (Gen. 8:20; 9:12-14) Pa nthawi imeneyo kulambira komwe kunalipo kunali koona basi. Koma nthawi ya Abulamu, womwe unali m’badwo wa 10 kuchokera pa Nowa, panali anthu ochepa chabe amene ankatsatira kulambira koona. Anthu ambiri ankalambira milungu yonyenga. Ngakhale Tera, yemwe anali bambo ake a Abulamu, nayenso ankalambira mafano ndipo n’kuthekanso kuti ankapanga mafanowo.—Yos. 24:2.
Kodi n’chiyani chinathandiza Abulamu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba?
3. Kodi Abulamu anasonyeza kuti anali ndi khalidwe liti, nanga zimenezi zingatithandize bwanji?
3 Koma Abulamu sankalambira nawo mafano chifukwa ankakhulupirira Mulungu. Ndipotu patapita nthawi mtumwi Paulo anamutchula kuti ndi “tate wa onse . . . okhala ndi chikhulupiriro.” (Werengani Aroma 4:11.) Tiyeni tione zimene zinachititsa kuti Abulamu akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Zimenezi zitithandiza kuona zomwe tingachite kuti nafenso tikhale ndi chikhulupiriro cholimba.
Kutumikira Yehova Pambuyo pa Chigumula
4, 5. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Abulamu ayenera kuti anaphunzira za Yehova kuchokera kwa Semu?
4 Kodi Abulamu anaphunzira bwanji za Yehova Mulungu? Timadziwa kuti pa nthawiyo panali atumiki okhulupirika a Yehova ndipo mmodzi mwa atumiki amenewa anali Semu. Ngakhale kuti Semu sanali wamkulu pa ana atatu a Nowa, nthawi zambiri amatchulidwa koyambirira. N’kutheka kuti ankatchulidwa koyambirira chifukwa anali ndi chikhulupiriro cholimba.b Patapita nthawi Chigumula chitachitika, Nowa anatchula Yehova kuti anali “Mulungu wa Semu.” (Gen. 9:26) Semu ankalemekeza Yehova komanso kulambira koona.
5 Kodi Abulamu ankadziwana ndi Semu? N’kutheka kuti ankadziwana. Abulamu ali mnyamata ayenera kuti anasangalala kudziwa kuti ali ndi agogo a zaka zoposa 400. Semu anaona zinthu zoipa zimene zinkachitika Chigumula chisanachitike komanso anaona Chigumula chimene chinawononga anthu onse oipa. Iye analipo pamene anthu anayambiranso kuchulukana padziko lapansi komanso pamene Nimurodi anapanduka n’kuyamba kumanga Nsanja ya Babele. Koma Semu anali munthu wokhulupirika ndipo sankamanga nawo nsanja ya Babele. Choncho, Yehova atasokoneza chilankhulo cha anthu amene ankamangawo, Semu ndi banja lake anapitirizabe kulankhula chinenero choyambirira, chimenenso Nowa ankalankhula. Abulamu anali m’gulu la anthu a m’banja la Semu omwe ankalankhulabe chinenero choyambirira. Choncho, Abulamu ayenera kuti ankalemekeza kwambiri Semu. Komanso Semu anamwalira Abulamu ali wamkulu kale. Motero Abulamu ayenera kuti anaphunzira za Yehova kuchokera kwa Semu.
6. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Abulamu anamvetsa chifukwa chake Yehova anabweretsa Chigumula? (b) Fotokozani mmene moyo unalili m’banja la Abulamu ndi Sarai.
6 Kaya Abulamu anaphunzira za Yehova kuchokera kwa Semu kapena ayi, iye anamvetsa chifukwa chake Yehova anabweretsa Chigumula ndipo ankafunitsitsa kutsatira chitsanzo cha Nowa. N’chifukwa chake sankalambira nawo mafano, ngakhale kuti abale ake ena ankalambira mafano. Kenako iye anakwatira Sarai, yemwe anali mkazi wabwino kwambiri, wokongola komanso ankakhulupirira Yehova.c Ngakhale kuti analibe ana, banja lawo linali losangalala ndipo ankatumikira limodzi Yehova. Iwo ankakhalanso ndi Loti, yemwe anali mwana wa m’bale wake wa Abulamu.
7. Kodi otsatira a Yesu angatsanzire bwanji Abulamu?
7 Ngakhale kuti anthu ambiri a mumzinda wa Uri ankalambira mafano, Abulamu ndi Sarai sanasiye kulambira Yehova. Iwo analolera kuti azisalidwa ndi anthu a mumzindawo. Ifenso ngati tikufuna kukhala ndi chikhulupiriro cholimba tiyenera kutsatira chitsanzo chawo. Yesu ananena kuti otsatira ake sayenera kukhala “mbali ya dzikoli.” Iye ananenanso kuti chifukwa cha zimenezi anthu adzadana nawo. (Werengani Yohane 15:19.) Ngati abale anu kapena anthu a kudera limene mumakhala amakusalani chifukwa choti munasankha kutumikira Yehova, dziwani kuti si muli nokha. Muli ndi Yehova ngati mmene Abulamu ndi Sarai analilinso ndi Yehova.
“Tuluka M’dziko Lako”
8, 9. (a) Kodi Abulamu anali ndi mwayi wapadera kwambiri uti? (b) Kodi Yehova anauza Abulamu uthenga wotani?
8 Tsiku lina Abulamu anali ndi mwayi wapadera kwambiri chifukwa analankhulana ndi Yehova Mulungu. Baibulo silifotokoza zambiri za zimene zinachitika pa nthawiyi koma limangonena kuti “Mulungu waulemerero” anaonekera kwa munthu wokhulupirikayu. (Werengani Machitidwe 7:2, 3.) Mwina kudzera mwa mngelo, Abulamu anaona ulemerero wa Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Abulamu ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona kusiyana kwa pakati pa Mulungu wamoyo ndi mafano amene anthu ambiri ankalambira.
9 Kodi uthenga wa Yehova kwa Abulamu unali wotani? Anamuuza kuti: “Tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako. Tiye ukalowe m’dziko limene ine ndidzakusonyeza.” Yehova sanamuuze Abulamu kuti apite dziko liti, anangomuuza kuti amusonyeza. Apa Abulamu anayenera kusiya dziko lakwawo komanso abale ake. Komatu anthu a ku Middle East wakale ankaona kuti kukhala pakati pa abale awo ndi chinthu chofunika kwambiri. Kuti munthu asiye abale ake n’kupita kudziko lakutali zinali zowawa kwambiri ngati imfa.
10. N’chifukwa chiyani zinali zovuta kuti Abulamu ndi Sarai asamuke ku Uri?
10 Zinali zovuta kwambiri kwa Abulamu kuti achoke ku Uri. Mzindawu unali wotukuka kwambiri komanso unali ndi anthu ambiri. (Onani bokosi lakuti “Kodi Mzinda Umene Abulamu ndi Sarai Ankakhala Poyamba Unali Wotani?”) Ofukula zinthu zakale anapeza kuti anthu a mumzinda wa Uri ankakhala ndi nyumba zabwino kwambiri ndipo zina zinkakhala ndi zipinda 12 kapena kuposa momwe munkagona anthu a m’banjamo komanso antchito. Zipindazi zinkamangidwa mozungulira bwalo lamkati lomwe linkakhala lokonzedwa bwino kwambiri. Mumzindawu munkapezekanso madzi a m’mipope, zimbudzi za madzi komanso ngalande zodutsa zinthu zoipa. Komanso kumbukirani kuti Abulamu ndi Sarai anali anthu akuluakulu. Abulamu ayenera kuti anali ndi zaka za m’ma 70, pamene mkazi wake anali ndi zaka za m’ma 60. Mofanana ndi zimene mwamuna aliyense wabwino amafunira mkazi wake, Abulamu ayenera kuti ankafuna kuti Sarai asamavutike kwambiri pa moyo wake komanso kuti azisamalidwa bwino. Taganizirani mafunso amene iwo anali nawo pa nthawi imene ankakambirana zosamukazo. Koma Abulamu ayenera kuti anasangalala kwambiri Sarai atavomera kusamuka. Mofanana ndi mwamuna wake, iye anali wokonzeka kusiya zinthu zonse zabwino zimene anali nazo.
11, 12. (a) Kodi Abulamu ndi Sarai anafunika kukonzekera zinthu ziti asananyamuke ulendo wawo? (b) Kodi mukuganiza kuti zinali bwanji pa nthawi imene anthuwa ankanyamuka?
11 Atagwirizana zosamukazo, Abulamu ndi Sarai anali ndi zambiri zochita pokonzekera ulendowu. Iwo anafunika kulongedza katundu wosiyanasiyana. Anafunikanso kusankha katundu amene angatenge pa ulendowu ndi amene angamusiye ndiponso kuganiza zimene achite ndi abale awo, antchito komanso makamaka Tera bambo a Abulamu, omwe pa nthawiyi anali wokalamba. Abulamu ndi Sarai anaona kuti ndi bwino kuti awatenge bambo awowa pa ulendowu. Tera ayenera kuti anavomereza ndi mtima wonse kupita nawo chifukwa nkhaniyi imatchula kuti iyeyo ndi amene anatenga banja lake kutuluka mumzinda wa Uri. Mwina amafotokoza choncho chifukwa iye ndi amene anali kholo la anthuwo. Tera ayenera kuti anasiya kulambira mafano. Nayenso Loti anapita nawo pa ulendowu.—Gen. 11:31.
12 Tsopano linafika tsiku loti anyamuke ulendo wawo. Yerekezerani kuti mukuwaona anthuwa atasonkhana kunja kwa mpanda wa mzinda wa Uri. Iwo anali atakweza katundu wawo pangamila ndi abulu komanso panali ziweto zimene anatenga ndipo anthu onse anali okonzeka kunyamuka.d Mwina onse ankangodikirira kuti Abulamu awauze kuti anyamuke. Kenako Abulamu anauzadi anthuwo kuti anyamuke kuchoka mumzinda wa Uri.
13. Kodi atumiki a Yehova ambiri asonyeza bwanji mzimu wodzimana ngati mmene anachitira Abulamu ndi Sarai?
13 Masiku anonso atumiki ambiri a Yehova amasamukira kumene kulibe olalikira Ufumu ambiri. Ena amaphunzira chinenero china n’cholinga choti azitha kulalikira anthu achinenerocho. Enanso amasankha kuchita utumiki winawake womwe poyamba ankaona kuti sangaukwanitse. Kuchita zimenezi kumafuna kudzimana koma kumasangalatsa kwambiri Yehova. Komanso anthu oterewa amakhala akutengera chitsanzo cha Abulamu ndi Sarai ndipo amasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro. Yehova amadalitsa kwambiri anthu amenewa ndipo sadzaiwala kukhulupirika kwawo. (Aheb. 6:10; 11:6) Koma kodi Yehova anadalitsa Abulamu chifukwa cha kukhulupirika kwake?
Anawoloka Mtsinje wa Firate
14, 15. (a) Fotokozani zimene zinachitika pa ulendo wochokera ku Uri kukafika ku Harana. (b) Kodi n’kutheka kuti Abulamu anaganiza zokhala ku Harana kwa kanthawi chifukwa chiyani?
14 Anthuwa anayenda kwa nthawi yaitali. Abulamu ndi Sarai ayenera kuti ankasinthana kukwera pabulu, wina akakwera wina ankayenda. Iwo ayeneranso kuti ankakambirana nkhani zosiyanasiyana pa ulendo wawowu komanso pankamveka kulira kwa tizitsulo ta zingwe za ngamila. Kenako anthu onse pa gululi anazolowera ulendowu moti sankavutika kumanga komanso kuphwasula mahema. Ayenera kuti anazoloweranso mmene angathandizire Tera kukhala bwinobwino pangamila kapena pabulu. Iwo anadutsa m’mbali mwa mtsinje wa Firate kulowera kumpoto chakumadzulo ndipo anapitirizabe kuyenda kwa masiku ambirimbiri.
15 Kenako, atayenda mtunda wamakilomita 960, anafika mumzinda wotukuka wa Harana momwe munkakumana misewu yosiyanasiyana imene amalonda akum’mawa ndi akumadzulo ankadutsa. Anthuwa anakhala mumzindawu kwa kanthawi. N’kutheka kuti Tera anali atatopa komanso atafooka kwambiri moti sakanatha kupitiriza kuyenda.
16, 17. (a) Kodi Abulamu anasangalala kwambiri ndi pangano liti? (b) Kodi Yehova anadalitsa bwanji Abulamu pa nthawi yomwe anakhala ku Harana?
16 Patapita nthawi Tera anamwalira ali ndi zaka 205. (Gen. 11:32) Pa nthawiyi Yehova analankhulanso ndi Abulamu ndipo izi zinamulimbikitsa kwambiri pa nthawi yovutayi. Yehova anabwereza malangizo amene anauza Abulamu ku Uri ndipo anawonjezera madalitso amene anamulonjeza. Anauza Abulamu kuti adzakhala “mtundu waukulu” ndipo kudzera mwa iye anthu onse a padziko lapansi adzapeza madalitso. (Werengani Genesis 12:2, 3.) Abulamu anasangalala kwambiri ndi pangano limeneli ndipo ananyamuka n’kuyamba kupitiriza ulendo wake.
17 Koma pa nthawiyi anali ndi zinthu zambiri zoti alongedze chifukwa Yehova anali atadalitsa kwambiri Abulamu. Nkhaniyi imafotokoza kuti iwo anatenga “chuma chawo chonse, komanso akapolo awo onse amene anapeza kudziko la Harana.” (Gen. 12:5) Kuti Abulamu akhale mtundu waukulu, banja lake linafunika kukhala ndi chuma komanso antchito. Sikuti nthawi zonse Yehova amadalitsa atumiki ake powapatsa chuma. Komabe iye amawapatsa zinthu zonse zofunika kuti akwaniritse cholinga chake. Abulamu ananyamuka ku Harana n’kuyamba kupitiriza ulendo wake.
18. (a) Kodi ndi liti pamene Abulamu anawoloka mtsinje wa Firate? (b) Kodi ndi zinthu zinanso zofunika ziti zimene zinachitika pa Nisani 14? (Onani bokosi lakuti “Deti Lofunika Kwambiri M’mbiri ya Baibulo.”)
18 Atayenda masiku angapo anafika pamalo otchedwa Karikemisi, pomwe anthu apaulendo ankawolokera mtsinje wa Firate. N’kutheka kuti pamalo amenewa ndi pamene panachitika zinthu zapadera kwambiri m’mbiri yonena za zimene Mulungu wakhala akuchitira anthu ake. Abulamu ndi anthu onse amene anali nawo anawoloka mtsinjewu m’chaka cha 1943 B.C.E pa 14, m’mwezi umene kenako unkadziwika kuti Nisani. (Eks. 12:40-43) Kum’mwera kwa derali kunali dziko limene Yehova anauza Abulamu kuti amusonyeza. Pangano limene Yehova anachita ndi Abulamu linayamba kugwira ntchito pa tsikuli.
19. Kodi Yehova anatchula za chiyani mu lonjezo limene anauza Abulamu, ndipo Abulamu ayenera kuti anakumbukira chiyani?
19 Abulamu anapitiriza ulendo wake kulowera kum’mwera ndipo kenako anaima ku Sekemu, pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya More. Pamenepa Yehova analankhulanso ndi Abulamu. Pa nthawiyi Mulungu alonjeza Abulamu kuti adzapereka dzikolo kwa mbewu yake. N’kutheka kuti Abulamu anakumbukira za ulosi umene Yehova ananena m’munda wa Edeni pamene anatchula za “mbewu” imene idzapulumutse anthu onse. (Gen. 3:15; 12:7) Iye ayenera kuti anayamba kuona kuti Yehova adzamugwiritsa ntchito pokwaniritsa ulosi umenewu.
20. Kodi Abulamu anasonyeza bwanji kuti ankayamikira madalitso amene Yehova anamulonjeza?
20 Abulamu anayamikira kwambiri madalitso amene Yehova anamupatsa. Pamene ankapitiriza ulendo wake, ayenera kuti ankayenda mosamala chifukwa m’deralo munali mudakakhalabe Akanani. Iye anaima malo awiri n’kumanga guwa limene anaperekerapo nsembe kwa Yehova. Choyamba anaima pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya More ndipo kenako anaima pafupi ndi Beteli. Iye anapemphera kwa Yehova ndipo ayenera kuti anamuyamikira kuchokera pansi pa mtima poganizira za mbewu yake. Abulamu ayenera kuti ankalalikiranso kwa Akanani omwe ankakhala pafupi. (Werengani Genesis 12:7, 8.) Komabe pambuyo pa zimenezi, Abulamu anakumana ndi zinthu zambiri zoyesa chikhulupiriro chake. Koma iye sankaganizira kwambiri za zinthu zimene anasiya ku Uri. Ankaganizira kwambiri za madalitso a m’tsogolo. Lemba la Aheberi 11:10 limanena za Abulamu kuti: “Anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.”
21. (a) Kodi zimene ife tikudziwa zokhudza Ufumu wa Mulungu zikusiyana bwanji ndi zimene Abulamu ankadziwa? (b) Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?
21 Masiku ano, tikudziwa zambiri zokhudza mzinda wophiphiritsa umenewu, womwe ndi Ufumu wa Mulungu, kuposa mmene Abulamu ankadziwira. Tikudziwa kuti Ufumuwu unayamba kale kulamulira ndipo posachedwapa uwononga dziko loipali. Tikudziwanso kuti Yesu Khristu, yemwe ndi mbewu ya Abulamu imene Mulungu analonjeza kalekale, ndiye Mfumu ya Ufumuwu. Tidzasangalala kwambiri kuona Abulamu ataukitsidwa. Pa nthawiyi, adzamvetsa bwino mmene Yehova anakwaniritsira cholinga chake. Kodi inuyo mungakonde kudzaona mmene Yehova adzakwaniritsire malonjezo ake onse? Ngati mungakonde, yesetsani kutsanzira chikhulupiriro cha Abulamu. Muziyesetsa kusonyeza mtima wodzimana, womvera komanso woyamikira madalitso amene Yehova wakupatsani. Mukatero, Abulamu yemwe ndi “tate wa onse . . . okhala ndi chikhulupiriro,” adzakhalanso tate wanu.
a Patapita zaka zambiri, Mulungu anamusintha dzina Abulamu n’kukhala Abulahamu. Dzina lakuti Abulahamu limatanthauza “Tate wa Mitundu Yambiri.”—Gen. 17:5.
b Nayenso Abulamu amatchulidwa koyambirira pa ana a Tera, ngakhale kuti sanali woyamba kubadwa.
c Patapita nthawi, Mulungu anasintha dzina la Sarai kuti likhale Sara, kutanthauza “Mfumukazi.”—Gen. 17:15.
d Akatswiri ena amakayikira zoti m’nthawi ya Abulamu anthu ankakhala ndi ngamila. Koma palibe umboni wosonyeza kuti anthu sankakhala ndi ngamila pa nthawiyi. Tikutero chifukwa m’Baibulo muli mavesi angapo amene amasonyeza kuti Abulamu anali ndi ngamila.—Gen. 12:16; 24:35.