Chigawo 3
Mmene Tingadziŵire Kuti Mulungu Aliko
1, 2. Kodi ndi lamulo lamakhalidwe abwino lotani limene limatithandiza kutsimikiza kaya ngati Mulungu aliko?
NJIRA imodzi yodziŵira kuti kaya ngati Mulungu aliko ndiyo kugwiritsira ntchito lamulo la makhalidwe abwino lodziŵika bwino ili: Chopangidwa chimafunikira wochipanga. Pamene chinthu chopangidwa chili chocholoŵanacholoŵana, momwemo wochipanga ayenera kukhala mmisiri waluso.
2 Mwachitsanzo, taunguzani m’nyumba mwanu. Magome, mipando, madesiki, makama, miphika, ziwaya, mbale, ndi ziwiya zodyera zonsezo zimafunikira wozipanga, chomwecho makoma, pansi panyumba ndi masiling’i. Komabe, zinthu zimenezo n’zosavutilapo kwambiri kuzipanga. Popeza kuti zinthu zosavutilapo zimafuna wozipanga, kodi sikuli koyenerera kuti zinthu zocholoŵana zimafunikiranso wozipanga wanzeru koposa?
Chilengedwe Chathu Chochititsa Mantha
3, 4. Kodi ndi motani mmene chilengedwe chonse chimatithandizira kudziŵa kuti Mulungu aliko?
3 Wotchi imafunikira wopanga mawotchi. Bwanji ponena za mapulaneti athu ozungulira dzuŵa, ocholoŵana kopambanitsawo, ophatikizapo Dzuŵa ndi maplaneti ake olizungulira m’timphindi tochepetsetsa mosaphonyetsa kwa zaka mazanamazana? Bwanji ponena za khamu la nyenyezi m’limene tili, lotchedwa Mlalang’amba, limodzi ndi nyenyezi zake zoposa mabiliyoni 100? Kodi munayamba mwaima kaye pausiku kuyang’anitsitsa Mlalang’ambawo? Kodi munachita chidwi? Pamenepo talingalirani za chilengedwe chonse chodabwitsa chimene chili ndi makamu a nyenyezi mabiliyoni amabiliyoni ake ofanana ndi Mlalang’amba wathu! Ndiponso, makamu a zakuthambowo ngodalirika kwambiri m’mayendedwe awo m’zaka mazanamazana kotero kuti ayerekezeredwa ndi makoloko osunga nthaŵi koposa.
4 Ngati wotchi imene ili yocholoŵana pang’ono, imasonyeza kukhalako kwa wopanga mawotchi, ndithudi chilengedwe chochititsa mantha ndi chocholoŵana koposa chimasonyeza kukhalako kwa wolinganiza ndi wopanga. Ndicho chifukwa chake Baibulo limatipempha ‘kutukula maso athu kumwamba ndi kuwona,’ ndiyeno limafunsa: “Kodi ndani walenga zinthu zimenezi?” Yankho ndilo: “Ali [Mulungu] amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndipo popeza ali wolimba mphamvu palibe imodzi isoŵeka.” (Yesaya 40:26) Chotero, chilengedwe chonse chinakhalako chifukwa cha mphamvu yosawoneka, yolamulira, ndi yaluntha—Mulungu.
Dziko Lapansi Lolinganizidwa Mwapadera
5-7. Kodi ndi maumboni ati onena za dziko lapansi amene amasonyeza kuti linali ndi Wolinganiza?
5 Pamene asayansi apenda mowonjezereka dziko lapansi, ndipamenenso iwo amazindikira mowonjezereka kuti ilo linalinganizidwa mwapadera kuti likhalidwe ndi anthu. Lili pamtunda woyenerera kwenikweni kuchokera kudzuŵa kuti lipeze mlingo woyenerera wa kuunika ndi kutentha. Kamodzi pachaka limayenda mozungulira dzuŵa, lili ndi mlingo woyenerera kwambiri wakupendama kutheketsa nyengo m’mbali zambiri zadziko lapansi. Dziko lapansi limazunguliranso pagudumu lake maola 24 aliwonse, likumapereka nyengo za nthaŵi zonse za kuunika ndi mdima. Lili ndi m’mwamba mokhala ndi msanganizo woyenerera kwambiri wa mipweya kotero kuti tikhoze kupuma ndi kutetezeredwa kucheza chovulaza chochokera kutali m’mlengalenga. Lilinso ndi madzi ofunika kwambiriwo ndi nthaka yofunika kulimapo chakudya.
6 Popanda zinthu zonsezo ndi zina kugwira ntchito pamodzi, moyo ukanakhala wosatheka. Kodi zonsezo zinachitika zokha? Science News imati: “Kukuwonekera ngati kuti mikhalidwe yeniyeni yotere ndi yotsimikizirika sikanangokhalapo yokha.” Ayi, sikanatero. Inaphatikizapo kulinganiza kokhala ndi chifuno ndi wolinganiza wapamwamba kopambana.
7 Ngati mutaloŵa m’nyumba yabwino ndipo nimupeza kuti inali ndi chakudya chochuluka, ndi kuti inali ndi dongosolo labwino koposa lothumitsira ndi kuziziritsira m’nyumba, ndi kuti inali ndi mipopi yabwino yamadzi, kodi mukananenanji? Kuti zonsezo zinangochitika zokha? Ayi, inu mukanatsimikiziradi kuti munthu waluntha analinganiza ndi kupanga mosamalitsadi. Dziko lapansi linalinganizidwanso ndi kupangidwa mosamalitsadi kuchitira kuti lipereke zofunika kwa okhalamo ake, ndipo lili locholoŵana kwambiri ndi lamwana alirenji kuposa nyumba iliyonse.
8. Kodi palinso chiyani ponena za dziko lapansi chimene chimasonyeza chisamaliro chachikondi cha Mulungu kwa ife?
8 Ndiponso, talingalirani kuchuluka kwa zinthu zimene zimawonjezera chikondwerero kukukhala ndi moyo. Tawonani mitundu yosiyanasiyanayo ya maluŵa amawonekedwe okongola ndi kununkhira kwawo kwabwino kumene anthu amasangalala nako ndiyeno pali zakudya zotikomera za mitundumitundu. Pali nkhalango, mapiri, nyanja, ndi zolengedwa zina zokondweretsa kuziyang’ana. Ndiponso, bwanji ponena za kuloŵa kwa dzuŵa kokongola kumene kumawonjezera chikondwerero chathu m’moyo? Ndipo pazinyama, kodi sitimakondwera ndi kulumphalumpha koseŵera kwa zinyama ndi mkhalidwe wokondweretsa wa tiana tagalu, tiana tamphaka, ndi tiana ta zinyama zina? Chotero dziko lapansi limapereka zozizwitsa zambiri zokondweretsa zimene sizili kwenikweni zofunika kuchirikiza moyo. Zimenezi zimasonyeza kuti dziko lapansi linalinganizidwa mwachisamaliro chachikondi molingalira anthu, kotero kuti ife tisangokhalapo kokha komanso tisangalale ndi moyo.
9. Kodi ndani amene anapanga dziko lapansi, ndipo analipangiranji?
9 Chifukwa chake, chinthu chanzeru kuchichita ndicho kuvomereza wopereka zinthu zonsezi, monga momwe anachitira wolemba Baibulo amene anati ponena za Mulungu: “Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Kaamba ka chifuno chanji? Iye anayankha mwakulongosola Mulungu monga “amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; analiumba akhalemo anthu.”—Yesaya 37:16; 45:18.
Selo Lamoyo Lozizwitsalo
10, 11. Kodi n’chifukwa ninji selo la moyo lili lozizwitsa kwambiri?
10 Bwanji ponena za zinthu zamoyo? Kodi izo sizimafunikira wozipanga? Mwachitsanzo, talingalirani za mipangidwe yozizwitsa ya selo lamoyo. Mu buku lake la Evolution: A Theory in Crisis katswiri wodziŵa zamoyo ndi mpangidwe wake Michael Denton anati: “Ngakhale dongosolo losacholoŵana konse la zamoyo za padziko lapansi lerolino, maselo atizilombo ali zinthu zocholoŵana kopambana. Ngakhale kuti maselo atizilombo tating’onong’ono koposa ali ochepetsetsa kwambiri, . . . lililonse molondola latchedwa fakitale yatochepetsetsa yodzala tamoyo tochulukitsitsa tolinganizidwa pamakina ocholoŵanacholoŵana a molekyula . . . ocholoŵana mopambanitsa kuposa makina alionse opangidwa ndi munthu ndi osayerekezereka konse pakati pa zinthu zopanda moyo.
11 Ponena za malamulo opanga khalidwe m’selo lonse, iye akulongosola kuti: “Kukhoza kwa DNA kwakusunga chidziŵitso kumaposa kwakukulukulu kwadongosolo lililonse lodziŵika; njokhoza kwambiri kotero kuti chidziŵitso chonse chofunika kulekanitsa chinthu chocholoŵana mofanana ndi munthu chimalemera yosakwanira zikwi zingapo za miliyoni za gawo la galamu imodzi. . . . Moyerekezeredwa ndi mlingo wanzeru ndi kucholoŵana kosonyezedwa ndi dongosolo la molekyula yamoyo, ngakhale [zopangidwa] zathu zapamwamba koposa zimawonekera kukhala zosanunkha kanthu. Timakhala osanunkha kanthu.”
12. Kodi n’chiyani chimene wasayansi adanena ponena za magwero a selo?
12 Denton akuwonjezera kuti: “Kucholoŵanacholoŵana kwa selo wamba lodziŵika kuli kwakukulu kwambiri kotero kuti kuli kosatheka kuvomereza kuti chinthu chotero chikanakhoza kudzilumikiza chokha mwadzidzidzi, zosathekadi konse.” Icho chinafunikira kukhala ndi wolinganiza ndi wopanga.
Ubongo Wathu Wochititsa Kakasi
13, 14. Kodi n’chifukwa ninji ubongo ulidi wozizwitsa kwambiri koposa selo la moyo?
13 Kenako wasayansi ameneyu akuti: “Ponena za kucholoŵana, selo lililonse silili kanthu poliyerekezera ndi dongosolo la ubongo wa zolengedwa zoyamwitsa. Ubongo wa munthu uli pafupifupi ndi maselo aminyewa mamiliyoni chikwi. Selo la mnyewa lililonse limatulutsa pafupifupi pakati pa mphote zolunzanitsira mazana khumi ndi zikwi zana limodzi zotumizira mauthenga kumaselo ena amitsempha a muubongo. Chiŵerengero chonse cha milunzo muubongo wa munthu chili pafupifupi . . . mamiliyoni zikwi mamiliyoni.”
14 Denton akupitiriza kuti: “Ngakhale ngati mbali imodzi mwa zana limodzi ya milunzo ya mu ubongo ikanalinganizidwa mwachindunji, imeneyi ikaimirabe dongosolo lokhala ndi milunzo yachindunji yochuluka kopambana koposa m’madongosolo athunthu akukambitsirana a padziko lapansi.” Iye kenako akufunsa kuti: “Kodi mtundu uliwonse wakuchitika wokha kotheratu ukanasonkhanitsa madongosolo otero?” Mwachiwonekere, yankho liyenera kukhala ayi. Ubongo uyenera kukhala unali ndi Wolinganiza ndi Wopanga wodera nkhaŵa.
15. Kodi ndi ndemanga zotani zimene ena anena ponena za ubongo?
15 Ubongo wamunthu umapangitsadi ngakhale makompyutala amakono kuwonekera kukhala achikale. Wolemba sayansi Morton Hunt anati: “Mphamvu zathu zachikumbukiro zogwira ntchito zili ndi chidziŵitso chachikulu kuŵirikiza nthaŵi mabiliyoni angapo kuposa mphamvu yaikulu yachikumbukiro ya kompyutala yofufuzira. Chotero, dokotala wa opaleshoni yaubongo Dr. Robert J. White anati: “Ndasiyidwa wopanda chosankha kusiyapo kuvomereza kukhalako kwa Wanzeru Wamkulu kopambana, amene analinganiza ndi kupanga chigwirizano cha ubongo ndi maganizo chochititsa kakasicho—kanthu kena kosakhoza kuzindikiridwa ndi munthu. . . . Ndifunikira kukhulupirira kuti zonsezi zinali ndi chiyambi cha luntha, kuti Munthu wina anazichititsa kukhalako.” Anafunikiranso kukhala Munthu wina amene amasamala.
Dongosolo la Mwazi Lapaderalo
16-18. (a) Kodi dongosolo lamwazi lili lapadera m’njira zotani? (b) Kodi tikukakamizika kunenanji?
16 Ndiponso, talingalirani, dongosolo la mwazi lapaderalo limene limayendetsa chakudya ndi mpweya ndi kutetezera matenda. Ponena za maselo a mwazi ofiira, mbali yaikulu ya dongosolo limeneli, buku la ABC’s of the Human Body limati: “Dontho limodzi la mwazi lili ndi maselo olekanalekana a mwazi oposa mamiliyoni 250 . . . Mwinamwake thupilo lili nawo mabiliyoni 25, ngati atayalidwa ngokwanira kudzaza mabwalo anayi a tenesi. . . . Oloŵa mmalo amapangidwa, paliŵiro la maselo atsopano mamiliyoni 3 pakamphindi [sekondi] kalikonse.
17 Ponena za maselo oyera a mwazi, mbali ina ya dongosolo la mwazi yapadera, buku limodzimodzili likutiuza kuti: “Pamene kuli kwakuti pali mtundu umodzi wokha wa selo lofiira, maselo amwazi oyera n’ngamitundumitundu, mtundu uliwonse uli ndi kukhoza kumenya nkhondo zathupi m’njira yosiyana. Mwachitsanzo, mtundu wina, umawononga maselo akufa. Mtundu wina umatulutsa mankhwala akupha tizilombo, kusukulutsa mphamvu yakupha ya zinthu zachilendo, kapena kwenikweni kumeza ndi kupukusa tizilombo.
18 Ndi dongosolo lolinganizidwa modabwitsa kwambiri ndi locholoŵana chotani nanga! Ndithudi chinthu chilichonse cholumikizidwa bwino lomwe chotero ndi chotetezera bwino lomwe kotheratu motero chiyenera kukhala ndi wolinganiza waluntha kwambiri ndi wosamalira—Mulungu.
Zozizwitsa Zina
19. Kodi diso n’lotani poliyerekezera ndi makina opangidwa ndi anthu?
19 Pali zozizwitsa zina zambiri m’thupi la munthu. Chimodzi ndicho diso, n’lolinganizidwa mwapamwamba kwambiri kotero kuti palibe kamera imene ingalitsanzire. Katswiri wa za mlengalenga Robert Jastrow anati: “Diso likuwonekera kukhala litalinganizidwa; palibe wolinganiza wa telesikopu akanachita bwino kuposa apa.” Ndipo buku lakuti Popular Photography limasimba kuti: “Maso a munthu amawona mipangidwe yochuluka kwambiri yachidziŵitso kuposa filimu. Amawona m’mbali zitatu, pamlingo waukulu kwambiri, mosalakwitsa, m’kuyenda kosadukiza . . . Sikuli koyenera kuyerekezera kamera ndi diso la munthu. Diso la munthu lili kwakukulukulu lofanana ndi kompyutala yapamwamba ndi yocholoŵana kopambana yokhala ndi luntha lochita kupangidwa, maluso akuloŵetsa chidziŵitso, liŵiro, ndi mipangidwe yakugwira ntchito zimene zili zapamwamba kuposa makina aliwonse opangidwa ndi munthu, kompyutala kapena kamera.”
20. Kodi n’ziti zimene zili mbali zina zozizwitsa za thupi la munthu?
20 Ndiponso, talingalirani, mmene ziŵalo zonse zathupi zocholoŵana zimagwirira ntchito mogwirizana popanda kuyesayesa kwathu kwamphamvu. Mwachitsanzo, timaika mitundu yosiyanasiyana ya chakudya ndi zakumwa m’mimba zathu, komabe thupi limazipukusa ndi kutulutsa nyonga. Yesani kuika zinthu zosiyanasiyana zimenezi m’thanki la petro wa galimoto ndi kuwona mmene zimazimiririkira mofulumira! Ndiyeno pali chozizwitsa chakubala, kutulutsidwa kwa khanda lokongola—lofanana ndendende ndi makolo ake—m’miyezi isanu ndi inayi yokha. Ndipo bwanji za luso la mwana wa zaka zoŵerengeka zokha zakubadwa la kuphunzira kulankhula chinenero chocholoŵana?
21. Polingalira zodabwitsa za thupi la munthu, kodi anthu aluntha akunenanji?
21 Inde, chiŵerengero chachikulu cha zolengedwa zodabwitsa ndi zocholoŵana m’thupi la munthu chimatichititsa mantha. Palibe injiniya amene angatsanzire zinthu zimenezo. Kodi zimenezo zingakhale ntchito wamba zongochitika zokha? Kutalitali. Mmalomwake, polingalira mbali zonse zodabwitsa za thupi la munthu, anthu anzeru amanena monga momwe anachitira wamasalmo kuti: “Ndikuyamikani [Mulungu] chifukwa kuti chipangidwe changa n’chowopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa.”—Salmo 139:14.
Mmisili Womanga Wapamwamba
22, 23. (a) Kodi n’chifukwa ninji tiyenera kuvomereza kukhalapo kwa Mlengi? (b) Kodi Baibulo molondola limanenanji ponena za Mulungu?
22 Baibulo limafotokoza kuti: “Ndithudi, nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu; koma Mulungu anamanga chinthu chilichonse chimene chiliko.” (Ahebri 3:4, The Jerusalem Bible) Popeza kuti nyumba iliyonse, mulimonse mmene ingakhalire yosacholoŵana, iyenera kukhala ndi woimanga, pamenepo chilengedwe chonse chocholoŵana kwambiricho limodzi ndi zamoyo zamitundumitundu padziko lapansi ziyeneranso kukhala ndi womanga. Ndipo popeza kuti tikuvomereza kukhalapo kwa anthu amene anatulukira makina onga ndege, mawailesi akanema, ndi makompyutala, kodi sitiyeneranso kuvomereza kukhalako kwa Uyo amene anapatsa anthu ubongo wakupanga zinthu zotero?
23 Baibulo limatero, likumamtcha “Mulungu [wowona] Yehova . . . amene analenga thambo nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m’menemo, iye amene amapatsa anthu a m’menemo mpweya.” (Yesaya 42:5) Molondola Baibulo limati: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemelero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa munalenga zonse ndipo mwachifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”—Chivumbulutso 4:11.
24. Kodi tingadziŵe bwanji kuti Mulungu aliko?
24 Inde, tingathe kuzindikira kuti Mulungu aliko mwazinthu zimene analenga. “Pakuti mikhalidwe [ya Mulungu] yosawoneka ikuwoneka bwino lomwe kuyambira pa kulengedwa kwa dziko kumka mtsogolo, chifukwa chakuti iyo ikuzindikiridwa ndi zinthu zopangidwa [ndi Mulungu].”—Aroma 1:20.
25, 26. Kodi n’chifukwa ninji kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa chinthu sikungakhale chigomeko chotsutsira kukhala kwake ndi wochipanga?
25 Chenicheni chakuti chinthu chopangidwa chikugwiritsidwa ntchito molakwa sichimatanthauza kuti chilibe wochipanga. Ndege ingagwiritsidwe ntchito kaamba ka zifuno za mtendere, monga yonyamula anthu. Koma ingathe kugwiritsidwanso ntchito kuwononga, monga yoponya mabomba. Kugwiritsidwa ntchito kwake mwanjira yakupha sikumatanthauza kuti inalibe woipanga.
26 Mofananamo, chenicheni chakuti anthu kaŵirikaŵiri aipa sichimatanthauza kuti iwo analibe Wowapanga, kuti kulibe Mulungu. Chifukwa chake, Baibulo molondola limati: “Ozolitsa inu! Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi chinthu chopangidwa chinganene za iye amene anachipanga, iye sanandipange ine konse; kapena kodi chinthu choumbidwa chinganene za iye amene anachiumba, iye alibe nzeru?”—Yesaya 29:16.
27. Kodi n’chifukwa ninji tingayembekezere Mulungu kuyankha mafunso athu onena za kuvutika?
27 Mlengiyo wasonyeza nzeru zake mwa kucholoŵanacholoŵana kozizwitsa kwa zimene wapanga. Iye wasonyeza kuti amatisamaliradi mwakupanga dziko lapansi kukhala loyenereradi kukhalapo ndi moyo, mwakupanga matupi athu ndi maganizo mwanjira yodabwitsa kwambiri chotero, ndi mwakupanga zinthu zabwino zochuluka kuti ife tisangalale nazo. Ndithudi iye akasonyeza nzeru imodzimodziyo ndi kusamalira mwakupereka mayankho amafunso onga akuti: Kodi n’chifukwa ninji Mulungu walola kuvutika? Kodi iye adzachitaponji?
[Chithunzi patsamba 5]
Dziko lapansi, ndi mpweya wake wotetezera, lili malo okhala apadera amene Mulungu wosamala anatilinganizira
[Chithunzi patsamba 6]
Dziko lapansi linapangidwa mwachisamaliro chachikondi kuti ife tisangalale ndi moyo mokwanira
[Chithunzi patsamba 7]
‘Ubongo umodzi uli ndi milunzo yochuluka kuposa nsambo za dongosolo lonse lakukambitsirana la dziko lapansi.’—Katswiri wodziŵa zamoyo ndi mpangidwe wake
[Chithunzi patsamba 8]
“Diso limawonekera kukhala litalinganizidwa; palibe wolinganiza matelesikopu akanachita bwino kuposa apa.”—Katswiri wa za mlengalenga