Mungapirire Kufika Kuchimaliziro
“Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.”—AHEBRI 12:1.
1, 2. Kodi kupirira kumatanthauzanji?
“CHIKUSOŴANI chipiriro,” analemba motero mtumwi Paulo kwa Akristu achihebri a m’zaka za zana loyamba. (Ahebri 10:36) Pogogomezera kufunika kwa mkhalidwe umenewu, mtumwi Petro nayenso analimbikitsa Akristu kuti: “Muwonjezerapo . . . pachikhulupiriro chanu, chipiriro.” (2 Petro 1:5, 6) Koma kodi chipiriro n’chiyani kwenikweni?
2 Buku lomasulira Chigiriki m’Chingelezi limamasulira mneni wachigiriki wotanthauza “pirira” kukhala “kusathaŵa . . . kuima nji, kusagonja.” Ponena za dzina la m’Chigiriki lotembenuzidwa kuti “chipiriro,” buku lina limati: “Ndi mzimu umene ungapirire zinthu, osati chifukwa cha kugonja, koma ndi chiyembekezo chotsimikizika . . . Ndi mkhalidwe umene umalimbitsa munthu kuti asafooke pokumana ndi mavuto. Ndi mkhalidwe wabwino umene ungasinthe chiyeso choŵaŵa zedi kukhala ulemerero chifukwa umaona zabwino zimene zidzatsatira zopwetekazo.” Chotero, chipiriro chimapangitsa munthu kukhala wolimba pokumana ndi zopinga ndi mavuto kutinso asataye chiyembekezo. Kodi ndani kwenikweni amene amafunikira mkhalidwe umenewu?
3, 4. (a) Kodi ndani ayenera kupirira? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupirira mpaka titafika kuchimaliziro?
3 Akristu onse ali pampikisano wothamanga wophiphiritsa umene umafuna chipiriro. Cha mu 65 C.E., mtumwi Paulo analembera wantchito mnzake ndi woyenda naye maulendo wokhulupirikayo Timoteo mawu otsimikizaŵa: “Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza [“ndathamanga mpaka ndamaliza,” NW] njirayo, ndasunga chikhulupiriro.” (2 Timoteo 4:7) Ponena mawu akuti “ndathamanga mpaka ndamaliza njirayo,” Paulo anali kuyerekeza moyo wake monga Mkristu ndi mpikisano wothamanga, wokhala ndi njira yake ndi polekezera. Panthaŵi imeneyo, Paulo anali kuyandikira mapeto a kuthamanga kwakeko mwachipambano, ndipo motsimikiza mtima anali kuyembekeza kulandira mphotho. Iye anapitiriza kuti: “Chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo.” (2 Timoteo 4:8) Paulo anali wotsimikiza kuti adzalandira mphotho chifukwa anapirira mpaka chimaliziro. Bwanji ponena za enafe?
4 Pofuna kulimbikitsa awo amene aloŵa nawo pamakani othamanga ameneŵa, Paulo analemba kuti: “Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” (Ahebri 12:1) Monga Akristu, timaloŵa nawo paliŵiro lachipiriro limeneli tikadzipatulira kwa Yehova Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu. Chiyambi chabwino panjira ya kukhala wophunzira n’chofunika, koma chofunika kwambiri ndicho kuti timalize njirayo. Yesu anati: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Mphotho imene omaliza bwino kuthamangako adzalandira ndiyo moyo wosatha! Chotero, pokhala tili ndi cholinga mumtima, tiyenera kupirira mpaka titafika kuchimaliziro. Kodi n’chiyani chidzatithandiza kukwaniritsa cholinga chimenecho?
Zakudya Zabwino N’zofunika Kwambiri
5, 6. (a) Kuti tipirire pampikisano wothamangira moyo, kodi tiyenera kusamala chiyani? (b) Ndi zogaŵira zauzimu ziti zimene tiyenera kugwiritsa ntchito, ndipo n’chifukwa chiyani?
5 Pafupi ndi mzinda wa Korinto, ku Girisi, panali malo kumene kunkachitikira maseŵero otchuka a Isthmian. Mosakayikira Paulo anali kudziŵa kuti abale a ku Korinto anali kudziŵa za mpikisano wa maseŵero osiyanasiyana ndi mipikisano ina imene inkachitikira kumeneko. Pogwiritsa ntchito zomwe iwo ankadziŵa kale, anaŵakumbutsa za mpikisano wothamangira moyo umene iwo analimo kuti: “Simudziŵa kuti pampikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti n’kukalandira mphothoyo.” Paulo anagogomezera kufunika kwa kusatuluka mumpikisanowo ndi kuthamangabe mpaka mapeto. Koma kodi n’chiyani chikanawathandiza kuchita zimenezo? “Aliyense wothamanga pampikisano wa liŵiro amadziletsa pazonse,” anawonjezera motero. Inde, opikisana m’maseŵero akalewo ankachita maseŵero olimbitsa thupi oŵaŵa, anali kusamala kwambiri zimene anali kudya ndi kumwa, ndipo ankasamala zochita zawo zonse kuti apambane.—1 Akorinto 9:24, 25, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.
6 Nangano bwanji za mpikisano wa liŵiro umene Akristu aloŵamo? “Muyenera kusamala zakudya zanu zauzimu ngati mukufuna kupirira pampikisano wothamangira moyo,” anatero mkulu wina mumpingo wa Mboni za Yehova. Talingalirani za chakudya chauzimu chimene Yehova, “Mulungu wa chipiriro,” watipatsa. (Aroma 15:5) Gwero lathu lalikulu la chakudya chauzimu ndiwo Mawu ake, Baibulo. Kodi sitiyenera kukhala ndi pologalamu yabwino yoŵerenga Baibulo? Kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” Yehova waperekanso magazini a panthaŵi yake amenewo a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi zofalitsa zina zofotokoza Baibulo. (Mateyu 24:45) Kuziphunzira mwakhama zimenezi kudzatilimbitsa mwauzimu. Inde, tiyenera kupeza nthaŵi—‘kuchita machaŵi’—kuti tichite phunziro laumwini.—Aefeso 5:16.
7. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhutira ndi kungodziŵa ziphunzitso zachikristu zoyambirira? (b) Kodi ndi motani mmene ‘tingapitirire kutsata ukulu msinkhu’?
7 Kuti tisachoke panjira ya kukhala wophunzira wachikristu, tifunikira kudziŵa zowonjezereka zoposa “mawu a chiyambidwe” ndipo tiyenera ‘kupitirira kutsata ukulu msinkhu.’ (Ahebri 6:1) Chotero tiyenera kukhala ndi chidwi chofuna kudziŵa “kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama” kwa choonadi ndi kupindula ndi “chakudya chotafuna [chimene] chili cha anthu akulu misinkhu.” (Aefeso 3:18, 19; Ahebri 5:12-14) Tiyeni mwachitsanzo titenge nkhani zodalirikazo zosimba moyo wa Yesu wa padziko lapansi—Mauthenga Abwino a Mateyu, Marko, Luka, ndi Yohane. Mwa kuphunzira mwakhama Mauthenga Abwino ameneŵa, tidzadziŵa zinthu zimene Yesu anachita ndi mtundu wa munthu amene iye anali ndipo tidzazindikiranso malingaliro amene anam’sonkhezera kuchita zinthu zimenezo. Kenako tingakhale ndi “mtima wa Kristu.”—1 Akorinto 2:16.
8. Kodi misonkhano yachikristu imatithandiza motani kupirira pampikisano wothamangira moyo?
8 Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Inde, misonkhano yachikristu imakhalatu yolimbikitsa zedi! Komanso n’kotsitsimula kwabasi kukhala pamodzi ndi abale ndi alongo achikondi amene amasamala za ife ndiponso amafuna kutithandiza kupirira kufika kuchimaliziro! Sitingayerekeze n’komwe kupeputsa chogaŵira chachikondi cha Yehova chimenechi. Mwa kuchita phunziro laumwini mwakhama ndi kusonkhana mosadumphadumpha, tiyeni tikhale ‘akulu misinkhu m’chidziŵitso.’—1 Akorinto 14:20.
Oonerera Okulimbikitsani
9, 10. (a) Kodi oonerera angakhale motani gwero lachilimbikitso paliŵiro la kupirira? (b) Kodi ‘mtambo waukulu wa mboni wotizinga’ wotchulidwa pa Ahebri 12:1 n’chiyani?
9 Kaya wothamangayo akhale wokonzekera chotani, zinthu zitha kuchitika panjira zimene zingam’sokoneze. “Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi?” anafunsa motero Paulo. (Agalatiya 5:7) Zikuoneka kuti Akristu ena a ku Galatiya anayamba kukhala ndi mayanjano oipa ndipo, chotsatirapo chake, anasokonezeka pampikisano wawo wothamangira moyo. Komabe, chichirikizo ndi chilimbikitso cha ena zingatipangitse kupirira mosavuta pampikisanowu. Zimenezo n’zofanana kwambiri ndi chisonkhezero chimene oonerera maseŵero amakhala nacho pa ochita maseŵerowo. Chinamtindi cha anthu ochemerera chimasonkhezera opikisanawo moti amalimbikira kuchokera pachiyambi mpaka kumapeto. Kuchemerera kwa oonerera, kumene nthaŵi zambiri amachita akumaimbanso nyimbo mofuula ndi kuomba m’manja, kungapatse opikisanawo mphamvu yapadera imene amafunikira akamayandikira kumapeto. Ndithudi, oonerera olimbikitsa angapatsedi nyonga ochita mpikisano wa liŵiro.
10 Mumpikisano wothamangira moyo umene Akristu aloŵamo, kodi oonerera ndani? Atalongosola mboni za Yehova za m’nthaŵi yoyambirira kusanakhale Chikristu, monga momwe zilili mu chaputala 11 cha Ahebri, Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, . . . tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” (Ahebri 12:1) Pogwiritsa ntchito phiphiritso la mtambo, Paulo sanagwiritse ntchito mawu achigiriki otanthauza mtambo weniweni wokhala ndi ukulu ndi malire oonekera bwino iyayi. M’malo mwake, iye anagwiritsa ntchito mawu amene malinga ndi kunena kwa mkonzi wa dikishonale W. E. Vine “amatanthauza chigulu cha zinthu chooneka ngati mtambo kuthambo, chosadziŵika bwino ukulu wake.” Ndithudi, Paulo anali kuganizira za khamu lalikulu la mboni—mboni zambirimbiri moti zinali ngati mtambo.
11, 12. (a) Kodi mboni zomwe zinaliko kusanakhale Chikristu zingatichemerere motani, titero kunena kwake, kuti tipitirize kuthamanga ndi chipiriro? (b) Kodi tingapindule kwambiri motani ndi ‘mtambo waukulu wa mboni’?
11 Kodi mboni zomwe zinaliko kusanakhale Chikristu zingakhale oonerera enieni amakono? Kutalitali. Onse anagona mu imfa, kuyembekeza chiukiriro. Komabe, iwowo anathamanga mwachipambano pamene anali amoyo, ndipo zitsanzo zawo n’zamoyobe m’masamba a m’Baibulo. Pamene tiphunzira Malemba, tingawakumbukire bwino lomwe anthu okhulupirika ameneŵa ndipo angatichemerere, titero kunena kwake, kuti tithamange kufika kuchimaliziro.—Aroma 15:4.a
12 Mwachitsanzo, ngati mwayi wakudziko winawake watiika pachiyeso, kodi kusinkhasinkha za mmene Mose anakanira ulemerero wa Igupto sikungatilimbikitse kukhalabe panjira yabwino? Ngati takumana ndi chiyeso choŵaŵa, kukumbukira chiyeso chachikulu chimene Abrahamu anakumana nacho pamene anapemphedwa kupereka mwana wake Isake nsembe kudzatilimbikitsadi kuti tisatope pampikisano wathu wa chikhulupiriro. Chisonkhezero chimene ‘mtambo waukulu’ wa mboni umatipatsa m’njira imeneyo chimadalira pa mmene timazionera bwino mbonizo ndi maso athu a kuzindikira.
13. Kodi ndi motani mmene Mboni za Yehova zamakono zingatipatsire nyonga pampikisano wothamangira moyo?
13 Tazingidwanso ndi Mboni za Yehova zambiri zedi m’nthaŵi zamakonozi. Akristu odzozedwa limodzinso ndi amuna ndi akazi a mu “khamu lalikulu” ameneŵa apereka zitsanzo zachikhulupiriro zokongola kwabasi! (Chivumbulutso 7:9) Nthaŵi ndi nthaŵi tingaŵerenge nkhani zosimba za moyo wawo m’magazini ino ndi m’zofalitsa zina za Watch Tower.b Pamene tisinkhasinkha za chikhulupiriro chawo, timalimbikitsidwa kuti tipirire mpaka kuchimaliziro. Ndipo n’zosangalatsatu kwambiri kuchirikizidwa ndi mabwenzi apamtima ndi achibale athu amenenso akutumikira Yehova mokhulupirika! Inde, tili ndi anthu ambiri amene angatipatse nyonga pampikisano wothamangira moyo.
Thamangani Paliŵiro Labwino
14, 15. (a) N’chifukwa chiyani kuthamanga paliŵiro labwino kuli kofunika kwa ife? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuika zolinga zathu mofatsa?
14 Pothamanga mtunda wautali, wothamangayo ayenera kuyamba ndi liŵiro labwino. “Kungoyamba ndi liŵiro la mtondo wadooka kungakupangitseni kuti mulephere,” inatero magazini yotchedwa New York Runner. “Chimene chingachitike n’chakuti mungavutike kwadzaoneni kuti mumalize makilomita angapo omalizira mwinanso mutha kungolephereratu.” Winawake wochita nawo mpikisano wothamanga pa mtunda wautali anakumbukira kuti: “Wochititsa msonkhano umene ndinakapezekapo pokonzekera mpikisanowu anachenjeza mosapita m’mbali kuti: ‘Musalimbane ndi othamanga a liŵiro la mtima bi. Thamangani paliŵiro lanu. Apo ayi mudzatopa ndipo mwina mungalephere kumaliza.’ Kulabadira malangizo ameneŵa kunandithandiza kumaliza mtunda wonse.”
15 Pampikisano wothamangira moyo, atumiki a Mulungu ayenera kuyesetsa mwamphamvu. (Luka 13:24) Komabe, wophunzira Yakobo analemba kuti: “Nzeru zochokera Kumwamba [ndi] . . . zofatsa.” (Yakobo 3:17, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Pamene kuli kwakuti zitsanzo zabwino za ena zingatilimbikitse kuchita zambiri, kufatsa kudzatithandiza kuika zolinga zofikirika malinga ndi zimene tingathe kuchita ndiponso mkhalidwe wathu. Malemba amatikumbutsa kuti: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina. Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.”—Agalatiya 6:4, 5.
16. Kodi kudzichepetsa kumatithandiza motani kuthamanga paliŵiro labwino?
16 Pa Mika 6:8, tikufunsidwapo funso lofika pamtima ili: “Yehova afunanji nawe koma . . . kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” Kudzichepetsa kumaphatikizapo kuzindikira zinthu zimene sitingathe kuchita. Kodi thanzi lovuta kapena ukalamba zatipangitsa kuti tisamathe kuchita zinthu zina muutumiki wa Mulungu? Tisakhumudwe. Yehova amalandira zoyesayesa zathu ndi kudzimana kwathu ‘monga momwe tili nazo, si monga tilibe.’—2 Akorinto 8:12; yerekezani ndi Luka 21:1-4.
Sumikani Maso Anu Pamphotho
17, 18. Kodi ndi kuyang’anabe pachiyani kumene kunathandiza Yesu kupirira pa mtengo wozunzirapo?
17 Posonyeza Akristu a ku Korinto kufunika kwa kupirira pampikisano wothamangira moyo, Paulo anatchula chochitika chinanso cha pamaseŵero a Isthmian chimene iwo anayenera kuchiganizira. Ponena za opikisana pamaseŵero amenewo, Paulo analemba kuti: “Ndipo iwoŵa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda. Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga.” (1 Akorinto 9:25, 26) Mphotho ya wopambana pamaseŵero amenewo inali korona, kapena chisoti, zopangidwa ndi masamba a mkungudza kapena zomera zina, mwinanso ngakhale udzu wouma wokhala ngati makaroti—‘koronadi wakuvunda.’ Koma tsono Akristu amene adzapirira kufika kuchimaliziro adzalandira chiyani?
18 Ponena za Chitsanzo chathu, Yesu Kristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda [“mtengo wozunzirapo,” NW], nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” (Ahebri 12:2) Yesu anapirira kufika kuchimaliziro cha moyo wake monga munthu wa padziko lapansi mwa kuyang’ana kutsogolo, mopyola pamtengo wozunzirapo, komwe kunali mphotho yake, imene ikuphatikizapo ntchito yosangalatsa imene ali nayo yothandizira kuyeretsa dzina la Yehova, kuwombola mtundu wa anthu ku imfa, ndi kulamulira monga Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe pamene abwezeretsa anthu omvera kumoyo wosatha padziko lapansi la paradaiso.—Mateyu 6:9, 10; 20:28; Ahebri 7:23-26.
19. Kodi tiyenera kumaganizirabe chiyani pamene tilondola njira ya kukhala wophunzira wachikristu?
19 Talingalirani chimwemwe chimene chili patsogolo pathu pamene tilondola njira ya kukhala wophunzira wachikristu. Yehova watipatsa ntchito yokhutiritsa kwambiri yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi yopatsa ena chidziŵitso cha m’Baibulo chopulumutsa moyo. (Mateyu 28:19, 20) Mmenetu zimapatsira chimwemwe kupeza munthu wofuna kuphunzira za Mulungu woona ndi kum’thandiza woteroyo kuti aloŵe mumpikisano wothamangira moyo! Ndipo mosasamala kanthu kuti amene tikuwalalikirawo akumvetsera kapena ayi, uli mwayi kutengamo mbali m’ntchito yokhudzana ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova. Pamene tipirira muutumiki mosasamala kanthu za kusoŵa chidwi kapena kutsutsa kwa anthu a m’gawo lathu lolalikiramo, timasangalala kuti tikukondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Ndiponso mphotho yaikulu imene akutilonjeza ndiwo moyo wosatha. Idzakhalatu mphotho yosangalatsa bwanji! Tiyenera kumaganizirabe madalitso ameneŵa ndi kulimbikirabe paliŵiro limeneli.
Pamene Chimaliziro Chikuyandikira
20. Kodi mpikisano wothamangira moyo ungakhale wovuta motani pamene ukuyandikira mapeto ake?
20 Mumpikisano wothamangira moyo, tifunikira kulimbana ndi mdani wathu wamkulu, Satana Mdyerekezi. Pamene tikuyandikira chimaliziro, akuyesetsa mwamphamphu kutipinga kapena kutipangitsa kuti tichepetse liŵiro. (Chivumbulutso 12:12, 17) Ndipo n’zovuta kupitirizabe kukhala olengeza Ufumu okhulupirika ndi odzipatulira chifukwa cha nkhondo, njala, miliri, ndi mavuto ena onse amene ali chizindikiro cha “nthaŵi ya chimaliziro.” (Danieli 12:4; Mateyu 24:3-14; Luka 21:11; 2 Timoteo 3:1-5) Komanso, chimaliziro chingaoneke ngati kuti chili kutali kwambiri kusiyana ndi mmene tinkaganizira, makamaka ngati tinaloŵa mumpikisanowu zaka zambirimbiri kalelo. Komabe, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti chimalizirocho chidzafika. Yehova akuti sichidzazengereza. Chimalizirocho chili pafupi kwenikweni.—Habakuku 2:3; 2 Petro 3:9, 10.
21. (a) Kodi n’chiyani chidzatilimbitsa pamene tipiritizabe kuthamanga mumpikisano wothamangira moyo? (b) Kodi tiyenera kutsimikiza mtima ponena za chiyani pamene chimaliziro chiyandikira?
21 Ndiye kuti ngati tikufuna kupambana pampikisano wothamangira moyo, tiyenera kupeza mphamvu pachakudya chauzimu chimene Yehova wapereka mwachikondi. Tifunikiranso chilimbikitso chonse chimene tingapeze mwa kuyanjana ndi okhulupirira anzathu nthaŵi zonse, amenenso akuthamanga mumpikisanowu. Ngakhale chizunzo choopsa ndi zochitika zotigwera zitapangitsa kuthamanga kwathu kukhala kovuta kwambiri, tingapirire kufika kuchimaliziro chifukwa chakuti Yehova amapereka “ukulu woposa wamphamvu.” (2 Akorinto 4:7) N’zolimbikitsatu kwambiri kudziŵa kuti Yehova akufuna kuti timalize makani a liŵiro ameneŵa mwachipambano! Motsimikizadi mtima, “tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira,” tikudziŵa pansi pa mtima kuti “panyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”—Ahebri 12:1; Agalatiya 6:9.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mukufuna nkhani yolongosola Ahebri 11:1–12:3, onani Nsanja ya Olonda, January 15, 1987, masamba 10-20.
b Zitsanzo zina zaposachedwapa za nkhani zolimbikitsa zimenezi zingapezeke mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1998, masamba 28-31; September 1, 1998, masamba 24-8; February 1, 1999, masamba 25-9.
Kodi Mukukumbukira?
◻ N’chifukwa chiyani tiyenera kupirira kufika kuchimaliziro?
◻ Kodi ndi zogaŵira ziti za Yehova zimene sitiyenera kunyalanyaza?
◻ N’chifukwa chiyani kuthamanga paliŵiro labwino kuli kofunika kwa ife?
◻ Kodi patsogolo pathu paikidwa chimwemwe chotani pamene tipitirizabe kuthamanga?
[Chithunzi patsamba 18]
Pezani chilimbikitso pamisonkhano yachikristu