Kuthamanga Makaniwo Mwachipiriro
‘Tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.’—AHEBRI 12:1.
1. (a) Kodi nchiyani chimene chimaikidwa patsogolo pathu pamene tidzipereka kwa Yehova Mulungu? (b) Kodi ndimakani a mtundu wanji amene Mkristu ayenera kukonzekera?
PAMENE tinadzipereka kwa Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu, Mulungu anatiikira makani, kunena mophiphiritsa. Pamapeto a makaniwo, mphotho idzaperekedwa kwa onse omaliza mwachipambano. Kodi ndimphotho yotani? Moyo wosatha! Kuti apate mphotho yopambana imeneyi, wothamanga Wachikristu afunikira kukhala wokonzekera, osati kaamba ka kuthamanga mofulimira pamtunda waufupi, koma kuthamanga kwa mtunda wautali. Chotero iye adzafunikira chipiriro. Adzafunikira kupirira zonse ziŵiri kutalika kwa makaniwo ndi zopinga zimene zidzapezeka m’makaniwo.
2, 3. (a) Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kuthamanga makani Achikristu mpaka kumapeto? (b) Kodi ndimotani mmene chimwemwe chinathandizira Yesu kuthamanga makaniwo ndi chipiriro?
2 Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kuthamanga makaniwo kufika kumapeto? Eya, kodi nchiyani chimene chinathandiza Yesu kupirira pamene anali munthu padziko lapansi? Iye anapeza nyonga yamkati kuchokera ku mkhalidwe wachimwemwe. Ahebri 12:1-3 amati: ‘Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chirichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. Pakuti talingirirani iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotero, kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.’
3 Muuminisitala wake wonse wapoyera, Yesu anali wokhoza kuthamangabe makaniwo chifukwa cha chimwemwe cha Yehova. (Yerekezerani ndi Nehemiya 8:10.) Chimwemwe chake chinamthandiza kupirira ngakhale imfa yodzetsa chitonzo pa mtengo wozunzirapo, ndipo pambuyo pake anakhala ndi chimwemwe chosaneneka cha kuuka kwa akufa ndi kukwera kudzanja lamanja la Atate wake, kukafikitsa kumapeto ntchito ya Mulungu. Mwachipiriro chake monga mwamuna wokhala kumbali ya Mulungu, iye anakhalabe ndi kuyenerera kwake kwa moyo wosatha. Inde, monga momwe Luka 21:19 amanenera kuti: ‘Mudzakhala nawo moyo wanu m’chipiriro.’
4. Kodi nchitsanzo chotani chimene Yesu anakhazikitsira othamanga anzake, ndipo kodi tiyenera kusumika maganizo athu pachiyani?
4 Yesu Kristu anakhazikitsa chitsanzo chabwino koposa kwa othamanga anzake, ndipo chitsanzo chake chimatitsimikizira kuti nafenso tikhoza kupambana. (1 Petro 2:21) Chimene Yesu atipempha kuchita, tikhoza kuchita. Monga momwe anapiririra, tikhoza kuteronso. Ndipo pamene tigwiritsa mochirimika kutsanzira iye, tiyenera kusumika maganizo athu pa zifukwa zathu zokhalira achimwemwe. (Yohane 15:11, 20, 21) Chimwemwe chidzatilimbikitsa kupirira m’kuthamanga makaniwo muutumiki wa Yehova kufikira pamene tidzapata mphotho ya ulemerero ya moyo wosatha.—Akolose 1:10, 11.
5. Kodi ndimotani mmene tingakhalire ndi chimwemwe ndi kulimbitsidwa kaamba ka makani amene taikiridwa?
5 Kutithandiza kupitiriza m’makaniwo, Yehova amapereka nyonga yoposa yaumunthu. Pamene tizunzidwa, nyongayo ndi kudziŵa chifukwa chimene tapatsidwira mwaŵi wakuzunzidwa zimatilimbitsa. (2 Akorinto 4:7-9) Chirichonse chimene tingavutike nacho pachifukwa cha kulemekeza dzina la Mulungu ndi kukweza uchifumu wake chiyenera kutipatsa chimwemwe chimene palibe amene angatilande. (Yohane 16:22) Ichi chimapereka chifukwa chimene atumwi, pambuyo pokwapulidwa molamulidwa ndi Bungwe la Akulu Lachiyuda chifukwa chopereka umboni wa zinthu zozizwitsa zimene Yehova Mulungu anakwaniritsa mwa Yesu, anakondwera ‘kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.’ (Machitidwe 5:41, 42) Chimwemwe chawo sichinachokere m’chizunzo chenichenicho koma m’chikhutiro chamkati chakudziŵa kuti anali kukondweretsa Yehova ndi Yesu.
6, 7. Kodi nchifukwa ninji wothamanga Wachikristu angasangalale ngakhale pamene ali m’masautso, ndipo ndi chotulukapo chotani?
6 Nyonga ina yochirikiza m’miyoyo yathu ndiyo chiyembekezo chimene Mulungu watiikira patsogolo pathu. Monga momwe Paulo ananenera: ‘Tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu; amene ife tikhoza kuloŵa naye ndi chikhulupiriro m’chisomo ichi m’mene tirikuimamo; ndipo tikondwera m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. Ndipo sichotero chokha, komanso tikondwera m’zisautso; podziŵa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizoloŵezi; ndi chizoloŵezi chichita chiyembekezo: Ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi.’—Aroma 5:1-5.
7 Masautso mwa iwo okha siokondweretsa, koma zipatso zamtendere zimene zimatulukapo pambuyo pake. Zipatso zimenezi ndizo chipiriro, mkhalidwe wovomerezedwa, chiyembekezo, ndi kukwaniritsidwa kwa chiyembekezocho. Chipiriro chathu chidzatibweretsera chivomerezo chaumulungu. Pamene tikhala ndi chivomerezo cha Mulungu, tikhoza kuyembekezera mwachidaliro kukwaniritsidwa kwa malonjezo amene iye wawapanga. Chiyembekezochi chimatisunga pa njira yoyenera ndi kutilimbikitsa pansi pa chisautso kufikira pamene chiyembekezocho chikwaniritsidwa.—2 Akorinto 4:16-18.
Achimwemwe Ali Awo Amene Apirira!
8. Kodi nchifukwa ninji nyengo yoyembekezera imeneyi siiri kutaya nthaŵi kwa ife?
8 Pamene tikuyembekezera nthaŵi yoikidwa mwaumulungu yakugaŵira mphotho kwa othamangawo, pali masinthidwe amene tikukumana nawo. Ameneŵa ndiwo kuwongokera kwathu kwauzimu kumene kumatulukapo pamene tiyang’anizana ndi mayesero mwachipambano, ndipo iko kumatipezetsa chiyanjo chachikulu cha Mulungu. Kumatsimikizira amene ife tiri ndipo kumatipatsa mwaŵi wakusonyeza mikhalidwe yabwino yofananayo imene okhulupirika a m’nthaŵi yakale, makamaka Chitsanzo chathu, Yesu Kristu, anasonyeza. Wophunzira Yakobo amanena kuti: ‘Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero a mitundu mitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chirema, osasowa kanthu konse.’ (Yakobo 1:2-4) Inde, tingayembekezere kukhala ndi mayesero osiyanasiyana, koma iwo adzatithandiza kukulitsabe mikhalidwe yoyenera. Mwakutero timasonyeza kuti tidzathamangabe m’makaniŵa kufikira pamene tidzapata mphothoyo, mosasamala kanthu za zopinga zimene tikumana nazo.
9, 10. (a) Kodi nchifukwa ninji awo amene amapirira mayesero ali achimwemwe, ndipo kodi tiyenera kuyang’anizana motani ndi mayesero? (b) Kodi ndani anali achimwemwe akale, ndipo kodi tingaphatikizidwe motani pakati pawo?
9 Pamenepa, nzosadabwitsa kuti Yakobo anati: ‘Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda iye’! (Yakobo 1:12) Tiyeni tilimbane nawo mayesero mosalekeza, pokhala okonzekeretsedwa ndi mikhalidwe yaumulungu imene idzatilimbitsa kuwalaka.—2 Petro 1:5-8.
10 Kumbukirani kuti njira imene Mulungu akuchitira nafe siyatsopano kapena yachilendo. “Mtambo . . . wa mboni” zokhulupirika za m’nthaŵi zakale zinachitidwa mwanjira yofananayo pamene zinatsimikizira kumamatira kwawo kwa Mulungu. (Ahebri 12:1) Chivomerezo cha Mulungu pa iwo chinalembedwa m’Mawu ake, ndipo tiwayesa onse kukhala achimwemwe chifukwa chakuti anapitirizabe m’chiyeso. Yakobo anati: ‘Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zoŵaŵa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la [Yehova, NW]. Tawonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwawona chitsiriziro cha [Yehova, NW], kuti [Yehova, NW] ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.’ (Yakobo 5:10, 11) Kunanenedweratu kuti mkati mwa masiku otsiriza ovutawa, ena akawonekera padziko omwe akatumikira Yehova ndi umphumphu, monga momwe anachitira aneneri aja m’zaka za mazana akale. Kodi sindife achimwemwe kukhala amene akuchita tero?—Danieli 12:3; Chibvumbulutso 7:9.
Kupeza Chichirikizo m’Mawu Olimbikitsa a Yehova
11. Kodi ndimotani mmene Mawu a Mulungu angatithandizire kupirira, ndipo kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhala ngati thanthwe la m’fanizo la Yesu?
11 Paulo anatchula chithandizo china chakupirira pamene ananena kuti “mwa chipiriro choleza mtima, ndi mwa chilimbikitso chochokera m’Malemba, tigwiritsetu chiyembekezo chathu.” (Aroma 15:4, The Twentieth Century New Testament) Chowonadicho, Mawu a Mulungu, chiyenera kukhala chozika mizu mozama mwa ife kotero kuti chitikhozetse kulabadira moyenerera nthaŵi zonse. Sitimapindula konse mwakukhala monga thanthwe lija lofotokozedwa m’fanizo la Yesu la wofesa kuti: ‘Iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mawu, awalandira pomwepo ndikusekera; ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthaŵi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mawu, pomwepo akhumudwa.’ (Marko 4:16, 17) Chowonadi cha Mawu a Mulungu sichimazika mizu mozama mwa oterowo; chifukwa chake, m’nthaŵi ya chisautso, sakhoza kukumbukira mfundo zake zimene ndimagwero enieni a nyonga ndi chiyembekezo.
12. Kodi sitiyenera kunyengedwa za chiyani polandira mbiri yabwino?
12 Aliyense amene amalandira mbiri yabwino ya Ufumu sayenera kudzinyenga ponena za chimene chidzatsatirapo. Iye akutenga njira ya moyo imene idzabweretsa chisautso kapena chizunzo. (2 Timoteo 3:12) Koma iye ayenera kuchiyesa ‘chimwemwe chokha’ kukhala ndi mwaŵi wakuvutika ndi mayesero osiyanasiyana kaamba ka kugwiritsa zolimba Mawu a Mulungu ndi kuwalankhula kwa ena.—Yakobo 1:2, 3.
13. Kodi ndimotani ndipo nchifukwa ninji Paulo anasangalala ndi Akristu a ku Tesalonika?
13 M’zaka za zana loyamba, otsutsa a ku Tesalonika anachita chiwawa chifukwa cha kulalikira kwa Paulo. Pamene Paulo anapita ku Bereya, ozunza ameneŵa anamtsatira kumeneko ndi cholinga chokabutsanso vuto kumeneko. Kwa okhulupirika omwe anatsala mu Tesalonika, mtumwi wozunzidwayo analemba kuti: ‘Tidziyamika Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake; kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m’mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m’mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva; ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu; kuti mukaŵerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa.’ (2 Atesalonika 1:3-5) Mosasamala kanthu za kuvutika kwawo m’manja mwa mdani, Akristu a ku Tesalonika anakulitsa mkhalidwe Wachikristu ndi kuchuluka m’ziŵerengero. Kodi zimenezo zinatheka motani? Chifukwa chakuti iwo anapeza nyonga m’Mawu olimbikitsa a Yehova. Iwo anamvera malangizo a Ambuye ndipo anathamanga makaniwo mwachipiriro.—2 Atesalonika 2:13-17.
Kaamba ka Chipulumutso cha Ena
14. (a) Kodi nzifukwa zotani zimene timakhalirabe muuminisitala mwachimwemwe mosasamala kanthu ndi zovuta? (b) Kodi timapempherera chiyani, ndipo chifukwa ninji?
14 Kwakukulukulu chifukwa cha kulemekezedwa kwa Mulungu, timapirira zovuta ndi mazunzo mokhulupirika ndi mosaŵiringula. Koma palinso chifukwa china chosakhala chadyera chimene timadziperekera ku zinthu zoterozo: kotero kuti tipereke mauthenga a Ufumu kwa ena kuti pakhale ofalitsa Ufumu wa Mulungu owonjezereka opereka “chilengezo chapoyera cha chipulumutso.” (Aroma 10:10, NW) Awo ogwira ntchito muutumiki wa Mulungu ayenera kupemphera kuti Mwini kututa adalitse ntchito yawo mwakubweretsa ofalitsa owonjezereka a Ufumu. (Mateyu 9:38) Paulo analembera Timoteo kuti: ‘Zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziŵa kuphunzitsa enanso. Umve zoŵaŵa pamodzi nane monga msirikali wabwino wa Kristu Yesu.’—2 Timoteo 2:2, 3.
15. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchita ngati asirikali ndi opikisana ‘m’maseŵera’?
15 Msirikali amadzipatula ku moyo wosasamala wa anthu wamba. Mofananamo, sitiyenera kudziloŵetsa m’machitachita a awo amene sali m’gulu lankhondo la Ambuye koma ali, kwenikweni, kumbali yotsutsa. Chifukwa chake, Paulo analembera Timoteo zowonjezereka kuti: ‘Msirikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usirikali. Koma ngatinso wina ayesana nawo m’makani a maseŵero, samveka korona ngati sanayesana monga adapangana.’ (2 Timoteo 2:4, 5) Poyesayesa kulakika m’makani a “korona wa moyo,” othamanga ayenera kudziletsa ndi kupeŵa kunyamula zolemera zopanda ntchito ndi zopinga. Mwanjirayi akhoza kusumika maganizo pakupereka mbiri yabwino ya chipulumutso kwa ena.—Yakobo 1:12; yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:24, 25.
16. Kodi nchiyani chimene sichingamangidwe, ndipo kodi timapirira kaamba ka phindu layani?
16 Chifukwa chakuti timakonda Mulungu ndi anthu onga nkhosa omwe amamfuna kuti ampeze, mwachimwemwe timapirira zambiri kotero kuti tifikire ena ndi mbiri yabwino yachipulumutso. Adani angatimange chifukwa chakulalikira Mawu a Mulungu. Koma Mawu a Mulungu sangamangidwe, ndipo kuwalankhula kaamba ka chipulumutso cha ena sikungamangidwe unyolo. Paulo anafotokozera Timoteo chifukwa chake anali wofunitsitsa kwambiri kuyang’anizana ndi chiyeso: ‘Kumbukira Yesu Kristu, wouka kwa akufa, wochokera m’mbewu ya Davide, monga mwa uthenga wabwino wanga; m’menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mawu a Mulungu samangika. Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Kristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha.’ (2 Timoteo 2:8-10) Lerolino timakumbukira osati kokha otsalira ochepa a awo okhala pamzera wa Ufumu wakumwamba komanso khamu lalikulu la nkhosa zina za Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, khamu lalikulu limene lidzalandira Paradaiso wa padziko lapansi pansi pa Ufumu wa Kristu.—Chibvumbulutso 7:9-17.
17. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuleka makaniwo, ndipo kodi pamakhala zotulukapo zotani ngati tipitiriza m’makaniwo mpaka kumapeto?
17 Ngati tileka, sitidzithandiza tokha kapena aliyense kupulumuka. Mwakupirira m’makani Achikristu, mosasamala kanthu za zopinga zimene tikumana nazo, timathamangabe mosalekeza pamzera wokapata mphotho ndipo tikhoza kuthandiza ena mwachindunji kukapulumuka, pamene tikukhala chitsanzo champhamvu chopereka nyonga kwa ena. Chirichonse chimene chingakhale chiyembekezo chathu, chakumwamba kapena chapadziko lapansi, mkhalidwe wa Paulo wa ‘kulondoletsa polekezerapo, kutsatira mfupo’ uli wabwino kuutsanzira.—Afilipi 3:14, 15.
Kupitiriza Kosalekeza m’Makaniwo
18. Kodi kupata mphotho kumadalira pachiyani, koma kuti tithamangebe kufika kumapeto, kodi tiyenera kupeŵanji?
18 Kumaliza njira yathu Yachikristu mwachilakiko ku chitamando cha Yehova ndi kupata mphotho imene watisungira kumadalira pa kupitiriza kwathu kosalekeza mtunda wonse wa makaniwo. Chotero, sitingafike kumapeto ngati tidzilemetsa ndi zinthu zosatumikira cholinga cha chilungamo. Ngakhale titachotsa zinthu zoterozo, ziyeneretso zofunikira zimakhalabe zovutirako kwakuti zifunikirabe nyonga yonse imene tingathe kukhala nayo. Chifukwa chake, Paulo akulimbikitsa kuti: ‘Titaye cholemetsa chirichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.’ (Ahebri 12:1) Mofanana ndi Yesu sitiyenera kulankhula mokulitsa mavuto amene angabuke koma kuwayesa mtengo waung’ono wolipirira mphotho yodzetsa chimwemwe.—Yerekezerani ndi Aroma 8:18.
19. (a) Kodi nchidaliro chotani chimene Paulo anafotokoza ali pafupi ndi mapeto a moyo wake? (b) Pamene tikuyandikira mapeto a makani a chipiriro, kodi nchidaliro chotani chimene tiyenera kukhala nacho ponena za mphotho yolonjezedwayo?
19 Poyandikira kumapeto kwa moyo wake, Paulo anakhoza kunena kuti: ‘Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro: Chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo.’ (2 Timoteo 4:7, 8) Tiri pamakani ameneŵa a chipiriro kuti tipate mphotho ya moyo wamuyaya. Ngati chipiriro chathu chitha chifukwa chakuti makaniwo awoneka kukhala aatali kuposa mmene tinayembekezerera pamene tinayamba, tidzalephera pamene tayandikira mphotho yolonjezedwayo. Palibe chikaikiro chirichonse. Mphothoyo irikodi.
20. Kodi cholinga chathu chotsimikiza mtima chiyenera kukhala chotani mpaka pamene tidzafika kumapeto kwa makaniwo?
20 Chotero lolani kuti maso athu asatope ndi kupenya kuti awone kuyambika kwa chisautso chachikulu, chikubweretsa chiwonongeko choyamba pa Babulo Wamkulu ndiyeno pa gulu lonse la Mdyerekezi. (2 Petro 3:11, 12) Powona zizindikiro zonse zotizinga, tiyeni tiyang’anetu kutsogolo mwachikhulupiriro. Tiyeni timange m’chiuno lamba la mphamvu zathu za chipiriro, ndipo tipitirizabe kuthamanga zolimba m’makani amene Yehova Mulungu watiikira, mpaka kufika kumapeto ndi kupata mphotho, m’kulemekeza Yehova kupyolera mwa Yesu Kristu.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimakani otani amene Mkristu ayenera kukonzekera?
◻ Kodi nchifukwa ninji chimwemwe chiri chofunika kwambiri pothamanga makaniwo?
◻ Kodi nzifukwa zazikulu ziti zimene timakhalirabe muuminisitala mosasamala kanthu ndi zovuta?
◻ Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuleka makani amene Mulungu watiikira?
[Chithunzi patsamba 15]
Monga m’makani a mtunda wautali, Akristu ayenera kupirira
[Chithunzi patsamba 17]
Pokalamira “korona wa moyo,” othamanga ayenera kudziletsa