Mtambo Waukulu Wotere wa Mboni!
“Popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, . . . tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira ife.”—AHEBRI 12:1.
1, 2. (a) Kodi ndi malo ophiphiritsira otani amene Paulo akanakhala anali nawo m’maganizo pamene anali kulembera kwa Akristu a Chihebri? (b) Kodi nchifukwa ninji akhulupiriri anzake a Chihebri anafunikira chikhulupiriro cholimba?
DZIYEREKEZENI inu mwini monga wothamanga musitediyamu. Mukulimbikira kupita patsogolo, kutanula mnofu uli wonse, maso anu olunjikitsidwa pa chonulirapo chanu. Koma bwanji ponena za oyang’anirawo? Nchiyani, onse a iwo ali othamanga opambana! Iwo sanali kokha apenyereri koma mboni za changu ponse pawiri m’mau ndi m’kachitidwe.
2 Mtumwi Paulo angakhale anali ndi malo ophiphiritsira amenewa m’maganizo pamene anali kulembera Akristu a ku Ahebri (c. 61 C.E.). Iwo anafunikira chikhulupiriro cholimba. (Ahebri 10:32-39) Kokha ndi chikhulupiriro iwo akanalabadira chenjezo la Yesu lakuthawa pamene Yerusalemu anazingidwa ndi magulu ankhondo (mu 66 C.E.) zaka zochepa pambuyo pa kuwonongedwa kwache m’manja mwa Aroma mu (70 C.E.). Chikhulupiriro chikanawachirikiza iwo pamene anali “kuzunzidwa kaamba ka chilungamo.”—Mateyu 5:10; Luka 21:20-24.
3. Pa Ahebri 12:1, kodi nchiyani chimene chiri “chimoli limangotizinga,” ndipo Akristu akufulu mizidwa kuthamanga makani amtundu wanji ndi chikhulupiriro?
3 Pambuyo pakubwereramo mu zochitika za chikhulupiriro za munthawi ya Chikristu chisanayambe [mu Ahebri, mutu 11), Paulo anafulumiza: “Chifukwa chache ifenso popeza tizingidwa nawo mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chiri chonse [chomwe chingachipangitse icho kukhala chovuta kwa ife mwauzimu] ndi chimo [kusoweka kwa chikhulupiriro] limangotizinga, ndipo tithamange mwa chikhulupiriro makaniwo [kaamba kamoyo wosatha] adatiikira.” (Ahebri 12:1) Kubwereramo kwa Paulo mu chikhulupiriro m’chenicheni kukupereka mfundo zazikulu zosiyanasiyana za mbali zosiyana za icho ndipo chidzatithandiza ife, kaya tiri Akristu odzozedwa omathamanga makani kaamba ka moyowosakhoza kufa kumwamba kapena tiri mbaliya “khamu lalikuru” lokhala ndi chonulirapo cha moyo wosatha mu paradaiso pa dziko lapansi. (Chivumbulutso 7:4-10; Luka 23:43; Aroma 8:16, 17) Koma kodi nchiyani chimene chiri chikhulupiriro? Kodi ndi ziti zomwe ziri mbali zina za chinthu cha mtengo wapatali chauzimu chimenechi? Ndipo ndi motani m’mene tinga chitire ngati tikufuna kukhala ndi chikhulu piriro? Pamene mukufunafuna mayankho ku mafunso amenewa, chonde werengani ndime zosonyezedwa za Ahebri mutu 11 ndi 12 mkati mwa phunziro la umwini ndi lapampingo
Chimene Chikhulupiriro Chiri
4. Kodi chikhulupiriro nchiyani?
4 Paulo poyamba analongosola chikhulupiriro. (Werengani Ahebri 11:1-3.) Kumbali ina, chikhulupiriro ndi [“chiyembekezo chotsimikiziridwa cha zinthu zoyembekezeredwa,”NW] Munthu wokhala ndi chikhulupiriro ali ndi kuthekera kwakuti chiri chonse chimene Mulungu walonjeza chiri monga ngati kuti china kwaniritsidwa. Chikhulupiriro chirinso[“chisonyezero chooneka bwino cha zinthu zosape nyeka,” NW] Chitsimikiziro chokhutiritsa cha zinthu zosawoneka chiri champhamvu koposa kotero kuti chikhulupiriro chikunenedwa kukhala chofanana ndi; chitsimikiziro.
5. Nchiyani chomwe timazindikira chifukwa cha chikhulupiriro?
5 Ndi chikhulupiriro “amuna anthawi zakale anachitidwira umboni kwa iwo” kuti anasangalatsa Mulungu. Ndiponso, “ndi chikhulupiriro timazindikira kuti mu dongosolo iri la zinthu’’—dziko lapansi, dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi—“zinakhazikitsidwa mu dongosolo ndi mau a Mulungu, kotero kuti zomwe ziri kuwoneka zatsimikizira kukhala zochokera ku zinthu zomwe siziwoneka.” Tiri otsimikizira kuti Yehova ali Mlengi wa zinthu zimenezo, angakhalekuti sitingathe kumuwona iye chifukwa chakuti iye, ali Mzimu wosaoneka.—Genesis 1:1; Yohane 4:24; Aroma 1:20.
Chikhulupiriro ndi “Dziko Lakale”
6. Kodi nchifukwa ninji Abeli anali ndi “chiyembekezo chotsimikizirika’’ chakuti mau olosera a Yeho va ponena za ‘mbeu ya mkazi’ adzakhala owona?
6 Chimodzi cha mbali zambiri za chikhulupiriro chiri chiyamikiro kaamba kakufunika kwa nsembe kaamba ka machimo. (Werengani Ahebri 11:4.) Mu “dziko lakale,” chikhulupiriro munsembe ya mwazi chinasonyezedwa ndi Abeli, mwana wachiwiri wabanja loyambirira laanthu, Adamu ndi Hava. (2 Petro 2:5) Mosaka ikira Abeli anazindikira mwa iye mwini zochitika zopatsa imfa zachimo la cholowa. (Genesis 2:16, 17; 3:6, 7; Aroma 5:12) Mwachiwonekere iye anazindikiranso kukwaniritsidwa kwa la mulo la Mulungu lomwe linabweretsa ntchito zotopetsa pa Adamu ndi kupweteka kwa nthawi yapathupi kwa Hava. (Genesis 3:16-19) Chotero Abeli anali ndi “chitsimikiziro cha zinthu zoyembekezeredwa” kuti zinthu zina zolankhulidwa ndi Yehova zidzakhala zowona. Izi zinaphatikiza mau olosera olunjikitsidwa kwa wonyenga wamkulu Satana pamene Mulungu ananena kwa chinjoka: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkazi ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. lye adzalalira mutu wako ndi iwe udzalalira chitende chake.”—Genesis 3:15.
7. (a) Ndi motani mmene Abeli anasonyezera chiyamikiro kaamba ka kufunikira kwa nsembe kaamba ka machimo? (b) Ndi mwanjira yotani mmeneMulungu ‘anachitira umboni ponena za mphatso yaAbeli’?
7 Abeli anasonyeze chikhulupiriro chake mu mbewu yolonjezedwa mwa kupereka nsembe ya nyama kwa Mulungu yomwe ikalowa mmalo mwa moyo weniweni wa Abeli. Koma mkulu wake wopanda chikhulupiriro Kaini anapereka nsembe ya zipatso za nthaka zopanda mwazi: Monga wakupha anthu, Kaini pambuyo pake anakhetsa mwazi wa Abeli. (Genesis 4:1-8) Komabe Abeli anafa akudziwa kuti Yehova anamulingalira iye monga wolungama, “Mulu ngu akumachitira umboni ponena za mphatso zake.” Motani? Mwa kulandira nsembe yoperekedwa ndi chikhulupiriro ya Abeli. Chifukwa cha chikhulupiriro chake ndi chivomerezo cha umulungu, ponena za chimene Mbiri Youziridwa ikupitiriza kuchitira umboni, ‘angakhale Abeli anafa, iye akulankhulabe.’ Iye anaona kufunika kwa nsembe kaamba ka machimo. Kodi muli ndi chikhulupiriro chachikulu koposa mu nsembe yowonekera ya dipo ya YesuKristu?—1 Yohane 2:1, 2; 3:23.
8. (a) Kodi nchiyani chomwe timaphunzira ponena za chikhulupiriro kuchokera ku kuchitira umboni kolimba mtima kwa Enoke? (b) Ndi motani mmene Enoke “anasamutsidwira kotero kuti asawone imfa”?
8 Chikhulupiriro chikatifulumiza ife kulankhula uthenga wa Mulungu mopanda mantha. (Werengani Ahebri 11:5, 6.) Mboniyoya mbirira ya Yehova Enoke molimba mtiina ana neneratu za chiweruzo chaumulungu pa anthu opanda umulungu. (Yuda 14, 15) Mosakaikira adani a Enoke anafuna kumupha iye, koma Mulungu “anamtenga iye” kotero kuti sanavutike ndi zowawa za imfa. (Genesis 5:24) Poyambirira, angakhale kuli tero, “iye anali ndi umboni wakuti anasangalatsa Mulungu bwino.” Mwanjira yotani? “Ndi chikhulupiriro Enoke anasamutsidwa kotero kuti asaone imfa.” Mofananamo, Paulo anasamutsidwa, kapena “kugwidwa kupita mu paradaiso,” mwachionekera kulandira masomphenya a paradaiso wauzimu wamtsogolo wa mpingo wa Chikristu. (2 Akorinto 12:1-4) Chotero Enoke mwachionekere anali kusangalala ndi masomphenya a paradaiso wa pa dziko lapansi wa kudzayo pamene Yehova anamuika iye m’kugona mu imfa, wosungika kuchoka ku manja a adani ake. Kuti tikhale osangalatsa kwa Mulungu ife, monga Enoke, tiyenera kulankhula uthenga wa Mulungu mopanda mantha. (Ma chitidwe 4:29-31) Tiyeneranso kukhulupirira kuti Mulungu aliko ndipo “ali wofupa awo amene mofunitsitsa akumufunafuna iye.”
9. Kodi ndi motani mmene njira ya Nowa inasonyezera kuti kutsatira malangizo a Mulungu mosamalitsa iri mbali imodzi ya chikhulupiriro?
9 Kutsatira malangizo a Mulungu mosamalitsa iri imodzi yambali ya chikhulupiriro. (Werengani Ahebri 11:7.) Mwakuchita mwachikhulupiriro, Nowa anachita ‘kokha mongam’mene Mulungu anamulamulira. (Genesis 6:22; 7:16) Nowa analandira “chenjezo laumulungu la zinthu zomwe zinali zisanaoneke” ndipoanakhulupirira mawu a Yehova akuti chigumula cha dziko lonse chidzaoneka. Mu chikhulupiriro ndi mantha aulemu a Mulungu, Nowa“anamanga chingalawa kaamba ka kusunga anthu am’nyumba yake.” Ndi kumvera ndi machitidwe achilungamo, iye mwakutero anatsutsa dziko losakhulupirira kaamba ka ntchitozake zoipa ndi kulisonyeza kuti linayenera chiwonongeko.—Genesis 6:13-22.
10. Angakhale Nowa anali kumanga chingalawa, iye anatenga nthawi kaamba ka ntchito ina iti?
10 Nowa anali m’modzi wa mboni za Yehova m’chakuti iye anali “mlaliki wa chilungamo.”(2 Petro 2:5)Angakhale anali wotanganitsidwa kumanga chingalawa, iye anatenga nthawi ya kulalikira, monga mmene zimachitira Mboni za Yehova lerolino. Ndithudi, Nowa analankhula mopanda mantha monga mthenga wa Mulungu kuchenjeza anthu amene anakhalako kanthu kufikira kumene chigumula chinadza chinapululutsa iwo onse.”—Mateyu 24:36-39.
Chikhulupiriro Pakati pa Makolo a Pambuyo pa Chigumula
11. (a) Kodi ndi motani mmene Abrahamu anasonyezera kuti chikhulupiriro chimaphatikizamo chidaliro chotheratu m’malonjezo a Yehova? (b) Mwachikhulupiriro Abrahamu anali kuyembekezera“mzinda uti?
11 Chikhulupiriro chimaphatikizamo chidaliro chotheratu mu malonjezo a Yehova. (Werengani Ahebri 11:8-12.) Ndi chikhulupiriro Abrahamu (Abramu) anamvera lamulo la Mulungu ndi kuchoka ku Uri wa Akadayo, mzinda wokhala ndi zopereka zambiri mu njira ya ku thupi. Iye anakhulupirira lonjezo la Yehova lakuti “mabanja onse apadziko lapansi” adzadzidalitsa iwo okha kudzera mwa iye ndi kuti mbewu yake idzapatsidwa dziko. (Genesis 12: 1-9; 15:18-21) Mwana wa Abrahamu Isake ndi mdzukulu wake Yakobo anali “olowa m’malo limodzi naye mu lonjezo limodzimodzilo.” Ndi chikhulupiriro Abrahamu “anakhala monga mlendo mu dziko lamalonjezo monga ngati dziko lachilendo.” Iye anayang’ana kutsogolo ku “mzinda wokhala ndi maziko enieni mmisiri wake ndi womanga wake wa mzinda umenewu ali Mulungu.” Inde, Abrahamu anayembekeze ra Ufumu wa kumwamba wa Mulungu pansi pa umene iye adzaukitsidwira ku moyo pa dziko lapansi. Kodi Ufumu umenewu umatenga mbali yofunika kwambiri m’moyo wanu?—Mateyu 6:33.
12. Kodi nchiyani chomwe chinachitika chifukwa chakuti Sara anali ndi chikhulupiriro m’malonjezo a Yehova?
12 Akazi a makolo owopa Mulungu amenewa analinso ndi chikhulupiriro mu malonjezo a Yehova. Mwachitsanzo, ndi chikhulupiriro mkazi wa Abrahamu Sara, angakhale anali wosabala kufikira pa zaka 90 zakubadwa ndi “wopitirira mu zaka,” anapatsidwa mphamvu “kukhala ndi pathupi pa mbewu, . . . popeza analemekeza iye [Mulungu] wokhulupirika yemwe analonjeza.” M’kupita kwa nthawi Sara anabala Isake. Mwakutero kuchokera kwa Abrahamu wa zaka 100 zakubadwa, “wofanana ndi wakufa” m’chiyang’aniro chakubereka, potsirizira “kunabadwa ana monga ngati nyenyezi za kumwamba kaamba ka Abrahamu.”—Genesis 17:15-17; 18:11; 21:1-7.
13, 14. (a) Ngakhale kuti Abrahamu, Isake, ndi Yakobo “sanawone kukwaniritsidwa kwa malonjezo,” ndi motani mmene iwo anachitira? (b) Kodi ndi motani mmene tingapindulire kuchokera kukuli ngalira kumvera Yehova kwa makolo amenewa angakhale kuti sitiwona kukwaniritsidwa kwa mwamsanga kwa malonjezo ake?
13 Chikhulupiriro chidzatipangitsa ife kukhala omvera kwa Yehova angakhale ngati sitiwona kukwaniritsidwa kwa mwamsanga kwa malonjezo ake. (Werengani Ahebri 11:13-16.) Makolo okhulupirika onse anafa osawona kukwaniritsidwa kwenikweni kwa malonjezo Mulungu kwa iwo, “iwo anaona [zinthuzolonjezedwa] ziri kutali kwambiri ndipo anazilandira izo ndikuzilalikira izo poyera kuti anali alendo ndi alendo ogonera m’dziko.” Inde, anakhala ndi miyoyo yawo mu chikhuhipiriro, popeza mibadwo inapita mbadwa za Abrahamu zisanatenge Dziko Lolonjezedwa.
14 Chenicheni chakuti sanalandire kukwaniritsidwa kwa maulosi aumulungu mu nthawi yawo sichinapweteketse mtima Abrahamu, Isake, ndi Yakobo kapena kuwapangitsa iwo kukhala ampatuko. Iwo sanamusiye Yehova ndi kubwerera ku Uri, kukhala omizidwa mu zochitika za dziko. (Yerekezani ndi Yohane 17:16; 2 Timoteo 4:10; Yakobo 1;27;1 Yohane 2:15-17. ) Ayi, makolo amenewo ‘anafikira’ kaamba ka malo abwinoko kuposa Uri, “kunena kuti, lakumwamba.” Chotero Yehova ‘sali wochititsidwa manyazi ku itanidwa ndi iwo monga Mulungu wawo.’ Iwo anasunga chikhulupiriro chawo mwa Wa m’mwambamwamba kufikira imfa ndipo posachedwapa adzaukitsidwa ku moyo pa dziko lapansi, mbali ya “mzinda,” weniweni, Ufumu Wau mesiya umene Mulungu anaukonzeratu kaamba kaiwo. Koma bwanji ponena za inu? Angakhale ngati ‘mwayenda mu chowonadi kwa zaka zambiri, kukula mu utumiki wa Yehova, muyenera kusungirira chidaliro chanu mu malonjezo ake adongosolo latsopano la zinthu. (3 Yohane 4;2 Petro 3:11-13) Ha ndi mphotho yapamwamba yotani imene inu ndi makolo okhulupirika mudzalandira kaamba ka chikhulupiriro chotero!
15. (a) Kodi nchiyani chomwe chinamutheketsa Abrahamu mwamsanga kumupereka Isake monga nsembe? (b) Ndi motani mmene chikhulupiriro chathu chiyenera kukhudzidwira ndi nkhani yophatikizamo Abrahamu ndi Isake? (c) Kodi nchiyani chimene molosera chinaimiridwa ndi chochitika chimenechi?
15 Kumvera kosakaikiritsa kwa Mulungu kuli mbali yofunika kwambiri ya chikhulupiriro. (WerenganiAhebri 11:17-19.) Chifukwa chakuti Abrahamu anamvera Yehova popanda chikaikiro, iye “mofanana ndi kumupereka nsembe Isake,” “mwana; wake wayekha”—mwana yekha yemwe anali naye ndi Sara. Ndi motani m’mene Abrahamu akanachitira ichi? Chifukwa chakuti “iye anazindikira kuti Mulungu anali wokhoza kumuukitsa [Isake] kuchokera kwa akufa,” ngati chinali choyenerera, kukwaniritsa lonjezo lambadwa kudzera mwa iye. Mu kamphindi mpeni womwe unali mdzanja la Abrahamu ukanatsiriza moyo wa Isake, koma mau a mngelo anatetezera ichi. Mwakutero, Abrahamu analandira Isake kuchokera ku imfa “m’njira yachitsanzo.” Ife mofananamo tiyenera kufulumizidwa kumvera Mulungu m’chukhulupiriro angakhale ngati moyo wathu kapena uwo wa ana athu uli pangozi. (1 Yohane 5:3) Chiri choyenera kudziwa kuti, Abrahamu ndi Isake mwa ulosi anaimira m’mene Yehova Mulungu akaperekera mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu monga dipo kotero kuti awo osonyeza chikhulupiriro mwa iye akakhale ndi moyo wosatha.—Genesis 22:1-19; Yohane 3:16.
16. M’chiyang’aniro ndi ana athu ndi chikhulupiriro chathu mu malonjezo a Mulungu, kodi ndi chitsanzo chotani chimene makolowo anachipereka?
16 Ngati tiri ndi chikhulupiriro, tidzathandiza mbadwa zathu kuika chiyembekezo chawo pa zimene Mulungu amalonjeza kaamba ka mtsogolo. (Werengani Ahebri 11:20-22.) Chikhulupiriro cha makolo chinali champhamvu kotero kuti angakhale kuti malonjezo a Yehova kwa iwo sanakwaniritsidwe kotheratu mu nthawi yawo, iwo anapatsira izi kwa ana awo monga cholowa chokondedwa. Mwakutero, “Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau ponena za zinthu zinalinkudza,” ndipo Yakobo woyandikira imfayo ananena madalitso kwa Efraimu ndi Manase ana a Yosefe. Popeza Yosefe iye mwini anali ndi chikhulu piriro champhamvu chakuti Aisrayeli adzachoka mu Igupto kupita ku dziko lolonjezedwa, iye anapanga abale ake kulumbira kuti adzatenga mafupa ake limodzi nawo pochoka (Genesis 27: 27-29, 38-40; 48:8-22; 50:24-26) Kodi mukulithandiza banja lanu kukulitsa chikhulupiriro chofananacho mu zimene Yehova walonjeza?
Chikhulupiriro Chimatipanga Ife Kuika Mulungu Poyamba
17 Ndi motani mmene makolo a Mose anachitira m’chikhulupiriro?
17 Chikhulupiriro chimatifulumiza ife kuika Yehova ndi anthu ake patsogolo pa china chirichonse chomwe dziko lingapereke. (WerenganiAhebri 11:23-26.) Aisrayeli anali akapolo ofunikira chipulumutso kuchokera ku ukapolo ku Igupto pamene makolo a Mose anachita mu chikhulupiriro. ‘Iwo sanaope lamulo la mfumu’ kupha ana amuna Achihebri pobadwa, m’malo mwake, iwo anamubisa Mose kwa miyezi itatu, pomalizira anamuika mu kabokosi kagumba pakati pa mabango mu mbali mwa mtsinje wa Nile. Atapezedwa ndi mwana wa mkazi wa Farao, iye ‘anamulera iye monga mwana wake.’ Poyambirira, komabe, Mose analeledwa ndi kuphunzitsidwa mwauzimu m’nyumba ya atate ndi mayi wake, Amramu ndi Yokobedi. Kenaka, monga membala wa nyumba ya Farao, iye “analangizidwa munzeru yonse ya Aigupto” ndi kukhala “wamphamvu m’mau ake ndi m’kachitidwe,” wa mpha mvu mu kuthekera kwa maganizo ndi kuthupi.—Machitidwe 7:20-22; Eksodo 2:1-10; 6:20.
18. Chifukwa cha chikhulupiriro chake, kodi ndi malo amtundu wanji amene Mose anatenga m’chigwirizano ndi kulambira Yehova?
18 Komabe, maphunziro a Aigupto ndi ulemerero wa zinthu zakuthupi wa m’nyumba ya chifumu sizinamupangitse Mose kusiya kulambira Yehova ndi kukhala wampatuko. M’malo mwake, “ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wache wa mwana wamkazi wa Farao,” njira yosonyezedwa pamene anachinjiriza mbale wake wa Chihebri (Eksodo 2:11, 12) Mose anasankha “kuchitidwa zoipa limodzi ndi anthu a Mulungu [Aisrayeli anzake olambira a Yehova] m’malo mwa kukhala ndi chikondwerero cha kanthawi cha chimo.” Ngati muli mtumiki wobatizidwa wa Yehova yemwe ali maziko olimba a chiphunzitso choyenerera chauzimu, kodi mudzatsatira chitsanzo cha Mose ndi kuima nji ku kulambira kowona?
19. (a) Kodi chiri chotsimikizirika motani kuti Mose anaika Yehova ndi anthu Ake choyamba m’moyo? (b) Kodi Mose anayang’ana kutsogolo kaamba ka kuperekedwa kwa mphoto yotani?
19 Mose anasankha kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Yehova “chifukwa anawerengera tonzo la Kristu chuma choposa zolemera za Igupto.” Mosakaikira Mose ‘anawerengera chitonzo chakukhala Kristu wakale, kapena Wodzozedwa wa Mulungu, monga chuma choposa cha Aigupto.’ Monga membala wa nyumba ya chifumu, iye akanakondwera ndi chuma ndi kutchuka muIgupto. Koma iye anasonyeza chikhulupiriro ndi “kupenyerera chobwezera champhotho”—moyo wosatha kudzera mu chiukiriro pa dziko lapansi mu dongosolo la zinthu latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu.
20. Kodi nchiyani chomwe chiripo ponena za chokumana nacho cha Mose chomwe chimasonyeza kuti chikhulupiriro chimatipangitsa ife kukhala atumiki opanda mantha a Yehova?
20 Chikhulupiriro chimatipanga ife kukhala opanda mantha chifukwa timadalira mwa Yehova monga mpulumutsi. (Werengani Ahebri 11: 27-29.) Pambuyo pakumva kuti Mose anapha M’aigupto, Farao anafuna kumupha iye. “Koma Mose anathawa pankhope pa Farao nakhala m’dziko la Midiyani.” (Eksodo 2:11-15) Chotero Paulo akuonekera kukhala ali kulankhula mwa chindunji Ponena za Kuturuka kotsatirapo kwa Ahebri kuchokera ku Igupto pamene iye akuti: “Ndi chikhulupiriro iye [Mose] anasiya Igupto, wosawopa mkwiyo wa mfumu [yemwe anamuopseza ndi imfa kaamba ka kuimira Mulungu m’malo mwa Aisrayeli,] pakuti anapirira mo limba monga ngati kuwona Wosawonekayo.” (Eksodo 10:28, 29) Ngakhale kuti Mose sanamu wone Mulungu mwachindunji, zochita za Yeho va ndi iye zinali zenizeni kotero kuti iye anachita ngati anamuwona ‘Wosawonekayo.’ (Eksodo 33: 20) Kodi unansi wanu ndi Yehova uli wampha- mvu motero?—Masalmo 37:5; Miyambo 16:3.
21. Ponena za kuturuka mu Igupto kwa Aisrayeli, kodi nchiyani chomwe chinachitika “mwa chikhulupiriro”?
21 Nthawi pang’ono pambuyo pa kuchoka kwa Israyeli ku Igupto, “ndi chikhulupiriro iye [Mose] anachita Paskha ndi kuwaza kwa mwazi, kuti akuwononga asakhudze ana awo oyamba [a Aisrayeli].” Inde, chinatenga chikhulupiriro ku panga Paskha limodzi ndi chidaliro chakuti ana oyamba a Israyeli sadzawonongedwa pamene awo a Aigupto adzafa, ndipo chikhulupiriro chimenechi chinafupidwa. (Eksodo 12:1-39) Ndiponso “ndi chikhulupiriro iwo [anthu a Israyeli] anapyola Nyanja Yofira pa malo owuma, koma mwakuyesera kupita pa iyo Aigupto anamezedwa.” Ha ndi mpulumutsi wodabwitsa chotani nanga m’mene Mulungu anatsimikizira kukhala! Ndipo chifukwa cha chipulumutso chimenechi, Aisrayeli “anayamba kuwopa Yehova ndi kuika chikhulupiriro mwa Yehova ndi mwa mtu miki wake Mose.”—Eksodo 14:21-31.
22. M’chigwirizano ndi chikhulupiriro, kodi ndi mafunso otani omwe atsala kaamba ka kulingalirapo rapo?
22 Chikhulupiriro cha Mose ndi makolo chiridi chitsanzo kaamba ka Mboni za Yehova lerolino. Koma kodi nchiyani chomwe chinachitika pamene Yehova anachita ndi mbadwa za Abrahamu monga mtundu wolinganizidwa mwa teokratiki? Kodi nchiyani chomwe tingaphunzire kuonjezerapo ponena za ntchito za chikhulupiriro mu nthawi zakale?
Kodi Mukanayankha Motani?
◻ Kodi chikhulupiriro nchiyani?
◻ Chitsanzo cha Enoke chimatiphunzitsa ife chiyani ponena za chikhulupiriro?
◻ Kodi ndi motani mmene makolo owopa Mulungu anasonyezera kuti chikhulupiriro chimaphatikiza chidaliro chotheratu mu malonjezo a Yehova?
◻ Kodi nkachitidwe ka mtundu wanji ka Abrahamu komwe kakusonyeza kuti kumvera Mulungu mosakaikira kuli mbali imodzi yofunika kwambiri ya chikhulupiriro?
◻ Ndi machitidwe a mtundu wanji a Mose omwe akusonyeza kuti chikhulupiriro chimatanthauza kuika Yehova ndi anthu Ake patsogolo pa china chiri chonse chimene dziko lingapereke?