Kodi Yesu Angakhale Anali ndi Chikhulupiriro mwa Mulungu?
Chothetsa Nzeru cha Okhulupirira Utatu
“KODI Yesu akanakhala bwanji ndi chikhulupiriro? Iye ndi Mulungu; amadziŵa ndi kuona kanthu kalikonse mosadalira aliyense. Koma chikhulupiriro ndicho kudalira munthu wina ndi kuvomereza chinthu chimene sichimaoneka; motero lingaliro lakuti Yesu-Mulungu anali ndi chikhulupiriro liyenera kuchotsedwapo.”
Malinga ndi kunena kwa wophunzitsa zaumulungu Wachifrenchi Jacques Guillet, limenelo ndilo lingaliro lalikulu mu Chikatolika. Kodi malongosoledwe ameneŵa akukudabwitsani? Mwinamwake mwakhala mukulingalira kuti popeza Yesu ali chitsanzo cha Akristu m’chinthu chilichonse, ayeneranso kukhala chitsanzo m’chikhulupiriro. Ngati munalingalira motero, simunagwirizane ndi chiphunzitso choikidwiratu cha Utatu cha Dziko Lachikristu.
Funso la chikhulupiriro cha Yesu lilidi lovuta kuliyankha kwa ophunzitsa zaumulungu Achikatolika, Achiprotestanti, ndi Achiorthodox omwe amakhulupirira kuti Utatu uli “chinsinsi chachikulu cha chikhulupiriro ndi moyo Wachikristu.”a Komabe, si onse amene amakana chikhulupiriro cha Yesu. Jacques Guillet akuvomereza kuti “kuli kosatheka kulingalira kuti Yesu analibe chikhulupiriro,” ngakhale kuti akuvomereza kuti, m’lingaliro la chiphunzitso cha Utatu, kuli “chozizwitsa.”
Mjesuit Wachifrenchi Jean Galot, limodzi ndi ophunzitsa zaumulungu ochuluka, amanena motsimikiza kuti pokhala “Mulungu weniweni ndi munthu weniweni, . . . Kristu sangakhulupirire mwa iyemwini.” “Chikhulupiriro ndicho kukhulupirira mwa wina, osati kudzikhulupirira wekha,” akutero magazini a La Civiltà Cattolica. Motero, chopinga pa kuzindikira chikhulupiriro cha Yesu ndicho chiphunzitso choikidwiratu cha Utatu, popeza kuti malingaliro aŵiriwo amawombana moonekeratu.
“Mauthenga Abwino samanena konse za chikhulupiriro cha Yesu,” amatero ophunzitsa zaumulungu. Kwenikweni, mawu ogwiritsiridwa ntchito m’Malemba Achigiriki Achikristu pi·steuʹo (khulupirira, khala ndi chikhulupiriro) ndi piʹstis (chikhulupiriro) kwakukulukulu amanena za chikhulupiriro cha ophunzirawo mwa Mulungu kapena Kristu, m’malo mwa chikhulupiriro cha Yesu mwa Atate wake wakumwamba. Chotero kodi tiyenera kuganiza kuti Mwana wa Mulungu analibe chikhulupiriro? Kodi tiyenera kuzindikiranji pazimene iye anachita ndi zimene ananena? Kodi Malemba amanenanji?
Mapemphero Opanda Chikhulupiriro?
Yesu anali munthu wa mapemphero. Iye anapemphera nthaŵi zonse—pamene anabatizidwa (Luka 3:21); usiku wonse asanasankhe atumwi ake 12 (Luka 6:12, 13); ndi pamene asanasandulike mozizwitsa paphiri, pamene anali ndi atumwiwo Petro, Yohane, ndi Yakobo. (Luka 9:28, 29) Iye anali kupemphera pamene mmodzi wa ophunzira ake anamfunsa kuti: “Tiphunzitseni ife kupemphera,” ndipo anawaphunzitsa Pemphero la Ambuye (la “Atate Wathu”). (Luka 11:1-4; Mateyu 6:9-13) Iye ankapemphera payekha ndipo kwa nthaŵi yaitali mmamaŵa (Marko 1:35-39); chakumadzulo, paphiri, atamasula ophunzira ake (Marko 6:45, 46); limodzi ndi ophunzira ake ndi kupempherera ophunzira ake. (Luka 22:32; Yohane 17:1-26) Inde, pemphero linali mbali yofunika kwambiri m’moyo wa Yesu.
Iye anapemphera asanachite zozizwitsa, mwachitsanzo, asanaukitse Lazaro bwenzi lake anati: “Atate, ndiyamika inu kuti munamva ine. Koma ndadziŵa ine kuti mumandimva ine nthaŵi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupire kuti inu munandituma ine.” (Yohane 11:41, 42) Kutsimikiza mtima kwake kwakuti Atate wake akayankhadi pemphero limenelo kumasonyeza mphamvu ya chikhulupiriro chake. Umboni wogwirizana umenewu pakati pa pemphero kwa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa Iye ndi zimene Kristu ananena kwa ophunzira ake kuti: “Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.”—Marko 11:24.
Ngati Yesu analibe chikhulupiriro, kodi anapemphereranji kwa Mulungu? Chiphunzitso chopanda Malemba cha Utatu cha Dziko Lachikristu, chakuti Yesu anali ponse paŵiri munthu ndi Mulungu panthaŵi imodzimodzi, chimaphimba uthenga wa Baibulo. Chimaletsa anthu kumvetsetsa choonadi chosavuta cha Baibulo ndi mphamvu yake. Kodi munthuyo Yesu analankhula kwa yani? Kwa iye mwini? Kodi iye sanadziŵe kuti anali Mulungu? Ndipo ngati anali Mulungu nadziŵa zimenezo, nchifukwa ninji anapemphera?
Mapemphero a Yesu patsiku lomaliza la moyo wake wa padziko lapansi amatipatsadi chidziŵitso chozamirapo cha chikhulupiriro chake mwa Atate wake wakumwamba. Posonyeza chiyembekezo ndi chidaliro, iye anapempha kuti: “Ndipo tsopano, Atate inu, lemekezani ine ndi inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nawo ndi inu lisanakhale dziko lapansi.”—Yohane 17:5.
Podziŵa kuti mayesero ake ovuta kwambiri ndi imfa yake zinali pafupi, usiku umene anali m’munda wa Getsemane pa Phiri la Azitona, ‘anayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuthedwa nzeru,’ ndipo anati: “Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho ku imfa.” (Mateyu 26:36-38) Ndiyeno anagwada napemphera kuti: “Atate, mukafuna inu, chotsani chikho ichi pa ine; koma sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.” Ndiyeno “anamuonekera iye mngelo wakumwamba namlimbitsa iye.” Mulungu anamva pemphero lake. Chifukwa cha kupsinjika mtima kwake kwakukuluko ndi kupweteka kwa chiyesocho, “thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.”—Luka 22:42-44.
Kodi kuvutika kwa Yesu, kufuna kwake chilimbikitso, ndi mapembedzero ake zimasonyeza chiyani? “Chinthu chimodzi nchotsimikizirika,” akulemba motero Jacques Guillet, “Yesu anapemphera, ndipo pemphero linali mbali yofunika kwambiri m’moyo wake ndi zochita zake. Iye anapemphera monga momwe anthu amapemphererera, ndipo anapemphereranso anthu. Pamenepo, mapemphero a anthu ngosatheka popanda chikhulupiriro. Kodi mapemphero a Yesu akanakhala otheka popanda chikhulupiriro?”
Ali chipachikire pamtengo wozunzirapo ali pafupi kufa, Yesu anafuula ndi liwu lokweza, akumagwira mawu salmo la Davide. Ndiyeno, mwa chikhulupiriro, ndi liwu lokweza, anafuula pembedzero lomalizira nati: “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga.” (Luka 23:46; Mateyu 27:46) Matembenuzidwe ena Achitaliyana a zipembedzo zoloŵana otchedwa Parola del Signore, amanena kuti Yesu ‘anaikiza moyo wake’ kwa Atateyo.
Jacques Guillet akunena kuti: “Mwa kutidziŵitsa za kupachikidwa kwa Kristu, kulilira Atate wake mwa kugwira mawu masalmo a Israyeli, olemba Mauthenga Abwino amatikhutiritsa kuti kulira kumeneko, kulira kwa Mwana wobadwa yekha, kulira kwa kusautsika kwenikweni, kulira kwa chidaliro chonse, ndiko kulira kwa chikhulupiriro, kulira kwa imfa m’chikhulupiriro.”
Poyang’anizana ndi umboni woonekeratu ndi waukulu umenewu wa chikhulupiriro, ophunzitsa zaumulungu ena amayesa kusiyanitsa chikhulupiriro ndi “chidaliro.” Komabe, kusiyanitsa koteroko kulibe maziko a Malemba.
Koma kodi nchiyani kwenikweni chimene mayesero osautsa amene iye anawapirira amasonyeza ponena za chikhulupiriro cha Yesu?
“Wokwaniritsa Chikhulupiriro Chathu” Akwaniritsidwa
M’chaputala cha 11 cha kalata yake kwa Ahebri, mtumwi Paulo akutchula mtambo waukulu wa amuna ndi akazi okhulupirika a m’nthaŵi za Chikristu chisanakhale. Iye akumaliza, mwa kusonya ku chitsanzo chachikulu koposa ndi changwiro cha chikhulupiriro kuti: ‘Tipenyerere [Woyambitsa ndi Wokwaniritsa, NW] chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi . . . Pakuti talingalirani iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m’moyo mwanu.’—Ahebri 12:1-3.
Ophunzitsa zaumulungu ochuluka amanena kuti vesi limeneli silimanena za “chikhulupiriro cha Yesu iye mwini” koma za mbali yake monga “woyambitsa kapena wokhazikitsa chikhulupiriro.” Liwu Lachigiriki lakuti te·lei·o·teś limene limapezeka pamawu ameneŵa limanena za munthu amene amakwaniritsa, amene amachita kapena kumaliza kanthu kena. Monga “Wokwaniritsa,” Yesu anamaliza chikhulupiriro m’lingaliro lakuti kubwera kwake padziko lapansi kunakwaniritsa maulosi a Baibulo motero anakhazikitsa maziko olimbirapo a chikhulupiriro. Koma kodi zimenezi zimatanthauza kuti iye analibe chikhulupiriro?
Ndime zochokera m’kalata ya kwa Ahebri zimene mutha kuona m’bokosilo patsamba 15 zimachotsa chikayikiro chilichonse. Yesu anakwaniritsidwa ndi zimene anavutika nazo ndi kumvera kwake. Ngakhale kuti anali kale munthu wangwiro, zokumana nazo zake zinampangitsa kukhala wangwiro ndi wokwanira m’zinthu zonse, ngakhale m’chikhulupiriro, kotero kuti akhale woyenerera bwino lomwe kukhala Mkulu Wansembe wa chipulumutso cha Akristu oona. Iye anapembedzera kwa Atate wake “pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi,” anali “wokhulupirika” kwa Mulungu, ndipo “anawopa Mulungu.” (Ahebri 3:1, 2; 5:7-9) Iye ‘anayesedwa m’zonse” mofananadi ndi “ife,” amatero Ahebri 4:15, ndiko kuti, mofanana ndi Mkristu aliyense wokhulupirika amene chikhulupiriro chake chimapyola “m’mayesero amitundumitundu.” (Yakobo 1:2, 3) Kodi nzomveka kukhulupirira kuti Yesu anaikidwa pachiyeso monga “momwe” anachitira otsatira ake koma chikhulupiriro chake osayesedwa monga momwe chawo chinayesedwera?
Mapembedzero, kumvera, kuvutika, mayesero, kukhulupirika, ndi kuwopa Mulungu zimachitira umboni chikhulupiriro chokwanira cha Yesu. Izo zimasonyeza kuti iye anakhala “Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu” kokha pamene anali atakwaniritsidwa m’chikhulupiriro. Mwachionekere, iye sanali Mulungu Mwana, monga momwe chiphunzitso cha Utatu chimanenera.—1 Yohane 5:5.
Kodi Iye Sanakhulupirire Mawu a Mulungu?
Chiphunzitso cha Utatu chimaumba kwambiri kalingaliridwe ka ophunzitsa zaumulungu kwakuti amafika pamlingo wonkitsa wa kukhulupirira kuti Yesu “sangakhulupirire Mawu a Mulungu ndi uthenga wa m’menemo” chifukwa chakuti “iye pokhala Mawu a Mulungu enieniwo, angangolengeza mawuwo.”—Angelo Amato, Gesù il Signore, lokhala ndi chilolezo cha tchalitchi cha kusindikiza.
Komabe, kodi kusonya ku Malemba kosalekeza kwa Yesu kumasonyezanji kwenikweni? Pamene anali kuyesedwa, iye anagwira mawu Malemba katatu. Yankho lake lachitatu linauza Satana kuti Yesu analambira Mulungu yekha. (Mateyu 4:4, 7, 10) Pazochitika zingapo Yesu anatchula maulosi omwe anasonya kwa iye, akumasonyeza chikhulupiriro chake m’kukwaniritsidwa kwake. (Marko 14:21, 27; Luka 18:31-33; 22:37; yerekezerani ndi Luka 9:22; 24:44-46.) Mwa kupenda kumeneku tiyenera kunena kuti Yesu anadziŵa Malemba ouziridwa ndi Atate wake, anawasunga mwa chikhulupiriro, ndipo anali ndi chidaliro chokwanira m’kukwaniritsidwa kwa maulosi omwe ananeneratu za mayesero ake, kuvutika, imfa, ndi chiukiriro chake.
Yesu, Chitsanzo cha Chikhulupiriro Choyenera Kutsanziridwa
Yesu anamenya nkhondo ya chikhulupiriro kufikira kumapeto kuti asunge kukhulupirika kwake kwa Atate wake ndi ‘kulaka dziko.’ (Yohane 16:33) Popanda chikhulupiriro, kuli kosatheka kupeza chilakiko choterocho. (Ahebri 11:6; 1 Yohane 5:4) Ponena za chikhulupiriro cholakika chimenecho, iye anali chitsanzo kwa otsatira ake okhulupirika. Iye analidi ndi chikhulupiriro mwa Mulungu woona.
[Mawu a M’munsi]
a Malongosoledwe ochuluka osonyeza kupanda maziko kwa chiphunzitso cha Utatu angapezedwe m’brosha lakuti Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Inc.
[Bokosi patsamba 15]
Yesu, “Wokwaniritsa,” Akwaniritsidwa
Ahebri 2:10: “Kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri aloŵe ulemerero, [kukwaniritsa, NW] mtsogoleri . . . wa chipulumutso chawo mwa zoŵaŵa.”
Ahebri 2:17, 18: “Kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m’zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m’zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu. Pakuti popeza adamva zoŵaŵa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.”
Ahebri 3:2: “Anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m’nyumba yake yonse.”
Ahebri 4:15: “Sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.”
Ahebri 5:7-9: “M’masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anawopa Mulungu, angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuŵaŵa nazo; ndipo pamene [anakwaniritsidwa] anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.”