“Ukwati Ukhaletu Wolemekezeka Pakati pa Onse”
“Ukwati ukhaletu wolemekezeka pakati pa onse, ndipo kama waukwati akhale wopanda chidetso.”—AHEBRI 13:4, NW.
1. Kodi anthu ambiri aphunziranji ponena za ukwati wachipambano?
ANTHU mamiliyoni ambiri, ngakhale m’nyengo ino imene chisudzulo chiri chosavuta, ali ndi maukwati okhalitsa. Apeza njira yopezera chipambano, mosasamala kanthu za kusiyana kwa maumunthu ndi kumene anachokera. Maukwati otero akupezeka pakati pa Mboni za Yehova. M’zochitika zochuluka okwatirana amenewa adzavomereza kuti akhala ndi nyengo zawo zakukondwera ndi za mavuto, ngakhale ndi zifukwa zodandaulira motsutsana wina ndi mnzake. Komabe, iwo aphunzira kupilira mavuto aang’ono ndi kuchititsa ukwati wawo kupitirizabe. Kodi ndizizoloŵezi zina ziti zimene zawakhozetsa kupitirizabe?—Akolose 3:13.
2. (a) Kodi ndizizoloŵezi zabwino ziti zimene zimalimbitsa ukwati? (b) Kodi ndizizoloŵezi ziti zimene zingaswe ukwati? (Wonani bokosi patsamba 14.)
2 Mawu onenedwa ndi ena amene maukwati awo Achikristu akhala achimwemwe ndi okhalitsa akusonyeza zimenezo. Mwamuna wina wokwatira kwa zaka 16 anati: “Nthaŵi iriyonse pamene vuto labuka, tapangadi kuyesayesa kumvetsera lingaliro la wina.” Izi zikugogomezera chimodzi cha zizoloŵezi zolimbikitsa m’maukwati ambiri—kulankhula zakukhosi, ndi kosabisa mawu. Mkazi wina, wokwatiwa kwa zaka 31, anati: “Kugwirana manja ndi kuchitira zinthu zoseketsa pamodzi kuti tipitirizebe kukondana pakati pathu nthaŵi zonse kwakhala chinthu choyamba.” Ndipo imeneyo iri mbali yowonjezera ya kulankhula. Okwatirana ena, amene atero pafupifupi zaka 40, anagogomezera kufunika kwa kukhala ndi mkhalidwe wakuseka, kukhala okhoza kudziseka ndi kusekana. Iwo ananenso kuti kunathandiza kuwona mikhalidwe yabwino koposa ndi yoipitsitsa mwa wina ndi mnzake ndi kukhozabe kusonyeza chikondi chokhulupirika. Mwamuna anatchula kufunitsitsa kuvomereza zophophonya ndiyeno kupepesa. Ngati pali mzimu wa kulapa, ukwati udzakhala wokhoza kupindika kulola kusinthika mmalo mwa kusweka.—Afilipi 2:1-4; 4:5, Kingdom Interlinear.
Kusintha kwa Mkhalidwe
3, 4. Kodi ndimasinthidwe otani m’kaimidwe kamaganizo amene achitika ponena za kukhulupirika muukwati? Kodi mungapereke zitsanzo?
3 Mkati mwa zaka makumi oŵerengeka zapitazo, padziko lonse lapansi, malingaliro asintha ponena za kukhulupirika mu ukwati. Anthu ena okwatirana amakhulupirira kuti palibe cholakwika kukhala ndi chibwenzi, mawu amakono olungamitsa chigololo, makamaka ngati mnzawo wamuukwatiyo akuchidziŵa ndipo akuchivomereza.
4 Woyang’anira Wachikristu wina anathirira ndemanga mkhalidwewo: “Dziko lafikira pakutaya kuyesayesa kwamphamvu kulikonse kwakukhala ndi moyo mogwirizana ndi makhalidwe abwino. Makhalidwe oyera afikira pakuwonedwa monga achikale.” Anthu otchuka andale zadziko, m’maseŵera, ndi m’zosangulutsa amaswa poyera miyezo ya Baibulo ya chikhalidwe cha mtima, ndipo anthu otero akupitirizabe kuwonedwa monga ngwazi. Kwenikweni palibe chitonzo chogwirizanitsidwa ndi mtundu uliwonse wa cholakwa cha makhalidwe kapena kululuzika. Kaŵirikaŵiri chiyero ndi umphumphu sizinaŵerengeredwe kwambiri m’chitaganya cha anthu otchedwa apamwamba. Pamenepa, mogwirizana ndi chiphunzitso chakuti ‘chimene chimagwira ntchito kwa munthu uyu chimagwiranso ntchito kwa winayo,’ anthu ochuluka amalondola chitsanzo chimenecho ndi kulolera zimene Mulungu amatsutsa. Kuli monga momwe Paulo adanenera mfundoyi: “Pokhala yopanda lingaliro lirilonse la makhalidwe abwino, inadzipereka ku khalidwe losadziletsa kuchita utchisi wa mtundu uliwonse waumbombo.”—Aefeso 4:19, NW; Miyambo 17:15; Aroma 1:24-28; 1 Akorinto 5:11.
5. (a) Kodi lingaliro la Mulungu nlotani pa chigololo? (b) Kodi chimaphatikizidwa nchiyani m’kugwiritsira ntchito kwa Baibulo liwu lakuti “dama”?
5 Miyezo ya Mulungu sinasinthe. Lingaliro lake nlakuti kukhalira limodzi popanda kulembetsa ukwati ndiko dama lachigololo. Kusakhulupirika mu ukwati kukali chikhalirebe chigololo.a Mtumwi Paulo anafotokoza momvekera bwino kuti: ‘Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, . . . sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa mzimu wa Mulungu wathu.’—1 Akorinto 6:9-11.
6. Kodi nchilimbikitso chotani chimene tingapeze m’mawu a Paulo pa 1 Akorinto 6:9-11?
6 Mfundo yolimbikitsa m’lemba limenelo ndiyo mawu a Paulo akutiwo: “Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa.” Inde, ambiri amene kalero anali mumkhalidwe wa dziko wosadziletsa wa “kuchita utchisi” analapa, anavomereza Kristu ndi nsembe yake, ndipo anayeretsedwa. Iwo asankha kukondweretsa Mulungu mwakukhala ndi miyoyo ya makhalidwe abwino ndipo chotulukapo chake nchakuti ali achimwemwe kwambiri.—1 Petro 4:3, 4.
7. Kodi nkusemphana kotani kumene kulipo m’kumvetsetsa liwulo “makhalidwe oipa, ndipo kodi lingaliro la Baibulo nlotani”?
7 Kumbali ina, mafotokozedwe a dziko lamakono a makhalidwe oipa ngopereŵera kwambiri kotero kuti samayenerana ndi lingaliro la Mulungu. Bukhu lotanthauzira mawu limafotokoza “mkhalidwe woipa” kukhala “khalidwe lotsutsana ndi makhalidwe ovomerezedwa.” “Makhalidwe ovomerezedwa,” a lerolino amene amalekerera kugonana popanda ukwati ndi kugonana kwa kunja kwa ukwati limodzi ndi kugonana kwa a ziŵalo zofanana, ndiwo amene Baibulo limatsutsa monga makhalidwe oipa. Inde, mogwirizana ndi lingaliro la Baibulo, makhalidwe oipa ndiwo kuswa kwakukulu lamulo la Mulungu la makhalidwe abwino.—Eksodo 20:14, 17; 1 Akorinto 6:18.
Mpingo Wachikristu Umayambukiridwa
8. Kodi ndimotani mmene makhalidwe oipa angayambukirire a mumpingo Wachikristu?
8 Makhalidwe oipa lerolino ali owanda kwambiri kotero kuti angathe kuyambukira ngakhale amumpingo Wachikristu. Angathe kuwayambukira kupyolera mwa maprogramu a TV owanda kwambiri, oluluzika, mavidiyo, ndi mabukhu osonkhezera chilakolako chakugonana. Ngakhale kuti Akristu oyambukiridwa ali chiŵerengero chochepa chabe, kuyenera kuvomerezedwa kuti milandu yambiri imene anthu amachotsedwera pa kukhala Mboni za Yehova chifukwa cha mkhalidwe wosalapa wosayenera Mkristu imaphatikizapo chisembwere. Kumbali yabwino, chiŵerengero chachikulu cha ochotsedwawo potsirizira pake amazindikira zolakwa zawo, amayambiranso njira yamoyo yoyera, ndipo m’kupita kwanthaŵi amabwezeretsedwera mumpingo.—Yerekezerani ndi Luka 15:11-32.
9. Kodi Satana amasonkhezera motani osasamalawo?
9 Palibe kukaikira kuti Satana akuyendayenda monga mkango wobuma, wokonzekera kulikwira osasamala. Machenjera ake, kapena ‘zochita zake zamachenjera,’ zikukola mumsampha Akristu osasamala chaka chirichonse. Mzimu wadziko lake umene ulipo nthaŵi zonse ngwadyera, wokonda zokondweretsa, ndi woluluzika. Umakondweretsa zilakolako zathupi. Umakana kudziletsa.—Aefeso 2:1, 2; 6:11, 12, NW mawu amtsinde; 1 Petro 5:8.
10. Kodi ndani amene amayesedwa, ndipo chifukwa ninji?
10 Kodi ndani mumpingo amene angakumane ndi ziyeso kuloŵa m’makhalidwe oipa? Akristu ochuluka, kaya akhale akulu mumpingo, oyang’anira oyendayenda, ziŵalo za pa Betele, apainiya olalikira maola ambiri mwezi uliwonse, makolo otanganitsidwa kulera ana, kapena achichepere oyang’anizana ndi chitsenderezo cha amsinkhu wawo. Chiyeso chathupi chimagwera onse. Kukopeka mtima pankhani zakugonana kungathe kuyambitsidwa panthaŵi imene kuli kosayembekezereka. Chotero Paulo anakhoza kulemba kuti: “Iye amene akuganiza kuti ali chiriri achenjere kuti angagwe. Palibe chiyeso chakugwerani kusiyapo chimene chiri chofala kwa amuna [ndi akazi].” Kuli komvetsa chisoni, kuti Akristu ena pokhala mmalo athayo agonjera kumsampha umenewu wachisembwere.—1 Akorinto 10:12, 13, NW.
Kukokedwa ndi Kunyengedwa
11-13. Kodi ndimikhalidwe ina iti yomwe yatsogolera m’makhalidwe oipa?
11 Kodi nziyeso ziti ndi mikhalidwe zimene zachititsa ena kuloŵa panjira yopusa yakuchita chigololo ndi dama? Mikhalidweyo njambiri ndipo njocholowana ndipo ingasiyane m’maiko osiyanasiyana kapena zitaganya. Komabe, pali mikhalidwe ina yofala imene imawonekera m’maiko ambiri. Mwachitsanzo, kwasimbidwa kuti ena alinganiza mapwando kumene zakumwa zoledzeretsa zinapezeka popanda chiletso. Ena akopeka ndi nyimbo zosonkhezera chilakolako za dziko ndi kuvina konyanyula. M’maiko ena a Afirika, muli amuna achuma—osakhulupirira—amene ali ndi adzakazi; akazi ena akopeka kufunafuna chisungiko m’zachuma mumkhalidwe wotero ngakhale kuti umaphatikizapo chisembwere. M’maiko ena amuna Achikristu asiya mabanja awo kukakhala kumigodi kapena kwina kulikonse. Pamenepo umphumphu wawo ndi kukhulupirika zimayesedwa kumlingo waukulu kapena m’njira zimene sakanakumana nazo akanakhala kumudzi kwawo.
12 M’maiko otukuka ena agwera mumsampha wa Satana mwakukhala kaŵirikaŵiri ndi munthu wa ziŵalo zosiyana ndipo popanda munthu wina wachitatu—monga ngati kukhala mopanikizana nthaŵi zonse m’galimoto pokaphunzira kuyendetsa galimoto.b Akulu ochita ntchito yaubusa afunikiranso kuchita mosamala kotero kuti asakhale okha ndi mlongo pompatsa uphungu. Zokambitsirana zingathe kukhala zodzutsa chilakolako ndipo zingatulukire mumkhalidwe wochititsa manyazi kwa onse aŵiri.—Yerekezerani ndi Marko 6:7; Machitidwe 15:40.
13 Mikhalidwe yotchulidwayo yachititsa Akristu ena kuchepetsa kukhala maso kwawo ndi kulowa m’machitachita a chisembwere. Monga momwedi zinaliri m’zaka za zana loyamba, iwo adzilola ‘kuyesedwa ndi kukokedwa ndi zilakolako zawo zathupi,’ zimene zatsogolera ku uchimo.—Yakobo 1:14, 15; 1 Akorinto 5:1; Agalatiya 5:19-21.
14. Kodi nchifukwa ninji dyera liri chochititsa chachikulu m’nkhani za chigololo?
14 Kupenda mosamalitsa ochotsedwawo kumasonyeza kuti machitidwe achisembwere ali ndi zochititsa zazikulu zofanana. M’zochitika zotero muli mpangidwe wadyera. Kodi tikutero chifukwa ninji? Chifukwa chakuti m’milandu yakuchita chigololo, munthu kapena anthu osalakwa amapwetekedwa. Angakhale wamuukwati walamulo. Motsimikizirika adzakhala ana, ngati alipo, chifukwa chakuti ngati chigololo chidzachititsa chisudzulo, ana, amene ali ndi chikhumbo chakupeza chitetezo cha banja logwirizana, angavutike koposa. Wochita chigololoyo akuganiza kwakukulukulu za chisangalalo cha iyemwini ndi phindu. Limenelo ndilo dyera.—Afilipi 2:1-4.
15. Kodi nchiyani chimene chingakhale chinali zochititsa zina zotsogolera kukuchita chigololo?
15 Kaŵirikaŵiri kuchita chigololo sindiko mchitidwe wamwadzidzidzi wochititsidwa ndi kufooka. Pakhala pali kunyonyotsoka kwapang’onopang’ono, ngakhale kosawoneka, mu ukwati weniweniwo. Mwinamwake kulankhulana kwafikira kukhala konyong’onya kapena kokakamiza. Pangakhale panali kulimbikitsana kochepekera. Aliyense wa iwo angakhale atalephera kuwona kufunika kwa mnzake. Okwatiranawo angakhale sanali kukhutiritsana pa mangawa aukwati kwanthaŵi yakutiyakuti. Ndithudi pamene chigololo chichitika, pakhalanso kuchepachepa kwa unansi ndi Mulungu. Yehova salinso wowonekera bwino monga Mulungu wamoyo amene akuwona maganizo athu onse ndi zochita. Kungakhale kwakuti m’maganizo a wochita chigololoyo, “Mulungu” wafikira kukhala mawu chabe, chinthu chopanda moyo chimene sichiri mbali ya moyo wa tsiku ndi tsiku. Pamenepo kumakhala kosavutirapo kuchimwira Mulungu.—Salmo 51:3, 4; 1 Akorinto 7:3-5; Ahebri 4:13; 11:27.
Chofunika Kukukaniza
16. Kodi ndimotani mmene Mkristu angakanizire chiyeso chakukhala wosakhulupirika?
16 Ngati Mkristu aliyense awona kuti ali kuyesedwa kuloŵa panjira ya kusakhulupirika, kodi ndizinthu ziti zimene ayenera kuzilingalira? Choyamba, ayenera kulingalira tanthauzo la chikondi Chachikristu, chochokera m’malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. Chikondi chakuthupi kapena chapakati pa mwamuna ndi mkazi sichiyenera kuloledwa konse kulamulira malingaliro a munthuwe ndi kusonkhezera kugwera m’kuchita dyera, lodzetsa mavuto kwa ena. Mmalo mwake, mkhalidwewo uyenera kupendedwa mogwirizana ndi lingaliro la Yehova. Uyenera kuwonedwa kwakukulukulu molingalira mpingo ndi mtonzo umene khalidwe loipalo likadzetsa pa mpingo ndi pa dzina la Yehova. (Salmo 101:3) Tsokalo lingapeŵedwe mwakukhala ndi maganizo a Kristu pankhaniyo ndiyeno kuchita moyenerera. Kumbukirani, chikondi chopanda dyera chonga cha Kristu sichimalephera konse.—Miyambo 6:32, 33; Mateyu 22:37-40; 1 Akorinto 13:5, 8.
17. Kodi ndizitsanzo zolimbikitsa zotani za kukhulupirika zimene tiri nazo?
17 Chofunika kukukaniza ndicho kulimbikitsa chikhulupiriro cha munthuwe ndi masomphenya achiyembekezo cha mtsogolo. Zimenezi zitanthauza kukumbukira kwambiri zitsanzo zapadera za umphumphu zimene amuna ndi akazi okhulupirika akale, ndi Yesu mwiniyo, anasiya. Paulo analemba kuti: “Chotero, pamenepa, chifukwa chakuti ife tiri ndi mtambo waukulu kwambiri wamboni wotizinga, tiyeninso tichotse cholemera chirichonse ndi tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tiyeni tithamange mwachipiriro mpikisano umene waikidwa pamaso pathu, pamene tikuyang’anitsitsa dwii pa Mtsogoleri ndi Wokwaniritsa wachikhulupiriro chathu, Yesu. Chifukwa cha chisangalalo chimene chinaikidwa pamaso pake iye anapirira mtengo wozunzirapo, akumanyoza manyazi, ndipo wakhala pansi kudzanja lamanja lampando wachifumu wa Mulungu. Ndithudi, lingalirani mosamalitsa uyo amene wapirira kulankhula kotsutsa koteroko kochitidwa ndi ochimwa motsutsana ndi zabwino za iwo eni, kuti inu musatope ndi kulefuka m’miyoyo yanu.” (Ahebri 12:1-3, NW) Mmalo mwakutaya padzala mgwirizano waukwatiwo, munthu wanzeru adzalingalira njira zakukonzera mowonongeka mulimonse kuti awukonzetse, chotero kupeŵa mbuna za machenjera ndi za chinyengo.—Yobu 24:15.
18. (a) Kodi nchifukwa ninji chiwembu liri liwu lonkitsa lofotokozera chigololo? (b) Kodi Mulungu amawona motani kukwaniritsa ziŵindo?
18 Kodi liwu lakutilo chiwembu, limene liri chipanduko nlonkitsa ponena za chisembwere? Chiwembu ndicho kusakhulupirika pa kudalirika kapena chidaliro. Ndithudi choŵinda cha ukwati chimaphatikizapo chidaliro ndi lonjezo la kukonda ndi kusamalira, ziipe zitani, m’nthaŵi zabwino ndi zoipa. Chimaphatikizapo kanthu kena kamene ambiri amalingalira kukhala kachikale m’nyengo zimene tikukhalamo—liwu lamunthuyo laulemu lonenedwa m’choŵinda chaukwati. Kusakhulupirika kuchidaliro chotero ndiko mpangidwe wachiwembu motsutsana ndi mnzanu wamuukwati. Lingaliro la Mulungu la choŵinda lafotokozedwa momvekera bwino m’Baibulo: ‘Utaŵinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwerera ndi zitsiru; chita chomwe unachiŵindacho.’—Mlaliki 5:4.
19. Kodi Satana akukondwera motsutsana nchiyani?
19 Pasakhale kukaikira kuli konse. Monga momwedi kumakhala chikondwerero chachikulu kumwamba pamene munthu mmodzi wochimwa apulumuka, chotero pamakhala chimwemwe chachikulu padziko lapansi pakati pa magulu a Satana, owoneka ndi osawoneka, pamene mmodzi wa Mboni za Yehova alephera kusunga umphumphu wake.—Luka 15:7; Chivumbulutso 12:12.
Ziyeso Zofala kwa Onse
20. Kodi tingakanize motani chiyeso? (2 Petro 2:9, 10)
20 Kodi chisembwere chiri chosapeŵeka m’zochitika zina? Kodi thupi ndi Satana ngamphamvu kwambiri kotero kuti Akristu sangathe kukaniza ndi kusunga umphumphu wawo? Paulo akupereka chilimbikitso m’mawu awa: ‘Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza, koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.’ M’dziko lamakono sitingapeŵe kotheratu chiyeso, koma mwakutembenukira kwa Mulungu m’pemphero, ndithudi tingathe kupirira ndi kugonjetsa chiyeso chirichonse.—1 Akorinto 10:13.
21. Kodi ndimafunso otani amene adzayankhidwa m’phunziro lathu lotsatira?
21 Kodi Mulungu amalonjeza chiyani kwa ife kutithandiza kupirira ziyeso ndi kutuluka tiri olakika? Kodi ife aliyense payekha tifunikira chiyani kuti titetezere maukwati athu, mabanja athu, kudzanso mbiri ya dzina la Yehova ndi ya mpingo? Nkhani yathu yotsatira idzayankha mafunso amenewo.
[Mawu a M’munsi]
a “‘Dama’ m’lingaliro lotakata, ndipo monga lagwiritsiridwa ntchito pa Mateyu 5:32 ndi 19:9, mwachiwonekere limasonya ku mitundu yambiri yamaunansi akugonana kosaloledwa ndi lamulo kapena koswa lamulo kwakunja kwaukwati. Porneia [liwu Lachigiriki logwiritsidwa ntchito m’malemba amenewo] limaphatikizapo kugwiritsidwa ntchito koipa kwa mpheto kochitidwa ndi munthu mmodzi kapena oposerapo (kaya kukhale mwanjira yachibadwa kapena yoluluzika); ndiponso, payenera kukhala panali chiŵalo china m’chisembwerecho—mwamuna kapena mkazi, kapena nyama.” (Nsanja ya Olonda, September 1, 1983, tsamba 31) Chigololo ndicho: “Kugonana kodzifunira pakati pa munthu wokwatira ndi munthu wina wosakhala mwamuna kapena mkazi wake walamulo.”—The American Heritage Dictionary of the English Language.
b Mwachiwonekere, pakakhala mikhalidwe yoyenerera pamene mbale akanyamula mlongo kumthandiza ndi choyendera, ndipo mikhalidwe yotero siyenera kuganiziridwa molakwa.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nzizoloŵezi zina ziti zimene zimathandiza kulimbitsa ukwati?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa lingaliro la dziko la makhalidwe abwino?
◻ Kodi nziti zimene ziri ziyeso zina ndi mikhalidwe zimene zingatsogolere ku chisembwere?
◻ Kodi chithandizo chachikulu chakukaniza uchimo nchiyani?
◻ Kodi Mulungu amatithandiza motani m’nthaŵi za chiyeso?
[Bokosi patsamba 14]
ZIZOLOŴEZI ZODZIŴIKA M’MAUKWATI OKHALITSA
◻ Kumamatira kwambiri ku malamulo a Baibulo amakhalidwe abwino
◻ Okwatirana onse aŵiri ali ndi unansi wolimba ndi Yehova
◻ Mwamuna amalemekeza mkazi wake, malingaliro ake ndi ziganizo zake
◻ Kulankhulana kwabwino kwa tsiku ndi tsiku
◻ Funafunani kukondweretsana
◻ Kuseketsana; kukhoza kudziseka
◻ Kuvomereza zolakwa; kukhululukira mwaufulu
◻ Kusonyezana chikondi monga mwamuna ndi mkazi
◻ Kukhala ogwirizana m’kulera ndi kulanga ana
◻ Nthaŵi zonse kugwirizana m’pemphero kwa Yehova
ZIZOLOŴEZI ZOIPA ZIMENE ZIMAFOOKETSA UKWATI
◻ Dyera ndi liuma
◻ Kulephera kuchitira zinthu pamodzi
◻ Kulankhula kosalimbikitsa
◻ Kusafunsana ndi mnzanu wamuukwati mokwanira
◻ Kuwawanya ndalama
◻ Kusiyanitsa miyezo pamene musamalira ana ndi/kapena ana olera
◻ Mwamuna kugwira ntchito kufikira usiku kapena kunyalanyaza banja moyanja ntchito zina
◻ Kulephera kusamalira zosoŵa zauzimu za banja
[Chithunzi patsamba 15]
Kusunga ukwati uli wolemekezeka kumadzetsa chimwemwe chokhalitsa