Kutumikira Yehova ndi Mzimu Wodzimana
“Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine.”—MATEYU 16:24.
1. Kodi ndimotani mmene Yesu anadziŵitsira ophunzira ake za imfa yake yoyandikirayo?
ALI munsi mwa Phiri la Hemoni lokutidwa pamwamba pake ndi chipale, Yesu Kristu afika panthaŵi ya chochitika chachikulu m’moyo wake. Chaka sichidzatha adakali ndi moyo. Iye akudziŵa zimenezo; koma ophunzira ake sakudziŵa. Tsopano nthaŵi yafika yakuti iwonso adziŵe. Inde, Yesu ananenapo za imfa yake yoyandikirayo pasadakhale, koma iyi ndiyo nthaŵi yoyamba pamene akulongosola zonse. (Mateyu 9:15; 12:40) Nkhani ya Mateyu imati: “Kuyambira pamenepo Yesu [Kristu, NW] anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe akulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.”—Mateyu 16:21; Marko 8:31, 32.
2. Kodi Petro anachita motani pamene Yesu anamuuza za kuvutika kumene kunali patsogolo Pake, ndipo kodi Yesu anayankha motani?
2 Imfa ya Yesu yayandikira. Komabe, Petro akunyanyuka pakumva lingaliro lochititsa mantha limenelo. Sakuvomereza kuti Mesiya adzaphedwadi. Chotero, Petro adzudzula Mbuye wake. Atasonkhezeredwa ndi zifukwa zake zabwino kwambiri, akumfulumiza mophanaphana ndi mtima nati: “Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa inu ayi.” Koma Yesu mwamsanga akutsutsa mwamphamvu kukoma mtima kwa Petro kolakwako, monga momwe munthu angatswanyire mutu wa njoka yaululu. “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.”—Mateyu 16:22, 23.
3. (a) Kodi ndimotani mmene Petro mosadziŵa anadzipangira mtumiki wa Satana? (b) Kodi Petro anali motani chokhumudwitsa panjira ya kudzimana?
3 Mosadziŵa, Petro wadzipanga mtumiki wa Satana. Kuyankha kwa Yesu nkotsimikizirika monga momwe anachitira poyankha Satana m’chipululu. Kumeneko Mdyerekezi anayesa Yesu ndi moyo wasavuta, ufumu wosavutikira. (Mateyu 4:1-10) Tsopano Petro akumlimbikitsa kusadzivutitsa kwambiri. Yesu akudziŵa kuti chimenechi sindicho chifuniro cha Atate wake. Moyo wake uyenera kukhala wodzimana, osati wodzikhutiritsa. (Mateyu 20:28) Petro akukhala chokhumudwitsa panjira yoteroyo; chifundo chake chokhala ndi cholinga chabwino chikukhala msampha.a Komabe, Yesu akuwona bwino lomwe kuti ngati asamalira lingaliro lililonse lopanda kudzimana, akataya chiyanjo cha Mulungu mwakukoledwa mumsampha wa imfa wa Satana.
4. Kodi nchifukwa ninji Yesu ndi otsatira ake sanafune moyo wodzifunira ubwino wokhawokha?
4 Chotero, lingaliro la Petro linafunikira kuwongoleredwa. Mawu ake kwa Yesu anasonyeza lingaliro la munthu, osati la Mulungu. Yesu sanafune moyo wofuna ubwino wokhawokha, njira yofeŵa yotulukira m’vuto; ndipo ngakhale otsatira ake sanayenera kufuna moyo woterowo, pakuti Yesu kenako akunena kwa Petro ndi ophunzira ake ena kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine.”—Mateyu 16:24.
5. (a) Kodi kukhala ndi moyo Wachikristu kuli ndi vuto lotani? (b) Kodi Mkristu ayenera kukhala wokonzekera kaamba ka zinthu zitatu zofunika zotani?
5 Mobwerezabwereza, Yesu akutchulanso mutu waukulu umenewu: vuto lokhala ndi moyo Wachikristu. Kuti akhale otsatira a Yesu, Akristu, mofanana ndi Mtsogoleri wawo, ayenera kutumikira Yehova ndi mzimu wodzimana. (Mateyu 10:37-39) Chotero, iye akundandalika zinthu zitatu zofunika zimene Mkristu ayenera kukhala wokonzekera kuchita: (1) kudzikana mwini yekha, (2) kunyamula mtengo wake wozunzirapo, ndi (3) kupitirizabe kumtsatira Iye.
“Ngati Munthu Afuna Kudza Pambuyo Panga”
6. (a) Kodi munthu amadzikana motani? (b) Kodi tiyenera kukondweretsa yani kuposa ife eni?
6 Kodi kudzikana kumatanthauzanji? Kumatanthauza kuti munthu ayenera kudzikana kotheratu, monga ngati imfa kwa iye yekha. Tanthauzo loyambirira la liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “kudzikana” ndilo “kunena kuti toto”; limatanthauza “kukana kwamtu wagalu.” Chifukwa chake, ngati mutenga thayo la moyo Wachikristu, mofunitsitsa muyenera kuleka zolakalaka zanu, ubwino, zikhumbo, chimwemwe, zokondweretsa. Kwenikwenidi, mumapatsa moyo wanu wonse ndi zonse zoloŵetsedwamo kwa Yehova Mulungu kunthaŵi yonse. Kudzikana kumatanthauza zoposa kungodzimana zokondweretsa zina mwakamodzikamodzi. Mmalomwake, kumatanthauza kuti munthuyo ayenera kupereka umwini wake wa iye yekha kwa Yehova. (1 Akorinto 6:19, 20) Munthu amene wadzikana samafuna kudzikondweretsa yekha, koma Mulungu. (Aroma 14:8; 15:3) Kumatanthauza kuti pamphindi iliyonse m’moyo wake, amakana zikhumbo zake zadyera ndi kuvomereza zofuna za Yehova.
7. Kodi mtengo wozunzirapo wa Mkristu nchiyani, ndipo amausenza motani?
7 Motero, kunyamula mtengo wanu wozunzirapo kumatanthauza zazikulu. Kusenza mtengowo ndiko nsautso ndi chizindikiro cha imfa. Mkristu amakhala wofunitsitsa kuvutika ngati kuli kofunika, kapena kuchititsidwa manyazi kapena kuzunzidwa kapena ngakhale kuphedwa chifukwa chakukhala wotsatira wa Yesu Kristu. Yesu anati: “Iye amene satenga [mtengo wake wozunzirapo, NW], natsata pambuyo panga, sayenera ine.” (Mateyu 10:38) Sikuti onse amene amavutika amanyamula mtengo wozunzirapo. Oipa ali ndi “zisoni” zambiri koma alibe mtengo wozunzirapo. (Salmo 32:10) Komabe, moyo wa Mkristu uli moyo wonyamula mtengo wozunzirapo wa utumiki wodzimana kwa Yehova.
8. Kodi Yesu anaikira otsatira ake chitsanzo cha moyo chotani?
8 Chifukwa chomalizira chimene Yesu anatchula ndicho chakuti tiyenera kumtsatira mosalekeza. Yesu samafuna kuti tingolandira ndi kukhulupirira zimene anaphunzitsa, komanso kuti kwa moyo wathu wonse, tipitirize kutsatira chitsanzo chimene anatipatsa. Ndipo kodi nziti zina za mbali zazikulu zimene tikuwona m’chitsanzo cha moyo wake? Pamene anapatsa otsatira ake malangizo omalizira, iye anati: “Chifukwa chake mukani ndi kupanga ophunzira . . . , mukumawaphunzitsa kusunga zinthu zonse ndakulamulirani.” (Mateyu 28:19, 20, NW) Yesu analalikira ndi kuphunzitsa mbiri yabwino ya Ufumu. Ophunzira ake omtsatira anateronso, ndiponso mpingo wonse woyambirira Wachikristu unatero. Ntchito yachangu imeneyi limodzinso ndi kusakhala kwawo mbali yadziko zinachititsa dziko kuwada ndi kuwatsutsa, kupangitsa mtengo wawo wozunzirapo kukhala wolemera kwambiri kusenza.—Yohane 15:19, 20; Machitidwe 8:4.
9. Kodi Yesu anawachitira motani anthu ena?
9 Chitsanzo china chachikulu chimene tikuwona m’moyo wa Yesu ndicho njira imene anachitira ndi anthu ena. Iye anali wokoma mtima ndi “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” Chifukwa chake, omvetsera ake anatsitsimulidwa ndipo analimbikitsidwa ndi kukhalapo kwake. (Mateyu 11:29) Iye sanawakakamize kuti amtsatire kapena kuwaikira malamulo ochuluka onena za mmene ayenera kutero; ndipotu sanawachititsa kumva aliwongo kotero kuti akakamizike kukhala ophunzira ake. Mosasamala kanthu za moyo wawo wodzimana, iwo anasonyeza chisangalalo chenicheni. Nkusiyana kwakukulu chotani nanga ndi awo okhala ndi mzimu wadziko wadyera umene umazindikiritsa “masiku otsiriza”!—2 Timoteo 3:1-4.
Kulitsani ndi Kusunga Mzimu Wodzimana wa Yesu
10. (a) Mogwirizana ndi Afilipi 2:5-8, kodi Yesu anadzikana motani? (b) Ngati tili otsatira a Kristu, kodi ndimkhalidwe wa maganizo wotani umene tiyenera kusonyeza?
10 Yesu mwiniyo anapereka chitsanzo cha kudzikana yekha. Iye ananyamula mtengo wake wozunzirapo napitiriza kuusenza mwakuchita chifuniro cha Atate wake. Paulo analembera Akristu a ku Filipi kuti: “Mukhale nawo mtima mkati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo mawonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’mawonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya [pamtengo wozunzirapo, NW].” (Afilipi 2:5-8) Kodi ndani amene angathe kudzikana mwanjira yoposa imeneyo? Ngati muli wa Kristu Yesu ndipo ndinu mmodzi wa otsatira ake, muyenera kusunga mkhalidwe wamaganizo umenewu.
11. Kodi kukhala ndi moyo wodzimana kumatanthauza kukhalira moyo chifuniro cha yani?
11 Mtumwi wina, Petro, akutiuza kuti popeza kuti Yesu anativutikira ndi kutifera, Akristu ayenera kunyamula zida, mofanana ndi asilikali okonzekera bwino, ndi mzimu wofananawo umene Kristu anali nawo. Iye akulemba kuti: “Popeza Kristu adamva zoŵaŵa m’thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zoŵaŵa m’thupi walekana nalo tchimo; kuti nthaŵi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.” (1 Petro 3:18; 4:1, 2) Moyo wa Yesu wodzimana unasonyeza bwino lomwe mmene anamverera ponena za chifuniro cha Mulungu. Iye anali nchinthu chimodzi m’maganizo m’kudzipereka kwake, nthaŵi zonse akumaika chifuniro cha Atate wake patsogolo pa chake, ngakhale kufikira imfa yonyazitsa.—Mateyu 6:10; Luka 22:42.
12. Kodi moyo wodzimana unali womuipira Yesu? Fotokozani.
12 Ngakhale kuti moyo wa Yesu wodzimana unali njira yothodwetsa ndi yopereka chiyeso kwa iye ndi otsatira ake, iye sanaipidwe nayo. M’malomwake, Yesu anasangalala pogonjera ku chifuniro cha Mulungu. Kwa iye, kuchita ntchito ya Atate wake kunali ngati chakudya. Inampatsa chikhutiritso chenicheni, monga momwedi munthu angakhutire ndi chakudya chabwino. (Mateyu 4:4; Yohane 4:34) Motero, ngati mufuna kukhaladi wokhutiritsidwa m’moyo wanu, palibe chimene mungachite choposa kutsatira chitsanzo cha Yesu mwakukulitsa mkhalidwe wake wa maganizo.
13. Kodi ndimotani mmene chikondi chiliri mphamvu yosonkhezera mzimu wodzimana?
13 Ndithudi, kodi nchiyani chimene chimasonkhezera mzimu wodzimana? M’liwu limodzi, chikondi. Yesu anati: “Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiŵiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (Mateyu 22:37-39) Mkristu sangakhale wofuna phindu la iye yekha, ndipo panthaŵi imodzimodziyo, nkumalabadira mawuwo. Chimwemwe chake ndi chikondwerero ziyenera kudalira kwakukulukulu pa chikondi chake kwa Yehova ndi kwa mnansi. Ndimmene Yesu anakhalira moyo wake, ndipo nzimene akuyembekezeranso otsatira ake kuchita.
14. (a) Kodi ndimathayo otani amene akulongosoledwa pa Ahebri 13:15, 16? (b) Kodi nchiyani chimene chimatisonkhezera kulalikira mbiri yabwino mwachangu?
14 Mtumwi Paulo anamvetsetsa lamulo la chikondi limeneli. Iye analemba kuti: “Mwa iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. Koma musaiŵale kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” (Ahebri 13:15, 16) Akristu samapereka kwa Yehova nsembe za nyama kapena zina zotero; motero, samafunikira ansembe aumunthu pakachisi wakuthupi kuwaimira m’kulambira kwawo. Nsembe yathu yachitamando timaipereka kupyolera mwa Kristu Yesu. Ndipo kwakukulukulu timasonyeza chikondi chathu kwa Mulungu mwa nsembe yachitamando imeneyo, chilengezo chapoyera cha dzina lake. Makamaka mzimu wathu wopanda dyera wozikidwa pachikondi umatisonkhezera kulalikira mbiri yabwino mwachangu, tikukhala okonzekera nthaŵi zonse kupereka kwa Mulungu chipatso cha milomo yathu. Mwanjira imeneyi timasonyezanso chikondi chathu kwa mnansi.
Kudzimana Kumadzetsa Madalitso Aakulu
15. Kodi ndimafunso akudzipenda otani onena za kudzimana amene tingadzifunse?
15 Taimani kaye ndi kulingalira mafunso otsatiraŵa: Kodi njira ya moyo wanga pakali pano imasonyeza mkhalidwe wa kudzimana? Kodi zonulirapo zanga zimasonyeza moyo woterowo? Kodi ziŵalo za banja langa zikututa zipatso zawo zauzimu mwa chitsanzo changa? (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:8.) Bwanji nanga za ana ndi akazi amasiye? Kodi nawonso amapindula mwa mzimu wanga wodzimana? (Yakobo 1:27) Kodi ndingathe kuwonjezera nthaŵi imene ndimathera m’kupereka nsembe yanga yachitamando yapoyera? Kodi ndikhoza kukalimira mwaŵi wa utumiki waupainiya, wa pa Beteli, kapena umishonale, kapena kodi ndingathe kusamukira kumene kusoŵa kwa olengeza Ufumu kuli kokulira?
16. Kodi kuchenjera kungatithandize motani kukhala ndi moyo wodzimana?
16 Nthaŵi zina pamangofunikira kuchenjera pang’ono kuti tifikire kukhoza kwathu kokwanira m’kutumikira Yehova ndi mzimu wodzimana. Mwachitsanzo, Janet, mpainiya wokhazikika mu Ecuador, ankagwira ntchito yakudziko ya tsiku lonse. Posakhalitsa, ndandanda yake inakuchititsa kukhala kovuta kwa iye kufitsa maola a mpainiya wokhazikika mwachisangalalo. Anasankha kufotokozera womlemba ntchito za vutolo napempha kumchepetsera maola a ntchito. Popeza kuti mwinintchitoyo anakana kumchepetsera maola antchito, mlongoyo tsopano anapita ndi Maria, yemwe anali kufunafuna ntchito ya theka la tsiku kuti achite upainiya. Aliyense wa aŵiriwo anapempha kugwira ntchito theka la tsiku, akumagaŵana ntchito ya tsiku lonse. Mwinintchitoyo anavomera lingalirolo. Tsopano alongo aŵiriwo ndiapainiya okhazikika. Atawona chotulukapo chabwino koposa chimenechi, Kaffa, amene nayenso anatopa ndi kugwira ntchito ya tsiku lonse pakampani imodzimodziyo ndipo akumavutikira kwambiri kuti akwaniritse maola ake aupainiya, anatengana ndi Magali nakapempha zofananazo. Nawonso anavomerezedwa. Motero, alongo anayi ali okhoza kuchita upainiya, mmalo mwa aŵiri amene anatsala pang’ono kuleka utumiki wanthaŵi yonse. Kuchenjera ndi kudzipezera njira kunadzetsa mapindu.
17-21. Kodi ndimotani mmene okwatirana aŵiri anapenderanso chifuno chawo m’moyo, nakhala ndi chotulukapo chotani?
17 Ndiponso, talingalirani kudzimana kumene Evonne anakuchita m’zaka khumi zapitazo. Iye analemba zotsatirazi ku Watch Tower Society m’May 1991:
18 “Mu October 1982, ine ndi banja lonse tinapita kukawona Beteli ya Brooklyn. Kuiwona kunandipangitsa kufuna kudzipereka pantchito kumeneko. Ndinaŵerenga fomu yofunsira, ndipo panali funso limodzi limene linandigwira mtima, ‘Kodi munali ndi avareji ya maola angati a utumiki wakumunda pamiyezi isanu ndi umodzi yapitayo? Ngati avareji yanu sinafike pamaola khumi, perekani chifukwa.’ Sindinapeze chifukwa chilichonse chomvekera bwino, chotero ndinaika chonulirapo ndi kuchifikira pamiyezi isanu.
19 “Ngakhale kuti ndinali ndi zifukwa zoŵerengeka zosachitira upainiya, pamene ndinaŵerenga 1983 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, ndinakhutiritsidwa kuti ena anagonjetsa zopinga zazikulu kuposa zanga kuti achite upainiya. Chotero, pa April 1, 1983, ndinasiya ntchito yanga ya tsiku lonse yapamwamba ndi kukhala mpainiya wothandiza, ndipo ndinayamba upainiya wokhazikika pa September 1, 1983.
20 “Pambuyo pake, ndinali wokondwa kukwatiwa ndi mtumiki wotumikira wabwino mu April 1985. Pambuyo pa zaka zitatu, nkhani ya pamsonkhano wachigawo yonena za upainiya inasonkhezera mwamuna wanga kundinong’oneza ndi kufunsa kuti, ‘Kodi ukuwona chifukwa chilichonse chondiletsa kuyamba upainiya pa September 1?’ Anagwirizana nane m’ntchitoyi kwa zaka ziŵiri zotsatira.
21 “Mwamuna wanga anadziperekanso kuchita ntchito yomanga pa Beteli ya Brooklyn kwa masabata aŵiri nafunsira kuloŵa m’gulu la antchito yomanga lotchedwa International Program. Chotero mu May 1989 tinapita ku Nigeria kwa mwezi umodzi kukathandiza kumanga nthambi. Maŵa tidzakhala tikupita ku Jeremani, kumene mavisa adzalinganizidwa oti tikaloŵere m’Poland. Tili achisangalalo kwambiri kukhalamo ndi phande m’ntchito yomanga yopanga mbiri imeneyi ndi kukhala mbali ya mtundu watsopano umenewu wa utumiki wanthaŵi yonse.”
22. (a) Kodi ndimotani mmene ife, mofanana ndi Petro, tingakhalire chokhumudwitsa mosadziŵa? (b) Kodi kutumikira Yehova ndi mzimu wodzimana sikumadalira pachiyani?
22 Ngati inuyo simuli okhoza kuchita upainiya, kodi mungalimbikitse awo amene ali muutumiki wanthaŵi yonse kuti amamatire kumwaŵi wawo ndipo mwinamwake ngakhale kuwathandiza kutero? Kapena kodi mudzafanana ndi ziŵalo za banja zina kapena mabwenzi okhala ndi chifuno chabwino amene, mofanana ndi Petro, angauze mtumiki wanthaŵi yonse kusadzivutitsa kwambiri, kudzikomera mtima, osazindikira mmene kumeneko kungakhalire kokhumudwitsa? Zowona, ngati mpainiya amadwaladwala kwambiri kapena akunyalanyaza mathayo Achikristu, iye angafunikire kuleka utumiki wanthaŵi yonse kwakanthaŵi. Kutumikira Yehova ndi mzimu wodzimana sikumadalira pa dzina lakuti mpainiya, wa pa Beteli, kapena ena otero. Mmalomwake, kumadalira pa amene tili monga munthu—mmene timaganizira, zimene timachita, mmene timachitira kwa ena, mmene timakhalira ndi moyo wathu.
23. (a) Kodi tingapitirize motani kukhala ndi chimwemwe cha kukhala antchito anzake a Mulungu? (b) Kodi timapeza chitsimikizo chotani pa Ahebri 6:10-12?
23 Ngati tilidi ndi mzimu wodzimana, tidzakhala ndi chimwemwe cha kukhala antchito anzake a Mulungu. (1 Akorinto 3:9) Tidzakhala ndi chikhutiro cha kudziŵa kuti tikukondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Ndipo tili ndi chitsimikiziro chakuti Yehova sadzatiiŵala konse kapena kutisiya malinga ngati tikhalabe okhulupirika kwa iye.—Ahebri 6:10-12.
[Mawu a M’munsi]
a M’Chigiriki, liwu lakuti “chokhumudwitsa” (σκάνδαλον, skanʹda·lon) poyambirira “linali dzina la mbali ya msampha kumene nyambo inaikidwako, chotero, linatchula msampha weniweniwo kapena diŵa.”—Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words.
Kodi Malingaliro Anu Ngotani?
◻ Kodi ndimotani mmene Petro mosadziŵa anakhalira chokhumudwitsa panjira ya moyo wodzimana?
◻ Kodi kudzikana kumatanthauzanji?
◻ Kodi ndimotani mmene Mkristu amasenzera mtengo wake wozunzirapo?
◻ Kodi timaukulitsa motani mzimu wodzimana ndi kuusunga?
◻ Kodi nchiyani chimene chili mphamvu yosonkhezera mzimu wodzimana?
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi muli ofunitsitsa kudzikana nokha, kunyamula mtengo wanu wozunzirapo, ndi kupitiriza kumtsatira Yesu?