NKHANI YOPHUNZIRA 42
Kodi Ndinu ‘Okonzeka Kumvera’?
“Nzeru yochokera kumwamba . . . ndi . . . yokonzeka kumvera.”—YAK. 3:17.
NYIMBO NA. 101 Tizigwira Ntchito Mogwirizana
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. N’chifukwa chiyani timavutika kukhala omvera?
KODI nthawi zina zimakuvutani kukhala omvera? Zimenezi zinkachitikiranso Mfumu Davide. Choncho iye anapemphera kwa Mulungu kuti: “Ndichirikizeni ndi mzimu wofunitsitsa [kumvera].” (Sal. 51:12) Davide ankakonda Yehova. Komabe, nthawi zina iye ankavutika kumvera ngati mmenenso zimakhalira ndi ifeyo. Chifukwa chiyani? Choyamba, tinatengera mtima wosafuna kumvera. Chachiwiri, nthawi zambiri Satana amachititsa kuti tisamvere Yehova ngati mmene iyeyo anachitira. (2 Akor. 11:3) Chachitatu, tikukhala m’dziko limene anthu ali ndi ‘kaganizidwe kamene tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.’ (Aef. 2:2) Tizichita khama kuti tizitha kulimbana ndi mtima wofuna kuchita tchimo komanso kupewa zimene Mdyerekezi ndi anthu a m’dzikoli amatilimbikitsa kuchita kuti tikhale osamvera. Tiyenera kuyesetsa kuti tizimvera Yehova komanso anthu amene wawasankha kuti azititsogolera.
2. Kodi kukhala ‘okonzeka kumvera’ kumatanthauza chiyani? (Yakobo 3:17)
2 Werengani Yakobo 3:17. Yakobo anauziridwa kulemba kuti anthu anzeru amakhala ‘okonzeka kumvera.’ Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Tiyenera kukhala ofunitsitsa komanso okonzeka kumvera anthu amene Yehova wawapatsa udindo. Komabe, Yehova samayembekezera kuti tizimvera anthu amene akutipempha kuti tichite zinthu zosemphana ndi malamulo ake.—Mac. 4:18-20.
3. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizimvera anthu amene amatitsogolera?
3 Nthawi zina tingamaone kuti n’zosavuta kumvera Yehova kusiyana ndi kumvera munthu. Ndipotu Yehova nthawi zonse amatipatsa malangizo abwino. (Sal. 19:7) Zimenezitu n’zosiyana kwambiri ndi anthu omwe ali ndi udindo. Ngakhale zili choncho, Atate wathu wakumwamba anapereka udindo kwa makolo, akulu mumpingo komanso akuluakulu a boma. (Miy. 6:20; 1 Ates. 5:12; 1 Pet. 2:13, 14) Tikamamvera anthu amenewa timakhala tikumvera Yehova. Tiyeni tione zimene tingachite kuti tizimvera anthu omwe Yehova wawapatsa udindo ngakhale kuti nthawi zina tingamaone kuti n’zovuta kuvomereza kapena kutsatira malangizo awo.
MUZIMVERA MAKOLO ANU
4. N’chifukwa chiyani ana ambiri samvera makolo awo?
4 Nthawi zambiri achinyamata amakhala ndi anzawo omwe ndi “osamvera makolo.” (2 Tim. 3:1, 2) N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri samamvera? Ena amaona kuti makolo awo ndi achinyengo. Anawo amauzidwa kuti azichita zimene makolowo sachita. Ena amaona kuti malangizo a makolo awo ndi achikale, osathandiza kapena opanikiza. Ngati ndinu wachinyamata, kodi inunso mumaona choncho? Ambiri amavutika kutsatira lamulo la Yehova lakuti: “Muzimvera makolo anu mwa Ambuye, pakuti kuchita zimenezi n’chilungamo.” (Aef. 6:1) Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzimvera?
5. Mogwirizana ndi Luka 2:46-52, n’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti Yesu ankamvera makolo ake?
5 Mungathe kuphunzira kumvera kuchokera kwa Yesu, yemwe ndi chitsanzo chabwino. (1 Pet. 2:21-24) Iye anali wangwiro, koma makolo ake sanali angwiro. Yesu ankalemekeza makolo ake ngakhale kuti nthawi zina iwo ankalakwitsa zinthu komanso sankamumvetsa. (Eks. 20:12) Chitsanzo ndi zimene zinachitika Yesu ali ndi zaka 12. (Werengani Luka 2:46-52.) Makolo ake anamusiya ku Yerusalemu. Yosefe ndi Mariya anali ndi udindo woonetsetsa kuti ana awo onse ali nawo limodzi pamene ankabwerera kunyumba kuchokera kuchikondwerero. Iwo atamupeza, Mariya anamuimba Yesu mlandu kuti anawavutitsa. Yesu akanatha kunena kuti iwo sanachite chilungamo. M’malomwake anayankha makolo akewo mwachidule komanso mwaulemu. Koma Yosefe ndi Mariya “sanamvetse zimene anali kuwauzazo.” Ngakhale zinali choncho, Yesu “anapitiriza kuwamvera.”
6-7. N’chiyani chingathandize achinyamata kuti azimvera makolo awo?
6 Kodi zimakuvutani kumvera makolo anu chifukwa chakuti amalakwitsa zinthu zina kapena sakumvetsani? Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni? Choyamba muziganizira mmene Yehova amamvera. Baibulo limanena kuti mukamamvera makolo anu ‘mumakondweretsa Ambuye.’ (Akol. 3:20) Yehova amadziwa ngati makolo anu sakumvetsani kapenanso ngati amakupatsani malamulo ovuta kuwatsatira. Komabe mukasankha kuwamvera, iye amasangalala.
7 Chachiwiri, muziganizira mmene makolo anu amamvera. Mukamamvera makolo anu, iwo amasangalala komanso kukukhulupirirani. (Miy. 23:22-25) Inunso mumayamba kugwirizana nawo kwambiri. M’bale wina wa ku Belgium, dzina lake Alexandre, ananena kuti: “Nditayamba kumvera makolo anga, tinayamba kugwirizana kwambiri ndipo tinkasangalala.”b Chachitatu, muziganizira mmene kumvera makolo anu panopa kungadzakuthandizireni m’tsogolo. Paulo, yemwe amakhala ku Brazil, ananena kuti: “Kumvera makolo anga kwandithandiza kuti ndizimvera Yehova komanso anthu ena audindo.” Mawu a Mulungu amatiuza chifukwa chabwino chotichititsa kumvera makolo. Amati: “Kuti zinthu zikuyendere bwino, ndiponso kuti ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.”—Aef. 6: 2, 3.
8. N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri amasankha kumvera makolo awo?
8 Achinyamata ambiri amaona kuti zinthu zimawayendera bwino akamamvera makolo awo. Luiza, yemwenso ndi wa ku Brazil, zinkamuvuta kumvetsa chifukwa chake makolo ake sankamulola kukhala ndi foni pa nthawi inayake. Zinkamudabwitsa chifukwa achinyamata ambiri amsinkhu wake anali ndi mafoni. Koma kenako anazindikira kuti makolo akewo ankamuteteza. Panopa iye amanena kuti: “Ndimaona kuti kumvera makolo anga si kopanikiza, koma kumanditeteza.” Mlongo wina wachitsikana wa ku United States dzina lake Elizabeth, nthawi zina zimamuvutabe kumvera makolo ake. Iye anati: “Ndikaona kuti sindikumvetsa chifukwa chake makolo anga akhazikitsira lamulo linalake, ndimaganizira mmene malamulo awo ananditetezera m’mbuyomu.” Monica, yemwe amakhala ku Armenia, ananena kuti nthawi zonse zinthu zimamuyendera bwino akamvera makolo ake, mosiyana ndi mmene zimakhalira akapanda kuwamvera.
‘MUZIMVERA OLAMULIRA AKULUAKULU’
9. Kodi maganizo a anthu ambiri ndi otani pa nkhani yomvera malamulo?
9 Anthu ambiri amavomereza kuti maboma ndi ofunika komanso kuti tiyenera kumvera ena mwa malamulo omwe “olamulira akuluakulu” amapereka. (Aroma 13:1) Koma anthu omwewo safuna kumvera lamulo limene sakulikonda kapenanso limene akuliona kuti si lachilungamo. Chitsanzo ndi zimene anthu amachita pa nkhani yolipira misonkho. Kafukufuku wina yemwe anachitika m’dziko lina ku Europe, anasonyeza kuti anthu ambiri ankakhulupirira kuti “ndi bwino kusapereka msonkho ngati ukuona kuti si wachilungamo.” Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri m’dzikolo samapereka misonkho yonse yomwe amafunika kupereka ku boma.
10. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera malamulo ngakhale amene satisangalatsa?
10 Baibulo limanena kuti maboma a anthu amayambitsa mavuto komanso kuti ali m’manja mwa Satana ndipo awonongedwa posachedwapa. (Sal. 110:5, 6; Mlal. 8:9; Luka 4:5, 6) Limanenanso kuti “aliyense amene akutsutsana ndi ulamuliro akutsutsana ndi dongosolo la Mulungu.” Panopa Yehova walola kuti maboma azilamulira n’cholinga choti pasakhale chisokonezo ndipo amayembekezera kuti tiziwamvera. Choncho tiyenera ‘kupereka kwa onse zimene amafuna,’ zomwe zikuphatikizapo misonkho, ulemu komanso kumvera. (Aroma 13:1-7) Tikhoza kumaona lamulo linalake ngati losayenera, lopanda chilungamo kapenanso lovuta kulimvera. Koma timamvera olamulirawa chifukwa Yehova amatiuza kuti tizitero ngati malamulo awowo sakusemphana ndi zimene iye amafuna.—Mac. 5:29.
11-12. Mogwirizana ndi Luka 2:1-6, kodi Yosefe ndi Mariya anachita zotani kuti amvere lamulo lovuta, nanga zotsatira zake zinali zotani? (Onaninso zithunzi.)
11 Tingaphunzirepo kanthu pa chitsanzo cha Yosefe ndi Mariya, omwe anali okonzeka kumvera olamulira akuluakulu ngakhale pamene zinali zovuta kutero. (Werengani Luka 2:1-6.) Pamene Mariya anali woyembekezera kwa miyezi 9, iye ndi Yosefe anauzidwa kuti achite zinthu zovuta. Augusto yemwe anali wolamulira wa ufumu wa Roma, anali atalamula kuti anthu akalembetse m’kaundula. Yosefe ndi Mariya ankafunika kuyenda ulendo wovuta wodutsa m’mapiri kupita ku Betelehemu, umene unali wamakilomita pafupifupi 150. Ulendo umenewu unali wovuta kwambiri, makamaka kwa Mariya. Iwo akanamadera nkhawa kwambiri zokhudza thanzi la Mariya komanso mwana amene ankayembekezerayo. Kodi zikanakhala bwanji ngati matenda akanamuyambira pamsewu? Iye amayembekezera kudzabereka mwana yemwe adzakhale Mesiya. Koma kodi zimenezi zinachititsa kuti iwo asamvere lamulo la boma?
12 Yosefe ndi Mariya sanalole kuti zinthu zimenezi ziwalepheretse kumvera lamulo. Yehova anawadalitsa chifukwa cha kumvera kwawo. Mariya anafika bwinobwino ku Betelehemu, anabereka mwana wathanzi ndipo anathandiza kuti ulosi wa m’Baibulo ukwaniritsidwe.—Mika 5:2.
13. Tikakhala omvera, kodi zingathandize bwanji abale athu?
13 Tikamamvera olamulira akuluakulu, zimathandiza kuti zinthu zitiyendere bwino ifeyo komanso anthu ena. N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, timapewa chilango chimene chimaperekedwa kwa anthu osamvera malamulo. (Aroma 13:4) Tikamamvera olamulira, iwo amaona kuti a Mboni za Yehova onse ndi anthu omvera. Mwachitsanzo, zaka zambiri m’mbuyomo, asilikali analowa m’Nyumba ya Ufumu ku Nigeria misonkhano ili m’kati. Iwo ankafufuza anthu amene ankachita zionetsero posafuna kupereka misonkho. Koma mkulu wa asilikaliwo anawauza kuti achoke ndipo ananena kuti: “A Mboni za Yehova nthawi zonse amapereka misonkho.” Nthawi iliyonse imene mwamvera lamulo, mumathandiza kuti anthu a Yehova akhale ndi mbiri yabwino ndipo zimenezi zikhoza kudzateteza Akhristu anzanu m’tsogolo.—Mat. 5:16.
14. N’chiyani chinathandiza mlongo wina kukhala ‘wokonzeka kumvera’ olamulira akuluakulu?
14 Nthawi zina tikhoza kumavutika kumvera olamulira akuluakulu. Mlongo wina wa ku United States, dzina lake Joanna, ananena kuti: “Zinali zovuta kwambiri kuti ndikhale womvera chifukwa anthu ena a m’banja langa anachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo ndi akuluakulu a boma.” Koma Joanna anayesetsa kuti asinthe maganizo ake. Choyamba, anasiya kuwerenga nkhani za pa intaneti zomwe zinkamuchititsa kudana kwambiri ndi akuluakulu a boma. (Miy. 20:3) Chachiwiri, anapempha Yehova kuti amuthandize kuti azimukhulupirira kwambiri, m’malo moganiza kuti kusintha boma kungathandize. (Sal. 9:9, 10) Chachitatu, anawerenga nkhani za m’mabuku athu zokhudza kusalowerera ndale. (Yoh. 17:16) Joanna ananena kuti panopa kulemekeza komanso kumvera akuluakulu a boma kwamuthandiza kukhala ndi “mtendere wosaneneka.”
TIZIMVERA MALANGIZO OCHOKERA KU GULU LA YEHOVA
15. N’chifukwa chiyani nthawi zina zingativute kumvera malangizo ochokera ku gulu la Yehova?
15 Yehova amatiuza kuti ‘tizimvera amene akutsogolera’ mumpingo. (Aheb. 13:17) Ngakhale kuti Mtsogoleri wathu Yesu ndi wangwiro, anthu amene amawagwiritsa ntchito kuti azititsogolera, si angwiro. Choncho zingamativute kuwamvera, makamaka ngati atiuza kuti tichite zinthu zimene sitikufuna. Pa nthawi ina, mtumwi Petulo sankafuna kumvera malangizo amene anapatsidwa. Mngelo atamuuza kuti adye nyama zimene zinali zodetsedwa mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, iye anakana, osati kamodzi kokha koma katatu. (Mac. 10:9-16) N’chifukwa chiyani anakana? Iye ankaona kuti malangizo atsopanowo anali osamveka. Anali atazolowera kuchita zinthu m’njira ina. Ngati Petulo zinamuvuta kumvera malangizo ochokera kwa mngelo wangwiro, ndiye kuli bwanji ifeyo? Nafenso nthawi zina zingativute kumvera malangizo ochokera kwa abale omwe si angwiro.
16. Kodi Paulo anatani ngakhale kuti malangizo amene anapatsidwa ankaoneka kuti ndi osamveka? (Machitidwe 21:23, 24, 26)
16 Mtumwi Paulo anali ‘wokonzeka kumvera’ ngakhale pamene analandira malangizo ooneka ngati osamveka. Akhristu a Chiyuda anali atamva mphekesera zakuti Paulo ankalalikira zoti anthu “apandukire Chilamulo cha Mose” ndiponso sankalemekeza Chilamulocho. (Mac. 21:21) Akulu a ku Yerusalemu analangiza Paulo kuti apite kukachisi ndi amuna 4 ndipo akadziyeretse posonyeza kuti amatsatira Chilamulo. Koma Paulo ankadziwa kuti Akhristu sankatsatiranso Chilamulo ndipo sanalakwitse chilichonse. Komabe nthawi yomweyo, iye anamvera zimene anamuuza. Choncho Paulo “anatenga amunawo tsiku lotsatira ndi kukachita mwambo wa kudziyeretsa pamodzi ndi iwo.” (Werengani Machitidwe 21:23, 24, 26.) Zimene anachitazi zinathandiza kuti pakhale mgwirizano.—Aroma 14:19, 21
17. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Stephanie?
17 Mlongo wina dzina lake Stephanie zinamuvuta kumvera zimene abale audindo anasankha m’dziko lake. Iye ndi mwamuna wake ankasangalala kutumikira m’kagulu ka chilankhulo china. Kenako ofesi ya nthambi inathetsa kaguluko ndipo banjali linafunika kubwerera kumpingo wachilankhulo chawo. Stephanie anati: “Zimenezi sizinandisangalatse. Ndinkaona kuti m’gawo la chilankhulo chathu muli kale olalikira ambiri.” Ngakhale zinali choncho, iye anaganiza zotsatira malangizo atsopanowo. Iye anati: “Patapita nthawi, ndinaona kuti malangizowo anali anzeru. Panopa tili ngati makolo auzimu a anthu ambiri mumpingo, omwe achibale awo sali mu choonadi. Ndikuphunzira ndi mlongo wina amene wathandizidwa kuti ayambirenso kusonkhana. Ndipo ndili ndi nthawi yambiri yophunzira pandekha. Tsopano ndili ndi chikumbumtima chabwino podziwa kuti ndayesetsa kukhala womvera.”
18. Kodi timapindula bwanji chifukwa chokhala omvera?
18 Tingathe kuphunzira kukhala omvera. Yesu “anaphunzira kumvera” osati chifukwa chakuti zinthu zinali bwino, koma chifukwa cha “mavuto amene anakumana nawo.” (Aheb. 5:8) Mofanana ndi Yesu, ifenso tingaphunzire kukhala omvera pamene takumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, chakumayambiriro kwa mliri wa COVID-19, tinalangizidwa kuti tisiye kupita ku Nyumba za Ufumu komanso kulalikira kunyumba ndi nyumba. Kodi inuyo zinakuvutani kumvera? Komatu kumvera kwanu kunakutetezani, kunathandiza kuti muzigwirizana ndi abale ndi alongo ndiponso kunasangalatsa Yehova. Panopa, tonsefe ndife okonzeka kudzamvera malangizo alionse amene tingadzalandire pa chisautso chachikulu. Kumvera kungadzathandize kuti tipulumuke.—Yobu 36:11.
19. N’chifukwa chiyani inuyo mumafuna kukhala omvera?
19 Munkhaniyi, taphunzira kuti kumvera kumabweretsa madalitso ambiri. Koma chifukwa chachikulu chimene chimatichititsa kumvera Yehova ndi chakuti timamukonda komanso timafuna kumusangalatsa. (1 Yoh. 5:3) Sitingathe kubwezera Yehova pa zabwino zonse zimene watichitira. (Sal. 116:12) Koma tingathe kumumvera komanso kumvera anthu amene wawalola kuti azititsogolera. Tikamamvera timasonyeza kuti ndife anzeru ndipo anthu anzeru amakondweretsa mtima wa Yehova.—Miy. 27:11.
NYIMBO NA. 89 Khalani Omvera Kuti Mulandire Madalitso
a Popeza si ife angwiro, nthawi zina timavutika kukhala omvera ngakhale pamene munthu amene akutipatsa malangizoyo ali ndi udindo woyenera kuchita zimenezo. Munkhaniyi, tiona mmene timapindulira ngati timamvera makolo athu, “olamulira akuluakulu” ndiponso abale amene amatsogolera mumpingo.
b Kuti mudziwe zimene mungachite polankhulana ndi makolo anu zokhudza malamulo omwe mukuona kuti ndi ovuta kuwamvera, onani nkhani ya pa jw.org yamutu wakuti, “Kodi Ndingakambirane Bwanji ndi Makolo Anga za Malamulo Amene Anakhazikitsa?”
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Yosefe ndi Mariya anamvera lamulo la Kaisara loti apite kukalembetsa ku Betelehemu. Akhristu masiku ano amamvera malamulo apansewu, malamulo okhudza misonkho ndiponso malangizo azaumoyo operekedwa ndi olamulira akuluakulu