MUTU 20
“Ali ndi Mtima Wanzeru” Koma Ndi Wodzichepetsa
1-3. N’chiyani chimatitsimikizira kuti Yehova ndi wodzichepetsa?
BAMBO akufuna kuphunzitsa mwana wake wamng’ono mfundo yofunika kwambiri. Akufunitsitsa kuti imufike pamtima. Kodi ayenera kumuphunzitsa bwanji? Kodi ayenera kuimirira momuopseza n’kumalankhula mwaukali? Kapena kodi ayenera kugwada kuti afanane ndi msinkhu wa mwanayo n’kumalankhula modekha komanso mokoma mtima? Kunena zoona, ngati bamboyo ndi wanzeru ndiponso wodzichepetsa angasankhe kulankhula naye mokoma mtima.
2 Kodi Yehova ndi Bambo wotani? Wodzikuza kapena wodzichepetsa? Waukali kapena wodekha? Yehova amadziwa zonse ndipo ndi wanzeru kuposa aliyense. Komabe mwina mukudziwa kuti si nthawi zonse pamene munthu wodziwa zinthu ndiponso wanzeru amakhala wodzichepetsa. Paja Baibulo limanena kuti “kudziwa zinthu kumachititsa munthu kukhala wodzikuza.” (1 Akorinto 3:19; 8:1) Koma ngakhale kuti “ali ndi mtima wanzeru,” Yehova ndi wodzichepetsa. (Yobu 9:4) Zimenezi sizikutanthauza kuti ndi wotsika kapenanso si wamkulu, zikungotanthauza kuti si wodzikuza. N’chifukwa chiyani tikutero?
3 Yehova ndi woyera. Choncho iye si wodzikuza chifukwa kudzikuza kumaipitsa munthu. (Maliko 7:20-22) Taonani zimene mneneri Yeremiya anauza Yehova. Iye anati: “Ndithu mudzandikumbukira ndi kundiweramira kuti mundithandize.”a (Maliro 3:20) Tangoganizani. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa anali wofunitsitsa ‘kuwerama,’ kapena kuti kugwada kuti afanane msinkhu ndi Yeremiya, n’cholinga choti athandize munthu yemwe sanali wangwiroyu. (Salimo 113:7) Kunena zoona, Yehova ndi wodzichepetsa. Koma kodi Mulungu amasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa? Kodi kudzichepetsa n’kogwirizana bwanji ndi kukhala wanzeru? Nanga kudzichepetsa kwa Yehova kumatithandiza bwanji?
Kodi Yehova Amasonyeza Bwanji Kuti Ndi Wodzichepetsa?
4, 5. (a) Kodi kudzichepetsa n’chiyani, nanga timadziwa bwanji kuti munthu ndi wodzichepetsa? N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti munthu wodzichepetsa ndi wofooka kapena wamantha? (b) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kudzichepetsa tikaganizira mmene anachitira zinthu ndi Davide, nanga kudzichepetsa kwa Yehova kumatithandiza bwanji?
4 Kudzichepetsa kumatanthauza kusadzikuza, kusadzikweza ndiponso kusakhala wonyada. Kudzichepetsa kumachokera mumtima ndipo munthu amene ali ndi khalidweli amakhalanso wofatsa, woleza mtima komanso wololera. (Agalatiya 5:22, 23) Komabe, tisamaganize kuti popeza Yehova ndi wodzichepetsa, wofatsa ndiponso woleza mtima, ndiye kuti sangakwiye ndi zinthu zopanda chilungamo. Tisamaganizenso kuti ndi wofooka kapena wamantha ndipo sangagwiritse ntchito mphamvu zake zowononga. M’malomwake, pokhala wodzichepetsa komanso wofatsa, Yehova amasonyeza kuti ali ndi mphamvu zopanda malire moti amatha kudziletsa bwinobwino. (Yesaya 42:14) Ndiye kodi kudzichepetsa kumagwirizana bwanji ndi nzeru? Buku lina lofotokoza za m’Baibulo limati: “Mwachidule tinganene kuti munthu amadziwika kuti ndi wodzichepetsa . . . ngati ali wosadzikonda ndipo kudzichepetsa n’kofunika kwambiri kuti munthu athe kuchita zinthu mwanzeru pa chilichonse.” Choncho munthu sangakhale ndi nzeru zenizeni ngati si wodzichepetsa. Kodi kudzichepetsa kwa Yehova kumatithandiza bwanji?
Bambo wanzeru amachita zinthu ndi ana ake modzichepetsa ndiponso mofatsa
5 Mfumu Davide anaimbira Yehova kuti: “Inu mumandipatsa chishango chanu chachipulumutso, dzanja lanu lamanja limandithandiza, ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.” (Salimo 18:35) Tingati Yehova anadzitsitsa kuti afanane msinkhu ndi munthu yemwe sanali wangwiroyu n’cholinga choti azimuteteza komanso kumusamalira tsiku lililonse. Davide ankadziwa kuti akanapulumutsidwa ndiponso kukhala mfumu yaikulu pokhapokha ngati Yehova akanadzichepetsa mwanjira imeneyi n’kumuthandiza. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Ndi ndani akanakhala ndi chiyembekezo chodzapulumuka zikanakhala kuti Yehova sanadzichepetse kuti atithandize ngati Bambo wofatsa komanso wokoma mtima?
6, 7. (a) N’chifukwa chiyani Baibulo silisonyeza kuti kudzichepetsa kwa Yehova n’kofanana ndi kwa anthu? (b) Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kufatsa ndi nzeru, nanga ndi ndani amene amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi?
6 Kudzichepetsa ndi khalidwe labwino kwambiri limene anthu okhulupirika ayenera kukhala nalo. Khalidweli limayendera limodzi ndi kukhala wanzeru. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 11:2 limati: “Anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru.” Komabe, Baibulo silinena kuti Yehova ndi wodzichepetsa m’njira yofanana ndi mmene anthu amayenera kukhalira odzichepetsa. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa m’Baibulo mawu akuti kudzichepetsa akamanena za anthu, amatanthauza kudziwa kuti pali zina zomwe sungathe kuchita kapena si udindo wako kuzichita. Koma Mulungu Wamphamvuyonse akhoza kuchita chilichonse kupatulapo zimene anachita kusankha kuti asamachite chifukwa chotsatira mfundo zake zolungama. (Maliko 10:27; Tito 1:2) Ndiponso popeza iye ndi Wam’mwambamwamba, palibe ali ndi ufulu womuuza zochita. Choncho kwa Yehova, kudzichepetsa sikutanthauza kudziwa kuti pali zina zomwe sangathe kuchita kapena si udindo wake kuzichita.
7 Komabe, Yehova ndi wodzichepetsa ndiponso wofatsa. Amaphunzitsa atumiki ake kuti kukhala wofatsa n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi nzeru zenizeni. Mawu ake amanena kuti ‘kufatsa ndi khalidwe limene limabwera chifukwa cha nzeru.’ (Yakobo 3:13) Taganizirani chitsanzo cha Yehova pa nkhaniyi.
Yehova Amapatsa Ena Zochita Komanso Amamvetsera
8-10. (a) N’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti Yehova amapatsa ena zochita komanso amamvetsera? (b) Kodi Wamphamvuyonse anasonyeza bwanji kudzichepetsa pochita zinthu ndi angelo ake?
8 Yehova amasonyezanso kuti ndi wodzichepetsa m’njira ina yochititsa chidwi kwambiri. Mofunitsitsa, iye amapatsa ena zochita ndiponso amamvetsera. N’zodabwitsa kwambiri kuti iye amachita zimenezi, chifukwatu Yehova safunika thandizo kapena malangizo. (Yesaya 40:13, 14; Aroma 11:34, 35) Koma m’Baibulo muli zitsanzo zambiri zimene zimasonyeza kuti Yehova amadzichepetsa n’kumapatsa ena zochita komanso amamvetsera.
9 Mwachitsanzo, taganizirani zinthu zosaiwalika zomwe zinachitikira Abulahamu. Abulahamu analandira alendo atatu ndipo mmodzi wa iwo ankamutchula kuti “Yehova.” Alendowo anali angelo, koma mmodzi anabwera m’dzina la Yehova ndipo ankachita zinthu m’dzina la Yehovayo. Mngelo ameneyo akamalankhula komanso kuchita zinthu, zinali ngati akuchita zimenezo ndi Yehova. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, Yehova anauza Abulahamu kuti anamva ‘madandaulo ambiri okhudza machimo a anthu am’mizinda ya Sodomu ndi Gomora.’ Yehova anati: “Ndipitako kuti ndikaone ngati akuchitadi zimene ndamvazo. Ndikufuna ndidziwe ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho.” (Genesis 18:3, 20, 21) Komabe mawu a Yehovawa sankatanthauza kuti Wamphamvuyonseyo ‘apitako’ yekha. Iye anatumanso angelo kuti akamuimire. (Genesis 19:1) Chifukwa chiyani? N’zodziwikiratu kuti Yehova, yemwe amaona zonse, akanatha ‘kudziwa’ zimene zinkachitika kuderalo. Koma modzichepetsa, anapatsa angelowo ntchito yoti akafufuze zimene zinkachitika ndiponso akaone Loti ndi banja lake ku Sodomu.
10 Komanso, Yehova amamvetsera. Pa nthawi ina anafunsa angelo ake kuti apereke maganizo awo pa zimene angachite kuti alimbikitse Ahabu kupita kunkhondo n’kukafa. Sikuti Yehova ankafunika thandizo pa nkhaniyi. Komatu anagwirizana ndi maganizo a mngelo wina n’kumutuma kuti akachite zimene ananenazo. (1 Mafumu 22:19-22) Kodi kudzichepetsa kupose pamenepa?
11, 12. Kodi Abulahamu anadziwa bwanji kuti Yehova ndi wodzichepetsa?
11 Yehova amakhalanso wokonzeka kumvetsera anthu omwe si angwiro akamafotokoza maganizo awo komanso zinthu zomwe zikuwadetsa nkhawa. Mwachitsanzo, Yehova atauza Abulahamu kuti akufuna kuwononga Sodomu ndi Gomora, munthu wokhulupirikayo anadabwa kwambiri. Iye anati: “Simungachite zimenezo. Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo?” Abulahamu anafunsa Yehova ngati sakanawononga mizindayo mukanapezeka anthu olungama 50. Yehova anamutsimikizira kuti sakanawononga. Koma Abulahamu anafunsanso. Anachepetsa nambala ya anthu olungamawo kufika pa 45, kenako pa 40 n’kumangoichepetsabe. Ngakhale kuti Yehova ankamutsimikizira kuti sakanawononga, Abulahamu anapitiriza kufunsa mpaka nambalayo inafika pa 10. Mwina pa nthawiyi Abulahamu anali asanamvetse kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri. Koma Yehova moleza mtima ndiponso modzichepetsa, analola kuti Abulahamu, yemwe anali mnzake komanso mtumiki wake, afotokoze zimene zinkamudetsa nkhawa.—Genesis 18:23-33.
12 Kodi ndi anthu angati anzeru ndiponso ophunzira amene angamvetsere moleza mtima chonchi kwa munthu wosaphunzira?b Komatu Mulungu wathu anachita zimenezi chifukwa ndi wodzichepetsa. Pa nthawi imene ankakambiranayi, Abulahamu anaonanso kuti Yehova ndi “wosakwiya msanga.” (Ekisodo 34:6) Mwina chifukwa chodziwa kuti analibe ufulu wofunsa Wam’mwambamwamba chifukwa chake akuchita zinazake, Abulahamu anapempha kawiri konse kuti: “Yehova, musandipsere mtima.” (Genesis 18:30, 32) Yehova sanamupseredi mtima. Iye ndi wofatsa, “khalidwe limene limabwera chifukwa cha nzeru.”
Yehova Ndi Wololera
13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi wololera?
13 Yehova ndi wololera ndipo khalidweli limasonyezanso kuti ndi wodzichepetsa. N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri anthu omwe si angwirofe timalephera kukhala ololera. Monga taona kale, Yehova amakhala wokonzeka kumvetsera angelo ake komanso anthu akamalankhula. Koma kuwonjezera pamenepa, amakhalanso wololera ngati mfundo zake sizikuphwanyidwa. Khalidwe limeneli ndi umboni winanso woti Yehova ndi wanzeru. Lemba la Yakobo 3:17 limati: ‘Nzeru yochokera kumwamba ndi yololera.’ Kodi Yehova, yemwe ndi wanzeru pa chilichonse, amasonyeza bwanji kuti ndi wololera? Njira imodzi ndi yakuti amatha kusintha n’kuchita zinthu mogwirizana ndi mmene zilili pa nthawiyo. Kumbukirani kuti dzina lake limatanthauza kuti amakhala chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse cholinga chake. (Ekisodo 3:14) Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Yehova ndi wololera ndipo amasintha pakafunika kutero?
14, 15. Kodi masomphenya a Ezekieli a galeta lakumwamba la Yehova amatiphunzitsa chiyani zokhudza mbali yakumwamba ya gulu la Yehova, ndipo limasiyana bwanji ndi mabungwe a anthu?
14 Chaputala china cha m’Baibulo chimatithandiza kumvetsa mfundo yoti Yehova amatha kusintha ngati pakufunika kutero. Mneneri Ezekieli anaona masomphenya a mbali yakumwamba ya gulu la Yehova, yomwe ndi angelo. Anaona galeta lalikulu ndiponso lochititsa mantha, lomwe lili ngati “galimoto” ya Yehova imene amaiwongolera. Galetali linkayenda mochititsa chidwi kwambiri. Linali ndi mawiro akuluakulu omwe anali ndi mbali 4 ndiponso maso paliponse moti ankatha kuona chilichonse. Galetali linkatha kusintha kopita mofulumira kwambiri popanda kuima kapena kukhota. Ngakhale kuti ndi lalikulu, silinkayenda pang’onopang’ono ngati mmene zimakhalira ndi chigalimoto chachikulu chopangidwa ndi anthu. Linkayenda pa liwiro lofanana ndi mphezi n’kumathanso kukhota likuthamanga choncho. (Ezekieli 1:1, 14-28) Choncho mofanana ndi Yehova, nalonso gulu lake limatha kusintha mofulumira mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo.
15 Nawonso anthu angafune kuti azichita zimenezi. Komabe nthawi zambiri anthuwa komanso mabungwe amavutika kuti asinthe n’kumachita mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Mwachitsanzo, sitima yapamadzi yonyamula mafuta kapena yapamtunda yonyamula katundu imachititsa chidwi kwambiri chifukwa choti imakhala yaikulu komanso yamphamvu. Koma kodi sitima zimenezi zimatani pakachitika zinthu zadzidzidzi? Ngati kutsogolo kwa sitima yonyamula katundu kutagwera chinthu, sizingatheke kuti ikhotere kumbali. Imavutikanso kuti iime mwadzidzidzi. Ndipo ngati yanyamula katundu wambiri ingayendebe pafupifupi mtunda wa makilomita awiri pambuyo poti amanga mabuleki. Nayonso sitima yapamadzi yonyamula mafuta ikhoza kuyendabe mtunda wa makilomita 8, atazimitsa injini zake. Ngakhale injini zake ataziika mu giya yobwerera m’mbuyo, sitimayi ingapitebe kutsogolo makilomita atatu, isanayambe kubwerera m’mbuyo. Zimenezi n’zofanana ndi zimene mabungwe a anthu amachita. Nthawi zambiri zinthu zikasintha amavutika kusintha ndipo sakhala ololera. Iwo amachita zimenezi chifukwa cha kunyada. Zotsatira zake zimakhala zakuti makampani amakumana ndi mavuto azachuma komanso maboma amagwa. (Miyambo 16:18) Koma timasangalala kwambiri chifukwa Yehova ndiponso gulu lake ndi osiyana kwambiri ndi anthu.
Kodi Yehova Amasonyeza Bwanji Kuti Ndi Wololera?
16. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kulolera pa zomwe anachitira Loti asanawononge Sodomu ndi Gomora?
16 Taganiziraninso nkhani yokhudza kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora. Mngelo wa Yehova anapatsa Loti ndi banja lake malangizo omveka bwino akuti: “Thawirani kudera lakumapiri.” Komabe zimenezi sizinamusangalatse Loti moti anapempha kuti: “Chonde Yehova, kumeneko ayi!” Loti ankaona kuti akathawira kumapiriko akafa, choncho anachonderera kuti iye ndi banja lake athawire kutauni ya Zowari, yomwe inali yapafupi. Koma Yehova ankafuna kuwononganso tauni imeneyi. Ndiponso panalibe zifukwa zomveka zoti Loti achitire mantha chifukwa Yehova akanatha kumuteteza kumapiriko. Komabe Yehova anavomera zimene Loti anapemphazi. Mngelo uja anauza Loti kuti: “Chabwino, ndavomera zimene wapempha. Sindiwononga tauni imene wanenayo.” (Genesis 19:17-22) Apatu Yehova anasonyeza kulolera.
17, 18. Pa zimene anachitira anthu a ku Nineve, kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi wololera?
17 Yehova amathanso kusintha munthu akalapa mochokera pansi pa mtima ndipo amamuchitira zinthu mwachifundo ndiponso mwachilungamo. Taganizirani zimene zinachitika mneneri Yona atatumidwa kumzinda wa Nineve womwe anthu ake ankachita zoipa komanso zachiwawa. Yona ankayenda m’misewu ya ku Nineve n’kumalengeza uthenga wosavuta kumva wochokera kwa Yehova wakuti mzinda wamphamvuwo uwonongedwa pakatha masiku 40. Komabe zinthu zinasintha kwambiri. Anthu a ku Nineve analapa.—Yona, chaputala 3.
18 Tingaphunzire zambiri tikayerekezera zimene Yehova anachita ndi zimene Yona anachita zinthu zitasintha chonchi. Yehova anasintha mogwirizana ndi mmene zinthu zinalili ndipo anakhala Wokhululukira machimo m’malo mokhala “msilikali wamphamvu.”c (Ekisodo 15:3) Koma Yona sanali wokonzeka kusintha ndipo sanasonyeze chifundo. M’malo mokhala wololera ngati Yehova, iye anachita zinthu ngati sitima yapamadzi yonyamula mafuta kapena yapamtunda yonyamula katundu ija. Popeza anali atalengeza kuti anthuwo awonongedwa, iye ankaona kuti akuyenera kuwonongedwa basi. Komabe, moleza mtima Yehova anaphunzitsa mneneri wake wosaleza mtimayu mfundo yofunika kwambiri pa nkhani ya kulolera ndiponso chifundo.—Yona, chaputala 4.
19. (a) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndi wololera pa zimene amayembekezera kuti tizichita? (b) Kodi lemba la Miyambo 19:17 likusonyeza bwanji kuti Yehova ndi Bwana wabwino, wololera komanso wodzichepetsa kwambiri?
19 Chomaliza, Yehova amasonyezanso kuti ndi wololera pa zimene amayembekezera kuti anthufe tizichita. Mfumu Davide inati: “Iye akudziwa bwino mmene anatipangira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:14) Yehova amadziwa zimene sitingathe kuchita ndiponso chifukwa chake timalakwitsa zinthu zina kuposa mmene eni akefe timadziwira. Sayembekezera kuti tizichita zomwe sitingathe. Baibulo limanena kuti pali mabwana “abwino ndi ololera,” komanso pali “ovuta kuwakondweretsa.” (1 Petulo 2:18) Kodi tingati Yehova ndi Bwana wotani? Taonani zimene lemba la Miyambo 19:17 limanena: “Amene amakomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova.” Kunena zoona, mabwana abwino komanso ololera okha ndi amene angamadziwe chinthu chabwino chilichonse chimene ena achitira anthu ovutika. Kuwonjezera pamenepa, lembali likusonyeza kuti Mlengi wa chilengedwe chonse amaona kuti ali ndi ngongole kwa anthu amene amachitira ena zinthu zachifundo zimenezo. Pamenepatu amasonyeza kuti ndi wodzichepetsa kwambiri.
20. Kodi n’chiyani chimatitsimikizira kuti Yehova amamva ndiponso kuyankha mapemphero athu?
20 Masiku anonso Yehova amasonyeza kuti ndi wofatsa komanso wololera akamachita zinthu ndi atumiki ake. Tikamapemphera tili ndi chikhulupiriro, iye amamvetsera. Ndipo ngakhale kuti satumiza angelo kuti adzalankhule nafe, tisamaganize kuti sayankha mapemphero athu. Kumbukirani kuti pamene mtumwi Paulo anapempha Akhristu anzake kuti ‘azimupempherera’ kuti amasulidwe m’ndende, anatinso: “Kuti ndibwerere kumeneko mwamsanga.” (Aheberi 13:18, 19) Choncho mapemphero athu akhoza kuchititsa kuti Yehova achite zinthu zimene mwina sakanazichita.—Yakobo 5:16.
21. Kodi sitiyenera kuganiza chiyani zokhudza kudzichepetsa kwa Yehova, koma tiyenera kuzindikira mfundo iti yokhudza iyeyo?
21 Komabe ngakhale kuti Yehova amasonyeza kuti ndi wodzichepetsa pokhala wofatsa, wokonzeka kumvetsera, woleza mtima ndiponso wololera, sanyalanyaza mfundo zake zolungama. Atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu angaganize kuti ndi ololera akamauza anthu awo kuti sikulakwa kuchita zinthu zimene Yehova amadana nazo, chifukwa choti zimenezo ndi zimene anthuwo angafune kumva. (2 Timoteyo 4:3) Anthu ali ndi chizolowezi chololera kuchita zolakwika pongofuna kusangalatsa ena, koma kulolera kumeneku n’kosagwirizana ndi kulolera kwa Mulungu. Yehova ndi woyera ndipo saphwanya mfundo zake zolungama. (Levitiko 11:44) Choncho tiyenera kumvetsa mfundo yoti Yehova ndi wololera chifukwa choti ndi wodzichepetsa ndipo tiyenera kumukonda kwambiri chifukwa cha zimenezi. Kodi si zosangalatsa kudziwa kuti Yehova, yemwe ndi wanzeru kwambiri m’chilengedwe chonse, ndi wodzichepetsa kwambiri? Ndi mwayitu waukulu kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu wogometsa ameneyu, yemwenso ndi wofatsa, woleza mtima komanso wololera.
a Anthu ena akale omwe ankakopera Baibulo otchedwa Asoferimu anasintha vesili kuti lizimveka ngati Yeremiya ndi amene akuwerama osati Yehova. Zikuoneka kuti iwo ankaganiza kuti n’zosayenera kunena kuti Mulungu angachite zinthu modzichepetsa chonchi kuti athandize munthu. Chifukwa cha zimenezi, Mabaibulo ambiri sanamasulire bwino mfundo yosangalatsa imene ili m’vesili. Komabe, Baibulo lina linamasulira molondola kuti Yeremiya anauza Mulungu kuti: “Kumbukirani, kumbukirani ndipo mundiweramire.”—The New English Bible.
b N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limanena kuti munthu wosaleza mtima amakhala wodzikuza. (Mlaliki 7:8) Choncho mfundo yoti Yehova ndi woleza mtima, ikusonyezanso kuti ndi wodzichepetsa.—2 Petulo 3:9.
c Pa Salimo 86:5, Baibulo limati Yehova ndi ‘wabwino ndiponso wokonzeka kukhululuka.’ Pamene Salimoli ankalimasulira m’Chigiriki, mawu akuti “wokonzeka kukhululuka” anawamasulira kuti e·pi·ei·kesʹ, kapena kuti “wololera.”