Kodi Mwaloŵa Mpumulo wa Mulungu?
“Iye amene adaloŵa mpumulo wake [“wa Mulungu,” NW], adapumulanso mwini wake ku ntchito zake.”—AHEBRI 4:10.
1. Kodi nchifukwa ninji mpumulo uli wofunika kwambiri?
MPUMULO. Ameneŵa ndi mawu okoma ndi osangalatsa chotani nanga! M’dziko lino lotanganika ndiponso lotopetsa, ambirife tingavomereze kuti kupumula ngakhale pang’ono chabe nkosangalatsa kwambiri. Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, okwatira kapena mbeta, tingaone kuti ndife opanikizika ndiponso otopa ndi moyo wathu watsiku ndi tsiku. Kwa amene ali ndi zovuta zina m’thupi kapena matenda ena, tsiku lililonse lingakhale lovuta kwambiri. Zili mongadi momwe Malemba amanenera kuti, “cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.” (Aroma 8:22) Munthu akamapumula sizitanthauza kuti ndi waulesi ayi. Mpumulo ngwofunika kwa munthu aliyense ndipo suyenera kunyalanyazidwa.
2. Kodi Yehova wakhala akupumula kuyambira liti?
2 Yehova Mulungu iyemwini wakhala akupumula. M’buku la Genesis, timaŵerenga kuti: “Zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lawo lonse. Tsiku lachisanu ndi chiŵiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ku ntchito yake yonse.” Yehova anasankha “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” kuti likhale lofunika mwapadera, popeza kuti nkhani youziridwayo ikupitiriza kuti: “Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, naliyeretsa limenelo.”—Genesis 2:1-3.
Mulungu Adapuma ku Ntchito Yake
3. Kodi ndi ziti zimene sizingakhale zifukwa zimene Mulungu anapumulira?
3 Kodi nchifukwa ninji Mulungu anapumula pa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri”? Ndithudi, iye sanapumule chifukwa chakuti anatopa ayi. Yehova ali ndi “mphamvu zake zazikulu” ndiponso “salefuka konse, salema.” (Yesaya 40:26, 28) Ndiponso Mulungu sanapumule chifukwa chakuti anafuna kukhala ndi nthaŵi yopuma kapena yochepetsako kagwiridwe kake ka ntchito ayi, popeza kuti Yesu anatiuza kuti: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito.” (Yohane 5:17) Mulimonse mmene zinalili, “Mulungu ndiye mzimu” ndipo zochita kapena zofuna za zolengedwa zathupi lanyama nzosiyana ndi zake.—Yohane 4:24.
4. Kodi “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” linali losiyana motani ndi ‘masiku’ asanu ndi limodzi oyambirira?
4 Kodi tingazindikire motani chifukwa chimene Mulungu anapumulira pa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri”? Mwa kulingalira kuti ngakhale kuti Mulungu anasangalala kwambiri ndi zimene anachita pa ‘masiku’ asanu ndi limodzi a kulenga, iye kwenikweni anadalitsa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” ndipo ‘analiyeretsa.’ Dikishonale yotchedwa Concise Oxford Dictionary imamasulira mawu akuti “kuyera” kuti ndiko “kupatulidwa kapena kusankhulidwa kotheratu (kuti chinthucho chikhale cha mulungu kapena kuti chigwire ntchito inayake yachipembedzo).” Choncho, kudalitsa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” ndi kuliyeretsa kumene Yehova anachita kumasonyeza kuti tsikulo pamodzi ndi “mpumulo” wake zinali zogwirizana m’njira inayake ndi chifuniro ndiponso cholinga chake chopatulika, osati kuti akwaniritse zosoŵa zake ayi. Kodi kugwirizana kumeneko nkotani?
5. Kodi Mulungu anayamba kuyendetsanji pa ‘masiku’ asanu ndi limodzi oyambirira a kulenga?
5 Pa ‘masiku’ olenga asanu ndi limodzi omwe anali atapita, Mulungu anali atapanga nayamba kuyendetsa zungulirezungulire ndi malamulo oyendetsa dziko lapansi ndi chinthu chilichonse chokhala mmenemo. Asayansi tsopano akufufuza za mmene zimenezi zinalinganizidwira modabwitsa. Pamapeto a “tsiku lachisanu ndi chimodzi,” Mulungu analenga anthu aŵiri oyamba ndipo anawaika “m’munda ku Edene chakummaŵa.” Pomalizira pake, Mulungu analengeza chifuniro chake chokhudza banja la anthu ndiponso dziko lapansi m’mawu aulosi akuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.”—Genesis 1:28, 31; 2:8.
6. (a) Pamapeto a “tsiku lachisanu ndi chimodzi,” kodi Mulungu anaziona motani zonse zimene analenga? (b) Kodi “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” lili loyeretsedwa m’lingaliro lotani?
6 Pamene “tsiku lachisanu ndi chimodzi” linafika pamapeto, nkhaniyi ikunena kuti: “Anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Mulungu anakhutira ndi chilichonse chimene anapanga. Choncho, iye anapumula, kapena kuti analekeza ntchito yake ya kulenga zapadziko lapansi. Komabe, ngakhale kuti munda wa paradaisowo panthaŵiyo unali wabwino ndiponso wokongola, unali wochepa, ndipo padziko lapansi panali zolengedwa zaumunthu ziŵiri zokha basi. Panali kudzapita nthaŵi yaitali kuti dziko lapansi ndi banja la anthu lidzafike mumkhalidwe umene Mulungu analinganiza. Nchifukwa chake iye anasankha “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” kuti likhale tsiku limene zinthu zonse zimene iye analenga pa ‘masiku’ asanu ndi limodzi oyambirira zikule mogwirizana ndi chifuniro chake chopatulika. (Yerekezerani ndi Aefeso 1:11.) Pamene “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” lidzafika pamapeto ake, dziko lonse lapansi lidzakhala litasanduka paradaiso wokhala ndi anthu angwiro omwe adzakhalamo kosatha. (Yesaya 45:18) “Tsiku lachisanu ndi chiŵiri” linasankhulidwa, kapena kuti linapatulidwa kuti lichite ndi kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu chokhudza dziko lapansi ndi mtundu wa anthu. Ndiye chifukwa chake lili ‘loyeretsedwa.’
7. (a) Kodi Mulungu anapumula pachiyani pa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri”? (b) Kodi zinthu zonse zidzakhala motani pamene “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” lidzafika pamapeto ake?
7 Choncho, Mulungu anapumula pantchito yake yolenga pa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri.” Zili monga kuti analekeza ntchitoyo pofuna kuti zinthu zimene analenga zifike pacholinga chake. Iye ali ndi chidaliro chonse chakuti pamapeto a “tsiku lachisanu ndi chiŵiri,” chilichonse chidzachitika monga momwe anachilinganizira. Zopinga zilizonse zimene zingadzakhalepo zidzalakidwa. Anthu onse omvera adzapindula pamene chifuniro chonse cha Mulungu chidzakwaniritsidwa. Palibe chimene chidzalepheretse zimenezi chifukwa chakuti Mulungu anadalitsa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri,” ndipo ‘analiyeretsa.’ Chimenecho nchiyembekezo chaulemerero chotani nanga kwa anthu omvera!
Aisrayeli Analephera Kuloŵa Mpumulo wa Mulungu
8. Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene Aisrayeli anayambira kusunga Sabata?
8 Mtundu wa Israyeli unapindula ndi makonzedwe a Yehova okhudza ntchito ndi kupumula. Ngakhale pamene Mulungu anali asanapatse Aisrayeli Chilamulo pa Phiri la Sinai, iye anawauza kudzera mwa Mose kuti: “Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku aŵiri; khalani yense m’malo mwake, munthu asatuluke m’malo mwake tsiku lachisanu ndi chiŵiri.” Chotsatirapo chake chinali chakuti “anthu anapumula [“anayamba kusunga sabata,” NW] tsiku lachisanu ndi chiŵiri.”—Eksodo 16:22-30.
9. Kodi nchifukwa ninji Aisrayeli mosakayikira anaona lamulo la Sabata monga kusintha kofunika?
9 Makonzedwe ameneŵa anali atsopano kwa Aisrayeli, amene anali atangolanditsidwa kumene mu ukapolo ku Igupto. Ngakhale kuti Aigupto ndi ena anali kuŵerengera nthaŵi mwa kupatula masiku kuti akhale asanuasanu kapena khumikhumi, nzokayikitsa ngati Aisrayeli omwe anali mu ukapolo anapatsidwa tsiku lopumula. (Yerekezerani ndi Eksodo 5:1-9.) Choncho, nkwanzeru kulingalira kuti Aisrayeli anayamikira kwambiri kusintha kumeneku. M’malo moona kusunga Sabata monga katundu wolemera kapena chiletso, iwo anafunikira kulisunga mosangalala. Ndithudi, Mulungu pambuyo pake anawauza kuti Sabata linakhazikitsidwa kuti liziwakumbutsa za ukapolo wawo ku Igupto ndiponso za kulanditsidwa kwawo.—Deuteronomo 5:15.
10, 11. (a) Mwa kukhala omvera, kodi Aisrayeli akanayembekezera kukhala ndi chiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji Aisrayeli analephera kuloŵa mpumulo wa Mulungu?
10 Ngati Aisrayeli amene anatuluka ku Igupto pamodzi ndi Mose anali omvera, iwo akanakhala ndi mwayi woloŵa ‘m’dziko [lolonjezedwa] loyenda mkaka ndi uchi.’ (Eksodo 3:8) Kumeneko, iwo akanakhala ndi mpumulo weniweni, osati pa Sabata pokha ayi koma moyo wawo wonse. (Deuteronomo 12:9, 10) Komabe, zinthu sizinali choncho. Ponena za iwo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka m’Aigupto ndi Mose? Koma [Mulungu] anakwiya ndi ayani zaka makumi anayi? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi awo adagwa m’chipululu? Ndipo adawalumbirira ayani kuti asaloŵe mpumulo wake? Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanakhoza kuloŵa chifukwa cha kusakhulupirira.”—Ahebri 3:16-19.
11 Limenelo ndi phunziro lalikulu chotani nanga kwa ife! Chifukwa cha kusakhulupirira Yehova, mbadwo umenewo sunalandire mpumulo umene anawalonjeza. M’malo mwake, iwo anafera m’chipululu. Analephera kuzindikira kuti monga mbadwa za Abrahamu, iwo anali okhudzidwa kwambiri ndi chifuniro cha Mulungu cha kudalitsa mitundu yonse ya padziko lapansi. (Genesis 17:7, 8; 22:18) M’malo mochita zinthu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu chimenecho, iwo anachenjenetsedwa kotheratu ndi zokhumba zawo zakudziko ndiponso zadyera. Tiyenitu tipeŵe khalidwe limeneli!—1 Akorinto 10:6, 10.
Utsalira Mpumulo
12. Kodi nchiyembekezo chotani chimene Akristu a m’zaka za zana loyamba anali nachobe, ndipo kodi iwo akanachipeza motani?
12 Atafotokoza za kulephera kwa Aisrayeli kuloŵa mpumulo wa Mulungu chifukwa cha kusakhulupirira, Paulo anasumika maganizo ake pa okhulupirira anzake. Malinga ndi mmene ananenera pa Ahebri 4:1-5, iye anawatsimikizira kuti “likatsala lonjezano lakuloŵa mpumulo wake [wa Mulungu].” Paulo anawalangiza kuti akhulupirire “uthenga wabwino,” pakuti “ife amene takhulupirira tiloŵa mpumulowo.” Popeza kuti Chilamulo chinali chitachotsedwa kale ndi nsembe ya dipo ya Yesu, panopo Paulo sanali kutanthauza kupumula mwakuthupi komwe kunali kuchitika pa Sabata ayi. (Akolose 2:13, 14) Mwa kugwira mawu Genesis 2:2 ndiponso Salmo 95:11, Paulo anali kulimbikitsa Akristu achihebri kuti aloŵe mpumulo wa Mulungu.
13. Pogwira mawu Salmo 95, kodi nchifukwa ninji Paulo anagogomezera mawu akuti “lero”?
13 Chiyembekezo choloŵa mpumulo wa Mulungu chinayenera kukhala “uthenga wabwino” kwa Akristu achihebri, monga momwe mpumulo wa Sabata unayenerera kukhala “uthenga wabwino” kwa Aisrayeli isanafike nthaŵi yawo. Choncho, Paulo anapempha okhulupirira anzake kuti asachitenso tchimo longa limene anachita Aisrayeli m’chipululu. Pogwira mawu amene tsopano ali pa Salmo 95:7, 8, Paulo anagogomezera mawu akuti “lero,” ngakhale kuti panali patapita nthaŵi yaitali kuchokera pamene Mulungu anali atapuma pantchito yolenga. (Ahebri 4:6, 7) Kodi Paulo anali kunenanji? Anali kunena kuti “tsiku lachisanu ndi chiŵiri,” limene Mulungu analipatula kuti cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndi mtundu wa anthu chikwaniritsidwe kotheratu, linali likupitirizabe kukhalapo. Choncho, kunali kofunika kuti Akristu anzakewo azichita zinthu mogwirizana ndi cholinga chimenechi m’malo motanganika ndi kulondola zinthu mwadyera. Iye anabwerezanso kupereka chenjezo lakuti: “Musaumitse mitima yanu.”
14. Kodi Paulo anasonyeza motani kuti “mpumulo” wa Mulungu unali ukupitirizabe kukhalapo?
14 Kuwonjezera pamenepo, Paulo anasonyeza kuti “mpumulo” wolonjezedwawo sunali chabe nkhani ya kukhala m’Dziko Lolonjezedwa motsogozedwa ndi Yoswa ayi. (Yoswa 21:44) “Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo,” anatero Paulo, “[Mulungu] sakadalankhula m’tsogolomo za tsiku lina.” Pachifukwa chimenecho, Paulo anawonjezera kuti: “Utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu.” (Ahebri 4:8, 9) Kodi “mpumulo wa Sabata” umenewo ndiwo chiyani?
Loŵani Mpumulo wa Mulungu
15, 16. (a) Kodi mawu akuti “mpumulo wa Sabata” amatanthauzanji? (b) Kodi ‘kupumula ku ntchito ya mwini wake’ kumatanthauzanji?
15 Mawu akuti “mpumulo wa Sabata” anatembenuzidwa kuchokera ku liwu lachigiriki lotanthauza “kusunga Sabata.” (Kingdom Interlinear) Profesa William Lane anati: “Liwu limeneli linayamba kudziŵika kwambiri chifukwa cha maphunziro okhudza Sabata omwe ankachitika m’Chiyuda ozikidwa pa Eksod 20:8-10, pamene anali kugogomezera kuti mpumulo ndi chitamando nzogwirizana . . . [Ilo] limagogomezera za mbali yapadera ya madyerero ndi chisangalalo, yomwe inkachitika polambira ndi kutamanda Mulungu.” Choncho, mpumulo wolonjezedwawo suli chabe kupuma pantchito ayi. Ndiwo kusintha, mwa kusiya ntchito yotopetsa ndi yopanda chifuno kenaka nkuyamba utumiki wosangalatsa umene umalemekeza Mulungu.
16 Zimenezi zinafotokozedwa m’mawu otsatira a Paulo akuti: “Pakuti iye amene adaloŵa mpumulo wake [“wa Mulungu,” NW], adapumulanso mwini wake ku ntchito zake, monganso Mulungu ku zake za Iye.” (Ahebri 4:10) Mulungu sanapumule pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la kulenga chifukwa chakuti anatopa ayi. M’malo mwake, iye analekeza ntchito yake yolenga zapadziko lapansi pofuna kuti ntchito ya manja akeyo ikule mokwanira, kuti kenaka iye atamandidwe ndi kulemekezedwa. Monga mbali ya chilengedwe cha Mulungu, tiyeneranso kuchita zinthu mogwirizana ndi makonzedwe amenewo. Tiyenera ‘kupumula ku ntchito zathu,’ kutanthauza kuti tiyenera kusiya zoyesayesa zathu zodzilungamitsa pamaso pa Mulungu ncholinga choti tipulumuke. M’malo mwake, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chakuti chipulumutso chathu chimadalira pa nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, ndipo mwa nsembeyo, zinthu zonse zidzakhalanso mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.—Aefeso 1:8-14; Akolose 1:19, 20.
Mawu a Mulungu Ngamphamvu
17. Kodi ndi khalidwe liti limene Israyeli wakuthupi anatsatira lomwe tiyenera kulipeŵa?
17 Aisrayeli analephera kuloŵa mpumulo wolonjezedwa wa Mulungu chifukwa cha kusamvera ndi kusakhulupirira kwawo. Nchifukwa chake Paulo analangiza Akristu achihebri kuti: “Chifukwa chake tichite changu cha kuloŵa mpumulowo, kuti wina angagwe m’chitsanzo chomwe cha kusamvera.” (Ahebri 4:11) Ayuda ambiri a m’zaka za zana loyamba sanakhulupirire Yesu, ndipo ambiri a iwo anavutika kwambiri pamene dongosolo lazinthu lachiyuda linafika pamapeto ake mu 70 C.E. Nkofunika chotani nanga kuti tikhulupirire mawu a Mulungu alonjezo lerolino!
18. (a) Kodi Paulo ananena kuti tiyenera kukhulupirira mawu a Mulungu pazifukwa ziti? (b) Kodi ndi motani mmene mawu a Mulungu alili “akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse”?
18 Tili ndi zifukwa zabwino zokhulupirira mawu a Yehova. Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Inde, mawu a Mulungu, kapena uthenga wake, ali “akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse.” Akristu achihebri anafunikira kukumbukira zimene zinachitikira makolo awo. Ngakhale kuti Yehova anawaweruza kuti adzafera m’chipululu, iwo ananyalanyaza chiweruzocho nayesa kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Koma Mose anawachenjeza kuti: “Aamaleki ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga.” Pamene Aisrayeliwo anapitirizabe ulendowo modzikuza, “anatsika Aamaleki, ndi Akanani, akukhala m’phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horima.” (Numeri 14:39-45) Mawu a Yehova ali akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, ndipo aliyense wowanyalanyaza dala ndithudi adzatuta zotsatirapo zake.—Agalatiya 6:7-9.
19. Kodi mawu a Mulungu ali ndi mphamvu ya ‘kupyoza’ yaikulu motani, ndipo kodi nchifukwa ninji tiyenera kuzindikira kuti tili akuŵerengeredwa mlandu kwa Mulungu?
19 Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yaikulu chotani nanga ‘yopyoza kufikira kugaŵira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa’! Amaloŵerera m’maganizo ndi zolingalira za anthu, mophiphiritsira kupyoza mpaka kukafika m’mafuta amkati mwenimweni mwa mafupa! Ngakhale kuti Aisrayeli amene anamasulidwa mu ukapolo ku Igupto anavomera kusunga Chilamulo, Yehova anadziŵa kuti m’mitima mwawo, iwo sanakondwere ndi zogaŵira ndiponso zofunika zake. (Salmo 95:7-11) M’malo mochita chifuniro chake, iwo anadera nkhaŵa kwambiri zokhumba zawo zakuthupi. Choncho, iwo sanaloŵe mpumulo wolonjezedwa wa Mulungu koma anafera m’chipululu. Tiyenera kusamala kuti tisachite zimenezo, popeza kuti “palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pake [pa Mulungu], koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye [“amene adzatiŵerengera mlandu,” NW].” (Ahebri 4:13) Choncho, tiyenera kukwaniritsa kudzipatulira kwathu kwa Yehova osati ‘kubwerera kuloŵa chitayiko.’—Ahebri 10:39.
20. Kodi nchiyani chomwe tikuyembekezera mtsogolo muno, ndipo kodi tsopano tiyenera kuchitanji kuti tiloŵe mpumulo wa Mulungu?
20 Ngakhale kuti “tsiku lachisanu ndi chiŵiri”—tsiku lopumula la Mulungu—likupitirizabe kukhalapo, iye akuonetsetsa kuti cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndi mtundu wa anthu chikwaniritsidwe. Posachedwapa, Mfumu Yaumesiya, Yesu Kristu, adzachitapo kanthu mwa kuchotsa onse otsutsana ndi chifuniro cha Mulungu padziko lapansi, kuphatikizapo Satana Mdyerekezi. Mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi, Yesu ndi olamulira anzake a 144,000 adzapangitsa dziko lapansi ndi mtundu wa anthu kukhala zofanana ndi mmene Mulungu analinganizira. (Chivumbulutso 14:1; 20:1-6) Ino ndiyo nthaŵi yakuti ifeyo tisonyeze kuti miyoyo yathu njofunitsitsa kuchita chifuniro cha Yehova Mulungu. M’malo mofunafuna kudzilungamitsa pamaso pa Mulungu ndi kuchita zokonda zathu, ino ndiyo nthaŵi yakuti ‘tipumule ku ntchito zathu’ ndi kuchita zinthu za Ufumu ndi mtima wonse. Ngati tichita zimenezo ndiponso ngati tikhalabe okhulupirika kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova, tidzakhala ndi mwayi wopeza mapindu a mpumulo wa Mulungu kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu anapumula pa “tsiku lachisanu ndi chiŵiri”?
◻ Kodi ndi mpumulo wotani umene Aisrayeli akanakhala nawo, koma kodi nchifukwa ninji iwo analephera kuloŵa mpumulowo?
◻ Kodi tiyenera kuchitanji kuti tiloŵe mpumulo wa Mulungu?
◻ Kodi ndi motani mmene mawu a Mulungu alili amoyo, amphamvu, ndiponso akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Aisrayeli anali kusunga Sabata, koma sanaloŵe mpumulo wa Mulungu. Kodi mukudziŵa chifukwa chake?