-
Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
7, 8. Kodi timakhala ndi mlandu wotani kwa Yehova ngati sitilankhula bwino?
7 Chifukwa chachitatu chimene tiyenera kukhalira osamala polankhula n’chakuti timakhala ndi mlandu kwa Yehova ngati sitilankhula bwino. Mmene timagwiritsira ntchito lilime lathu zimakhudza ubwenzi wathu ndi anthu ena komanso ndi Yehova. Lemba la Yakobo 1:26 limati: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.”b Monga tinaonera m’mutu wapitawu, zimene timalankhula zimakhudza kwambiri kulambira kwathu. Ngati sitilamulira lilime lathu ndipo timalankhula zopweteka komanso zovulaza ena, ndiye kuti zonse zimene timachita potumikira Mulungu zingakhale zopanda phindu. Ndithudi, m’pofunika kusamala kwambiri ndi kalankhulidwe kathu.—Yakobo 3:8-10.
-
-
Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
-
-
b Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti ‘kupanda pake’ anamasuliridwanso kuti ‘chopanda ntchito.’—1 Akorinto 15:17.
-