Kuthandiza Akazi Amasiye M’mayesero Awo
IMODZI mwa nkhani zotchuka kwambiri zokhudza akazi amasiye ndi nkhani ya m’Baibulo ya Rute ndi mpongozi wake Naomi. Onse aŵiri anali akazi amasiye. Komabe, Naomi anali ataferedwa osati mwamuna wake yekha komanso ana ake amuna aŵiri. Mmodzi wa ana ameneŵa ndiye anali mwamuna wa Rute. Iwo analidi pavuto lalikulu chifukwa choti ankakhala m’dera laulimi lomwe amuna anali odalirika kwambiri.—Rute 1:1-5, 20, 21.
Komabe, Naomi anali ndi bwenzi ndiponso wom’limbikitsa wapadera. Bwenzi limeneli linali Rute amene anakana kuchoka kumusiya yekha Naomi. M’kupita kwanthaŵi, Rute anam’thandizadi Naomi ‘kuposa ana aamuna asanu ndi aŵiri.’ Iye anam’thandiza osati kokha chifukwa choti anali kumukonda Naomiyo komanso chifukwa chakuti anali kukonda Mulungu kwambiri. (Rute 4:15) Naomi atauza Rute kuti atha kubwerera kubanja lakwawo ndiponso kwa anzake achimoabu, Rute anayankha ndi mawu ogwira mtima osonyeza kukhulupirika omwe anali asanalembedwepo m’nthaŵiyo akuti: “Kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga; kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova nawonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.”—Rute 1:16, 17.
Yehova Mulungu anaona mtima wabwinowu wa Rute. Iye anadalitsa banja laling’onolo la Naomi ndi Rute ndipo m’kupita kwanthaŵi, Rute anakwatiwa ndi Mwiisrayeli dzina lake Boazi. Mwana wawo amene anadzakhala fuko lobadwira la Yesu Kristu, analeredwa bwino kwambiri ndi Naomi ngati wake yemwe. Nkhani yakale imeneyi n’chitsanzo cha mmene Yehova amasamalira akazi amasiye amene amayandikira ndiponso kudalira iye. Komanso, Baibulo limatiuza kuti iye amayamikira anthu amene mwachikondi amathandiza akazi amasiye m’mayesero awo. Choncho kodi ife lerolino tingathandize motani akazi amasiye amene timakhala nawo?—Rute 4:13, 16-22; Salmo 68:5.
Athandizeni Mwachindunji Osati Mopondereza
Pothandiza mkazi wamasiye ndi bwino kulankhula momveka ndiponso mwachindunji osati mopambanitsa. Peŵani kulankhula mawu osamveka bwino monga akuti, “Ndiuzeni ngati mukufuna kanthu.” Mawu ameneŵa n’chimodzimodzi ndi kuuza munthu amene akusoŵa chofunda kapena chakudya kuti “Fundani ndipo mudye mukhute” koma osam’patsa chofunda kapena chakudyacho. (Yakobo 2:16) Anthu ambiri satha kupempha ngati akufuna chinthu chinachake, m’malo mwake, amangovutikira mumtima. Pothandiza anthu otereŵa pamafunika kuzindikira kaye zosoŵa zawo. Komabe, kupitirira muyeso mpaka kulamulira moyo wa mkazi wamasiye kungakhale kokhumudwitsa mwinanso kungayambitse mikangano. N’chifukwa chake Baibulo limagogomeza kufunika kokhala ndi malire pankhani za ena. Ngakhale limatilimbikitsa kuganizira ena, ilo limatikumbutsa kusakhala anthu odudukira pankhani za ena.—Afilipi 2:4; 1 Petro 4:15.
Rute anasonyeza mzimu wosapambanitsa woterowo kwa Naomi. Pamene anali kukhala mokhulupirika kwa mpongozi wakeyo, Rute sanali kukakamiza kapena kulamulira Naomi. Iye ankachita zinthu mwanzeru. Anali kupeza chakudya cha Naomi pamodzi ndi chake, komanso kutsatira malangizo a Naomi.—Rute 2:2, 22, 23; 3:1-6.
N’zoona kuti zinthu zofunika zingasiyane kutengera ndi anthu amene akufuna zinthuzo. Sandra yemwe tam’tchula koyambirira uja ananena kuti: “Ndinali ndi zonse zomwe ndinkafuna pa masautso anga—anzanga onse apamtima anasonkhana kukhala m’mphepete mwanga.” Mosiyana ndi zimenezo, Elaine, yemwe tam’tchula koyamba uja, anali kufuna kukhala payekha. Choncho, kukhala munthu wothandiza kumafuna kuzindikira ndi kusamala kusaloŵerera pankhani za ena komanso kufunitsitsa kuthandiza pamene kuli kofunika kutero.
Thandizo Labanja
Banja labwino ndi lachikondi, ngati lilipo, lingathandize kwambiri kuti mkazi wamasiye apirire ndi umasiye. Ngakhale kuti ena m’banjalo angathandize kuposa ena, onse angathandizire ndithu. “Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi n’cholandirika pamaso pa Mulungu.”—1 Timoteo 5:4.
Nthaŵi zambiri, thandizo landalama kapena “chipukuta misozi” zingakhale zosafunika. Akazi amasiye ena ali ndi ndalama zokwanira kusamalira zosoŵa zawo. Ndipo m’mayiko ena akazi amasiye amakhala ndi mwayi wolandira chipukuta misozi kuchokera ku boma. Komabe, ngati akazi amasiye akufuna thandizo, abanja ayenera kuthandiza. Ngati mkazi wamasiye alibe achibale oti angamuthandize kapena ngati achibalewo sangathe kuthandiza, Malemba amalimbikitsa wokhulupirira anzake kumuthandiza. Malemba amati: “Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.”—Yakobo 1:27.
Anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo zimenezi amalemekezadi akazi amasiye. (1 Timoteo 5:3) Kulemekeza munthu, makamaka kumatanthauza kuchitira munthuyo ulemu. Anthu amene amalemekezedwa amadziona kukhala ofunika okondedwa ndiponso oganiziridwa. Iwo samaona kuti anthu ena akuwathandiza chifukwa chakuti ndi udindo wawo ayi. Ngakhale kuti nayenso Rute anali mkazi wamasiye, ankalemekeza kwambiri Naomi, mwa kuchita zonse mofunitsitsa kuti Naomiyo apeze zofunika pa moyo wake ndiponso kukhazikitsa mtima wake pansi. Ndipotu mtima wa Rute unam’tchukitsa kwambiri moti yemwe anali kudzakhala mwamuna wake m’tsogolo anati: “Onse a pamudzi wa anthu a mtundu wanga adziŵa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu.” (Rute 3:11) Komanso, Naomi anali munthu wokonda Mulungu kwambiri ndiponso wosafuna zinthu zambiri. Kuyamikira kwake zimene Rute anali kum’chitira mosakayikira kunam’chititsa Rute kumam’thandiza mosangalala. Naomi alitu chitsanzo chabwino kwambiri kwa akazi amasiye lerolino.
Yandikirani kwa Mulungu
N’zoona kuti am’banja kapena mabwenzi sangaloŵe m’malo mwa wokwatirana naye womwalirayo. Pachifukwa chimenechi, n’kofunika kuti wofedwayo ayandikire kwambiri kwa “Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Talingalirani chitsanzo cha Anna, mkazi wamasiye wokhulupirika amene anali ndi zaka 84 pamene Yesu ankabadwa.
Mwamuna wake atamwalira atakhala m’banja zaka zisanu ndi ziŵiri zokha, Anna anatembenukira kwa Yehova kuti am’limbikitse. “[Iye] sanachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.” (Luka 2:36, 37) Kodi Yehova anachitapo kanthu pa kudzipereka kwaumulungu kwa Anna? Inde! Mulungu anasonyeza chikondi chake m’njira yapadera kwambiri mwa kumulola kuona mwana wakhanda amene anali kudzakhala Mpulumutsi wa dziko lonse. Zinalitu zosangalatsa ndiponso zolimbikitsa kwambiri kwa Anna! Mwachionekere iye anaona kukwaniritsidwa kwa mawu a pa Salmo 37:4 akuti: “Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.”
Ntchito za Mulungu Kudzera mwa Akristu Anzathu
Elaine ananena kuti: “Kwanthaŵi yaitali ndithu David atamwalira, ndinkamva kuwawa ngati kuti mpeni ukundibaya m’nthiti. Ndinkaganiza kuti kunali kudzimbidwa. Tsiku lina zinthu zinafika pothina kwambiri moti ndinaganiza zokaonana ndi dokotala. Mlongo mnzanga mwauzimu wozindikira anandiuza kuti mwina chisoni changa ndicho chikuchititsa zimenezi. Iye anandilangiza kuti ndim’pemphe Yehova kuti andithandize ndi kundilimbikitsa. Ndinatsatira malangizo akewo nthaŵi yomweyo. Ndinapemphera kwa Yehova mwakachetechete koma mochokera pansi pa mtima, kum’pempha kuti andilimbikitse. Ndipo anaterodi!” Elaine anayamba kupeza bwino ndipo posakhalitsa anasiya kumva kuwawa.
Makamaka akulu mumpingo angalimbikitse akazi amasiye mwa kukhala aubwenzi. Mwa kuwachilikiza mwauzimu nthaŵi zonse ndiponso kuwalimbikitsa mwanzeru ndi mozindikira, akulu angathandize akazi amasiye kuyandikira kwambiri kwa Yehova ngakhale pa mayesero awo. Akulu angathandizenso kulinganiza thandizo la zinthu zina zofunika m’moyo ngati kuli koyenera kutero. Akulu achifundo ndiponso ozindikira oterowo atha kukhaladi “pobisalira mphepo.”—Yesaya 32:2; Machitidwe 6:1-3.
Kulimbikitsidwa Kwamuyaya ndi Mfumu Yatsopano Yadziko Lapansi
Mwana amene Anna wokalambayo anakondwera atamuona zaka pafupifupi masauzande aŵiri zapitazo tsopano ndi Mfumu Yaumesiya ya boma lakumwamba la Mulungu. Boma limeneli posachedwapa lidzachotsa chilichonse chomwe chimabweretsa chisoni kuphatikizapo imfa. Pankhani imeneyi, Chivumbulutso 21:3, 4 amati: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu . . . ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Kodi mwaona kuti mawu ameneŵa akunena za “anthu”? Inde, anthu adzamasulidwa ku imfa ndi maliro ndiponso kulira komwe imfayo imachititsa.
Komanso padzakhala zinthu zina zabwino kwambiri! Baibulo limalonjezanso za kuuka kwa anthu akufa. ‘Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, [a Yesu] nadzatuluka.’ (Yohane 5:28, 29) Mofanana ndi Lazaro amene Yesu anamuukitsa ku imfa, iwo adzatuluka ali anthu enieni osati mizimu ayi. (Yohane 11:43, 44) Kenako amene ‘adzachite zabwino’ adzakhala anthu angwiro ndipo adzaona chikondi cha atate Yehova. Iye adzaolowetsa dzanja lake, nakwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.’—Salmo 145:16.
Anthu amene wokondedwa wawo anamwalira ndipo amakhulupirira chiyembekezo chodalirika chimenechi amalimbikitsidwa kwambiri. (1 Atesalonika 4:13) Choncho, ngati ndinu mkazi wamasiye, onetsetsani kuti ‘mukupempherera kosaleka’ chilimbikitso ndi chithandizo chomwe mukufuna tsiku n’tsiku kuti muthane ndi masautso anu osiyanasiyana. (1 Atesalonika 5:17; 1 Petro 5:7) Ndipo ŵerengani Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku kuti akulimbikitseni. Mukachita zimenezi, mudzaona nokha kuti ngakhale pa mayesero ndi mavuto anu monga mkazi wamasiye, Yehova adzakuthandizani kupeza mtendere.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Kukhala munthu wothandiza kumafuna kusamala kusaloŵerera pankhani za ena ndiponso kufunitsitsa kuthandiza ngati kuli kofunika kutero
[Chithunzi patsamba 7]
Mulungu anadalitsa mkazi wamasiye wokalambayo Anna