Chikhulupiriro Chimatisonkhezera Kuchitapo Kanthu!
“Upenya kuti chikhulupiriro [cha Abrahamu] chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro.”—YAKOBO 2:22.
1, 2. Kodi tidzachita chiyani ngati tili ndi chikhulupiriro?
AMBIRI amanena kuti amakhulupirira Mulungu. Komabe, chikhulupiriro wamba chongotchula pakamwa nchakufa monga mtembo. “Chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo,” analemba motero wophunzira Yakobo. Iye ananenanso kuti Abrahamu amene anali woopa Mulungu anali ndi chikhulupiriro chimene “chidachita pamodzi ndi ntchito zake.” (Yakobo 2:17, 22) Kodi mawuwa ali ndi tanthauzo lanji kwa ife?
2 Ngati tili ndi chikhulupiriro chenicheni, sitidzangokhulupirira chabe zimene timamva pamisonkhano yachikristu. Tidzapereka umboni wakuti tili ndi chikhulupiriro pokhala kuti ndife Mboni zokangalika za Yehova. Inde, chikhulupiriro chidzatisonkhezera kutsatira Mawu a Mulungu pamoyo wathu ndiponso chidzatisonkhezera kuchitapo kanthu.
Kukondera ndi Chikhulupiriro Siziyenderana
3, 4. Kodi chikhulupiriro chiyenera kukhudza motani mmene timachitira ndi ena?
3 Ngati tili ndi chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu ndi Kristu, sitidzakondera. (Yakobo 2:1-4) Ena amene Yakobo analembera sanali kusonyeza kusakondera kumene Akristu oona ayenera kusonyeza. (Aroma 2:11) Choncho, Yakobo akuti: “Musakhale nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Kristu, Ambuye wa ulemerero, ndi kusamala maonekedwe.” Wosakhulupirira wachuma wovala mphete zagolidi ndi zovala zokometsetsa atafika pamsonkhano limodzinso ndi wosakhulupirira amene ali ‘munthu wosauka wovala chovala chodetsa,’ onse aŵiri anayenera kulandiridwa bwino, koma iwo anali kusamala kwambiri achuma. Anali kupatsidwa pokhala “pabwino,” pamene kuli kwakuti osakhulupirira osauka anali kuuzidwa kuimirira kapena kukhala pansi pamapazi a wina.
4 Yehova anapereka nsembe ya dipo ya Yesu Kristu kaamba ka achuma ndi osauka omwe. (2 Akorinto 5:14) Chotero, ngati tikondera achuma, tingakhale tikupatuka pa chikhulupiriro cha Kristu, amene ‘anakhala wosauka, kuti ife ndi kusauka kwake tikakhale olemera.’ (2 Akorinto 8:9) Tisaweruze konse anthu m’njira imeneyo—ndi kulemekeza anthu kaamba ka cholinga choipa. Mulungu sakondera, koma ngati tikondera, ndiye kuti ‘tikuganizira zoipa.’ (Yobu 34:19) Pokhumba kukondweretsa Mulungu, ndithudi sitidzagonja pachiyeso cha kukondera kapena “kutama anthu chifukwa cha kupindula nako.”—Yuda 4, 16.
5. Kodi Mulungu wasankha ndani kukhala “olemera ndi chikhulupiriro,” ndipo kaŵirikaŵiri olemera mwakuthupi amatani?
5 Yakobo akutchula amene alidi achuma nalimbikitsa kuti chikondi chisonyezedwe kwa onse mosasankha. (Yakobo 2:5-9) ‘Mulungu wasankha osauka akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi oloŵa nyumba a ufumu.’ Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti osauka ndiwo amafunitsitsa kumvetsera uthenga wabwino. (1 Akorinto 1:26-29) Monga gulu, olemera mwakuthupi amapondereza ena pangongole, malipiro, ndi milandu. Amanyoza Kristu ndiponso amatizunza chifukwa chakuti tikunyamula dzina lake. Koma tiyeni titsimikize mtima kuti tidzalabadira ‘lamulo lachifumu,’ limene limafuna kuti tikonde mnansi—kukonda achuma ndi osauka mosasankha. (Levitiko 19:18; Mateyu 22:37-40) Popeza kuti ndizo zimene Mulungu amafuna, kukondera ndiko ‘kuchita uchimo.’
“Chifundo Chidzitamandira Kutsutsana Nacho Chiweruziro”
6. Kodi tingakhale motani akuswa lamulo ngati sitinachitire ena chifundo?
6 Ngati tikukondera mopanda chifundo, ndiye kuti tikuswa lamulo. (Yakobo 2:10-13) Mwa kuchita choipa chimenechi, timalakwira malamulo onse a Mulungu. Aisrayeli amene sanali kuchita chigololo koma amene anali mbala analakwira Chilamulo cha Mose. Pokhala Akristu, tikuweruzidwa ndi “lamulo la anthu aufulu [NW]”—Israyeli wauzimu amene ali m’pangano latsopano, wokhala ndi lamulo lake m’mitima mwawo.—Yeremiya 31:31-33.
7. Kodi nchifukwa ninji amene apitiriza kukondera sayenera kuyembekezera chifundo kwa Mulungu?
7 Ngati tinena kuti tili ndi chikhulupiriro koma nkupitirizabe kukondera, tili pangozi. Amene alibe chikondi ndi chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo. (Mateyu 7:1, 2) Yakobo akuti: “Chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.” Ngati tivomereza chitsogozo cha mzimu woyera wa Yehova mwa kusonyeza chifundo pazochita zathu zonse, sitidzatsutsidwa poweruzidwa. M’malo mwake, adzatichitira chifundo ndipo tidzapulumuka pa chilungamo chenicheni kapena chiweruzo choŵaŵa.
Chikhulupiriro Chimabala Ntchito Zabwino
8. Kodi munthu amene amanena kuti ali ndi chikhulupiriro koma amene sachita ntchito ali mumkhalidwe wotani?
8 Kuwonjezera pa kutipanga kukhala achikondi ndi achifundo, chikhulupiriro chimabala ntchito zinanso zabwino. (Yakobo 2:14-26) Ndithudi, chikhulupiriro chongotchula pakamwa chopanda ntchito sichidzatipulumutsa. Zoonadi, sitingakhale olungama pamaso pa Mulungu mwa ntchito za Chilamulo. (Aroma 4:2-5) Yakobo akunena za ntchito, osati zosonkhezeredwa ndi mpambo wa malamulo, koma ndi chikhulupiriro ndi chikondi. Ngati mikhalidwe imeneyi ndiyo imatisonkhezera, wolambira mnzathu wosoŵa sitidzangomfunira mafuno abwino. Tidzapereka thandizo lakuthupi kwa mbale kapena mlongo wosoŵa zovala kapena wanjala. Yakobo akufunsa kuti: ‘Ngati muuza mbale wausiŵa kuti: Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta, koma osampatsa zosoŵa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?’ Palibe. (Yobu 31:16-22) “Chikhulupiriro” chotero nchakufa!
9. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro?
9 Tingamayanjane ndi anthu a Mulungu pa zinthu zina, koma ntchito zochokeradi pansi pa mtima zokha nzimene zingachitire umboni mawu athu akuti timakhulupirira. Zili bwino ngati takana chiphunzitso cha Utatu ndipo tikukhulupirira kuti kuli Mulungu woona mmodzi. Komatu, kungokhulupirira sindiko chikhulupiriro chenicheni. “Ziŵanda zikhulupiranso,” ndipo “zinthunthumira” mwamantha chifukwa chakuti zidzawonongedwa. Ngati tili ndi chikhulupiriro chenicheni, icho chidzatisonkhezera kuchita ntchito monga kulalikira uthenga wabwino ndi kupatsa okhulupirira anzathu zakudya ndi zovala. Yakobo akufunsa kuti: “Ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe [wopanda chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu], kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe?” Inde, chikhulupiriro chimafuna ntchito.
10. Kodi nchifukwa ninji Abrahamu akutchedwa kuti “kholo la onse akukhulupira”?
10 Chikhulupiriro cha kholo lakalelo loopa Mulungu, Abrahamu, chinamsonkhezera kuchitapo kanthu. Pokhala “kholo la onse akukhulupira,” ‘anayesedwa wolungama ndi ntchito, paja adapereka mwana wake Isake nsembe pa guwa la nsembe.’ (Aroma 4:11, 12; Genesis 22:1-14) Bwanji ngati Abrahamu anasoŵa chikhulupiriro chakuti Mulungu angaukitse Isake ndi kukwaniritsa lonjezo Lake la mbewu kudzera mwa iye? Abrahamu sakanayesa nkomwe kupereka mwana wake nsembe. (Ahebri 11:19) Ntchito za Abrahamu zosonyeza kumvera ndizo zinachititsa kuti ‘chikhulupiriro chake chiyesedwe changwiro,’ kapena kuti chikhale chokwanira. Chotero, “anakwaniridwa malembo [Genesis 15:6] onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudaŵerengedwa kwa iye chilungamo.” Ntchito ya Abrahamu poyesa kupereka nsembe Isake inatsimikiza mawu oyamba a Mulungu akuti Abrahamu anali wolungama. Mwa ntchito zachikhulupiriro, iye anasonyeza chikondi chake kwa Mulungu nadzatchedwa kuti “bwenzi la Mulungu.”
11. Kodi tili ndi umboni wotani wa chikhulupiriro ponena za Rahabi?
11 Abrahamu anasonyeza “kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha.” Zinalinso motero ndi Rahabi, mkazi wadama wa ku Yeriko. ‘Anayesedwa wolungama ndi ntchito, popeza adalandira amithenga [achiisrayeli], nawatulutsa adzere njira ina’ moti anazemba adani awo achikanani. Asanaonane ndi azondi a Israyeli, iye anazindikira kuti Yehova ndiye Mulungu woona, ndipo zimene ananena pambuyo pake ndi kusiya kwake dama zinachitira umboni chikhulupiriro chake. (Yoswa 2:9-11; Ahebri 11:31) Pambuyo pa chitsanzo chachiŵirichi cha chikhulupiriro chosonyezedwa ndi ntchito, Yakobo akuti: “Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.” Munthu atafa, samakhalanso ndi mphamvu yopatsa moyo, kapena kuti “mzimu,” ndipo samatha kuchita kalikonse. Chikhulupiriro wamba chongotchula pakamwa nchakufa ndiponso chopanda pake monga mtembo. Komabe, ngati tili ndi chikhulupiriro chenicheni, chidzatisonkhezera kuchitapo kanthu mwaumulungu.
Lamulirani Lilimelo!
12. Kodi akulu a mumpingo ayenera kuchita chiyani?
12 Kulankhula ndi kuphunzitsa nakonso kungapereke umboni wa chikhulupiriro, koma kudziletsa nkofunika. (Yakobo 3:1-4) Pokhala aphunzitsi mumpingo, akulu ali ndi udindo waukulu ndi mangaŵa aakulu kwa Mulungu. Chotero, ayenera kupenda zolinga zawo ndi ziyeneretso zawo modzichepetsa. Kuwonjezera pa chidziŵitso ndi luso, amunawa ayenera kukonda kwambiri Mulungu ndi okhulupirira anzawo. (Aroma 12:3, 16; 1 Akorinto 13:3, 4) Akulu ayenera kusumika uphungu wawo pa Malemba. Ngati mkulu walakwitsa pophunzitsa ndipo zimenezi zachititsa mavuto kwa ena, iye adzaweruzidwa koŵaŵa ndi Mulungu kudzera mwa Kristu. Choncho akulu ayenera kukhala odzichepetsa ndi akhama, omamatira ku Mawu a Mulungu mokhulupirika.
13. Kodi nchifukwa ninji timakhumudwa pamawu?
13 Ngakhale aphunzitsi aluso—tingoti tonsefe—‘timakhumudwa pa zinthu zambiri’ chifukwa cha kupanda ungwiro. Kukhumudwa m’mawu ndiko chimodzi mwa zolakwa zimene timalakwa mobwerezabwereza koposa ndiponso zowononga kwambiri. Yakobo akuti: “Munthu akapanda kukhumudwa pamawu, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.” Mosiyana ndi Yesu Kristu, ifeyo sitimatha kulamulira lilime lathu mwangwiro. Ngati tingatero, tingathenso kulamulira ziŵalo zina za thupi lathu. Ndi iko komwe, zogwirira za m’kamwa zimapangitsa akavalo kupita kumene tikuwasonyeza, ndipo mwa kugwiritsira ntchito tsigiro laling’ono, wogwira tsigiro angapotoze monga momwe akufunira ngakhale chombo chachikulu chotengedwa ndi mphepo yamphamvu.
14. Kodi Yakobo akugogomezera motani za kuyesayesa kulamulira lilime?
14 Tonsefe tiyenera kuvomereza moona mtima kuti kulamulira lilime lathu kumafuna kuyesayesa. (Yakobo 3:5-12) Chogwirira kavalo nchaching’ono pochiyerekezera ndi kavalo; chimodzimodzinso ndi tsigiro poliyerekezera ndi chombo. Ndipo poliyerekezera ndi thupi, lilime nlaling’ono “ndipo lidzikuzira zazikulu.” Popeza Malemba amafotokoza bwino lomwe kuti kudzitama sikumakondweretsa Mulungu, tiyeni tipemphe thandizo lake kuti tikupeŵe. (Salmo 12:3, 4; 1 Akorinto 4:7) Timangenso lilime lathu pamene taputidwa, pokumbukira kuti kamoto kakang’ono kangayatse nkhalango yonse. Monga momwe Yakobo akusonyezera, “lilime ndilo moto” umene ungawononge zinthu zambiri. (Miyambo 18:21) Ndithudi, lilime losaweruzika ndilo “dziko la chosalungama”! Kalikonse koipa m’dzikoli losaopa Mulungu nkokhudzana ndi lilime losalamulirika. Ilo ndilo limachititsa zinthu zowonongazi monga zinenezo ndi chiphunzitso chonyenga. (Levitiko 19:16; 2 Petro 2:1) Mukutipo bwanji? Kodi chikhulupiriro chathu sichiyenera kutisonkhezera kulimbikira kulamulira lilime lathu?
15. Kodi lilime losamangidwa lingawononge motani?
15 Lilime losamangidwa ‘lidetsa thupi lonse.’ Mwachitsanzo, ngati mobwerezabwereza atigwira bodza, tingadziŵike kuti ndife abodza. Koma kodi lilime losaweruzika ‘limayatsa mayendedwe achibadwidwe’ motani? Mwa kuchititsa moyo kukhala ngati wodzaza mavuto okhaokha. Mpingo wonse ungasokonezeke ndi lilime limodzi losalamulirika. Yakobo akutchula “gehena,” Chigwa cha Hinomu. Chigwachi, kumene kale anali kuperekerako nsembe ana, chinadzakhala kotenthera zinyalala za Yerusalemu. (Yeremiya 7:31) Choncho Gehena amatanthauza chiwonongeko. M’lingaliro lina, Gehena wapatsa mphamvu yake yowononga kwa lilime losaweruzika. Ngati sitimanga lilime lathu, ife tomwe tikhoza kuvutika ndi moto woyatsa tokha. (Mateyu 5:22) Tikhozanso kuchotsedwa mumpingo chifukwa cholalatira munthu.—1 Akorinto 5:11-13.
16. Polingalira za kuwononga kumene lilime losaweruzika lingachite, kodi tiyenera kuchitanji?
16 Monga momwe mumadziŵira poŵerenga Mawu a Mulungu, Yehova analamula kuti munthu ayenera kulamulira nyama. (Genesis 1:28) Ndipo mitundu yonse ya zolengedwa yaphunzitsidwa. Mwachitsanzo, mbalame za mphamba zophunzitsidwa azigwiritsira ntchito mu uzimba. ‘Zokwawa’ zimene Yakobo akutchula zingaphatikizepo njoka zimene oseŵeretsa njoka amaseŵera nazo. (Salmo 58:4, 5) Munthu amalamulira ngakhale anamgumi, koma pokhala anthu ochimwa timalephera kuphunzitsa lilime kotheratu. Ngakhale zili tero, tiyenera kupeŵa kulankhula mawu otukwana, onyoza, kapena oneneza. Lilime losaweruzika lingakhale chiŵiya choopsa chodzaza ululu wakupha. (Aroma 3:13) Mwachisoni, lilime la aphunzitsi onyenga linachititsa Akristu ena oyambirira kukana Mulungu. Choncho tisadzilole kukopeka ndi mawu aululu a ampatuko, kaya olankhulidwa pakamwa kapena olembedwa.—1 Timoteo 1:18-20; 2 Petro 2:1-3.
17, 18. Kodi nkusinthasintha kotani kumene kwatchulidwa pa Yakobo 3:9-12, ndipo tiyenera kuchitanji pankhaniyi?
17 Chikhulupiriro mwa Mulungu ndi kukhumba kumkondweretsa zingatitetezere ku mpatuko ndipo zingatichinjirize kuti tisagwiritsire ntchito lilime mosinthasintha. Ponena za kusinthasintha kwa ena, Yakobo akunena kuti ‘timayamika nalo Atate wathu, Yehova, ndi kutemberera anthu okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu.’ (Genesis 1:26) Yehova ndiye Atate wathu chifukwa chakuti “apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:24, 25) Alinso Atate wa Akristu odzozedwa m’lingaliro lauzimu. Tonsefe tili ndi “mafanizidwe a Mulungu” pamalingaliro athu ndi khalidwe, kuphatikizapo chikondi, chilungamo, ndi nzeru zimene zimatisiyanitsa ndi nyama. Choncho, kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikhulupirira Yehova?
18 Ngati tatemberera anthu, ndiye kuti tawafunira zoipa kapena kuti kuwaitanira tsoka kuti liwagwere. Popeza sindife aneneri ouziridwa ndi Mulungu opatsidwa mphamvu zoitanira tsoka pa munthu aliyense, kalankhulidwe koteroko kangakhale umboni wakuti timawada, zimene zingachititse kuti kulambira kwathu Mulungu kukhale kwachabe. Nzosayenera kuti zonse ziŵiri “chiyamiko ndi temberero” zituluke m’kamwa mwa munthu mmodzimodzi. (Luka 6:27, 28; Aroma 12:14, 17-21; Yuda 9) Kungakhale kuchimwa kotani nanga kuimba zitamando kwa Mulungu pamisonkhano ndiyeno pambuyo pake kulankhula zoipa ponena za okhulupirira anzathu! Madzi okoma ndi oŵaŵa omwe sangatuluke pakasupe mmodzi. Monga momwe ‘mkuyu sukhoza kubala azitona, kapena mpesa kubala nkhuyu,’ madzi amchere sangatulutse madzi okoma. Ngati ife, amene tiyenera kulankhula zinthu zabwino, nthaŵi zonse timalankhula mawu oipa, ndiye kuti pali kenakake kolakwika mwauzimu. Ngati tili ndi chizoloŵezi chimenechi, tiyeni tipemphere kuti Yehova atithandize kusiya kulankhula m’njira imeneyo.—Salmo 39:1.
Chitani Zinthu Mwanzeru Yochokera Kumwamba
19. Ngati timatsogozedwa ndi nzeru yochokera kumwamba, kodi tidzachita zotani kwa ena?
19 Tonsefe tifunikira nzeru kuti tilankhule ndi kuchita zinthu zoyenerera awo amene ali ndi chikhulupiriro. (Yakobo 3:13-18) Ngati timasonyeza mantha aulemu kwa Mulungu, iye amatipatsa nzeru zochokera kumwamba, luso la kugwiritsira ntchito chidziŵitso molongosoka. (Miyambo 9:10; Ahebri 5:14) Mawu ake amatiphunzitsa mmene tingasonyezere “nzeru yofatsa.” Ndipo chifukwa chakuti ndife ofatsa, timachirikiza mtendere wa mumpingo. (1 Akorinto 8:1, 2) Alionse amene amadzitamandira kuti ndi aphunzitsi aluso a okhulupirira anzawo ‘akunama motsutsana nacho choonadi chachikristu,’ chimene chimatsutsa kudzikuza kwawo. (Agalatiya 5:26) “Nzeru” yawo ili ya “padziko”—ya anthu ochimwa olekanitsidwa ndi Mulungu. Iyo ili “yachifuniro cha chibadwidwe,” yochititsidwa ndi zikhumbo za thupi. Ndithudi, ilinso “ya ziŵanda,” popeza kuti mizimu yoipa imadzitukumula! (1 Timoteo 3:6) Chotero tiyeni tichite zinthu mwanzeru ndiponso modzichepetsa kuti tisachite kalikonse kosonkhezera kukula kwa ‘zinthu zoipa’ monga kunenezana ndi kukondera.
20. Kodi nzeru yochokera kumwamba mungaifotokoze motani?
20 “Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera,” yotiyeretsa ife m’makhalidwe ndiponso mwauzimu. (2 Akorinto 7:11) Ili “yamtendere,” yotisonkhezera kulondola mtendere. (Ahebri 12:14) Nzeru yakumwamba imatipanga kukhala ‘aulere [“ololera,” NW]’ osati aliuma ndi osayanjanitsika. (Afilipi 4:5) Nzeru yochokera kumwamba ili “yomvera bwino,” yosonkhezera kumvera pophunzitsidwa ndi Mulungu ndi kugwirizana ndi gulu la Yehova. (Aroma 6:17) Nzeru yochokera kumwamba imatipanganso kukhala achifundo. (Yuda 22, 23) Popeza kuti ili yodzala ndi “zipatso zabwino,” imatisonkhezera kuganizira ena ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi ubwino, chilungamo, ndi choonadi. (Aefeso 5:9) Ndiponso pokhala okonda mtendere, tili ndi “chipatso cha chilungamo” chimene chimakula m’mikhalidwe yamtendere.
21. Malinga ndi Yakobo 2:1–3:18, kodi kukhulupirira kwathu Mulungu kuyenera kutisonkhezera kuchita chiyani?
21 Kunena zoona chikhulupiriro chimatisonkhezeradi kuchitapo kanthu. Chimatichititsa kusakondera, kukhala achifundo, ndi okangalika pantchito zabwino. Chikhulupiriro chimatithandiza kulamulira lilime ndi kuchita zinthu mwanzeru yochokera kumwamba. Koma si zokhazo zimene tingaphunzire m’kalatayi. Yakobo ali ndi uphungu wina wowonjezereka umene ungatithandize kukhala ndi khalidwe labwino loyenerera awo amene amakhulupirira Yehova.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi cholakwika nchiyani ndi kukondera?
◻ Kodi chikhulupiriro ndi ntchito zimayenderana motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kulamulira lilime nkofunika kwambiri?
◻ Kodi nzeru yochokera kumwamba njotani?