Tiyenera Kudalira Yehova
“Pakuti Yehova adzadalirika kwa iwe.”—MIYAMBO 3:26, NW.
1. Ngakhale kuti ambiri amati amadalira Mulungu, kodi nchiyani chomwe chikusonyeza kuti iwo sachita zimenezo nthaŵi zonse?
MAWU akuti “Timadalira Mulungu” analembedwa pandalama ya ku United States of America. Koma kodi onse amene amagwiritsira ntchito ndalamayi, m’dzikomo kapena m’dziko lina, amadaliradi Mulungu? Kapena kodi iwo amadalira kwambiri ndalama yeniyeniyo? Kudalira ndalama ya m’dziko limenelo kapena ya m’dziko lina nkosiyana ndi kudalira Mulungu wamphamvuyonse wachikondi, amene sagwiritsira ntchito molakwa mphamvu zake, yemwenso sali waumbombo mpang’ono pomwe. Ndithudi, iye amadana kwambiri ndi umbombo.—Aefeso 5:5.
2. Kodi Akristu oona amaiona motani mphamvu ya chuma?
2 Akristu oona amadalira Mulungu, osati chuma chokhala ndi “mphamvu yonyenga.” (Mateyu 13:22, NW) Iwo amadziŵa kuti ndalama zili ndi mphamvu yochepa kwambiri yodzetsa chimwemwe ndi kutchinjiriza moyo. Koma sizili choncho ndi mphamvu ya Mulungu Wamphamvuyonse. (Zefaniya 1:18) Choncho, uphungu wotsatirawu ngwopindulitsadi: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu”!—Ahebri 13:5.
3. Kodi nkhani ya pa Deuteronomo 31:6 ikusonyeza motani lingaliro la mawu a Paulo amene anagwira pavesilo?
3 Pamene anali kulemba mawu ali pamwambawo kwa Akristu achihebri, mtumwi Paulo anali kugwira mawu malangizo amene Mose anapatsa Aisrayeli pamene iye anali pafupi kufa, ndipo anati: “Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; iye sadzakusoŵani, kapena kukusiyani.” (Deuteronomo 31:6) Nkhaniyi ikusonyeza kuti Mose anali kuwalimbikitsa kuti azidalira Yehova pazinthu zonse osati kungomdalira kuti adzawapatsa zosoŵa zakuthupi zokha ayi. Motani?
4. Kodi nzinthu ziti zimene Mulungu anachita zomwe zinapangitsa kuti Aisrayeli azimdalira?
4 Pazaka 40 zimene Aisrayeli anali kuyendayenda m’chipululu, Mulungu anali kuwapatsa zosoŵa zawo zonse mokhulupirika. (Deuteronomo 2:7; 29:5) Iye anawatsogoleranso. Njira ina imene anasonyezera zimenezi inali mwa kuwapatsa mtambo masana ndi moto usiku, zimene zinawatsogolera paulendo wawo wokaloŵa “m’dziko moyenda mkaka ndi uchi.” (Eksodo 3:8; 40:36-38) Pamene nthaŵi yoloŵadi m’Dziko Lolonjezedwalo inafika, Yehova anasankha Yoswa kuti aloŵe m’malo mwa Mose. Iwo anali kulingalira kuti anthu okhala m’dzikomo adzawalepheretsa kuloŵamo. Koma Yehova anayenda ndi anthu ake kwazaka makumi ambiri, kotero kuti iwo sanafunikire kuchita mantha. Aisrayeli anali ndi umboni waukulu wotsimikizira kuti Yehova ndiye Mulungu amene anayenera kumdalira!
5. Kodi mkhalidwe wa Akristu lerolino ngwofanana motani ndi mkhalidwe wa Aisrayeli kalelo asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa?
5 Lerolino, Akristu akhala akuyenda m’chipululu cha dziko loipa lilipoli paulendo wawo wokaloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. Ena a iwo akhala akuyenda m’chipululuchi kwa zaka zoposa 40. Tsopano aima m’malire a dziko latsopano la Mulungu. Komabe, adani akudikirirabe m’maliremo ncholinga cholepheretsa aliyense wofuna kuloŵa m’dziko limene lidzakhala longa Dziko Lolonjezedwa, laulemerero waukulu kuposa lija lakale loyenda mkaka ndi uchi. Choncho, kwa Akristu lerolino, mawu a Mose omwe anabwerezedwa ndi Paulo ngoyenereradi, pamene anati: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu”! Onse amene adzapitirizabe kulimba mtima, kukhala ndi chikhulupiriro chosagwedera, ndi kudalira Yehova adzalandiradi mphothoyo.
Chidaliro Chozikidwa pa Chidziŵitso ndi Ubwenzi
6, 7. (a) Kodi nchiyani chomwe chinaika pachiyeso chidaliro cha Abrahamu mwa Yehova? (b) Kodi Abrahamu ayenera kuti anamva bwanji popita kumalo okaperekera nsembe Isake?
6 Nthaŵi inayake, Abrahamu, kholo la Aisrayeli, analamulidwa kuti apereke mwana wake Isake monga nsembe yopsereza. (Genesis 22:2) Kodi nchiyani chomwe chinapangitsa atate wachikondi ameneyu kudalira kwambiri Yehova mpaka kukhala wofunitsitsa kuchita zimenezo mosanyinyirika? Ahebri 11:17-19 akuyankha kuti: “Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha; amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbewu yako idzaitanidwa: poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.”
7 Kumbukirani kuti Abrahamu ndi Isake anayenda masiku atatu popita kumene anali kukaperekera nsembe. (Genesis 22:4) Abrahamu anali ndi nthaŵi yokwanira yoti akanatha kusintha maganizo pazimene anapemphedwa kuchita. Tangolingalirani mmene anamvera mumtima mwake? Kubadwa kwa Isake kunali chinthu chosangalatsa kwambiri chosayembekezereka. Umboni umenewo wa kuloŵererapo kwa Mulungu unakulitsa ubwenzi wapakati pa iye ndi Abrahamu ndi mkazi wake Sara, yemwe poyambirira anali wosabala. Choncho, iwo anayembekezera mwachidaliro zimene zinali kudzachitikira Isake ndi mbadwa zake. Malinga nzimene Mulungu anawapempha kuti achite, kodi tsopano imeneyi inali nthaŵi yogwiritsidwa mwala pachikhumbo chawo?
8. Kodi chidaliro cha Abrahamu mwa Mulungu chinaposa motani kungokhulupirira kuti Iye akanaukitsa Isake?
8 Komabe, Abrahamu anali ndi chidaliro chifukwa chakuti anadziŵa mmene mabwenzi amakonderana. Monga “bwenzi la Mulungu,” Abrahamu “anakhulupirira Mulungu, ndipo kudaŵerengedwa kwa iye chilungamo.” (Yakobo 2:23) Abrahamu anadalira Yehova osati chifukwa cha kungokhulupirira kuti Mulungu angaukitse Isakeyo ayi. Abrahamu anadziŵa kuti zimene Yehova anampempha zinali zoyenera, ngakhale kuti Abrahamuyo sanadziŵe zonse zimene zinali kudzachitika. Analibe chifukwa chokayikirira chilungamo cha Yehova pamene anampempha zimenezi. Kenaka, chidaliro cha Abrahamu chinalimbitsidwa pamene mngelo wa Yehova analoŵererapo potetezera Isake kuti asaperekedwe nsembe.—Genesis 22:9-14.
9, 10. (a) Kodi ndi liti kumbuyoko pamene Abrahamu anasonyeza kuti anali kudalira Yehova? (b) Kodi ndi phunziro lofunika liti limene tingatengepo pazimene zinachitikira Abrahamu?
9 Abrahamu anasonyezanso kuti anadalira chilungamo cha Yehova zaka 25 kumbuyoko. Atachenjezedwa kuti Sodomu ndi Gomora anali kudzawonongedwa, iye anadera nkhaŵa kwambiri anthu olungama okhala mmenemo, kuphatikizapo Loti, mwana wa mbale wake. Abrahamu anadandaulira Mulungu kuti: “Musamatero ayi, kupha olungama pamodzi ndi oipa, [kuti] olungama akhale monga oipa; musamatero ayi; kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?”—Genesis 18:25.
10 Khololo Abrahamu anadziŵa kuti Yehova sachita zosalungama. Pambuyo pake wamasalmo anaimba kuti: “Yehova ali wolungama m’njira zake zonse, ndi wachifundo m’ntchito zake zonse.” (Salmo 145:17) Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimavomereza zimene Yehova walola kuti ndiyang’anizane nazo mosakayikira konse za chilungamo chake? Kodi ndili wotsimikiza kuti chilichonse chimene iye adzalola kuti chindichitikire chidzakhala chondipindulitsa ndiponso chopindulitsa ena?’ Ngati yankho lathu nlakuti inde, ndiye kuti tatengapo phunziro lothandiza pa zimene zinachitikira Abrahamu.
Kudalira Anthu Osankhidwa ndi Yehova
11, 12. (a) Kodi ndi mbali iti ya chidaliro imene ili yofunika kwa atumiki a Mulungu? (b) Kodi nthaŵi zina tingayang’anizane ndi vuto lotani?
11 Anthu amene amadalira Yehova amadaliranso anthu amene amasankhidwa ndi Yehova kuti akwaniritse zolinga zake. Kwa Aisrayeli, zimenezi zinatanthauza kudalira Mose ndipo pambuyo pake kudalira woloŵa m’malo mwake, Yoswa. Kwa Akristu oyambirira, zinatanthauza kudalira atumwi ndiponso amuna omwe anali akulu a mumpingo wa ku Yerusalemu. Kwa ife lerolino, zimatanthauza kudalira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” woikidwa kuti azitipatsa “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake,” ndiponso kudalira ena a m’kagulu kameneka amene amapanga Bungwe Lolamulira.—Mateyu 24:45.
12 Zoonadi, kudalira anthu amene amatsogolera mumpingo wachikristu kumapindulitsa ife enife. Timauzidwa kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.”—Ahebri 13:17.
Peŵani Kukayikira Anthu Osankhidwa ndi Yehova
13. Kodi nchifukwa ninji timadalira anthu amene amaikidwa kuti azititsogolera?
13 Baibulo limatithandiza kuti tizikhala olingalira bwino pamene tidalira amene amatsogolera pakati pa anthu a Yehova. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi Mose sankalakwa? Kodi atumwi nthaŵi zonse ankasonyeza mzimu wa Kristu umene Yesu anafuna kuti iwo akhale nawo?’ Mayankho ake ngodziŵikiratu. Yehova wasankha amuna okhulupirika ndiponso odzipereka kuti atsogolere anthu ake, ngakhale kuti iwo ngopanda ungwiro. Mofananamo, popeza kuti akulu omwe tili nawo lerolino ngopanda ungwiro, tiyenera kuwaonabe monga ‘[oikidwa ndi] Mzimu Woyera [kuti akhale] oyang’anira, kuti aŵete Eklesia wa Mulungu.’ Tiyenera kuwathandiza ndiponso kuwalemekeza.—Machitidwe 20:28.
14. Kodi nchiyani chomwe chinali chapadera kwambiri pamene Yehova anasankha Mose osati Aroni kapena Miriamu kuti akhale mtsogoleri?
14 Aroni anali wamkulu kuposa Mose ndi zaka zitatu, koma mlongo wawo Miriamu anali wamkulu kuposa onsewo. (Eksodo 2:3, 4; 7:7) Ndipo popeza kuti Aroni ankalankhula bwino kusiyana ndi Mose, iye anaikidwa kuti azitumikira monga wolankhulira mbale wakeyo. (Eksodo 6:29–7:2) Komabe, pofuna kuti atsogolere Aisrayeli, Yehova sanasankhe wamkuluyo, Miriamu, kapena wolankhula bwinoyo, Aroni. Iye anasankha Mose podziŵa bwino zochitika ndi zofunika za panthaŵiyo. Nthaŵi inayake atasoŵa nzeru imeneyi, Aroni ndi Miriamu anadandaula kuti: “Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga?” Miriamu, amene mwinamwake anali woyambitsa, analangidwa chifukwa cha khalidwe lake losachitira ulemu munthu amene anasankhidwa ndi Yehova, amene iyeyo ndi Aroni anayenera kumuona monga “wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.”—Numeri 12:1-3, 9-15.
15, 16. Kodi Kalebi anasonyeza motani kuti anali kudalira Yehova?
15 Pamene azondi 12 anatumidwa kukazonda Dziko Lolonjezedwa, azondi 10 anabwerako ndi lipoti loipa. Iwo anachititsa mantha Aisrayeli mwa kunena za Akanani omwe anali “anthu aatali misinkhu.” Zimenezi zinapangitsa kuti Aisrayeliwo ayambe ‘kudandaulira Mose ndi Aroni.’ Koma si azondi onse amene sanadalire Mose ndi Yehova. Timaŵerenga kuti: “Koma Kalebi anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene.” (Numeri 13:2, 25–33; 14:2) Yoswa, mzondi mnzake, anachirimikanso mofanana ndi Kalebi. Onse aŵiriwa anasonyeza kuti anadalira Yehova pamene anati: “Yehova akakondwera nafe, adzatiloŵetsa m’dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Chokhachi . . . musamaopa anthu a m’dzikomo; . . . Yehova ali nafe; musamawaopa.” (Numeri 14:6-9) Iwo anafupidwa chifukwa chodalira Yehova. Mwa akulu onse a mumbadwo wa panthaŵiyo, anali Kalebi, Yoswa, ndi Alevi angapo okha amene anapeza mwayi woloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.
16 Patapita zaka zingapo, Kalebi anati: “Koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse. . . . Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi makumi anayi ndi zisanu kuyambira nthaŵi ija Yehova ananena kwa Mose mawu awa, poyenda Israyeli m’chipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wazaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lerolino. Koma lerolino ndili wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano.” (Yoswa 14:6-11) Taonani kuti Kalebi anali kuyembekezera zabwino, anali wokhulupirika, ndiponso anali wamphamvu. Komatu Yehova sanasankhe Kalebiyo kuti aloŵe m’malo mwa Mose. Mwayi umenewu unaperekedwa kwa Yoswa. Tingatsimikize kuti panali zifukwa zimene Yehova anamsankhira, ndipo anasankhadi bwino.
17. Kodi nchiyani chimene chingatipangitse kulingalira kuti Petro sanali woyenerera kupatsidwa udindo?
17 Mtumwi Petro anakana Ambuye wake katatu. Anachitanso zinthu mopupuluma, nadula khutu la kapolo wa mkulu wa ansembe. (Mateyu 26:47-55, 69-75; Yohane 18:10, 11) Ena anganene kuti Petro anali wamantha, munthu wosakhazikika, wosayenera kupatsidwa udindo wapadera. Komabe, kodi ndani amene anapatsidwa mafungulo a Ufumu, kupatsidwa mwayi wotsegula njira ya maitanidwe akumwamba kaamba ka magulu atatu? Anali Petro.—Machitidwe 2:1-41; 8:14-17; 10:1-48.
18. Malinga nkunena kwa Yuda, kodi ndi tchimo liti limene tiyenera kulipeŵa?
18 Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti tiyenera kupeŵa khalidwe lokayikira ena chifukwa cha maonekedwe akunja. Ngati timadalira Yehova, sitidzakayikira anthu osankhidwa ndi iye. Ngakhale kuti mpingo wake wapadziko lapansi ngwopangidwa ndi anthu opanda ungwiro, amene sadzinenera kukhala olungama, iye akuwagwiritsira ntchito mwamphamvu. Yuda, mbale wa Yesu mwa atate ena, anachenjeza Akristu a m’zaka za zana loyamba ponena za anthu ‘opeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero.’ (Yuda 8-10) Tisakhaletu monga iwo.
19. Kodi nchifukwa ninji palibe chifukwa chokayikirira anthu amene amasankhidwa ndi Yehova?
19 Mwachionekere, Yehova amasankha anthu kuti agwire ntchito zina ngati iwo ali ndi mikhalidwe yoyenerera yowatheketsa kutsogolera anthu ake m’njira imene iye akufuna kuti iwo ayendemo panthaŵiyo. Tiyenera kuyesetsa kuzindikira bwino mfundo imeneyi, osati kukayikira anthu amene Mulungu amasankha, koma tiyenera kukhala okhutira tikumatumikira Yehova modzichepetsa pantchito imene iye watipatsa aliyense payekha. Tikatero tidzasonyeza kuti tikudaliradi Yehova.—Aefeso 4:11-16; Afilipi 2:3.
Kudalira Chilungamo cha Yehova
20, 21. Kodi tingaphunzireponji pazimene Mulungu anachita kwa Mose?
20 Ngati nthaŵi zina timadzidalira kwambiri osadalira kwenikweni Yehova, tiyeni tiphunzire pazimene zinachitikira Mose. Pamene anali ndi zaka 40 zakubadwa, popanda womuuza, iye anafuna kupulumutsa Aisrayeli mu ukapolo ku Igupto. Malingaliro akewo anali abwinodi, koma sanathandizire kuti Aisrayeli alanditsidwe mwamsanga, komanso sanampindulire. Chotsatirapo chake iye anakakamizika kuthaŵa m’dzikomo. Ataphunzira phunziro loŵaŵa kwazaka 40 m’dziko lachilendo mpamene iye anayenerera kusankhidwa kukachita zimene anafuna poyamba paja. Panthaŵiyi, anali ndi chidaliro chakuti Yehova adzamchirikiza popeza kuti zinthu zinali kuchitika monga momwe Yehova anafunira panthaŵi Yake yoikika.—Eksodo 2:11–3:10.
21 Aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nthaŵi zina ndimayamba ndine kuchita zinthu zomwe Yehova ndi akulu oikidwa mumpingo sananene kuti zichitike, ndikumayesa kufulumiza zinthuzo kapena kuzichita mmene ndikufunira? M’malo molingalira kuti ndikumanidwa udindo wina, kodi ndikuvomera mofunitsitsa maphunziro amene ndikulandirabe?’ Kwenikweni, kodi tatengapo phunziro lofunika pazimene zinachitikira Mose?
22. Ngakhale kuti anataya mwayi waukulu, kodi Mose anali ndi malingaliro otani ponena za Yehova?
22 Ndiponso, tingaphunzire phunziro lina pazimene zinachitikiranso Mose. Numeri 20:7-13 akutiuza za tchimo limene iye anachita, limene linamtayitsa mwayi waukulu. Iye anataya mwayi wotsogolera Aisrayeli kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Kodi iye ananena kuti Yehova sanaweruze mwachilungamo? Kodi iye anakakhala kwayekha, kunena kwake titero, nakwiya kwambiri akumalingalira kuti Mulungu anamchitira zoipa? Kodi Mose anasiya kudalira chilungamo cha Mulungu? Tingapeze mayankho ake m’mawu amene Mose iyemwini anauza Aisrayeli iye atakhala pang’ono kufa. Ponena za Yehova, Mose anati: “Ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Ndithudi, Mose anapitirizabe kudalira Yehova mpaka mapeto. Nanga bwanji za ife? Kodi ifeyo aliyense payekha akuchitapo kanthu pofuna kulimbitsa chidaliro chake mwa Yehova ndi chilungamo chake? Kodi tingachite zimenezo motani? Tiyeni tione.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Aisrayeli anayenera kudalira Yehova pazifukwa ziti?
◻ Ponena za chidaliro, kodi tingaphunzireponji pazimene zinachitikira Abrahamu?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa khalidwe lokayikira anthu amene amasankhidwa ndi Yehova?
[Chithunzi patsamba 13]
Kudalira Yehova kumaphatikizapo kulemekeza anthu amene amatsogolera mumpingo