‘Funafunani Mtendere ndi Kuulondola’
‘Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.’ —SALMO 35:27.
1. Kodi ndi mtendere wotani umene timasangalala nawo lerolino?
HA, NCHOSANGALATSA chotani nanga kukhala pamtendere m’dziko logawikana ili! Nchokondweretsa chotani nanga kulambira Yehova, “Mulungu wa mtendere yekha,” ndikugawana madalitso a “pangano [lake] la mtendere”! Nkotonthoza chotani nanga, pakati pa zotsendereza moyo, kudziŵa ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse’ ndikukumana ndi ‘chimangiriro cha mtendere’ chimene chimagwirizanitsa anthu a Mulungu mosasamala kanthu za mtundu wawo, chinenero, fuko, kapena chiyambi cha mayanjano!—1 Atesalonika 5:23; Ezekieli 37:26; Afilipi 4:7; Aefeso 4:3.
2, 3. (a) Pamene kuli kwakuti anthu a Mulungu monga gulu adzapirira, kodi nchiyani chingachitikire Mkristu aliyense? (b) Kodi Baibulo limatifulumiza kuchitanji?
2 Monga Mboni za Yehova, timaukonda kwambiri mtendere umenewu. Komabe, sitingautenge mosasamala. Mtendere sumadzisunga wokha kokha chifukwa chakuti tiri ogwirizana ndi mpingo Wachikristu kapena kukhala mbali ya banja Lachikristu. Pamene kuli kwakuti otsalira odzozedwa ndi anzawo a “nkhosa zina” adzapirira monga gulu limodzi lankhosa kufikira kumapeto, munthu aliyense payekha angataikiridwe mtenderewu ndikugwa.—Yohane 10:16; Mateyu 24:13; Aroma 11:22; 1 Akorinto 10:12.
3 Mtumwi Paulo anachenjeza Akristu odzozedwa a m’tsiku lake kuti: “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.” (Ahebri 3:12) Chenjezoli limagwiranso ntchito ku khamu lalikulu. Chotero Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti: ‘Funafunani mtendere ndi kuulondola. Pakuti maso a Yehova ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Yehova iri pa ochita zoipa.’—1 Petro 3:10-12; Salmo 34:14, 15.
‘Chisamaliro cha Thupi’
4. Kodi nchiyani chomwe chingawononge mtendere wathu ndi Mulungu?
4 Kodi nchiyani chomwe chingadodometse kulondola kwathu mtendere? Paulo akutchula chinthu chimodzi pamene akuti: ‘Chisamaliro cha thupi chiri imfa; koma chisamaliro cha mzimu chiri moyo ndi mtendere. Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu.’ (Aroma 8:6, 7) Potchula “thupi,” Paulo akusonya kumkhalidwe wathu wofooka monga anthu opanda ungwiro obadwa ndi zikhoterero zauchimo. Kugonjera ku zikhoterero za thupi lofooka kudzawononga mtendere wathu. Ngati Mkristu akuchita chisembwere, akunama, akuba, akumwa mankhwala ogodomalitsa, kapena akuswa lamulo laumulungu mwanjira inayake osalapa, iye amausokoneza mtendere wake ndi Yehova umene anasangalala nawo poyamba. (Miyambo 15:8, 29; 1 Akorinto 6:9, 10; Chibvumbulutso 21:8) Kuwonjezera apa, ngati iye alola chuma chakuthupi kukhala chofunika kwambiri kwa iye kuposa zinthu zauzimu, mtendere wake ndi Mulungu umawopsezedwa kwambiri.—Mateyu 6:24; 1 Yohane 2:15-17.
5. Kodi nchiyani chomwe chimaloŵetsedwa m’kulondola mtendere?
5 Kumbali ina, Paulo anati: ‘Chisamaliro cha mzimu chiri moyo ndi mtendere.’ Mtendere uli mbali ya chipatso cha mzimu, ndipo ngati tiphunzitsa mtima wathu kuyamikira zinthu zauzimu, kupempherera mzimu wa Mulungu kuti utithandize kuchita tero, pamenepo tidzapeŵa ‘chisamaliro cha thupi.’ (Agalatiya 5:22-24) Pa 1 Petro 3:10-12, mtendere wagwirizanitsidwa ndi chilungamo. (Aroma 5:1) Petro akuti kulondola mtendere kumaphatikizapo ‘kupatuka pachoipa ndikuchita chabwino.’ Mzimu wa Mulungu ungatithandize ‘kulondola chilungamo’ ndipo chotero kusungabe mtendere wathu ndi Mulungu.—1 Timoteo 6:11, 12.
6. Kodi ndiliti lomwe liri limodzi la mathayo a akulu ponena za mtendere wa mpingo?
6 Kulondola mtendere kuyenera kukhala nkhaŵa yaikulu kwa akulu mumpingo. Mwachitsanzo, ngati munthu wina ayesera kuyambitsa machitidwe oipitsa, akulu ali ndi thayo la kuchinjiriza mpingo mwa kuyesera kudzudzula wochimwayo. Atavomereza chidzudzulocho, iye adzaupezanso mtendere wake. (Ahebri 12:11) Ngati sitero, iye angafunikire kuchotsedwa kotero kuti unansi wamtendere wa mpingo ndi Yehova ungasungidwe.—1 Akorinto 5:1-5.
Mtendere ndi Abale Athu
7. Kodi nkusonyezedwa kuti kwa ‘chisamaliro cha thupi’ kumene Paulo akuchenjeza Akorinto?
7 ‘Chisamaliro cha thupi’ chingawononge osati mtendere wathu wokha ndi Mulungu komanso unansi wathu wabwino ndi Akristu ena. Paulo analembera Akorinto kuti: ‘Pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndewu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?’ (1 Akorinto 3:3) Nkhwidzi ndi ndewu nzosemphana kwambiri ndi mtendere.
8. (a) Kodi nchiyani chingachitikire munthu amene achititsa nkhwidzi ndi ndewu mumpingo? (b) Kodi mtendere wathu ndi Muungu umadalira pachiyani?
8 Kusokoneza mtendere wampingo mwakuchititsa nkhwidzi ndi ndewu nkoipa kwambiri. Polankhula za mkhalidwe wogwirizana ndi mtendere monga chipatso cha mzimu, mtumwi Yohane anachenjeza kuti: ‘Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.’ (1 Yohane 4:20) Mofananamo, ngati munthu achititsa nkhwidzi kapena ndewu pakati pa abale, kodi iye angakhaledi pamtendere ndi Mulungu? Ayi ndithudi! Tikufulumizidwa kuti: ‘Kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.’ (2 Akorinto 13:11) Inde, ngati ife tipitiriza kukhala mumtendere wina ndi mnzake, pamenepo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nafe.
9. Kodi tikudziŵa bwanji kuti Akristu nthaŵi zina adzasemphana maganizo ndi kusamvana?
9 Ichi sichikutanthauza kuti sipadzakhala kusemphana maganizo pakati pa Akristu. M’milungu yotsatira Pentekoste, munali kusamvana mumpingo waung’ono Wachikristu ponena za kugaŵira zakudya kwatsiku ndi tsiku. (Machitidwe 6:1) M’chochitika china kusamvana kwa pakati pa Paulo ndi Barnaba kunatsogolera ku “kupsetsana mtima.” (Machitidwe 15:39) Paulo anafunikira kulangiza Euodiya ndi Suntuke, omwe mosakaikira anali alongo abwino, achangu, kuti ‘alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.’ (Afilipi 4:2) Nkosadabwitsa kuti Yesu anapereka uphungu watsatanetsatane wonena za mmene kusokoneza mtendere kungathetsedwere pakati pa Akristu ndipo anagogomezera kufunika kwa kuŵasamalira mofulumira mavuto oterowo! (Mateyu 5:23-25; 18:15-17) Iye sakanapereka uphunguwu ngati sanayembekezere kuti padzakhala mavuto pakati pa atsatiri ake.
10. Kodi ndimikhalidwe yotani imene nthaŵi zina imabuka mumpingo, ndipo kodi ndithayo liti limene ichi chimaika pa oloŵetsedwamo onse?
10 Pamenepo, nkothekeradi kuti munthu wina lerolino angakwiyitsidwe ndi mawu omyula mtima kapena kutazindikiridwa kuti Mkristu mnzakeyo akumnyoza. Kakhalidwe ka munthu kokwiyitsa kangapute mkwiyo wamphamvu mwa wina. Maumunthu angawombane. Winawake angatsutse kwamtu wagalu chosankha cha akulu. M’bungwe la akulu lenilenilo, mkulu mmodzi angakhale wodzitukumula kwambiri ndikuyesa kumakakamiza akulu ena kuvomereza zosankha zake. Mosasamala kanthu ndikuti zinthu zoterezi zimachitika, timafunikirabe kufunafuna mtendere ndi kuulondola. Chitokoso chomwe chiripo nchakusamalira mavutowa m’njira Yachikristu kotero kuti tisunge ‘chimangiriro cha mtendere.’—Aefeso 4:3.
11. Kodi ndimakonzedwe otani amene Yehova wapanga kutithandiza kulondola mtendere ndi wina ndi mnzake?
11 Baibulo limati: ‘Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake.’ (Salmo 35:27) Inde, Yehova amafuna kuti tikhale pamtendere. Chotero, watipangira makonzedwe aŵiri apadera otithandiza kusunga mtendere pakati pathu ndi iye. Chimodzi cha awa ndicho mzimu woyera, womwe mtendere nchipatso chake, limodzi ndi mikhalidwe ina yamtendere yogwirizana nawo yonga ngati kuleza mtima, chifundo, chifatso, ndi kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Ena ndi nzeru yaumulungu, yomwe timaŵerenga za iyo kuti: ‘Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino.’—Yakobo 3:17, 18.
12. Kodi tiyenera kuchitanji ngati mtendere wathu ndi abale athu wasokonezedwa?
12 Chotero, pamene mtendere wathu ndi ena wasokonezeka, tiyenera kupempherera nzeru yochokera kumwamba kuti itisonyeze mmene tingachitire, ndipo tiyenera kupempha mzimu woyera kuti utilimbitse kuchita chabwino. (Luka 11:13; Yakobo 1:5; 1 Yohane 3:22) Mogwirizana ndi pemphero lathu, pamenepo tingafufuze m’magwero a nzeru yaumulungu, Baibulo, kaamba ka chitsogozo, limodzinso ndi kusanthula mabuku Abaibulo omwe alipo kaamba ka uphungu wonena za mmene tingagwiritsire ntchito Malemba. (2 Timoteo 3:16) Tingakhumbenso kufuna uphungu kuchokera kwa akulu mumpingo. Sitepe lomalizira likakhala kutsatira chitsogozo cholandiridwacho. Yesaya 54:13 amati: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” Ichi chikutanthauza kuti mtendere wathu umadalira pakugwiritsira ntchito kwathu zinthu zimene Yehova amatiphunzitsa.
“Achimwemwe Ali Ochita Mtendere”
13, 14. (a) Kodi chikutanthauzidwa nchiyani ndi mawu a Yesu akuti “ochita mtendere”? (b) Kodi ndimotani mmene tingakhalire opanga mtendere?
13 Yesu, Muulaliki wake wa pa Phiri anati: “Achimwemwe ali ochita mtendere, popeza kuti adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’” (Mateyu 5:9, NW) Mawu akuti “ochita mtendere” panopa sakusonya kwa munthu wodekha chabe mwachibadwa. Liwu loyambirira Lachigiriki limatanthauza “opanga mtendere.” Wopanga mtendere amakhala waluso pakubwezeretsa mtendere utasokonezedwa. Komabe, chofunika kwenikweni nchakuti wopanga mtendere amakalamira choyamba kupeŵa kusokoneza mtenderewo. ‘Mtendere umachita ufumu mumtima mwake.’ (Akolose 3:15) Ngati atumiki a Mulungu akalamira kukhala opanga mtendere, pamenepo mavuto adzachepetsedwa pakati pawo.
14 Kukhala wopanga mtendere kumaphatikizapo kuzindikira zofooka zathu. Mwachitsanzo, Mkristu angakhale wokwiya msanga kapena kukhala wamtima wapachala ndikukwiyitsidwa msanga. Atatsenderezedwa, kukwiya kwakeko kungampangitse kuiŵala malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo. Ichi chimayembekezeredwa kwa anthu opanda ungwiro. (Aroma 7:21-23) Komabe, udani, ndewu, ndi kupsa mtima zandandalitsidwa kukhala ntchito zathupi. (Agalatiya 5:19-21) Ngati tipeza zikhoterero zoterezi mwa ife—kapena ngati zasonyedwa kwa ife ndi ena—tiyenera kupemphera ndi mtima wonse ndi mosalekeza kaamba ka mzimu wa Yehova kuti ukulitse kudziletsa ndi kufatsa mwa ife. Ndithudi, aliyense ayenera kukalamira kupititsa patsogolo mikhalidwe yoteroyo monga mbali ya umunthu wake watsopano.—Aefeso 4:23, 24; Akolose 3:10, 15.
15. Kodi nzeru yochokera kumwamba imasiyana motani ndi kuwuma mutu kosalingalira?
15 Nthaŵi zina, mpingo kapena bungwe la akulu limasokonezedwa ndi winawake wouma mutu, woumirira nthaŵi zonse kunjira yake. Zowona, ponena za chilamulo chaumulungu, Mkristu ayenera kukhala wolimba, wosasunthikadi. Ndipo ngati tikuganiza kuti tiri ndi lingaliro labwino limene lingapindulitse ena, palibe cholakwika nkulifotokoza poyera, malinga titazilongosola zifukwa zathu. Koma sitikufuna kufanana ndi anthu akudziko “osayanjanitsika.” (2 Timoteo 3:1-4) Nzeru yochokera kumwamba njopanga mtendere, yolingalira. Anthu amene machitidwe awo amapanga chikhoterero chouma mutu chosasunthika ayenera kulabadira uphungu wa Paulo kwa Afilipi wa ‘kusachita kanthu modzitama.’—Afilipi 2:3, NW.
16. Kodi ndimotani mmene uphungu wa Paulo m’bukhu la Afilipi ungatithandizire kulaka kudzitama?
16 M’kalata imodzimodziyo, Paulo akuchonderera kuti ‘ndi kudzichepetsa mtima,’ tiyenera mowona mtima ‘kuyesa ena kukhala otiposa.’ Ichi ndicho chosiyana ndi kudzitama. Mkristu wachikulire choyamba samalingalira za kukakamiza malingaliro ake, kudzipaka ungwiro, kapena kutetezera udindo ndi ukumu wake. Uku kukakhala kosemphana ndi kulangiza kwa Paulo kwa ‘kusapenyerera zake za iye yekha, koma kupenyereranso za mnzake.’—Afilipi 2:4; 1 Petro 5:2, 3, 6.
Mawu Ochita Mtendere
17. Kodi ndikugwiritsira ntchito kolakwika kuti kwa lilime kumene kungasokoneze mtendere wa mpingo?
17 Munthu wolondola mtendere amakhala wosamala mwapadera ponena za kugwiritsira ntchito kwake lilime. Yakobo akuchenjeza kuti: ‘Kotero lilimenso liri chiwalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Tawonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri!’ (Yakobo 3:5) Miseche yoipa, kusuliza ena mseri, mawu oipa ndi onyoza, kung’ung’uza ndi kudandaula, limodzinso ndi kuneneza kosawona mtima ncholinga cha kupeza phindu laumwini—zonsezi ndintchito zathupi zomwe zimasokoneza mtendere wa anthu a Mulungu.—1 Akorinto 10:10; 2 Akorinto 12:20; 1 Timoteo 5:13; Yuda 16.
18. (a) Ponena za kugwiritsira ntchito lilime kolakwika, kodi ndinjira yolonda iti kaamba ka aliyense woloŵetsedwamo? (b) Pamene mkwiyo walankhulitsa munthu mawu opsetsa mtima, kodi Akristu achikulire ama motani chitira?
18 Zowonadi, Yakobo anati: “Lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa.” (Yakobo 3:8) Nthaŵi zina ngakhale Akristu achikulire amanena zinthu zomwe amadzachita nazo chisoni pambuyo pake. Tonsefe timayembekezera kuti ena adzatikhululukira zophophonya zoterozo mongadi mmene timaŵakhululukira. (Mateyu 6:12) Nthaŵi zina kukwiya kwamphamvu kungatulutse mawu opsetsa mtima. Zitatero, wopanga mtendere adzakumbukira kuti ‘mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu owawitsa aputa msunamo.’ (Miyambo 15:1) Kaŵirikaŵiri, munthuyo adzangofunikira kuleza mtima ndi kukana kuyankha mawu aukaliwo mwaukali. Pambuyo pake, mitima itakhala pansi, munthu wa mtima wopanga mtendere amadziŵa kunyalanyaza zinthu zolankhulidwa munthu atakwiya. Ndipo Mkristu wofatsa adzadziŵa mmene angapemphere chikhululukiro ndikuyesa kuchiritsa bala lirilonse limene walipangitsa. Kukhala wokhoza kunena kuti, “Pepani,” nchizindikiro cha kukhala ndi nyonga yolamulira mkhalidwe.
19. Kodi tikuphunziranji kwa Paulo ndi Yesu ponena za mmene tingaperekere uphungu?
19 Lilime lingafunikire kugwiritsiridwa ntchito kulangiza ena. Paulo anamdzudzula poyera Petro pamene anachita molakwika mu Antiokeya. Ndipo Yesu anapereka uphungu wamphamvu m’mauthenga ake onka kumipingo isanu ndi iŵiri. (Agalatiya 2:11-14; Chibvumbulutso, mitu 2, 3) Titasinkhasinkha pazitsanzozi, timaphunzira kuti uphungu suyenera kukhala wofewa kwambiri kwakuti mfundo yake sikuwoneka. Komabe, Yesu ndi Paulo sanali ankhalwe kapena ankhanza. Uphungu wawo sunagwiritsiridwe ntchito kukhala povumbulira kukhumudwitsidwa kwawo. Iwo ankayeseradi kuthandiza abale awo. Ngati munthu wopereka uphungu azindikira kuti sakulilamulira mokwanira lilime lake, angasankhe kupuma pang’ono ndi kukhazika mtima pansi asananene chirichonse. Apo phuluzi, iye angalankhule mawu oipa ndi kupangitsa vuto loipitsitsa kuposa limene akufuna kulisamalira.—Miyambo 12:18.
20. Kodi nchiyani chimene chiyenera kulamulira chirichonse chomwe timanena kwa abale athu ndi alongo kapena zokhudza iwo?
20 Monga momwe zatchulidwira kale, mtendere ndi chikondi nzogwirizana mwathithithi monga zipatso zamzimu. Ngati zomwe timalankhula kwa abale athu—kapena ponena za iwo—nthaŵi zonse zimasonyeza kuwakonda kwathu, pamenepo zidzathandizira mtendere mumpingo. (Yohane 15:12, 13) Mawu athu ayenera kukhala ‘m’chisomo, okoleretsedwa.’ (Akolose 4:6) Ayenera kukhala ozuna, kunena kwake titero, okhumbirika mumtima. Yesu analangiza kuti: ‘Khalani nawo mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.’—Marko 9:50.
‘Chitani Changu’
21. Kodi chimawonedwa nchiyani kwa anthu a Mulungu pamisonkhano yawo ya mlungu ndi mlungu ndi pamisonkhano ndi misonkhano yachigawo?
21 Wamasalmo analemba kuti: “Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!” (Salmo 133:1) Zowonadi, timakondwera kukhala ndi abale athu, makamaka pamisonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu ndi pamisonkhano ndi misonkhano yaikulu. Panthaŵizi mtendere wathu umawonekera ngakhale kwa akunja.
22. (a) Kodi ndi mtendere wonyenga uti umene mitundu posachedwapa idzaganiza kuti ikuwufikira, ukumatsogolera kuchiyani? (b) Kodi ndi mtendere weniweni wotani umene pangano la Mulungu la mtendere lidzatsogolerako?
22 Posachedwapa mitundu idzalingalira kuti ikuwufikira mtendere popanda Yehova. Koma pamene akunena kuti, “Mtendere ndi mosatekeseka” chiwonongeko chamwadzidzidzi chidzagwera onse osakhala pamtendere ndi Mulungu. (1 Atesalonika 5:3) Pambuyo pake, Kalonga wa Mtendere wamkulu adzapitiriza kuchiritsa anthu ku zotulukapo zatsoka za kutaikiridwa koyamba kwa mtendere ndi Mulungu. (Yesaya 9:6, 7; Chibvumbulutso 22:1, 2) Pamenepo, pangano la mtendere la Mulungu lidzatulukapo bata lapadziko lonse. Ngakhale nyama za m’nkhalango zidzapeza mpumulo ku chidani.—Salmo 37:10, 11; 72:3-7; Yesaya 11:1-9; Chibvumbulutso 21:3, 4.
23. Ngati timaliŵerengera lonjeza la dziko latsopano lamtendere, kodi tiyenera kuchitanji tsopano?
23 Idzakhala nthaŵi yaulemerero chotani nanga! Kodi mukuliyembekezera molakalaka? Ngati nditero, “londolani mtendere ndi anthu onse.” Funafunani mtendere tsopano lino ndi abale anu, ndipo makamaka ndi Yehova. Inde, ‘popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chirema.’—Ahebri 12:14; 2 Petro 3:14.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchiyani chimene chingaswe mtendere wathu ndi Yehova?
◻ Kodi ndimtundu uti wa kusemphana maganizo umene ungafunikire kuthetsedwa mumpingo?
◻ Kodi ndimakonzedwe otani amene Yehova wapanga potithandiza kufunafuna mtendere ndi kuulondola?
◻ Kodi ndi mikhalidwe yakuthupi yotani imene ingasokoneze mtendere wampingo, ndipo kodi tingaithetse motani?
[Chithunzi patsamba 22]
Mtendere umachuluka pakati pa awo ophunzitsidwa ndi Yehova
[Chithunzi patsamba 24]
Ngwosangalatsa chotani nanga mtendere wa abale omwe amatumikira mogwirizana!