Musaiwale Yehova
AISIRAELI ena anali atachitapo kale zinthu ngati zimenezi. Koma panthawi ino, ambiri mwa iwo kanali koyamba ndiponso komaliza kuwoloka pamadzi popanda kunyowa. Panthawiyi, Yehova anachititsa madzi a mtsinje wa Yorodano kusiya kuyenda. Ndiyeno Aisiraeli ambirimbiri anayenda mwadongosolo, kuwoloka pa malo ouma n’kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Monga mmene zinalili ndi makolo awo zaka 40 m’mbuyomo pa Nyanja Yofiira, ambiri mwa amene anawoloka mtsinje wa Yorodano n’kutheka anaganiza kuti, ‘Sindidzaiwala zimene Yehova wachitazi.’—Yos. 3:13-17.
Komabe, Yehova anadziwa kuti Aisiraeli ena ‘adzaiwala ntchito zake msanga.’ (Sal. 106:13) Choncho analamula Yoswa, yemwe anali mtsogoleri wa Aisiraeli, kutenga miyala 12 mumtsinje ndi kukaiunjika pamalo amene Aisiraeliwo anakagona atawoloka mtsinjewo. Yoswa anafotokoza kuti: “Miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israyeli.” (Yos. 4:1-8) Mulu wa miyala umenewu unakumbutsa mtunduwu za mphamvu ndi zochita za Yehova, ndiponso chifukwa chake anayenera kutumikira Yehova mokhulupirika nthawi zonse.
Kodi nkhani imeneyi ndi yofunika kwa anthu a Mulungu masiku ano? Inde. Ifenso sitiyenera kuiwala Yehova ndipo tiyenera kupitiriza kumutumikira mokhulupirika. Zinthu zina zimene Aisiraeli anachenjezedwa zingakhudze atumiki a Yehova masiku ano. Taganizirani za mawu a Mose awa: “Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake.” (Deut. 8:11) Mawu amenewa akusonyeza kuti chifukwa cha kuiwala, munthu angasiye kumvera Yehova. Kuchita zimenezi kunali koopsa kwa Aisiraeli, ndipo ngakhalenso kwa ife masiku ano. Polembera Akhristu, mtumwi Paulo anachenjeza za ‘kusamvera konga kumene’ Aisiraeli anasonyeza m’chipululu.—Aheb. 4:8-11.
Tsopano tikambirana zinthu zina zimene zinachitikira Aisiraeli, zimene zikusonyeza bwino mfundo yakuti sitiyenera kuiwala Mulungu. Ndiponso zimene tiphunzire zokhudza Aisiraeli awiri okhulupirika, zitithandiza kukhala opirira komanso oyamikira potumikira Yehova.
Zifukwa Zokumbukirira Yehova
Pazaka zonse zimene Aisiraeli anali ku Iguputo, Yehova sanawaiwale. Iye “anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo.” (Eks. 2:23, 24) Ndipo zimene iye anachita powamasula kuukapolo zinali zosaiwalika.
Yehova anakantha Aiguputo ndi miliri 9 ndipo amatsenga a Farao analephera kuletsa miliri imeneyi. Komabe Farao anapitiriza kuchitira mwano Yehova ndipo anakana kulola Aisiraeli kupita. (Eks. 7:14–10:29) Koma mliri wa 10 unachititsa wolamulira wodzikudzayu kugonjera zimene Mulungu ankafuna. (Eks. 11:1-10; 12:12) Motsogozedwa ndi Mose, mtundu wa Isiraeli ndi khamu la anthu osiyanasiyana, mwina okwana 3,000,000, anachoka ku Iguputo. (Eks. 12:37, 38) Aisiraeli asanayende mtunda wautali, Farao anasintha maganizo. Iye analamula ankhondo ake apakavalo ndi apamagaleta, omwe anali amphamvu kwambiri padziko lonse panthawiyi, kuti akagwirenso akapolo awowa. Nthawi yomweyo Yehova anauza Mose kuti atsogolere Aisiraeli kupita kumalo otchedwa Pihahiroti omwe anali pakati pa Nyanja Yofiira ndiponso mapiri. Malowa anali opanikizika, choncho zinkaoneka ngati Aisiraeli sangapulumuke.—Eks. 14:1-9.
Farao anaganiza kuti Aisiraeli apanikizika moti sangapulumuke, ndipo gulu lake la nkhondo linatsala pang’ono kuwagwira. Koma Yehova anachedwetsa Aiguputo poika mtambo ndi moto pakati pa Aiguputowo ndi Aisiraeli. Kenako Mulungu anagawa Nyanja Yofiira n’kupangitsa kuti pakhale njira, ndipo madzi a mbali zonse anaima makoma aatali mamita 15. Kenako Aisiraeli anayamba kuwoloka panthaka youma. Pasanapite nthawi, Aiguputo anafika panyanjayi ndipo anaona Aisiraeli akuwoloka kupita tsidya lina.—Eks. 13:21; 14:10-22.
Farao akanakhala mtsogoleri wanzeru, akanangobwerera. Koma chifukwa chodzidalira kwambiri, iye analamula ankhondo ake apamagaleta ndi apakavalo kulowa m’nyanjayo. Aiguputo anapitirizabe kutsatira Aisiraeli. Koma iwo asanawapeze, ulendo wawo unatha mwadzidzidzi. Magaleta a Aiguputo sanathenso kuyenda chifukwa Yehova anali atagulula njinga za magaletawo.—Eks. 14:23-25; 15:9.
Pamene Aiguputo amavutika kuyenda ndi magaleta awowa, Aisiraeli onse anafika tsidya lina, kum’mawa kwa nyanjayo. Tsopano Mose anatambasulira dzanja lake ku Nyanja Yofiira. Atachita zimenezi, Yehova anagwetsa makoma awiri a madzi aja. Ndipo madzi ambiri anachititsa Farao ndi ankhondo ake kumira. Palibe mdani ngakhale mmodzi amene anapulumuka. Ndipo Aisiraeli anamasuka.—Eks. 14:26-28; Sal. 136:13-15.
Mbiri ya zimene zinachitikazi inachititsa mantha mitundu yapafupi kwa nthawi yayitali. (Eks. 15:14-16 ) Patatha zaka 40, Rahabi wa ku Yeriko, anauza amuna awiri Achiisiraeli kuti: “Kuopsa kwanu kwatigwera . . . Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m’Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka m’Aigupto.” (Yos. 2:9, 10) Inde, ngakhale anthu osalambira Mulungu woona sanaiwale mmene Yehova anapulumutsira anthu ake. Ndiyetu n’zoonekeratu kuti Aisiraeli anali ndi zifukwa zambiri zokumbukirira Yehova.
‘Anawasunga Ngati Kamwana ka M’diso’
Atawoloka Nyanja Yofiira, Aisiraeli anafika ku chipululu cha Sinai, chomwe chinali “chachikulu ndi choopsa.” Iwo anayenda “mouma mopanda madzi” ndiponso analibe chakudya chokwanira anthu onsewo, koma Yehova sanawasiye. Patapita nthawi, Mose anati: “[Yehova] anam’peza [Isiraeli] m’dziko la mabwinja, ndi m’chipululu cholira chopanda kanthu; anam’zinga, anam’langiza, anam’sunga ngati kamwana ka m’diso.” (Deut. 8:15; 32:10) Kodi Mulungu anawasamalira bwanji?
Yehova anawapatsa mkate wochokera kumwamba, wotchedwa mana, womwe unkagwa mozizwitsa “pankhope pa chipululu.” (Eks. 16:4, 14, 15, 35) Yehova anachititsanso madzi kutuluka “m’thanthwe lansangalabwi.” Komanso, chifukwa chodalitsidwa ndi Mulungu, zovala zawo sizinathe ndipo mapazi awo sanatupe pazaka 40 zimene anakhala m’chipululu. (Deut. 8:4) Ndiyeno kodi Yehova anayembekezera Aisiraeli kumuchitira chiyani? Mose anauza Aisiraeli kuti: “Dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu.” (Deut. 4:9) Ngati Aisiraeli akanakhala kuti akuyamikira ndi kukumbukira zimene Yehova anachita kuti awapulumutse, akanamutumikira nthawi zonse ndipo akanayesetsa kumvera malamulo ake. Kodi Aisiraeli anachita chiyani?
Chifukwa Choiwala Anasiya Kuyamikira
Mose anawauza kuti: “Mwaleka Thanthwe limene linakubalani, mwaiwala Mulungu.” (Deut. 32:18) Aisiraeli ananyalanyaza ndiponso kuiwala zimene Yehova anawachitira pa Nyanja Yofiira, zinthu zimene ankawapatsa m’chipululu ndiponso zina zonse zabwino zimene iye anawachitira. Iwo anapanduka.
Panthawi ina Aisiraeli anamunyoza Mose chifukwa choganiza kuti angafe ndi ludzu. (Num. 20:2-5) Pankhani ya mana yemwe ankadya kuti akhale ndi moyo, iwo anadandaula kuti: “Mtima wathu walema nawo mkate wachabe uwu.” (Num. 21:5) Iwo anaganiza kuti Mulungu sanachite bwino kuwachotsa ku Iguputo ndiponso iwo sanafune kuti Mose apitirize kuwatsogolera. Iwo anati: “Mwenzi tikadafa m’dziko la Aigupto; kapena mwenzi tikadafa m’chipululu muno! . . . Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Aigupto.”—Num. 14:2-4.
Kodi Yehova anamva bwanji chifukwa cha kusamvera kwa Aisiraeli? Pokumbukira zimene zinachitikazo, wamasalmo analemba kuti: “Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako, nam’mvetsa chisoni m’chipululu. Pakuti anabwerera m’mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israyeli. Sanakumbukira dzanja lake, tsikuli anawawombola kwa msautsi. Amene anaika zizindikiro zake m’Aigupto.” (Sal. 78:40-43) Kunena zoona, kuiwala kwa Aisiraeli kunam’pweteketsa mtima Yehova.
Anthu Awiri Amene Sanaiwale
Aisiraeli ena sanaiwale Yehova. Awiri mwa amenewa anali Yoswa ndi Kalebi. Iwo anali m’gulu la anthu 12 amene anatumidwa kuchokera ku Kadesi-Barinea kukazonda Dziko Lolonjezedwa. Atabwerako, anthu 10 ananena mawu osalimbikitsa, koma Yoswa ndi Kalebi anauza anthu kuti: “Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu. Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m’dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Chokhachi musamapikisana naye Yehova.” Anthuwo atamva zimenezi, anauzana kuti aponye miyala Yoswa ndi Kalebi. Koma awiriwa sanachite mantha ndipo anadalira Yehova.—Num. 14:6-10.
Patapita zaka, Kalebi anauza Yoswa kuti: “Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi-Barinea, kukazonda dziko; ndipo ndinam’bwezera mawu, monga momwe anakhala mumtima mwanga. Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinam’tsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.” (Yos. 14:6-8) Chifukwa chokhulupirira Yehova, Kalebi ndi Yoswa anapirira mavuto osiyanasiyana. Iwo sanasiye kukumbukira Yehova masiku onse a moyo wawo.
Kalebi ndi Yoswa anasonyezanso kuti ndi oyamikira mwa kuzindikira kuti Yehova anakwaniritsa lonjezo lopatsa anthu ake dziko labwino. Inde, Aisiraeli akanayenera kuyamikira Yehova chifukwa kuti akhale ndi moyo, zinadalira iyeyo. Yoswa analemba kuti: “Yehova anawapatsa Israyeli dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo awo . . . Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.” (Yos. 21:43, 45) Kodi ifeyo masiku ano tingasonyeze bwanji mtima woyamikira ngati mmene anachitira Kalebi ndi Yoswa?
Khalani Oyamikira
Munthu wina woopa Mulungu anafunsa kuti: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?” (Sal. 116:12) Tili ndi zifukwa zambiri zoyamikirira Mulungu. Mwachitsanzo, iye amatipatsa zinthu zakuthupi, malangizo auzimu ndiponso wakonza njira yotipulumutsira. Ngakhale umuyaya ndi wosakwanira kuti tibwezere zonse zimene Yehova watichitira. Kunena zoona, n’zosatheka. Komabe tonsefe tingathe kumuyamikira.
Kodi malangizo a Yehova akuthandizani kupewa mavuto? Kodi kukhululuka kwa Mulungu kwakuthandizani kukhala ndi chikumbumtima choyera? Zinthu zimenezi timapindula nazo nthawi zonse, choncho tiyeneranso kuyamikira Mulungu nthawi zonse. Mtsikana wina wazaka 14, dzina lake Sandra, ankakumana ndi mavuto aakulu koma Yehova anamuthandiza kuwagonjetsa. Iye anati: “Ndinkapemphera kuti Yehova andithandize, ndipo ndinagoma ndi mmene Yehova amachitira zinthu. Tsopano ndikudziwa chifukwa chimene bambo anga ankakondera kundiuza mawu a pa Miyambo 3:5, 6, akuti: ‘Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.’ Ndikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kundithandiza monga m’mene wakhala akuchitira.”
Sonyezani Kuti Mumakumbukira Yehova mwa Kupirira
Baibulo limafotokoza za khalidwe lina lofunika limene lingatithandize kukumbukira Yehova. Limati: “Mulole chipiriro chimalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kanthu.” (Yak. 1:4) Kodi ‘kukhala okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse’ kumafuna chiyani? Kumafuna kuti tikhale ndi makhalidwe amene angatithandize kuti tikakumana ndi mayesero, tizidalira Yehova ndipo tizifunitsitsa kupirira, osati kugonja. Kupirira kotereku kumatithandiza kuti tikhale osangalala kwambiri mayeserowo akatha. Ndipo amathadi.—1 Akor. 10:13.
Munthu wina amene watumikira Yehova kwanthawi yaitali ndipo wakhala akudwala matenda osiyanasiyana, anafotokoza chimene chimamuthandiza kupirira. Iye anati: “Ndimayesetsa kuganizira za chifuniro cha Yehova, osati changa. Ndimaona kuti kukhulupirika kumatanthauza kuganizira kwambiri zolinga za Mulungu, osati zokhumba zanga. Ndikamakumana ndi mavuto, sindinena kuti, ‘Yehova, n’chifukwa chiyani ndikukumana ndi mavuto oterewa?’ Ndimangopitirizabe kumutumikira ndi kum’mamatira, ngakhale ndikumane ndi mavuto mwadzidzidzi.”
Masiku ano, mpingo wachikhristu umalambira Yehova “ndi mzimu ndi choonadi.” (Yoh. 4:23, 24) Mosiyana ndi Aisiraeli, Akhristu oona, monga gulu, sadzaiwala Mulungu. Koma kukhala mumpingo pakokha, sikutanthauza kuti tingakhalebe okhulupirika. Mofanana ndi Kalebi ndiponso Yoswa, aliyense payekha ayenera kusonyeza kuyamikira ndi kupirira pamene akutumikira Yehova. Tili ndi chifukwa chomveka chochitira zimenezi. Tikutero chifukwa Mulungu akupitirizabe kutitsogolera ndi kutisamalira aliyense payekha m’nthawi yovuta ndi yamapeto ino.
Mofanana ndi miyala ya chikumbutso imene Yoswa anaunjika, nkhani zofotokoza zimene Yehova wachita kuti apulumutse anthu ake, zimatsimikizira kuti iye sadzataya anthu ake. Ndiyetu muyenera kugwirizana ndi wamasalmo amene analemba kuti: “Ndidzakumbukira zimene adazichita Ambuye; inde, ndidzakumbukira zodabwiza zanu zoyambira kale. Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita inu.”—Sal. 77:11, 12.
[Chithunzi patsamba 7]
Mtundu wonse unayenda “mouma mopanda madzi”
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 8]
Aisiraeli atamanga misasa ku Kadesi-Barinea, anatumiza anthu ena kukazonda Dziko Lolonjezedwa
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 9]
Aisiraeli anatha zaka zambiri m’chipululu, choncho anafunika kuyamikira Dziko Lolonjezedwa lomwe linali labwino
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 10]
Kuganizira kwambiri zolinga za Yehova kumatithandiza kupirira mavuto alionse amene tikukumana nawo