Zimene Kugonjera Kwaumulungu Kumafuna kwa Ife
“Potero, gonjerani Mulungu.”—YAKOBO 4:7.
1. Kodi nzotani zimene zinganenedwe ponena za Mulungu amene timlambira?
YEHOVA ndi Mulungu wodabwitsa chotani nanga! Ngwosayerekezereka, ngwosasanthulika, ngwosafanizirika, ngwapadera m’njira zochuluka kwambiri! Iye Ngwam’mwambamwamba, Mfumu Yachilengedwechonse amene ulamuliro wonse woyenera uli m’manja mwake. Iye alibe chiyambi ndiponso alibe mapeto, ndipo ngwaulemerero kwambiri kwakuti palibe munthu amene angathe kumuwona nakhalabe ndi moyo. (Eksodo 33:20; Aroma 16:26) Ali wamphamvuzonse ndi wanzeruzonse, wangwiro kotheratu m’chiweruzo cholungama, ndipo ndiye chitsanzo changwiro cha chikondi. Ndiye Mlengi wathu, Woweruza wathu, Wopereka Malamulo wathu, ndi Mfumu yathu. Mpatso yabwino iriyonse ndi chininkho changwiro chirichonse zifumira kwa iye.—Salmo 100:3; Yesaya 33:22; Yakobo 1:17.
2. Kodi kugonjera kwaumulungu kumaloŵetsamo zinthu zotani?
2 Polingalira mfundo zonsezi, sipangakhale chikaikiro chirichonse ponena za thayo lathu lakukhala wogonjera kwa iye. Koma kodi zimenezi zimafunanji kwa ife? Zinthu zingapo. Popeza kuti sitikhoza kuwona Yehova Mulungu, kumgonjera kumaloŵetsamo kulabadira liwu la chikumbumtima chathu chophunzitsidwa, kugwirizana ndi gulu la Mulungu la padziko lapansi, kumvera maulamuliro akudziko, ndi kulemekeza lamulo laumutu m’banja.
Kukhala ndi Chikumbumtima Chabwino
3. Kuti tisunge chikumbumtima chabwino, kodi tiyenera kumvera ziletso zotani?
3 Kuti tisunge chikumbumtima chabwino, tiyenera kumvera malamulo osatheka kusungitsidwa ndi wina—ndiko kuti, malamulo kapena malamulo achikhalidwe chabwino amene sangasungitsidwe ndi anthu. Mwachitsanzo, lamulo lakhumi la Malamulo Khumi, limene linaletsa kusirira, linali losakhoza kusungitsidwa ndi olamulira aumunthu. Kutereku, izi zikuchitira umboni kuti Malamulo Khumiwo anachokera kwa Mulungu, popeza kuti palibe bungwe lopanga malamulo la anthu limene likanapanga lamulo losakhoza kusungitsidwa mwa zilango ngati munthu aswa lamulolo. Mwa lamuloli, Yehova Mulungu anapatsa Mwisrayeli aliyense thayo lakukhala mlonda wa iye mwini—ngati anafuna kukhala ndi chikumbumtima chabwino. (Eksodo 20:17) Mofananamo, pakati pa ntchito za thupi zimene zikaletsa munthu kuloŵa Ufumu wa Mulungu pali “kaduka” ndi “njiru”—mikhalidwe imene ziletso zake sizikhoza kusungitsidwa ndi oweruza aumunthu. (Agalatiya 5:19-21) Koma kuti tikhale ndi chikumbumtima chabwino, tiyenera kupeŵa zimenezi.
4. Kuti tisunge chikumbumtima chabwino, kodi ndimalamulo achikhalidwe chabwino a Baibulo otani amene tiyenera kumvera?
4 Inde, tiyenera kumvera malamulo achikhalidwe chabwino a Baibulo. Malamulo achikhalidwe chabwino amenewo angaikidwe m’malamulo aŵiri okha amene Yesu Kristu anapereka poyankha funso lakuti ndiliti limene linali lamulo lalikulu la Chilamulo cha Mose. ‘Udzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. . . . Udzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.’ (Mateyu 22:36-40) Mawu a Yesu olembedwa pa Mateyu 7:12 amasonyeza zimene zikuloŵetsedwamo m’lachiŵiri la malamulo ameneŵa: ‘Chifukwa chake zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho Chilamulo ndi Aneneri.’
5. Kodi tingasunge motani unansi wabwino ndi Yehova Mulungu?
5 Tiyenera kuchita chimene tikudziŵa kuti nchoyenera ndi kusachita chimene tikudziŵa kuti nchosayenera, kaya ena achizindikira kapena ayi. Tiyenera kuchita motero ngakhale ngati tingakhale okhoza kupambana mwakusachita chimene tiyenera kuchita kapena mwakuchita chimene sitiyenera kuchita. Kumatanthauza kusunga unansi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba, tikukumbukira chenjezo limene mtumwi Paulo akupereka pa Ahebri 4:13: ‘Palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa iye amene tichita naye.’ Kupitiriza kuchita choyenera kudzatithandiza kulimbana ndi misampha ya Mdyerekezi, kukaniza zitsenderezo zadziko, ndi kulimbana ndi chikhoterero chachibadwa cha dyera.—Yerekezerani ndi Aefeso 6:11.
Kugonjera ku Gulu la Mulungu
6. Kodi ndinjira zolankhulira zotani zimene Yehova anagwiritsira ntchito m’nthaŵi zakale Chikristu chisanakhale?
6 Yehova Mulungu sanaike zonse m’manja mwathu kuti aliyense adzisankhire mmene adzagwiritsirira ntchito malamulo achikhalidwe chabwino m’miyoyo yathu. Kuyambira pachiyambi cha mbiri ya anthu, Mulungu wagwiritsira ntchito anthu monga njira zolankhuliramo. Chotero, Adamu anali wolankhulira wa Mulungu kwa Hava. Lamulo lonena za chipatso choletsedwa linapatsidwa kwa Adamu, Hava asanalengedwe, motero Adamu ayenera kukhala atauza Hava za chifuniro cha Mulungu ponena za iye. (Genesis 2:16-23) Nowa anali mneneri wa Mulungu kwa banja lake ndi kwa dziko lokhalapo chigumula chisanachitike. (Genesis 6:13; 2 Petro 2:5) Abrahamu anali wolankhulira wa Mulungu kwa banja lake. (Genesis 18:19) Mneneri wa Mulungu amene analinso njira yolankhulira kwa mtundu wa Israyeli anali Mose. (Eksodo 3:15, 16; 19:3, 7) Pambuyo pa iye, mpaka kudzafika kwa Yohane Mbatizi, aneneri ambiri, ansembe, ndi mafumu anagwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu kulankhulira mwa iwo chifuniro chake kwa anthu ake.
7, 8. (a) Pamene Mesiya anafika, kodi ndani amene agwiritsiridwa ntchito monga olankhulira a Mulungu? (b) Kodi kugonjera kwaumulungu kumafunanji kwa Mboni za Yehova lerolino?
7 Pamene anafika Mesiya, Yesu Kristu, Mulungu anamgwiritsira ntchito limodzi ndi atumwi ndi ophunzira ake kutumikira monga olankhulira Ake. Pambuyo pake, otsatira odzozedwa okhulupirika a Yesu Kristu anali kudzatumikira monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” m’kulankhula kwa anthu a Yehova mmene angagwiritsirire ntchito malamulo achikhalidwe chabwino a Baibulo m’miyoyo yawo. Kugonjera kwaumulungu kunathanthauza kuzindikira gulu limene Yehova anali kuligwiritsira ntchito.—Mateyu 24:45-47; Aefeso 4:11-14.
8 Maumboni amasonyeza kuti lerolino “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ali wogwirizanitsidwa ndi Mboni za Yehova ndipo akuimiridwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni zimenezi. Ndiponso, bungwelo limaika oyang’anira m’maudindo osiyanasiyana—monga akulu ndi oimira oyendayenda—kutsogoza ntchito m’malo akwawoko. Kugonjera kwaumulungu kumafunikiritsa kuti Mboni yodzipereka iriyonse ikhale yogonjera kwa oyang’anira ameneŵa mogwirizana ndi Ahebri 13:17: ‘Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni; pakuti ichi sichikupindulitsani inu.’
Kulandira Uphungu
9. Kodi kugonjera kwaumulungu kaŵirikaŵiri kumaloŵetsamo chiyani?
9 Kugonjera kwaumulungu kaŵirikaŵiri kumaloŵetsamo kulandira uphungu wa otumikira monga oyang’anira. Ngati nthaŵi zonse sitidzilanga ife eni moyenerera, tingafunikire kupatsidwa uphungu ndi kulangidwa ndi awo okhala ndi chidziŵitso ndi ulamuliro wakutero, monga ngati akulu ampingo wathu. Kulandira uphungu woterowo ndiko njira yanzeru.—Miyambo 12:15; 19:20.
10. Kodi awo amene amapereka chilango ali ndi thayo lotani?
10 Mwachiwonekere, akulu opereka chilangowo ayenera iwo eni kukhala zitsanzo zabwino za kugonjera kwaumulungu. Motani? Malinga nkunena kwa Agalatiya 6:1, iwo sayenera kungokhala ndi njira yabwino yoperekera uphungu koma ayeneranso kukhala opereka chitsanzo: ‘Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakutikwakuti, inu auzimu, mubweze woteroyo mu mzimu wachifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.’ M’kunena kwina, uphungu wa mkulu uyenera kugwirizana ndi chitsanzo chake. Kuteroko kumagwirizana ndi uphungu woperekedwa pa 2 Timoteo 2:24, 25 ndi pa Tito 1:9. Inde, awo opereka chidzudzulo kapena kuwongolera ayenera kukhala osamala kwambiri kusayesa konse kuchita mwaukali. Nthaŵi zonse ayenera kukhala odekha, okoma mtima, komabe olimba pakuchirikiza miyezo ya Mawu a Mulungu. Ayenera kukhala omvetsera opanda tsankho, otsitsimula kwa olema ndi othodwa.—Yerekezerani ndi Mateyu 11:28-30.
Kugonjera Maulamuliro Aakulu
11. Kodi Akristu afunikiranji m’maunansi awo ndi olamulira akudziko?
11 Kugonjera kwaumulungu kumafunanso kuti timvere olamulira akudziko. Tikupatsidwa uphungu pa Aroma 13:1 wakuti: ‘Anthu onse amvere maulamuliro aakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.’ Mawuwa amafuna kuti, pakati pa zinthu zina, timvere malamulo apamsewu ndi kukhala osamala ponena zakupereka misonkho ndi thangata, monga momwe mtumwi Paulo akunenera pa Aroma 13:7.
12. Kodi kugonjera kwathu kwa Kaisara kuli ndi polekezera m’lingaliro lotani?
12 Komabe mwachiwonekere, kugonjera Kaisara konseko kuyenera kukhala ndi polekezera. Chimene tiyenera kukumbukira nthaŵi zonse ndicho lamulo lachikhalidwe chabwino limene Yesu Kristu ananena lolembedwa pa Mateyu 22:21: ‘Patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.’ Mawu amtsinde a Aroma 13:1 mu Oxford NIV [New International Version] Scofield Study Bible amati: “Izi sizimatanthauza kuti ayenera kumvera malamulo osayenera kapena otsutsana ndi Chikristu. M’zochitika zoterozo liri thayo lake kumvera Mulungu koposa anthu. (Machitidwe 5:29; cp. Dan. 3:16-18; 6:10ff).”
Kugonjera Kwaumulungu Mkati mwa Banja
13. Kodi kugonjera kwaumulungu mkati mwa banja kumafunanji kwa ziŵalo zake?
13 Mkati mwa banja, mwamuna ndi atate amakhala mutu. Izi zimafuna kuti akazi alabadire uphungu woperekedwa pa Aefeso 5:22, 23 wakuti: ‘Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa mpingo.’a Ponena za ana, iwo samadzipangira malamulo koma amafunikira kusonyeza kumvera kwaumulungu kwa makolo awo onse aŵiri, monga momwe Paulo akufotokozera pa Aefeso 6:1-3 kuti: ‘Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndikuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko lapansi.’
14. Kodi kugonjera kwaumulungu kumafunanji kwa mitu ya banja?
14 Ndithudi, kumakuchititsa kukhala kosavuta kwa akazi ndi ana kusonyeza kugonjera kwaumulungu koteroko pamene amuna ndi atate iwo eniwo asonyeza kugonjera kwaumulungu. Amachita zimenezi mwakuchita umutu mogwirizana ndi malamulo achikhalidwe chabwino a m’Baibulo, monga aja opezeka pa Aefeso 5:28, 29 ndi 6:4: ‘Koteronso amuna adzikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu [mpingo, NW].’ ‘Atate inu, musakwiitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].’
Zotithandiza Kusonyeza Kugonjera Kwaumulungu
15. Kodi nchipatso chotani cha mzimu chimene chidzatithandiza kuwonetsa kugonjera kwaumulungu?
15 Kodi nchiyani chidzatithandiza kusonyeza kugonjera kwamulungu m’mbali zimenezi? Choyamba, pali chikondi chopanda chinyengo—chikondi pa Yehova Mulungu ndi awo amene wawaika kutiyang’anira. Tikuuzidwa pa 1 Yohane 5:3 kuti: ‘Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.’ Yesu anatchula mfundo yofananayo pa Yohane 14:15 pamene anati: ‘Ngati mukonda ine, sungani malamulo anga.’ Kunena zowona, chikondi—chipatso choyambirira ndi chofunika koposa cha mzimu—chidzatithandiza kuyamikira zonse zimene Yehova watichitira ndiponso chidzatithandiza kusonyeza kugonjera kwaumulungu.—Agalatiya 5:22.
16. Kodi mantha aumulungu amathandiza motani m’kusonyeza kugonjera kwaumulungu?
16 Chachiŵiri, pali mantha aumulungu. Kuwopa kusakondweretsa Yehova kudzatithandiza chifukwa chakuti “ndiko kuda zoipa.” (Miyambo 8:13) Mosakaikira, kuwopa kusakondweretsa Yehova kudzatithandiza kusalolera pa zolakwa kaamba ka kuwopa munthu. Kudzatithandizanso kumvera malangizo a Mulungu mosasamala kanthu za mavuto amene tidzafunikira kuwagonjetsa. Ndiponso, kudzatiletsa kugonja kuziyeso kapena zikhoterero zakuchita choipa. Malemba amasonyeza kuti kunali kuwopa Yehova kumene kunakhozetsa Abrahamu kufuna kupereka nsembe mwana wake Isake, ndipo kunali kuwopa kusakondweretsa Yehova kumene kunakhozetsa Yosefe kutsutsa mwachipambano machitidwe achisembwere a mkazi wa Potifara.—Genesis 22:12; 39:9.
17. Kodi ndimbali yanji imene chikhulupiriro chimachita m’kusonyeza kwathu kugonjera kwaumulungu?
17 Chithandizo chachitatu ndicho chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu. Chikhulupiriro chidzatikhozetsa kulabadira uphungu woperekedwa pa Miyambo 3:5, 6 wakuti: ‘Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika paluntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendwe ako.’ Chikhulupiriro chidzatithandiza makamaka pamene tikuwonekera kukhala tikuvutika ndi chisalungamo kapena kulingalira kuti tikuchitiridwa tsankho chifukwa cha fuko lathu kapena mtundu kapena chifukwa cha kusemphana kwa maumunthu. Ena angalingalirenso kuti analumphidwa molakwika pamene sanavomerezedwe kutumikira monga mkulu kapena mtumiki wotumikira. Ngati tiri ndi chikhulupiriro, tidzadikira Yehova kuwongolera zinthu panthaŵi yake. Pakali pano tingafunikire kukulitsa chipiriro choleza mtima.—Maliro 3:26.
18. Kodi nchiyani chimene chiri chithandizo chachinayi m’kusonyeza kugonjera kwaumulungu?
18 Chithandizo chachinayi ndicho kudzichepetsa. Sikumakhala kovuta kwa munthu wodzichepetsa kusonyeza kugonjera kwaumulungu chifukwa chakuti ‘mwakudzichepetsa m’maganizo, amalingalira ena kukhala omposa.’ Munthu wodzichepetsa amakhala wofunitsitsa kuchita monga “wamng’onong’ono.” (Afilipi 2:2-4; Luka 9:48) Koma munthu wonyada samafuna kukhala wogonjera ndipo amanyansidwa nako. Kwanenedwa kuti munthu woteroyo angakonde ngakhale kufuna chithandizo chakuti apeŵe kusulizidwa chifukwa kumampweteka mtima.
19. Kodi nchitsanzo chabwino chotani chakudzichepetsa chimene pulezidenti wakale wa Watch Tower Society anapereka?
19 Chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa ndi kugonjera kwaumulungu chinaperekedwa ndi Joseph Rutherford, pulezidenti wachiŵiri wa Watch Tower Bible and Tract Society. Pamene Hitler analetsa ntchito ya Mboni za Yehova m’Jeremani, abale kumeneko anamlembera kalata kufunsa zimene anayenera kuchita powona kuti chiletso chinaikidwa pamisonkhano yawo ndi ntchito yakulalikira. Iye anatchulira zimenezi banja la Beteli ndipo anavomereza mosabisa kuti sanadziŵe chimene anayenera kuuza abale a ku Jeremani, makamaka polingalira za zilango zowopsa zimene zinaloŵetsedwamo. Iye anati ngati aliyense anadziŵa choyenera kuwauza abalewo, anakondwa kuchimva. Unali mzimu wodzichepetsa chotani nanga!b
Mapindu Ochokera m’Kuwonetsa Kugonjera Kwaumulungu
20. Kodi ndimadalitso otani amene amadza mwakuwonetsa kugonjera kwaumulungu?
20 Wina angafunse, Kodi mapindu akuwonetsa kugonjera kwaumulungu ngotani? Alipo ochulukadi. Timapeŵa nkhaŵa ndi zogwiritsa mwala zimene zimakhala ndi amene amachita zinthu modziimira paokha. Timasangalala ndi unansi wabwino ndi Yehova Mulungu. Tiri ndi mayanjano abwino kopambana ndi abale anthu Achikristu. Ndiponso, mwakudzisungira momvera malamulo, timapeŵa kuloŵa m’mavuto osafunikira kwa olamulira akudziko. Timasangalalanso ndi moyo wabanja wachimwemwe monga amuna ndi akazi, monga makolo ndi ana. Ndiponso, mwakusunga kugonjera kwaumulungu, timachita mogwirizana ndi uphungu woperekedwa pa Miyambo 27:11: ‘Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; Kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.’
[Mawu a M’munsi]
a Minisitala wina mpainiya anatamanda ulemu ndi kuchirikiza kwachikondi kwa mkazi wake kwa mpainiya wosakwatira. Mpainiya mbetayo anaganiza kuti mnzakeyo anafunikira kunenanso kanthu kena ponena za maluso ena a mkazi wake. Koma pambuyo pa zaka zingapo, pamene mpainiya mbetayo anakwatira, anazindikira mmene kuchirikiza kwachikondi mkazi kuliri kofunika ku mtendere waukwati.
b Pambuyo pa mapemphero ochuluka ndi kuphunzira Mawu a Mulungu, Joseph Rutherford anazindikira bwino lomwe yankho limene anayenera kuwapatsa abalewo ku Jeremani. Sikunali kwa iye kuwauza chimene anayenera kuchita kapena kusachita. Iwo anali ndi Mawu a Mulungu amene anawauza momveka bwino chimene anayenera kuchita ponena za kusokhana pamodzi ndi kuchitira umboni. Chotero abale aku Jeremani anayamba kuchita zinthu mwakabisira koma anapitiriza kumvera malamulo a Yehova a kusonkhana pamodzi ndi kuchitira umboni ponena za dzina lake ndi Ufumu.
Mafunso Openda
◻ Kodi ndianthu ati amene Mulungu wagwiritsira ntchito monga njira zolankhulira, ndipo kodi atumiki ake anafunikira kuchitanji kwa iwo?
◻ Kodi kugonjera kwaumulungu kumagwira ntchito m’maunansi osiyanasiyana otani?
◻ Kodi ndimikhalidwe yotani imene idzatithandiza kusonyeza kugonjera kwaumulungu?
◻ Kodi kugonjera kwaumulungu kumadzetsa madalitso otani?
[Chithunzi patsamba 16]
Mulungu anagwiritsira ntchito makonzedwe a pakachisi wa m’Yerusalemu kulankhula kwa anthu ake za chifuniro chake
[Zithunzi patsamba 18]
Mbali m’zimene tingawonetse kugonjera kwaumulungu