NKHANI YOPHUNZIRA 35
Pitirizani Kukhala Oleza Mtima
“Valani . . . kuleza mtima.”—AKOL. 3:12.
NYIMBO NA. 114 “Khalani Oleza Mtima”
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. N’chifukwa chiyani mumasangalala ndi anthu omwe ndi oleza mtima?
TONSEFE timasangalala ndi anthu omwe ndi oleza mtima. N’chifukwa chiyani? Chifukwa timalemekeza anthu amene amayembekezera kapena kudikirira chinachake popanda kukhumudwa. Timayamikira anthu ena akatilezera mtima pamene talakwitsa zinazake. Timayamikiranso kuti amene ankatiphunzitsa Baibulo ankaleza nafe mtima pamene tinkavutika kuphunzira, kuvomereza kapenanso kugwiritsa ntchito mfundo inayake ya m’Baibulo. Koposa zonse, timathokoza kwambiri kuti Yehova Mulungu amatilezera mtima.—Aroma 2:4.
2. Kodi nthawi zina tingalephere kukhala oleza mtima pa zinthu ziti?
2 Ngakhale kuti timasangalala ena akamaleza mtima, si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kuti ifeyo tisonyeze khalidweli. Mwachitsanzo, tingalephere kukhala oleza mtima ngati mumsewu muli magalimoto ambiri, makamaka pamene tachedwa. Nthawi zina tingalephere kuugwira mtima ena akatikhumudwitsa. Ndipo nthawi zinanso tingamavutike kuyembekezera dziko latsopano limene Yehova anatilonjeza. Kodi inuyo mukufuna kuti muzileza mtima kwambiri? Munkhaniyi tikambirana zimene kuleza mtima kumatanthauza komanso chifukwa chake khalidweli lili lofunika. Tikambirananso zimene tingachite kuti tizikhala oleza mtima kwambiri.
KODI MUNTHU WOLEZA MTIMA AMATANI?
3. Kodi munthu woleza mtima amatani ena akamukhumudwitsa?
3 Taganizirani njira 4 zomwe tingasonyezere kuleza mtima. Choyamba, munthu woleza mtima sakwiya msanga. Iye amayesetsa kukhala wodekha akakhala ndi nkhawa kapenanso ena akamukhumudwitsa. Mawu akuti “wosakwiya msanga” amapezeka koyamba m’Baibulo pamene Yehova amafotokozedwa kuti ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.”—Eks. 34:6.
4. Kodi munthu woleza mtima amatani ngati akufunika kudikira?
4 Chachiwiri, munthu woleza mtima amadikira modekha. Ngati zinazake zikuchedwa kuposa mmene amayembekezerera, munthu wotereyu amapewa kukwiya. (Mat. 18:26, 27) Pali zochitika zambiri pamene timafunika kudikira moleza mtima. Mwachitsanzo, timafunika kumvetsera moleza mtima wina akamalankhula kuti tisamudule mawu. (Yobu 36:2) Timafunikanso kuleza mtima tikamathandiza munthu amene tikuphunzira naye Baibulo kumvetsa mfundo inayake ya m’Malemba kapenanso kuti asiye khalidwe linalake loipa.
5. Kodi tingasonyeze kuleza mtima m’njira inanso iti?
5 Chachitatu, munthu woleza mtima sachita zinthu mwaphuma. N’zoona kuti pa zinthu zina timafunika kuchita zinthu mofulumira. Komabe munthu woleza mtima akamafuna kuchita zinazake zofunika, samangofulumira kuzichita kapenanso kumazichita mothamanga. M’malomwake amakhala ndi nthawi yokwanira yokonzekera zimene akufuna kuchitazo, kenako amachita zinthuzo mogwirizana ndi kuchuluka kwa nthawi yomwe zikufunika kuti zichitike.
6. Kodi munthu woleza mtima amatani akamakumana ndi mavuto kapena mayesero?
6 Cha 4, munthu woleza mtima amapirira mayesero popanda kudandaula. Pamenepa tingati kuleza mtima n’kogwirizana kwambiri ndi kupirira. N’zoona kuti sikulakwa kumufotokozera mnzathu momasuka mmene tikumvera pa nkhani ya mayesero ena ake amene tikukumana nawo. Komabe munthu wopirira amachita zonse zomwe angathe kuti apitirizebe kupirira n’kumaona zabwino zimene zikuchitika. (Akol. 1:11) Choncho monga Akhristu, tiyenera kukhala oleza mtima m’mbali zonsezi za moyo wathu. Chifukwa chiyani? Tiyeni tione zifukwa zingapo.
CHIFUKWA CHAKE KULEZA MTIMA NDI KHALIDWE LOFUNIKA KWAMBIRI
7. Mogwirizana ndi Yakobo 5:7, 8, n’chifukwa chiyani kuleza mtima n’kofunika? (Onaninso chithunzi.)
7 Kuleza mtima ndi kofunika kuti tidzapulumuke. Mofanana ndi atumiki okhulupirika akale, timafunika kuyembekezera moleza mtima kuti Mulungu akwaniritse malonjezo ake. (Aheb. 6:11, 12) Baibulo limatiyerekezera ndi mlimi. (Werengani Yakobo 5:7, 8.) Mlimi amachita khama kudzala mbewu komanso kuthirira koma sadziwa kuti zikula liti. Komabe mlimiyo amayembekezera moleza mtima n’kumakhulupirira kuti adzakolola. Mofanana ndi zimenezi, timatanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira, ngakhale kuti ‘sitidziwa tsiku limene Ambuye wathu adzabwere.’ (Mat. 24:42) Timayembekezera moleza mtima n’kumakhulupirira kuti pa nthawi yake Yehova adzakwaniritsa zonse zimene analonjeza. Koma ngati sitingakhale oleza mtima, tikhoza kutopa n’kuyamba kusiya pang’onopang’ono choonadi. Tingayambenso kufunafuna zinthu zimene tikuona kuti zingatibweretsere chimwemwe panopa. Koma tikakhala oleza mtima, tingathe kupirira mpaka pamapeto komanso kudzapulumuka.—Mika 7:7; Mat. 24:13.
8. Kodi kuleza mtima kumatithandiza bwanji tikamachita zinthu ndi ena? (Akolose 3:12, 13)
8 Kuleza mtima kumatithandiza tikamachita zinthu ndi ena. Timatha kumvetsera mwatcheru ena akamalankhula. (Yak. 1:19) Kuleza mtima kumalimbikitsanso mtendere. Pamene takhumudwa, kuleza mtima kumatiteteza kuti tisachite zinthu mofulumira kwambiri kapena kulankhula zinthu zimene zingakhumudwitse ena. Ndipo ngati ndife oleza mtima, sitikwiya msanga munthu wina akatikhumudwitsa. M’malo mobwezera, timapitiriza “kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.”—Werengani Akolose 3:12, 13.
9. Kodi kuleza mtima kumatithandiza bwanji tikamafuna kusankha zochita? (Miyambo 21:5)
9 Kuleza mtima kungatithandizenso kuti tizisankha zochita mwanzeru. M’malo mochita zinthu mwaphuma kapena mosaganiza bwino, tidzafufuza komanso kuganizira zimene tikufuna kusankhazo kenako n’kusankha zimene zili zabwino kwambiri. (Werengani Miyambo 21:5.) Mwachitsanzo, ngati tikufunafuna ntchito, tikhoza kutengeka kuti tivomere ntchito imene yapezeka mwamsanga, ngakhale kuti ingamatisokoneze pa nkhani yolambira Yehova. Komabe ngati tili oleza mtima, tidzaganizira zinthu zina monga kumene tizikagwirira ntchitoyo, kuchuluka kwa nthawi yomwe izifunika komanso mmene ingakhudzire banja lathu ndiponso ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuleza mtima kumatithandiza kuti tisasankhe zinthu molakwika.
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIKHALA OLEZA MTIMA KWAMBIRI
10. Kodi Mkhristu angatani kuti akhale woleza mtima komanso kuti nthawi zonse azisonyeza khalidweli?
10 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala oleza mtima kwambiri. Kuleza mtima ndi limodzi mwa makhalidwe omwe mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Choncho tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake kuti tikhale ndi makhalidwe omwe umatulutsa. Ngati tikuyesedwa pa nkhani yokhala oleza mtima, tiyenera ‘kupitiriza kupempha’ mzimu woyera kuti utithandize kukhala oleza mtima. (Luka 11:9, 13) Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kuti tiziona zinthu mmene iyeyo amazionera. Kenako pambuyo popemphera, tizichita zomwe tingathe kuti tizikhala oleza mtima tsiku lililonse. Tikamapemphera kwambiri kuti tikhale oleza mtima n’kumayesetsa kusonyeza khalidweli, m’pamenenso limakhazikika kwambiri mumtima ndipo limangokhala ngati mbali ya moyo wathu.
11-12. Kodi Yehova wakhala akusonyeza bwanji kuti ndi woleza mtima?
11 Muziganizira mozama za anthu otchulidwa m’Baibulo. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. Tikhoza kuphunzira mmene tingasonyezere kuleza mtima poganizira mozama zitsanzozi. Tisanakambirane zitsanzozi, tiyeni tikambirane za Yehova yemwe ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kuleza mtima.
12 M’munda wa Edeni, Satana ananyoza dzina la Yehova ndiponso ananena kuti Mulungu si Wolamulira wachikondi komanso wachilungamo. M’malo mowononga Mdyerekezi nthawi yomweyo, Yehova analeza mtima komanso anadziletsa podziwa kuti pangafunike nthawi yaitali kuti zidziwike kuti ulamuliro wake ndi wabwino kwambiri. Poyembekezera zimenezi, Yehova wakhala akupirira nthawi yonse imene dzinali lakhala likunyozedwa. Kuwonjezera pamenepo, wakhalanso akuyembekezera moleza mtima n’cholinga choti anthu ambiri akhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. (2 Pet. 3:9, 15) Zimenezi zachititsa kuti anthu mamiliyoni amudziwe. Tikamaganizira madalitso obwera chifukwa cha kuleza mtima kwa Yehova, zingakhale zosavuta kuti tiziyembekezera nthawi yomwe adzawononge dziko loipali.
13. Kodi Yesu wakhala akusonyeza bwanji kuti amatsanzira Atate wake pa nkhani ya kuleza mtima? (Onaninso chithunzi.)
13 Yesu amatsanzira ndendende Atate wake pa nkhani ya kuleza mtima ndipo anasonyeza khalidweli ali padziko lapansi. N’kutheka kuti si nthawi zonse pamene zinali zophweka kuti azisonyeza khalidweli makamaka kwa alembi ndi Afarisi, omwe anali achinyengo. (Yoh. 8:25-27) Komabe mofanana ndi Atate wake, Yesu sankakwiya msanga. Sankabwezera ena akamamunyoza kapena kumukhumudwitsa. (1 Pet. 2:23) Yesu ankapirira moleza mtima mayesero omwe ankakumana nawo ndipo sankadandaula. Ndipotu mpake kuti Baibulo limatiuza kuti ‘tiziganizira mozama za munthu amene anapirira malankhulidwe onyoza ngati amenewo a anthu ochimwa.” (Aheb. 12:2, 3) Mothandizidwa ndi Yehova, ifenso tingathe kumapirira moleza mtima mayesero alionse omwe tingakumane nawo.
14. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Abulahamu pa nkhani yoleza mtima? (Aheberi 6:15) (Onaninso chithunzi.)
14 Bwanji ngati zimene takhala tikuyembekezera pa nkhani yamapeto sizinachitikebe? N’kutheka kuti tinkayembekezera kuti mapeto afika pa nthawi inayake zaka zambiri m’mbuyomu. Mwinanso tingamade nkhawa kuti sitidzakhala ndi moyo pa nthawi imene mapeto azidzafika. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipitirize kuyembekezera moleza mtima? Taganizirani chitsanzo cha Abulahamu. Pa nthawi yomwe anali ndi zaka 75, ndipo analibe mwana, Yehova anamulonjeza kuti: “Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe.” (Gen. 12:1-4) Kodi Abulahamu anaona zinthu zonse zokhudza lonjezoli zikukwaniritsidwa? Ayi. N’zoona kuti atawoloka mtsinje wa Firate n’kuyembekezera kwa zaka 25, Abulahamu anaona mwana wake Isaki atabadwa m’njira yodabwitsa. Ndipo pambuyo pa zaka zina 60, anaonanso zidzukulu zake, Esau ndi Yakobo zitabadwa. (Werengani Aheberi 6:15.) Koma Abulahamu sanaone mbadwa zake zikukhala mtundu waukulu komanso kulandira Dziko Lolonjezedwa. Ngakhale zinali choncho, mwamuna wokhulupirikayu anali pa ubwenzi wolimba ndi Mlengi wake. (Yak. 2:23) Ndipo akadzaukitsidwa, adzasangalala kudziwa kuti mitundu yonse ya anthu inadalitsidwa chifukwa cha chikhulupiriro komanso kuleza mtima kwake. (Gen. 22:18) Kodi tikuphunzirapo chiyani? N’kutheka kuti ifenso sitingaone panopa zimene Yehova analonjeza zikukwaniritsidwa. Komabe ngati tili oleza mtima ngati Abulahamu, tingakhale otsimikiza kuti Yehova atidalitsa panopa komanso adzatidalitsa kwambiri m’dziko latsopano lomwe walonjeza.—Maliko 10:29, 30.
15. Kodi tikhoza kufufuza chiyani tikamaphunzira Baibulo patokha?
15 M’Baibulo muli zitsanzo zinanso zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. (Yak. 5:10) Bwanji osakonza zoti mufufuze zitsanzozi pamene mukuphunzira Baibulo panokha?b Mwachitsanzo, ngakhale kuti Davide anadzozedwa ali mwana kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli, anafunika kudikira kwa zaka zambiri asanapatsidwe ufumuwo. Simiyoni ndi Anna ankatumikira Yehova mokhulupirika pamene ankayembekezera kubwera kwa Mesiya. (Luka 2:25, 36-38) Mukamaphunzira nkhanizi muzifufuza mayankho a mafunso awa: Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinathandiza munthuyu kuti akhale woleza mtima? Kodi kukhala woleza mtima kunamuthandiza bwanji? Kodi ndingamutsanzire bwanji? Mungapindulenso ngati mutaphunzira za anthu omwe sanasonyeze kuleza mtima. (1 Sam. 13:8-14) Mungadzifunse kuti: ‘Kodi mwina n’chiyani chinachititsa kuti asakhale woleza mtima? Nanga zotsatirapo zake zinali zotani?’
16. Kodi kukhala oleza mtima kumatithandiza m’njira zina ziti?
16 Muziganizira ubwino wokhala woleza mtima. Tikakhala oleza mtima timakhala osangalala komanso odekha. Ndipotu kukhala ndi khalidweli kungatithandize kuti tiziganiza bwino komanso tikhale ndi thanzi labwino. Tikamachita zinthu moleza mtima ndi ena, timakhala nawo pa ubwenzi wabwino. Timakhalanso ogwirizana kwambiri mumpingo. Ngati wina watikhumudwitsa sitimakwiya msanga, zomwe zimachititsa kuti zinthu zisaipe kwambiri. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koposa zonse, timakhala tikutsanzira Atate wathu wakumwamba ndipo timakhala naye pa ubwenzi wabwino kwambiri.
17. Kodi tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuchita chiyani?
17 Kunena zoona, kuleza mtima ndi khalidwe losangalatsa komanso lothandiza kwambiri. N’zoona kuti si nthawi zonse pamene kuleza mtima kungakhale kophweka. Koma mothandizidwa ndi Yehova, tikhoza kupitiriza kukhala ndi khalidweli. Pamene tikuyembekezera moleza mtima dziko latsopano, tisamakayikire kuti “diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa, amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha.” (Sal. 33:18) Tiyeni tonse tikhale otsimikiza mtima kuti tipitirizabe kukhala oleza mtima.
NYIMBO NA. 41 Mulungu Imvani Pemphero Langa
a M’dziko lolamuliridwa ndi Satanali, anthu ambiri si oleza mtima. Komabe, Baibulo limatiuza kuti tikhale oleza mtima. Nkhaniyi ifotokoza chifukwa chake khalidweli lili lofunika komanso zimene tingachite kuti tizikhala oleza mtima kwambiri.
b Kuti mupeze nkhani za m’Baibulo za anthu amene anasonyeza kuleza mtima, mungapite pa mutu wakuti “Patience” mu Watch Tower Publications Index.