‘Achimwemwe Ali Awo Amene Apirira’
1. Chiyambire 1914, kodi ndi mkhalidwe wotani padziko lapansi umene wakwaniritsa Mateyu 24:3-8, ndipo kodi ndi zonena zotani za Chigwirizano Chamitundu ndi Mitundu Yogwirizana zomwe zalephera?
MU BUKHU lake lakuti The Present Age, Robert Nisbet akunena za “Nkhondo ya Zaka Makumi Asanu ndi Aŵiri Mphambu Zisanu yomwe yakhala ikuchitika, yodukizidwa mocheperacheperadi, chiyambire 1914.” Inde, “nkhondo ndi mbiri zankhondo,” kuphatikizapo nkhondo zadziko—chimenecho nchimenedi Yesu Kristu ananeneratu kaamba ka nthaŵi ino yamapeto. (Mateyu 24:3-8) Chigwirizano Chamitundu chinapangidwa mu 1920 “kuchinjiriza nkhondo kosatha.” Ndimomvetsa chisoni chotani nanga mmene icho chinalepherera! Mitundu Yogwirizana inalinganizidwa mu 1945 “kupulumutsa mibadwo yotsatira ku chipiyoyo chankhondo.” Koma bukhu la Max Harrelson lakuti Fires All Around the Horizon likusimba kuti: “Sipanakhalepo tsiku nlimodzi lomwe chiyambire mapeto a Nkhondo Yadziko ya II pamene sikunakhalepo kumenyana kwinakwake.”
2. Kodi nchiyani chimene anthu ena amafunsa ponena za mikhalidwe yadziko, koma kodi ndi mafunso otani amene tiyenera kuwafunsa?
2 Uchigawenga ndi chiwawa, chinyengo ndi umphaŵi, mankhwala ogodomalitsa ndi miliri—zonsezi zimawonjezera ku chithunzi chomvetsa chisonicho. Anthu ena angafunse kuti: ‘Kodi ndimotani mmene anthu angapitirizire kupilira mikhalidwe yosokoneza choteroyo?’ Ngakhale kuli tero, chofunika koposa ife tiyenera kufunsa kuti: ‘Kodi ndimotani mmene Mulungu akupilirira ndi kuwonongedwa kwa zolengedwa zake za dziko lapansi? Kodi ndi kwautali wotani umene iye adzalola anthu oipa kuwononga dziko lapansi ndi kuwunjika chitonzo pa dzina lake lamtengolo?’
3. (a) Kodi ndi funso lotani limene mneneri Yesaya anafunsa, ndipo kodi nchifukwa ninji? (b) Kodi ndi yankho lotani limene Yehova anapereka, ndipo kodi chimenechi chimasonyezanji kaamba ka tsiku lathu?
3 Mneneri Yesaya anadzutsa funso lofananalo. Iye anagaŵiridwa kulengeza kwa anthu am’dziko lakwawo uthenga wochokera kwa Yehova. Koma anachenjezedweratu kuti iwo sakalabadira kaya iye kapena Mulungu yemwe anamutuma. Chotero Yesaya anafunsa kuti: “Mpaka liti, [Yehova, NW]?” Inde, kodi ndikwautali wotani umene Yesaya akafunikira kulalikira kwa anthu ake ouma mutu, ndipo kodi nkwautali wotani umene Yehova akafunikira kupirira ndi kukana kwawo konyoza kulabadira uthenga wake? Yehova anayankha kuti: “Mpaka midzi ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu.” (Yesaya 6:8-11) Mofananamo lerolino, Mulungu akupirira ndi mitonzo yoteroyo kufikira nthaŵi yake yoikika ya kupereka chiweruzo padziko limene wolakwa wamkulu wakhala Dziko Lachikristu losakhulupirika.
4. Kodi nchiyani chimene chinali choturukapo cha chipiriro cha Yobu, ndipo kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene ichi chimatipatsa lerolino?
4 Yehova wapirira kwanthaŵi yaitali kutonza kwa Satana. Zaka 3,600 zapitazo, Yobu wokhulupirika nayenso anapirira, akumatsutsa chitokoso cha Satana chakuti sakakhoza kusunga umphumphu pansi pa chiyeso. Ichi chinapangitsa mtima wa Yehova kusangalala chotani nanga! (Yobu 2:6-10; 27:5; Miyambo 27:11) Monga mmene Yakobo mbale wopeza wa Yesu ananenera pambuyo pake kuti: “Tawonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwawona chitsiriziro cha [Yehova, NW], kuti [Yehova, NW] ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” Mofananamo, awo amene amapirira ndi Yehova lerolino akutsimikiziridwa zoturukapo zachimwemwe.—Yakobo 5:11.
5. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti chipiriro chikafunikira kwa anthu a Mulungu lerolino, ndipo kodi ndi pochita ntchito iti pamene iwo akafunikira kupirira?
5 Yesu anasonyeza mowonekera bwino kuti chipiriro chikafunikira kwa anthu a Mulungu mtsiku lathu. Poneneratu za chizindikiro cha “mapeto a ndongosolo iri lazinthu,” iye ananena kuti: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimariziro, yemweyo adzapulumuka.” Kupirira pamene akuchita chiyani? Mawu otsatira a Yesu enieniwo akuyankha kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse.” (Mateyu 24:3, 13, 14, NW) Kokha pamenepo ‘ndi pamene mapeto adzafika.’—Onaninso Marko 13:10, 13; Luka 21:17-19.
Chifukwa Chimene Yehova Amapirira
6. Kodi nchifukwa ninji Yehova ali chitsanzo chapadera cha chipiriro, ndipo kodi ndi chiti chimene chiri chifukwa chimodzi chimene iye wapirira?
6 Mtumwi Paulo analongosola kuti “Mulungu, ngakhale kuti anali ndi chifuno cha kusonyeza mkwiyo wake ndi kudziŵitsa mphamvu zake, analekerera ndi kuleza mtima kokulira zotengera za mkwiyo zoyenerera chiwonongeko.” (Aroma 9:22, NW) Kodi nchifukwa ninji Yehova wapirira kukhalapo kopitirizabe kwa kuipa, zotengera za mkwiyozi? Chifukwa chimodzi ndi ichi: kuti asonyeze kuti kulamulira kwa anthu, kodziimira pawokha kuchoka kwa Mlengi, kwalephereratu. (Yeremiya 10:23) Mwamsanga, ulamuliro wa Mulungu udzayeretsedwa pamene atsimikizira kuti iye yekha ndi amene angabweretse mtendere, chigwirizano, ndi chimwemwe ku banja la munthu, kupyolera m’kulamulira kwa Ufumu wa Yesu.—Salmo 37:9-11; 45:1, 6, 7.
7. Kodi Yehova wapiriranso kaamba ka chifukwa china chiti, ndipo kodi ndi madalitso otani amene ichi chabweretsa kwa mamiliyoni chiyambire ma 1930?
7 Kuwonjezerapo, Yehova wapirira “ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukuru pa zotengera zachifundo.” (Aroma 9:23) Zotengera zimenezi zachifundo ndizo odzozedwa osunga umphumphu omwe “agulidwa kuchokera pakati pa mtundu wa anthu” kukalamulira ndi Kristu Yesu mu Ufumu wake wakumwamba. Kusindikiza chizindikiro kwa a 144,000 kwapitirizabe kuchokera m’nthaŵi za atumwi. Iko tsopano kukuyandikira mapeto. (Chibvumbulutso 7:3; 14:1, 4) Ndipo tawonani! Chiyambire ma 1930 chipiriro chopitirizabe cha Yehova chalola kusonkhanitsidwa kwa mamiliyoni ena, “khamu lalikulu . . . lochokera m’mitundu yonse,” omwe akusangalala m’chiyembekezo cha kupulumuka chisautso chomalizira kuti aloŵe m’moyo wosatha wa paradaiso ya dziko lapansi. (Chibvumbulutso 7:4, 9, 10, 13-17) Kodi ndinu mmodzi wa khamu lalikulu limenelo? Ngati ndi tero, kodi sindinu wosangalala kuti Yehova wapirira kukhalapo kwa zotengera zamkwiyo kufikira tsopano? Komabe, muyenera kupitirizabe kupirira, monga mmene Yehova wapiririra.
Chipiriro Chifupidwa
8. Kodi nchifukwa ninji tonsefe timafunikira chipiriro, ndipo kodi ndi chitsanzo chiti cha chipiriro chimene tiyenera kulingalira mosamalitsa?
8 Tonsefe timafunikira kupirira ngati titi tilandire malonjezano. Pambuyo ponena chowonadi chachikulu chimenechi pa Ahebri 10:36, mtumwi Paulo akulongosola mwatsatanetsatane chikhulupiriro chowala ndi chipiriro cha “mtambo waukulu wa mboni” za nthaŵi zakale. Kenaka akutichonderera kuti “tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womarizira wa chikhulupiro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake,” Yesu anapirira mu utumiki wa mtima wonse, osaphonya konse mphotoyo. Chitsanzo chake chimatilimbitsanso ife kupirira chotani nanga!—Ahebri 12:1, 2.
9. Kodi nchiyani chimene chaturukapo kuchokera m’zitsanzo zamakono za chipiriro?
9 Zitsanzo zamakono za chipiriro ziri zochurukanso. Inu mungadziŵe, kapena mwadziŵa abale ndi alongo omwe akhala owonekera m’chipiriro chawo. Chikhulupiriro chawo chatifulumiza chotani nanga! Ndipo chaka chirichonse, pamene Mboni za Yehova zichitira ripoti ntchito yawo yadziko lonse ku Watch Tower Society, nkhani zina zosangalatsa za chipiriro ndi kusunga umphumphu zimalandiridwa. Tchati pa masamba anayi omwe akutsatira chikuwunikira ntchito yokulira yokwaniritsidwa mkati mwa 1989 pamene Mboni zimenezi ‘zawonjezera chipiriro ku chikhulupiriro chawo.’—2 Petro 1:5, 6.
Chaka Chathu Chachikulu Koposa
10. (a) Kodi ndi maiko angati ndi unyinji wa zisumbu amene anagawanamo m’kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu mu 1989, ndipo kodi ndi angati amene anakhalamo ndi phande mu ntchito imeneyi? (b) Kodi ndi apainiya angati amene anachitira ripoti mwezi wokhala ndi chiŵerengero chapamwamba, ndipo kodi chiwonkhetso cha maola otheredwa mu utumiki wakumunda chinali chotani?
10 Monga momwe tchati chapitacho chikusonyezera, maiko 212 ndi unyinji wa zisumbu anagawanamo m’kulalikira Ufumu ukudzawo wa Yehova. Muŵerengi wa Nsanja ya Olonda wokondedwawe, kodi unali ndi mwaŵi wa kukhala mmodzi wa 3,787,188 omwe anagawanamo m’nchito yaikulu imeneyi? Kodi unali mmodzi wa 808,184 omwe anachitira ripoti monga apainiya m’mwezi wokhala ndi chiŵerengero chapamwamba kaamba ka utumiki umenewo? Chirichonse chimene munathandizira ku chiwonkhetso cha dziko lonse cha 1989 cha maola 835,426,538 otheredwa mu utumiki wakumunda, inu muli ndi chifukwa chosangalalira.—Salmo 104:33, 34; Afilipi 4:4.
11. (a) Kodi ndi chiŵerengero chiti cha opezekapo pa Chikumbutso March 22 yapita chimene chiri chodzetsa chisangalalo, ndipo kodi nchifukwa ninji? (b) Kodi ndi angati amene anabatizidwa, ndipo kodi ndi maiko ati pa tchaticho omwe anali owonekera m’nkhaniyi?
11 Sangalalaninso, ndi chiwonkhetso chija chabwino koposa cha opezekapo 9,479,064, March 22 yapita, pa phwando la dziko lonse la Chikumbutso cha imfa ya Yesu! Ichi chimasonyeza kuthekera komwe kulipo kwa alengezi Aufumu owonjezereka 5,691,876, ngati kokha onga nkhosa okondwerera amenewa angawetedwe mwachikondi m’khola lankhosa, ndi kugawanamo mokhazikika m’kutumikira Yehova. Kodi tingawathandize iwo m’zimenezi? (Yohane 10:16; Chibvumbulutso 7:9, 15) Ambiri akuyankha kale, monga momwe chasonyezedwera ndi chiwonkhetso chonse cha Mboni zatsopano 263,855 zobatizidwa mkati mwa chaka chautumiki cha 1989.
12. Kodi ndi mbali zina ziti zimene tchaticho sichikuvumbula (a) ponena za mafakitale a Watch Tower Society? (b) ponena za kugawiridwa kwa magazine ndi kulembetsa?
12 Pali mbali zina zimene tchaticho sichikuvumbula. Ludzu la zofalitsidwa—Mabaibulo, mabuku, mabroshuwa, magazine—anali olakalakidwa. Monga choturukapo, mafakitale a Watchtower mu New York anagwiritsira ntchito matani 25,999 a mapepala kusindikiza Mabaibulo, mabuku, ndi mabroshuwa 35,811,000, kuwonjezeka kwa 101 peresenti kuposa 1988. Mafakitale ena aakulu a Watch Tower Society, makamaka mu Germany, Italy, ndi Japan, anagwira ntchito mosinthanasinthana, kuchilikiza “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” m’kupereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45) Mkati mwa April ndi May, kugawira magazine kwapadera ndi kulembetsa kunachitiridwa ripoti mmaiko angapo, okhala ndi chigogomezero chapadera pa kugaŵiridwa kwa makope a Nsanja ya Olonda onena za “Babulo Wamkulu.” (Chibvumbulutso 17:5) Mosakaikira, April yomwe ikudzayo, apainiya othandiza ndi Mboni zina adzakuta munda wa dziko m’chimene chiyenera kutsimikiziranso kukhala ndawala yathu ya kuchitira umboni kwabwino koposa m’chaka chautumiki cha 1990.—Yerekezani ndi Yesaya 40:31; Aroma 12:11, 12.
13. Kodi ndi maiko ati omwe andandalitsidwa m’tchati amene sanandandalitsidwe chaka chatha? Longosolani.
13 Yang’ananinso pa tchati. Kodi mukuwawona maiko ena amene sanandandalitsidwe motchulidwa maina chaka chatha? Nkulekeranji, inde! Hungary ndi Poland, kumene ntchito yathu yakhalitsidwa yalumulo. Tiri achiyamikiro kwa aulamuliro m’maiko amenewa kuti iwo tsopano akusonyeza kulingalira koteroko kaamba ka Mboni za Yehova. M’nkhaniyi, mapemphero a ubale wadziko lonse ayankhidwa, “kuti m’moyo mwathu tikakhale odekha mtima ndi achete [odzala ndi kudzipereka kwaumulungu, NW] ndi mkulemekeza monse.”—1 Timoteo 2:1, 2.
14. Tchulani kupambana kwa Misonkhano Yachigawo ya “Kudzipereka Kwaumulungu” mu Poland.
14 “Kudzipereka kwaumulungu”! Nkulekeranji, popeza kuti Misonkhano Yachigawo ya “Kudzipereka Kwaumulungu” inakhozadi kuchitidwa mu Poland, m’madera atatu, m’kati mwa August! Ndi ochereza alendo abwino koposa chotani nanga mmene abale athu a ku Poland 91,024 anatsimikizira kukhala! (Ahebri 13:1, 2, 16) Monga chozizwitsa, makumi a zikwi za abale—a ku Czechoslovakia, Germany, Russia, ndi ena—anapeza ziphaso zoyendera ndi basi, sitima, ndipo ngakhale ndi miyendo. Zikwizikwi ena anabwera ndi ndege kuchokera ku maiko a ku Amerika, Western Europe, ndi dera lakutali longa zisumbu za Pacific ndi Japan. Mabwalo amaseŵera aakulu, oyeretsedwa mwaudongo ndi abale athu, anali aakulu mokwanira kusonkhanitsa 65,710 pa Chorzów 40,442 pa Poznan, ndi 60,366 pa Warsaw—chiwonkhetso chachikulu cha opezekapo 166,518! Pamalo aliwonse, openyerera ubatizo anadumpha ndi malingaliro achisangalalo. Pa Poznan wa zaka 9 zakubadwa ndi a zaka 90 zakubadwa anamizidwa, ndipo chiwonkhetso cha 6,093 omizidwa pa misonkhano itatu anaphatikizapo a zaka za pakati pa 13 ndi 19 ambiri, ochurukira a amenewa anachokera ku maiko amene zinanenedwa kuti chipembedzo chikatha ndi kutha kwa okalamba. Siziri tero ndi chipembedzo chowona chozikidwa pa Mawu a Mulungu! (Yerekezani ndi Salmo 148:12, 13; Machitidwe 2:41; 4:4.) Ndi modabwitsa chotani nanga mmene chipiriro cha abale athu mu Eastern Europe chafupidwira!
Chikhulupiriro Chopitirizabe Pansi pa Chiyeso
15. Kodi ndimotani mmene Mboni mu Lebanon zasonyezera chipiriro ndi kusagwedezeka, ndipo ndi zoturukapo zotani?
15 Mofanana ndi mtumwi Paulo, Mboni za Yehova zimaitanidwa kusonyeza chipiriro pansi pa mikhalidwe yambiri ndi yosiyanasiyana. (2 Akorinto 11:24-27) Mu Lebanon nkhondo ya chiweniweni idakamenyedwabe. Kodi abale athu akuchita motani? Mosagwedezeka ndi mogamulapo. Chaka cha 1989 chidawona kusakaza ndi kuphulitsa mabomba kokulira, koma ngakhale kumene izi zidali zokakala, abale adali ogamulapo kusafooka. Mpingo wa mu Beirut ukusimba kuti: “Magulu okhazikika kaamba ka utumiki wa kumunda anakonzekeretsedwa mmadzulo monse mwa mlungu. Mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta ya chisungiko, abale sanabwevutsidwe. Tinakuta magawo ochurukira kuposa ndi kale lonse. Mu April tinali ndi chiŵerengero chapamwamba cha apainiya. Maphunziro atsopano a Baibulo anayambidwa, ndipo magazine ndi mabuku owonjezereka anagawiridwa.”
16. Kodi ndimotani mmene abale athu mu Colombia asonyezera chipiriro mwa kupereka mbiri yabwino ku matauni kumene kunalibe Mboni?
16 Colombia yakhala yotchuka chifukwa cha kupitsa mankhwala ogodomalitsa ndi chiwawa. Koma chipiriro chokhulupirika cha Akristu kumeneko chimapanganso kutchuka. Posachedwapa, apainiya apadera apakanthaŵi anatumizidwa ku matauni 31 a nzika zikwi khumi kapena kuposapo kumene kunalibe Mboni. M’tauni imodzi, pamene anthu okondwerera chatsopano anapeza kuti apainiyawo akakhala kumeneko kwa milungu yowerengeka yokha, iwo anachonderera kuti apainiyawo akhalebe. Mu ina, anthu okondwerera 18 anasaina kalata ya chiyamikiro kaamba ka thandizo lauzimu limene linaperekedwa mkati mwa kukhalako kwa miyezi itatu kwa apainiya ndipo anapempha thandizo lowonjezereka. “Iyi ndi ntchito yofunikadi,” iwo anatero. Mosapita m’mbali, m’zochitika zonsezo makonzedwe anapangidwa kupitirizabe kulimirira chikondwererocho. Kukulitsa gawo lakutali loterolo kumafunikira chipiriro, koma ntchito yolimba ya apainiya omwe amatero imadalitsidwa molemera.
17, 18. (a) Kodi ndi pansi pa mikhalidwe yotani imene Mboni za Yehova zapirira mu Italy? (b) Kodi ndimotani mmene Mboni zakhalira mosasamala kanthu za kufalitsa bodza yonena za iwo?
17 Mu Italy, Mboni za Yehova zimayang’anizana ndi chitsutso champhamvu cha atsogoleri a chipembedzo, koma mwa mphamvu ya Yehova iwo apirira. M’magawo osiyanasiyana, atsogoleri achipembedzo anagawira mapepala odzamamatizidwa pa zitseko za anthu a m’magawo awo kuwuza Mboni za Yehova kuti zisalize belu ya pachitseko. Ansembe ambiri analoŵetsa ntchito anyamata aang’ono kukamamatiza mapepala amenewa pa zitseko zonse m’madera achindunji—ngakhale m’nyumba za mabanja a Mboni! Komabe, Mbonizo sizimalowereredwa mopepuka, ndipo kaŵirikaŵiri zimagwiritsira ntchito mapepalawo kuyambitsa kukambitsirana. Kuwonjezerapo, owurutsa nkhani ndi wailesi ya kanema yadziko anafalitsa nkhaniyo mwakuya, akumatsutsa kupanda chipiriro kwa chipembedzo kosonyezedwako ndi kundandalitsa kuti machenjera onga amenewa alidi chizindikiro cha kufooka kumbali ya tchalitchi. Profesa mmodzi wa pa yunivesiti anakhumudwitsidwa kwenikweni ndi mkangano wa mapepala oletsa Mboni kotero kuti analembetsa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
18 Tchalitchi cha Katolika mu Italy chimagwiritsiranso ntchito ampatuko kufalitsa bodza ponena za anthu a Yehova, koma izi sizimagwira ntchito mpang’ono pomwe chifukwa chakuti ofalitsa 172,382 ndiodziŵika bwino lomwe ndipo amalemekezedwa. Mwamuna wina anauza Mboni zochezera kuti anali adaŵerengapo zinthu zoipa ponena za ife m’mabuku olembedwa ndi yemwe kale anali Mboni. Chotero, iye anali wotsutsa kwenikweni pamene mbale wake anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Ngakhale ndi tero, patapita kanthawi kochepa, iye anawona chiyambukiro chabwino chimene kusintha kwa chipembedzo kochitidwa ndi mbale wake kunadzetsa pa iye. Iye anadabwa kuti: ‘Kodi chingatheke motani kwa chinachake choipa kuturutsa zoturukapo zabwino chotero?’ Ndiponso, iye anapempha phunziro la Baibulo kwa Mboni yochezerayo.—Yerekezani ndi Akolose 3:8-10.
Kuchita ndi Chitsutso
19, 20. (a) Kodi ndi m’khalidwe wotani womwe wafunikira chipiriro kumbali ya Mboni mu Finland, ndipo kodi nchiyani chimene chiri chapadera kwenikweni ponena za kupenda kwa tchalitchi? (b) Kodi ndi chokumana nacho chotani chimene chimasonyeza kufunika kwa chipiriro m’kulalikira mbiri yabwino?
19 M’maiko amene Mboni zimafikira mobwerezabwereza, kaŵirikaŵiri pamakhala chitsutso chofalikira ku mbiri yabwino. Izi ziridi tero mu Finland. Tchalitchi m’dziko limenelo chinapenda ndipo chinapeza kuti 70 peresenti ya chiŵerengero chadziko samakonda Mboni kuchezera manyumba awo. Komabe, 30 peresenti samatsutsa mwampmhamvu, ndipo pakati pa amenewa, 4 peresenti ananenadi kuti amakonda Mboni za Yehova. Ichi chiri chiŵerengero chapadera. Maperesenti anayi a chiŵerengero cha anthu a ku Finland amatanthauza anthu 200,000. Yerekezerani chimenecho ndi chiŵerengero cha ofalitsa cha pakali pano cha 17,303!
20 Wofalitsa wina yemwe adali kunja mu utumiki anakokedwera chisamaliro chake ku kupendaku ndipo anafunsidwa kuti: “Kodi simudziŵa kuti 70 peresenti ya ife timalingalira anthu inu kukhala osafunika? Kodi nchifukwa ninji mumapitirizabe kubwera ku makomo athu?” Wofalitsayo anayankha kuti: “Inde, koma kufufuza komwe kuja kunasonyeza kuti maperesenti 4 a inu mumatikonda. Tikuyesera kufunafuna anthu amenewa. Ngakhale ngati iwo anali kokha 1 peresenti, tikanapitabe kunyumba ndi nyumba kuyesera kuwapeza iwo.” Mwini nyumbayo analingalira kwakamphindi ndipo ananena kuti: “Kodi uthenga wanu ulidi wofunika kwa iwo?” Wofalitsayo anayankha mwa kufunsa kuti: “Kodi mungakonde kuwumva?” Mwamsanga mwininymba ameneyu anasonyeza chikondwerero mu mbiri yabwino.
Chimene Chiri Mtsogolo
21. (a) Kodi ndi mtundu wotani wa nkhondo imene tiyenera kupirira nayo m’dongosolo lino, ndipo kodi nchifukwa ninji? (b) Kodi nchiyani chimene tiyenera kupirira nacho, ndipo kodi ulosi wa Habukuku umatitsimikizira chiyani?
21 Bwanji ponena za tonsefe lerolino? Kodi ndife ogamulapo kupirira ndi Yehova ndi Kristu Yesu mpaka kumapeto? Iwo sangakhale kutali, koma tiyenera kupirira! M’dongosolo la Satana, tiyenera kulimbana nayo nkhondo ya chikhulupiriro, pamene chisembwere, chinyengo, ndi udani wadziko ukutizinga m’mbali zonse. (Yuda 3, 20, 21) Tingafunikire kupirira chizunzo cha mtundu uwu ndi wina. Ngakhale tsopano, zikwizikwi za abale athu akuvutika m’ndende, ndipo ena akumenyedwa mwankhalwe. Awa amayamikira mapemphero athu. (2 Atesalonika 3:1, 2) Mwamsanga, dongosolo liripoli silidzakhalapo! Monga mmene Habakuku akunenera kuti: “Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.”—Habakuku 2:3.
22. Kodi ndi choturukapo chotani chimene tingayembekezere mwachidaliro ngati tikhala ndi kuleza mtima kwa aneneri ndi chipiriro cha Yobu?
22 Mtumwi Yakobo mwachikondi akutiwuza kuti: “Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la [Yehova, NW].” Ife lerolino amene tikulankhula m’dzina la Yehova tingakhale osunga umphumphu mkati mwa ziyeso zokakala, monga mmene analiri Yesaya, Yeremiya, Danieli, ndi ena. Mofanana ndi Yobu, ife tingapirire. Ndi modabwitsa chotani nanga mmene iye anafupidwira kaamba ka chipiriro chake! Chifundo cha Yehova ndi chikondi chokoma mtima chidzatibweretsera ife mphoto zofananazo—titapirira mpaka kumapeto. Ndipo lolani kuti mawu a Yakobo akwaniritsidwe mwa aliyense wa ife akuti: ‘Tawonani tiwayesera achimwemwe awo amene apirira.’—Yakobo 5:10, 11; Yobu 42:10-13.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi ndi chifuno chotani cha chipiriro chimene Yesu anagogomezera?
◻ Kodi Yehova wapirira kaamba ka chifukwa chotani?
◻ Kodi ndi kuwonekera kwina kuti kwa ntchito yaikulu yokwaniritsidwa mkati mwa 1989?
◻ Kodi ndimotani mmene chipiriro cha abale athu mu Poland chafupidwira?
◻ Kodi ndimotani mmene Mboni mu Lebanon, Colombia, ndi Italy zasonyezera chikhulupiriro pansi pa chiyeso?
[Tchati pamasamba 20-23]
LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1989 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)