‘Itanani Akulu’
“Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a mpingo.” —YAKOBO 5:14.
1, 2. (a) Kodi ndimumkhalidwe wochititsa mantha wotani umene atumiki a Yehova alimo tsopano lino, ndipo kodi iwo angalingalire motani? (b) Kodi ndimafunso otani tsopano amene akufuna mayankho?
“NTHAŴI zoŵaŵitsa” zafika. Anthu akuchita modzikonda, mokondetsa zinthu zakuthupi, modzitamandira, kaŵirikaŵiri akumachititsa chisokonezo ‘m’masiku ano otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1-5) Monga Akristu okhala m’dongosolo loipa lilipoli la zinthu, timaukiridwa ndi zinthu zitatu zazikulu zowopsa: Satana Mdyerekezi, dziko la anthu osapembedza Mulungu, ndi choloŵa chathu cha zikhoterero zauchimo.—Aroma 5:12; 1 Petro 5:8; 1 Yohane 5:19.
2 Poopsezedwa ndi maupandu ameneŵa, nthaŵi zina tingakhale othedwa nzeru. Nangano, kodi nkuti kumene tingapeze chichilikizo chotithandiza kupirira mokhulupirika? Kodi tingatembenukire kwa yani kaamba ka chitsogozo titayang’anizana ndi zosankha ponena za ntchito Zachikristu ndi kulambira kwathu?
Chithandizo Chomwe Chilipo
3. Kodi nkwayani kumene tingapeze chilimbikitso chotonthoza, ndipo motani?
3 Kudziŵa kuti Yehova ndiye Magwero a nyonga yathu kumatipatsa chilimbikitso chotonthoza. (2 Akorinto 1:3, 4; Afilipi 4:13) Wamasalmo Davide, amene anawona chithandizo cha Mulungu, analengeza kuti: “Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso iye, adzachichita.” “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 37:5; 55:22) Tili oyamikira chotani nanga chifukwa cha chichilikizo chotero!
4. Kodi ndimotani mmene Petro ndi Paulo yemwe amaperekera chitonthozo?
4 Tingathenso kupeza chitonthozo mwa kudziŵa kuti sitili tokha pokumana ndi mayeso ndi maupandu. Mtumwi Petro anafulumiza Akristu anzake kuti: “Ameneyo [Satana Mdyerekezi] mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilinkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.” (1 Petro 5:9) Ndithudi, Akristu onse amakhumba kuima nji m’chikhulupiriro. Zowonadi, kaŵirikaŵiri tingadzimve kukhala mumkhalidwe ‘wosautsika monsemo,’ monga momwe mtumwi Paulo anachitira. Komabe, iye sanali ‘wopsinjika.’ Mofanana naye, tingavutike maganizo “koma osakhala kakasi.” Ngakhale ngati tizunzidwa, sitili ‘otayika.’ Ngati ‘tigwetsedwa,’ ‘sitionongeka.’ Chifukwa chake, “sitifooka.” Timayesayesa ‘kupenyerera osati pazinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka.’ (2 Akorinto 4:8, 9, 16, 18) Kodi tingachite motani zimenezi?
5. Kodi ndichithandizo cha mbali zitatu chotani chimene Yehova amapereka?
5 Yehova, “Wakumva pemphero,” amapereka chithandizo cha mbali zitatu. (Salmo 65:2; 1 Yohane 5:14) Yoyamba, iye amapereka malangizo kupyolera m’Mawu ake ouziridwa, Baibulo. (Salmo 119:105; 2 Timoteo 3:16) Yachiŵiri, mzimu wake woyera umatipatsa mphamvu ya kuchita chifuniro chake. (Yerekezerani ndi Machitidwe 4:29-31.) Ndipo yachitatu, gulu la Yehova la padziko lapansi lili lokonzekera kutithandiza. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tilandire chithandizo?
“Mphatso mwa Amuna”
6. Kodi ndichithandizo chotani chimene Yehova anapereka pa Tabera, ndipo motani?
6 Chochitika china m’tsiku la mneneri Mose chimatithandiza kuzindikira chisamaliro chachikondi cha Yehova m’kupereka chithandizo kwa atumiki Ake. Chinachitika pa Tabera, kutanthauza “kuyaka; kunyeketsa; kulilima.” Pamalo ameneŵa a chipululu cha Sinai, Mulungu anachititsa moto kulilimira Aisrayeli ong’ung’udzawo. “Khamu losanganikirana” (NW) limene linatsagana ndi anthu a Israyeli potuluka mu Igupto linagwirizana nawo m’kusonyeza kusakhutira ndi chakudya choperekedwa ndi Mulungu. Powona mkwiyo wa Mulungu ndi pokhala wotopa ndi thayo la kuyang’anira anthu ndi zosoŵa zawo, Mose anadandaula kuti: “Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine. Ndipo ngati mundichitira chotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang’ane tsoka langa.” (Numeri 11:1-15) Kodi Yehova anayankha motani? Iye anasankha “amuna makumi asanu ndi aŵiri mwa akulu a Israyeli” naika mzimu wake pa iwo kotero kuti iwo moyenerera akhale ndi phande m’ntchito yoyang’anira ndi Mose. (Numeri 11:16, 17, 24, 25) Pokhala ndi amuna oyeneretsedwa otero ogaŵiridwa, chithandizo chinalipo mosavuta kwambiri kwa Aisrayeli ndi kwa “khamu lalikulu losanganikirana.”—Eksodo 12:38, NW.
7, 8. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anaperekera “mphatso mwa amuna” mu Israyeli wakale? (b) Kodi ndikugwira ntchito kotani kwa Salmo 68:18 m’zaka za zana loyamba kumene Paulo akunena?
7 Aisrayeli atakhala m’Dziko Lolonjezedwa kwa zaka zambiri, Yehova mophiphiritsira anakwera ku phiri la Ziyoni napanga Yerusalemu kukhala malikulu a ufumu weniweni ndipo Davide kukhala mfumu yake. Potamanda Mulungu, “Wamphamvuyonse,” Davide anakweza mawu ake naimba kuti: “Mwakwera pamwamba; mwatenga ogwidwa ukapolo; mwatenga mphatso mumpangidwe wa amuna.” (Salmo 68:14, 18, NW) Ndithudi, anthu otengedwa ukapolo mkati mwa kugonjetsedwa kwa Dziko Lolonjezedwa anagwiritsiridwa ntchito kuthandiza Alevi pantchito zawo.—Ezara 8:20.
8 M’zaka za zana loyamba C.E., mtumwi Wachikristu Paulo ananena za kukwaniritsidwa kwa ulosi wa mawu a wamasalmoyo. Paulo analemba kuti: “Kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Kristu. Chifukwa chake anena, Mmene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende, naninkha [mphatso mwa amuna, NW]. Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso [kuzigawo zapansi, ndiko kuti, padziko lapansi, NW]? Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.” (Aefeso 4:7-10) Kodi ndani amene ali “yemweyonso”? Simunthu wina konse kusiyapo woimira Yehova, Davide Wamkulu ndi Mfumu Yaumesiya, Yesu Kristu. Iye ndiye amene Mulungu anaukitsa “namkwezetsa.”—Afilipi 2:5-11.
9. (a) Kodi ndani m’zaka za zana loyamba amene anali mphatso mwa amuna? (b) Kodi ndani amene ali mphatso mwa amuna m’nthaŵi zamakono?
9 Nangano, kodi ndani amene ali “mphatso mwa amuna” ameneŵa (kapena, “zimene zili amunawo”)? Paulo akufotokoza kuti Woimira Wamkulu wa Mulungu “anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki kumangirira thupi la Kristu.” (Aefeso 4:11, 12) Otsatira onse a Kristu amene anatumikira monga atumwi, aneneri, alaliki, abusa, ndi aphunzitsi anatero pansi pa chitsogozo chateokratiki. (Luka 6:12-16; Machitidwe 8:12; 11;27, 28; 15:22; 1 Petro 5:1-3) M’tsiku lathu, amuna oyeneretsedwa mwauzimu oikidwa ndi mzimu woyera amatumikira monga oyang’anira m’mipingo pafupifupi 70,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse. Iwo ndiwo mphatso zathu mwa amuna. (Machitidwe 20:28) Popeza kuti ntchito ya kulalikira Ufumu ikupitirizabe kufutukuka padziko lonse, abale owonjezereka “akukalimira” (NW) ndi kusenza mathayo ochita ndi “udindo wa woyang’anira.” (1 Timoteo 3:1) Ataikidwa, nawonso amakhala mphatso mwa amuna.
10. Kodi ndimotani mmene mafotokozedwe a Yesaya a “akalonga” amayenerera bwino lomwe ntchito ya akulu Achikristu lerolino?
10 Akulu Achikristu ameneŵa, kapena mphatso mwa amuna, amayenerera bwino lomwe mafotokozedwe amene mneneri Yesaya anapereka pamene anali kuneneratu za ntchito ya “akalonga,” oyang’anira muulamuliro wa Ufumu. Aliyense ayenera kukhala “monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:1, 2) Zimenezi zimasonyeza mmene kuyang’anira kwachikondi kwa amuna oikidwa ameneŵa kuyenera kukhalira kochilikiza. Kodi ndimotani mmene mungapindulire nako mokwanira?
Kukhala Woyamba Kuchitapo Kanthu
11. Pamene tichita tondovi mwauzimu, kodi tingalandire motani chithandizo?
11 Mwachibadwa munthu womamira m’madzi amakuwa kuti athandizidwe. Samazengereza. Pamene moyo uli pachiswe, palibe munthu amene amafuna kusonkhezeredwa kufuula kuti athandizidwe. Kodi Mfumu Davide sanabwerezebwereze kufuulira Yehova kaamba ka chithandizo? (Salmo 3:4; 4:1; 5:1-3; 17:1, 6; 34:6, 17-19; 39:12) Pamene tichita tondovi mwauzimu, mwinamwake tikumira m’kuthedwa nzeru, ife mofananamo timatembenukira kwa Yehova m’pemphero ndi kumchonderera kuti atitsogoze ndi mzimu wake woyera. (Salmo 55:22; Afilipi 4:6, 7) Timafunafuna chitonthozo m’Malemba. (Aroma 15:4) Timafufuza zinthu m’zofalitsidwa Zachikristu za Watch Tower Society kaamba ka chilangizo chopindulitsa. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimatikhozetsa kuthetsa mavuto a ife eni. Komabe, ngati tikhala othedwa nzeru ndi zovuta tingafunefunenso uphungu kwa akulu ampingo oikidwa. Kwenikweni, pangakhale nthaŵi zina pamene tifunikiradi ‘kuitana akulu.’ Kodi nkuitaniranji akulu Achikristu? Kodi angathandize motani awo amene afunikira chithandizo chauzimu?
12-14. (a) Kodi ndiiti imene iri njira yanzeru yotsatira pamene munthu adwala? (b) Malinga nkunena kwa Yakobo 5:14, kodi Akristu ‘odwala’ akulangizidwa kuchitanji? (c) Kodi ndimtundu wotani wa kudwala umene Yakobo 5:14 akunena, ndipo nchifukwa ninji mukuyankha motero?
12 Pamene tidwala, timagona kuti tilole mphamvu yochilitsa yathupi kugwira ntchito. Koma ngati matenda athuwo apitirizabe, mwanzeru timakafunafuna chithandizo cha madokotala odziŵa. Kodi sitiyenera kuchitanso mofananamo ngati tikhala ofooka mwauzimu?
13 Wonani zimene wophunzira Yakobo amatilangiza ponena za zimenezi. Iye amati: “Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la [Yehova, NW].” (Yakobo 5:14) Kodi Yakobo panopa akunena za mtundu wotani wa matenda? Othirira ndemanga pa Baibulo ena amanena kuti ndiwo matenda akuthupi, akumalingalira kuti kudzoza ndi mafutako kunali mchitidwe wa mankhwala wofala m’nthaŵiyo. (Luka 10:34) Amakhulupiriranso kuti Yakobo anali kulingalira za kuchiritsa kozizwitsa kupyolera m’mphatso ya kuchiritsa. Komabe, kodi nchiyani chimene mawu apatsogolo ndi apambuyo amasonyeza?
14 ‘Kusekera’ nkosiyana ndi “kumva zoŵaŵa.” Zimenezi zimapereka lingaliro lakuti Yakobo anali kunena za kudwala kwauzimu. (Yakobo 5:13) “Akulu a mpingo,” osati madokotala kapena ngakhale awo amene anali ndi mphatso yozizwitsa ya kuchiritsa, ndiwo amene anafunikira kuitanidwa. Ndipo kodi iwo anafunikira kudzachitanji? Yakobo akuti: “Apemphere pa iye, . . . ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo.” (Yakobo 5:14, 15; yerekezerani ndi Salmo 119:9-16.) Chotitsimikiza mokhutiritsa maganizo kuti Yakobo akunena za kudwala kwauzimu ndicho chenicheni chakuti iye akulimbikitsa kuululidwa kwa machimo mogwirizana ndi kuchiritsidwa koyembekezeredwako. Iye akulemba kuti: “Muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe.” Ngati tchimo lalikulu ndilo chochititsa kudwala kwauzimu kumeneko, munthu wodwalayo angayembekezeredwe kuchira kokha ngati alabadira moyenera machenjezo ozikidwa pa Mawu a Mulungu, alapa, natembenuka kuchoka panjira yake yauchimo.—Yakobo 5:16; Machitidwe 3:19.
15. Kodi ndimchitidwe wotani umene ukulimbikitsidwa pa Yakobo 5:13, 14?
15 Pali kanthu kenanso kofuna kukadziŵa muuphungu umene Yakobo akupereka. Pomva zoŵaŵa, Mkristu ayenera ‘kupitirizabe kupemphera.’ Ngati akusekera, “ayimbire.” Mkhalidwe uliwonse—kaya munthu akumva zoŵaŵa kapena akusekera—umafuna kuchitapo kanthu. Pemphero limafunika kumbali ina, ndipo kukondwera kumbali inayo. Chotero, kodi tiyenera kuyembekezera chiyani pamene Yakobo akufunsa kuti: “Pali wina kodi adwala mwa inu?” Kachiŵirinso iye akulimbikitsa kuchitapo kanthu, inde, kukhala woyamba kuchitapo kanthu. “Adziitanire akulu a mpingo.”—Salmo 50:15; Aefeso 5:19; Akolose 3:16.
Mmene “Akulu” Amathandizira
16, 17. Kodi ndimotani mmene akulu amatithandizira kugwiritsira ntchito malamulo a mkhalidwe a Baibulo?
16 Nthaŵi zina kumativuta kudziŵa mmene tingagwiritsire ntchito malamulo a makhalidwe a Baibulo pamikhalidwe ya ife eni. Panopo ndipo pamene akulu Achikristu angakhaledi magwero amtengo wapatali a chithandizo. Mwachitsanzo, iwo amapempherera wodwala mwauzimu ndi ‘kumdzoza ndi mafuta m’dzina la Yehova’ mwa kugwiritsira ntchito mwaluso malangizo ochiritsa a m’Mawu a Mulungu. Motero akulu angakhale ochilikiza kwambiri pakuchira kwathu kwauzimu. (Salmo 141:5) Kaŵirikaŵiri, chinthu chokha chimene timafunikira ndicho chitsimikizo chakuti tikulingalira m’njira yoyenera. Kukambitsirana zinthu ndi mkulu Wachikristu wachidziŵitso kudzalimbikitsa chitsimikizo chathu cha kuchita choyenera.—Miyambo 27:17.
17 Pamene apemphedwa kukachezera ena, akulu Achikristu ayenera ‘kulimbikitsa amantha mtima.’ ‘Adzachilikizanso ofooka, [ndi] kukhala oleza mtima ndi onse.’ (1 Atesalonika 5:14) Unansi womvana, wapafupi kwambiri wotero pakati pa “akulu” ndi “ofooka” umawonjezera kuthekera kwa kuchira kotheratu kwa thanzi lauzimu.
Thayo la Munthu Mwini ndi Pemphero
18, 19. Kodi ndintchito yotani imene akulu Achikristu amachita mogwirizana ndi Agalatiya 6:2, 5?
18 Akulu Achikristu ayenera kusenza thayo lawo la nkhosa za Mulungu. Ayenera kukhala ochilikiza. Mwachitsanzo, Paulo anati: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Kristu.” Mtumwiyo analembanso kuti: “Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.”—Agalatiya 6:1, 2, 5.
19 Kodi ndimotani mmene tinganyamulirane zothodwetsa pamene kuli kwakuti tanyamula katundu wathu? Kusiyana kumene kulipo m’tanthauzo la mawu Achigiriki otembenuzidwa kuti “zothodwetsa” ndi “katundu” kumapereka yankho lake. Ngati Mkristu aloŵa muvuto lauzimu limene lili lomthodwetsa, akulu ndi okhulupirira anzake ena angamthangate, motero akumamthandiza kusenza “zothodwetsa” zake. Komabe, munthu mwiniyo akuyembekezeredwa kusenza “katundu” wa iye mwini wa thayo lake kwa Mulungu.a Akulu mosangalala amasenza “zothodwetsa” za abale awo kupyolera mwa chilimbikitso, uphungu Wamalemba, ndi pemphero. Komabe, akulu samatichotsera “katundu” wa ife eni wa thayo lathu lauzimu.—Aroma 15:1.
20. Kodi nchifukwa ninji pemphero siliyenera kunyalanyazidwa?
20 Pemphero lili lofunika ndipo siliyenera kunyalanyazidwa. Koma Akristu ambiri odwala amawona kupemphera kukhala kovuta. Pamene akulu aperekera pemphero la chikhulupiro kaamba ka munthu wodwala mwauzimu, kodi cholinga chake nchiyani? “[Yehova, NW] adzamuukitsa,” m’kupanda chiyembekezo, ndipo adzamlimbitsa kulondola njira ya chowonadi ndi chilungamo. Mkristu wodwala mwauzimu angakhale ndi mkhalidwe wa maganizo wolakwika koma osati kuti anali atachita kwenikweni tchimo lalikulu, pakuti Yakobo amati: “Ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.” Uphungu Wamalemba wa akulu wophatikizidwa ndi pemphero laphamphu nthaŵi zina umasonkhezera munthu wofooka mwauzimu kuulula machimo aakulu amene angakhale atachita ndi kusonyeza mzimu wolapa. Zimenezinso, zimasonkhezera Mulungu kukhululukira.—Yakobo 5:15, 16.
21. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu ena ali ozengereza kuitana akulu? (b) Kodi nchiyani chimene chidzalingaliridwa m’nkhani yotsatira?
21 Poyang’anizana ndi thayo lalikulu la kusamalira namtindi wa anthu atsopano omwe akuloŵa mumpingo Wachikristu, akulu okhala ndi chikumbumtima chabwino ali nzambiri zoti achite m’kupereka uyang’aniro wokwanira. Ndithudi, mphatso mwa amuna zimenezi ndizo chogaŵira chabwino kwambiri chochokera kwa Yehova kutithandiza kupirira m’nthaŵi zoŵaŵitsa zino. Komabe, Akristu ena amazengereza kuitana akulu kudzawathandiza, akumaganiza kuti abale ameneŵa ngotanganitsidwa kwambiri kapena ngochulukiridwa ndi mavuto. Nkhani yotsatirayo idzatithandiza kuzindikira kuti amuna ameneŵa amakonda kuthandiza, popeza kuti amatumikira mofunitsitsa monga abusa aang’ono mumpingo Wachikristu.
[Mawu a M’munsi]
a Buku lotchedwa A Linguistic Key to the Greek New Testament, lolembedwa ndi Fritz Rienecker, limafotokoza phor·tiʹon kukhala “katundu amene munthu akuyembekezeredwa kunyamula” ndipo limanenanso kuti: “Linagwiritsiridwa ntchito monga mawu a kunkhondo onena za phukusi la munthu kapena katundu wa msilikali.”
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Pamene tifuna chithandizo, kodi ndichithandizo cha mbali zitatu chotani chimene Yehova amapereka?
◻ Kodi ndani amene ali mphatso mwa amuna m’nthaŵi zamakono?
◻ Kodi ndiliti pamene tiyenera kuitana akulu?
◻ Kodi nchithandizo chotani chimene tingayembekezere kwa akulu Achikristu?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mumasangalala ndi mapindu auzimu a pemphero, phunziro la Baibulo, ndi chithandizo cha akulu Achikristu?