Kodi Mulungu Amafuna Kuti Tiziulula Ndiponso Kulapa Machimo Athu?
M’matchalitchi ambiri, anthu amaona kuti kuulula ndiponso kulapa machimo awo kwa wansembe kapena mtsogoleri wachipembedzo ndi mwambo wa chipembedzo chawo ndiponso ndi mbali ya kulambira. Komano masiku ano, anthu amaona kuti ali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna. Choncho, kodi kuulula machimo n’kothandizabe? Nanga kodi n’kofunikadi?
ANTHU ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo nyuzipepala ina ya ku Canada inafotokoza za munthu wina amene anavomereza kuti ndi zovuta kuuza munthu wina za machimo ako. Komabe munthuyo ananena kuti “ukaulula machimo kwa munthu wina, akapemphera nawe limodzi ndiponso kukupatsa malangizo, umakhala ndi mtendere wa mu mtima.” (National Post) Mosiyana ndi maganizo amenewa, buku lina linagwira mawu a munthu wina amene ananena kuti: “Chimodzi mwa zinthu zosokoneza maganizo kwambiri m’matchalitchi ndi kuulula machimo kwa wansembe, chifukwa kuchita zimenezo kumangowonjezera nkhawa.” (Bless Me, Father, for I Have Sinned) Koma kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani imeneyi?
Zimene Baibulo Limanena pa Nkhaniyi
M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa mtundu wa Aisiraeli, muli malangizo osapita m’mbali onena zimene munthu ankayenera kuchita akachimwa. Mwachitsanzo, munthu akachimwira mnzake kapena akaphwanya limodzi mwa malamulo a Mulungu, ankafunika kuulula tchimo lakelo kwa wansembe wa fuko la Levi. Wansembeyo ankapereka nsembe kwa Mulungu kuti tchimo la munthuyo likhululukidwe.—Levitiko 5:1-6.
Patapita zaka zambiri Mulungu atapereka malamulo amenewo, mneneri Natani anadzudzula Mfumu Davide chifukwa cha machimo amene Davideyo anachita. Kodi Davide anatani? Iye anavomereza machimo ake nthawi yomweyo ndipo anati: “Ndachimwira Yehova.” (2 Samueli 12:13) Ndiponso iye anapemphera, kuchonderera Mulungu kuti amuchitire chifundo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Patapita nthawi, Davide analemba kuti: “Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.”—Salmo 32:5; 51:1-4.
M’nthawi ya atumwi, Mulungu ankafunabe kuti munthu wa mu mpingo wachikhristu akachimwa aziulula machimo ake. Yakobe, amenenso anali mmodzi mwa akulu a mu mpingo wa ku Yerusalemu, analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Muululirane machimo anu poyera ndi kupemphererana wina ndi mnzake, kuti muchiritsidwe.” (Yakobe 5:16) Ndiyeno kodi Akhristu ayenera kuulula chiyani? Nanga kodi aziulula kwa ndani?
Kodi ndi Machimo Ati Amene Munthu Ayenera Kuulula?
Anthu opanda ungwirofe timalakwirana chifukwa tsiku ndi tsiku timachita zinthu zina mosaganiza bwino ndipo nthawi zina sitilankhula bwino. (Aroma 3:23) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuulula kwa akulu a mpingo chilichonse chimene talakwira anthu ena?
N’zoona kuti Mulungu amadana ndi tchimo lililonse, komabe iye amadziwa kuti nthawi zina timalephera kuchita zinthu bwino chifukwa chakuti tinabadwa ndi uchimo. Ndiye chifukwa chake wolemba masalmo analemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.” (Salmo 130:3, 4) Nthawi zina titha kuchimwa ndi kulakwira anthu ena mosadziwa. Kodi zikatero tiyenera kuchita chiyani? Kumbukirani kuti m’pemphero lachitsanzo limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake mulinso mawu akuti: “Mutikhululukire machimo athu, pakuti nafenso timakhululukira aliyense amene amatilakwira.” (Luka 11:4) Ndithudi, Mulungu adzatikhululukira ngati titamupempha m’dzina la Yesu kuti atikhululukire.—Yohane 14:13, 14.
Mlembali, Yesu anasonyeza kuti Mulungu angatikhululukire machimo athu pokhapokha ngati ifenso takhululukira “amene amatilakwira.” Mtumwi Paulo anakumbutsa okhulupirira anzake kuti: “Khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso anakukhululukirani Mulungu ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.” (Aefeso 4:32) Ngati timakhululukira anthu ena, tingakhale ndi chidaliro chonse chakuti Mulungu adzatikhululukira.
Nanga bwanji ngati munthu wachita tchimo lalikulu ngati kuba, kunama mwadala, chiwerewere, kuledzera ndi machimo ena ngati amenewa? Aliyense wochita zimenezi akuphwanya malamulo a Mulungu, kumene n’kulakwira Mulungu. Kodi ayenera kuchita chiyani?
Kodi Munthu Ayenera Kuulula Machimo Ake Kwa Ndani?
Mulungu sanapatse anthu udindo wokhululukira anthu amene amuchimwira iyeyo. Iye yekha ndi amene angathe kukhululukira machimo. Baibulo limatiuza momveka bwino kuti: “Ngati tivomereza machimo athu, [Mulungu] ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu ndi kutiyeretsa kusalungama konse.” (1 Yohane 1:9) Komano kodi munthu ayenera kuulula machimo ake kwa ndani?
Popeza Mulungu yekha ndi amene angakhululukire machimo, ndiye kuti machimo ayenera kuululidwa kwa iye. Monga taonera, zimenezi n’zimene Davide anachita. Koma kodi kuti Mulungu atikhululukire machimo athu tiyenera kuchita chiyani? Baibulo limatiuza kuti: “Chotero lapani, ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe. Ndi kutinso nyengo za chitsitsimutso zibwere kuchokera kwa Yehova mwiniyo.” (Machitidwe 3:19) Izi zikusonyeza kuti munthu amakhululukidwa machimo ake osati kokha chifukwa choti wazindikira kuti analakwa ndipo waulula machimo akewo. Iye amayeneranso kukhala wofunitsitsa kusiya njira zake zoipazo. Kawirikawiri, kusiya njira zoipa n’kumene kumakhala kovuta. Koma thandizo lilipo.
Kumbukirani mawu a Yakobe amene tawatchula poyamba paja akuti: “Muululirane machimo anu poyera ndi kupemphererana wina ndi mnzake, kuti muchiritsidwe.” Kenako Yakobe ananenanso kuti: “Pembedzero la munthu wolungama, limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.” (Yakobe 5:16) “Munthu wolungama” ameneyu angakhale mmodzi mwa “akulu a mpingo” amene Yakobe anawatchula m’vesi 14. Mu mpingo wachikhristu, muli “akulu” auzimu amene anaikidwa kuti azithandiza anthu amene akufuna kuti Mulungu awakhululukire. Sikuti “akulu” amenewa angafafanize machimo a munthu. Zimenezi zili choncho chifukwa palibe amene anapatsidwa udindo wokhululukira machimo a munthu mnzake amene walakwira Mulungu.a Koma “akulu” amenewa anapatsidwa udindo wodzudzula ndi kuwongolera munthu amene wachita tchimo lalikulu. Zimenezi zimamuthandiza kuzindikira kukula kwa tchimo lake ndi kufunika kolapa.—Agalatiya 6:1.
N’chifukwa Chiyani Munthu Ayenera Kuulula Machimo Ake?
Kaya tchimo likhale lalikulu kapena laling’ono, wochimwayo amakhala kuti wawononga ubwenzi wake ndi mnzakeyo komanso ndi Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, munthuyo angamavutike maganizo kapena kuda nkhawa. Zimenezi zimachitika chifukwa cha chikumbumtima chimene Mlengi wathu anatipatsa. (Aroma 2:14, 15) Kodi zikatere munthu ayenera kuchita chiyani?
M’buku la Yakobe mulinso mawu olimbikitsa akuti: “Kodi pali wina amene akudwala [mwauzimu] pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo am’pempherere, am’pake mafuta m’dzina la Yehova. Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamuutsa. Ndiponso ngati anachita machimo, iye adzakhululukidwa.”—Yakobe 5:14, 15.
Apanso tikuona kuti akulu akupemphedwa kuthandiza nkhosa. Kodi angachite bwanji zimenezi? Osati mwa kungomvetsera pamene munthu akuulula machimo ake. Koma ayenera kuthandiza ‘wodwala mwauzimuyo kuti achire.’ Yakobe anatchula zinthu ziwiri zimene akulu ayenera kuchita.
Choyamba, ayenera ‘kum’paka mafuta.’ Mafuta amenewa akutanthauza mphamvu yochiritsa ya Mawu a Mulungu. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. . . . Amathanso kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima,” kutanthauza kuti amalowerera m’maganizo ndi mu mtima mwa munthu. (Aheberi 4:12) Akulu amagwiritsa ntchito Baibulo mwaluso kuthandiza munthu wodwala mwauzimuyo kuona chimene chinachititsa kuti achite tchimo. Amamuthandizanso kudziwa zimene ayenera kuchita kuti akonze zimene analakwitsazo n’kuyamba kuchita zimene Mulungu amafuna.
Ndiyeno pamafunikanso “pemphero la chikhulupiriro.” Ngakhale kuti mapemphero a akulu sangachititse kuti Mulungu asinthe chilango chimene angapereke kwa munthuyo mogwirizana ndi chilungamo chake, Iye amamvetsera mapemphero amenewo ndipo amakhala wofunitsitsa kukhululukira machimo pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo la Khristu. (1 Yohane 2:2) Mulungu ndi wokonzeka kuthandiza munthu aliyense wochimwa amene walapadi ndipo akuonetsa “ntchito zosonyeza kulapa.”—Machitidwe 26:20.
Munthu akachimwira Mulungu kapena munthu mnzake, ayenera kuulula tchimo lakelo kuti akhale pa ubale wabwino ndi Mulungu. Chimenechi ndiye chifukwa chachikulu chimene munthuyo ayenera kuululira tchimo lake kwa Mulungu. Yesu Khristu ananena kuti choyamba tiyenera kukambirana vuto lililonse limene tingakhale nalo ndi munthu mnzathu, n’kukhalanso naye pa mtendere. Kenako tikhoza kulambira Mulungu ndi chikumbumtima chabwino. (Mateyo 5:23, 24) Lemba la Miyambo 28:13 limati: “Wobisa machimo ake sadzaona mwayi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.” Tikadzichepetsa pamaso pa Yehova Mulungu n’kupempha kuti atikhululukire, iye adzasangalala nafe ndipo adzatikweza pa nthawi yake.—1 Petulo 5:6.
[Mawu a M’munsi]
a Ena amaganiza kuti mawu a Yesu olembedwa pa Yohane 20:22, 23 amasonyeza kuti pali anthu ena amene ali ndi udindo wokhululukira machimo. Kuti mumve zambiri pa nkhani imeneyi, werengani Nsanja ya Olonda, ya April 15, 1996, tsamba 28 ndi 29.
[Mawu Otsindika patsamba 23]
Mulungu angatikhululukire zolakwa zathu ngati titamupempha kuti atikhululukire m’dzina la Yesu
[Chithunzi patsamba 24]
Chifukwa chachikulu choululira tchimo ndicho kukhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu