CHIGAWO 9
Mutha Kupindula ndi Chipembedzo Choona Kosatha!
1. Kodi chidzachitika n’chiyani ‘tikayandikira kwa Mulungu’?
YEHOVA amakonda anthu amene amam’tumikira. Ngati mumalambira Yehova, adzakudalitsani lero ndi m’tsogolo. Baibulo limati: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”—Yakobo 4:8.
2. Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tiyandikire kwa Mulungu, ndipo tikatero adzatani nawo mapemphero athu?
2 Kuti muyandikire kwa Mulungu, mufunika kuphunzira Mawu ake ndi kuwatsatira. Mukamapemphera mogwirizana ndi chifuniro chake, Yehova adzamva mapemphero anu ndi kukuyankhani. Yohane, mtumwi wachikristu, analemba kuti: “Uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa [Mulungu], kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziŵa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziŵa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.”—1 Yohane 5:14, 15.
3-7. Kodi nzeru ya Mulungu tingaipeze mwa kuchita chiyani, ndipo ingatithandize bwanji?
3 Ndiponso, pamene muyandikira kwa Mulungu, adzakupatsani nzeru yosamalira nkhani za moyo wa tsiku ndi tsiku. Baibulo limati: “Wina wa inu ikam’soŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu.”—Yakobo 1:5.
4 Nanga kodi nzeru ya Mulungu imeneyo ingakuthandizeni bwanji? Makamaka, ingakuthandizeni kudziŵa zinthu zimene sizim’sangalatsa Yehova. Mungadziŵenso chifukwa chake zinthu zimenezo zili zolakwa ndi zimene mufunika kuchita kuti muzipeŵe. Kudziŵa zimenezi kungakutetezeni ku mavuto ambiri amene anthu ochuluka ali nawo. Mwachitsanzo, kumvera malangizo a Mulungu akuti anthu ake azikhala ndi makhalidwe abwino kumawathandiza kupeŵa mimba za pathengo, matenda opatsirana m’njira yachiwerewere, ndi kupeŵa kukhala ndi mabanja osasangalala kapena kusudzulana.
5 N’chiyaninso chimene nzeru ya Mulungu ingakuchitireni? Ingatheketse kuti mupindule kwambiri ndi moyo wanu. Ingakuthandizeni kupanga zosankha zanzeru pankhani zofuna kuganiza, monga mmene mungayendetsere ndalama zanu. Mudzatha kutsata zolinga zanzeru ndi kupeŵa zolinga zosapindulitsa kwenikweni.
6 Nzeru ya Mulungu ingakuthandizeninso pa ubale wanu ndi anthu ena. Mungakhale ndi banja losangalala ndithu. Mungakhale pa ubwenzi wolimba ndi anthu ena, inde, ubwenzi wokhalitsa, ndipo anthu angamakulemekezeni, ngakhale aja amene satumikira Mulungu.
7 Ndiponso, kukhala kwanu ndi nzeru ya Mulungu kudzasintha maganizo anu pa moyo ndipo mudzayamba kuuona bwino. Idzakuthandizani kupirira zovuta ndi zokhumudwitsa zina. Ndiponso, muziti mukaganiza za m’tsogolo, mtima wanu uzikhala mwaphe, osatekeseka. Ndiyeno, mtima wanu wosatekesekawo udzakuthandizani kupeŵa kuvutika maganizo ndipo mudzakhala wathanzi.—Miyambo 14:30; Yesaya 48:17.
8. Mukamatumikira Mulungu, simudzaopa chiyani?
8 Mukamatumikira Mulungu woona, simudzakhala ndi mantha amene amasautsa aja amene sam’tumikira. Podziŵa kuti akufa ali kumanda ndipo saali amoyo, simudzawaopa. Komanso chifukwa chokhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti adzautsa akufa, simudzaopa kufa. Ndiponso podziŵa kuti Mulungu ali wamphamvuyonse, simudzaopa ufiti kapena matsenga.—Yohane 8:32.
Olungama Adzalandira Dziko Lapansi
9-11. Kodi adzakhala m’Paradaiso ndani, ndipo ndani sadzakhalamo?
9 Mukayandikira kwa Mulungu, simudzaopa za m’tsogolo. Monga momwe taonera, Baibulo linalosera ambiri mwa mavuto amene tikuwaona padziko lapansi masiku ano. Yehova akutiuza kuti zimenezi ndi zakanthaŵi chabe; Ufumu wa Mulungu usandutsa dziko lapansili kukhala paradaiso posachedwa.—Luka 21:10, 11, 31; 23:43.
10 Amene adzakhala m’Paradaiso ndi aja okha amene amayandikira kwa Yehova ndi kum’tumikira. Baibulo limati: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:10, 11.
11 Anthu ouma khosi amene amakana kumvera malamulo olungama a Mulungu adzataya miyoyo yawo kwamuyaya. (2 Atesalonika 1:8, 9) Sadzakhalakonso. Adzafa pamodzi ndi Satana ndi ziŵanda zake, imfa yoti sadzakhalanso ndi moyo mpaka muyaya. (Chivumbulutso 20:10, 14) Koma amene amaphunzira za Yehova ndi kum’tumikira adzakhala ndi chimwemwe chodzaza tsaya m’Paradaiso padziko lapansi.
Tsogolo Labwino Kwambiri!
12. Kodi Baibulo limati chiyani za m’tsogolo?
12 Yehova wasungira anthu amene amam’konda zinthu zabwino kwambiri! Tangoonani mmene Mawu ake amafotokozera mmene moyo udzakhalira m’Paradaiso padziko lapansi:
Chakudya chochuluka: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu [kapena kuti, chakudya] dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.”—Salmo 72:16.
Nyumba zabwino: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo.”—Yesaya 65:21.
Ntchito yosangalatsa: “Osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe.”—Yesaya 65:22, 23.
Moyo wopanda matenda: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
Moyo wopanda kulemala: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.”—Yesaya 35:5, 6.
Moyo wopanda zopweteka, chisoni, imfa: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
Moyo wopanda nkhondo: “[Mulungu] aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi.”—Salmo 46:9.
Moyo wosatha: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
13. Ndani yekha angathe kusandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso, ndipo chifukwa chiyani?
13 Anthu sangathe kuchita zinthu zimenezi, koma Yehova ali nazo mphamvu zochita chilichonse chimene wanena kuti adzachita. Palibe chingam’letse kuchita zimene akufuna. Baibulo limati: “Palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.”—Luka 1:37.
14. Kodi mufunika kuchita chiyani kuti muloŵe panjira ya kumoyo wosatha
14 Yehova, kudzera mwa Mboni zake, akupatsa anthu kulikonse mwayi ‘woloŵa pa chipata chopapatiza’ ndi kuyenda panjira ya kumoyo wosatha. Mukhaletu pakati pa anthu osangalala amene akulabadira pempholo. Tsatani chipembedzo choona ndipo landirani madalitso a Yehova kosatha!—Mateyu 7:13, 14.