Mphatso Yodabwitsa ya Ufulu
KODI mumayamikira kuti muli ndi ufulu wa kusankha mmene mudzayendera nawo moyo wanu, chimene mudzachita ndikunena? Kapena kodi mungafune munthu wina kukukonzerani mmene liwu lirilonse ndi kachitidwe ziyenera kukhalira, mphindi iriyonse yatsiku, kuutali umene inu mudzakhala ndi moyo?
Palibe munthu wolongosoka amene angafune kuti moyo wake ulandidwe kwa iye ndikulamulidwa kotheratu motero ndi munthu wina. Kukhala ndi moyo m’njira imeneyo kukakhaladi kotsendereza kwenikweni ndi kokhwethemula. Timafunikira ufulu.
Koma kodi nchifukwa ninji tiri ndi chikhumbo choterocho cha ufulu? Kumvetsetsa mmene timaukondera ufulu wathu wa kudzisankhira chinthu ndiko mfungulo ya kumvetsetsa mmene kuipa ndi kuvutika kudayambira. Kudzatithandizanso kumvetsetsa chifukwa chimene Mulungu wayembekezera kufikira tsopano asanachitepo kanthu kubweretsa kuipa ndi kuvutika kumapeto ake.
Mmene Tinapangidwira
Pamene Mulungu analenga anthu, pakati pa mphatso zambiri zimene iye anawapatsa panali ufulu. Baibulo limatiuza kuti Mulungu analenga munthu ‘m’chifanizo ndi chikhalidwe’ chake, ndipo mkhalidwe umodzi umene Mulungu ali nawo ndiwo ufulu wodzisankhira chinthu. (Genesis 1:26; Deuteronomo 7:6) Chotero, pamene iye analenga anthu, anawapatsa mkhalidwe wodabwitsa womwe uja—mphatso ya ufulu.
Ichi ndicho chifukwa chake timakonda ufulu mmalo mwa ukapolo wodzetsedwa ndi olamulira otsendereza. Ndicho chifukwa chake mkwiyo umakula motsutsana ndi malamulo oipa ndi otsendereza kwakuti anthu kaŵirikaŵiri amagalukira kuti apate ufulu.
Kukhumba ufulu sindiko ngozi chabe. Baibulo limapereka chifukwa chake. Ilo limati: ‘Pamene pali mzimu wa Yehova pali ufulu.’ (2 Akorinto 3:17) Chotero kufuna ufulu kuli mbali ya chibadwa chathu chifukwa chakuti Mulungu anatilenga mwanjirayo. Ndicho chinthu chimene amafuna kuti tikhale nacho chifukwa chakuti mwiniyekhayo ndiye Mulungu waufulu.—2 Akorinto 3:17.
Mulungu anatipatsanso nyonga ya maganizo, monga ngati mphamvu ya kudziŵa zinthu, kuzindikira, ndi kuweruza, kumene kumagwirizana ndi ufuluwo. Izi zimatitheketsa kuganiza, kusanthula nkhani, kupanga zosankha, ndi kudziŵa zabwino pa zoipa. (Ahebri 5:14) Sitinalengedwe kukhala ngati maroboti opanda maganizo amene alibe ufulu wawo; ndipo sitinalengedwenso ndi maganizo olinganizidwira chochita, monga mmene zinalengedwera nyama.
Kuphatikiza paufulu, makolo athu oyambirira anapatsidwa chinthu chirichonse chimene munthu aliyense akachifuna mwanzeru: Iwo anaikidwa m’paradaiso yonga paki; iwo anali ndi chuma chakuthupi cha mwana alirenji; iwo anali ndi malingaliro ndi matupi angwiro omwe sakakalamba kapena kudwala ndi kufa; iwo akakhala ndi ana amene akakhalanso ndi mtsogolo mwachimwemwe; ndipo chiŵerengero chomawonjezerekacho chikakhala ndi ntchito yokhutiritsa ya kusintha dziko lapansi lonse kukhala paradaiso.—Genesis 1:26-30; 2:15.
Ponena za zonse zimene Mulungu anazipanga, Baibulo limati: ‘Ndipo anawona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, tawonani, zinali zabwino ndithu.’ (Genesis 1:31) Baibulo ponena za Mlengi limanenanso kuti: ‘Ntchito yake ndi yangwiro.’ (Deuteronomo 32:4) Inde, iye analipatsa banja la munthu chiyambi changwiro. Silikanakhala labwino kupanda iye.
Ufulu Wokhala ndi Polekezera
Komabe, kodi mphatso yodabwitsa yaufuluyi ikakhala yopanda polekezera? Eya, kodi inuyo mukadakonda kuyendetsa galimoto m’msewu woyendamo magalimoto ambiri pakadapanda kukhala malamulo a pamsewu, mukadakhala aufulu kuyendetsa mumzere uliwonse, m’njira iriyonse, paliŵiro lirilonse? Ndithudi, zotulukapo za ufulu wopanda polekezera woterowo m’kayendedwe ka magalimoto zikakhala zatsoka kwenikweni.
Nzofanana ndi malamulo a anthu. Ufulu wopanda polekezera kwa ena ungatanthauze kulandidwa ufulu kwa ena. Ufulu wopanda malire ungatulukepo kuponderezana, kumene kumavulaza ufulu wa munthu aliyense. Payenera kukhala polekezera. Chotero, mphatso ya Mulungu ya ufulu siimatanthauza kuti iye analinganiza anthu kudzichitira m’njira iriyonse popanda kulingalira ubwino wa ena.
Mawu a Mulungu pankhaniyi amati: “Muzichita mayendedwe anu monga mfulu, koma ufulu wanuwo usakhale ngati chinthu chophimbira zoipa.” (1 Petro 2:16, The Jerusalem Bible) Chotero Mulungu amafuna kuti ufulu wathu ulamulidwe mwaubwino wa onse. Iye sanalinganizire anthu kukhala ndi ufulu wonse, koma kukhala nawo ufulu waung’ono, wogonjera ku chonena lamulo.
Kodi ndi Malamulo Ayani?
Kodi tinalinganizidwira kumvera malamulo ayani? Kodi ndi malamulo ayani amene amatichitira zabwino? Mbali ina ya lemba la 1 Petro 2:16 lomwe lafotokozedwa pamwambalo limati: “Sindinu kapolo wa munthu aliyense koma Mulungu.” Ichi sichikutanthauza kuti pali ukapolo wotsenderezedwa koma, mmalo mwake, kuti tinalengedwera kugonjera ku malamulo a Mulungu. Timakhala achimwemwe kwabasi titakhala ogonjera kwa iwo.
Malamulo a Mulungu, kuposa mpambo uliwonse wa malamulo omwe angapangidwe ndi munthu, ndiwo amene amapereka chitsogozo chabwinopo kwa munthu aliyense. Monga mmene Yesaya 48:17 akunenera motere: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” Komabe, panthaŵi imodzimodziyo, malamulo a Mulungu amapatsa ufulu waukulu wokhala ndi polekezerawo. Ichi chimalola munthu kudzisankhira yekha zosiyanasiyana, kupangitsa banja la munthu kukhala lokondweretsa kwenikweni, lochititsadi chidwi.
Anthu ngogonjeranso ku malamulo akuthupi a Mulungu. Mwachitsanzo, titanyalanyaza mphamvu yanthaka yokoka zinthu kuchoka mumlengalenga ndi kudumpha kuchokera pamwamba kwenikweni, tidzavulazidwa kapena kuphedwa. Titakhala pansi pamadzi popanda chiwiya chothandizira kupuma, tidzafa m’mphindi zochepa. Ndipo titanyalanyaza malamulo amkati mwa thupi ndikuleka kudya zakudya kapena kumwa madzi, tidzafanso.
Chotero, makolo athu oyamba, ndi anthu onse amene anachokera kwa iwo, analengedwa ndi chifuno cha kumvera malamulo amakhalidwe abwino a Mulungu kapena malamulo amayanjano limodzinso ndi malamulo a kuthupi. Ndipo kumvera malamulo a Mulungu sikungakhale kolemetsa. Mmalo mwake, kukagwira ntchito mokomera ubwino wawo ndi wa banja lonse la anthu lomwe liri kutsogolo. Kukadakhala kuti makolo athu oyambirira sanapyole polekezera malamulo a Mulungu, anthu onse akadakhaladi bwino.
Kodi nchiyani chimene chinachitika kuti chiyambi chabwinochi chiwonongedwe? Kodi nchifukwa ninji mmalo mwake, kuipa ndi kuvutika kwachulukira? Kodi nchifukwa ninji Mulungu wakulola kwanthaŵi yaitali tero?
[Chithunzi patsamba 7]
Mphatso yodabwitsa yaufulu imatisiyanitsa ndi maroboti opanda maganizo ndi nyama zimene zimalinganizidwiratu zochita