Akazi, Muzilemekeza Kwambiri Amuna Anu
‘Akazi gonjerani amuna anu.’—AEFESO 5:22.
1. N’chifukwa chiyani nthawi zambiri akazi amavutika kulemekeza amuna awo?
M’MAYIKO ambiri anthu akamakwatirana, mkwatibwi amalumbira kuti adzalemekeza kwambiri mwamuna wake. Koma mmene amuna ambiri amakhalira ndi akazi awo, zingachititse kuti akaziwo azivutika kuwalemekeza. Komabe ukwati unali ndi chiyambi chabwino. Mulungu anatenga nthiti ya mwamuna woyamba Adamu, n’kupanga mkazi. Adamu ananena mosangalala kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.”—Genesis 2:19-23.
2. Kodi khalidwe la akazi ndi kaonedwe kawo ka ukwati zasintha bwanji m’zaka zaposachedwapa?
2 Ngakhale kuti ukwati unali ndi chiyambi chabwino choterocho, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1960, ku United States kunayambika magulu omenyera ufulu wa akazi omwe cholinga chake chinali choti akazi asamaponderezedwe ndi amuna. Panthawi imeneyo, pafupifupi anthu onse amene ankasiya mabanja awo anali amuna. Pofika kumapeto kwa zaka za m’ma 1960, chiwerengero cha akazi amene ankasiya mabanja awo chinawonjezeka kwambiri. Panopa, zikuoneka kuti chiwerengero cha akazi amene amatukwana, kumwa mowa, kusuta fodya, ndi kuchita zachiwerewere n’chofanana ndi cha amuna. Koma kodi zimenezi zachititsa akazi kukhala osangalala kuposa kale? Ayi. M’mayiko ena, pafupifupi theka la anthu amene amakwatirana amadzasudzulana. Kodi zimene akazi ena akhala akuchitazi pofuna kuti moyo wawo wa m’banja ukhale wabwino zathandiza?—2 Timoteyo 3:1-5.
3. Kodi vuto lenileni mu ukwati n’chiyani?
3 Kodi vuto lenileni n’chiyani? Mwa zina, ndi vuto lomwe lakhalapo kuyambira pamene Hava ananyengedwa ndi mngelo wopanduka, “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.” (Chivumbulutso 12:9; 1 Timoteyo 2:13, 14) Satana wapotoza zimene Mulungu amaphunzitsa. Mwachitsanzo, Mdyerekezi wachititsa ukwati kuoneka ngati chinthu chopanikiza ndi chosautsa. Monga wolamulira wa dzikoli, Satana amapangitsa malangizo a Mulungu kuoneka opanda chilungamo ndi achikale kudzera m’zinthu zimene zimafalitsidwa m’mawailesi, ma TV, ndi zina zotero. (2 Akorinto 4:3, 4) Koma tikaona bwinobwino zimene Mulungu amaphunzitsa zokhudza udindo wa akazi mu ukwati, tingaone kuti Mawu a Mulungu ndi anzeru ndi othandiza.
Chenjezo kwa Ofuna Kukwatiwa
4, 5. (a) N’chifukwa chiyani mkazi ayenera kukhala wosamala akamaganizira zokwatiwa? (b) Kodi mkazi ayenera kuchita chiyani asanavomere zokwatiwa?
4 Baibulo limachenjeza kuti, m’dziko limene likulamulidwa ndi Mdyerekezi lino, ngakhale anthu amene ali ndi ukwati wabwino adzakhala ndi “nsautso.” Choncho, ngakhale kuti ukwati ndi makonzedwe a Mulungu, Baibulo limachenjeza anthu amene akufuna kulowa m’banja. Wolemba Baibulo wina anati mkazi amene mwamuna wake wamwalira ndipo ndi womasuka kukwatiwanso, ‘angakhale wosangalala kwambiri ngati apitiriza mmene alili.’ Yesu analimbikitsanso umbeta kwa anthu “amene angathe kuchita zimenezi.” Komabe, ngati munthu wasankha kulowa m’banja, ayenera kutero “mwa Ambuye,” kutanthauza kuti, ayenera kukwatirana ndi wolambira Mulungu wodzipereka ndi wobatizidwa.—1 Akorinto 7:28, 36-40; Mateyo 19:10-12.
5 Chenjezo la m’Baibulo loti “mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwa lamulo” liyenera kuchititsa mkazi kuganizira mozama za munthu amene akufuna kukwatiwa naye. Mkaziyo “amamasuka pa lamulo la mwamuna wake” kokha ngati mwamunayo wamwalira kapena wachita chigololo ndipo asudzulana chifukwa cha zimenezi. (Aroma 7:2, 3) N’zotheka kukhala pa chibwenzi chosangalatsa ndi munthu chifukwa chongokopeka naye, koma amenewa si maziko okwanira a ukwati wachimwemwe. Choncho mkazi wosakwatiwa ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wokonzeka kukhala pansi pa lamulo la mwamuna ameneyu?’ Ayenera kuganizira funso limeneli asanakwatiwe, osati atakwatiwa kale.
6. Kodi akazi ambiri masiku ano ali ndi ufulu wosankha chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani kusankha mwanzeru kuli kofunika?
6 M’madera ambiri masiku ano, mkazi ali ndi ufulu wosankha kulola kapena kukana akafunsiridwa ukwati. Komabe, zingam’vute kwambiri kuti asankhe mwanzeru, chifukwa choti angamalakelake kwambiri ubwenzi ndi chikondi zimene angazipeze mu ukwati. Wolemba wina anati: “Tikamafuna kwambiri kuchita chinthu, kaya ndi kukwatiwa kapena kukwera phiri linalake, timangoyang’ana zinthu zabwino zokha zimene tikufuna n’kunyalanyaza mavuto ena onse amene angakhalepo.” Ngati munthu wokwera phiri saganiza mwanzeru akhoza kutaya moyo wake, ndipo ngati munthu amene akufuna kukwatiwa sasankha mwanzeru, zinthu zingamuipirenso kwambiri.
7. Kodi pankhani yofufuza munthu wodzamanga naye banja pali malangizo anzeru otani?
7 Mkazi ayenera kuganizira kwambiri zimene angafunikire kuchita akadzakhala pansi pa lamulo la mwamuna amene akumufunsira. Zaka zingapo zapitazo, mtsikana wina wa ku India ananena modzichepetsa kuti: “Makolo athu n’ngachikulire ndiponso anzeru poyerekezera ndi ifeyo, ndipo sapusitsidwa msanga. . . . Ineyo nditha kulakwitsa mosavuta.” N’zoona, makolo ndi anthu ena akhoza kutithandiza kwambiri. Kwa zaka zambiri, mlangizi wina wanzeru ankalimbikitsa achinyamata kudziwa bwino makolo a munthu amene akuganiza zodzamanga naye banja komanso kuona bwinobwino mmene munthuyo amakhalira ndi makolo ake ndi achibale ake ena.
Mmene Yesu Anasonyezera Kuti Anali Wogonjera
8, 9. (a) Kodi Yesu ankakuona bwanji kugonjera Mulungu? (b) Kodi kugonjera kuli ndi ubwino wotani?
8 Akazi akhoza kuona kugonjera ngati kolemekezeka monga mmene Yesu anachitira, ngakhale kuti kungakhale kovuta. Iye ankasangalala kugonjera Mulungu ngakhale kuti anafunika kuzunzika kuti achite zimenezo, mpaka kufera pa mtengo wozunzikirapo. (Luka 22:41-44; Aheberi 5:7, 8; 12:3) Baibulo limati: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna; ndi mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Choncho akazi ayenera kutsatira chitsanzo cha Yesu. Koma mfundo yofunika n’njoti akazi ayenera kugonjera amuna ngakhale asanakwatiwe.
9 Baibulo limafotokoza kuti akazi, kaya ndi okwatiwa kapena osakwatiwa, ayenera kugonjera amuna amene amayang’anira mu mpingo wachikhristu. (1 Timoteyo 2:12, 13; Aheberi 13:17) Akazi akamvera malangizo a Mulungu amenewa, amapereka chitsanzo kwa angelo amene ali m’gulu la Mulungu. (1 Akorinto 11:8-10) Komanso, akazi achikulire okwatiwa, mwa chitsanzo chawo ndi malangizo awo abwino, amaphunzitsa akazi ocheperapo msinkhu ‘kumvera amuna awo.’—Tito 2:3-5.
10. Kodi Yesu anapereka bwanji chitsanzo cha kugonjera?
10 Yesu anazindikira kufunika kogonjera moyenerera. Panthawi ina, anauza mtumwi Petulo kuti akhome msonkho wa iyeyo ndi Petulo kwa anthu olamulira, ndipo anam’patsa ndalama zokhomera msonkhowo. Kenako Petulo anadzalemba kuti: “Chifukwa cha Ambuye, gonjerani makonzedwe alionse opangidwa ndi anthu.” (1 Petulo 2:13; Mateyo 17:24-27) Ponena za chitsanzo chabwino kwambiri cha kugonjera chomwe Yesu anapereka, timawerenga kuti: “Anakhuthula zonse za mwa iye n’kukhala ngati kapolo, nakhala wofanana ndi anthu. Kuposanso pamenepo, atakhala munthu, anadzichepetsa nakhala womvera mpaka imfa.”—Afilipi 2:5-8.
11. N’chifukwa chiyani Petulo analimbikitsa akazi kugonjera ngakhale amuna osakhulupirira?
11 Petulo analimbikitsa Akhristu kuti atsanzire Yesu mwa kugonjera olamulira a m’dziko lino ngakhale atakhala ankhanza ndi opanda chilungamo. Anati: “Ndipotu, anakuitanirani ku moyo umenewu, pakuti ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa.” (1 Petulo 2:21) Kenako, anafotokoza momwe Yesu anavutikira ndi momwe anapiririra chifukwa chogonjera. Ndiyeno analimbikitsa akazi a amuna osakhulupirira kuti: “Momwemonso inu akazi, muzigonjera amuna anu, kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.”—1 Petulo 3:1, 2.
12. Kodi kugonjera kwa Yesu kunali ndi ubwino wotani?
12 Kugonjera pamene mukunyozedwa ndi kuchitiridwa chipongwe kungaonedwe ngati kufooka. Koma Yesu ankaona zimenezi mosiyana. Petulo analemba kuti: “Pamene anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze.” (1 Petulo 2:23) Ena amene anaona Yesu akuvutika, kuphatikizapo wachifwamba amene anapachikidwa pa mtengo pafupi naye ndi msilikali amene anamuona akuphedwa, anayamba kukhulupirira, ngakhale kuti ena sanakhale okhulupirira enieni. (Mateyo 27:38-44, 54; Maliko 15:39; Luka 23:39-43) Mofanana ndi zimenezi, Petulo anasonyeza kuti amuna ena osakhulupirira, ngakhale ankhanza, angathe kukhala Akhristu ataona kugonjera kwa akazi awo. Zimenezi zikuchitikadi masiku ano.
Zimene Akazi Angachite Kuti Akope Amuna Awo
13, 14. Kodi kugonjera amuna osakhulupirira kwathandiza bwanji?
13 Akazi ena okhulupirira akopa amuna awo chifukwa cha khalidwe lawo lachikhristu. Pamsonkhano wina wachigawo wa Mboni za Yehova posachedwapa, mwamuna wina yemwe mkazi wake anali wachikhristu, anati: “Ndikuona kuti ndinali mwamuna wovuta. Koma mkazi wanga ankandilemekezabe kwambiri. Sanayambe wandinyozapo kapena kundikakamiza kutsatira chipembedzo chake. Anandisamalira mwachikondi. Akamapita ku msonkhano waukulu, ankayesetsa kukonzeratu chakudya changa ndi kugwiriratu ntchito zapakhomo. Khalidwe lake linandichititsa kuti ndikhale ndi chidwi ndi Baibulo. N’chifukwa chake lero ndili pano.” Inde, mwamunayu ‘anakopekadi opanda mawu’ chifukwa cha khalidwe la mkazi wake.
14 Petulo anagogomezera kuti zochita za mkazi n’zimene zimakhala zothandiza kwambiri kuposa zonena zake. Mkazi wina amene anaphunzira choonadi cha m’Baibulo ndipo ankafunitsitsa kumapita ku misonkhano yachikhristu, anasonyeza bwino zimenezi. Mwamuna wa mkaziyo anakalipa kuti: “Agnes, ukatuluka pa khomo ilo, usabwerenso!” Iye sanatulukire ‘pa khomo limenelo,’ koma anatulukira pa khomo lina. Tsiku la msonkhano wotsatira, mwamunayo anaopseza kuti: “Ukamabwera sundipeza.” Sanam’pezedi. Anachoka kwa masiku atatu. Atabwera, mkaziyo anam’funsa mwaulemu kuti: “Kodi mungakonde kuti ndikuphikireni chakudya?” Agnes anapitirizabe kukhala wodzipereka kwa Yehova. Patapita nthawi mwamuna wake anavomera kuphunzira Baibulo, anadzipereka kwa Mulungu, ndipo anadzakhala woyang’anira yemwe anali ndi maudindo ambiri.
15. Kodi akazi achikhristu akulimbikitsidwa “kudzikongoletsa” m’njira yotani?
15 Mtumwi Petulo analimbikitsa akazi kuchita zinthu zimene akazi amene tawatchulawa anachita, zomwe ndi “kudzikongoletsa,” koma osati mwa kuganizira kwambiri za “malukidwe a tsitsi” kapena “kuvala malaya apamwamba.” M’malo mwake, Petulo anati: “Kudzikongoletsa kwanu . . . kukhale kwa munthu wa mkati, wa mu mtima, pomuveka zovala zosawonongeka, ndizo mzimu wabata ndi wofatsa umene uli wamtengo wapatali m’maso mwa Mulungu.” Mzimu umenewu umaonekera m’khalidwe ndi kalankhulidwe kabwino, osati kotsutsa kapena kolamula. Mwakutero, mkazi wachikhristu amasonyeza kuti amalemekeza kwambiri mwamuna wake.—1 Petulo 3:3, 4.
Zitsanzo Zofunika Kutsatira
16. Kodi Sara n’chitsanzo chabwino kwa akazi achikhristu m’njira ziti?
16 Petulo analemba kuti: ‘Kale akazi oyera amene anali kuyembekeza Mulungu anali kudzikongoletsa, pogonjera amuna awo.’ (1 Petulo 3:5) Akazi amenewa anazindikira kuti kusangalatsa Yehova mwa kumvera malangizo ake kudzawabweretsera chimwemwe m’banja ndi mphoto ya moyo wosatha. Petulo anatchula za Sara, mkazi wokongola wa Abulahamu, ndipo anati “anali kumvera Abulahamu, ndipo anali kumuitana kuti ‘mbuyanga.’” Sara ankathandiza mwamuna wake woopa Mulungu, amene Mulungu anamutuma kuti akatumikire ku dziko lakutali. Sara anasiya moyo wapamwamba ndiponso anaika moyo wake pachiswe. (Genesis 12:1, 10-13) Petulo anayamikira Sara chifukwa cha chitsanzo chake cha kulimba mtima, ndipo anati: “Inu mwakhala ana ake, mukhalabe ana ake ngati mupitiriza kuchita zabwino ndi kukhala osaopa chochititsa mantha chilichonse.”—1 Petulo 3:6.
17. N’chifukwa chiyani mwina Petulo anali kuganizira za Abigayeli monga chitsanzo kwa akazi achikhristu?
17 Abigayeli ndi mkazi winanso wopanda mantha amene anakhulupirira Mulungu, ndipo mwina Petulo anali kuganiziranso za iye. Anali “wa nzeru yabwino,” koma mwamuna wake Nabala “anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake.” Nabala atakana kuthandiza Davide ndi amuna ake, iwo anaganiza zoti apululutse Nabala ndi banja lake lonse. Koma Abigayeli anachitapo kanthu kuti apulumutse banja lake. Anatenga zakudya n’kuzikweza pa abulu n’kukakumana ndi Davide ndi amuna ake ankhondo ali pa njira. Ataona Davide, anatsika pa bulu nagwada pa maso pake, n’kumuchonderera kuti adekhe. Davide anakhudzidwa mtima kwambiri, ndipo anati: “Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine; ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako.”—1 Samueli 25:2-33.
18. Kodi akazi okwatiwa akamafunidwa ndi mwamuna wina angaganizire chitsanzo cha ndani, ndipo n’chifukwa chiyani chitsanzo chimenechi chili chabwino?
18 Chitsanzo china chabwino kwa akazi ndi Msulami wachitsikana amene anakhalabe wokhulupirika kwa m’busa wosauka amene anali naye pachibwenzi. Iye anapitirizabe kukonda kwambiri m’busayo ngakhale kuti mfumu yolemera inkamufunanso. Chifukwa chokonda kwambiri m’busa wachinyamatayo, mtsikanayo anati: “Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa . . . Madzi ambiri sangazimitse chikondi, ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola.” (Nyimbo ya Solomo 8:6, 7) Choncho, akazi onse amene avomera kukwatiwa nawonso atsimikize mtima kukhalabe okhulupirika kwa amuna awo ndi kuwalemekeza kwambiri.
Malangizo Enanso Ochokera kwa Mulungu
19, 20. (a) Kodi n’chifukwa chiyani akazi ayenera kugonjera amuna awo? (b) Kodi akazi ayenera kutsatira chitsanzo chabwino chiti?
19 Pomaliza, taganizirani nkhani yomwe pachokera lemba la mutu wa nkhani ino, loti: ‘Akazi gonjerani amuna anu.’ (Aefeso 5:22) N’chifukwa chiyani kugonjera koteroko kuli kofunika? Vesi lotsatira likupitiriza kuti: “Chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Khristu alili mutu wa mpingo.” Choncho akazi akulimbikitsidwa kuti: “Monga mpingo umagonjera Khristu, akazinso agonjere amuna awo m’chilichonse.”—Aefeso 5:23, 24, 33.
20 Kuti akazi amvere lamulo limeneli, ayenera kuphunzira ndi kutsatira chitsanzo cha mpingo wa Khristu wa odzozedwa. Tawerengani 2 Akorinto 11:23-28 kuti muone zimene mtumwi Paulo, yemwe anali mu mpingowo, anapirira pokhala wokhulupirika kwa Yesu Khristu, Mutu wake. Mofanana ndi Paulo, akazi komanso onse mu mpingo ayenera kugonjerabe Yesu mokhulupirika. Akazi amasonyeza zimenezi mwa kugonjera amuna awo.
21. Kodi n’chiyani chingalimbikitse akazi kupitirizabe kugonjera amuna awo?
21 Ngakhale kuti akazi ambiri masiku ano safuna kugonjera, mkazi wanzeru amaganizira ubwino wake. Mwachitsanzo, ngati mwamuna ali wosakhulupirira, kumugonjera m’nkhani zonse zomwe sizikuphwanya malamulo kapena mfundo za Mulungu, kungakhale ndi zotsatirapo zosangalatsa zoti mkaziyo ‘angapulumutse mwamuna wake.’ (1 Akorinto 7:13, 16) Komanso, akhoza kukhala wachimwemwe podziwa kuti Yehova Mulungu akusangalala ndi zochita zake ndipo adzamudalitsa kwambiri chifukwa chotsatira chitsanzo cha Mwana wake wokondedwa.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani mkazi angavutike kulemekeza mwamuna wake?
• N’chifukwa chiyani mkazi ayenera kuganiza mozama asanavomere kukwatiwa?
• Kodi Yesu anali chitsanzo kwa akazi m’njira yotani, ndipo kutsatira chitsanzo chake kungawapindulitse bwanji?
[Chithunzi patsamba 19]
N’chifukwa chiyani mkazi ayenera kuganiza mozama asanavomere kapena kukana kukwatiwa?
[Chithunzi patsamba 21]
Kodi akazi angaphunzire chiyani ku zitsanzo za anthu a m’Baibulo ngati Abigayeli?