-
Malangizo Anzeru kwa OkwatiranaNsanja ya Olonda—2005 | March 1
-
-
15, 16. Kodi ndi khalidwe lotani limene mkazi wachikristu angaonetse kuti asinthe mwamuna wake wosakhulupirira?
15 Kodi ndi khalidwe lotani limene lingasinthe mwamuna? Ndi khalidwe limene akazi achikristu amakhala nalo mongadi Akristu. Petro anati: “Kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golidi, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu. Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna awo a iwo okha; monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chili chonse.”—1 Petro 3:3-6.
-
-
Malangizo Anzeru kwa OkwatiranaNsanja ya Olonda—2005 | March 1
-
-
17. Kodi Sara ndi chitsanzo chabwino motani kwa akazi achikristu?
17 Sara anatchulidwa monga chitsanzo, ndipotu iyeyu ndi chitsanzodi chabwino kwa akazi okwatiwa, ngakhale amuna awo atakhala osakhulupirira. N’zosakayikitsa kuti Sara ankaona Abrahamu ngati mutu wake. Ngakhale mumtima mwake, iye ankamutcha Abrahamu kuti ‘Ambuye.’ (Genesis 18:12) Komatu zimenezi sizinamunyozetse Sarayo ayi. N’zoonekeratu kuti iye anali mkazi wolimba mwauzimu ndipo payekha, anali ndi chikhulupiriro champhamvu mwa Yehova. Inde, iyeyu ali m’gulu la ‘mtambo waukulu wa mboni’ zimene chitsanzo chawo cha chikhulupiriro chiyenera kutilimbikitsa kuti “tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” (Ahebri 11:11; 12:1) Mkazi wachikristu akakhala ngati Sara sindiye kuti akunyozeka ayi.
-