Abrahamu ndi Sara Mungatsanzire Chikhulupiriro Chawo!
MWAMUNAYO amatchedwa kuti “kholo la onse akukhulupirira.” (Aroma 4:11) Nayenso mkazi wake wokondedwa kwambiri anali ndi chikhulupiriro. (Ahebri 11:11) Tikunena za tate wa Aisrayeli Abrahamu ndi mkazi wake, Sara, ndipo onse aŵiri anali oopa Mulungu. N’chifukwa chiyani aŵiriŵa anali zitsanzo zabwino za chikhulupiriro? Kodi zina mwa ziyeso zomwe anakumana nazo zinali zotani? Ndipo kodi nkhani yofotokoza za moyo wawo ili ndi phindu lanji kwa ife?
Abrahamu anasonyeza chikhulupiro pamene Mulungu anamuuza kuti achoke kumudzi kwawo. Yehova anati: “Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe.” (Genesis 12:1) Kholo lokhulupirikali linamvera, chifukwa timauzidwa kuti: “Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka ku malo amene adzalandira ngati choloŵa; ndipo anatuluka wosadziŵa kumene akamukako.” (Ahebri 11:8) Tiyeni tione zomwe zinafunika kuti asamuke.
Abrahamu ankakhala ku Uri, komwe tsopano ndi kum’mwera kwa dziko la Iraq. Uri unali mzinda wotukuka kwambiri wa ku Mesopotamiya ndipo mzindawu unkachita malonda ndi mayiko a ku Persian Gulf ndiponso mwachionekere mayiko a kuchigwa cha mtsinje wa Indus. Bwana Leonard Woolley, amene anatsogolera ntchito yofukula mosamala kwambiri mabwinja a Uri, ananena kuti m’masiku a Abrahamu nyumba zambiri za mumzindawu zinali zomangidwa ndi njerwa, zamakoma a pulasitala ndiponso opaka laimu. Mwachitsanzo, nyumba ya nzika ina yolemera kwambiri inali yosanjikizana ndipo inali ndi bwalo limene pansi pake anamangapo ndi miyala. Nyumba ya pansi munkakhala antchito ndi alendo. Nyumba yapamwamba inali ndi khonde lamatabwa ndipo pamenepo panali makomo oloŵera m’zipinda zimene anthu a m’banjalo ankagwiritsa ntchito. Popeza nyumbazi zinkatha kukhala ndi zipinda 10 mpaka 20, zinali “zazikulu bwino zoyenerana ndi moyo wotukuka, wapamwamba ndiponso, malinga n’kuona kwa anthu a m’mayiko a Kum’maŵa panthaŵiyo, zogwirizana ndi moyo wam’tawuni,” anatero Woolley. Zinali “nyumba za anthu otukuka kwambiri ndiponso zogwirizana ndi zofunika pa moyo wotukuka zedi wam’tawuni.” Ngati Abrahamu ndi Sara anasiya nyumba yotero akudziŵa kuti azikakhala m’mahema, ndiye kuti anadzimana kwambiri pofuna kumvera Yehova.
Abrahamu choyamba anapita ndi banja lake ku Harana, mzinda wa kumpoto kwa Mesopotamiya, ndipo kenako anapita ku Kanani. Unali mtunda wa makilomita pafupifupi 1,600, umene unali ulendo wautali kwambiri kwa banja lokalamba ngati limeneli. Pamene ankachoka ku Harana, Abrahamu anali ndi zaka 75 ndipo Sara anali ndi zaka 65.—Genesis 12:4.
Kodi Sara angakhale kuti anamva bwanji Abrahamu atamuuza kuti iwo asamuka ku Uri? N’kutheka kuti anada nkhaŵa poganizira zochoka m’nyumba yabwino yotetezeka, kupita kumalo achilendo mwinanso a anthu ankhanza kwambiri, ndi kukakhala moyo wotsikirapo. Komabe, Sara anali womvera, ndipo anali kuona Abrahamu monga “mbuye” wake. (1 Petro 3:5, 6) Akatswiri ena a zamaphunziro amaona kuti Sara poona Abrahamu monga mbuye wake anasonyeza “chizoloŵezi chake ndiponso khalidwe lake lolemekeza mwamuna wake,” umene uli umboni wa “zinthu zimene anali kuganiza ndiponso wa mmene ankamvera mumtima mwake.” Koma koposa zonsezi, Sara ankakhulupirira Yehova. Kumvera ndiponso chikhulupiriro chake, ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa akazi achikristu.
N’zoona kuti sitipemphedwa kusiya nyumba yathu kuti timvere Mulungu, ngakhale kuti alaliki ena anthaŵi zonse achoka kudziko lawo n’cholinga chokalalikira uthenga wabwino kudziko lina. Mosaganizira kuti tikutumikira Mulungu kudera liti, iye adzatipatsa zosoŵa zathu malinga ngati tiika zinthu zauzimu pamalo oyamba m’moyo.—Mateyu 6:25-33.
Onse aŵiri, Sara ndi Abrahamu sanadandaule ndi zomwe anasankha kuchita. Mtumwi Paulo anati: ‘Akadakumbukira lijalo adatulukamo akadaona njira yakubwerera nayo.’ Koma sanabwerere. Pokhala ndi chikhulupiriro kuti Yehova “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye,” iwo anakhulupirira malonjezo ake. Nafenso tiyenera kutero kuti tipitirizebe kukhala odzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse.—Ahebri 11:6, 15, 16.
Chuma Chauzimu Ndiponso Chuma Chakuthupi
Abrahamu atafika ku Kanani, Mulungu anamuuza kuti: “Ndidzapatsa mbewu yako dziko lino.” Ndi mawu ameneŵa Abrahamu anamangira Yehova guwa lansembe ndi kuitanira pa “dzina la Yehova.” (Genesis 12:7, 8) Yehova analemeretsa Abrahamu, ndipo anthu amene anali kukhala naye paulendo wake anali ochuluka kwambiri. Popeza kuti nthaŵi ina anatsogolera anyamata, omwe anali akapolo obadwira kunyumba kwake okwana 318 ophunzira bwino nkhondo, ena amati “gulu lake lonse liyenera kuti linapitirira anthu chikwi chimodzi.” Sitikudziŵa kuti panali chifukwa chotani, koma anthu anali kumuona monga “kalonga wamkulu.”—Genesis 13:2; 14:14; 23:6.
Abrahamu anali kutsogolera pankhani ya kulambira, ankaphunzitsa anthu a m’nyumba yake “kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro.” (Genesis 18:19) Mitu ya mabanja achikristu masiku ano ingalimbikitsidwe ndi chitsanzo cha Abrahamu monga munthu amene zinamuyendera bwino pophunzitsa anthu a m’nyumba yake kuti azidalira Yehova ndi kuchita chilungamo. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti mdzakazi wa Sara wochokera ku Igupto, Hagara, ndi wantchito wamkulu wa Abrahamu, ndiponso mwana wamwamuna wa Abrahamu, Isake, anadalira Yehova Mulungu.—Genesis 16:5, 13; 24:10-14; 25:21.
Abrahamu Anali Wokonda Mtendere
Zochitika pamoyo wa Abrahamu zimasonyeza kuti Abrahamu anali ndi khalidwe lina lomwenso Mulungu ali nalo. M’malo molola kuti mkangano upitirire pakati pa abusa ake ndi abusa a mphwake, Loti, Abrahamu anaganiza zoti asiyane malo okhala ndipo anapempha Loti wachinyamatayo kuti asankhe dera lakukhosi kwake. Abrahamu anali wokonda mtendere.—Genesis 13:5-13.
Ngati ife titakhala ndi mwayi wosankha pakati pa kuumirira ufulu wathu kapena kukhala wololera n’cholinga choti pakhale mtendere, tingakumbukire kuti Yehova sanalole kuti Abrahamu azivutika chifukwa choti wasonyeza kuganizira Loti. Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, Mulungu pambuyo pake analonjeza Abrahamu ndi mbewu yake kuti adzawapatsa dziko lonse lomwe Abrahamu ankaliona ku mbali zonse. (Genesis 13:14-17) “Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu,” anatero Yesu.—Mateyu 5:9.
Kodi Ndani Anali Kudzaloŵa M’malo mwa Abrahamu?
Ngakhale kuti anawalonjeza kuti adzakhala ndi mbewu, Sara anakhalabe wosabereka. Abrahamu anafotokozera Mulungu nkhaniyi. Kodi wantchito wake Eliezere ndiye anali kudzatenga zonse zimene anali nazo? Ayi, chifukwa Yehova ananena kuti: “Uyu sadzakhala wakuloŵa m’malo mwako; koma iye amene adzatuluka m’chuuno mwako, ndiye adzakhala wakuloŵa m’malo mwako.”—Genesis 15:1-4.
Koma anakhalabe opanda mwana, ndipo Sara yemwe anali ndi zaka 75 analibenso chiyembekezo choti n’kukhala ndi pakati. Motero anauza Abrahamu kuti: “Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: loŵanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana.” Motero Abrahamu anatenga Hagara kukhala mkazi wake wachiŵiri, nagona naye, ndipo anakhala ndi pakati. Hagara atangozindikira kuti ali ndi pakati anayamba kupeputsa mbuye wake Sara. Sara anadandaula kwambiri kwa Abrahamu ndipo anavutitsa Hagara, mpaka mdzakaziyu anathaŵa.—Genesis 16:1-6.
Abrahamu ndi Sara anachita zomwe iwo ankaona kuti n’zothandiza, potsatira mwambo womwe unali wovomerezeka panthaŵiyo. Koma imeneyi sinali njira ya Yehova yopatsira Abrahamu mbewu. Mwina chikhalidwe chathu chingakhale ndi miyambo ina yovomerezeka nthaŵi zina, koma izi sizitanthauza kuti Yehova akugwirizana nayo. Mmene iye akuonera zimene zikutichitikira zingasiyane kwambiri ndi mmene ife tikuzionera. Motero tifunika kufunafuna malangizo a Mulungu, ndi kupemphera kuti atisonyeze zimene iye akufuna kuti tichite.—Salmo 25:4, 5; 143:8, 10.
Palibe “Chinthu Chom’laka Yehova”
M’kupita kwa nthaŵi, Hagara anabalira Abrahamu mwana wamwamuna amene anam’patsa dzina lakuti Ismayeli. Koma iye sanali Mbewu yolonjezedwayo. Sara ndiye anali kudzabereka woloŵa m’malo ameneyo, ngakhale kuti anali atakalamba.—Genesis 17:15, 16.
Mulungu atanena kuti Sara adzabalira mwamuna wake mwana wamwamuna, “Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m’mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anayi adzabala?” (Genesis 17:17) Mngelo atabwereza mawu ameneŵa Sara akumva, zinapangitsa Sara ‘kuseka mu mtima mwake.’ Koma palibe “chinthu chom’laka Yehova.” Tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti iye angathe kuchita chilichonse chomwe akufuna.—Genesis 18:12-14.
Chinali ‘chikhulupiriro chomwe chinachititsa Sara kulandira mphamvu yakukhala ndi pakati, nthaŵi yake itapitirira, popeza anamuŵerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza.’ (Ahebri 11:11) M’kupita kwa nthaŵi Sara anabereka Isake, amene dzina lake limatanthauza “Kuseka.”
Kukhulupirira Malonjezo a Mulungu Kotheratu
Yehova anasonyeza kuti Isake ndiye anali woloŵa m’malo amene anali kuyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali. (Genesis 21:12) Motero Abrahamu ayenera kuti anadabwa pamene Mulungu anamuuza kuti akapereke mwana wakeyo nsembe. Komabe Abrahamu anali ndi zifukwa zokwanira zokhulupirira Mulungu kotheratu. Kodi Yehova sakanatha kuukitsa Isake kwa akufa? (Ahebri 11:17-19) Kodi poyamba paja, Mulungu sanasonyeze mphamvu zake mwa kubwezeretsa mphamvu zoberekera mwa Abrahamu ndi Sara n’cholinga choti abereke Isake? Pokhulupirira kuti Mulungu angathe kukwaniritsa malonjezo Ake, Abrahamu anali wokonzeka kumvera. N’zoona kuti analetsedwa kuphadi mwana wakeyo. (Genesis 22:1-14) Komabe, zimene Abrahamu anachita pankhaniyi zimatithandiza kuona mmene zinalili zovuta kwa Yehova Mulungu kuti ‘apatse Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.’—Yohane 3:16; Mateyu 20:28.
Chifukwa chokhulupirira Mulungu, Abrahamu anazindikira kuti munthu wodzalandira malonjezo a Yehovayo sanayenera kukwatira mkazi wa m’dziko la Kanani wolambira milungu yonyenga. Kodi kholo loopa Mulungu lingavomereze bwanji kuti mwana wake akwatire kapena kukwatiwa ndi munthu wosatumikira Yehova? Motero Abrahamu anakafunira Isake mkazi wabwino kwa abale ake ku Mesopotamiya, mtunda wa makilomita oposa 800. Mulungu anadalitsa zimenezo mwa kusonyeza kuti iye wasankha Rebeka kuti akhale mkazi wa Isake ndi kholo lalikazi la Mesiya. Zoonadi, Yehova “anadalitsa Abrahamu m’zinthu zonse.”—Genesis 24:1-67; Mateyu 1:1, 2.
Madalitso ku Mitundu Yonse
Abrahamu ndi Sara anasonyeza chitsanzo chabwino popirira mayesero ndiponso pokhulupirira malonjezo a Mulungu. Kukwaniritsidwa kwa malonjezo amenewo kukukhudza tsogolo la anthu, chifukwa Yehova anatsimikizira Abrahamu kuti: “M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mawu anga.”—Genesis 22:18.
N’zoona kuti Abrahamu ndi Sara anali opanda ungwiro, monganso momwe ife tilili. Koma iwo ankati akamvetsa chomwe Mulungu akufuna, ankamvera mosanyinyirika, mosaganizira kuti pafunika kuchita zinthu zotani. Motero Abrahamu amakumbukiridwa monga “bwenzi la Mulungu” ndipo Sara amakumbukiridwa monga ‘mkazi woyera mtima, wakuyembekezera Mulungu.’ (Yakobo 2:23; 1 Petro 3:5) Mwa kuyesetsa kutsanzira chikhulupiriro cha Abrahamu ndi Sara, nafenso tingakhale paubwenzi wamtengo wapatali ndi Mulungu. Tingapindulenso ndi malonjezo amtengo wapatali amene Yehova analonjeza Abrahamu.—Genesis 17:7.
[Chithunzi patsamba 26]
Chifukwa chakuti Abrahamu ndi Sara anali ndi chikhulupiriro, Yehova anawadalitsa ndi mwana muukalamba wawo
[Chithunzi patsamba 28]
Chitsanzo cha Abrahamu chimatithandiza kuona mmene Yehova zinamukhudzira polola kuti Mwana wake wobadwa yekha afe