Kodi Mumawalemekeza?
ATASONKHANITSIDWA monga nyama ndi kupakiridwa m’malo auve ndiponso onunkha kwadzaoneni, eni nthaka ya Afirika anatengedwa monga katundu wamba kupita ku maiko a ku America. Pafupifupi theka la chiŵerengero chawo anayembekezeredwa kufa asanafike nkomwe kumene akupita. Apabanja limodzi analekanitsidwa mwankhanza, ndipo sanaonanenso. Malonda ogulitsa akapolo anali amodzi mwa nkhanza zoipa koposa zimene munthu wachitira munthu mnzake. Nkhanza zina ngati zimenezi zinachitika pamene ogonjetsa amphamvu anazunza eni maiko opanda chitetezo chilichonse.
Kuvula munthu ulemu wake kungakhale nkhanza yaikulu kuposa kummenya kwenikweni. Kumaswa mzimu wa munthu. Ngakhale kuti ukapolo unatha m’maiko ambiri, kuvula anthu ulemu wawo kukupitirizabe, mwinamwake m’njira zovuta kuzizindikira.
Komabe, Akristu oona, amayesetsa kutsatira uphungu wa Yesu Kristu wonena za ‘kukonda mnansi wawo monga iwo eni.’ Choncho amadzifunsa kuti, ‘Kodi ndimalemekeza anthu ena?’—Luka 10:27.
Chitsanzo cha Kulemekezeka
Kulemekezeka, malinga ndi kunena kwa dikishonale ina, ndiwo mkhalidwe wa kukhala wofunika, wolemekezeka kapena wokwezeka. Mawuwo ali mafotokozedwe oyenerera chotani nanga a malo a Mfumu Yachilengedwe Chonse, Yehova Mulungu! Kwenikweni, mobwerezabwereza pamene Malemba amafotokoza za Yehova ndi uchifumu wake, iwo amasonyeza kulemekezeka kwake. Mose, Yesaya, Ezekieli, Danieli, mtumwi Yohane, ndi ena anali ndi mwaŵi wopatsidwa masomphenya ouziridwa osonyeza Wam’mwambamwambayo ndi mabwalo ake akumwamba, ndipo nthaŵi zonse mafotokozedwe awo anasonyeza ulemerero wauchifumu wochitisa nthumanzi ndi kulemekezeka. (Eksodo 24:9-11; Yesaya 6:1; Ezekieli 1:26-28; Danieli 7:9; Chivumbulutso 4:1-3) M’pemphero lomtamanda, Mfumu Davide anati: “Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse za m’mwamba ndi zapadziko lapansi ndi zanu.” (1 Mbiri 29:11) Ndithudi, palibe amene ali woyenerera ulemerero ndi kukwezeka kuposa mmene Yehova Mulungu iyemwini alili.
Polenga munthu m’chifanizo ndi m’chikhalidwe chake, Yehova anagaŵira anthu mlingo wina wa kufunika, kudzilemekeza, ndi kulemekezeka. (Genesis 1:26) Choncho, pochita zinthu ndi ena, tiyenera kupereka ulemu woyenerera kwa munthu aliyense. Tikachita zimenezo, ndiye kuti, kwenikweni, tikulemekeza Magwero a kulemekezeka kwa anthu, Yehova Mulungu.—Salmo 8:4-9.
Ulemu m’Maunansi a m’Banja
Mouziridwa, mtumwi Petro, amene anali mwamuna wokwatira, analangiza amuna achikristu okwatira kuti azichitira akazi awo “ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu.” (1 Petro 3:7; Mateyu 8:14) “Ndipo mkaziyo,” analangiza motero mtumwi Paulo, “akumbukire kuti aziwopa mwamuna.” (Aefeso 5:33) Choncho, mu ukwati, ulemu kwa mnzako ndi chofunika cha m’Baibulo. Kodi zimenezi zingasonyezedwe motani?
Monga momwe madzi amapatsira nyonga chomera chomwe chikukula, mawu okoma ndi majesichala abwino pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, poyera ndiponso kwaokha, zingakulitse unansi wawo wathithithi. Mosiyana ndi zimenezo, mawu oipa ndiponso otukwana kapena kusuliza kopanda ulemu ndiponso konyonza, monga komwe kumamveka m’nthabwala za pa TV, nkowononga. Kungayambitse malingaliro odzimva kukhala wopanda pake, kuchita tondovi, ndi kuipidwa; ndiponso kungapweteke mtima, wovuta kuuchiritsa.
Kulemekeza ena kumatanthauzanso kuwalandira monga momwe alili, kusayesa kuwaloŵetsa mumkhalidwe wina womwe tinkawaganizira poyamba kapena kuwayerekezera ndi ena mosayenerera. Zimenezi nzofunika kwambiri makamaka pakati pa amuna ndi akazi awo. Pamene pali kulankhulana ndi kuchitirana zinthu momasuka ndiponso mosavuta ndiponso pamene palibe amene akuwopa kudzudzulidwa kapena kusulizidwa, unansi wathiththi umakula. Pamene munthu amatha kukhala mu ukwati monga momwe alili, panyumba pamakhaladi pothaŵira dziko lankhanza ndi lopanda ulemu kunjaku.
Ana akulamulidwa ndi Malemba kuti ayenera kulemekeza ndi kumvera makolo awo. Komanso, makolo anzeru ndiponso achikondi angachite bwino kulemekeza ana awo. Kuwayamikira mwachikondi pakhalidwe lawo labwino, pamodzinso ndi chilango choperekedwa moleza mtima ngati nchofunika, kumathandiza kwambiri kusungitsa “chilangizo cha Ambuye.” Kuwadzudzula nthaŵi zonse, kuwakalipira, ndi kuwaitana maina onyoza pamodzi ndi mawu opweteka monga akuti “wopusa” kapena “chitsiru” kudzangowakwiyitsa.—Aefeso 6:4.
Mkulu wina wachikristu amenenso ali atate, amene akulera ana aamuna atatu ndi ana aakazi atatu, akuti: “Ku Nyumba ya Ufumu, tinali kupereka chilango chofunika mwakachetechete kwambiri. Kukodola pang’ono kapena kutuzula maso monga chenjezo nthaŵi zambiri kunali kokwanira. Ngati panafunikira chilango chachikulu, tinali kuchiperekera mseri kunyumba kwathu kutali ndi ana ena. Tsopano pamene anawa akula, chilango chimaphatikizapo kupatsa aliyense uphungu wachikondi ndi wanzeru wochokera m’Mawu a Mulungu malinga ndi zosoŵa za aliyense payekha. Timayesetsa kusunga chinsinsi pankhani zaumwini zimenezi, choncho timalemekeza ufulu wa mwana aliyense wa kusunga chinsinsi ndi kumpatsa ulemu.”
Kufunikira kwa khalidwe labwino m’mawu ndi m’zochita m’banja nkofunika. Kuzoloŵerana sikuyenera kuiŵalitsa mawu onga akuti “zikomo,” “pepani,” ndi “khululukireni.” Khalidwe labwino nlofunika kwambiri pofuna kudzisungira ulemu ndiponso polemekeza ena.
Mumpingo Wachikristu
“Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu,” anatero Yesu. (Mateyu 11:28) Othodwa, ochita tondovi, ngakhale ana aang’ono, onse anali kukopeka ndi Yesu mosaletseka. Iwo anali kunyodoledwa ndi atsogoleri achipembedzo ndi olamulira odzikuza ndiponso odzilungamitsa okha a m’nthaŵiyo. Koma anapeza kuti Yesu anali kuwapatsa ulemu wawo woyenerera.
Motsanzira Yesu, ifenso tiyenera kukhala otsitsimula okhulupirira anzathu. Zimenezi zimatanthauza kufunafuna mpata woti tiwamangirire mwa zonena ndi zochita zathu. Nkoyenera kukhala wokonda kunena mawu okoma ndiponso olimbikitsa moona mtima pokambitsirana ndi ena. (Aroma 1:11, 12; 1 Atesalonika 5:11) Timasonyeza kuti tikuzindikira malingaliro a ena mwa kusamala zomwe tikunena ndi momwe tikuzinenera. (Akolose 4:6) Kuvala bwino ndiponso udongo pamisonkhano yachikristu kumasonyezanso kuti tikupereka ulemu waukulu kwa Mulungu wathu, kulambira kwake, ndiponso kwa olambira anzathu.
Yesu anali kulemekeza anthu ngakhale powachitira zinthu. Iye sanadzikweze mwa kuwanyalanyaza kapena mwa kuwachititsa manyazi. Pamene wakhate anadza kwa iye akumapempha kuti amchiritse, Yesu sanapitikitse mwamunayo kuti ndi wodetsedwa ndiponso wopanda pake, ndiponso sanadzionetsere mwa kudzikweza. M’malo mwake, pamene wakhateyo anapempha Yesu kuti, “Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza,” Iye anamlemekeza wakhateyo mwa kunena kuti, “Ndifuna.” (Luka 5:12, 13) Nkosangalatsa chotani nanga kwa ife kuti tisamangothandiza chabe osoŵa komanso tiziwatsimikizira kuti siali mtolo koma timawafuna ndiponso timawakonda! Amanyazi, ochita tondovi, ndi opunduka nthaŵi zambiri amawanyalanyaza, kuwapeŵa, kapena kuwanyoza m’dzikoli. Koma akakhala pakati pa abale ndi alongo awo achikristu, iwo ayenera kupeza ubwenzi weniweni ndi kulandiridwa. Tiyenera kuchita mbali yathu kuti tithandizire mzimu umenewu.
Yesu anakonda ophunzira ake monga “ake a Iye yekha” ndipo “anawakonda kufikira chimaliziro” mosasamala kanthu za zophophonya zawo ndi maumunthu awo. (Yohane 13:1) Anawaona kukhala a mitima yoona ndipo odzipereka ndi mtima wonse kwa Atate wake. Momwemonso, sitiyenera konse kuona monga kuti alambiri anzathu ali ndi zolinga zoipa chabe chifukwa chakuti mwina sakuchita zinthu mmene ifeyo timazichitira kapena chifukwa chakuti zochita zawo kapena umunthu wawo umatikwiyitsa. Kulemekeza abale athu kudzatisonkhezera kuwakonda ndi kuwalandira monga momwe alili, tikumakhulupirira kuti iwonso amakonda Yehova ndipo akumtumikira ndi zolinga zabwino.—1 Petro 4:8-10.
Makamaka, akulu, ayenera kusamala kwambiri kuti sakudetsa nkhaŵa mosayenerera anthu amene aikizidwa kwa iwo kuti awasamalire. (1 Petro 5:2, 3) Pokambitsirana ndi wa mumpingo amene wachimwa, kungakhale bwino kuti akulu azilankhula mwachifundo ndiponso momganizira ndi kupeŵa kufunsa mosayenerera mafunso ochititsa manyazi. (Agalatiya 6:1) Ngakhale ngati pakufunika chidzudzulo kapena chilango champhamvu, iwo adzayenera kupitirizabe kupereka ulemu woyenerera kwa wochimwayo.—1 Timoteo 5:1, 2.
Kudzisungira Ulemu
Pokhala tinalengedwa m’chifanizo ndi m’chikhalidwe cha Mulungu, tiyenera kusonyeza, pamlingo umene tingathe, mikhalidwe yapamwamba ya Mulungu—kuphatikizapo kulemekezeka kwake—pamoyo wathu watsiku ndi tsiku. (Genesis 1:26) Mofananamo, m’lamulo lakuti “uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini” mukuonekera kufunika kwa kudzilemekeza kolinganizika bwino. (Mateyu 22:39) Choonadi nchakuti ngati tikufuna kuti ena atisonyeze ulemu ndi kutilemekeza, tiyenera kusonyeza kuti ndife oyenerera zimenezo.
Chofunika kwambiri pofuna kudzisungira ulemu ndicho kusunga chikumbumtima choyera. Chikumbumtima chodetsedwa ndiponso kusautsidwa mtima ndi liwongo zimachititsa mosavuta kudzimva kukhala wopanda pake, kukhumudwa, ndi kuchita tondovi. Chotero, ngati munthu wachita tchimo lalikulu, ayenera kuchitapo kanthu mwamsanga kuti alape ndi kufunafuna thandizo lauzimu la akulu kuti iye akhale ndi “nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye.” Kutsitsimutsa kumeneko kukuphatikizapo kubwezeretsa kudzilemekeza.—Machitidwe 3:19.
Kuli bwino kwambiri panopo kuyesetsa mosalekeza kutetezera chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo, osalola kalikonse kuchidetsa kapena kuchifooketsa. Kudziletsa pambali zonse za moyo wathu watsiku ndi tsiku—pakudya, kumwa, pochita malonda, zosangulutsa, pochita zinthu ndi osiyana nawo ziŵalo—kudzatithandiza kukhala ndi chikumbumtima choyera ndi kutipangitsa kusonyeza ulemerero ndi ulemu wa Mulungu pamoyo wathu.—1 Akorinto 10:31.
Bwanji ngati liwongo pa zolakwa zathu silikuchepa? Kapena bwanji ngati nkhanza zimene ena anatichitira zikupitirizabe kutipweteka mtima tikazikumbukira? Malingaliro ameneŵa angaswe ulemu wathu ndi kutichititsa tondovi kwambiri. Mawu a Mfumu Davide opezeka pa Salmo 34:18 ngotonthoza chotani nanga! Iwo amati: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi”! Yehova ali wokonzekera ndiponso wofunitsitsa kulimbitsa atumiki ake pamene akulimbana ndi kuchita tondovi ndiponso ndi malingaliro odzimva kukhala opanda pake. Mapembedzero kwa iye limodzinso ndi kufunafuna thandizo la awo amene ali ndi ziyeneretso zauzimu, monga makolo achikristu, akulu, ndi enanso okhwima mumpingo, ndiyo njira yobwezeretsera ulemu waumwini.—Yakobo 5:13-15.
Komanso, tiyenera kusamala kwambiri kuti sitikudumpha mzere wosiyanitsa kudzilemekeza ndi kudzitukumula. Uphungu wa m’Malemba ndiwo ‘kusadziyesa koposa kumene uyenera kudziyesa; koma kuganiza modziletsa wekha, monga Mulungu anagaŵira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.’ (Aroma 12:3) Pamene kuli kwakuti kukulitsa ulemu wathu nkoyenera, sitiyenera kukokomeza kufunika kwathu kapena kusokoneza pakati pa kulemekezeka kwaumunthu ndi kuyesayesa kodzikonda ndiponso konkitsa kumene ena amachita kuti adzikweze pamaso pa ena.
Inde, kulemekeza ena kuli chofunika chachikristu. A m’banja lathu ndiponso Akristu anzathu onse ngoyenerera ulemu wathu, ndi kukwezeka. Yehova wapatsa aliyense wa ife mlingo wina wa ulemu umene tiyenera kusonyeza ndi kusunga. Koma chofunika kwambiri pazonse, tiyenera kukhala ndi ulemu waukulu kwambiri ku uchifumu waukulu koposa wa Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu.
[Chithunzi patsamba 31]
Achichepere angasonyeze ulemu kwa opunduka