Kumwamba
Tanthauzo: Malo okhala Yehova Mulungu ndi zolengedwa zauzimu zokhulupirika; chigawo chosawoneka ndi maso aumunthu. Baibulo limagwiritsiranso ntchito liwu lakuti “kumwamba” m’malingaliro ena osiyanasiyana; mwachitsanzo: Kuimira Mulungu mwiniyo, gulu lake la zolengedwa zauzimu zokhulupirika, malo a chiyanjo cha Mulungu, chilengedwe chakuthupi chosaphatikizapo dziko lapansi, m’mlengalenga mozungulira planetili Dziko Lapansi, maboma aumunthu otsogozedwa ndi Satana, ndi boma latsopano lolungama lakumwamba m’limene Yesu Kristu limodzi ndi oloŵa nyumba anzake apatsidwa mphamvu ndi Yehova kulamulira.
Kodi tonsefe tinayamba takhala m’chigawo chamizimu tisanabadwe monga anthu?
Yoh. 8:23: “[Yesu Kristu anati] Inu ndinu ochokera pansi; ine ndine wochokera kumwamba; inu ndinu a m’dziko lino lapansi; sindiri ine wa dziko lino lapansi.” (Yesu anachokera ku malo a mizimu. Koma monga momwe Yesu adanenera, anthu anewo sanatero.)
Aroma 9:10-12: “Rebeka anakhala ndi pakati pa amapasa . . . asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, sichifukwa cha ntchito ayi, koma chifukwa cha wakuitananiyo, chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.” (Ndithudi, ngati amapasa Yakobo ndi Esau anali atakhala ndi moyo kalelo m’malo a mizimu iwo akanakhaladi ndi cholembedwa chozikidwa pamkhalidwe wawo kumeneko, kodi sichoncho? Koma analibe cholembedwa chotero kufikira pambuyo pa kubadwa kwawo monga anthu.)
Kodi anthu onse abwino amapita kumwamba?
Mac. 2:34: “Davide [amene Baibulo limamtchula kukhala ‘mwamuna wovomerezedwa mu mtima wa Yehova’] sanakwera kumwamba ayi.”
Mat. 11:11: “Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.” (Chotero Yohane sanapite kumwamba pamene anafa.)
Sal. 37:9, 11, 29: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. . . . Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”
Ngati Adamu sakanachimwa, kodi iye potsirizira pake akanapita kumwamba?
Gen. 1:26: “Anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m’nyanja ndi pambalame za m’mlengalenga, ndi pang’ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pa zokwaŵa zonse zakukwaŵa padziko lapansi.” (Chotero, chifuno cha Mulungu kwa Adamu chinali chakuti akhale wosamalira dziko lapansi ndi kusamalira zinyama mmenemo. Palibe zimene zanenedwa ponena za kupita kwake kumwamba.)
Gen. 2:16, 17: “Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Sichinali chifuno choyambirira cha Yehova kuti tsiku lina munthuyo akafe. Lamulo la Mulungu logwidwa mawu panopa limasonyeza kuti anachenjeza motsutsana ndi njira imene ikatsogolera ku imfa. Imfa inali kudzakhala chilango cha kusamvera, koma osati khomo loloŵera kumoyo wabwino kwambiri kumwamba. Kumvera kukanafupidwa ndi moyo wopanda mapeto, moyo wamuyaya, m’Paradaiso amene Mulungu adapereka kwa munthu. Wonaninso Yesaya 45:18.)
Kodi munthu ayenera kupita kumwamba kuti akhaledi ndi mtsogolo mwachimwemwe?
Sal. 37:11: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”
Chiv. 21:1-4, NW: “Ndinawona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano . . . Ndinamva mawu ofuula ochokera kumpando wachifumu akuti: ‘Tawonani! Chihema cha Mulungu chiri ndi anthu, ndipo iye adzakhala pamodzi ndi iwo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Ndipo Mulungu mwiniyo adzakhala limodzi nawo. Ndipo iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo sikudzakhalanso imfa, ngakhale kulira maliro ngakhale kufuula ngakhale kupweteka sizidzakhalakonso. Zinthu zoyambazo zapita.’”
Mika 4:3, 4: “Mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wa kuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wamukamu padanena.”
Kodi Yesu anatsegula njira yakumwamba kaamba ka awo amene anali atafa imfa yake isanachitike?
Kodi nchiyani chimene 1 Petro 3:19, 20 amatanthauza? “Mmenemonso [mu mzimu, pambuyo pa chiukiriro chake] anapita [Yesu], nalalikira mizimu inali m’ndende, imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzekera chingalaŵa, mmenemo oŵerengeka, ndiwo amoyo [“miyoyo,” KJ, Dy; “anthu,” TEV, JB; “anthuwo,” RS], asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi.” (Kodi ‘mizimu imene inali m’ndende’ inali miyoyo ya anthu aja amene adakana kulabadira kulalikira kwa Nowa Chigumula chisanakhale, ndipo kodi tsopano njira inawatsegukira yopitira kumwamba? Kuyerekezera 2 Petro 2:4 ndi Yuda 6 ndi Genesis 6:2-4 kumasonyeza kuti mizimu imeneyi inali ana aungelo a Mulungu amene anavala matupi nakwatira m’tsiku la Nowa. Pa 1 Petro 3:19, 20 liwu Lachigiriki la “mizimu” ndilo pneuʹma·sin, pamene liwu lotembenuzidwa kuti “miyoyo” ndilo psy·khaiʹ. “Mizimuyo” sinali mizimu yovula matupi koma angelo osamvera; “miyoyo” yotchulidwa panopa inali anthu amoyo, anthu enieni, Nowa ndi banja lake. Chifukwa chake zimene zinalalikidwa ku “mizimu ya m’ndende” ziyenera kukhala uthenga wachiŵeruzo.)
Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la 1 Petro 4:6? “Pakuti chifukwa cha ichi walalikidwa uthenga wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaŵeruzidwe monga mwa anthu m’thupi koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu.” (Kodi “akufa” amenewa anali anthu amene anali atafa imfa ya Kristu isanachitike? Monga momwe kwasonyezedwera kale, akufa saali “mizimu m‘ndende.” Mizimu imeneyo inali angelo osamvera. Ndipo kulalikira sikukanapindulitsa mwakuthupi anthu akufa chifukwa chakuti monga momwe Mlaliki 9:5 amanenera, iwo “sadziŵa kanthu bi,” ndipo Salmo 146:4 imawonjezera kuti pa imfa ‘zolingalira za munthu ziwonongeka.’ Koma Aefeso 2:1-7, 17 amatchula anthu amene anali akufa mwauzimu ndi amene anakhala ndi moyo mwauzimu chifukwa cha kuvomereza mbiri yabwino.)
Kodi moyo wakumwamba watchulidwa mu “Chipangano Chatsopano” kukhala chiyembekezo cha Akristu onse?
Yoh. 14:2, 3: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha; kuti kumene kuli ineko, mukakhale inunso.” (Panopa Yesu akusonyeza kuti atumwi ake okhulupirika, amene anali kulankhula nawo, m’nthaŵi yokwanira, akakhala, mu “nyumba” ya Atate wake, kumwamba, limodzi ndi Yesu. Koma iye panopa sakusonyeza kuchuluka kwa ena amene akapitanso kumwamba.)
Yoh. 1:12, 13: “Onse amene anamlandira iye [Yesu], kwa iwo anapatsa mphamvu ya kukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.” (Tawonani kuti mawu apatsogolo ndi pambuyo, m’vesi 11, akusonyeza kwa ‘anthu ake amwini yekha’ a Yesu, Ayuda. Ochuluka a iwo amene anamlandira pamene anadza kwa iwo m’zaka za zana loyamba anakhala ana a Mulungu, okhala ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba. Aneniwo m’lembali ali mu mpangidwe wanthaŵi yapita, chotero mavesi sakusonya kwa anthu onse amene akhala Akristu kuyambira nthaŵiyo.)
Aroma 8:14, 16, 17: “Onse amene atsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso oloŵa nyumba; inde oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi iye.” (Panthaŵi imene mawuwa analembedwa zinalidi choncho kuti onse amene anatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu anali ana a Mulungu amene chiyembekezo chawo chinali chakuti akalemekezedwa limodzi ndi Kristu. Koma izi sizinakhale choncho nthaŵi zonse. Luka 1:15 amanena kuti Yohane Mbatizi akadzadzidwa ndi mzimu woyera, koma Mateyu 11:11 amasonyeza momvekera bwino kuti iye sadzakhala ndi phande mu ulemerero wa Ufumu wakumwamba. Choteronso, pambuyo pa kusonkhanitsa oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba, pakakhala ena amene akatumikira monga otsatira a Mwana wake ndipo komabe osakhala ndi mbali mu ulemerero wakumwamba.)
Kodi ndimalemba enieni otani amene ali mu “Chipangano Chatsopano” osonyeza kakonzedwe kakuti Akristu akafupidwa moyo wamuyaya padziko lapansi?
Mat. 5:5: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.”
Mat. 6:9, 10: “Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Kodi nchiyani chimene chiri chifuniro cha Mulungu ponena za dziko lapansi? Kodi nchiyani chimene Genesis 1:28 ndi Yesaya 45:18 amasonyeza?)
Mat. 25:31-33, 40, 46: “Pamene Mwana wa munthu adzadza muulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu amitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere. . . . Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo [nkhosa], Indetu ndinena kwa inu, chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale aang’onong’ono awa, munandichitira ichi ine. Ndipo amenewa [mbuzi] adzachoka kumka ku chilango chanthaŵi zonse; koma olungama [nkhosa] kumoyo wanthaŵi zonse.” (Tawonani kuti “nkhosa” zimenezi siziri anthu amodzimodziwo ndi abale a Mfumu, amene ali “olandirana maitanidwe akumwamba.” [Aheb. 2:10–3:1] Koma onga nkhosa amenewa akakhala ndi moyo mkati mwa nthaŵi imene Kristu anali pa mpando wake wachifumu m’nthaŵi pamene ena a “abale” ake akakhala akuvutitsidwabe padziko lapansi.)
Yoh. 10:16: “Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola iri; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Kodi “nkhosa zina” zimenezi ndizo ayani? Ndizo otsatira a Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, koma siziri m’khola lankhosa la “pangano latsopano,” okhala ndi chiyembekezo chakumwamba. Komabe izo zikusonkhanitsidwa mwathithithi ndi awo amene ali m’khola lankhosa limenelo.)
2 Pet. 3:13, NW: “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene tikuyembekezera monga mwa lonjezo lake, ndipo mmenemu mudzakhala chilungamo.” (Ndiponso Chivumbulutso 21:1-4)
Chiv. 7:9, 10, NW: “Zitatha zinthu izi [mtumwi Yohane atawona chiŵerengero chokwanira cha “oikidwa chizindikiro” amene anali “ogulidwa kuchokera kudziko” kukakhala ndi Kristu pa Phiri la Ziyoni wakumwamba; wonani Chivumbulutso 7:3, 4; 14:1-3] ndinawona, ndipo, tawonani! khamu lalikulu limene palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, lochokera m’mitundu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, lirinkuimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, lovala miinjiro yoyera; ndipo m’manja mwawo munali makhwatha a kanjedza. Ndipo amafuula ndi mawu aakulu, kumati: ‘Chipulumutso tikuchipeza kwa Mulungu wathu, amene wakhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’”
Kodi ndiangati amene Baibulo limanena kuti ali ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba?
Luka 12:32:, NW: “Musawope, kagulu kankhosa, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.”
Chiv. 14:1-3: “Ndinapenya, tawonani, Mwanawankhosayo [Yesu Kristu] alinkuimirira pa phiri la Ziyoni [kumwamba; wonani Ahebri 12:22-24], ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pawo. . . . Ndipo aimba ngati nyimbo yatsopono . . . ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimbo, koma zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, ogulidwa kuchokera kudziko.”
Kodi 144 000 ali Ayuda akuthupi okha?
Chiv. 7:4-8: “Ndipo ndinamva chiŵerengero cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anayi mphambu anayi, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israyeli. . . . la Yuda . . . la Rubeni . . . la Gadi . . . la Aseri . . . la Nafitali . . . la Manase . . . la Simeoni . . . la Levi . . . la Isakara . . . la Zebuloni . . . la Yosefe . . . la Benjamini.” (Awa sangakhale mafuko a Israyeli wakuthupi chifukwa kunalibe konse fuko la Yosefe, fuko la Efraimu ndi la Dani sakuphatikizidwa mu mpambowu panopo, ndipo Alevi anapatulidwa kaamba ka utumiki wa pakachisi koma sanali kuŵeregeredwa monga limodzi la mafuko 12. Wonani Numeri 1:4-16.)
Aroma 2:28, 29: “Saali Myuda amene akhala wotero pamaso, kapena, suuli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mu mtima; ndipo mdulidwe uli wamtima, mu mzimu, sim’malembo ayi.”
Agal. 3:26-29: “Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwachikhulupiriro cha mwa Yesu Kristu. . . . Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu. Koma ngati muli a Kristu, muli mbewu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.”
Kodi chiŵerengero cha 144 000 nchophiphiritsira chabe?
Yankho lasonyezedwa ndi chenicheni chakuti, pambuyo pa kutchula chiŵerengero chenicheni cha 144 000, Chivumbulutso 7:9 chimasonya ku “khamu lalikulu limene palibe munthu anakhoza kuliŵerenga.” Ngati chiŵerengero cha 144 000 sichinali chenicheni chikanakhala chopanda tanthuzo pochiyerekezera ndi “khamu lalikulu.” Kuwona chiŵerengerocho kukhala chenicheni kumagwirizana ndi mawu a Yesu pa Mateyu 22:14 onena za Ufumu wakumwamba akuti: “Oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndi oŵerengeka.”
Kodi a “khamu lalikulu” otchulidwa pa Chivumbulutso 7:9, 10 amapitanso kumwamba?
Chivumbulutso sichimanena motero za iwo, monga momwe chimanenera ndi 144 000, kuti ali “ogulidwa kuchokera kudziko” kukakhala ndi Kristu pa Phiri la Ziyoni wakumwamba.—Chiv. 14:1-3.
Malongosoledwe awo a “kuimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa” amasonyeza, osati kwenikweni malo, koma mkhalidwe wovomerezedwa. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 6:17; Luka 21:36.) Liwu lakuti “pamaso pa mpando wachifumu” (Chigiriki, e·noʹpi·on tou throʹnou; kwenikweni limatanthauza, “mowonedwa ndi mpando wachifumu”) samafunikira kuti akhale kumwamba. Malo awo ali kokha “owonedwa” ndi Mulungu, amene amatiuza kuti kuchokera kumwambako iye amawona ana a anthu.—Sal. 11:4; yerekezerani ndi Mateyu 25:31-33; Luka 1:74, 75; Machitidwe 10:33.
“Khamu lalikulu kumwamba” lotchulidwa pa Chivumbulutso 19:1, 6 siliri limodzimodzilo ndi “khamu lalikulu” la pa Chivumbulutso 7:9. Awo akumwamba samafotokozedwa kukhala “ochokera ku mafuko onse” kapena onena kuti chipulumutso chawo chikuchokera kwa Mwanawankhosa; amenewa ndiwo angelo. Liwu lakuti “khamu lalikulu” likugwiritsiridwa ntchito mwanjira zosiyanasiyana m’mawu apatsogolo ndi pambuyo m’Baibulo.—Marko 5:24; 6:34; 12:37.
Kodi nchiyani chimene opita kumwambawo adzachita kumeneko?
Chiv. 20:6: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.” (Ndiponso Danieli 7:27)
1 Akor. 6:2: “Kodi simudziŵa kuti oyera mtima adzaŵeruza dziko lapansi?”
Chiv. 5:10: “Mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu [“pa,” RS, KJ, Dy; “pamwamba pa,” AT, Da, Kx, CC] padziko.” (Liwu Lachigiriki lofananalo ndi mpangidwe wa gramala wofananawo ukupezedwa pa Chivumbulutso 11:6. Pamenepo RS, KJ, Dy, ndi ena otero, onsewo amalitembenuza kuti “pamwamba pa.”)
Kodi ndani amene amasankha amene adzapita kumwamba?
2 Ates. 2:13, 14: “Tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha mzimu ndi chikhulupiriro cha chowonadi; kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Kristu.”
Aroma 9:6, 16: “Onse a kuchokera kwa Israyeli siali Israyeli . . . sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.”