Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’makalata a Yakobe ndi Petulo
PATADUTSA zaka pafupifupi 30 kuchokera pa Pentekosite mu 33 C.E., mtumwi Yakobe, yemwe anali m’bale wake wa Yesu, analemba kalata yopita ku “mafuko 12” a Isiraeli wauzimu. (Yak. 1:1) Cholinga cha kalata yake chinali kuwalimbikitsa kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti apirire poyesedwa. Iye anafunanso kupereka malangizo othandiza pa mavuto amene anali m’mipingo.
Mu 64 C.E., kutangotsala pang’ono kuti wolamulira wachiroma dzina lake Nero ayambe kuzunza Akhristu, mtumwi Petulo analembera Akhristuwo kalata yake yoyamba pofuna kuwalimbikitsa kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Atalemba kalatayi, panangopita nthawi yochepa ndipo analemba kalata yachiwiri. M’kalata yachiwiriyi Petulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti azitsatira Mawu a Mulungu ndiponso anawachenjeza za Tsiku la Yehova. Ifenso tingapindule kwambiri tikamaganizira mosamala uthenga umene uli m’makalata a Yakobe ndi Petulo.—Aheb 4:12.
MULUNGU AMAPEREKA NZERU KWA AMENE ‘AMAMUPEMPHA NDI CHIKHULUPIRIRO’
Yakobe analemba kuti: “Ali wosangalala munthu wopirira mayesero, chifukwa akadzavomerezedwa, adzalandira kolona wa moyo.” Yehova amapereka nzeru yothandiza kupirira mayesero kwa anthu ‘amene amamupempha ndi chikhulupiriro.’—Yak. 1:5-8, 12.
“Aphunzitsi” mumpingo ayenera kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso nzeru. Yakobe atafotokoza kuti lilime ndi “kachiwalo kakang’ono” kamene kamatha ‘kudetsa thupi lonse,’ anachenjezanso kuti m’pofunika kusamala ndi makhalidwe a m’dzikoli amene angasokoneze ubale wathu ndi Mulungu. Iye anafotokozanso zinthu zimene munthu wodwala mwauzimu ayenera kuchita kuti achire.—Yak. 3:1, 5, 6; 5:14, 15.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:13—Kodi n’zotheka bwanji kuti ‘chifundo chikhale chopambana kwambiri kuposa chiweruzo’? Kuti Mulungu atichitire chifundo tikalakwa, iye amaona ngati nafenso timachitira ena chifundo. Ndiyeno amatikhululukira chifukwa cha nsembe ya dipo imene Mwana wake anapereka. (Aroma 14:12) Motero nthawi zonse tiyenera kuyesetsa kuchitira ena chifundo.
4:5—Kodi mawu a Yakobe pa vesili akuchokera pa lemba linalake? Mawu a Yakobe pa vesili sakuchokera pa lemba lililonse. Komabe mfundo ya m’mawu ouziridwa amenewa iyenera kuti ikuchokera pa mfundo za m’malemba monga Genesis 6:5; 8:21; Miyambo 21:10 ndi Agalatiya 5:17.
5:20—Kodi munthu “amene wabweza wochimwa pa njira yake yoipa,” amakwirira machimo a ndani? Mkhristu amene wabweza munthu wochita zoipa pa njira yake yoipa amapulumutsa wochimwayo kuti asafe mwauzimu komanso mwina kuti asadzawonongedwe. Izi zimachitika ngati wochimwayo walapa. Munthu akathandiza wochimwa m’njira imeneyi ‘amakwiriranso machimo ambiri’ a munthu wochimwayo.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:14, 15. Kulakalaka zinthu zoipa n’kumene kumachititsa kuti munthu achimwe. Motero si bwino kuganizira kwambiri zinthu zoipa mpaka kuyamba kuzilakalaka. M’malomwake tiyenera ‘kupitiriza kuganizira’ zinthu zolimbikitsa n’kulola kuti zikhazikike m’maganizo ndi m’mitima yathu.—Afil. 4:8.
2:8, 9. “Lamulo lachifumu” lonena za chikondi limaletsa “kukhala okondera.” Motero Akhristu sayenera kukhala okondera.
2:14-26. ‘Timapulumutsidwa chifukwa cha chikhulupiriro osati ntchito’ za Chilamulo cha Mose kapena ntchito zathu zachikhristu. Kukhala ndi chikhulupiriro kumafuna zambiri osati kungokhulupirira kuti kuli Mulungu. (Aef. 2:8, 9; Yoh. 3:16) Chikhulupiriro chiyenera kutithandiza kuchita zimene Mulungu amafuna.
3:13-17. “Nzeru yochokera kumwamba” imaposa nzeru “ya padziko lapansi, yaumunthu ndi yauchiwanda.” Tisasiye ‘kupitiriza kuifunafuna ngati chuma chobisika.’—Miy. 2:1-5.
3:18, “Anthu odzetsa mtendere amafesa” mbewu ya uthenga wabwino wa Ufumu “mu mtendere.” Motero ndi bwino kukhala odzetsa mtendere osati odzikuza, okonda kukangana ndi ena, kapena okonda chisokonezo.
‘KHALANI OLIMBA M’CHIKHULUPIRIRO’
Petulo anakumbutsa okhulupirira anzake za “chiyembekezo chamoyo” chakuti adzalandira cholowa kumwamba. Petulo anawauza kuti: “Inu ndinu ‘fuko losankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera.’” Pambuyo popereka malangizo pankhani ya kugonjera, analimbikitsa onse kuti akhale a maganizo amodzi, omverana chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu, a maganizo odzichepetsa.”—1 Pet. 1:3, 4; 2:9; 3:8.
Popeza mapeto a dongosolo la zinthu la Ayuda anali pafupi, Petulo analangiza abale kuti: “Khalani oganiza bwino, ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.” Kenako anawauza kuti: “Sungani maganizo anu, khalani maso . . . Pokhala olimba m’chikhulupiriro, mulimbane naye [Satana].”—1 Pet. 4:7; 5:8, 9.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
3:20-22—Kodi ubatizo umatipulumutsa motani? Anthu amene akufuna kupulumuka ayenera kubatizidwa. Komabe si kuti munthu akangobatizidwa ndiye kuti basi wapulumuka. Kwenikweni munthu amapulumutsidwa “mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.” Munthu amene akufuna kubatizidwa ayenera kukhulupirira kuti tidzapulumuka chifukwa chakuti Yesu anatifera, anaukitsidwa, panopa “ali ku dzanja lamanja la Mulungu” ndipo wapatsidwa mphamvu pa anthu amoyo ndi akufa omwe. Munthu akabatizidwa chifukwa chokhulupirira zimenezi, m’pamene amafanana ndi ‘miyoyo isanu ndi itatu imene inapulumutsidwa pamadzi.’
4:6—Kodi “uthenga wabwino unalengezedwa” kwa “akufa” ati? Awa ndi anthu amene anafa mwauzimu ‘chifukwa cha zolakwa zawo ndi machimo awo.’ Iwo anali akufa asanamve uthenga wabwino. (Aef. 2:1) Koma atakhulupirira uthenga wabwino anakhalanso “amoyo” mwauzimu.
Zimene Tikuphunzirapo
1:7. Kuti chikhulupiriro chathu chikhale chamtengo wapatali chiyenera kuyesedwa. Chikhulupiriro cholimba chonchi chimakhaladi “chosunga moyo.” (Aheb. 10:39) Motero sitiyenera kubwerera m’mbuyo tikakumana ndi mayesero.
1:10-12. Angelo analakalaka kusunzumira m’zinthu zozama za choonadi cha Mulungu zimene aneneri a Mulungu akale analemba zokhudza mpingo wa Akhristu odzozedwa. Zinthu zimenezi zinayamba kudziwika bwino pamene Yehova anayamba kutsogolera mpingowo. (Aef. 3:10) Mofanana ndi angelowo, ifenso tiyenera kuchita khama pofufuza “zinthu zozama za Mulungu.”—1 Akor. 2:10.
2:21. Yesu Khristu ndi chitsanzo chathu, motero tiyenera kulolera kuzunzidwa ngakhale kuphedwa kumene pofuna kugonjera ulamuliro wa Yehova.
5:6, 7. Tikatula nkhawa zathu kwa Yehova iye amatithandiza kuti tiike kulambira koona patsogolo m’moyo wathu, ndipo sitidera nkhawa mopitirira muyezo zimene zichitike mawa.—Mat. 6:33, 34.
“TSIKU LA YEHOVA LIDZAFIKA”
Petulo analemba kuti: “Ulosi sunayambe wadzapo mwa kufuna kwa anthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” Kuganizira mosamala mawu a ulosi kumatiteteza kwa “aphunzitsi onyenga” komanso anthu ena amene angatisokoneze.—2 Pet. 1:21; 2:1-3.
Petulo anachenjeza kuti: “M’masiku otsiriza kudzakhala onyodola ndi kunyodola kwawo.” Koma “tsiku la Yehova lidzafika ngati mbala.” Pomaliza kalata yake, Petulo anapereka malangizo abwino kwa onse amene ‘akuyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku limeneli.’—2 Pet. 3:3, 10-12.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:19—Kodi “nthanda” ikuimira ndani ndipo iyeyo anatuluka liti? Nanga tikudziwa bwanji kuti zimenezi zinachitika kale? “Nthanda” ikuimira Yesu Khristu atakhala mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Chiv. 22:16) Mu 1914, Yesu anaimirira pamwamba pa zolengedwa zonse monga Mfumu Mesiya, ndipo nthawi imeneyi inali ngati mbandakucha wa tsiku latsopano. Kusandulika kwake kunasonyeza ulemerero wake komanso wa Ufumu wake ndipo zimenezi zinatsimikizira kuti mawu a ulosi a Mulungu ndi oona. (Maliko 9:1-3) Kuganizira mosamala mawu amenewa kumatithandiza kumvetsa zinthu. N’chifukwa chake tikutha kudziwa kuti Nthanda anatuluka kale.
2:4—Kodi “Tatalasi” n’chiyani ndipo kodi angelo opanduka anaponyedwamo liti? Tatalasi ndi ndende yophiphiritsira imene munaponyedwa zolengedwa zauzimu zokha osati anthu. Zolengedwa zimenezi sizidziwa zolinga za Mulungu komanso zilibe chiyembekezo, moti tingati zili mumdima wandiweyani. Mulungu anaponya angelo osamvera ku Tatalasi m’masiku a Nowa kuti akhale kumeneko mpaka pamene adzawonongedwe.
3:17—Kodi Petulo anatanthauza chiyani pamene ananena za kukhala “odziwiratu”? Petulo ankanena za kudziwiratu zinthu zam’tsogolo zimene iye ndi olemba Baibulo ena analemba mouziridwa ndi Mulungu. Komabe iwo sanadziwitsidwe zinthu zonse. Ngakhale kuti Akhristu oyambirira ankadziwa zinthu zina zimene zidzachitike mtsogolo, iwo sankadziwa bwinobwino mmene zinthu zonse zidzachitikire.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:2, 5-7. Tikamayesetsa kuti tikhale ndi makhalidwe monga chikhulupiriro, kupirira ndi kudzipereka kwa Mulungu, timapitiriza “kudziwa molondola Mulungu ndi Yesu.” Ndiponso sitikhala ozirala kapena osabala zipatso pa zinthu zolondola zimene tadziwazo.—2 Pet. 1:8.
1:12-15. Kuti tikhale “okhazikika molimba m’choonadi,” tiyenera kukumbutsidwa pafupipafupi mfundo za choonadi ku misonkhano yampingo, pa phunziro laumwini komanso powerenga Baibulo.
2:2. Tiyenera kusamala kuti zochita zathu zisanyozetse Yehova ndi gulu lake.—Aroma 2:24.
2:4-9. Tikaona zimene Yehova wachita m’mbuyomu sitikayika kuti iye “amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye m’mayesero. Koma osalungama amawasungira tsiku loweruza kuti akawawononge.”
2:10-13. Ngakhale kuti nthawi zina “anthu aulemerero” kapena kuti akulu achikhristu amalakwitsa zinthu, sitiyenera kulankhula za iwo monyoza.—Aheb. 13:7, 17.
3:2-4, 12. Kumvetsera mosamala “mawu amene aneneri oyera ananena kale, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu,” kudzatithandiza kukumbukira kuti tsiku la Yehova lili pafupi.
3:11-14. Popeza ‘tikuyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse za kukhalapo kwa tsiku la Yehova,’ tiyenera (1) ‘kukhala ndi khalidwe loyera,’ kutanthauza kuti tiyenera kukhala oyera mwakuthupi, mwamaganizo, mwamakhalidwe komanso mwauzimu (2) kutanganidwa ndi ntchito zosonyeza “kudzipereka kwa Mulungu,” monga ntchito zogwirizana ndi kulalikira za Ufumu komanso kupanga ophunzira. (3) kuyesetsa kuti khalidwe lathu ndi zochita zathu zikhale zopanda ‘mathotho’ a m’dzikoli (4) kukhala “opanda chilema” n’kumachita zinthu zonse ndi zolinga zabwino (5) kukhala “mu mtendere” ndi Mulungu, Akhristu anzathu komanso anthu ena onse.