Khalani Anzeru Pamene Mapeto Akuyandikira
1 Mawu a Mulungu amafotokoza mobwerezabwereza kuti tsiku la Yehova lidzadza “monga mbala usiku”—kutanthauza kuti modzidzimutsa ndi mwakachetechete. (1 Ates. 5:2; Mat. 24:43; 2 Pet. 3:10; Chiv. 3:3; 16:15) Yesu anati: “Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.” (Mat. 24:44) Kodi tingachite chiyani kuti tikhale okonzekera mwauzimu pamene mapeto akuyandikira? Yankho lake ndi mawu ouziridwa akuti: “Khalani anzeru.”—1 Pet. 4:7.
2 Kukhala anzeru kumaphatikizapo kuona zinthu mmene Yehova amazionera. (Aef. 5:17) Kumatithandiza kukhala “alendo ndi ogonera” m’dzikoli. (1 Pet. 2:11) Kumatithandizanso kuzindikira zofunika kwenikweni, kuika zinthu zoyamba pa malo ake, ndi kusankha zinthu mwanzeru.—Afil. 1:10.
3 Khalani ndi Zolinga Zauzimu: Kukhala ndi zolinga zauzimu ndi kuzikwaniritsa kumatithandiza kukhala anzeru. Kodi muli ndi zolinga zauzimu zimene mukufuna kukwaniritsa? Kodi mukuyesetsa kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, kupezeka pamisonkhano yachikristu, kuŵerenga magazini iliyonse ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kapena kuwonjezera utumiki wanu? Mukakhala ndi zolinga zokuyenerani, kuzilimbikira, ndi kupempha Yehova kuti akudalitseni pakhama lanu, mungadzadabwe ndi zotsatira zake.
4 Mkulu wina anafunsa banja lina lachinyamata ngati linali ndi zolinga zauzimu. Funso lakelo linawathandiza kuona kuti atha kuchita upainiya ngati angapunguleko zina ndi zina m’moyo wawo ndi kubweza ngongole yaikulu imene anali nayo. Zimenezo zinakhaladi cholinga chawo. Anachita khama kubweza ngongoleyo ndipo anapeza njira zosiyira zinthu zina zosafunika kwenikweni zimene zimawadyera nthaŵi ndi nyonga. Patangopita chaka chimodzi chokha, anakwaniritsa cholinga chawo. Mapeto ake? Mwamunayo akuti: “Pakanapanda zolinga, sitikanakhala mmene tililimu. Tikusangalala kwambiri. Moyo wathu tsopano ndi wa phee, ndiponso wamtendere. Komanso uli ndi tanthauzo.”
5 Pamene tikuyembekeza tsiku la Yehova, tikhalebe okonzeka mwauzimu mwa kukhala anzeru, ndipo mtima wathu ukhale pa kuchita chifuniro cha Mulungu.—Tito 2:11-13.