‘Pitirizani Kukhululukirana Eni Okha’
“[Pitirizani, NW] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha.”—AKOLOSE 3:13.
1. (a) Pamene Petro analingalira kuti tizikhululukira ena “kufikira kasanu ndi kaŵiri,” kodi nchifukwa ninji ayenera kuti anaganiza kuti anali kupereka lingaliro labwino? (b) Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena kuti tiyenera kukhululuka “kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri”?
“AMBUYE, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kaŵiri kodi?” (Mateyu 18:21) Petro ayenera kuti anaganiza kuti anali kupereka lingaliro labwino kwambiri. Panthaŵiyo, lamulo la arabi linanena kuti munthu sayenera kukhululukira mnzake koposa katatu pa cholakwa chimodzimodzicho.a Ndipo tangolingalirani mmene Petro anazizwira pamene Yesu anayankha kuti: “Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri”! (Mateyu 18:22) Kubwereza kasanu ndi kaŵiri kunali kofanana ndi kunena kuti “kosaŵerengeka.” Mogwirizana ndi malingaliro a Yesu, kwenikweni palibe malire a mmene Mkristu angakhululukire ena.
2, 3. (a) Kodi ndi pazochitika zina ziti pamene kungaoneke kovuta kukhululukira ena? (b) Nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro chakuti kukhululukira ena kumatipindulitsa?
2 Komabe, kugwiritsira ntchito uphungu umenewo nthaŵi zambiri kumakhala kovuta. Kodi ndani wa ife amene sanayang’anizanepo ndi chokhumudwitsa? Mwinamwake munthu wina amene inu munali kumkhulupirira anaulula nkhani yachinsinsi imene munamuuza. (Miyambo 11:13) Mawu ansontho a bwenzi lanu lapamtima angakhale kuti ‘anakupyozani ngati kupyoza kwa lupanga.’ (Miyambo 12:18) Zochita zokhumudwitsa za winawake amene munali kumkonda ndi kumkhulupirira zingakhale kuti zinakupwetekani mtima kwambiri. Pamene zinthu zotero zichitika, mwachibadwa tingathe kukwiya nazo. Mwina tingaganizenso zosiya kulankhulana ndi wolakwayo, kumpeŵeratu monga momwe tingathere. Zingaoneke ngati kuti kumkhululukira kungapangitse kuti iye asalangidwe. Komatu pamene timasunga mkwiyo, mpamenenso timadzipweteka mtima tokha.
3 Choncho Yesu akutiphunzitsa kukhululuka—“makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri.” Ndithudi ziphunzitso zake sizingativulaze. Chilichonse chimene iye anaphunzitsa chinachokera kwa Yehova, ‘amene atiphunzitsa kupindula.’ (Yesaya 48:17; Yohane 7:16, 17) Kunena zoona, chiyenera kukhaladi chinthu chotipindulitsa kwambiri kukhululukira ena. Tisanafotokoze chifukwa chake tiyenera kukhululukira ena ndi mmene tingakhululukire, zingakhale zothandiza kufotokoza bwino zimene kukhululuka kumatanthauza ndi zimene sikutanthauza. Kudziŵa chifukwa chake tiyenera kukhululukira ena kungatisonkhezere mmene tingakhululukire ena pamene atichimwira.
4. Kodi kukhululukira ena sikutanthauzanji, koma kodi kukhululuka kwatanthauzidwa motani?
4 Kukhululukira ena pazolakwa zawo sikutanthauza kuti tikupeputsa kapena kuchepetsa zolakwazo; komanso sikutanthauza kuti ena atione ngati opanda pake. Ndi iko komwe, pamene Yehova atikhululukira, ndithudi sizitanthauza kuti iye akuchepetsa machimo athu, ndipo iye sadzalola anthu ochimwa kupondereza chifundo chake. (Ahebri 10:29) Malinga nkunena kwa buku la Insight on the Scriptures, kukhululuka kumatanthauza “mchitidwe wa kusaimba mlandu munthu wopalamula; kusiya kukwiya naye chifukwa cha cholakwa chake ndi kusafuna kuti apereke chinthu chilichonse chotipepesera.” (Volyumu 1, tsamba 861)b Baibulo limatipatsa zifukwa zomveka bwino zokhululukira ena.
Nchifukwa Ninji Tiyenera Kukhululukira Ena?
5. Kodi ndi chifukwa chofunika kwambiri chokhululukira ena chiti chimene chasonyezedwa pa Aefeso 5:1?
5 Chifukwa china chofunika kwambiri chokhululukira ena chasonyezedwa pa Aefeso 5:1 kuti: “Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” Kodi ndi motani mmene ‘tingakhalire akutsanza a Mulungu’? Mawu akuti “chifukwa chake” akugwirizanitsa vesili ndi vesi lapitalo, limene limati: ‘Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.’ (Aefeso 4:32) Inde, pankhani ya kukhululuka, tiyenera kukhala akutsanza a Mulungu. Monga momwe mnyamata wamng’ono amayesetsera kukhala monga atate ake, ifenso, monga ana okondedwa a Yehova, tiyenera kufunitsitsa kukhala monga Atate wathu wakumwamba wokhululukira. Zingakondweretsedi mtima wa Yehova, pamene ayang’ana pansi ali kumwamba naona ana ake a padziko lapansi akuyesetsa kukhala monga iye mwa kukhululukirana wina ndi mnzake!—Luka 6:35, 36; yerekezerani ndi Mateyu 5:44-48.
6. Kodi ndi motani mmene kukhululuka kwa Yehova kulili kosiyana kwakukulu ndi kukhululuka kwathu?
6 Kunena zoona, sitingathe kukhululukirana mwaungwiro monga momwe Yehova amachitira. Koma chimenecho ndi chifukwa chinanso chimene tiyenera kukhululukirana. Talingalirani: Pali kusiyana kwakukulu pakati pa kukhululuka kwa Yehova ndi kukhululuka kwathu. (Yesaya 55:7-9) Pamene tikhululukira anthu amene atichimwira, timadziŵa kuti mwina pasanapite nthaŵi yaitali nafenso tingathe kuwachimwira ndi kuwapempha kuti atikhululukirenso. Tikanena za anthu, imakhala nkhani ya ochimwa kukhululukira ochimwa anzawo. Komabe, kunena za Yehova, kukhululuka kwake nthaŵi zonse kumakhala kwa mbali imodzi. Iye amatikhululukira, koma sitidzafunikira konse kuti timkhululukire. Ngati Yehova, amene sachimwa, amatikhululukira mwachikondi chotero ndiponso kotheratu, kodi ifeyo anthu ochimwa sitiyenera kuyesetsa kukhululukirana?—Mateyu 6:12.
7. Ngati tikana kukhululukira ena pamene tili ndi mwaŵi wa kuchitira chifundo, kodi zimenezi zingaipitse motani unansi wathu ndi Yehova?
7 Chinthu chinanso chofunika kwambiri nchakuti, ngati tikana kukhululukira ena pamene tili ndi mwaŵi wa kuchitira chifundo, zimenezo zingaipitse unansi wathu ndi Mulungu. Yehova sangotipempha kuti tizikhululukirana; iye amayembekezeranso kuti tizitero. Mongadi momwe Malemba amanenera, chifukwa china chimene ife timafunikira kukhululukirana nchakuti Yehova atikhululukire kapena chifukwa chakuti iye watikhululukira. (Mateyu 6:14; Marko 11:25; Aefeso 4:32; 1 Yohane 4:11) Ndipo ngati sitifuna kukhululukira ena pamene tili ndi chifukwa chabwino chochitira zimenezo, kodi tingafunedi kuti Yehova atikhululukire?—Mateyu 18:21-35.
8. Kodi kukhululuka kumatipindulitsa motani?
8 Yehova amaphunzitsa anthu ake “njira yokoma [imene] ayenera kuyendamo.” (1 Mafumu 8:36) Pamene iye amatilangiza kuti tizikhululukirana, tingakhale ndi chidaliro chakuti iye amasamala za ife. Ndi chifukwa chabwino, Baibulo limatiuza ‘kupatuka pamkwiyo.’ (Aroma 12:19) Mkwiyo ndiye katundu wolemera kuunyamula m’moyo. Ngati tiusunga, umasokoneza maganizo athu, umatisoŵetsa mtendere, ndiponso umatilepheretsa kukhala ndi chimwemwe. Mkwiyo wopitirizabe, monga nsanje, ungavulaze thanzi la matupi athu. (Miyambo 14:30) Ndipotu pamene tikuchita zonsezi, wopalamulayo angakhale kuti sakudziŵa zimene zikutivutitsa mumtima! Mlengi wathu wachikondi amadziŵa kuti timafunikira kukhululukira ena mofunitsitsa osati ncholinga chakuti zipindulitse iwo okha koma kuti zipindulitsenso ife tomwe. Ndithudi, uphungu wa m’Baibulo wa kukhululukirana ndiyo ‘njira yokoma yoyenera kuyendamo.’
“Pitirizani Kulolerana Wina ndi Mnzake”
9, 10. (a) Kodi ndi pazochitika ziti pamene sipafunikira kuchita kukambirana ndi opalamula kuti tiwakhululukire? (b) Kodi mawu akuti “[pitirizani, NW] kulolerana wina ndi mnzake” akupereka lingaliro lotani?
9 Kuvulala kungayambire pa mabala ang’onoang’ono mpaka akuluakulu, ndipo zonsezo zimafuna chisamaliro chosiyana. Zilinso chimodzimodzi ndi kukhumudwa—zokhumudwitsa zina zimakhala zazikulu kuposa zina. Kodi nkoyenerera kudandaula ndi chokhumudwitsa chilichonse chaching’ono chimene anzathu atichitira? Zokhumudwitsa zazing’ono, monga mnyozo, ndiponso kusulizidwa zili mbali ya moyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndipo sipafunikira kuchita kukambirana ndi olakwawo kuti tiwakhululukire. Ngati tili ndi mbiri yakuti timapeŵa ena chifukwa cha chophophonya chilichonse chaching’ono ndi kufunabe kuti apepese kaye tisanayanjane nawonso, tingapangitse kuti azikhala omangika kwambiri pamene ali nafe—kapena kuti azitipeŵa!
10 M’malo mwake, kuli bwino kwambiri ‘kukhala ndi mbiri yakuti ndife ololera.’ (Afilipi 4:5, Phillips) Monga zolengedwa zopanda ungwiro zotumikira mogwirizana, tingayembekezere kuti nthaŵi ndi nthaŵi abale athu angatikhumudwitse, ndipo ifenso tingachite zofananazo kwa iwo. Akolose 3:13 akutilangiza kuti: “[Pitirizani, NW] kulolerana wina ndi mnzake.” Mawu ameneŵa akutanthauza kuti tiyenera kuleza mtima ndi ena, kukankhira kunkhongo zinthu zosasangalatsa zimene amachita kapena mikhalidwe imene imatikhumudwitsa. Kuleza mtima ndi kudziletsa kotero kungatithandize kusakhumudwa ndi zolakwa zochepa zimene anzathu amatichitira—popanda kusokoneza mtendere wa mpingo.—1 Akorinto 16:14.
Pamene Tipwetekedwa Mtima Kwambiri
11. Pamene ena atichimwira, kodi chingatithandize nchiyani kuti tiwakhululukire?
11 Komabe, bwanji ngati anzathu atichimwira, ndi kutipweteka mtima kwambiri? Ngati tchimolo silalikulu kwambiri, kungakhale kosavuta kugwiritsira ntchito uphungu wa m’Baibulo wakuti ‘tikhululukirane tokha.’ (Aefeso 4:32) Mtima umenewo wokhululukirana ngwogwirizana ndi mawu ouziridwa a Petro akuti: “Koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” (1 Petro 4:8) Kukumbukira kuti ifenso ndife ochimwa kumatithandiza kulolera zophophonya za ena. Choncho, pamene tikhululuka, timasiya mkwiyo m’malo mosunga chinthu kukhosi. Chotsatirapo chake, unansi wathu ndi wopalamulayo sungawonongeke, ndipo timathandiziranso kusunga mtendere wa mpingo. (Aroma 14:19) M’kupita kwa nthaŵi, tingaiŵale zimene anatichitira.
12. (a) Kodi tingafunikire kuchita chiyani kuti tikhululukire wina amene watikhumudwitsa kwambiri? (b) Kodi mawu a pa Aefeso 4:26 amasonyeza motani kuti tiyenera kuthetsa nkhani mofulumira?
12 Nanga bwanji ngati wina wake achita machimo aakulu kwa ife, zikumatipweteka mtima kwambiri? Mwachitsanzo, yemwe ali bwenzi lanu lodalirika angakhale kuti anaulula nkhani yachinsinsi kwambiri imene munamuuza. Mukupweteka maganizo, kuchita manyazi, ndiponso mukuona kuti munanyengedwa. Mwayesetsa kuinyalanyaza nkhaniyo, koma mukulephera kuiiŵala. Zikatere, mungafunikire kuchitapo kanthu kuti muthetse vutolo, mwinamwake mwa kulankhulana ndi wopalamulayo. Ndi bwino kuchita zimenezi nkhaniyo isanafike poipa. Paulo anatilangiza kuti: “Kwiyani, koma musachimwe [ndiko kuti, tisasunge mkwiyo kapena kuchita zinthu mwaukali]; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Mawu a Paulo ameneŵa analidi ndi tanthauzo lomveka bwino chifukwa chakuti kwa Ayuda, tsiku linali kutha pa kuloŵa kwa dzuŵa ndipo kumeneku kunalinso kuyamba kwa tsiku lotsatira. Choncho, uphungu wake ngwakuti: Thetsani nkhaniyo mofulumira!—Mateyu 5:23, 24.
13. Pamene tifikira wina amene watichimwira, kodi cholinga chathu chiyenera kukhala chiyani, ndipo ndi malingaliro ati amene angatithandize kuchikwaniritsa?
13 Kodi wopalamulayo mungamfikire motani? ‘Funafunani mtendere ndi kuulondola,’ amatero 1 Petro 3:11. Choncho, cholinga chanu sindicho kumkalipira koma kuti mukhale pamtendere ndi mbale wanuyo. Kuti zimenezo zitheke, ndi bwino kupeŵa kulankhula mawu onyoza ndiponso kulozaloza; zimenezi zingapangitse kuti winayo abwezere. (Miyambo 15:18; 29:11) Kuwonjezera pamenepo, muyenera kupeŵa mawu ena ansontho monga akuti, “Umakonda . . . !” kapena kuti, “Nthaŵi zonse suchita . . . !” Mawu osafunika oterowo angampangitse kufuna kudzitchinjiriza. M’malo mwake, malankhulidwe anu ndiponso nkhope yanu isonyeze kuti mukufunadi kuthetsa nkhani imene yakupwetekani mtima kwambiri. Fotokozani bwino lomwe mmene zochitikazo zikukukhudzirani. Perekani mpata wakuti mnzanuyo aperekepo maganizo ake. Mvetserani zimene iye akunena. (Yakobo 1:19) Kodi zimenezo zidzathandiza motani? Miyambo 19:11 ikufotokoza kuti: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.” Kumvetsetsa malingaliro a mnzanuyo ndi zifukwa zimene anachitira zinthuzo kungathetse maganizo ndi malingaliro anu oipa ponena za munthuyo. Pamene tikambirana ncholinga chakuti pakhale mtendere ndikupitiriza kukhala ndi mzimu umenewo, nzosakayikitsa konse kuti tingathetse kusiyana maganizoko, tingapepesane, ndiponso tingathe kukhululukirana.
14. Pamene tikhululukira ena, kodi tiyenera kuiŵala m’lingaliro lotani?
14 Kodi kukhululukira ena kumatanthauza kuti tiyenera kuiŵaliratu zimene zinachitika? Kumbukirani chitsanzo cha Yehova pankhani imeneyi, monga momwe inafotokozera nkhani yapitayo. Pamene Baibulo linena kuti Yehova amaiŵala machimo athu, zimenezi sizitanthauza kuti iye sangathe kuwakumbukira ayi. (Yesaya 43:25) Kwenikweni, iye amaiŵala m’lingaliro lakuti pamene akhululuka, iye sadzachita kanthu kena kwa ife chifukwa cha machimo amenewo panthaŵi ina mtsogolo. (Ezekieli 33:14-16) Mofananamo, kukhululukira anthu anzathu kwenikweni sikutanthauza kuti sitidzakumbukira zimene iwo anachita. Komabe, tingathe kuiŵala m’lingaliro lakuti sitiganiza zodzachita kanthu kena kwa wopalamulayo kapena kukumbutsa tchimo lakelo mtsogolo. Choncho, ngati nkhaniyo yathetsedwa, sibwino kumakachitanso manenanena uku ndi uku; kungakhalenso kupanda chikondi kumpeŵeratu wopalamulayo, kumuona ngati wachotsedwa mumpingo. (Miyambo 17:9) Zoonadi, pangapite nthaŵi yaitali kuti unansi wathu udzayambenso kuyenda bwino; sitingakhale oyandikana kwambiri monga momwe tinkachitira kale. Koma tiyenera kumkondabe monga mbale wathu wachikristu ndi kuyesetsa zolimba kuti tipitirizebe kukhala mwamtendere.—Yerekezerani ndi Luka 17:3.
Pamene Kukhululuka Kukuoneka Ngati Kosatheka
15, 16. (a) Kodi Akristu afunikira kukhululukira ochimwa amene sakufuna kulapa? (b) Kodi tingagwiritsire ntchito motani uphungu wa Baibulo wopezeka pa Salmo 37:8?
15 Nanga tingatani ngati ena achita tchimo lalikulu kwambiri kwa ife, komabe iwo sakufuna kuvomereza kuchimwa kwawo, sakufuna kulapa, ndiponso sakupepesa? (Miyambo 28:13) Malemba amafotokoza momveka bwino kuti Yehova sakhululukira ochimwa osalapa ndi oumitsa khosi. (Ahebri 6:4-6; 10:26, 27) Nanga ifeyo tingatani? Buku la Insight on the Scriptures likuti: “Akristu safunikira kukhululukira ochimwa osafuna kulapa amene amavutitsa anzawo ndi kuchimwira dala. Amenewo amakhala adani a Mulungu.” (Volyumu 1, tsamba 862) Mkristu amene wakumana ndi chisalungamo, kuchitiridwa zinthu zonyansa, kapena kuchitiridwa nkhanza zoopsa sayenera kuumirizidwa kuti akhululukire wopalamula amene ali wosalapa.—Salmo 139:21, 22.
16 Mwachionekere amene achitiridwa nkhanza angakhumudwe ndiponso angakwiye. Komabe, tikumbukire kuti kupsa mtima nthaŵi zonse ndi kusunga mkwiyo kungativulaze kwambiri. Poyembekezera kuti wina avomereze kulakwa kwake kapena kuti apepese, mkwiyo wathu ungawonjezereke ngati iye sakutero. Kumangolingalirabe za chisalungamo chimenecho kungawonjezere mkwiyo wathu, ndipo zimenezi zingawononge thanzi lathu lauzimu, lamaganizo, ndiponso la thupi lathu. Chotsatirapo chake, timapangitsa kuti munthu amene anatikhumudwitsayo apitirizebe kutikhumudwitsa. Baibulo limalangiza mwanzeru kuti: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo.” (Salmo 37:8) Choncho, Akristu ena anaona kuti m’kupita kwa nthaŵi iwo anasankha kukhululuka mwa kusasunga mkwiyo—osati chifukwa cha kupeputsa zimene zinawachitikirazo, koma chifukwa chosafuna kuvulazidwa ndi mkwiyowo. Pamene anasiya nkhani yonseyi m’manja mwa Mulungu wa chiweruzo, iwo anatha kuthetsa mkwiyowo ndipo anapitiriza kukhala mosangalala.—Salmo 37:28.
17. Kodi lonjezo la Yehova lolembedwa pa Chivumbulutso 21:4 likupereka chitsimikizo chotonthoza chiti?
17 Ngati tchimolo ndi lalikulu kwambiri, mwinamwake sitingathe kuliiŵaliratu, inde osati m’dongosolo lino la zinthu. Koma Yehova akulonjeza dziko latsopano mmene iye “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Chilichonse chimene tingadzachikumbukire panthaŵiyo sichidzatikhumudwitsa, kapena kutipsetsa mtima, zimene zingalemetse mtima wathu lerolino.—Yesaya 65:17, 18.
18. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kukhala okhululukira abale ndi alongo athu pamene atichimwira? (b) Pamene ena atichimwira, kodi tingakhululuke ndi kuiŵala m’lingaliro lotani? (c) Kodi zimenezi zimatipindulitsa motani?
18 Tsopano lino, tiyenera kukhalira pamodzi komanso kugwirira ntchito pamodzi monga abale ndi alongo amene ali anthu opanda ungwiro ndi ochimwa. Tonsefe timalakwa. Nthaŵi ndi nthaŵi, timakhumudwitsana ndipo ngakhale kukwiyitsana. Yesu anadziŵadi bwino kuti tiyenera kukhululukira ena, ‘osati kufikira kasanu ndi kaŵiri, koma kufikira makumi asanu ndi aŵiri kubwerezedwa kasanu ndi kaŵiri’! (Mateyu 18:22) Zoonadi, sitingathe kukhululuka kotheratu monga momwe Yehova amachitira. Komabe, nthaŵi zambiri pamene abale athu atichimwira, tingathe kuwakhululukira m’lingaliro la kuthetsa mkwiyo ndiponso tingathe kuiŵala m’lingaliro la kusasunga nkhaniyo ncholinga chodzaikumbutsira mtsogolo. Pamene tikhululuka ndi kuiŵala chotero, timathandizira kusunga mtendere osati wampingo wokha komanso wamaganizo ndi mtima wathu. Koposa zonse, tidzakhala ndi mtendere umene angatipatse ndi Mulungu wathu wachikondi yekha, Yehova.—Afilipi 4:7.
[Mawu a M’munsi]
a Malinga nkunena kwa Talmud yachibabulo, lamulo lina la arabi linati: “Ngati munthu wachita cholakwa, nthaŵi yoyamba, yachiŵiri ndiponso nthaŵi yachitatu iye akhululukidwa, nthaŵi yachinayi sakhululukidwa.” (Yoma 86b) Zimenezi zinali choncho makamaka chifukwa cha kusamvetsetsa malemba ena monga Amosi 1:3; 2:6; ndi Yobu 33:29.
b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Mafunso a Kupenda
◻ Nchifukwa ninji tiyenera kukhala ofunitsitsa kukhululukira ena?
◻ Kodi ndi pazochitika ziti pamene timayenera ‘kupitiriza kulolerana wina ndi mnzake’?
◻ Ngati takhumudwa kwambiri ndi machimo a ena, kodi tingatani kuti tithetse nkhaniyo mwamtendere?
◻ Pamene tikhululukira ena, kodi tiyenera kuiŵala m’lingaliro lotani?
[Chithunzi patsamba 16]
Pamene tisunga mkwiyo, wopalamula angakhale kuti sakudziŵa zimene zikutivutitsa
[Chithunzi patsamba 17]
Ngati mufikira ena ncholinga chodzetsa mtendere, mungathe kuthetsa mosavuta kusiyana maganizo