“Tizisonyezana Chikondi Chenicheni M’zochita Zathu”
“Tisamakondane ndi mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma tizisonyezana chikondi chenicheni m’zochita zathu.”—1 YOH. 3:18.
1. Kodi chikondi chapamwamba kwambiri ndi chiti, ndipo n’chifukwa chiyani tikutero? (Onani chithunzi choyambirira.)
CHIKONDI chimene munthu amachisonyeza chifukwa chotsatira mfundo zabwino (a·gaʹpe) ndi mphatso yochokera kwa Yehova. Zili choncho chifukwa chakuti Yehova ndi amene anayambitsa chikondi chimenechi. (1 Yoh. 4:7) Chikondichi ndi chapamwamba kwambiri. Munthu amene ali ndi chikondi chimenechi amachitira ena zabwino popanda kufuna phindu lililonse, ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa anthu amene si anzake. Buku lina limanena kuti “zochita za munthu n’zimene zimasonyeza” kuti ali ndi chikondi cha a·gaʹpe. Tikamasonyeza chikondi chimenechi kapena munthu wina akatisonyeza chikondichi timakhala osangalala.
2, 3. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amakonda kwambiri anthu?
2 Yehova asanalenge Adamu ndi Hava anali atasonyeza kale kuti amakonda anthu. Iye analenga dziko n’cholinga choti anthu akhalemo mpaka kalekale komanso mosangalala. Yehova anachita zimenezi kuti atithandize ifeyo, osati kuti apindulepo kenakake. Iye anasonyezanso chikondi chapamwamba popereka mwayi kwa anthu woti akhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso amene anawakonzera.
3 Adamu ndi Hava atachimwa, Yehova anasonyezanso chikondi chimenechi m’njira yaikulu kwambiri. Iye anakonza zoti pakhale dipo lowombola ana awo ndipo sankakayikira kuti ana ena adzayamikira chikondi chake. (Gen. 3:15; 1 Yoh. 4:10) Ndipo kungoyambira pamene analonjeza zoti adzapulumutsa anthu, m’maganizo mwake zinali ngati zachitika kale. Patapita zaka pafupifupi 4,000, Yehova analolera kuti Mwana wake aphedwe n’cholinga choti apulumutse anthu. (Yoh. 3:16) Timayamikira kwambiri kuti Yehova analolera kuchita zimenezi ngakhale kuti zinali zopweteka kwambiri.
4. N’chiyani chikusonyeza kuti tikhoza kusonyeza chikondi chapamwamba ngakhale kuti ndife ochimwa?
4 Popeza tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, nafenso tikhoza kusonyeza chikondi chapamwambachi. N’zoona kuti timavutika kusonyeza chikondichi chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa Adamu, koma sikuti n’zosatheka. Mwachitsanzo, Abele anasonyeza kuti amakonda Mulungu pamene anasankha zinthu zabwino kwambiri n’kupereka nsembe. (Gen. 4:3, 4) Nowa anasonyezanso chikondi pogwira ntchito youza anthu uthenga wa Mulungu kwa zaka zambiri ngakhale kuti sankamumvera. (2 Pet. 2:5) Nayenso Abulahamu anasonyeza kuti ankakonda kwambiri Mulungu pololera kuchita zinthu zovuta kwambiri. Iye analolera kuti apereke mwana wake nsembe. (Yak. 2:21) Mofanana ndi anthu okhulupirika amenewa, tiyenera kusonyeza ena chikondi ngakhale kuti si zophweka.
TIZISONYEZA CHIKONDI CHENICHENI OSATI CHACHINYENGO
5. Kodi tingasonyeze chikondi chenicheni m’njira ziti?
5 Baibulo limanena kuti tiyenera kusonyeza chikondi chenicheni, osati ndi ‘mawu okha kapena ndi pakamwa pokha, koma m’zochita zathu.’ (1 Yoh. 3:18) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitingalankhule mawu osonyeza chikondi? Ayi si choncho. (1 Ates. 4:18) Koma zikutanthauza kuti sitiyenera kusonyeza chikondi ndi mawu okha pa nthawi imene tikufunikira kuchisonyeza ndi zochita zathu. Mwachitsanzo, ngati Mkhristu mnzathu akusowa zofunika pa moyo, tiyenera kumuthandiza osati kungomuuza kuti tikumufunira zabwino zonse. (Yak. 2:15, 16) Chifukwa chokonda Yehova ndi anzathu, timayesetsanso kuchita zambiri pa ntchito yolalikira, osati kungopempha Mulungu kuti “atumize antchito” ambiri oti azigwira ntchitoyi.—Mat. 9:38.
6, 7. (a) Kodi “chikondi chopanda chinyengo” n’chotani? (b) Perekani zitsanzo za anthu amene anasonyeza chikondi chachinyengo.
6 Mtumwi Yohane analemba kuti tiyenera kusonyeza “chikondi chenicheni m’zochita zathu.” Choncho chikondi chathu sichiyenera kukhala “cha chiphamaso” kapena ‘chachinyengo.’ (Aroma 12:9; 2 Akor. 6:6) Zimenezi zikutanthauza kuti n’zosatheka kunamizira kuti tili ndi chikondi chenicheni. Munthu amene amasonyeza chikondi chachinyengo sitinganene kuti ndi wachikondi.
7 Tiyeni tikambirane zitsanzo za anthu amene anasonyeza chikondi chachinyengo. M’munda wa Edeni, Satana ananamizira kuti akuthandiza Hava koma anali wodzikonda ndipo zimene ankachitazo zinali zachinyengo. (Gen. 3:4, 5) Nayenso Ahitofeli sanasonyeze chikondi chenicheni kwa Davide ndipo anamuchitira chiwembu poganiza kuti akatero zimuyendera bwino. (2 Sam. 15:31) Masiku anonso, anthu ampatuko komanso anthu ena amene amasokoneza mtendere mumpingo amalankhula “mawu okopa ndi achinyengo” n’cholinga choti anthu aziganiza kuti amawakonda koma amachita zimenezi ali ndi zolinga zoipa.—Aroma 16:17, 18.
8. Kodi tiyenera kudzifunsa funso liti?
8 Kusonyeza chikondi chachinyengo n’koipa kwambiri chifukwa munthu wochita zimenezi amanamizira kuti akusonyeza chikondi chochokera kwa Mulungu. Chinyengo chimenechi chikhoza kupusitsa anthu koma osati Yehova. Ndipotu Yesu ananena kuti anthu achinyengo adzalandira “chilango choopsa.” (Mat. 24:51) Choncho atumiki a Yehova sayenera kusonyeza chikondi chachinyengo ngakhale pang’ono. Koma tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimasonyeza chikondi chenicheni nthawi zonse kapena nthawi zina ndimakhala ndi kamtima kodzikonda kapena kachinyengo?’ Tiyeni tsopano tikambirane njira 9 zimene tingasonyezere “chikondi chopanda chinyengo.”
MMENE TINGASONYEZERE “CHIKONDI CHENICHENI M’ZOCHITA ZATHU”
9. Kodi munthu amene ali ndi chikondi chenicheni amatani?
9 Tizitumikira abale athu popanda kudzionetsera. Ngati zingatheke, tingachite bwino kuthandiza abale athu m’njira zosaonekera kwa anthu. (Werengani Mateyu 6:1-4.) Hananiya ndi Safira analephera kuchita zimenezi ndipo analangidwa chifukwa cha chinyengo chawo. Iwo ankafuna kuti anthu adziwe zimene anapereka ndipo ananama kuti apereka ndalama zonse zimene anapeza. (Mac. 5:1-10) Koma munthu amene ali ndi chikondi chenicheni amasangalala kutumikira anthu ena popanda kudzionetsera kapena kudzitchukitsa. Mwachitsanzo, abale amene amathandiza Bungwe Lolamulira pokonza chakudya chauzimu sadzionetsera kapena kuuza anthu zimene achita.
10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhala patsogolo posonyeza ulemu?
10 Tizikhala patsogolo posonyeza ulemu. (Werengani Aroma 12:10.) Yesu anasonyeza kuti ankalemekeza anthu ena posambitsa mapazi ophunzira ake. (Yoh. 13:3-5, 12-15) Tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa kuti tizitsanzira Yesu pa nkhani yolemekeza ena, ngakhale kuti nthawi zina zingativute. Paja nawonso ophunzira a Yesu sanamvetse chifukwa chake iye anawasambitsa mapazi, mpaka atalandira mzimu woyera. (Yoh. 13:7) Tingasonyeze kuti timalemekeza ena tikamapewa kudziona kuti ndife apamwamba chifukwa cha maphunziro athu, chuma chathu kapena udindo umene tili nawo m’gulu la Yehova. (Aroma 12:3) Nthawi zina anthu ena angayamikiridwe pa zinthu zimene ifeyo tikuona kuti tiyeneranso kuyamikiridwa. Zoterezi zikachitika tiyenera kusangalala nawo limodzi, osati kuwachitira nsanje.
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira abale athu kuchokera mumtima?
11 Tiziyamikira abale athu kuchokera mumtima. Tiyenera kuyesetsa kuyamikira anzathu pamene achita zabwino chifukwa zimenezi zimawalimbikitsa. (Aef. 4:29) Koma tiyenera kuchita zimenezi kuchokera mumtima. Kupanda kutero kuyamikira kwathuko kumakhala kwachinyengo komanso tingakhale tikupewa udindo wathu wopereka malangizo amene munthuyo angafunikire. (Miy. 29:5) Ngati timayamikira munthu pamaso pake koma kenako n’kukanena zoipa kumbali, ndiye kuti ndife achinyengo. Mtumwi Paulo ankapewa chinyengo choterechi ndipo anapereka chitsanzo chabwino poyamikira anthu kuchokera mumtima. Mwachitsanzo, iye anayamikira Akhristu a ku Korinto chifukwa cha zinthu zabwino zimene ankachita. (1 Akor. 11:2) Koma pamene iwo anachita zinthu zolakwika, iye sanawayamikire koma anawalangiza mwachikondi komanso momveka bwino.—1 Akor. 11:20-22.
12. Kodi tingasonyeze bwanji chikondi chenicheni pochereza anthu?
12 Tizikhala ochereza. Yehova amatiuza kuti tiyenera kuthandiza abale ndi alongo athu. (Werengani 1 Yohane 3:17.) Koma tiyenera kuchita zimenezi ndi zolinga zabwino osati pofuna kupindulapo kenakake. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nthawi zambiri ndimangochereza anzanga apamtima, anthu otchuka kapena amene akhoza kudzandicherezanso? Kapena kodi ndimayesetsa kucherezanso abale ndi alongo amene sindikuwadziwa bwino kapena amene sangakwanitse n’komwe kundicherezanso?’ (Luka 14:12-14) Nanga bwanji ngati Mkhristu mnzathu akufunikira thandizo chifukwa chochita zinthu mosaganiza bwino kapena ngati sanatithokoze pamene tinamuthandiza? Zikatero, tiyenera kutsatira malangizo akuti: “Muzicherezana popanda kudandaula.” (1 Pet. 4:9) Mukamatsatira malangizowa mudzakhala osangalala kwambiri chifukwa chothandiza anthu muli ndi zolinga zabwino.—Mac. 20:35.
13. (a) N’chiyani chingachititse kuti kuthandiza ofooka kukhale kovuta? (b) Kodi tingachite zinthu ziti pothandiza ofooka?
13 Tizithandiza ofooka. Zimene timachita potsatira lamulo la m’Baibulo lakuti “thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse” zingasonyezenso ngati tili ndi chikondi chenicheni kapena ayi. (1 Ates. 5:14) Ngakhale kuti anthu ambiri ofooka amayambanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba, pali ena amene amafunika kuti tiziwathandizabe moleza mtima. Tingafunike kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Malemba, kuyenda nawo mu utumiki kapena kupeza nthawi yowamvetsera akamafotokoza mavuto awo. Komanso, m’malo mongoganiza kuti Mkhristu uyu ndi wofooka kapena wolimba, tiyenera kuzindikira kuti aliyense amakhala ndi zinthu zina zimene amachita bwino ndi zina zimene sachita bwino. Ngakhale mtumwi Paulo anavomereza kuti panali zinthu zina zimene sankachita bwino. (2 Akor. 12:9, 10) Choncho tonsefe tikhoza kuthandizidwa ndi Akhristu anzathu.
14. Kodi tingatani kuti tizikhala mwamtendere ndi abale athu?
14 Tizikhazikitsa mtendere. Tiyenera kuyesetsa kukhala mwamtendere ndi anzathu ngakhale pamene tikuona kuti sanatimvetse kapena sanatichitire zinthu mwachilungamo. (Werengani Aroma 12:17, 18.) Kupepesa kumathandiza kuti mtima wa munthu amene wakhumudwa ukhale m’malo, koma kupepesako kuyenera kukhala kochokera mumtima. Mwachitsanzo, m’malo mongonena kuti, “Pepani kuti mwakhumudwa,” ndi bwino kuvomereza zimene talakwitsa ponena kuti, “Pepani kuti zimene ndinanena zija zakukhumudwitsani.” Mtendere ndi wofunika kwambiri makamaka m’banja. Si bwino kuti mwamuna ndi mkazi akakhala pa gulu azinamizira kuti amakondana koma akakhala kwaokha n’kumangokhala osalankhulana, kulankhulana mawu achipongwe kapena kuchitirana nkhanza.
15. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhululuka ndi mtima wonse?
15 Tizikhululuka ndi mtima wonse. Munthu wina akatilakwira tiyenera kumukhululukira ndipo tisamamusungire chakukhosi. Nthawi zina anthu ena akhoza kutilakwira mosazindikira. Zikatero ndi bwino kutsatira malangizo oti ‘tizikhala mololerana m’chikondi. Tiziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa ndipo umodziwo timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.’ (Aef. 4:2, 3) Kuti tikhululukire munthu ndi mtima wonse tiyenera kusamala ndi zimene timaganiza n’cholinga choti ‘tisamusungire zifukwa.’ (1 Akor. 13:4, 5) Vuto ndi lakuti tikamasungira Akhristu anzathu zifukwa tikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi anzathuwo komanso ndi Yehova. (Mat. 6:14, 15) Tingasonyezenso kuti takhululuka ndi mtima wonse tikamapempherera anthu amene atilakwira.—Luka 6:27, 28.
16. Kodi tiyenera kuona bwanji udindo umene tapatsidwa m’gulu la Yehova?
16 Tisamafune zongodzipindulitsa tokha. Tikapatsidwa udindo m’gulu la Yehova tiyenera kuona kuti umenewo ndi mwayi woti tisonyeze kuti tili ndi chikondi chenicheni. Tiyenera kuyesetsa kuganizira ‘zopindulitsa ena osati kudzipindulitsa tokha.’ (1 Akor. 10:24) Mwachitsanzo, abale olandira alendo amafika msanga pamisonkhano yadera kapena yachigawo. M’malo moona kuti umenewu ndi mwayi woti apeze malo abwino oti akhalepo ndi mabanja awo, ambiri amalolera kukhala m’mipando imene ena sangaifune m’chigawo chimene akuyang’aniracho. Akamatero amasonyeza kuti ali ndi chikondi chenicheni ndipo si odzikonda. Kodi inuyo mukuganiza kuti mungatsanzire bwanji abale amenewa?
17. Kodi munthu amene ali ndi chikondi chenicheni amatani akachita tchimo lalikulu?
17 Tiziulula machimo aakulu n’kuwasiya. Akhristu ena amene anachita tchimo lalikulu amabisa poopa kuti achita manyazi kapena akhumudwitsa anthu ena. (Miy. 28:13) Munthu amene amabisa machimo si wachikondi chifukwa zimenezi sizimangosokoneza iyeyo koma zimasokonezanso anthu ena. Zikhoza kulepheretsa mzimu woyera kuti uzigwira ntchito bwino mumpingo ndipo zingasokonezenso mtendere mumpingo. (Aef. 4:30) Munthu amene ali ndi chikondi chenicheni akachita tchimo lalikulu, amauza akulu kuti amuthandize moyenera.—Yak. 5:14, 15.
18. Kodi chikondi chenicheni n’chofunika bwanji?
18 Pa makhalidwe onse abwino, khalidwe lalikulu kwambiri ndi chikondi. (1 Akor. 13:13) Tikakhala achikondi timasonyeza kuti timatsatira Khristu komanso timatsanzira Yehova yemwe anayambitsa chikondi. (Aef. 5:1, 2) Paulo analemba kuti ngati “ndilibe chikondi, sindili kanthu.” (1 Akor. 13:2) Choncho tiyeni tonse tipitirize kusonyeza “chikondi chenicheni m’zochita zathu” osati “ndi mawu okha.”