NKHANI YOPHUNZIRA 16
Muzisangalala ndi Zonse Zomwe Mukuchita Potumikira Yehova
“Aliyense payekha ayese ntchito yake.”—AGAL. 6:4.
NYIMBO NA. 37 Kutumikira Yehova ndi Moyo Wathu Wonse
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi n’chiyani chimatithandiza kuti tizisangalala kwambiri?
YEHOVA amafuna kuti tizisangalala. Tikudziwa zimenezi chifukwa chimwemwe ndi limodzi mwa makhalidwe omwe mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22) Popeza kuti kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira, timasangalala kwambiri tikamagwira nawo mwakhama ntchito yolalikira komanso kuthandiza abale athu m’njira zosiyanasiyana.—Mac. 20:35.
2-3. (a) Mogwirizana ndi Agalatiya 6:4, kodi ndi zinthu ziwiri ziti zomwe zingatithandize kuti tizisangalalabe potumikira Yehova? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Pa Agalatiya 6:4, mtumwi Paulo anatchula zinthu ziwiri zimene zingatithandize kupitirizebe kukhala osangalala. (Werengani.) Choyamba, cholinga chathu chiyenera kukhala kupatsa Yehova zinthu zabwino koposa zomwe tingathe. Tikamamupatsa zonse zomwe tingathe, tingamakhale osangalala. (Mat. 22:36-38) Chachiwiri, tizipewa kudziyerekezera ndi ena. Tiyenera kuyamikira Yehova pa zilizonse zimene timakwanitsa kuchita chifukwa cha thanzi, maphunziro kapena luso limene tili nalo. Ndipotu zilizonse zimene tili nazo, anatipatsa ndi iyeyo. Komanso ngati ena ali ndi luso pambali zina za utumiki kuposa ifeyo, tiyenera kumasangalala kuti akugwiritsa ntchito luso lawo potamanda Yehova osati pongofuna kudzionetsera kapena kuchita zofuna zawo. Choncho m’malo momapikisana nawo, tiyenera kuphunzira mmene amachitira zinthu.
3 Munkhaniyi tikambirana zimene zingatithandize ngati tikuona kuti sitikutha kuchita zambiri potumikira Yehova. Tionanso zimene tingachite kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphatso iliyonse yomwe tingakhale nayo komanso zomwe tingaphunzire kwa ena.
TIKAMAONA KUTI SITINGATHE KUCHITA ZAMBIRI
4. Kodi n’chiyani chimene chingatifooketse nthawi zina? Perekani chitsanzo.
4 Atumiki ena a Yehova zimawavuta kusintha akaona kuti akulephera kuchita zambiri chifukwa cha uchikulire kapena thanzi lawo. Zimenezi ndi zomwe zinachitikira Carol. Pa nthawi ina, iye ankatumikira kudera limene kunkafunika olalikira ambiri. Ankachititsa maphunziro a Baibulo 35 ndipo anathandiza anthu ambiri kufika podzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa. Zinthu zinkamuyendera bwino kwambiri mu utumiki. Koma kenako anayamba kudwala ndipo nthawi zambiri sankatha kuchoka panyumba. Iye ananena kuti: “Ndimadziwa kuti chifukwa cha matenda angawa, sindingathe kuchita zomwe ena amachita, ndimaona kuti si ine wokhulupirika kwambiri ngati mmene iwowo alili. Sindingathe kuchita zonse zomwe ndimafuna ndipo zimenezi zimandikhumudwitsa.” Carol amafuna atamachita zambiri potumikira Yehova. Kunena zoona, maganizo amenewatu ndi abwino ndipo sitikukayikira kuti Mulungu wathu wachifundo amayamikira zimene iye akuchita pomutumikira.
5. (a) Kodi tizikumbukira chiyani tikakhumudwa chifukwa cholephera kuchita zinazake? (b) Pazithunzizi, kodi m’baleyu wakhala akuchita bwanji zonse zomwe angathe potumikira Yehova?
5 Ngati nthawi zina mumafooka chifukwa cholephera kuchita zina zake, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amafuna kuti ndichite chiyani?’ Iye amafuna kuti muzichita zimene mungathe malinga ndi mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Mlongo wina yemwe ali ndi zaka za m’ma 80, amakhumudwa chifukwa sangathenso kuchita zambiri mu utumiki ngati mmene ankachitira ali ndi zaka za m’ma 40. Iye akuona kuti ngakhale kuti amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe, Yehova sakusangalala nazo. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Taganizirani izi. Ngati mlongoyo ankachita zonse zomwe akanatha m’zaka zake za m’ma 40, ndipo akuyesetsabe kuchita zimenezi m’zaka zake za m’ma 80, ndiye kuti sanasiye kuchita zonse zomwe angathe potumikira Yehova. Ngati titayamba kuona kuti sitikuchita zokwanira potumikira Yehova, tizidzikumbutsa kuti iye ndi amene amasankha kuvomereza zimene akuona kuti zimamusangalatsa kapena ayi. Tikamachita zonse zomwe tingathe, Yehova adzasangalala nafe n’kutiuza kuti: “Wachita bwino kwambiri.”—Yerekezerani ndi Mateyu 25:20-23.
6. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Maria?
6 Zingakhale zosavuta kuti tizisangalala ngati titamaganizira zimene tingakwanitse kuchita osati zimene sitingakwanitse. Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina dzina lake Maria, yemwe ali ndi matenda omwe amamulepheretsa kuchita zambiri mu utumiki. Poyamba iye ankada nkhawa kwambiri ndipo ankadziona ngati wosafunika. Koma kenako anaganizira za mlongo wina wa mumpingo mwawo, yemwe ankangokhala chigonere chifukwa cha matenda ndipo ankafuna kumuthandiza. Maria anati: “Ndinakonza zoti ndizilalikira naye limodzi pafoni komanso polemba makalata. Nthawi iliyonse imene ndalalikira naye limodzi, ndinkabwerera kunyumba ndili wosangalala komanso wokhutira kuti ndathandiza mlongo wanga.” Ifenso tingawonjezere chimwemwe chathu tikamaganizira zimene tingakwanitse osati zimene sitingakwanitse. Koma bwanji ngati tingathe kuchita zambiri kapenanso ngati timachita bwino zinthu zina potumikira Yehova?
NGATI MULI NDI MPHATSO INA YAKE, “IGWIRITSENI NTCHITO”
7. Kodi mtumwi Petulo anapereka malangizo othandiza ati kwa Akhristu?
7 M’kalata yake yoyamba, mtumwi Petulo analimbikitsa abale ake kugwiritsa ntchito mphatso zili zonse komanso luso limene anali nalo polimbikitsa Akhristu anzawo. Iye analemba kuti: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana monga oyang’anira abwino amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (1 Pet. 4:10) Sitiyenera kulephera kugwiritsira ntchito mokwanira mphatso zimene tili nazo poopa kuti ena achita nsanje kapena akhumudwa. Ngati titamachita zimenezi, sitingakhale kuti tikupatsa Yehova zonse zomwe tingathe.
8. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 4:6, 7, n’chifukwa chiyani sitiyenera kudzitama ndi mphatso zimene tili nazo?
8 Tiyenera kugwiritsa ntchito mokwanira mphatso zimene tili nazo koma tizisamala kuti tisayambe kudzitama. (Werengani 1 Akorinto 4:6, 7.) Mwachitsanzo, mwina mungamachite bwino kwambiri pankhani yoyambitsa maphunziro a Baibulo. Choncho musamalephere kugwiritsa ntchito mphatsoyo. Komabe pali kusiyana pakati pa kugwiritsa ntchito mphatso ndi kudzitama nayo. Tiyerekeze kuti zinthu zakuyenderani bwino kwambiri mu utumiki ndipo mwayambitsa phunziro la Baibulo. Ndiye mukufuna kufotokozera abale ndi alongo a m’kagulu kanu ka utumiki. Koma mutafika kukaguluko mwapeza kuti mlongo wina akufotokoza zomwe zamuchitikira mu utumiki ndipo wagawira magazini. Mlongoyo wagawira magazini koma inuyo mwayambitsa phunziro. Ndiye pamenepa mungatani? Mukudziwa kuti abale ndi alongowo angalimbikitsidwe kudziwa kuti mwayambitsa phunziro la Baibulo koma mungasankhe kuti mudzawafotokozere zimenezi nthawi ina, kuopera kuti mlongo uja angasiye kusangalala poganiza kuti palibe chimene wachita. Kumenekutu kungakhale kukoma mtima. Koma zimenezi sizikutathauza kuti musiye kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Imeneyi ndi mphatso imene muli nayo, igwiritseni ntchito.
9. Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito bwanji mphatso zimene tili nazo?
9 Tizikumbukira kuti maluso aliwonse omwe tingakhale nawo, ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. Tizigwiritsa ntchito mphatsozi polimbikitsa ena mumpingo osati pofuna kuti titchuke. (Afil. 2:3) Tikamagwiritsa ntchito mphamvu komanso luso lathu pochita zimene Mulungu amafuna, tidzakhala osangalala kwambiri osati chifukwa chakuti tikuposa ena kapena kuti tikuoneka apamwamba, koma chifukwa chakuti tikugwiritsa ntchito mphatso zathu potamanda Yehova.
10. N’chifukwa chiyani si bwino kudziyerekezera ndi anthu ena?
10 Ngati sitingasamale, tikhoza kukodwa mumsampha woyerekezera zimene timachita bwino ndi zimene ena amalephera kuchita. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti m’bale wina amakamba bwino nkhani za onse. M’baleyo angakhale ndi luso limeneli, ndiye mwina mumtima mwake angayambe kupeputsa m’bale wina yemwe zimamuvuta kukamba nkhani. Koma m’baleyo angakhale kuti amachita bwino pankhani yochereza alendo, kuphunzitsa ana ake kapenanso amachita khama mu utumiki. Timayamikira kuti tili ndi abale ndi alongo ambiri aluso omwe amagwiritsa ntchito mphatso zawo potumikira Yehova komanso kuthandiza ena.
MUZIPHUNZIRA PA ZITSANZO ZA ENA
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizitsanzira Yesu?
11 Ngakhale kuti sitiyenera kumadziyerekezera ndi ena, tingapindule pophunzira pa zitsanzo za atumiki okhulupirika a Yehova. Chitsanzo chabwino kwambiri ndi Yesu. Ngakhale kuti iye anali wangwiro, tingaphunzire zambiri pa makhalidwe ake abwino komanso mmene ankachitira zinthu. (1 Pet. 2:21) Tikamayesetsa kumutsanzira mosamala kwambiri, tingakhale atumiki abwino a Yehova ndipo tingamachite zambiri pa utumiki wathu.
12-13. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Mfumu Davide?
12 M’Mawu a Mulungu timapezamo zitsanzo zambiri za amuna ndi akazi okhulupirika omwe tingatengere chitsanzo chawo ngakhale kuti sanali angwiro. (Aheb. 6:12) Taganizirani za Mfumu Davide, yemwe Yehova anamutchula kuti “munthu wapamtima panga” kapena monga mmene Baibulo lina limanenera kuti, “munthu amene amandisangalatsa kwambiri.” (Mac. 13:22) Komatu Davide sanali wangwiro ndipo anachita machimo ena akuluakulu. Ngakhale zili choncho iye ndi chitsanzo chabwino kwa ife. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa iye sankayesa kudziikira kumbuyo pamene ankapatsidwa malangizo. M’malomwake ankavomera malangizo amphamvu amene ankapatsidwa komanso kudzimvera chisoni chifukwa cha zimene anachita. Zimenezi zinachititsa kuti Yehova amukhululukire.—Sal. 51:3, 4, 10-12.
13 Tingaphunzirepo kathu kwa Davide podzifunsa kuti: ‘Kodi ndimatani ndikapatsidwa malangizo? Kodi ndimavomereza mwamsanga zimene ndalakwitsa kapena ndimadziikira kumbuyo? Kodi ndimafulumira kuimba ena mlandu? Kodi ndimayesetsa kuti ndisabwerezenso zimene ndalakwitsa?’ Mungamadzifunse mafunso ngati amenewa mukamawerenga nkhani za amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo. Kodi iwo anakumana ndi mavuto amene inunso mukukumana nawo? Nanga anasonyeza makhalidwe abwino ati? Pa nkhani iliyonse imene mwawerenga muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndingamutsanzire bwanji mtumiki wa Yehova wokhulupirikayu?’
14. Kodi tingapindule bwanji poona zimene Akhristu anzathu amachita?
14 Tingapindulenso poona zimene Akhristu anzathu amachita, kaya ndi achikulire kapena achinyamata. Mwachitsanzo, kodi pali wina wake mumpingo wanu yemwe akupirira mokhulupirika mayesero monga matenda, kukakamizidwa ndi anzake kuti achite zosayenera kapena kutsutsidwa ndi anthu a m’banja lake? Kodi mumaona makhalidwe ena ake abwino mwa munthu ameneyo, omwe inunso mukufunitsitsa kukhala nawo? Kuganizira chitsanzo chake chabwino, kungakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muthe kupirira mayesero amene mukukumana nawo. Timayamikira komanso kusangalala kuti tili ndi abale ndi alongo okhulupirika omwe tingatengere chitsanzo chawo.—Aheb. 13:7; Yak. 1:2, 3.
MUZISANGALALA POTUMIKIRA YEHOVA
15. Kodi Paulo anapereka malangizo ati omwe angatithandize kuti tipitirize kusangalala potumikira Yehova?
15 Tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizilimbikitsa mtendere ndi mgwirizano mumpingo. Taganizirani chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Iwo anali ndi mphatso komanso mautumiki osiyanasiyana. (1 Akor. 12:4, 7-11) Koma zimenezi sizinawachititse kuti azipikisana ndi kugawikana. M’malomwake Paulo analimbikitsa aliyense kuchita zimene zikanathandiza kuti “amange thupi la Khristu.” Paulo analembera Aefeso kuti: “Thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwachikondi, . . . malinga ndi ntchito yoyenerera ya chiwalo chilichonse.” (Aef. 4:1-3, 11, 12, 16) Anthu omwe anatsatira malangizowa ankalimbikitsa mtendere ndi mgwirizano, makhalidwe omwe timawaonanso m’mipingo yathu masiku ano.
16. Kodi tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuchita chiyani? (Aheberi 6:10)
16 Tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuti tisamadziyerekezere ndi ena. M’malomwake, tiziphunzira kwa Yesu n’kumayesetsa kutsanzira makhalidwe ake. Muziphunziranso pa zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo komanso atumiki okhulupirika a Yehova a masiku ano. Pamene mukuyesetsa kuchita zonse zomwe mungathe potumikira Yehova, mungakhale otsimikiza kuti iye “si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu.” (Werengani Aheberi 6:10.) Pitirizani kusangalala potumikira Yehova podziwa kuti amayamikira zonse zomwe mukuyesetsa kuchita pomusangalatsa.
NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo
a Tonsefe tingapindule poona zimene ena akuchita potumikira Yehova. Koma tiyenera kupewa kudziyerekezera ndi ena. Nkhaniyi itithandiza kuti tizisangalalabe n’kumapewa mtima wonyada kapena kufooka chifukwa choyerekezera zimene ena akuchita ndi zimene ife tikuchita.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale anayamba kutumikira pa Beteli ali wachinyamata. Kenako anakwatira n’kumachita upainiya ndi mkazi wake. Atakhala ndi ana, iye ankawaphunzitsa kulalikira. Panopa wakalamba koma akupitirizabe kuchita zonse zomwe angathe ndipo akulalikira pogwiritsa ntchito makalata.