-
Kodi Mukutsanzira Yehova mwa Kukhala ndi Mtima Wosamalira Ena?Nsanja ya Olonda—2007 | June 15
-
-
Yehova amatisamalira mwachikondi ndipo zimenezi zimaonekera mu mpingo wachikhristu. Pokhala Mutu wa mpingo, Yesu Khristu anauza akulu kuti azisamalira nkhosa. (Yohane 21:15-17) Mawu akuti oyang’anira mu Chigiriki amafananako ndi mawu amene amatanthauza “kuyang’ana mosamala.” Potsindika mmene akulu ayenera kuchitira zimenezi, Petulo anawalangiza kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe anakuikizani, osati mokakamizika, koma mwaufulu; osatinso chifukwa chofuna kupindulapo, koma ndi mtima wonse; osati mochita ufumu pa aja ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”—1 Petulo 5:2, 3.
-
-
Kodi Mukutsanzira Yehova mwa Kukhala ndi Mtima Wosamalira Ena?Nsanja ya Olonda—2007 | June 15
-
-
Koma mawu a Petulo amene tatchula kalewo, akuchenjeza akulu za ‘kuchita ufumu’ mumpingo. Njira imodzi yosonyeza kuti mkulu wayamba kuchita ufumu ndiyo kuika malamulo osafunikira mumpingo. Pofuna kuteteza kwambiri anthu mumpingo, mkulu angayambe kuchita zinthu mopyola malire. Mumpingo wina kumayiko a kum’mawa, akulu anaika malamulo a mmene anthu ayenera kulonjerana ku Nyumba ya Ufumu. Mwachitsanzo, iwo anaika lamulo lonena za amene aziyamba kupereka moni. Ankaona kuti malamulo amenewa angathandize kuti mumpingo mukhale mtendere. Ngakhale kuti akulu amenewo mosakayikira anali ndi zolinga zabwino pochita zimenezi, kodi anali kutsanzira mmene Yehova amasamalira anthu ake? Yehova amakhulupirira anthu ake ndipo tingaone zimenezi m’mawu a mtumwi Paulo, yemwe ankatsanzira Yehova. Iye anati: “Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe, pakuti ndinu okhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chanu.”—2 Akorinto 1:24.
-