Myanmar (Burma)
DZIKO la Myanmar lili pakati pa dziko la India ndi China, omwe ndi mayiko akuluakulu a ku Asia ndipo m’dzikoli mumachitika zinthu zambiri zochititsa chidwi.a Mzinda waukulu m’dzikoli ndi wa Yangon (womwe poyamba unkatchedwa Rangoon). Mumzindawu muli nyumba zitalizitali zambiri, masitolo odzaza ndi katundu, komanso m’misewu yake mumakhala magalimoto ambiri. Kunja kwa mzindawu kuli midzi ndipo kumeneko anthu amalima pogwiritsa ntchito njati zoweta. Anthu a m’midziyi amachita chidwi akaona azungu komanso amakhala moyo wosatanganidwa kwambiri.
Masiku ano, dziko la Myanmar limatikumbutsa mmene mayiko a ku Asia analili zaka zapitazo. M’misewu yokumbikakumbika ya m’dzikoli mumadutsa mabasi othaitha, omwe amadutsana ndi ngolo zomwe zanyamula mbewu kupita nazo kumsika. M’mbali mwa misewuyi mumakhala abusa akudyetsa mbuzi zawo. Azibambo ambiri a m’dzikoli amavalabe lungi, chomwe ndi chovala chokhala ngati siketi. Pofuna kudzikongoletsa, azimayi amadzola thanaka kunkhope zawo. Thanaka ndi zodzoladzola zopangidwa kuchokera ku makungwa a mtengo. Anthu a m’dzikoli ndi okonda kupemphera. Abuda amalemekeza kwambiri Amonke, omwe ndi anthu odzipereka kwambiri pa nkhani ya chipembedzo chawo. Iwo amalemekeza kwambiri anthu amenewa kuposa anthu otchuka pa zinthu zosiyanasiyana, ndipo tsiku lililonse amadzoza mafuta agolide zifaniziro za Buddha kuti zizinyezimira.
Anthu a ku Myanmar ndi ofatsa, ochita zinthu moganizira ena, komanso ali ndi mtima wofuna kuphunzira zinthu zatsopano. M’dzikoli muli mitundu ikuluikulu 8 komanso ing’onoing’ono 127. Anthu a mtundu uliwonse ali ndi chinenero chawochawo, kavalidwe, chakudya komanso chikhalidwe chawochawo. Anthu ambiri amakhala m’chigwa chachikulu momwe munadutsa mtsinje waukulu wa Ayeyarwady (Irrawaddy). Mtsinjewu ndi wautali makilomita 2,170 ndipo ukuchokera m’phiri la Himalaya kukathira m’nyanja ya Andaman. Anthu enanso ambirimbiri amakhala m’mphepete mwa nyanja komanso m’malo okwera amene ali m’malire a mayiko a Bangladesh, China, India, Laos ndi Thailand.
Kwa zaka pafupifupi 100, a Mboni za Yehova ku Myanmar anasonyeza m’njira zosiyanasiyana kuti ali ndi chikhulupiriro champhamvu komanso kuti ndi opirira. Iwo sanachite nawo zachiwawa kapena zipolowe zimene anthu ankachita chifukwa cha ndale. (Yoh. 17:14) Anthu a Yehova m’dzikoli akhala akulalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Achita zimenezi ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana, ankazunzidwa chifukwa cha chipembedzo chawo, komanso zinali zovuta kuti alankhulane ndi abale awo a m’mayiko ena. M’ndime zotsatirazi timva nkhani yolimbikitsa yokhudza abale a m’dziko limeneli.
Kwa zaka pafupifupi 100, abale athu ku Myanmar anasonyeza m’njira zosiyanasiyana kuti ali ndi chikhulupiriro champhamvu komanso kuti ndi opirira
Mmene Ntchito Yolalikira Inayambira
M’chaka chosaiwalika cha 1914, anthu awiri a ku England anatsika sitima padoko lina lotentha kwambiri ku Yangon. Anthuwa anali a Hendry Carmichael ndi mnzawo amene ankachita naye upainiya. Pa ulendowu ankachokera ku India ndi cholinga chodzayambitsa ntchito yolalikira m’dziko la Burma, ndipo zimenezi sizinali zophweka. Gawo lawo linali dziko lonseli.
“Zili ndi inu, ngati mukufunanso kuti tidzakulowereni m’dziko latsopano”
Iwo anayamba ndi kulalikira ku Yangon, ndipo pasanapite nthawi anakumana ndi azibambo awiri achikaladi omwe anachita chidwi kwambiri ndi uthenga wa Ufumu.b Azibambo awiriwa anali a Bertram Marcelline ndi a Vernon French. Atamva uthengawo, nthawi yomweyo anasiyiratu kupita kuchipembedzo chawo chakale ndipo anayamba kulalikira kwa anzawo. Patangopita nthawi yochepa, anthu pafupifupi 20 anayamba kusonkhana mlungu uliwonse kunyumba kwa a Marcelline n’kumaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda.c
Mu 1928, mpainiya wina wa ku England yemwe ankakhala ku India, dzina lake George Wright, anabwera kudzacheza ku Burma ndipo anagawira mabuku ambiri ofotokoza Baibulo m’madera osiyanasiyana a dzikolo kwa miyezi isanu. Mbewu za choonadi zimene anabzala zinaphatikizapo buku limene linatuluka m’chaka cha 1920 la mutu wakuti Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa! Limeneli linali buku lathu loyamba kumasuliridwa m’Chibama.
Patapita zaka ziwiri apainiya awiri, a Claude Goodman ndi a Ronald Tippin, anafika kuchokera ku Yangon. Iwo anapeza kuti kuli kagulu kakang’ono ka abale omwe ankachita misonkhano mokhulupirika koma analibe dongosolo lililonse lolalikira. A Goodman anati: “Tinalimbikitsa abalewo kuti azibwera Lamlungu lililonse kuti tizilowa mu utumiki. M’bale wina anafunsa ngati zili zotheka kuti tizimulalikirira, iye azingothandiza apainiyafe ndi ndalama. A Tippin anamuyankha kuti: ‘Zili ndi inu, ngati mukufunanso kuti tidzakulowereni m’dziko latsopano.’” Mawu osapita m’mbali amenewa anali okwanira kulimbikitsa abalewo kuyamba ntchito yolalikira. Pasanapite nthawi, a Goodman ndi a Tippin anapeza anthu ambiri oyenda nawo mu utumiki.
“Rachel, Inetu Ndapeza Choonadi!”
Chaka chomwecho, a Tippin ndi a Goodman anakumana ndi a Sydney Coote, omwe anali bwana wa pamalo okwerera sitima ku Yangon. A Coote analandira mabuku 10 omwe ankatchedwa mpukutu wa utawaleza chifukwa anali amitundu yosiyanasiyana yowala kwambiri. Atangowerenga kachigawo ka buku limodzi, a Coote anafuula kwa mkazi wawo kuti, “Rachel, inetu ndapeza choonadi!” Pasanapite nthawi, banja lonse la a Coote linayamba kutumikira Yehova.
A Coote ankaphunzira Malemba mwakhama. Mwana wawo wamkazi dzina lake Norma Barber, yemwe watumikira monga mmishonale kwa zaka zambiri ndipo tsopano akutumikira pa nthambi ya ku Britain anati: “Bambo analemba buku lawolawo lowathandiza kupeza malemba. Nthawi iliyonse akapeza lemba lomwe likufotokoza chiphunzitso chinachake cha m’Baibulo, ankalilemba m’bukulo pakamutu koyenerera kogwirizana ndi mfundo yomwe ili pa lembalo. Bukulo ankalitchula kuti Kodi Ili Pati?”
A Coote ankafuna kuphunzira Baibulo komanso kuuzako ena mfundo zomwe ankaphunzira. Choncho, analemba kalata ku ofesi ya nthambi ya ku India yofunsa ngati ku Burma kuli wamboni aliyense. Pasanapite nthawi, analandira bokosi lalikulu lomwe linali ndi mabuku komanso mndandanda wa mayina a abale. Mlongo Barber anati, “Bambo analembera kalata munthu aliyense amene anali pa mndandandawo ndipo anamupempha kuti adzatichezere kwa tsiku limodzi. Patapita nthawi, abale mwina 5 kapena 6 anabwera kunyumba kwathu n’kutisonyeza mmene tingamalalikirire kwa anthu amene tinkakumana nawo tikamagwira ntchito zathu za tsiku ndi tsiku. Nthawi yomweyo makolo anga anayamba kugawa mabuku aja kwa anzawo komanso anthu oyandikana nawo nyumba. Iwo anatumizanso makalata komanso mabuku kwa achibale athu onse.”
A Daisy D’Souza, omwe ndi achemwali awo a m’bale Coote, ndipo ankakhala ku Mandalay, analandira kalata yochokera kwa a Coote ndiponso buku lakuti Chiyembekezo cha Dziko Lonse Chili pa Ufumu (The Kingdom, the Hope of the World). Iwo anayankha kalatayo nthawi yomweyo ndipo anapempha kuti awatumizire mabuku ena ndiponso Baibulo. Mwana wamkazi wa a D’Souza, dzina lake Phyllis Tsatos, anati: “Mayi anga anasangalala kwambiri kulandira mabukuwa ndipo anawawerenga usiku wonse mpaka m’bandakucha. Kenako anasonkhanitsa ana tonse 6 n’kulengeza kuti: ‘Kuyambira lero ndasiya Tchalitchi cha Katolika, chifukwa ndapeza choonadi!’” Patapita nthawi, amuna awo a mlongo D’Souza ndiponso ana awo anaphunziranso choonadi. Panopa, ana ndiponso zidzukulu za a D’Souza zikutumikirabe Yehova Mulungu mokhulupirika.
Apainiya Olimba Mtima
Pofika kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, n’kuti apainiya akhama akufalitsa uthenga wabwino m’mbali mwa njanji yochokera ku Yangon kupita ku tauni ya Myitkyina, yomwe ili pafupi ndi malire a dziko la China. Apainiyawo ankalalikiranso m’tauni ya Mawlamyine (Moulmein) yomwe ili m’mphepete mwa nyanja kum’mawa kwa mzinda kwa Yangon komanso m’tauni ya Sittwe (Akyab), yomwenso ili m’mphepete mwa nyanja, kumpoto chakumadzulo kwa mzindawo. Zimenezi zinachititsa kuti mipingo ing’onoing’ono ikhazikitsidwe ku Mawlamyine ndi ku Mandalay.
Mu 1938 udindo woyang’anira ntchito yolalikira m’dziko la Burma unachoka m’manja mwa nthambi ya India n’kupita m’manja mwa nthambi ya Australia. Izi zinachititsa kuti apainiya ochokera ku Australia ndi ku New Zealand ayambe kufika m’dziko la Burma. Pa gulu la alaliki akhamawa panali a Fred Paton, a Hector Oates, a Frank Dewar, a Mick Engel, ndi a Stuart Keltie. Abale onsewa anali akhama ndipo anali oyamba kufikitsa uthenga wabwino m’madera ambiri m’dzikoli.
A Fred Paton anafotokoza kuti: “Pa zaka zinayi zimene ndakhala ku Burma, ndalalikira madera ambiri m’dzikoli. Pa nthawi imeneyi ndapirira zinthu zosiyanasiyana monga matenda a malungo, tayifodi, kamwazi ndi matenda ena. Kawirikawiri ndinkasowa malo ogona pambuyo pogwira ntchito tsiku lonse mu utumiki. Komabe, Yehova ankandisamalira nthawi zonse ndipo ankandilimbikitsa pondipatsa mphamvu ya mzimu wake.” A Frank Dewar, mlaliki wolimba mtima wa ku New Zealand, ananena kuti: “Ndinkakumana ndi achifwamba, zigawenga komanso akuluakulu aboma odzikuza kwambiri. Koma ndinaona kuti kukhala waulemu, woleza mtima, wodzichepetsa komanso wodekha zimathandiza kuthetsa zopinga zilizonse zimene tingakumane nazo. Anthu ambiri amazindikira mwamsanga kuti a Mboni za Yehova si anthu oopsa.”
Zinali zoonekeratu kuti apainiyawa ndi osiyana kwambiri ndi anthu ena ochokera m’mayiko ena, omwe kawirikawiri ankanyoza anthu a m’dzikoli. Apainiyawo ankalemekeza komanso kukonda anthu. Anthu a ku Burma amakonda anthu odzichepetsa komanso osamala polankhula. Iwo sakonda anthu ongolankhula mopanda ulemu ndiponso okonda mikangano. Choncho anthu a ku Burma ankachita chidwi ndi apainiyawo chifukwa anali anthu okoma mtima. Zochita komanso zolankhula za apainiyawo zinasonyeza kuti Mboni za Yehova ndi Akhristu oona.—Yoh. 13:35.
Msonkhano Wosaiwalika
Patapita miyezi ingapo kuchokera pamene apainiyawa anafika m’dzikoli, nthambi ya ku Australia inakonza zoti ku Yangon kuchitike msonkhano. Iwo anasankha kuti msonkhanowu uchitikire mu Yangon City Hall. Holo imeneyi inali yaikulu, yokongoletsedwa ndi miyala ya mabo ndipo inali ndi zitseko zikuluzikulu zamkuwa. Anthu obwera ku msonkhanowu anachokera ku Thailand, Malaysia, ndi ku Singapore. Koma m’bale Alex MacGillivray, amene anali mtumiki wa nthambi ya ku Australia, anabwera ndi gulu la abale ochokera ku Sydney.
Anthu ankayembekezera kuti m’dzikoli mukhoza kuyambika nkhondo nthawi iliyonse. Choncho anthu ambiri anachita chidwi ndi uthenga umene unafalitsidwa kwambiri woitanira anthu kuti adzamvetsere nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Nkhondo Yapadziko Lonse Yayandikira.” A Fred Paton ananena kuti: “Sindinaonepo holo itadzaza mofulumira ngati mmene zinalili pa nthawi imeneyi. Nditangotsegula zitseko zakutsogolo, khamu la anthu linapanikizana kulowa muholomo. Pasanathe mphindi 10, anthu 1,000 anapanikizana muholo imene inkafunika kulowa anthu 850 okha.” A Frank Dewar anawonjezera kuti: “Tinachita kutseka zitseko kuti musalowenso anthu ena ndipo anthu amene tinawatsekera kunja anakwananso 1,000. Ngakhale kuti tinatseka pakhomo, achinyamata ena akhama analowabe kudzera m’makomo a m’mbali.”
Abale anasangalala ndi kuchuluka kwa anthu amene anasonyeza chidwi komanso chifukwa chakuti ku msonkhanoko kunabwera anthu a mitundu yosiyanasiyana. M’mbuyomo, tsiku limeneli lisanafike, anthu ambiri sankachita chidwi ndi choonadi chifukwa chakuti ambiri anali Abuda okonda kwambiri chipembedzo chawo. Anthu ambiri a m’dzikomo omwe ankati ndi Akhristu, makamaka a mtundu wa Chikayin, (Chikaren), Chikachin, ndi Chichin, ankakhala m’madera akumidzi kumene kunali kusanafike uthenga wabwino. Zikuoneka kuti nthawi inali itakwana kuti ntchito yokolola iyambike m’munda wa m’dzikoli. Posakhalitsa, “khamu lalikulu” la anthu a mitundu yonse loloseredwa m’Baibulo linaphatikizapo anthu a mitundu yosiyanasiyana a m’dziko la Burma.—Chiv. 7:9.
Ophunzira Oyambirira a Mtundu wa Chikayin
Mu 1940 mpainiya wina dzina lake Ruby Goff ankalalikira ku Insein, tauni yaing’ono imene ili kunja kwa mzinda wa Yangon. Popeza kuti sanapeze anthu achidwi tsiku limenelo, a Goff anapemphera kuti, “Yehova, chonde ndithandizeni kuti ndipeze ‘nkhosa’ imodzi yokha ndisanabwerere kunyumba.” Atatero, panyumba yotsatira anakumana ndi a Hmwe Kyaing amene anamvetsera uthenga wa Ufumu mwachidwi kwambiri. A Kyaing anali a mtundu wa Chikayin ndipo anali m’chipembedzo cha Baptist. Posakhalitsa, a Kyaing komanso ana awo aakazi, Chu May (Daisy) ndi Hnin May (Lily), anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anapita patsogolo mwauzimu. Ngakhale kuti a Kyaing anamwalira pasanapite nthawi, Lily, mwana wawo wamng’ono anali munthu woyamba wa mtundu wa Chikayin kubatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Daisy nayenso anabatizidwa.
Lily ndi Daisy anakhala apainiya akhama kwambiri ndipo anthu akuwakumbukirabe mpaka pano. Panopa zidzukulu zawo zambirimbiri komanso anthu amene ankaphunzira nawo Baibulo akutumikira Yehova ku Myanmar ndiponso m’mayiko ena.
Mavuto a pa Nthawi ya Nkhondo Yachiwiri Yapadziko Lonse
Mu 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayambika ku Ulaya ndipo inasokoneza zinthu zambiri padziko lonse. Pamene mantha a anthu ankawonjezeka chifukwa cha nkhondo imeneyi, akuluakulu a matchalitchi amene amati ndi achikhristu ku Burma anayesetsa kukakamiza boma kuti liletse mabuku athu m’dzikoli. Chifukwa cha zimenezi, a Mick Engel, amene ankayang’anira malo otumizira mabuku ku Yangon, anapita kwa mkulu wa asilikali a ku United States kukatenga chikalata chowaloleza kunyamula mabuku olemera pafupifupi makilogalamu 2000 pa magalimoto a asilikali amene ankapita ku China.
A Fred Paton ndi a Hector Oates anatenga mabukuwo kupita nawo kusiteshoni ya sitima ya m’tauni ya Lashio, yomwe ili m’malire a dzikoli ndi dziko la China. Atakumana ndi msilikali amene ankayang’anira magalimoto opita ku China, msilikaliyo anakwiya kwambiri. Iye anafuula kuti: “Mwati chiyani? Ndinganyamule bwanji mapepala opanda ntchito ngati amenewa pamene ndikusowa malo onyamulira zinthu zofunika kwambiri monga katundu wa asilikali komanso mankhwala ali apawa?” Pamenepo a Paton anangotulutsa kalata ya chilolezo ija m’chikwama chawo, n’kumuuza msilikaliyo kuti nkhaniyi ikula kwambiri ngati anganyalanyaze zimene akuluakulu a ku Yangon alamula. Atamva zimenezo, woyang’anira magalimoto uja anawapatsa abalewo galimoto yaing’ono, dalaivala komanso zinthu zina zofunikira. Iwo anayenda mtunda wa makilomita 2,400 kupita ku Chongqing (Chungking), chakum’mwera kwa China. Atafika kumeneko anagawira mabukuwo komanso analalikira pamasom’pamaso kwa Chiang Kai-shek, amene anali pulezidenti wa dzikoli pa nthawi imene linkalamuliridwa ndi chipani cha Chinese Nationalist.
Akuluakulu aboma aja atafika anapeza kuti mabukuwo palibe
Kenako mu May 1941, boma la atsamunda ku India linatumiza uthenga ku Yangon wolamula akuluakulu aboma mumzindawo kuti atilande mabuku athu. Abale awiri amene ankagwira ntchito mu ofesi yotumiza mauthenga anaona uthengawo ndipo mwamsanga anadziwitsa a Mick Engel. Ndiyeno a Engel anadziwitsa Lily ndi Daisy ndipo mwamsanga anapita kudepoti kukatenga makatoni 40 otsala aja n’kukawabisa m’nyumba ina ku Yangon komweko. Akuluakulu aboma aja atafika anapeza kuti mabukuwo palibe.
Ndiyeno pa December 11, 1941, dziko la Japan linayamba kuponya mabomba m’dziko la Burma. Apa n’kuti patangopita masiku atatu kuchokera pamene dzikoli linakaphulitsa mabomba ku Pearl Harbor. Kumapeto kwa mlungu umenewo kagulu ka Mboni kanali katasonkhana m’kachipinda kena kakang’ono kumtunda kwa siteshoni ya sitima ya Yangon Central Railway Station. Kumeneko, pambuyo pokambirana mfundo za m’Malemba, Lily anabatizidwira m’bafa.
Patapita milungu 12, asilikali a ku Japan analowa mumzinda wa Yangon ndipo sanapezemo wina aliyense. Anthu oposa 100,000 anali atathawira ku India, ndipo ambiri anafera m’njira chifukwa cha njala, kutopa kwambiri ndiponso matenda. A Sydney Coote, amene anathawa limodzi ndi banja lawo, anamwalira chifukwa cha malungo aakulu pafupi ndi malire a dziko lawo ndi la India. M’bale wina anawomberedwa ndi asilikali a dziko la Japan, ndipo mkazi wa m’bale wina komanso anthu ena a m’banja lake anamwalira asilikali ataphulitsa nyumba yawo ndi bomba.
M’dziko la Burma munangotsala Mboni zochepa kwambiri. Lily ndi Daisy anasamukira ku Pyin Oo Lwin (Maymyo), mzinda wabata umene uli pafupi ndi mzinda wa Mandalay. Kumeneko iwo anafesa mbewu za choonadi zimene patapita nthawi zinabala zipatso. Mboni yachitatu, yomwe ndi a Cyril Gay, anakakhala ku mudzi waung’ono wa Thayarwaddy, umene unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 100 kumpoto kwa mzinda wa Yangon. Iwo anakhala kumeneko mwabata pa nthawi yonse imene kunkachitika nkhondoyo.
Anasangalala Atakumananso
Nkhondo itatha, abale ndi alongo ambiri amene anathawira ku India anayamba kubwerera ku Burma. Pofika mu April 1946, mpingo wa Yangon unali ndi ofalitsa 8 akhama pa ntchito yolalikira. Kumapeto kwa chakacho, mpingowu utakula n’kukhala ndi ofalitsa 24, abale anaganiza zochita msonkhano waukulu.
Msonkhanowo unali wa masiku awiri ndipo unachitikira pasukulu ku Insein. Pokumbukira zimene zinachitika pa nthawiyo, a Theo Syriopoulos, amene anaphunzira choonadi ku Yangon mu 1932 anati: “Nditabwerera kwathu kuchokera ku India, ndinadabwa kumva kuti ndikufunika kukamba nkhani ya onse ya ola limodzi. Chiyambire ndinali nditangokamba nkhani ziwiri zokha za mphindi 5 pa misonkhano ya mpingo ku India. Komabe, msonkhanowo unali wosangalatsa kwambiri ndipo panafika anthu oposa 100.”
Patapita milungu ingapo, mtsogoleri wa anthu a mtundu wa Chikayin amene ankachita chidwi ndi choonadi, anapereka malo ku mpingo. Malowo anali ku Ahlone, dera limene linali m’mphepete mwa mtsinje, chapakati pa mzinda wa Yangon. Pamalowa abale anamangapo Nyumba ya Ufumu ya nsungwi, yokhalamo anthu pafupifupi 100. Abale mumpingowu anasangalala kwambiri. Abale ndi alongo anali atapirira pa nthawi ya nkhondo ndipo chikhulupiriro chawo chinali cholimba moti anali okonzeka komanso ofunitsitsa kupitiriza kugwira ntchito yolalikira.
Amishonale Oyambirira a Giliyadi Anafika
Kumayambiriro kwa chaka cha 1947, gulu la abale osangalala linasonkhana padoko lina ku Yangon kukalandira a Robert Kirk. A Kirk anaphunzira m’sukulu ya Giliyadi ndipo anali mmishonale woyambirira kulowa m’dziko la Burma. Posakhalitsa, kunafikanso amishonale ena atatu. Amishonalewa anali a Norman Barber, a Robert Richards, ndi a Hubert Smedstad. Iwo anafika limodzi ndi a Frank Dewar, amene ankachita upainiya ku India pa nthawi ya nkhondo ija.
Amishonalewa anafikira mumzinda umene unawonongedwa pa nthawi ya nkhondo. M’malo ambiri munali mabwinja okhaokha. Anthu ambiri ankakhala m’nyumba zosalimba zomangidwa ndi nsungwi zomwe zinali m’mbali mwa misewu ndipo ankaphika, kuchapa komanso kukhala m’misewuyo. Komabe, amishonalewo anabwera kudzaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Choncho iwo anasintha zinthu zambiri pa moyo wawo kuti ugwirizane ndi mmene zinthu zinalili m’dzikolo ndipo anatanganidwa ndi ntchito yolalikira.
Pa September 1, 1947, ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society inakhazikitsidwa pa nyumba ya amishonale m’mbali mwa msewu wa Signal Pagoda, mkatikati mwa mzindawo. A Robert Kirk anasankhidwa kuti akhale woyang’anira nthambi. Posakhalitsa, mpingo wa Yangon unasamuka muholo ya nsungwi ku Ahlone kuja n’kukalowa m’chipinda china m’nyumba yosanja imene inali m’mbali mwa msewu wa Bogalay Zay. Nyumbayi inali pafupi kwambiri ndi nyumba yaikulu mmene munali maofesi a boma la atsamunda a ku Britain, omwe ulamuliro wawo unali utatsala pang’ono kutha m’dzikoli.
Nkhondo Yapachiweniweni Inayamba
Pa January 4, 1948, boma la Britain linapereka ulamuliro ku boma latsopano la Burma. Apa tsopano dziko la Burma linalandira ufulu wodzilamulira pambuyo pa zaka 60 za ulamuliro wa dziko la Britain. Koma tsopano m’dzikoli munayamba nkhondo yapachiweniweni.
Anthu a mitundu yosiyanasiyana ankamenyana pofuna kuti akhale ndi madera odzilamulira okha. Ndipo asilikali ena ndi magulu a zigawenga ankamenyana polimbirana madera osiyanasiyana. Pofika kumayambiriro kwa chaka cha 1949, zigawenga zinali zikulamulira mbali yaikulu ya dzikoli, ndipo nkhondo inayambika m’madera akumidzi mumzinda wa Yangon.
Mkati mwa nkhondo yoopsayi, abale ankalalikirabe mosamala kwambiri. Ofesi ya nthambi inasamutsidwa kuchoka ku nyumba ya amishonale imene inali m’mbali mwa msewu wa Signal Pagoda ija n’kupita m’nyumba ina yaikulu yosanjikizana m’mbali mwa msewu wotchedwa 39th Street. Nyumba imeneyi inali pamalo otetezeka ndipo munali maofesi angapo a akazembe a mayiko osiyanasiyana komanso inali pa mtunda woyenda mphindi zitatu zokha kupita ku positi ofesi.
Pang’ono ndi pang’ono asilikali a dziko la Burma anayamba kulamulira madera ambiri ndipo zigawengazo anazithamangitsira kumapiri. Pofika chapakati pa zaka za m’ma 1950, boma linali litalandanso madera ambiri amene anali m’manja mwa zigawenga. Koma nkhondoyo inapitirizabe, ndipo ikupitirizabe m’njira zosiyanasiyana mpaka pano.
Kulalikira Ndiponso Kuphunzitsa M’Chibama
M’mbuyo monsemu mpaka kudzafika chapakatikati pa zaka za m’ma 1950, nthawi zambiri abale ku Burma ankalalikira m’Chingerezi, chinenero chimene chinkalankhulidwa ndi anthu ophunzira m’matauni ndi m’mizinda ikuluikulu. Koma anthu mamiliyoni ambiri ankalankhula Chibama (Chimyanima), Chikayin, Chikachin, Chichin kapena zinenero zina. Kodi anthu amenewa akanamva bwanji uthenga wabwino?
M’chaka cha 1934, a Sydney Coote anakonza zoti mphunzitsi wina wa Chikayin amasulire timabuku tingapo m’Chibama ndi m’Chikayin. Patapita nthawi, ofalitsa ena anamasulira buku lakuti “Mulungu Akhale Woona” ndi timabuku tina tambiri m’Chibama. Kenako mu 1950, a Robert Kirk anapempha a Ba Oo kuti amasulire nkhani zophunzira za mu Nsanja ya Olonda m’Chibama. Nkhani zolembedwa pamanjazo ankazikonza bwinobwino ndipo zinkasindikizidwa ndi kampani ina yosindikiza mabuku ku Yangon. Kenako nkhanizo zinkaperekedwa kwa anthu amene afika pa misonkhano ya mpingo. Patapita nthawi, ofesi ya nthambi inagula makina olembera kuti ntchito yomasulira iziyenda mofulumira.
Omasulira oyambirirawo anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Pofotokoza mmene ntchitoyi inkayendera, a Naygar Po Han, amene analowa m’malo mwa a Ba Oo pa ntchito yomasulira, ananena kuti: “Ndinkagwira ntchito masana kuti ndizitha kusamalira banja langa ndipo usiku ndinkamasulira nkhani zosiyanasiyana mpaka pakati pa usiku, ngakhale kuti getsi limene ndinkaunikira silinkawala mokwanira. Chingelezi sindinkachidziwa kwenikweni, choncho n’kutheka kuti zimene ndinkamasulirazo sizinali zolondola kwenikweni. Komabe, tinkafunitsitsa kuti athu ambiri awerenge magazini athu.” Nthawi ina a Kirk atapempha a Doris Raj kuti amasulire Nsanja ya Olonda m’Chibama, anachita mantha kwambiri moti anangoyamba kulira. Mlongo Raj anafotokoza kuti: “Sukulu sindinapite nayo patali komanso ndinali ndisanagwirepo ntchito yomasulira. Komabe, M’bale Kirk anandilimbikitsa kuti ndingoyesa. Choncho ndinapemphera kwa Yehova kenako n’kuyamba kugwira ntchitoyo.” Panopa papita zaka pafupifupi 50 kuchokera nthawi imeneyo, ndipo mlongo Raj akugwirabe ntchito yomasulira ku Beteli ya ku Yangon. A Naygar Po Han, amene panopa ali ndi zaka 93, akutumikiranso pa Beteli ndipo akugwirabe mwakhama ntchito ya Ufumu wa Mulungu.
Mu 1956, M’bale Nathan Knorr wochokera ku likulu la dziko lonse anabwera ku Burma ndipo analengeza za kutuluka kwa Nsanja ya Olonda m’Chibama. Iye analimbikitsanso amishonale kuti aphunzire chinenerochi kuti azilalikira mogwira mtima. Amishonalewa analimbikitsidwa ndi mawu amenewo ndipo anayesetsa mwakhama kuphunzira Chibama. Chaka chotsatira, M’bale Frederick Franz, amenenso anachokera ku likulu la dziko lonse, anakamba nkhani ya mlendo pa msonkhano wa masiku asanu umene unachitikira muholo ya Yangon Railway Institute. Iye analimbikitsa abale kuti awonjezere ntchito yolalikira potumiza apainiya m’mizinda ndi m’matauni a m’deralo. Mzinda woyamba kupindula ndi apainiya atsopano unali wa Mandalay, womwe kale unali likulu la dziko la Burma komanso ndi wachiwiri pa mizinda ikuluikulu m’dzikomo.
Zotsatira za Ntchito Yolalikira ku Mandalay
Kumayambiriro kwa chaka cha 1957, apainiya 6 apadera anafika ku Mandalay. Kumeneko anakumana ndi amishonale awiri amene anali atangokwatirana kumene, a Robert Richards ndi mkazi wawo wachikayin dzina lake Baby. Apainiyawo anaona kuti mzinda wa Mandalay ndi gawo lovuta kulalikiramo. Izi zinali choncho chifukwa chakuti ku Mandalay n’kuchimake kwa Chibuda ndipo pafupifupi hafu ya anthu odzipereka kwambiri n’chipembedzochi, amakhala mumzindawu. Komabe, apainiyawo anazindikira kuti Yehova anali ndi “anthu ambiri mumzinda” umenewu ngati mmene zinalili mumzinda wa Korinto m’nthawi ya atumwi.—Mac. 18:10.
Mmodzi wa anthu amenewo anali a Robin Zauja, wophunzira wachikachin wa zaka 21. A Zauja anati: “M’mawa wa tsiku lina, a Robert ndi a Baby Richards anandipeza kunyumba kwathu n’kundiuza kuti iwowo ndi a Mboni za Yehova. Iwo anandiuza kuti akulalikira uthenga wabwino kunyumba ndi nyumba mogwirizana ndi lamulo la Yesu pa nkhani yolalikira. (Mat. 10:11-13) Anandiuza uthengawo kenako anandipatsa adiresi yawo limodzi ndi magazini komanso mabuku. Usiku wa tsiku limenelo ndinatenga buku limodzi n’kuyamba kuliwerenga. Ndinawerenga bukuli usiku wonse moti pamene dzuwa limatuluka n’kuti nditalimaliza. Tsiku lomwelo ndinapita kunyumba kwa a Richards ndipo ndinawapanikiza ndi mafunso kwa maola ambiri. Koma a Richards anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo.” Posakhalitsa, a Zauja anakhala munthu woyamba wa mtundu wachikachin kuphunzira choonadi. Patapita nthawi anayamba kutumikira monga mpainiya wapadera kumpoto kwa dziko la Burma ndipo anachita utumikiwu kwa zaka zambiri. Pa nthawiyi anathandiza anthu pafupifupi 100 kudziwa choonadi. Panopa ana awo awiri akutumikira pa Beteli ku Yangon.
Wophunzira wina wakhama pa ntchito yolalikira anali Pramila Galliara, mtsikana wa zaka 17 amene anali atangophunzira kumene choonadi ku Yangon. Pramila anati: “Bambo anga omwe anali m’chipembedzo cha Jain, ananditsutsa kwambiri chifukwa cha chipembedzo changa chatsopanochi. Kawiri konse iwo ananditenthera Baibulo ndi mabuku anga ofotokoza nkhani za m’Baibulo, ndipo anandimenya kambirimbiri anthu ena akuonerera. Komanso ankanditsekera m’nyumba kuti ndisapite ku misonkhano yachikhristu ndipo anaopseza kuti ndikapitiriza, akatentha nyumba ya M’bale Richards. Koma ataona kuti alephera kuwononga chikhulupiriro changa, anayamba kusiya pang’onopang’ono kunditsutsa.” Pramila anasiya maphunziro a ku yunivesite n’kukhala mpainiya wakhama kwambiri ndipo kenako anakwatiwa ndi woyang’anira dera dzina lake Dunstan O’Neill. Kuchokera nthawi imeneyo, Pramila wathandiza anthu 45 kubwera m’choonadi.
Pamene ntchito inali kupita patsogolo ku Mandalay, ofesi ya nthambi inatumizanso amishonale kapena apainiya m’madera enanso, monga ku Pathein (Bassein), Kalaymyo, Bhamaw, Myitkyina, Mawlamyine, ndi ku Myeik (Mergui). N’zoonekeratu kuti Yehova anadalitsa ntchitoyo chifukwa chakuti m’tauni iliyonse pa matauni amenewa munakhazikitsidwa mipingo yolimba kwambiri.
Amishonale Athamangitsidwa!
Pamene ntchito yolalikira inkapita patsogolo, zinthu zinafika poipa kwambiri chifukwa cha zipolowe za anthu andale komanso mitundu yosiyanasiyana. Kenako m’mwezi wa March 1962 asilikali analanda boma. Zitatero amwenye ambirimbiri a ku India anathamangitsidwa m’dzikolo ndipo anabwerera kwawo, koma ena anapita ku Bangladesh (pa nthawiyo linkadziwika kuti East Pakistan). Anthu ochokera kumayiko ena ankawalola kukhala m’dzikomo kwa maola 24 okha basi. Apatu mwayi wochita zinthu ndi anthu a m’mayiko ena unayamba kuchepa.
Abale ankangoyang’ana zimene zikuchitika osadziwa kuti zitha bwanji. Boma la asilikali linanena kuti lipereka ufulu wa kulambira pokhapokha ngati zipembedzo zitasiya kulowerera ndale. Koma mwachizolowezi chawo, amishonale a matchalitchi amene amati ndi achikhristu anapitiriza kulowerera ndale. Ndiyeno pofika m’mwezi wa May 1966, boma linatopa ndi zimenezi ndipo linalamula kuti amishonale onse achoke m’dzikomo. Amishonale a Mboni sankalowerera ndale, komabe posakhalitsa nawonso anathamangitsidwa m’dzikomo.
Abale a m’dzikolo anakhumudwa kwambiri koma sanataye mtima. Iwo ankadziwa kuti Yehova Mulungu ali nawo. (Deut. 31:6) Komabe abale ena ankada nkhawa kuti mwina ntchito ya Ufumu sipitirira.
Koma posakhalitsa zinali zoonekeratu kuti Yehova akutitsogolera. Pa nthawiyo, a Maurice Raj amene m’mbuyomo anali woyang’anira dera ndipo anaphunzitsidwa zina ndi zina ku nthambi, anaikidwa kuti aziyang’anira ofesi ya nthambi. Ngakhale kuti a Raj anali a ku India, sanathamangitsidwe m’dzikoli limodzi ndi anthu ena a ku India. Pofotokoza chifukwa chake, iwo anati: “Zaka zingapo m’mbuyomu ndinalemba kalata ku boma yopempha kuti ndikhale nzika ya dziko la Burma. Koma ndinalibe ndalama zokwana 450 kyatsd zogulira chiphaso, choncho ndinangosiya osachitaponso kanthu. Ndiyeno tsiku lina pamene ndinkadutsa pa ofesi ya kampani ina kumene ndinkagwirako ntchito zaka zingapo m’mbuyomu, bwana wanga wakale anandiona. Choncho anandiitana kuti: ‘Iwe, Maurice, bwera udzatenge ndalama zako. Unaiwala kutenga ndalama zako za penshoni pamene unkachoka.’ Ndalama zonse zinakwana 450 kyats.
“Pamene ndinkatuluka muofesimo ndinkaganizira zinthu zosiyanasiyana zimene ndikanagula ndi ndalamazi. Koma popeza kuti ndalamazi zinali zokwanira ndendende kuti ndipeze chiphaso chija, ndinaona kuti Yehova akufuna kuti ndalamazi ndikalipirire chiphasocho kuti ndikhale nzika ya dzikoli. N’zimenedi ndinachita ndipo zinthu zinayenda bwino kwambiri. Pamene anthu ena a ku India ankathamangitsidwa m’dzikoli, ine sanandithamangitse ndipo ndinkayenda momasuka, ndinkaitanitsa mabuku kuchokera kunja ndipo ndinkachita zinthu zina zofunika pa ntchito yathu yolalikira chifukwa ndinali nzika.”
M’bale Raj limodzi ndi m’bale Dunstan O’Neill anayendera mipingo komanso magulu akutali m’dziko lonselo n’kumalimbikitsa abale. A Raj anati: “Tinkauza abale kuti: ‘Musadandaule, Yehova ali nafe. Tikakhala okhulupirika kwa iye, adzatithandiza.’ Yehova anatithandizadi moti posakhalitsa apainiya apadera atsopano anaikidwa ndipo ntchito yolalikira inapita patsogolo mofulumira.”
Kuchokera pa nthawiyo padutsa zaka 46, ndipo a Raj amene ali mu Komiti ya Nthambi, amayendabe m’dziko lonse la Myanmar n’kumalimbikitsa mipingo. Mofanana ndi Kalebe wa m’nthawi ya Yoswa, akupitiriza kutumikira Mulungu mwakhama.—Yos. 14:11.
Ntchito Yolalikira Inafika M’Chigawo cha Chin
Limodzi mwa madera oyambirira kulandira apainiya apadera linali la Chin. Limeneli ndi dera lamapiri limene lili kumalire kwa dziko la Bangladesh ndi India. Kumeneku n’kuchimake kwa anthu amene amati ndi Akhristu, chifukwa n’kumene kunkakhala amishonale a Baptist pa nthawi imene dzikoli linkalamuliridwa ndi boma la Britain. Choncho anthu ambiri a ku Chin amalemekeza kwambiri Baibulo ndiponso zimene limaphunzitsa.
Chakumapeto kwa chaka cha 1966, m’bale Lal Chhana, amene kale anali msilikali, koma tsopano ndi mpainiya wapadera, anafika m’tauni ya Falam, imene pa nthawiyo inali tauni yaikulu m’chigawo cha Chin. Kumeneko anakumana ndi a Dunstan ndi a Pramila O’Neill komanso a Than Tum, amenenso kale anali msilikali ndipo anali atangobatizidwa kumene. Anthu amenewa, omwe anali akhama pa ntchito yolalikira anapeza mabanja ambiri amene anachita chidwi ndi uthenga wabwino ndipo posakhalitsa anakhazikitsa mpingo waung’ono koma wamphamvu.
Chaka chotsatira, a Than Tum anasamukira ku Hakha, tauni imene ili kum’mwera kwa Falam. Kumeneko anayamba upainiya ndipo anakhazikitsa kagulu kakang’ono. Patapita nthawi anapita kukalalikira m’chigawo chonse cha Chin ndipo anathandiza kukhazikitsa mipingo ku Vanhna ndi Surkhua, komanso ku Gangaw ndi m’madera ena. Panopa padutsa zaka 45 kuchokera nthawi imeneyo ndipo a Than Tum akutumikirabe ngati mpainiya wapadera kumudzi kwawo ku Vanhna.
A Than Tum atachoka ku Hakha, Donald Dewar, wa zaka 20 ndi amene analowa m’malo mwawo. Popeza kuti makolo a Donald, omwe ndi a Frank ndi a Lily Dewar (omwe poyamba anali a Lily May), anali atangothamangitsidwa kumene m’dzikoli, Samuel wa zaka 18 yemwe ndi mng’ono wake wa Donald, anabwera n’kumakhala naye. Donald anati: “Tinkakhala m’kanyumba ka malata okhaokha ndipo nthawi yotentha kankatentha kwambiri komanso m’nthawi yozizira kankazizira kwambiri. Koma vuto lalikulu kwa ine linali kusungulumwa. Nthawi zambiri ndinkayenda ndekha mu utumiki ndipo zinkandivuta kulankhula chinenero cha kuderalo chomwe ndi Chihakha Chin. Pa misonkhano tinkangokhalapo ine ndi mng’ono wanga Samuel, komanso wofalitsa wina mmodzi kapena awiri. Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kutopa moti ndinaganizapo zosiya utumiki.
“Cha pa nthawi imeneyi ndinawerenga nkhani yolimbikitsa kwambiri m’Buku Lapachaka yokhudza abale a ku Malawi amene anakhalabe okhulupirika pa nthawi imene ankazunzidwa mwankhanza.e Ndiyeno ndinadzifunsa kuti, ‘Ngati ndikulephera kupirira vuto la kusungulumwa kodi ndidzatha kupirira chizunzo?’ Ndinatula nkhawa zanga kwa Yehova m’pemphero ndipo ndinayamba kumva bwino mumtima. Ndinapezanso mphamvu chifukwa chowerenga ndi kusinkhasinkha nkhani za m’Baibulo ndi mu Nsanja ya Olonda. Tsiku lina a Maurice Raj ndi a Dunstan O’Neill, anangobwera mwadzidzidzi kudzandichezera. Zinangokhala ngati ndikuona angelo awiri. Pang’ono ndi pang’ono ndinayambanso kusangalala ndi utumiki.”
Kenako a Donald Dewar akutumikira monga woyang’anira dera analimbikitsa abale amene anali m’madera akutali pogwiritsa ntchito zimene anakumana nazo pa moyo wake. Ntchito imene anagwira mwakhama ku Hakha inabala zipatso. Tsopano ku Hakha kuli mpingo wolimba ndipo nthawi zonse kumachitika misonkhano ikuluikulu. Anthu awiri aja, amene ankabwera ku misonkhano ku Hakha, omwe mayina awo ndi a Johnson Lal Vung ndi a Daniel Sang Kha, anakhala apainiya apadera akhama ndipo anathandiza kulalikira uthenga wabwino m’mbali yaikulu ya chigawo cha Chin.
‘Kukwera Mapiri’
Chigawo cha Chin chili pamalo okwera kwambiri ndipo mapiri ena a m’chigawochi ndi aatali mamita 3,000. Mapiri ambiri ndi odzaza ndi mitengo ya mitundumitundu monga mlombwa, paini, ndiponso maluwa okongola amitundu yosiyanasiyana. M’dzikoli muli zitunda zambiri zimene zimachititsa kuti kuyenda kukhale kovuta. Misewu imene imalumikiza matauni a m’chigawochi ndi yafumbi komanso yovuta kudutsa kukagwa mvula ndipo nthawi zambiri matope ogumuka m’mapiri amatseka misewuyi. M’madera ena akumidzi sikupita galimoto, moti anthu amangoyenda pansi. Koma mavuto amenewa sanalepheretse atumiki a Yehova kukwaniritsa cholinga chawo chofikira anthu ambiri ndi uthenga wabwino.
Mlongo Aye Aye Thit, amene ankatumikira ndi mwamuna wake yemwe anali woyang’anira dera m’chigawo cha Chin, anati: “Ndinakulira m’chigwa cha Ayeyarwady ndipo ndinachita chidwi kwambiri ndi mapiri okongola a Chin. Phiri loyamba ndinalikwera ndi mphamvu koma nditafika pamwamba pa phirilo ndinakomoka chifukwa chotopa. Mmene ndinkakwera mapiri ena otsala n’kuti nditatoperatu moti ndinkangoganiza kuti ndifa. M’kupita kwa nthawi ndinaphunzira mmene ndingayendere m’mapiri. Ndinkafunika kuyenda pang’onopang’ono kuti mphamvu zisathe. Pasanapite nthawi, ndinkatha kuyenda makilomita 32 pa tsiku, pa ulendo wa masiku 6 kapena kuposa.”
Kwa zaka zambiri abale a ku chigawo cha Chin akhala akugwiritsa ntchito zoyendera zosiyanasiyana monga abulu, mahatchi ndi njinga. Ndipo posachedwapa ayambanso kugwiritsa ntchito njinga zamoto, malole ndi magalimoto ang’onoang’ono. Koma kawirikawiri amangoyenda pansi. Mwachitsanzo, kuti akafike kutauni ya Matupi, a Kyaw Win ndi a David Zama, omwe anali apainiya apadera ankayenda mtunda wautali wodutsa m’mapiri. Iwo ankayenda mtunda wautaliwu kuti akapezeke pa misonkhano ikuluikulu yachikhristu ku Hakha. Anthu a mu mpingo wa Matupi, umene unali pa mtunda wa makilomita 270 kukafika kumalo a msonkhanowo, ankayenda masiku 6 kapena 8 kupita kokha. Popita kumeneko abale ankaimba nyimbo za Ufumu zimene zinkamveka m’mapiri okongola a m’derali.
Pa maulendowa, abalewa ankakumana ndi nyengo zovuta za m’mapiri komanso ankalumidwa ndi udzudzu ndiponso tizilombo tambirimbiri touluka nthawi ya mvula. Mwachitsanzo, woyang’anira dera wina, dzina lake Myint Lwin, anati: “Ndikuyenda m’nkhalango ina ndinangoona misundu ikundikwera m’miyendo. Nditaichotsa, inanso iwiri inandikwera. Ndinalumphira pamtengo wina wakugwa, koma misundu yambirimbiri inayambanso kukwera mtengowo. Nditagwidwa ndi mantha, ndinayamba kuthamanga kudutsa m’nkhalangomo. Pamene ndinkafika kumsewu n’kuti misundu itandikwerakwera thupi lonse.”
Koma anthu amene amadutsa m’chigawo cha Chin amakumana ndi mavuto ambiri kuposa amenewa. Ku Myanmar kumapezekanso nguluwe, zimbalangondo, akambuku, ndiponso malinga ndi zimene mabuku ena amanena, m’dzikoli mumapezekanso mitundu yambiri ya njoka zapoizoni kuposa dziko lina lililonse padziko lapansi. Woyang’anira chigawo wina dzina lake Gumja Naw ndi mkazi wake Nan Lu, akamayendera mipingo yosiyanasiyana m’chigawo cha Chin, usiku ankachita kukoleza moto kuzungulira pamalo amene akhala kuti pasafike nyama zakutchire.
Mpaka pano anthu amayamikirabe zimene alaliki akhamawa anachita. A Maurice Raj anati: “Anthu amenewa ankatumikira Yehova ndi mphamvu zawo zonse. Iwo atachoka m’chigawo cha Chin anali okonzeka kubweranso m’chigawochi. Ntchito imene anagwira mwakhama inaperekadi ulemerero kwa Yehova.” Masiku ano m’chigawo cha Chin muli mipingo 7 ndi magulu ambiri akutali, ngakhale kuti chigawochi chili m’gulu la madera omwe kuli anthu ochepa kwambiri kuposa madera ena onse a m’dzikoli.
“Ku Myitkyina Kulibe ‘Nkhosa’”
Mu 1966 apainiya apadera ambiri anafika mu tauni yaing’ono yokongola ya Myitkyina. Tauniyi ili m’mbali mwa mtsinje wa Ayeyarwady, m’chigawo cha Kachin, kumalire ndi dziko la China. Zaka 6 m’mbuyomu, m’bale Robert Richards ndi mkazi wawo Baby anali atalalikira m’dera limeneli kwa nthawi yochepa. Iwo anati: “Ku Myitkyina kulibe ‘nkhosa.’” Koma apainiya amene anabwera m’mbuyo mwawo anapeza anthu ali ndi njala ya choonadi.
Mmodzi mwa anthu amenewo anali mnyamata wa zaka 19 dzina lake Mya Maung amene anali wa Baptist. Iyeyu ankapemphera kuti Mulungu amuthandize kumvetsa Baibulo. Mya Maung anafotokoza kuti: “Ndinasangalala kwambiri mpainiya wina atandipeza kuntchito n’kundipempha kuti aziphunzira nane Baibulo. Ndinaona kuti Mulungu wayankha pemphero langa lija. Ine ndi mng’ono wanga San Aye, tinkaphunzira kawiri pamlungu ndipo mofulumira kwambiri tinapita patsogolo mwauzimu.
“Tinathandizidwa ndi m’bale Wilson Thein amene anali mphunzitsi wabwino kwambiri. M’malo mongotiuza zochita, ankatisonyeza mmene tingachitire zinthuzo. Tinkayeserera kukamba nkhani komanso kuchita zitsanzo za ulaliki. Zimenezi zinatithandiza kuphunzira kugwiritsa ntchito Baibulo mwaluso kwambiri komanso kulalikira molimba mtima. Zinatithandizanso kudziwa zimene tingachite tikamatsutsidwa komanso mmene tingakonzekerere ndi mmene tingakambire nkhani kumpingo. A Thein ankatimvetsera tikamayeserera nkhani iliyonse ndipo ankatiuza zoyenera kukonza. Zimenezi zinatilimbikitsa kuti tikhale ndi mtima wofuna kukwaniritsa zolinga zauzimu.
“Masiku ano, m’matauni amene ali m’mbali mwa njanji imeneyi, omwe ndi Namti, Hopin, Mohnyin ndi Katha, muli mipingo yolimba”
“M’chaka cha 1968, ine ndi San Aye tinayamba kuchita upainiya ndipo chiwerengero cha apainiya chinakwana 8 ku Myitkyina. Anthu oyambirira kuwaphunzitsa Baibulo anali amayi athu ndi azibale athu ndipo patapita nthawi onse anabatizidwa. Nthawi zina tinkayenda ulendo wa tsiku limodzi mpaka masiku atatu n’kumalalikira m’matauni ndi m’midzi ya m’mbali mwa njanji yochokera ku Myitkyina kupita ku Mandalay. Patapita nthawi, mbewu zimene tinafesa zinabala zipatso. Masiku ano, m’matauni amene ali m’mbali mwa njanji imeneyi, omwe ndi Namti, Hopin, Mohnyin ndi Katha, muli mipingo yolimba.”
Tsiku lina San Aye akulalikira m’gawo lamalonda ku Myitkyina anakumana ndi a Phum Ram amtundu wa Chikachin. Iwo ankagwira ntchito kumaofesi a boma ndipo anali m’chipembedzo cha Baptist. A Phum Ram anaphunzira choonadi ndipo kenako anasamukira m’tauni yaing’ono ya Putao, imene ili m’munsi mwa phiri la Himalaya. Kumeneko analalikira kwa abale awo ambiri ndipo posakhalitsa anthu 25 anayamba kupezeka pa misonkhano yachikhristu. Pa nthawi imene a Phum Ram ankachita upainiya anathandiza mkazi wawo, ana awo 7 ndi achibale awo ambiri kuphunzira choonadi. Panopa akutumikira ngati mpainiya komanso mkulu ku Myitkyina.
Mabogi a Sitima Atsala
Ofesi ya nthambi itaona kuti chiwerengero cha Mboni chikuwonjezeka m’chigawo cha Kachin, anakonza zoti msonkhano wa mayiko wa chaka cha 1969, wakuti “Mtendere Padziko Lapansi,” uchitikire ku Myitkyina m’malo mwa ku Yangon komwe unkachitikira nthawi zambiri. Pofuna kunyamula anthu opita ku msonkhano kuchokera ku Yangon kupita ku Myitkyina, womwe ndi mtunda wa makilomita oposa 1,100, ofesi ya nthambi inapempha kampani yasitima ya dziko la Burma kuti iwalole kuchita hayala mabogi 6 a sitima. Pempho limeneli linali lachilendo kwambiri chifukwa m’chigawo cha Kachin munali zigawenga zambiri, ndipo zinali zovuta kulowa kapena kutuluka m’chigawochi. Komabe abale anadabwa chifukwa akuluakulu a kampani ya sitimayo anavomera mosavuta kupereka mabogiwo.
Tsiku limene ankayembekezera kufika kwa sitima yonyamula abale opita ku msonkhanowo litakwana, m’bale Maurice Raj ndi abale ena anapita kusiteshoni ya sitima ku Myitkyina kukalandira abalewo. A Raj anafotokoza kuti: “Pamene tinkayembekezera, bwana wa pasiteshonipo anabwera kudzatiuza kuti walandira uthenga wakuti akuluakulu aboma amasula mabogi 6 amene ananyamula anthu obwera ku msonkhano aja ndipo anawasiya pakati pa tauni ya Mandalay ndi Myitkyina. Zikuoneka kuti sitimayo sikanatha kukwera phiri chifukwa cha mabogi owonjezerawo.
“Kodi tikanatani pamenepa? Maganizo oyambirira kubwera anali oti tisinthe tsiku la msonkhano. Koma zimenezi zinatanthauza kuti tipemphenso chilolezo china ndipo zikanatenga milungu ingapo. Pamene tinkapemphera kwa Yehova tinangoona sitima ija yatulukira. Tinadabwa kwambiri kuona kuti mabogi onse 6 mmene munali abale athu aja afika. Abalewo ankamwetulira ndiponso kusangalala kwambiri. Titafunsa zimene zinachitika, m’bale wina anafotokoza kuti, ‘Asiyadi mabogi ena 6 koma osati athuwa.’”
“Asiyadi mabogi ena 6 koma osati athuwa”
Msonkhano wa ku Myitkyina unayenda bwino kwambiri. Pa msonkhanowu panatulutsidwa mabuku atatu m’Chibama ndiponso asanu m’Chingelezi. Zaka zitatu m’mbuyomu pamene amishonale anathamangitsidwa m’dzikoli, zinali zovuta kwambiri kuti chakudya chauzimu chilowe m’dziko la Burma. Koma tsopano vuto limeneli linali litatha.
Kuphunzitsa Anthu a Mtundu wa Chinaga
Patapita miyezi inayi msonkhano wa ku Myitkyina utachitika, abale a ku ofesi ya nthambi analandira kalata yochokera kwa a Ba Yee, omwe anali kalaliki wa ku positi ofesi ya m’tauni ya Khamti. Tauni imeneyi ili m’mphepete mwa mtsinje womwe uli m’munsi mwa mapiri amene ali m’malire mwa dziko la Burma ndi India. Kudera limeneli kumapezeka anthu a mtundu wa Chinaga womwe ndi wopangidwa ndi anthu a mitundu yosiyanasiyana omwe poyamba anali alenje oopsa ndipo ankadula mitu ya anthu. M’kalata ija kalalikiyu, amene poyamba anali m’chipembedzo cha Seventh Day Adventist, anapempha kuti aphunzire Baibulo. Mwamsanga ofesi ya nthambi inatumiza a Aung Naing ndi a Win Pe, omwe anali apainiya apadera.
A Win Pe anafotokoza kuti: “Titafika pabwalo la ndege la ku Khamti tinachita mantha kwambiri titaona asilikali a mtundu wa Chinaga atangovala tinsalu tomangira m’chiuno. Kenako a Ba Yee anabwera mofulumira kudzatilonjera n’kutitenga mwamsanga kuti tikakumane ndi anthu ena achidwi. Pasanapite nthawi yaitali tinayamba kuphunzira Baibulo ndi anthu asanu.
“Koma akuluakulu aboma ankaganiza kuti ndife abusa a Baptist omwe ankagwirizana ndi zigawenga za m’deralo. Ngakhale kuti tinawatsimikizira kuti sitilowerera ndale, iwo anatilamula kuti tichoke m’deralo pasanathe mwezi kuchokera pa tsiku limene tinafika.”
Patatha zaka zitatu, kunabwera akuluakulu ena a boma ndipo Biak Mawia amene anali mpainiya wa zaka 18, anapitiriza pamene apainiya ena aja anasiyira. Posakhalitsa a Ba Yee anasiya ntchito ku positi ofesi kuja ndipo anayamba upainiya. Kenako kunafika apainiya ena ambiri ndipo apainiya akhamawa anakhazikitsa mpingo wamphamvu ku Khamti. Anakhazikitsanso timagulu ting’onoting’ono tambiri m’midzi yozungulira. A Biak Mawia anati: “Abale ndi alongo a mtundu wa Chinaga anali osaphunzira ndipo sankadziwa kulemba ndi kuwerenga. Koma ankakonda kwambiri Mawu a Mulungu ndipo ankalalikira mwakhama komanso ankagwiritsa ntchito mwaluso zithunzi za m’mabuku athu. Ankalowezanso pamtima malemba ambiri ndiponso nyimbo za Ufumu.”
Masiku ano misonkhano yachigawo imachitika nthawi ndi nthawi ku Khamti ndipo anthu ena amene amabwera ku misonkhanoyi amachokera ku tauni ya Homalin, yomwe ili kutali kwambiri koyenda maola 15 paboti.
Kutsutsidwa ku “Golden Triangle”
Pa nthawiyi kumbali ina ya dzikoli ntchito yolalikira inapitiriza kukula moti inafalikira mpaka kukafika kumalire a dzikoli ndi mayiko a China, Laos komanso Thailand. Dera limeneli ndi limene limadziwika kuti Golden Triangle, ndipo ndi lokongola kwambiri chifukwa kuli mapiri aatali komanso zigwa zachonde. Komabe derali limatchuka ndi mbiri yoipa. Zili choncho chifukwa amalimako mankhwala osokoneza bongo, kumapezeka zigawenga zoukira boma, komanso zinthu zina zosemphana ndi malamulo aboma. Apainiya amene anali oyambirira kuphunzitsa choonadi kudera loopsali ankachita zinthu mosamala kwambiri. (Mat. 10:16) Koma panali gulu limodzi limene linkatsutsa kwambiri ntchito yawo yolalikira, ndipo gulu lake ndi la atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi achikhristu.
Ndiyeno m’bale Robin Zauja ndi m’bale David Abraham, omwe anali apainiya, anafika m’tauni ya Lashio, yomwe inali yotchuka kwambiri m’chigawo cha Shan. Atangofika kumeneko, mwamsanga atsogoleri achipembedzo anayamba kunena kuti apainiyawo anali m’gulu la zigawenga. A Zauja anati: “Anatimanga n’kutitengera pangolo kupita kundende. Kumeneko tinaonetsa apolisi zikalata zosonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu. Pasanapite nthawi yaitali, mkulu wa asilikali anafika. Ndinangodabwa akuti: ‘Muli bwanji a Zauja? Ndaona kuti Mboni za Yehova zafika kuno ku Lashio.’ Mkulu wa asilikaliyo anali munthu amene ndinaphunzira naye sukulu, ndipo nthawi yomweyo anatimasula.”
Kenako apainiya aja anayamba ntchito yolalikira ndipo pasanapite nthawi yaitali anakhazikitsa mpingo. Pambuyo pake, anamanga Nyumba ya Ufumu. Patapita zaka ziwiri, anaitanidwa kukaonekera kulikulu la boma komwe kunasonkhana mafumu, akuluakulu a asilikali oposa 70, ndiponso atsogoleri a chipembedzo. A Zauja anati: “Atsogoleri achipembedzo anafotokoza mokwiya kuti tikumakakamiza anthu kuti asiye miyambo ya chipembedzo chawo. Tcheyamani wa msonkhanowo atatipatsa mpata woti tifotokoze mbali yathu, ndinapempha kuti andilole kugwiritsa ntchito Baibulo poyankha. Iye anandilola ndipo nthawi yomweyo ndinapemphera chamumtima. Kenako ndinafotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya miyambo ya chipembedzo chonyenga, ntchito ya usilikali, ndiponso miyambo yokondwerera dziko lako. Nditamaliza kulankhula, tcheyamani uja anaimirira n’kufotokoza kuti malamulo a dziko la Burma amalola chipembedzo china chilichonse. Zitatero anatimasula n’kutilola kupitiriza kulalikira koma zimenezi zinakhumudwitsa atsogoleri achipembedzo.”
Patapita nthawi, m’mudzi waung’ono wa Mongpaw, womwe uli pafupi ndi malire a dzikoli ndi dziko la China, gulu la anthu okwiya a mpingo wa Baptist linawotcha Nyumba ya Ufumu imene inali m’mphepete mwa mudziwo. Popeza kuti Mboni za m’derali sizinachite mantha ndi zimenezi, gululi linawotchanso nyumba ya mpainiya wapadera komanso linayamba kupita kunyumba za abale ndi alongo n’kumawazunza. Abale atakadandaula zimenezi kwa mkulu wa m’deralo, iye anaikira kumbuyo anthu a Baptist aja. Komabe pamapeto pake, boma linalowererapo ndipo linapereka chilolezo kwa abalewo kuti amange Nyumba ya Ufumu yatsopano. Abomawo anauza abalewo kuti amange nyumba yatsopanoyi pakatikati pa mudziwo, osati m’mphepete mwa mudziwo ngati poyamba.
Pa nthawiyi, nayenso m’bale Gregory Sarilo ankatsutsidwa kwambiri ndi tchalitchi cha Katolika. M’baleyu ankakhala m’mudzi wa Leiktho, umene uli kum’mwera kwa dzikoli m’chigawo cha Kayin, kufupi ndi Golden Triangle. M’bale Sarilo anati: “Wansembe wa m’mudzimo anapempha anthu a mumpingo wake kuti akawononge dimba langa la ndiwo zamasamba. Kenako anandipatsa mphatso ya chakudya koma mnzanga anandichenjeza kuti m’chakudyacho anali atathiramo poizoni. Tsiku lina, anthu amene ankatumikira wansembeyu anandifunsa njira imene ndidutse tsiku lotsatira. Tsikulo litafika, ndinadutsa njira ina ndipo zimenezi zinachititsa kuti chiwembu chawo chofuna kundipha chilephereke. Nditakanena za chiwembu chimenechi kwa akuluakulu a boma, iwo analamula mwamphamvu wansembeyo limodzi ndi otsatira ake kuti asiye kundivutitsa. Apa ndinaona kuti Yehova ananditeteza kwa anthu ‘ofunafuna moyo wanga.’”—Sal. 35:4.
Anakaniratu Kulowerera Ndale Komanso Kumenya Nkhondo
Kwa zaka zambiri chikhulupiriro cha abale ndi alongo a m’dziko la Burma chakhala chikuyesedwa m’njira inanso yapadera. Iwo akhala akuyesedwa pa nkhani yolowerera ndale chifukwa cha nkhondo zapachiweniweni zomwe zimachitikachitika m’dzikoli.—Yoh. 18:36.
Kum’mwera kwa dzikoli kuli tauni ya Thanbyuzayat, yomwe imadziwika kwambiri chifukwa cha siteshoni ya sitima imene inamangidwa pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. M’tauni imeneyi, mpainiya wina wapadera dzina lake Hla Aung anapezeka pakatikati pa zigawenga ndi asilikali aboma amene ankamenyana. Iye anafotokoza kuti: “Asilikaliwo ankalowa m’mudzi usiku n’kugwira amuna kuti azikawanyamulira zida zawo zankhondo. Anthu ogwidwawo ankawatenga atawaloza ndi mfuti ndipo ambiri ankaphedwa. Tsiku lina usiku, asilikaliwo analowa m’mudzi mwathu. Pa nthawiyo n’kuti ine ndi m’bale Donald Dewar tikucheza m’nyumba mwanga. Mwamsanga, mkazi wanga anatichenjeza ndipo tinathawira kutchire. Zimenezi zitachitika, ndinakonza malo m’nyumba mwanga oti ndidzabisalemo asilikaliwo akadzabweranso.”
M’bale Rajan Pandit, yemwe anali mpainiya wapadera anabwera m’tauni ya Dawei, yomwe inali kum’mwera kwa dera la Thanbyuzayat. Atangofika anayambitsa maphunziro ambirimbiri m’mudzi wina wapafupi komwe kunali zigawenga zambiri. M’baleyo anati: “Tsiku lina ndikuchokera m’mudziwu, asilikali anandigwira n’kundimenya. Iwo ankanena kuti ndimagwirizana ndi zigawengazo. Nditawauza kuti ndine wa Mboni za Yehova, anandifunsa kuti ndayenda bwanji kuti ndidzafike ku Dawei. Ndinawaonetsa tikiti ya ndege monga umboni woti ndinabwera pa ndege, chifukwa pa nthawiyo zigawenga sizinkayenda pa ndege. Nditatero sanandimenyenso ndipo kenako anandimasula. Koma asilikaliwo anapanikiza wophunzira wanga ndi mafunso koma iye anawatsimikizira kuti tinkangophunzira Baibulo basi. Zitachitika zimenezo, asilikaliwo sanandivutitsenso ndipo ena ndinayamba kumawapatsa magazini nthawi ndi nthawi.”
Nthawi zina akuluakulu a mumzinda ankakakamiza abale kuti azilowerera ndale. Iwo ankawakakamiza kuti azivota pa nthawi ya chisankho kapena kuchita miyambo ina yosonyeza kuti amakonda dziko lawo. Mwachitsanzo, akuluakulu a m’tauni ya Zalun, yomwe ili m’mphepete mwa mtsinje, pa mtunda wa makilomita 130 kumpoto kwa mzinda wa Yangon, ankakakamiza Mboni za kumeneko kuti zikavote nawo pa chisankho. Koma abalewo anakana kuvota ndipo anasonyeza akuluakuluwo zifukwa zochokera m’Baibulo. (Yoh. 6:15) Zitatero, akuluakuluwo anakasiya nkhaniyi kwa oyang’anira mzindawo n’cholinga choti alamule a Mboniwo kuti avote. Koma oyang’anira mzindawo ankadziwa kuti a Mboni za Yehova salowerera ndale. Choncho abalewo sanakakamizidwenso kuvota.
Pasukulu ina m’tauni ya Khampat, yomwe ili kumalire a dziko la Burma ndi India, ana 23 a Mboni anakana kuweramira mbendera. Atatero, mphunzitsi wamkulu anawachotsa sukulu. Kenako mphunzitsiyo anaitana akulu awiri a mpingo kuti akaonane ndi gulu la akuluakulu a boma, kuphatikizapo woweruza milandu ndi mkulu wa asilikali. Mmodzi wa akuluwo, anali m’bale Paul Khai Khan Thang, ndipo ananena kuti: “Pamene tinkawafotokozera zimene timakhulupirira pa nkhaniyi pogwiritsa ntchito malemba, zinkachita kuonekeratu kuti akuluakulu ena akwiya nazo. Kenako tinawaonetsa chikalata chaboma chonena kuti pakamachitika chilichonse chokhudza kugwiritsa ntchito mbendera, a Mboni za Yehova akhoza ‘kungoima mwaulemu, osachita chilichonse.’ Apa akuluakulu abomawo anangoti kakasi kusowa chonena. Kenako mkulu wa asilikali uja analamula mphunzitsi wamkuluyo kuti alole ana anawachotsa sukulu aja kuti ayambenso kuphunzira. Zitatero mphunzitsi wamkuluyo anapereka chikalatacho m’dipatimenti iliyonse pasukulupo.”
Panopa akuluakulu a boma la Myanmar amadziwa kuti a Mboni za Yehova salowerera ndale. Atumiki a Yehova achitira umboni monga mmene Yesu Khristu ananenera. Iwo achita zimenezi poyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pokana kulowerera ndale.—Luka 21:13.
Asilikali Anakhala Akhristu
Popeza kuti zinthu sizimayenda bwino kwenikweni ku Myanmar, anthu ambiri a m’dzikoli anagwirapo ntchito ya usilikali kapena anakhalapo zigawenga. Mofanana ndi Koneliyo amene anali mkulu wa asilikali wachiroma m’nthawi ya atumwi, ena mwa anthu amenewa ndi ‘opembedza ndi oopa Mulungu.’ (Mac. 10:2) Akaphunzira choonadi, amayesetsa kusintha moyo wawo kuti uzigwirizana ndi mfundo zolungama za Yehova.
Udani wa anthu awiriwa unatha ndipo tsopano chikondi chinawagwirizanitsa. Zonsezi zinatheka chifukwa cha mphamvu ya mawu a Mulungu
Mmodzi mwa anthu oterewa ndi Hlawn Mang, yemwe kale anali msilikali wapamadzi. Iyeyu anaphunzira choonadi akugwira ntchito ku Mawlamyine. M’bale Mang anafotokoza kuti: “Nditangomva uthenga wa m’Baibulo koyamba, ndinafuna kuyamba kulalikira nthawi yomweyo. Koma ndikukonza zoti ndisiye ntchito ya usilikali ndinamva zoti akufuna kundikweza pa ntchito komanso kunditumiza kusukulu ya usilikali kudziko lina lolemera. Koma pa nthawiyo ndinali nditatsimikiza mtima kugwira ntchito ya Mulungu. Mabwana anga anadabwa kwambiri ndikuwapatsa kalata yosiya ntchito kuti ndikayambe kutumikira Yehova. Padutsa zaka 30 tsopano, koma sindinong’oneza bondo chifukwa palibe chimene chingafanane ndi kutumikira Mulungu woona.”
Munthu wina, dzina lake La Bang Gam, anagonekedwa m’chipatala cha asilikali. Ali kumeneko, M’bale Robin Zauja anamuonetsa buku lotchedwa Kucokera ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Wopezekanso.f Iye anachita nalo chidwi ndipo anapempha kuti amupatse. Koma popeza kuti m’bale Zauja anali ndi buku limodzi lokhali, anangomubwereka kuti aliwerenge usiku umodzi wokha. Tsiku lotsatira, a Zauja atapitanso kukamuona, La Bang Gam anati: “Eni buku lanu lija, tsopano ndili ndi langa!” La Bang Gam anachezera usiku wonse akukopera bukuli. Bukuli linali la masamba 250 ndipo iye analikopera m’makope ambirimbiri. Pasanapite nthawi, La Bang Gam, anasiya usilikali ndipo anathandiza anthu ambiri kuphunzira choonadi pogwiritsa ntchito buku la “Paradaiso” limene anakopera lija.
Sa Than Htun Aung, anali mtsogoleri wa asilikali a Burma ndipo Aik Lin anali mkulu wa asilikali m’gulu la United Wa State Army. Kwa nthawi yaitali, magulu awiriwa ankamenyana m’nkhalango ya kudera lamapiri la Shan. Magulu awo atagwirizana zosiya kumenyana, asilikali awiriwa anakhazikika m’chigawo cha Shan. Patapita nthawi, aliyense payekha anaphunzira choonadi n’kusiya usilikali ndipo anabatizidwa. Kenako anthu amenewa, omwe kale ankadana kwambiri, anakumana ku msonkhano wadera ndipo anakumbatirana mosangalala monga abale achikhristu. Tsopano udani unatha ndipo chikondi chinawagwirizanitsa. Zonsezi zinatheka chifukwa cha mphamvu ya Mawu a Mulungu.—Yoh. 8:32; 13:35.
Kukambirana ndi Anthu Amitundu Yonse
Pakati pa 1965 ndi 1976, chiwerengero cha ofalitsa ku Burma chinakwera ndi 300 peresenti. Ambiri mwa anthu amenewa, omwe ankamvetsera uthenga wabwino umene a Mboni ankalalikira, anali ochokera m’matchalitchi amene amati ndi achikhristu. Komabe, abale ankadziwa kuti Mulungu amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Choncho kuyambira pakati pa zaka za m’ma 1970, iwo anayamba kulalikira mwakhama kwa anthu azipembedzo zina monga Abuda, Ahindu ndi achipembedzo chamakolo.
Polalikira ankakumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, Abuda sakhulupirira kuti kuli Mulungu kapena Mlengi, Ahindu amalambira milungu yambirimbiri ndipo anthu achipembedzo cha makolo amakhulupirira mizimu. Komanso zipembedzo zimenezi zimakhulupirira kwambiri malodza, kuombeza maula ndi kukhulupirira mizimu. Ngakhale kuti anthuwa amaona kuti Baibulo ndi buku loyera, kawirikawiri amadziwa zochepa kapena sadziwa n’komwe za anthu otchulidwa m’Baibulo komanso zimene limaphunzitsa.
Abale ankadziwa kuti m’Mawu a Mulungu muli choonadi champhamvu ndipo chingathe kusintha wina aliyense. (Aheb. 4:12) Choncho ankangofunika kudalira mzimu wa Mulungu ndiponso kugwiritsa ntchito “luso la kuphunzitsa” kapena kuti kufotokoza mfundo mogwira mtima n’cholinga choti anthuwo asinthe mitima yawo.—2 Tim. 4:2.
Mwachitsanzo, Rosaline yemwe wakhala akuchita upainiya wapadera kwa zaka zambiri, amafotokoza mfundo mowafika pamtima Abuda. Iye anati: “Abuda akauzidwa kuti kuli Mlengi, amakonda kufunsa kuti, ‘Nanga Mlengiyo anamulenga ndani?’ Popeza kuti Abuda amakhulupirira kuti munthu akafa amauka n’kukhala nyama, ndimakambirana nawo pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ziweto zawo.
“Ndimawafunsa kuti, ‘Kodi ziweto zanu zimakudziwani?’
“Iwo amayankha kuti, ‘Inde.’
“Ndiye ndimawafunsa kuti, ‘Kodi zimadziwa za ntchito imene mumagwira, banja lanu kapena za moyo wanu?’
“Amayankha kuti, ‘Ayi.’
“Choncho ndimawafunsa kuti, ‘Popeza kuti anthu ndi osiyana ndi Mulungu amene ndi Mzimu, kodi tingadziwe chilichonse chokhudza Mulungu ndi kumene anachokera?’
“Amayankhanso kuti, ‘Ayi.’”
“Chikondi chimene abale anandisonyeza chinandilimbikitsa kwambiri”
Zimenezi zathandiza Abuda ambiri kufufuza umboni wina wosonyeza kuti kuli Mulungu. Kuwonjezera pa kuwafotokozera mfundo zogwira mtima za m’Malemba anthu amamvetsera choonadi tikamawasonyeza chikondi chochokera pansi pa mtima. Mwachitsanzo, Ohn Thwin, yemwe poyamba anali m’Buda, ananena kuti: “Nditayerekezera zimene Abuda amakhulupirira zoti anthu amapita ku malo amtendere otchedwa Nirvana, ndi lonjezo la m’Baibulo la Paradaiso, ndinkaona kuti lonjezo la Paradaiso ndi limene linkandisangalatsa kwambiri. Koma chifukwa choti ndinkakhulupirira kuti pali njira zambirimbiri zodziwira choonadi, sindinkagwiritsa ntchito zimene ndinkaphunzira. Kenako ndinayamba kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Chikondi chimene abale anandisonyeza chinandilimbikitsa kwambiri. Chikondi chimenecho chinandithandiza kuyamba kugwiritsa ntchito zimene ndinkaphunzira.”
Kuthandiza anthu kuti asinthe zikhulupiriro zawo kumafuna luso ndi kuleza mtima. Mwachitsanzo, bambo ake a Kumar Chakarabani yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 10, anapempha m’bale Jimmy Xavier yemwe amatumikira pa Beteli kuti aziphunzitsa mwana wawoyo kuwerenga. Bambo a Kumar anali Mhindu weniweni wa paphata. Choncho Kumar anati: “Bambo anachenjeza m’bale Xavier kuti azingondiphunzitsa kuwerenga osati zachipembedzo. Ndiye a Xavier anauza bambo angawo kuti buku lothandiza kwambiri pophunzitsa ana kuwerenga ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Komanso a Xavier ankati akamaliza kundiphunzitsa kuwerenga, ankacheza ndi bambo. Akamacheza, bambo ankafunsa mafunso okhudza zachipembedzo ndipo a Xavier ankawauza mochenjera kuti: ‘Mayankho ali m’Baibulo. Tiyeni tiwerengere limodzi.’ Patapita nthawi, bambo anaphunzira choonadi komanso achibale anga 63 anakhalanso a Mboni za Yehova.”
Kuchita Misonkhano Yachigawo pa Nthawi ya Zipolowe
Chamkatikati mwa zaka za m’ma 1980 zinthu zandale zinayamba kusokonekera kwambiri m’dzikoli. Kenako m’chaka cha 1988, anthu ambirimbiri anayamba kuyenda m’misewu n’kumachita zionetsero zotsutsana ndi boma. Koma mwamsanga asilikali analetsa zionetserozo ndipo posakhalitsa mbali yaikulu ya dzikoli inayamba kulamulidwa ndi asilikaliwo.
M’bale Kyaw Win, amene akutumikira pa Beteli ananena kuti, “Chifukwa cha zimenezi asilikaliwo anaika malamulo okhwima oletsa anthu kuyenda usiku, komanso analetsa kuti pasapezeke anthu oposa 5 ali limodzi. Choncho tinayamba kuganiza kuti mwina tiimitse kaye misonkhano yathu yachigawo ya chaka chimenecho. Komabe tinkadalira Yehova ndipo tinapita kukaonana ndi mkulu wa asilikali wa ku Yangon kukapempha kuti atilole kuchita msonkhano wa anthu 1,000. Patapita masiku awiri, tinalandira kalata yotiloleza kuchita msonkhanowo. Ndiyeno akuluakulu aboma a m’madera ena titawaonetsa kalatayo, anatilolezanso kuchita misonkhano m’madera awo. Yehova anatithandiza ndipo misonkhano yonse inayenda bwino kwambiri.”
Sanaleke Kusonkhana Pamodzi
Zipolowe za m’chaka cha 1988 zitatha, chuma cha dziko la Burma chinalowa pansi. Komabe abale ndi alongo anakhulupirira kwambiri Mulungu popitiriza kuika zinthu za Ufumu patsogolo pa moyo wawo.—Mat. 6:33.
Mwachitsanzo, m’bale Cin Khan Dal ankakhala ndi banja lake m’mudzi wina ku Sagaing. Iye anati: “Nthawi ina tinkafunika kupita ku msonkhano wachigawo m’tauni ya Tahan yomwe ili pa mtunda woyenda masiku awiri ndi boti komanso galimoto. Koma panalibe woti azisamalira nkhuku zathu ife titachoka. Komabe tinadalira Yehova ndipo tinapitabe ku msonkhanowo. Titabwerako tinapeza nkhuku 19 zitasowa. Zimenezi zinatibwezera m’mbuyo pa nkhani ya za chuma. Patangotha chaka chimodzi, nkhuku zochepa zomwe zinatsala zinayamba kuswana mpaka kukwana 60. Komanso ngakhale kuti nkhuku za anthu ambiri zinafa chifukwa cha matenda chaka chimenecho, zathu sizinafe.”
Enanso amene anaika zaufumu pa malo oyamba ndi la a Aung Tin Nyunt limodzi ndi mkazi wawo Nyein Mya ndi ana awo 9. Iwo ankakhala m’mudzi wina waung’ono wotchedwa Kyonsha, womwe uli pa mtunda wamakilomita 64 kumpoto chakum’mwera kwa Yangon. M’baleyu anati: “Nthawi zambiri banja lathu linkangodya phala la mpunga ndi ndiwo zamasamba basi. Tinalibe ndalama komanso chilichonse choti n’kugulitsa. Koma zimenezi sizinkatidetsa nkhawa. Ndinkauza banja langa kuti, ‘Yesu analibe potsamira mutu wake. Ndiye ngakhale nditamagona pansi pa mtengo kaya kufa ndi njala, sindidzasiya kulambira Mulungu mokhulupirika.’
“Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”—Aheb. 13:6
“Koma tsiku lina tinalibe chakudya chilichonse, moti mkazi ndi ana anga ankangondiyang’ana momvetsa chisoni. Ndiye ndinawauza kuti: ‘Musadandaule, Mulungu atithandiza.’ Titachoka mu utumiki wakumunda, ndinatenga ana anga aamuna kuti tikaphe nsomba. Koma tinangopha zokwanira kudya kamodzi kokha. Ndiyeno tinasiya mabasiketi ogwirira nsomba pafupi ndi maluwa a m’madzi n’kuuza anyamatawo kuti: ‘Tibweranso misonkhano ikatha.’ Masana a tsiku limenelo kunali mphepo yambiri. Choncho titabwerera kopha nsomba kuja, tinapeza kuti nsomba zambiri zabisala kunsi kwa maluwa aja. Apa tinangoti laponda lamphawi. Tinatenga mabasiketi aja n’kuyamba kugwira nsombazo. Tinagwira nsomba zambiri ndipo tinakazigulitsa n’kukagula chakudya chokwana mlungu wonse.”
Nthawi ndi nthawi atumiki a Yehova a ku Myanmar aona kukwaniritsidwa kwa lonjezo lolimbikitsa la Mulungu. Iye anatilonjeza kuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Ndipo iwo amanena kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”—Aheb. 13:5, 6.
Ntchito Yosindikiza Mabuku Inapita Patsogolo
Kuyambira m’chaka cha 1956, anthu a ku Myanmar akhala akupindula ndi chakudya chauzimu kudzera mu Nsanja ya Olonda ya m’chinenero cha Chibama. Ngakhale kuti m’dzikoli munkachitika nkhondo zapachiweniweni, zipolowe komanso mavuto azachuma, panalibe nthawi imene analephera kulandira chakudya chauzimu. Ndiye kodi magazini ankasindikizidwa bwanji pa nthawiyo?
Kwa zaka zambiri, ofesi ya nthambi inkatumiza makope angapo a magazini yomasuliridwa m’Chibama kwa akuluakulu a boma oona za mmene nkhani zalembedwera. Akuluakuluwo akaona kuti mulibe zilizonse zolimbikitsa kuukira boma, ofesi ya nthambi inkapempha kuti apatsidwe chikalata chowaloleza kugula mapepala osindikizira. Akagula mapepalawo, m’bale wina ankatenga zimene amasulirazo limodzi ndi mapepalawo n’kupita nazo kokasindikiza. Kenako m’baleyo ankawerenga ndi kukonza zimene zalakwika. Akatero ankasindikiza magaziniwo pamakina enaake othaitha. Kenako, ankatenga magaziniwo n’kuwapititsanso kwa akuluakulu aboma aja amene ankapereka zikalata zovomereza kuti magaziniwo afalitsidwe. Kunena zoona, ntchitoyi inali yotopetsa ndipo inkatenga milungu yambiri. Komanso mapepala ndi zilembo zake zinali zosaoneka bwino.
Mu 1989, ofesi ya nthambi inalandira makina atsopano osindikizira. Zimenezi zinathandiza kuti ntchito yosindikiza ikhale yosavuta. Pulogalamu ya pakompyuta yomwe inakonzedwa ku likulu la Mboni za Yehova, [Multilanguage Electronic Phototypesetting System (MEPS)], inkathandiza kusindikiza magazini m’zinenero zokwana 186 kuphatikizapo Chimyanima.g
M’bale wina, dzina lake Mya Maung yemwe ankagwira ntchito ku nthambi ananena kuti: “Mboni za Yehova zinali zoyambirira kugwiritsa ntchito pulogalamu yapakompyuta. Pulogalamuyi inkagwiritsa ntchito zilembo za Chimyanima zimene zinalembedwa ku nthambi yathu. Choncho inachititsa kuti makampani ena osindikiza mabuku m’dzikoli asinthe zina ndi zina pa makina awo osindikizira. Anthu sankamvetsa kuti n’chifukwa chiyani zilembo za m’mabuku athu zinkaoneka zokongola.” Pulogalamuyi inkalolanso kugwiritsa ntchito njira zatsopano zosindikizira zothandiza kuti zilembo zizioneka zokongola. Inathandizanso kuti zithunzi za mu Nsanja ya Olonda zizioneka zokongola kwambiri.
M’chaka cha 1991 boma la Myanmar linavomereza kuti tizifalitsa magazini ya Galamukani! Zimenezi zinasangalatsa kwambiri abale komanso anthu ena. Munthu wina waudindo waukulu mu Unduna Woona Zofalitsa Nkhani anafotokoza zimene anthu ambiri ankanena. Iye anati: “Magazini ya Galamukani! ndi yosiyana ndi magazini ena a azipembedzo. Mumakhala nkhani zosiyanasiyana komanso ndi yosavuta kumva. Ine ndimaikonda kwabasi.”
Kwa zaka 20 zapitazi, chiwerengero cha magazini osindikizidwa chinawonjezereka ndi maperesenti oposa 900
Kwa zaka 20 zapitazi, chiwerengero cha magazini amene ofesi ya nthambi imafalitsa mwezi uliwonse chinawonjezereka ndi pafupifupi 900 peresenti, kuchoka pa 15,000 kufika pa magazini oposa 141,000. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi osasowa mumzinda wa Yangon ndipo anthu ambiri m’dzikoli amawakonda.
Tinkafunikira Nthambi Yatsopano
Zipolowe za mu 1988 zitatha, akuluakulu a asilikali anapempha mabungwe azipembedzo komanso mabungwe ena kuti alembetse m’kaundula waboma. Mwamsanga ofesi ya nthambi inachitadi zimenezo. Choncho patapita zaka ziwiri, pa January 5, 1990, boma la Myanmar linalemba m’kaundula bungwe lathu la “Jehovah’s Witnesses (Watch Tower) Society.”
Pa nthawi imeneyi n’kuti abale atasamutsa ofesi ya nthambi kuchoka ku 39th Street kupita m’nyumba ina yosanja imene ili m’mbali mwa msewu wa Inya ndipo ili pamalo okwana hafu ya ekala. Kudera limeneli kuli anthu ambiri olemera ndipo derali lili kumpoto kwa mzinda wa Yangon. Koma nyumba yatsopanoyi inali yochepa kwambiri. M’bale Viv Mouritz yemwe anali woyendera nthambi pa nthawiyo ananena kuti: “Anthu 25 omwe ankatumikira pa Beteli ankakumana ndi mavuto ambiri. Kukhitchini kunalibe chophikira chachikulu moti mlongo ankaphikira pa chophikira chamagetsi chaching’ono. Komanso analibe makina ochapira zovala moti mlongo ankachapa pamanja. Abalewo ankafuna kugula chophikira chachikulu ndi makina ochapira koma zinali zosatheka kuitanitsa zinthu zimenezi kuchokera kunja.”
Zinali zoonekeratu kuti abalewa ankafunika ofesi yaikulu. Choncho Bungwe Lolamulira linavomereza kuti agwetse ofesiyo, yomwe inali ya nsanjika ziwiri, n’kumangapo ya nsanjika zinayi zogona komanso maofesi. Komabe abalewa asanayambe kumanga, panali mavuto ena omwe ankafunika kuthana nawo. Choyamba, ankafunika kuonana ndi madipatimenti 6 aboma ogwira ntchito zosiyanasiyana. Chachiwiri, makampani omanga nyumba m’dzikoli sakanatha kugwira ntchitoyo chifukwa sankadziwa bwino kumanga nyumba pogwiritsa ntchito zitsulo. Chachitatu, zinali zovuta kuti anthu odzipereka ochokera m’mayiko ena abwere m’dzikoli. Ndipo vuto lomaliza linali lakuti m’dzikoli munalibe zipangizo zomangira komanso zinali zovuta kuitanitsa zipangizozo kuchokera kumayiko ena. Choncho zinkaoneka ngati ntchitoyi ilephereka. Komabe abalewo ankadalira Yehova. Iwo ankanena kuti ngati Yehova walola kuti ofesi ya nthambi imangidwe, zitheka basi.—Sal. 127:1.
‘Kuti Zonsezi Zichitike Sipakufunika Mphamvu, Koma Mzimu Wanga’
M’bale Kyaw Win wa mu Dipatimenti ya Zamalamulo ya pa ofesi ya nthambi anapitiriza kufotokoza kuti: “Madipatimenti 5 aboma anavomereza mosavuta pempho lathu kuphatikizapo a Unduna Woona za Zipembedzo. Koma Komiti Yoona za Chitukuko mumzinda wa Yangon, inakana kuvomereza ponena kuti nyumba ya nsanjika zinayi yatalikitsa. Titakapempha kachiwiri, anatikaniranso. A Komiti ya Nthambi anandilimbikitsa kuti ndisagwe ulesi. Choncho ndinapemphera mobwerezabwereza kwa Yehova. Kenako ndinapita kukapemphanso kachitatu ndipo anavomereza.
“Kenako tinakaonana ndi a Unduna Woona za Anthu Olowa ndi Kutuluka M’dziko. Kumeneko anatiuza kuti anthu ochokera kumayiko ena akumaloledwa kukhala m’dzikoli kwa masiku 7 okha. Koma titawafotokozera kuti anthu amene tikufuna kuti abwerewo ndi oti aphunzitse anthu a m’dzikoli ntchito ya zomangamanga, iwo anatiloleza kuti angathe kukhala kwa miyezi 6.
“Kenako tinapita ku Unduna wa Zamalonda. Kumeneko anatiuza kuti aletsa kugula chilichonse kuchokera kunja. Koma titawauza mtundu wa ntchito imene tikufuna kugwira, anatipatsa chilolezo choti tiitanitse zipangizo zomangira nyumba, zokwana madola oposa 1 miliyoni a ku America. Nanga nkhani ya misonkho inatha bwanji? Tinapita ku Unduna wa Zachuma kumene anatiuza kuti tisalipire msonkho uliwonse. Zonsezi zinatsimikizira kuti mawu amene Mulungu ananena ndi oona akuti: ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,” watero Yehova wa makamu.’”—Zek. 4:6.
Mu 1997, anthu odzipereka anayamba kufika pamalo a ntchito. Zipangizo zambiri zinachokera kwa abale a ku Australia ndipo zina zinachokera ku Malaysia, Singapore, ndi Thailand. M’bale Bruce Pickering, yemwe ankayang’anira ntchitoyi anati: “Abale ambiri a ku Australia ankadula ndi kukonzeratu zitsulozo ndipo ankabwera nazo ku Myanmar n’kudzazilumikiza. Ngakhale kuti ankapangira zimenezi padera koma zinkalumikizana bwinobwino mogwirizana ndi mmene pulani ya nyumbayo inalili.” Anthu ena odzipereka ankachokera ku Britain, Fiji, Germany, Greece, New Zealand, ndi ku United States.
Kanali koyamba patadutsa zaka 30 kuti abale ndi alongo a ku Myanmar achitire zinthu limodzi ndi abale a m’mayiko ena. M’bale Donald Dewar ananena kuti: “Tinasangalala kwambiri. Tinkangoona ngati n’kutulo. Tinalimbikitsidwa kwambiri mwauzimu. Komanso tinalimbikitsidwa kuona chikondi ndi kudzipereka kumene abale ochokera m’mayiko ena anasonyeza.” M’bale wina ananenanso kuti: “Tinaphunzira ntchito zosiyanasiyana zamanja. Mwachitsanzo, ofalitsa omwe anali asanagwiritsepo ntchito magetsi anaphunzira kuika mawaya amagetsi m’nyumba. Ena anaphunzira kuika zipangizo zoziziritsira m’nyumba. Komanso tinaphunzira kugwiritsa ntchito zida zogwiritsa ntchito magetsi.”
Nawonso abale ochokera m’mayiko ena analimbikitsidwa kwambiri poona chikhulupiriro ndi chikondi cha abale ndi alongo a ku Myanmar. M’bale Bruce Pickering anati: “Ngakhale kuti abalewo anali osauka, anali ndi mtima wopatsa. Mwachitsanzo, ambiri anatiitanira kunyumba kwawo kuti tikadye nawo chakudya chimene akanatha kudya ndi mabanja awo kwa masiku ambiri. Zimene tinaona zinatikumbutsa mfundo yoti zinthu zofunika kwambiri pa moyo ndi kukhala ndi banja losangalala, kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, kusangalala ndi ubale wathu wachikhristu komanso kulandira madalitso ochokera kwa Mulungu.”
Pa January 22, 2000, panali mwambo wapadera wotsegulira ofesi ya nthambi yatsopano ndipo mwambowo unachitikira muholo ina ya m’dzikoli. Abale anasangalala kulandira m’bale John E. Barr wa m’Bungwe Lolamulira yemwe anakamba nkhani yotsegulira nyumbayi.
Kumanga Nyumba za Ufumu Zatsopano
Ntchito yomanga ofesi ya nthambi itatsala pang’ono kutha, abale anayamba kuganizira za ntchito inanso yofunikira kwambiri yomanga Nyumba za Ufumu. Mu 1999 m’bale Nobuhiko Koyama ndi mkazi wake Aya anafika kuchokera ku Japan. M’baleyu anathandiza kukhazikitsa Dipatimenti Yoyang’anira Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu ya pa ofesi ya nthambi. M’bale Koyama anati: “Tinayamba ndi kuyendera malo amene abale ankachitira misonkhano ya mpingo m’dziko lonselo. Kuti tifike m’malo onsewa tinkafunika kukwera basi, ndege, njinga zamoto, njinga zakapalasa, boti komanso kuyenda pansi. Kawirikawiri tinkafunika kukhala ndi makalata aboma otiloleza kuyenda m’madera osiyanasiyana chifukwa chakuti anthu a kumayiko ena ankaletsedwa kufika kumadera ambiri. Tikapeza malo ofunika kumangapo Nyumba ya Ufumu yatsopano, Bungwe Lolamulira linkapereka ndalama kuchokera m’thumba la ndalama zomangira Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka.
“Titasankha anthu odzipereka, tinawatumiza kudera la Shwepyitha lomwe lili mumzinda wa Yangon kuti akayambe kumanga Nyumba ya Ufumu yoyamba. Abale ochokera kumayiko ena ndi abale a m’dzikoli ankagwira ntchito limodzi. Zimenezi zinadabwitsa apolisi a m’derali moti anaimitsa ntchitoyo maulendo angapo kuti akafunse kwa mabwana awo ngati n’zololeka kuti abale a ku Myanmar azigwira ntchito limodzi ndi abale ochokera kumayiko ena. Komabe ena ankayamikira abalewa. Mwachitsanzo, munthu wina ananena kuti: ‘Ndaona munthu wochoka kunja akukolopa m’chimbudzi. Sindinaonepo munthu wakunja akugwira ntchito yotereyi. Anthu inu ndinu osiyana kwambiri ndi ena onse.’
“Pa nthawiyi, gulu lina linayamba ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu yatsopano ku tauni ya Tachileik imene ili m’malire mwa dziko la Myanmar ndi Thailand. Tsiku lililonse, abale ambiri ochokera ku Thailand ankalowa m’dziko la Myanmar kudzathandizana ndi abale awo pa ntchitoyi. Abalewa ankagwira ntchito mogwirizana ngakhale kuti ankalankhula zinenero zosiyana. Pa nthawi imene abale a ku Myanmar ankathandizana ntchito ndi abale a ku Thailand, asilikali a mayiko awiriwa anayamba kumenyana m’malire a mayikowa. Apa n’kuti ntchito yomanga Nyumba ya Ufumuyo itatsala pang’ono kutha. Mabomba komanso zipolopolo zinkagwera pafupi ndi Nyumba ya Ufumuyo koma sinawonongeke. Asilikaliwo atasiya kumenyana, abale ndi alongo okwana 72 anasonkhana pa mwambo wopereka nyumbayo kwa Yehova, Mulungu wa mtendere.”
Kuchokera mu 1999, magulu omanga Nyumba za Ufumu amanga nyumba zatsopano zoposa 65 m’dziko lonseli
Kuchokera mu 1999, magulu omanga Nyumba za Ufumu amanga nyumba zatsopano zoposa 65 m’dziko lonseli. Kodi abale anakhudzidwa bwanji? Anthu ambiri anayamikira ntchito imeneyi. Mwachitsanzo, mlongo wina analankhula akusangalala komanso misozi ili m’maso kuti: “Sindinkaganiza m’pang’ono pomwe kuti tingadzakhale ndi nyumba yatsopano komanso yokongola ngati imeneyi. Choncho ndiyesetsa mmene ndingathere kuitanira anthu achidwi ku misonkhano. Ndikuthokoza Yehova komanso gulu lake chifukwa cha kukoma mtima kumene watisonyeza.”
Amishonale Anayambiranso Kubwera
Cha m’ma 1990, patadutsa zaka zambiri dziko la Myanmar lisakulandira alendo a m’mayiko ena, tsopano linayambiranso kuwalola kubwera. Ofesi ya nthambi inapempha chilolezo ku boma kuti amishonale ayambirenso kulowa m’dzikoli. Ndiyeno mu January 2003, kunabwera m’bale Hiroshi Aoki ndi mkazi wake Junko omwe anamaliza maphunziro awo ku sukulu ya Giliyadi. Iwo anali ochokera ku Japan ndipo anali amishonale oyamba kubwera ku Myanmar patadutsa zaka 37.
M’bale Aoki anati: “Popeza kuti tinalipo alendo ochepa m’dzikoli, tinafunika kulalikira mochenjera kuti aboma asatikayikire. Choncho koyambirira tinkaonetsetsa kuti tikuyenda limodzi ndi abale ndi alongo a komweko popita kumaphunziro ndi maulendo awo obwereza. Tinaona kuti anthu ambiri a ku Myanmar amakonda kukambirana za Mulungu. Tsiku loyamba kulalikira, tinayambitsa maphunziro a Baibulo okwana 5.”
Mlongo Aoki anawonjezera kuti: “Nthawi zambiri tinkaona kuti Yehova akutithandiza. Tsiku lina tikuchokera kopangitsa phunziro m’mudzi wina pafupi ndi mzinda wa Mandalay njinga yathu yamoto inatiphwera tayala. Tinayamba kuikankha n’kuipititsa pa fakitale ina kuti akatikonzere. Mlonda anauza mwamuna wanga Hiroshi kuti alowe ndi njingayo koma ine anandiuza kuti ndidikire pageti. Mlondayu anachita nafe chidwi.”
“Ndiye anandifunsa kuti: ‘Munabwera kudzatani m’dziko lino?’
“Ndinamuyankha kuti: ‘Tinabwera kudzaona anzathu.’
“Anandifunsanso kuti: ‘Kudzangowaona basi, kapena mwabwerera zachipembedzo?’
“Ndinangokhala chete chifukwa sindimadziwa kuti akundifunsira chiyani.
“Anapitirizabe kundifunsa kuti: ‘Tandiyankhani zoona, ndinu a chipembedzo chanji?’
“Ndinangopisa m’chikwama changa n’kutenga magazini ya Nsanja ya Olonda n’kumuonetsa.
“Ataona magaziniyo anati: ‘Ndinadziwa ine!’ Kenako anauza antchito anzake kuti: ‘Waphwetsa tayala lija ndi mngelo kuti a Mboni za Yehova abwere kuno.’
“Mlonda uja anatulutsa Baibulo ndi kapepala kathu m’chikwama chake. Iye ankaphunzira Baibulo ndi Mboni kudera lina, koma atasamukira ku Mandalay sanaonanenso ndi abalewo. Choncho tinayamba kuphunzira naye Baibulo nthawi yomweyo. Patapita nthawi, anzake ena ogwira nawo ntchito anayambanso kuphunzira.”
Mu 2005, amishonale enanso anayi anafika ku Myanmar. Amishonale amenewa anachokera ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki (imene panopa imadziwika kuti Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira) ya ku Philippines. Koma m’bale mmodzi, dzina lake Nelson Junio ankasungulumwa, vuto limene amishonale ambiri amakumana nalo. Iye anati: “Nthawi zambiri ndinkalira komanso kupemphera ndisanagone. Kenako m’bale wina wokoma mtima anandisonyeza lemba la Aheberi 11:15, 16. Lembali limanena za Abulahamu ndi Sara kuti sankangoganizira zakwawo ku Uri koma anapitiriza kutumikira Mulungu. Nditawerenga lembali sindinalirenso. Ndinayamba kuona kuti kwathu ndi gawo lomwe ndinkatumikiralo.”
Chitsanzo Chawo Chabwino Chinathandiza Anthu Ambiri
M’nthawi ya atumwi, mtumwi Paulo analangiza Timoteyo kuti: “Zinthu zimene unazimva kwa ine . . . uziphunzitse kwa anthu okhulupirika amene nawonso, adzakhala oyenerera bwino kuphunzitsa ena.” (2 Tim. 2:2) Pomvera malangizo amenewa ndi mtima wonse, amishonale anayesetsa kuthandiza mipingo ya ku Myanmar kuti izichita zinthu motsatira dongosolo limene anthu a Yehova akutsatira padziko lonse.
Mwachitsanzo, amishonalewa anaona kuti ofalitsa ambiri akamaphunzitsa Baibulo ankauza ophunzira awo kuti akawafunsa funso azingowerenga yankho lake mmene lilili m’buku. Iwo ankachita zimenezi potengera zimene zinkachitika m’masukulu ambiri a ku Myanmar. M’bale Joemar Ubiña anati: “Moleza mtima tinalimbikitsa ofalitsa kuti azigwiritsa ntchito mafunso othandiza munthu kufotokoza maganizo ake komanso mmene akumvera. Mwamsanga ofalitsawo anagwiritsa ntchito malangizo amenewa ndipo anayamba kuphunzitsa mogwira mtima.”
Amishonalewa anaonanso kuti m’mipingo yambiri munali mkulu mmodzi kapena mtumiki wothandiza basi. Akulu ena ndi atumiki othandiza, ngakhale kuti anali okhulupirika komanso olimbikira, ankalamulira nkhosa ngati mabwana. Zimenezi ziyenera kuti zinkachitikanso m’nthawi ya atumwi moti mtumwi Petulo anauza akulu kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu . . . Osati mochita ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:2, 3) Kodi amishonalewa anawathandiza bwanji abale awowa? M’bale Benjamin Reyes ananena kuti: “Tinayesetsa kukhala zitsanzo zabwino pokhala okoma mtima, odekha kwambiri komanso ochezeka.” Pang’ono ndi pang’ono chitsanzo chawo chabwino chinathandiza kwambiri abalewo. Akulu ambiri anasintha ndipo ankasamalira nkhosa mwachifundo kwambiri.
Anthu Anayamba Kupindula ndi Mabuku Omasuliridwa Mwaluso
Kwa zaka zambiri anthu a ku Myanmar ankagwiritsa ntchito Baibulo lomwe linamasuliridwa m’zaka za m’ma 1800. Baibulo limeneli linamasuliridwa ndi amishonale a matchalitchi omwe amati ndi achikhristu ndipo anathandizidwa ndi Amonke. Baibuloli linali lovuta kumva chifukwa munali mawu achikale achibuda. Choncho abale anasangalala kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu litatulutsidwa m’Chimyanima, mu 2008. Maurice Raj anati: “Pa nthawiyi abale anawombera m’manja kwa nthawi yaitali, ndipo ena ankalira chifukwa chosangalala atalandira Baibulo lawolawo. Baibulo latsopanoli ndi lomveka bwino, losavuta komanso ndi lolondola ndipo ngakhale Abuda amalimva mosavuta.” Baibulo limeneli litatulutsidwa, chiwerengero cha maphunziro a Baibulo m’dzikoli chinawonjezereka ndi maperesenti oposa 40.
Mofanana ndi zinenero zina zambiri, Chimyanima chili pawiri. Pali chimene chinachokera ku chinenero cha Chipali ndi Chisansikiriti komanso pali chimene chimalankhulidwa tsiku ndi tsiku. Zonse ziwiri zimalankhulidwa komanso kulembedwa. M’mabuku athu akale mumapezeka Chimyanima chakale chimene anthu ambiri masiku ano chimawavuta kumva. Chifukwa cha zimenezi, posachedwapa ofesi ya nthambi inayamba kumasulira mabuku athu m’Chimyanima chimene anthu amalankhula tsiku ndi tsiku ndipo ndi chosavuta kumva.
Anthu anasangalala kwambiri ndi mabuku atsopanowa. Mwachitsanzo, m’bale Than Htwe Oo yemwe ndi woyang’anira Dipatimenti Yomasulira Mabuku ananena kuti: “Poyamba anthu ankanena kuti, ‘Mabuku anu ndi apamwamba kwambiri koma ndi ovuta kumva.’ Koma panopa amasangalala kwambiri akalandira mabukuwa ndipo amayamba kuwerenga nthawi yomweyo. Ambiri amanena kuti, ‘Bukuli ndi losavuta kumva.’” Ngakhalenso ku misonkhano ya mpingo anthu ambiri anayamba kuyankha chifukwa chakuti tsopano amamvetsa mfundo za m’mabuku athu.
Panopa m’Dipatimenti Yomasulira Mabuku muli abale ndi alongo okwana 26 amene akumasulira zinenero zitatu, Chimyanima, Chihakha Chini ndi Chisokayini. Palinso mabuku ena omwe anamasuliridwa m’zinenero zina 11 za m’dzikoli.
Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Nargis
Pa May 2, 2008, m’dziko la Myanmar munachitika chimphepo cha mkuntho chotchedwa Nargis chomwe chinkathamanga makilomita 240 pa ola limodzi. Chimphepochi chinapha anthu ndi kuwononga zinthu kuchokera kumene kwathera mtsinje wa Ayeyarwady mpaka kukafika kumalire ndi dziko la Thailand. Anthu oposa 2 miliyoni anakhudzidwa ndi chimphepochi ndipo anthu 140,000 anafa kapena kusowa.
Mboni za Yehova masauzande ambiri anakhudzidwa ndi chimphepochi koma chosangalatsa n’choti palibe amene anaphedwa kapena kuvulala. Ambiri anathawira m’Nyumba za Ufumu zomwe zinali zitangomangidwa kumene. M’mudzi wina wotchedwa Bothingone womwe uli pafupi ndi mtsinje wa Ayeyarwady, Mboni zokwanira 20 ndiponso anthu ena 80 anabisala kudenga la Nyumba ya Ufumu kwa maola 9. Iwo anabisala kudengako chifukwa chakuti madzi ankawonjezereka mpaka kutsala pang’ono kufika kudengako koma kenako anaphwa.
Mwamsanga ofesi ya nthambi inatumiza abale othandiza pakagwa tsoka kumadera amene anakhudzidwa kwambiri. Abalewa anadutsa m’malo ovuta mmene munali mitembo yokhayokha mpaka kukafika kumudziwo kukapereka chakudya, madzi ndi mankhwala. Iwo anali anthu oyambirira kufika kuderali kukapereka chithandizo. Abalewo atapereka zinthu zosiyanasiyana kwa abale ndi alongo, anakamba nkhani za m’Malemba zolimbikitsa kwambiri ndiponso anawapatsa Mabaibulo ndi mabuku chifukwa choti zinthu zawo zonse zinali zitakokoloka.
Pofuna kuti ntchito yaikulu yopereka thandizo kwa anthu okhudzidwawo iyende bwino, ofesi ya nthambi inakhazikitsa makomiti opereka thandizo pakagwa tsoka ku Yangon ndi ku Pathein. Makomiti amenewa anapeza anthu ambiri odzipereka kuti akapereke madzi, mpunga ndi zinthu zina zofunika kwa anthu amene anakhudzidwa ndi chimphepocho. Anapanganso magulu a anthu odziwa zomangamanga ndi kuwatumiza kuti akamange nyumba za Mboni zimene zinawonongedwa ndi chimphepo chimenechi.
Mmodzi mwa anthu amene anadzipereka kuthandiza anthu pa nthawiyi anali a Tobias Lund. Iwo anafotokoza kuti: “Ine ndi mkazi wanga Sofia tinapeza mtsikana wina wa zaka 16, dzina lake May Sin Oo, atayanika Baibulo lake padzuwa pa bwinja la nyumba yawo. M’banja mwawo, mtsikana yekhayu ndi amene anali wofalitsa. Atationa anamwetulira, misozi ikutsikira m’masaya mwake. Pasanapite nthawi, gulu la abale odziwa zomangamanga aja linafika litavala zipewa zodzitetezera pogwira ntchito ndipo anabwera ndi zipangizo zosiyanasiyana. Kenako anayamba kumangira banjali nyumba yatsopano. Anthu oyandikana nawo anadabwa kwambiri, ndipo kwa masiku ambiri ankabwera kudzaonerera ntchitoyi. Anthu ambiri m’dera lonselo anachita chidwi ndi zimene zinkachitikazo moti ankanena kuti: ‘Zoterezi sitinazionepo chiyambire. Anthu a m’chipembedzo chanu ndi ogwirizana ndipo amakondana kwambiri. Ifenso tikufuna tikhale a Mboni za Yehova.’ Panopa makolo a May Sin Oo komanso abale ake akusonkhana nafe ndipo banja lonse likupita patsogolo mwauzimu.”
Ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi tsoka limeneli inachitika kwa miyezi ingapo. Pa nthawiyi, abale anapereka zinthu zambiri kwa anthu komanso anakonza kapena kumanganso nyumba za abale zokwana 160 ndi Nyumba za Ufumu 8. N’zoona kuti mphepo yamkuntho ya Nargis inabweretsa mavuto aakulu ku Myanmar, komabe inathandizanso kuti anthu aone okha chikondi chimene chimagwirizanitsa anthu a Mulungu ndi kuchititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe.
Msonkhano Wosaiwalika
Kumayambiriro kwa chaka cha 2007, ofesi ya nthambi ku Myanmar inalandira kalata yosangalatsa kwambiri. M’bale Jon Sharp, limodzi ndi mkazi wake Janet, amene anali atangotha chaka chimodzi m’dzikoli, anati: “Bungwe Lolamulira linatipempha kuti tikonzekere msonkhano wa mayiko umene udzachitikire mumzinda wa Yangon mu 2009. Iwo anatiuza kuti ku msonkhanowu kudzabwera alendo ambiri ochokera m’mayiko 10, zimene zinali zisanachitikepo chitsegulireni nthambi yathu.”
M’bale Sharp anapitiriza kufotokoza kuti: “Tinali ndi mafunso ambirimbiri monga akuti: ‘Kodi malo oti adzakwane anthu onsewo tidzawapeza kuti? Kodi abale akumidzi adzabwera ku msonkhanowu? Kodi adzakhala kuti? Nanga adzayenda bwanji? Kodi adzakwanitsa kupezera mabanja awo chakudya? Kodi boma la Myanmar lidzatilola kuchita msonkhano waukulu chonchi?’ Tinaganizira zinthu zambirimbiri zomwe tinkaona kuti n’zovuta. Komabe tinakumbukira mawu a Yesu akuti: ‘Zinthu zosatheka ndi anthu n’zotheka ndi Mulungu.’ (Luka 18:27) Choncho tinadalira Mulungu, ndipo tinayamba kukonzekera msonkhanowo.
“Posakhalitsa tinapeza malo abwino odzachitira msonkhanowo. Malo ake anali bwalo lamasewera lotchedwa National Indoor Stadium. Bwaloli linali ndi malo okwana anthu 11,000. Bwaloli linali mkati mwa mzinda ndipo linali ndi denga komanso zipangizo zoziziritsira pamalopo. Mwamsanga tinapempha akuluakulu oyang’anira malowo kuti atilole kudzawagwiritsa ntchito. Komabe panadutsa miyezi yambiri asanatiyankhe pempho lathu moti kunangotsala milungu yochepa kuti masiku a msonkhano afike. Kenako tinalandira nkhani yokhumudwitsa. Oyang’anira bwalolo anakonza zoti pachitike masewera ankhonya pa bwaloli pa masiku a msonkhano wathu omwewo. Popeza kuti tinalibe nthawi yofufuza malo ena, tinakambirana ndi munthu amene anakonza masewera ankhonyawo komanso akuluakulu ena kuti atithandize. Kenako wokonza masewera uja anavomera kuti angasinthe masikuwo ngati akatswiri 16 omenyanawo angalole zimenezi. Akatswiriwo atamva kuti a Mboni za Yehova akufuna kudzachita msonkhano wapadera pamalowa, onse anavomera kusintha.”
M’bale Kyaw Win yemwenso ali m’Komiti ya Nthambi anati: “Komabe tinkafunikira chilolezo cha boma kuti tigwiritse ntchito malowa ndipo anali atatikaniza kale maulendo anayi. Titapemphera kwa Yehova, tinakumana ndi mkulu wa asilikali yemwe ankayang’anira mabwalo onse a masewera ku Myanmar. Kunali kutangotsala milungu iwiri kuti msonkhanowo uchitike ndipo kanali koyamba kulankhula ndi munthu wa udindo waukulu m’boma. Koma tinasangalala kuti anatilola.”
Popeza kuti anthu sankadziwa za mavuto onsewa, alendo ochokera m’madera osiyanasiyana m’dzikoli ndi kumayiko ena anayamba kubwera ku Yangon pa ndege, pa sitima, pa boti, pa basi, m’malole komanso ena ankayenda wapansi. Mabanja ambiri ankasungira ndalama zoti adzagwiritse ntchito pa msokhanowu. Ambiri analima mbewu, ena anaweta nkhumba, ena ankasoka zovala ndipo ena ochepa ankafufuza golide m’mitsinje. Ambiri anali asanapite kumzinda waukulu komanso anali asanaonepo azungu.
Anthu oposa 1,300 ochokera kumpoto kwa Myanmar anasonkhana pasiteshoni ya sitima ku Mandalay kuti akwere sitima yopita ku Yangon imene anachita hayala. Anthu ena ochokera kudera la Naga Hills anayenda kwa masiku 6 atabereka anthu awiri olumala omwe njinga zawo zinawonongeka atangonyamuka kumene. Anthu ambiri anasonkhana pasiteshoni ya sitima, ndipo ankacheza, kuseka komanso kuimba nyimbo za Ufumu. M’bale Pum Cin Khai yemwe ankayang’anira za mayendedwe pa msonkhanowu anati: “Aliyense ankasangalala. Anthuwo tinawapatsa chakudya, madzi ndiponso zogonera. Sitima itafika, akulu anathandiza gulu lililonse kukakwera m’mabogi awo. Kenako munthu wina analankhula pa chokuzira mawu kuti: ‘Sitima ya Mboni za Yehova ikunyamuka.’ Atatero ndinayang’ana uku ndi uku kuti ndione ngati pali amene watsala, kenako ndinadumphira m’sitimayo.”
Pa nthawiyi n’kuti alendo pafupifupi 700 ochokera ku mayiko ena atafika kale m’mahotela. Koma nkhawa inali yoti nanga abale a kuno ku Myanmar oposa 3,000 azikagona kuti? M’bale Myint Lwin yemwe anali mu Dipatimenti Yoona za Malo Ogona anati: “Yehova anachititsa Mboni za ku Yangon kuchereza abale ndi alongo awo. Mabanja ena analandira mpaka alendo 15. Anakalipira ndalama zolembetsera alendowo kuboma, kuwagawira chakudya cham’mawa komanso kuwalipirira thiransipoti yopita ndi kubwera ku msonkhano tsiku lililonse. Alendo ena ambiri ankagona m’Nyumba za Ufumu ndipo enanso ambirimbiri ankagona mufakitale ina yaikulu. Ngakhale kuti tinayesetsa kuti tipezere anthuwo malo ogona, panatsalabe alendo ena 500 amene ankasowa pogona. Tinafotokoza vutoli kwa eni malowo ndipo analola kuti alendowo azigona pamalo a msonkhano pomwepo. Zimenezi zinali zisanachitikepo n’kale lonse.”
“Yehova anachititsa Mboni za ku Yangon kuchereza abale ndi alongo awo”
Popeza kuti malowo anali osasamalika, abale ongodzipereka oposa 350 anagwira ntchito yokonza malowo kwa masiku 10 kuti msonkhanowo udzachitikire pamalo abwino. M’bale Htay Win amene anali woyang’anira msonkhanowo ananena kuti: “Tinakonza mapaipi amadzi, zinthu zokhudzana ndi magetsi komanso zipangizo zoziziritsira pamalowo. Kenako tinapaka penti ndi kuyeretsa malo onsewo. Ntchito imeneyi inathandiza kuchitira umboni za Mulungu woona. Mwachitsanzo, mkulu wa asilikali amene ankayang’anira malo amenewo ananena kuti: ‘Zikomo kwambiri! Zikomo kwambiri! Ndikupempha kwa Mulungu kuti anthu inu muzigwiritsa ntchito malo ano chaka chilichonse.’”
Msonkhanowu unachitika kuyambira pa 3 mpaka pa 6 December, 2009 ndipo panasonkhana anthu oposa 5,000. Pa tsiku lomaliza, anthu ambiri anavala zovala zachikhalidwe chakwawo ndipo zinali zokongola ndi zochititsa chidwi kwambiri. Mlongo wina ananena kuti: “Pa tsiku lomalizali, anthu ankakumbatirana n’kumalira, msonkhanowo usanayambe n’komwe.” M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira atapereka pemphero lomaliza, anthu anawomba m’manja ndi kubaibitsana kwa nthawi yaitali. Anthu ambiri ankamva ngati mmene mlongo wina wa zaka 86 ankamvera. Iye anati: “Ndinkangoona ngati ndili m’dziko latsopano.”
Akuluakulu a boma ambiri anachitanso chidwi. Mwachitsanzo, mkulu wina waboma anati: “Msonkhanowu ndi wosiyana ndi misonkhano ina yonse. Palibe amene amatukwana, kusuta fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Anthu ake ndi ogwirizana ngakhale kuti ndi a mitundu yosiyanasiyana. Sindinaonepo anthu ngati amenewa.” M’bale Maurice Raj ananena kuti, “Nayenso mkulu wa asilikali wa ku Yangon anatiuza kuti iyeyo ndi anzake anali asanaonepo msonkhano wosangalatsa ngati umenewu.”
Alendo ambiri anavomereza kuti msonkhanowu unali wapadera kwambiri. Mwachitsanzo m’bale wina wakomweko anati: “Tisanachite msonkhanowu tinkangomva za ubale wathu wa padziko lonse, koma pano tadzionera tokha. Sitidzaiwala chikondi chimene abale athu atisonyeza.”
“Tisanachite msonkhanowu tinkangomva za ubale wathu wa padziko lonse, koma pano tadzionera tokha”
“Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”
Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35) Zinthu zilinso chimodzimodzi ku Myanmar masiku ano. Panopa m’dzikoli muli ofalitsa 3,790, ndipo wofalitsa aliyense akufunika kulalikira kwa anthu 15,931. Izi zikusonyeza kuti ku Myanmar kulidi ntchito yambiri yokolola. Anthu 8,005 anapezeka pa Chikumbutso cha 2012, womwe ndi umboni wakuti chiwerengero cha Mboni m’dzikoli chikhoza kuwonjezeka.
Umboni wina woti chiwerengero cha Mboni chikhoza kuwonjezeka tikuuona tikaganizira zimene zikuchitika ku dera la Rakhine, limene lili m’mbali mwa nyanja kumalire ndi dziko la Bangladesh. M’derali muli anthu pafupifupi 4 miliyoni koma kulibe wa Mboni za Yehova ngakhale mmodzi. Ponena za dera limeneli, m’bale Maurice Raj, anati: “Mwezi uliwonse timalandira makalata ambiri ochokera kwa anthu a m’derali opempha mabuku athu ndiponso amafunsa mafunso okhudza Baibulo. Komanso Abuda ambiri ku Myanmar, makamaka achinyamata, akusonyeza chidwi chofuna kuphunzira choonadi. Choncho tikupitirizabe kupempha Mwini zokolola kuti atumize antchito ambiri kukakolola.”—Mat. 9:37, 38.
“Tikupitirizabe kupempha Mwini zokolola kuti atumize antchito ambiri kukakolola”
Pafupifupi zaka 100 zapitazo, apainiya awiri olimba mtima anabweretsa uthenga wabwino m’dziko lino, limene anthu ambiri ndi Abuda. Kuchokera nthawi imeneyo, anthu ambiri amitundu yosiyanasiyana m’dzikoli aphunzira choonadi. Anthu a Mboni za Yehova m’dziko la Myanmar asonyeza kuti ndi odzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Khristu. Iwo achita zimenezi ngakhale kuti m’dzikoli munkachitika nkhondo, zipolowe, muli umphawi ndipo abale akhala akuzunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Mavuto ena ndi akuti boma limaletsa anthu a m’mayiko ena kulowa m’dzikoli komanso mumachitika masoka achilengedwe. Komabe abale ndi otsimikiza ndi mtima wonse kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu komanso “kupirira zinthu zonse ndi kukhala oleza mtima ndiponso achimwemwe.”—Akol. 1:11.
a Poyamba dziko la Myanmar linkatchedwa Burma, potengera dzina la mtundu waukulu wa anthu a m’dzikoli, otchedwa Abamara (Abama). Dzinali analisintha mu 1989 n’kukhala Union of Myanmar (Mgwirizano wa Anthu a ku Myanmar). Anachita zimenezi pofuna kusonyeza kuti m’dzikoli mulinso mitundu ina yambiri ya anthu. M’buku lino tigwiritsa ntchito dzina lakuti Burma pofotokoza zinthu zomwe zinachitika chaka cha 1989 chisanafike ndipo tigwiritsa ntchito dzina lakuti Myanmar pofotokoza zinthu zomwe zinachitika chakachi chitadutsa.
b Makaladi amene tikunena apa ndi anthu amene kholo lawo lina ndi Mmwenye pamene lina ndi lochokera ku Britain. Pa nthawi imene dzikoli linkalamuliridwa ndi dziko la Britain, amwenye ambiri anasamukira ku Burma ndipo ankatengedwa monga nzika za dzikolo.
c A Bertram Marcelline anali munthu woyamba kubatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova m’dziko la Burma. Iwo anamwalira ali wokhulupirika kumapeto kwa zaka za m’ma 1960.
d Pa nthawiyo ndalamazi zinali zambiri ndithu chifukwa zinali zokwana madola 95 a ku America.
e Onani Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1966 tsamba 192.
f Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma panopa anasiya kulisindikiza.
g Masiku ano pali zinenero zoposa 600 zimene zimasindikizidwa pogwiritsa ntchito pulogalamu imeneyi.
Yehova Ananditsegulira Njira
MAURICE RAJ
CHAKA CHOBADWA 1933
CHAKA CHOBATIZIDWA 1949
MBIRI YAKE Wakhala akuchita utumiki wanthawi zonse ku Myanmar kwa zaka zoposa 50 ndipo kwa zaka zambiri wakhala akutumikira ngati woyang’anira nthambi. Panopa akutumikirabe m’Komiti ya Nthambi.h
◆ MU 1988, mumzinda wa Yangon munayamba kuchitika zachiwawa chifukwa anthu ambiri ankachita zionetsero m’misewu pofuna kuti boma lisinthe. Zinthu zitafika povuta kwambiri, asilikali analanda boma ndipo anakhazikitsa malamulo achisilikali m’madera ambiri adzikolo. Anthu ambiri amene ankachita zionetserozo anaphedwa.
M’mwezi womwewo, tinkafunika kutumiza lipoti lapachaka la nthambi yathu kulikulu ku New York. Koma njira zonse zotumizira mauthenga zinali zitatsekedwa, moti tinkaona kuti palibe njira iliyonse yomwe tingatumizire lipotili kunja kwa dzikolo. Kenako ndinamva zoti a ku ofesi ya kazembe wa dziko la United States akufuna kutumiza makalata awo kunja kwa dzikolo pa ndege. Ndinaganiza zokapempha kuti ndegeyo itengenso lipoti lathu lija. Choncho ndinavala suti imene ndinkaidalira komanso taye n’kuyamba ulendo wapagalimoto wopita kuofesi ya kazembeyo.
Pamene ndinkadutsa mumzindawo, womwe unali matope okhaokha chifukwa cha mvula, ndinadabwa kuona kuti munalibiretu munthu aliyense. Kenako ndinapeza kuti msewu womwe ndinayenera kudutsa watsekedwa ndi chimtengo, moti ndinangoimika galimoto ija pambali pa msewu n’kuyenda wapansi mtunda wotsalawo.
Nditayandikira pageti la ofesiyo, ndinaona chigulu cha anthu omwe ankafuula pofuna kuti alowe koma asilikali okwiya anali atatseka khomo. Ndinaima kaye n’kupereka pemphero la mumtima. Mwana wina wasukulu ataona mmene ndinavalira anafuula kuti, “Munthu uyu ayenera kuti amagwira ntchito konkuno.” Atatero ndinadzipanikiza kudutsa khamu la anthulo. Nditafika pagetilo, lomwe linali lokhoma, msilikali wina wamtali komanso wooneka wamphamvu anandiyang’ana mosonyeza kuti akundikayikira.
Anandifunsa mwaukali kuti, “Ndiwe ndani, ndipo ukufuna chiyani?”
Ndinamuyankha kuti, “Ndikufuna kuonana ndi kazembe. Ndili ndi uthenga wofunika kwambiri wopita ku America.”
Choncho iye anandiyang’anitsitsa kwa nthawi yaitali. Atatero anatsegula getilo mofulumira kwambiri n’kundikokera mkati. Kenako anatsekanso getilo mwamsanga khamu la anthu lija likufuna kuyamba kulowa.
Ndiyeno anandiuza kuti, “Tiye kuno.”
Titafika pakhomo la ofesi ya kazembe, msilikaliyo anandipereka kwa munthu wina amene ankaoneka wotopa ndipo anandifunsa chimene ndikufuna.
Pamenepo ndinafotokoza kuti, “Ndachokera ku ofesi ya Watch Tower Society. Ndili ndi lipoti lofunika kwambiri limene likuyenera kukafika kulikulu lathu ku New York mwezi womwe uno. Kodi munganditumizireko lipotili pamene mukutumiza makalata anu?” Ndiyeno ndinatenga envulopu yanga n’kumupatsa, kenako ndinamuuza kuti, “Koma pepani ndilibe sitampu.”
Ndiyeno ndinatenga envulopu yanga n’kumupatsa, kenako ndinamuuza kuti, “Koma pepani ndilibe sitampu.”
Modabwa munthuyo anandifunsa mafunso angapo, kenako ananditsimikizira kuti atumiza lipotilo. Patapita nthawi ndinamva kuti lipotilo linafika kulikulu pa nthawi yake.
h Nkhani ya M’bale Raj inatuluka mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2010.
Woweruza Milandu Woona Mtima Anaphunzira Choonadi
MANG CUNG
CHAKA CHOBADWA 1934
CHAKA CHOBATIZIDWA 1981
MBIRI YAKE Anali mphunzitsi wamkulu pa sukulu ina komanso woweruza milandu wotchuka amene, patapita nthawi anakhala mpainiya wakhama.
◆ MPAINIYA wina atandipatsa magazini ya Nsanja ya Olonda kwa nthawi yoyamba, ndinamuuza kuti, “Ndilibe nthawi yowerenga zimenezi. Ndimatanganidwa kwambiri.” Koma popeza kuti ndinkasuta fodya kwambiri, ndinaganiza kuti ndingolandirabe magaziniwo kuti ndizikapichirira fodya. Choncho ndinalandira magaziniwo.
Pamene ndinkathothola pepala kuti ndipichirepo fodya, ndinaona kuti ndingachite bwino kuwerenga kaye zomwe zili papepalapo ndisanaliwononge. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kukonda kuwerenga Nsanja ya Olonda. Zimene ndinkawerenga zinandilimbikitsa kusiya kusuta ndiponso kusintha moyo wanga kuti ugwirizane ndi mfundo zolungama za Mulungu. Pasanapite nthawi ndinabatizidwa.
Nditabwerera kwathu pa tsiku limene ndinabatizidwalo, m’busa komanso akulu a tchalitchi anandipatsa ndalama pondinyengerera kuti ndibwerere ku chipembedzo changa chakale. Nditakana, anayamba kuuza anthu zabodza kuti a Mboni anandipatsa ndalama kuti andibatize. Ngakhale kuti ankandinenera zoipa, ine sindinafooke. Ndinasangalala kwambiri kuti ndinadziwa Mulungu woona ndi kuyamba kumutumikira.
Yehova Anandidalitsa Chifukwa Chopirira
AH SHE
CHAKA CHOBADWA 1952
CHAKA CHOBATIZIDWA 1998
MBIRI YAKE Asanaphunzire choonadi anali Mkatolika ndipo nthawi zina ankalalikira m’tchalitchi.
◆ KWA zaka zambiri, ndinali Mkatolika ndipo ndinkapatsidwa mwayi wolalikira m’tchalitchi cha m’dera la Golden Triangle. Nditakumana ndi a Mboni za Yehova n’kuona mmene ankagwiritsira ntchito Baibulo mwaluso, ndinavomera kuti azindiphunzitsa.
Posakhalitsa ndinayamba kulalikira m’tchalitchi Lamlungu m’mawa, koma madzulo ndinkapita ku misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu. Pasanapite nthawi, ndikamalalikira m’tchalitchi, ndinayamba kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo, ndipo zimenezi zinakwiyitsa atsogoleri achipembedzo komanso wansembe. Ndiyeno nditasiya kulalikira, atsogoleri a chipembedzowo ananditengera kukhoti n’cholinga choti andithamangitse m’mudzimo. Koma woweruza milandu anawauza kuti ndili ndi ufulu wopembedza mmene ndikufunira. Mkazi wanga sanasangalale ndi chigamulo chimenechi. Choncho anafuula kuti, “Uchoke kuno ndi Baibulo komanso chikwama chakochi!” Ngakhale kuti anandilankhula mwaukali choncho, ine sindinayankhe chilichonse, ndipo ndinapitiriza kumusamalira limodzi ndi ana athu. Ndikusangalala kwambiri kuti Yehova anandidalitsa chifukwa cha kupirira kwanga. Panopa mkazi wanga Cherry, ndiponso ana athu, akutumikira Yehova mosangalala.
Ndinasiya Kukayikira Mboni za Yehova
GREGORY SARILO
CHAKA CHOBADWA 1950
CHAKA CHOBATIZIDWA 1985
MBIRI YAKE Kale ankagwira ntchito ku tchalitchi cha Katolika ndipo ankaganiza kuti Mboni za Yehova ndi aneneri onyenga.
◆ KWA zaka zambiri ndinali wodzipereka ku tchalitchi cha Katolika ndipo ndinkatsogolera zochitika za tchalitchichi m’mudzi mwathu. Pa nthawiyi ndinaona kuti atsogoleri a tchalitchi ankalekerera anthu kumachita zachiwerewere, kupereka nsembe kwa mizimu, komanso kuchita zinthu zosonyeza kukhulupirira mizimu. Chifukwa chonyansidwa ndi zimenezi, ndinasiya kugwira ntchito za tchalitchi koma ndinapitirizabe kutsatira zikhulupiriro za Katolika.
Mu 1981, ndinakumana ndi Mboni za Yehova. Ndinachita chidwi kwambiri chifukwa iwo ankalidziwa bwino Baibulo ndipo ndinavomera kuti azindiphunzitsa. Komabe, pa nthawiyi ndinkakayikira kwambiri zimene iwo ankaphunzitsa ndipo nthawi zambiri ndinkatsutsa zonena zawo. Koma iwo ankayankha mafunso anga moleza mtima pogwiritsa ntchito Baibulo.
Kenako ndinapita ku msonkhano wachigawo kuti ndikaone ngati a Mboni onse amaphunzitsa zinthu zofanana. Pa nthawi yopuma, ndinaiwala chikwama changa pansi pa mpando umene ndinakhala. M’chikwamachi munali chiphaso changa, ndalama ndiponso zinthu zina zofunika. Ndinkakhulupirira kuti chikwamacho chibedwa moti sindikachipeza. Koma abale ananditsimikizira kuti: “Usadandaule. Ukachipeza ukabwerera.” Ndinathamanga kupita pomwe ndinakhala paja ndipo ndinadabwa kupeza kuti chinalidi pomwepo. Kuyambira pomwepo, ndinasiya kukayikira Mboni za Yehova.
Ndinapeza “Chuma Chopambana”
SA THAN HTUN AUNG
CHAKA CHOBADWA 1954
CHAKA CHOBATIZIDWA 1993
MBIRI YAKE Kale anali wodzipereka kwambiri m’chipembedzo cha Chibuda komanso anali msilikali. Ataphunzira choonadi, anachita upainiya kwa zaka zambiri.
◆ NDINAKULIRA m’banja lachibuda ndipo kwa nthawi ndithu ndinali mmonke wachibuda. Sindinkakhulupirira kuti kuli Mulungu kapena Mlengi. Kenako mnzanga wina amene ankati ndi “Mkhristu” ananditenga kutchalitchi kwawo kumene ndinamva zoti anthu ali ndi Atate wawo kumwamba. Choncho ndinkafunitsitsa nditawadziwa Atate amenewo komanso kukhala nawo pa ubwenzi.
Nthawi yanga yokhala mmonke itatha, ndinalowa usilikali. Pogwira ntchito ya usilikali ndinkalemba zochitika za tsiku ndi tsiku. Ndikafuna kulemba chilichonse chimene chachitika ndinkayamba ndi mawu akuti “Atate, Mulungu wakumwamba.” Patapita nthawi ndinapempha kuti ndisiye usilikali kuti ndikakhale m’busa wa tchalitchi, koma akuluakulu anga sanandilole. Kenako anandikweza udindo ndipo ndinakhala kaputeni. Chifukwa cha udindo umenewu, ndinatchuka kwambiri komanso ndinapeza ndalama zochuluka. Koma mumtima mwangamu ndinkamva njala yauzimu.
Mu 1982, ndinakwatira Htu Aung. Mkulu wake wa mkazi wangayu anali wa Mboni za Yehova ndipo anatipatsa buku lakuti Kuchokera ku Paradaiso Wotayika Kunka ku Paradaiso Wopezekanso. Nditawerenga m’bukuli zoti dzina la Mulungu ndi Yehova, ndinakayikira kwambiri zimenezo. Ndiyeno ndinauza mkazi wanga kuti, “Ngati ungandionetse dzina lakuti Yehova m’Baibulo la Chimyanima, ine ndidzakhala wa Mboni za Yehova.” Iye anayesetsa kufufuza dzinali m’Baibulo lake koma sanalipeze. Koma mnzake wina dzina lake Mary, amenenso anali wa Mboni, analipeza mosavuta. Nthawi yomweyo anandisonyeza dzina lakuti Yehova. Pambuyo pake, ine ndi mkazi wanga pamodzi ndi ana athu tinayamba kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo tinavomera kuti tiziphunzira Baibulo.
Pamene ndinkaphunzira zinthu zambiri za m’Baibulo, mtima wofuna kutumikira Mulungu unakulirakulira. Kenako mu 1991, ndinapemphanso kuti ndisiye usilikali. Pa nthawiyi ndinaganiza zosiya usilikaliwo kuti ndikakhale wa Mboni za Yehova. Patadutsa zaka ziwiri, ndinaloledwa kusiya ntchito ya usilikali, ndipo chaka chomwecho, ine ndi mkazi wanga tinabatizidwa.
Ndiyeno ndinayamba kugulitsa chakudya kumsika kuti ndizitha kuthandiza banja langa. Koma achibale anga ndi anzanga ankandinena kuti sindinaganize bwino kusiya ntchito yabwino ya usilikali n’kumagwira ntchito yonyozeka. Komabe ndinakumbukira kuti pofuna kutumikira Mulungu, Mose anachoka m’nyumba yachifumu ya Farao n’kukakhala m’busa. (Eks. 3:1; Aheb. 11:24-27) Patapita nthawi ndinakwaniritsa cholinga changa chachikulu chokhala mpainiya wokhazikika.
Anzanga ena amene ndinkagwira nawo ntchito ya usilikali anapatsidwa maudindo akuluakulu ndipo analemera kwambiri. Koma ine ndapeza “chuma chopambana,” chomwe ndi madalitso amene amabwera chifukwa chodziwa komanso kutumikira Atate wathu wakumwamba. (Aef. 2:7) Chifukwa cha zimenezi, panopa mwana wanga wamkulu akutumikira ku Beteli ya ku Myanmar ndipo ana angapo a mlamu wanga akuchita utumiki wa nthawi zonse.
Ndinaphunzira Choonadi Chifukwa cha Kukoma Mtima Kwawo
ZAW BAWM
CHAKA CHOBADWA 1954
CHAKA CHOBATIZIDWA 1998
MBIRI YAKE Poyamba ankagulitsa mankhwala osokoneza bongo ndipo ankatsutsa kwambiri choonadi. Koma Akhristu ena atamusonyeza kukoma mtima, zinamukhudza mtima kwambiri ndipo anasintha.
◆ MKAZI wanga Lu Mai atayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova, sindinagwirizane nazo ndipo ndinachita zinthu zoipa zambiri n’cholinga choti asiye kuphunzirako. Baibulo lake ndinalitayila m’chimbudzi ndipo a Mboni akafika kwathu ndinkawathamangitsa.
Kenako ndinayamba kugulitsa mankhwala osokoneza bongo ndipo zotsatira zake ndinamangidwa ndi kuikidwa m’ndende. Nditakhala kundendeko tsiku limodzi, mkazi wanga ananditumizira Baibulo ndi kalata yolimbikitsa. M’kalatayo analembamonso malemba. Patapita nthawi ananditumiziranso makalata ena olimbikitsa mwauzimu. Kenako ndinazindikira kuti ndikanatsatira malangizo a m’Baibulo, sindikanapezeka ndili m’ndende.
Tsiku lina mosayembekezera kundendeko kunafika alendo awiri amene anabwera kudzandiona. Anthuwo anali a Mboni za Yehova ndipo anandiuza kuti mkazi wanga ndi amene anawapempha kuti abwere kudzandilimbikitsa. Kuti adzafike kundendeko, iwo anayenda kwa masiku awiri. Zimene anachitazi zinandipatsa chidwi ndipo ndinawayamikira kwambiri. Pa nthawiyi panalibe m’bale wanga aliyense yemwe anabwera kudzandiona. Koma amene anabwera ndi anthu amene poyamba ndinkawachita chipongwe.
Pasanathe masiku ambiri, ndinadwala tayifodi ndipo ndinagonekedwa m’chipatala koma ndinalibe ndalama zolipirira kuchipatalako. Cha pa nthawi yomweyi, kuchipatalako kunafika munthu wina wa Mboni yemwe anatumidwanso ndi mkazi wanga kuti adzandione. Wa Mboniyo anandimvera chisoni ndipo anandilipirira ndalama zomwe zinkafunika kuti ndilandire chithandizo. Zimene anachitazi zinandichititsa kuzindikira kuti zomwe ndinkachita poyamba zinali zolakwika moti ndinachita manyazi ndipo ndinalumbira kuti nanenso ndikhala wa Mboni za Yehova. Patadutsa zaka zisanu ananditulutsa kundende kuja ndipo ndinakwaniritsadi zomwe ndinalonjeza.
Ndidzakwera Phiri Ngati Mbawala Yamphongo
LIAN SANG
CHAKA CHOBADWA 1950
CHAKA CHOBATIZIDWA 1991
MBIRI YAKE Poyamba anali msilikali ndipo anaduka miyendo yonse kunkhondo. Panopa akutumikira monga mtumiki wothandiza.
◆ NDINABADWIRA komanso kukulira m’mudzi wa Matupi, womwe uli kumapiri m’chigawo cha Chin. Tonse m’banja lathu tinkalambira mizimu yomwe tinkakhulupirira kuti inkakhala m’nkhalango ndiponso m’mapiri a m’deralo. Munthu wina akadwala m’banja lathu, tinkaika chakudya paguwa lathu lansembe n’kupemphera kwa mizimu kuti ibwere kudzadya nsembeyo. Tinkakhulupirira kuti tikachita zimenezi, mizimuyo ichiritsa wodwalayo.
Nditakwanitsa zaka 21, ndinalowa usilikali. Pa nthawi yomwe ndinkagwira ntchito ya usilikaliyi, ndinamenya nawo nkhondo zokwana 20. Mu 1977, zigawenga zinaukira kampu yathu yomwe inali pafupi ndi tauni ya Muse, m’chigawo cha Shan. Nkhondo yomenyana ndi zigawengazo inatha masiku 20. Kenako tinawapanikiza kwambiri ndipo tinayamba kuwathamangitsa. Pa nthawiyi ndinaponda bomba lomwe linakwiriridwa m’nthaka. Nditayang’ana miyendo yanga, ndinaona kuti yangotsala mafupa okhaokha opanda mnofu. Ndinkamva kuwotcha m’miyendo ndiponso ndinali ndi ludzu kwambiri, koma sindinkachita mantha. Ananditengera kuchipatala komwe anakandidula miyendo yonse. Patadutsa miyezi inayi, ananditulutsa kuchipatalako ndipo usilikali unathera pompo.
M’Paradaiso ndidzakweradi phiri ngati mmene mbawala imachitira, komanso ndidzathamanga ndi kudumpha chifukwa chachisangalalo
Ine ndi mkazi wanga, Sein Aye, tinasamukira m’tauni ya Sagaing, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Mandalay. Kumeneko ndinayamba kuluka mipando ya nsungwi kuti ndizipeza ndalama zothandizira banja langa. Ndiyeno ndinakumana ndi m’busa wa Baptist amene anandiuza kuti kuduka kwa miyendo yangayi chinali chifuniro cha Mulungu. Patapita nthawi, ine ndi Sein Aye tinakumana ndi mpainiya wina dzina lake Rebecca. Mlongoyu anatiuza kuti m’dziko lapansi la Paradaiso ndingathe kudzakhala ndi miyendo yabwinobwino ngati mmene ndinalili poyamba. Kenako, tinayamba kuphunzira Baibulo mwakhama, osati ndi m’busa uja ayi, koma ndi Rebecca.
Kuchokera nthawi imeneyi, padutsa zaka pafupifupi 30. Panopa ine ndi mkazi wanga komanso ana athu 7 omwe ndi obatizidwa, tikukhala m’mudzi wina waung’ono pafupi ndi tauni ya Pyin Oo Lwin. Tauni imeneyi ndi yosangalatsa kwambiri ndipo ili pamwamba pa phiri, pa mtunda wa makilomita 65 kuchokera mumzinda wa Mandalay. Ine ndikutumikira monga mtumiki wothandiza mumpingo wa Pyin Oo Lwin ndipo ana anga atatu ndi apainiya okhazikika. Ine ndi mkazi wanga tinayesetsa kulera ana athu m’choonadi ndipo tikusangalala kwambiri kuti anawo anamvera malangizo athu ndipo akutumikira Yehova.
Nthawi zambiri ndimayenda panjinga ya olumala n’kumalalikira m’mudzi wathu. Ndipo popita ku misonkhano, munthu wina amanditenga panjinga yamoto. Komanso ndimakwawa pogwiritsa ntchito matabwa awiri.
Lemba limene ndimalikonda kwambiri ndi la Yesaya 35:6. Lembali limati: “Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo.” Ndikuyembekezera nthawi imene miyendo yanga idzabwererenso ngati kale. Pa nthawiyo ndidzakweradi phiri ngati mmene mbawala imachitira, komanso ndidzathamanga ndi kudumpha chifukwa chachisangalalo.
Oyang’anira Oyendayenda Akhama
Oyang’anira oyendayenda akuyesetsa mwakhama kulimbikitsa abale ndi alongo awo m’dziko lonseli. Kodi ntchito yawo imayenda bwanji? Tiyeni tiyendere limodzi ndi woyang’anira woyendayenda pamene akuchezera mipingo m’dera la ku Naga Hills. Woyang’anira dera wina dzina lake Myint Lwin amene amayenda limodzi ndi mkazi wake, analemba kuti: “Chakum’mawa, ine ndi mkazi wanga tinachoka ku Kalaymyo. Tinakwera bokosibode yopanikizana kwambiri moti miyendo yathu inapanikizika pakati pa makatoni a katundu wosiyanasiyana. Anthu ena anakhala m’mbali mwa galimotolo kapena padenga pake. Galimotolo linkachita mabampu chifukwa cha kukumbika kwa msewu, ndipo kumene tinkachokera kunali chifumbi chokhachokha. Tinavala chophimba kumutu popewa fumbi.
“Patadutsa maola awiri tinafika ku tauni ya Kalaywa imene ili pafupi ndi mtsinje ndipo tinafunika kukwera boti. Poyembekezera botilo, tinkalalikira kwa anthu ogulitsa m’mashopu komanso kwa apaulendo anzathu. Ambiri mwa anthu amenewa sanamvepo kuti kuli Mboni za Yehova. Boti lathu litafika, anthu anatsika ndipo ena anakwera molimbirana kuti akapeze malo okhala. M’botimo munakwera anthu pafupifupi 100 moti tinapanikizana kwambiri ndipo likanatha kutembenuzika. Choncho tinaika mabotolo apulasitiki m’zikwama zathu n’cholinga choti ngati titagwera mumtsinje zikwamazo ziyandame.
“Patadutsa maola asanu, tinafika m’tauni ya Mawlaik kumene tinagona m’kanyumba kakang’ono ka alendo, ndipo tinapitiriza ulendo wathu nthawi ya 5 koloko m’mawa. Popeza kuti inali nyengo yadzuwa, mtsinjewo unali utaphwa. Choncho boti lathu linatitimira mumchenga maulendo anayi. Ine ndi azibambo ena tinatsika n’kuyamba kukankha botilo. Patapita maola 14 tinafika ku Homalin titatopa kwambiri ndipo tinapeza abale ndi alongo a mpingo wakumeneko akutiyembekezera. Titaona nkhope zawo zachimwemwe, tinapezanso mphamvu. Tinadziwa kuti usiku umenewo tisangalala kucheza ndi abalewo, ndipo tsiku lotsatira tipitiriza ulendo wathu wopita ku Khamti, womwe ndi mtunda woyenda maola 15.
“Tsiku lotsatira tinanyamuka ulendo wathu m’mawa kwambiri. Pa tsikuli boti lathu silinadzaze kwambiri ndipo malowa ankaonekanso osiyana ndi kumene tinachokera. Tinayenda ulendo wathu kulowera kumtunda kwa mtsinjewo ndipo m’njira tinadutsa anthu ambiri akufufuza golide mumtsinjewo. Kenako tinafika ku Khamti titatopa ndiponso thupi lonse likuwawa, koma sitinapeze m’bale wina aliyense wodzatichingamira. N’kutheka kuti kalata imene tinawatumizira, yowadziwitsa za ulendowu, sinawapeze. Choncho tinakwera matola a njinga yamoto kukafika ku Nyumba ya Ufumu ndipo tinangofikira kugona m’kachipinda kena ka pa Nyumba ya Ufumuyo.
“Kutacha tinakumana ndi ofalitsa 25 a mu mpingowo amene anabwera ku Nyumba ya Ufumu kuti adzakonzekere utumiki wakumunda. Ambiri anali a mtundu wa Chinaga umene umapezeka kumapiri amene anakafika m’dziko la India. Tinanyamuka nawo limodzi kupita kokalalikira. Mzindawu uli pamalo amene mtsinje unakhota kwambiri, pakatikati pa mapiri. Ine ndi mnzanga amene ndinayenda naye tinafika panyumba ina yansungwi. Titaodira, m’nyumbamo munatuluka mwamuna wa mtundu wa Chinaga ndipo anatiuza kuti tilowe. Iye ndi mkazi wake anamvetsera mwatcheru uthenga wa Ufumu ndipo analandira mabuku athu mosangalala. Anthu ambiri a mtundu wa Chinaga amanena kuti ndi Akhristu ndipo amachita chidwi ndi uthenga wabwino. Madzulo tinakhala nawo pa msonkhano wa mpingo. Msonkhanowu unali woyamba pa misonkhano ingapo imene inachitika mlungu umenewo.
Titaona nkhope zawo zachimwemwe, tinapezanso mphamvu
“Patadutsa mlungu umodzi, tinawoloka mtsinjewo kupita ku tauni ina yaing’ono ya Sinthe, kumene kunali ofalitsa 12. Tinachezeranso magulu atatu akutali, ndipo gulu lakutali kwambiri linali pa mtunda wa makilomita 11. Tinkapita ku gulu lililonse kuti tikalalikire nawo ndiponso kukakamba nkhani. Ofalitsa m’dera limeneli ndi osauka kwambiri ndipo ambiri tinawapeza akudwala malungo kapena chifuwa chachikulu. Komanso ofalitsawa amatsutsidwa kwambiri ndi anthu a zipembedzo zina. Ngakhale kuti akukumana ndi mavuto onsewa, iwo amalalikirabe mwakhama. Lamlungu, tinasangalala kwambiri kuona anthu 76 amene anabwera kudzamvetsera nkhani ya onse. Pa gulu limeneli panali anthu ena amene anayenda maola ambiri kuti adzafike ku Nyumba ya Ufumu.
“Kenako nthawi yoti tibwerere inakwana. Zinali zovuta kwambiri kusiyana ndi abale ndi alongo okondedwa amenewa, omwe asonyeza m’njira zosiyanasiyana kuti amakonda kwambiri Yehova. Titakwera boti lathu n’kumalowera kum’mwera, tinkaganizira kulimba kwa chikhulupiriro chawo. Ngakhale kuti mwakuthupi abalewo ndi osauka, mwauzimu ndi olemera. Tikufunitsitsa titapitanso kukawachezera.”
Ndikufuna Kulalikira Padziko Lonse Lapansi
SAGAR RAI
CHAKA CHOBADWA 1928
CHAKA CHOBATIZIDWA 1968
MBIRI YAKE Msilikali amene analandira nyota zambiri, koma kenako anaphunzira choonadi. Iye anapitirizabe kulalikira ngakhale kuti ankatsutsidwa kwambiri.
◆ NDINABADWIRA m’chigawo chamapiri cha Shan, chomwe chili kumpoto cha kum’mawa kwa dziko la Myanmar. Banja lathu linachokera mu mtundu wa Gurkha ku Nepal, ndipo chipembedzo chathu chinali Chihindu. Komanso tinkachita nawo miyambo ya chipembedzo chamakolo chokhulupirira mizimu. Potengera chikhalidwe cha mtundu wathu, ndinalowa usilikali ngati mmene anachitiranso bambo anga ndi azichimwene anga anayi. Ndinali msilikali wa dziko la Burma kwa zaka 20 ndipo ndinamenya nawo nkhondo zambiri. Mwamwayi, pa nkhondo zonsezi sindinavulale kwambiri.
Nditawerenga magazini ya Nsanja ya Olonda koyamba, ndinaphunzira kuti Baibulo limafotokoza kuti pali Mulungu woona m’modzi yekha ndipo dzina lake ndi Yehova. Zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri. Popeza ndinali Mhindu, ndinkakhulupirira kuti kuli milungu yambirimbiri. Ndinayang’ana dzina lakuti Yehova m’madikishonale azinenero zosiyanasiyana, monga Chinepali, Chihindi, Chibama ndi Chingelezi. Dikishonale iliyonse inkafotokoza kuti Yehova ndi dzina la Mulungu amene amatchulidwa m’Baibulo.
Kenako, ine ndi mkazi wanga, Jyoti, tinasamukira ku Pathein komwe a Frank Dewar, omwe anali mmishonale anandiuza kuti akhoza kumaphunzira nane Baibulo. Ndinavomera phunzirolo ndipo nayenso mkazi wanga anavomera. Pasanapite nthawi, tinatsimikizira kuti palibe Mulungu wina woona koma Yehova yekha ndipo tinaona kuti tiyenera kumatumikira iye yekha basi. Choncho mafano onse amene tinali nawo tinakawataya mumtsinje wa Pathein, n’cholinga choti wina aliyense asawatole.—Deut. 7:25; Chiv. 4:11.
Patangopita nthawi yochepa, ndinasiya usilikali ndipo ndinasamuka limodzi ndi mkazi wanga komanso ana anga kubwerera kwathu kobadwira. Titafika tinayamba kusonkhana ndi kagulu ka Mboni komwe kanatiphunzitsa kulalikira. Kenako, tinapita m’nkhalango n’kusonkhanitsa zipangizo zomangira nyumba ndipo tinamanga Nyumba ya Ufumu yaing’ono kutsogolo kwa nyumba yathu. Zimenezi zinakwiyitsa komiti yoimira anthu a mtundu wa Gurkha ndipo anatifunsa kuti: “Kodi chilolezo chomanga tchalitchi chachikhristu m’dera lachihindu mwachitenga kuti? Musiyiretu kulalikira kwa anthu oti ali kale ndi chipembedzo chawo.”
Komiti ija inakadandaula ku boma ndipo akuluakulu abomawo anandifunsa kuti: “Bambo Rai, kodi n’zoona kuti mukulalikira kwa anthu a m’dera lanu n’kumawakakamiza kuti alowe Chikhristu?”
Ndinayankha kuti: “Ndine wa Mboni za Yehova ndipo ndikufuna kulalikira padziko lonse lapansi, osati m’dera lino lokha ayi. Koma anthuwo angasankhe okha kusiya chipembedzo chawo kapena ayi.”
Pa zaka 40 zapitazi, ine ndi mkazi wanga Jyoti tathandiza anthu oposa 100 kuphunzira choonadi
N’zosangalatsa kuti akuluakulu abomawo anatilola kupitiriza kulalikira m’deralo mwaufulu.
Pa zaka 40 zapitazi, ine ndi mkazi wanga Jyoti tathandiza anthu oposa 100 kuphunzira choonadi. Ambiri mwa anthu amenewa akutumikira monga apainiya apadera, oyang’anira oyendayenda, ndipo ena akutumikira ku Beteli. Tikusangalalanso chifukwa chakuti ambiri mwa ana athu auzimu akutumikira Yehova mokhulupirika.
“Ufumu wa Yehova” Sindikuupeza
SOE LWIN
CHAKA CHOBADWA 1960
CHAKA CHOBATIZIDWA 2000
MBIRI YAKE Kale anali M’buda, koma atawerenga nkhani yonena za “Ufumu wa Yehova” ankafuna kukaona Ufumuwo.
◆ TSIKU lina ndikupita kuntchito m’tauni ya Tachileik, imene ili kufupi ndi malire a dziko la Thailand, ndinatola magazini a Nsanja ya Olonda omwe anatayidwa mumsewu. Magaziniwo ankafotokoza za madalitso osangalatsa a Ufumu wa Yehova. Popeza ndinali M’buda, ndinali ndisanamvepo za Yehova, choncho ndinaganiza kuti “Ufumu wa Yehova” uyenera kuti ndi dziko linalake ku Africa. Ndiyeno ndinatenga buku la mapu kuti ndione pamene pali “Ufumu wa Yehova” koma sindinaupeze. Ndinafunsa anthu ena, koma sanandithandize.
Patapita nthawi, ndinamva kuti mnyamata wina wa kuntchito kwathu ankaphunzira ndi Mboni za Yehova. Choncho ndinamufunsa kuti, “Kodi Ufumu wa Yehova umapezeka kuti?” Nditamva zoti Ufumu wa Yehova uli kumwamba ndipo udzabweretsa Paradaiso padziko lapansi, ndinadabwa komanso kusangalala kwambiri. Ndinameta tsitsi langa, ndinasiya kugwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, ndiponso ndinasiya kuchita miyambo yachibuda. Panopa ndikuyembekezera mwachidwi kwambiri kudzakhala mu Ufumu wa Yehova.—Mat. 25:34.