Kodi Mufunikiradi Kupepesa?
‘SINDIMAPEPESA konse,’ analemba motero George Bernard Shaw. ‘Zimene zachitidwa zachitidwa,’ ena angatero.
Mwinamwake ifeyo sitimafuna kuvomera cholakwa chifukwa cha kuwopa kutaya ulemu wathu. Mwinamwake timaŵiringula tikumati winayo ndiye ali ndi vuto. Kapena tingafune kupepesa koma nkuzikankhira kutsogolo mpaka pamene tidzaona kuti nkhaniyo yaiŵalika pomalizira pake.
Chotero, kodi kupepesa nkofunika? Kodi kungakwaniritsedi chilichonse?
Chikondi Chimatikakamiza Kupepesa
Chikondi cha pa abale ndicho chizindikiro cha otsatira oona a Yesu Kristu. Iye anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Malemba amalimbikitsa Akristu ‘kukondana kwenikweni kuchokera kumtima.’ (1 Petro 1:22) Chikondi chenicheni chimatikakamiza kupepesa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kupanda ungwiro kwa munthu nthaŵi zonse kumachititsa kukhumudwa kumene kumaletsa chikondi ngati sikuthetsedwa.
Mwachitsanzo, chifukwa cha kusamvana ndi wina wake mumpingo wachikristu, tingasankhe kusamlankhuza. Ngati ndife tinali olakwa, kodi unansi wachikondi ungabwezeretsedwe motani? Nthaŵi zambiri, mwa kupepesa ndiyeno kuyesayesa kulankhulana m’njira yachikondi. Tili ndi mangawa a chikondi kwa okhulupirira anzathu, ndipo pamene tinena kuti pepani ndinalakwa, timalipa ena a mangawa amenewo.—Aroma 13:8.
Mwachitsanzo: Mari Carmen ndi Paqui ndi akazi aŵiri achikristu amene anali mabwenzi kwa nthaŵi yaitali. Komabe, chifukwa chakuti Mari Carmen anakhulupirira mseche wina woipa, ubwenzi wake ndi Paqui unazimiririka. Popanda kufotokoza, analekeratu kuyanjana ndi Paqui. Patapita pafupifupi chaka chimodzi, Mari Carmen anazindikira kuti msechewo unali wabodza. Kodi anachitanji? Chikondi chinamsonkhezera kupita kwa Paqui ndi kufotokoza modzichepetsa chisoni chake chachikulu kaamba ka khalidwe loipa kwambirilo. Onse aŵiri analira kwambiri, ndipo akhala mabwenzi apamtima kuyambira pamenepo.
Ngakhale kuti sitikulingalira kuti talakwitsa chilichonse, kupepesa kungathetse kusamvana. Manuel akukumbukira kuti: “Zaka zambiri kumbuyoku ineyo ndi mkazi wanga tinakhala m’nyumba ya mmodzi wa alongo athu auzimu pamene anali m’chipatala. Tinachita zonse zotheka kumthandiza iye ndi ana ake mkati mwa kudwala kwake. Koma atabwerera kunyumba, anadandaula kwa mnzake kuti sitinayendetse bwino ndalama za m’nyumba.
“Tinapitako ndi kufotokoza kuti mwinamwake chifukwa cha ubwana wathu ndi kupanda chidziŵitso, sitinasamalire zinthu monga momwe akanachitira. Nthaŵi yomweyo anayankha mwa kunena kuti ndiye amene anali ndi mangawa kwa ife ndi kuti anali woyamikiradi kaamba ka zonse zimene tinamchitira. Vutolo linatha. Chochitika chimenecho chinandiphunzitsa kufunika kwa kupempha chikhululukiro modzichepetsa pamene kusamvana kuchitika.”
Yehova anadalitsa okwatirana ameneŵa kaamba ka kusonyeza chikondi ndi ‘kulondola zinthu za mtendere.’ (Aroma 14:19) Chikondi chimaphatikizaponso kuzindikira malingaliro a ena. Petro akutipatsa uphungu wakuti tikhale “ochitirana chifundo.” (1 Petro 3:8) Ngati timachitirana chifundo, ndiye kuti tidzazindikira mosavuta kupweteka kumene tachititsa mwa mawu kapena mchitidwe wopanda nzeru ndipo tidzasonkhezeredwa kupepesa.
‘Valani Kudzichepetsa’
Ngakhale akulu okhulupirika achikristu nthaŵi zina angakhale ndi mkangano waukulu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 15:37-39.) Izi ndizo nthaŵi pamene kupepesa kumakhala kopindulitsa kwambiri. Koma kodi nchiyani chimene chidzathandiza mkulu kapena Mkristu wina aliyense amene amaona kupepesa kukhala kovuta?
Kudzichepetsa ndiko mfungulo. Mtumwi Petro anapereka uphungu kuti: “Muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane.” (1 Petro 5:5) Ngakhale kuti ndi zoona kuti m’mikangano yambiri anthu onse aŵiri amakhala ndi mlandu, Mkristu wodzichepetsa amazindikira zolakwa zake ndipo amakhala wofunitsitsa kuzivomereza.—Miyambo 6:1-5.
Wolandira kupepesako ayenera kukulandira modzichepetsa. Mwafanizo, tiyeni tinene kuti amuna aŵiri amene ayenera kulankhuzana aima pansonga za mapiri aŵiri osiyana. Kukambitsirana modutsa chigwa chimene chikuwasiyanitsa nkosatheka. Komabe, pamene mmodzi wa iwo atsikira ku chigwa ndipo winayo atsatira chitsanzo chake, akhoza kukambitsirana mosavuta. Mofananamo, ngati Akristu aŵiri akufuna kuthetsa kusamvana kwawo, aliyense akumane ndi mnzake m’chigwa, titero kunena kwake, ndi kupepesa moyenerera.—1 Petro 5:6.
Kupepesa Nkofunika Kwambiri Muukwati
Ukwati wa anthu aŵiri opanda ungwiro nthaŵi zonse umakhala ndi nthaŵi pamene kupepesa kumafunika. Ndipo ngati onse aŵiri mwamuna ndi mkazi wake amachitirana chifundo, adzasonkhezeredwa kupepesa ngati alankhula kapena kuchita kanthu kena mosalingalira mnzake. Miyambo 12:18 imati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” ‘Kupyozedwa mwansontho’ sikungasinthidwe koma kungachiritsidwe mwa kupepesa koona mtima. Komabe, zimenezi zimafuna kuzindikira ndi kuyesayesa nthaŵi zonse.
Ponena za ukwati wake, Susana akuti: “Ineyo ndi Jackb takhala mu ukwati kwa zaka 24, koma tikuphunzirabe zinthu zatsopano ponena za yense wa ife. Mwachisoni, nthaŵi ina kumbuyoku, tinapatukana ndi kukhala kwayekhakwayekha kwa milungu ingapo. Komabe, tinamvetsera uphungu wa m’Malemba wa akulu ndipo tinayanjananso. Tsopano tikuzindikira kuti popeza tili ndi maumunthu osiyana kwambiri, padzakhala mikangano. Pamene zimenezi zichitika, mwamsanga timapepesa ndi kuyesetsadi kumvetsa lingaliro la wina. Ndili wachimwemwe kunena kuti ukwati wathu wawongokera kwambiri.” Jack akuwonjezera kuti: “Taphunziranso kuzindikira nthaŵi pamene timakhumudwa. Panthaŵi zimenezi timachitirana mosamala koposa.—Miyambo 16:23.
Kodi muyenera kupepesa ngati mukulingalira kuti wolakwa si ndinu? Pamene mwakhumudwa kwambiri, nkovuta kuona pamene pali vuto. Koma chinthu chofunika ndicho mtendere muukwati. Talingalirani za Abigayeli, mkazi wachiisrayeli amene mwamuna wake anachitira nkhanza Davide. Ngakhale kuti sakanapatsidwa mlandu wa kupusa kwa mwamuna wake, iye anapepesa. “Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu,” anachonderera motero. Davide anayankha mwa kuchita naye mokoma mtima, akumavomereza modzichepetsa kuti pakadapanda iye, akanakhetsa mwazi wosalakwa.—1 Samueli 25:24-28, 32-35.
Mofananamo, mkazi wina wachikristu wotchedwa June, amene wakhala mu ukwati kwa zaka 45, akulingalira kuti ukwati wachipambano umafuna kuti munthu azikhala wokonzekera kuyambirira kupepesa. Iye akuti: “Ndimadziuza kuti ukwati wathu uli wofunika kwambiri kuposa malingaliro anga pandekha. Chotero pamene ndipepesa, ndimaona kuti ndikuthandizira ukwati.” Mwamuna wina wachikulire wotchedwa Jim akuti: “Ndimapepesa kwa mkazi wanga ngakhale pa zinthu zazing’ono. Kuyambira pamene anakhala ndi opaleshoni yaikulu, amapsinjika mtima msanga. Choncho nthaŵi zonse ndimamufungatira ndi kunena kuti, ‘Pepa, Wokondedwa. Sindinafune kukukhumudwitsa.’ Monga chomera chimene chathiriridwa, amakhalanso wokondwa nthaŵi yomweyo.”
Ngati takhumudwitsa munthu amene timakonda koposa, kupepesa nthaŵi yomweyo kumagwiradi ntchito. Milagros akuvomereza moona mtima, akumati: “Ndili ndi vuto la kusadzidalira, ndipo liwu lopyoza lochokera kwa mwamuna wanga limandikhwethemula. Koma pamene apepesa, ndimamva bwino nthaŵi yomweyo.” Moyenereradi, Malemba amatiuza kuti: “Mawu okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.”—Miyambo 16:24.
Luso la Kupepesa Likhale Chizoloŵezi Chanu
Ngati tili ndi chizoloŵezi cha kupepesa pamene kuli koyenera, tidzapeza kuti anthu adzamvetsera. Ndipo mwinamwake ngakhale iwowo adzapepesa. Pamene tiganiza kuti takhumudwitsa wina wake, bwanji osapanga kupepesa kukhala mwambo m’malo motaya nthaŵi yaitali tikumapeŵa kuvomereza kulakwa kulikonse? Dziko lingaganize kuti kupepesa kuli chizindikiro cha kufooka, koma kumaperekadi umboni wa uchikulire wachikristu. Komabe, sitingafune kukhala monga aja amene amavomereza kulakwa kwakutikwakuti koma nkupeputsa mlandu wawo. Mwachitsanzo, kodi timanena mosaona mtima kuti tili achisoni? Ngati tafika mochedwa ndipo tapepesa kwambiri, kodi timatsimikiza mtima kuwongolera nthaŵi ya kufika kwathu?
Chotero, kodi tifunikiradi kupepesa? Inde, tifunikira kutero. Tili ndi mangawa a ife eni ndi a ena a kuchita motero. Kupepesa kungathandize kuthetsa kupweteka kumene kupanda ungwiro kumachititsa, ndipo kungachiritse maunansi osokonezeka. Kupepesa kulikonse kumene timachita kuli phunziro la kudzichepetsa ndipo kumatiphunzitsa kusamala kwambiri za malingaliro a ena. Chotero, okhulupirira anzathu, anzathu a muukwati, ndi ena adzationa monga awo oyenerera chikondi ndi chidaliro chawo. Tidzakhala ndi mtendere wa maganizo, ndipo Yehova Mulungu adzatidalitsa.
[Mawu a M’munsi]
a Si maina awo enieni.
b Si maina awo enieni.
[Zithunzi patsamba 23]
Kupepesa koona mtima kumasonkhezera chikondi chachikristu