NKHANI YOPHUNZIRA 41
Zimene Tikuphunzira M’makalata Awiri a Petulo
“Nthawi zonse ndizikukumbutsani zinthu zimenezi.”—2 PET. 1:12.
NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Petulo atatsala pang’ono kufa, kodi Yehova anamugwiritsa ntchito bwanji?
MTUMWI Petulo anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri. Pa nthawiyi, iye anayenda ndi Yesu, analalikira kwa anthu a mitundu ina komanso anatumikira m’bungwe lolamulira. Komabe atatsala pang’ono kufa, Yehova anamupatsa ntchito ina yoti agwire. Cha m’ma 62 mpaka 64 C.E., anauziridwa kulemba makalata awiri a m’Baibulo, omwe ndi buku la 1 Petulo ndi 2 Petulo. Iye ankakhulupirira kuti makalatawa adzathandiza Akhristu pambuyo pa imfa yake.—2 Pet. 1:12-15.
2. N’chifukwa chiyani makalata omwe Petulo analemba ali a pa nthawi yake?
2 Petulo analemba makalata ake ouziridwawa pa nthawi imene Akhristu anzake ankavutika ndi “mayesero osiyanasiyana.” (1 Pet. 1:6) Anthu oipa ankayambitsa ziphunzitso zabodza komanso makhalidwe oipa mumpingo. (2 Pet. 2:1, 2, 14) Akhristu omwe ankakhala ku Yerusalemu anali atatsala pang’ono kuona “mapeto a zinthu zonse.” Asilikali a Aroma anali atatsala pang’ono kuwononga mzindawo komanso kachisi wake. (1 Pet. 4:7) Mosakayikira, makalata a Petulo anathandiza Akhristuwo kudziwa zimene angachite kuti azipirira mayesero omwe ankakumana nawo komanso kukonzekera zimene akanakumana nazo m’tsogolo.b
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira makalata ouziridwa a Petulo?
3 Ngakhale kuti Petulo ankalembera Akhristu a mu nthawi yake, Yehova anachititsa kuti makalatawo akhale mbali ya Baibulo. Choncho ifenso makalata amenewa angatithandize. (Aroma 15:4) Mofanana ndi mmene zinalili pa nthawiyo, ifenso tikukhala m’dziko limene limalimbikitsa makhalidwe oipa ndipo izi zingachititse kuti kukhale kovuta kutumikira Yehova. Kuwonjezera apo, posachedwapa tikumana ndi chisautso chachikulu kwambiri kuposa kuwonongedwa kwa Yerusalemu. M’makalata awiri a Petulo timapezamo mfundo zofunika kwambiri. Mfundo zimenezi zingatithandize kuti tiziyembekezera tsiku la Yehova, tisamaope anthu komanso tizikondana kwambiri. Mfundozi zingathandizenso akulu kuti azisamalira bwino nkhosa.
PITIRIZANI KUYEMBEKEZERA
4. Mogwirizana ndi 2 Petulo 3:3, 4, kodi n’chiyani chingafooketse chikhulupiriro chathu?
4 Tikukhala pakati pa anthu omwe sakhulupirira maulosi a m’Baibulo. Otsutsa angamatinyoze chifukwa choti takhala tikuyembekezera mapeto kwa zaka zambiri. Anthu ena amanena kuti mapeto sadzafika. (Werengani 2 Petulo 3:3, 4.) Ngati titamva mwininyumba, mnzathu wakuntchito kapena wachibale akunena zimenezi, chikhulupiriro chathu chikhoza kufooka. Ndiyeno Petulo anafotokoza zimene zingatithandize pa nkhaniyi.
5. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyembekezera moleza mtima mapeto a dziko loipali? (2 Petulo 3:8, 9)
5 Ena angamaone ngati Yehova akuchedwa kuwononga dziko loipali. Mawu a Petulo angatithandize kuti tikhale ndi maganizo oyenera ndipo amatikumbutsa kuti Yehova amaona nthawi mosiyana kwambiri ndi mmene anthufe timaionera. (Werengani 2 Petulo 3:8, 9.) Kwa Yehova, zaka 1, 000 zili ngati tsiku limodzi. Iye ndi woleza mtima ndipo sakufuna kuti wina aliyense adzawonongedwe. Komabe tsiku lake likadzafika, adzawononga dziko loipali. Tilitu ndi mwayi wogwiritsa ntchito nthawi yotsalayi kuchitira umboni kwa anthu a mitundu yonse.
6. Kodi tingatani kuti ‘tizikumbukira nthawi zonse’ tsiku la Yehova? (2 Petulo 3:11, 12)
6 Petulo anatilimbikitsa kuti ‘tizikumbukira nthawi zonse’ tsiku la Yehova. (Werengani 2 Petulo 3:11, 12.) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Ngati n’zotheka, tsiku lililonse tiziganizira madalitso omwe tidzapeze m’dziko latsopano. Muziyerekezera mukupuma kampweya kabwino, mukudya zakudya zopatsa thanzi, mukulandira okondedwa anu omwe aukitsidwa komanso mukuphunzitsa anthu akale mmene maulosi a m’Baibulo anakwaniritsidwira. Kuganizira zimenezi kungakuthandizeni kuti muziyembekezera tsiku la Yehova komanso musamakayikire zoti tikukhala m’nthawi ya mapeto. ‘Kudziwiratu’ zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo, kungatithandizenso kuti ‘tisasocheretsedwe’ ndi aphunzitsi abodza.—2 Pet. 3:17.
TISAMAOPE ANTHU
7. Kodi kuopa anthu kungatisokoneze bwanji?
7 Tikamakumbukira kuti tsiku la Yehova lili pafupi, timafunitsitsa kuuza ena uthenga wabwino. Komabe nthawi zina timachita mantha kuti tilalikire. Chifukwa chiyani? Mwina tingamaope zimene anthu angaganize kapena kuchita. Zimenezi ndi zomwe zinachitikiranso Petulo. Pa usiku womwe Yesu ankaimbidwa mlandu, Petulo sankafuna kuti anthu ena adziwe kuti anali wophunzira wake ndipo mobwerezabwereza anakana kuti sankamudziwa. (Mat. 26:69-75) Koma pambuyo pake mtumwi yemweyu ndi amene analemba motsimikiza kuti: “Musaope zimene iwo amaopa, ndipo musade nazo nkhawa.” (1 Pet. 3:14) Mawu akewa akutilimbikitsa kuti ifenso tingathe kusiya kuopa anthu.
8. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamaope anthu? (1 Petulo 3:15)
8 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisamaope anthu? Petulo anati: “Vomerezani m’mitima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera.” (Werengani 1 Petulo 3:15.) Zimenezi zikuphatikizapo kuganizira udindo komanso mphamvu zimene Ambuye ndi Mfumu yathu Khristu Yesu ali nazo. Ngati mutapeza mwayi woti muuze winawake uthenga wabwino koma mukuchita mantha, muzikumbukira Mfumu yathu. Muziyerekezera mukuona Yesu akulamulira kumwamba, atazunguliridwa ndi angelo ambirimbiri. Kumbukirani kuti iye wapatsidwa “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi” komanso kuti adzakhala “ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:18-20) Petulo anatilimbikitsa kuti tizikhala “okonzeka nthawi zonse” kuuza ena zimene timakhulupirira. Kodi mukufuna kuti muzilalikira kuntchito, kusukulu kapena kwina kulikonse? Muziganiziriratu za nthawi yomwe mungachite zimenezi komanso kukonzekera zimene munganene. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima komanso kuti musaope anthu.—Mac. 4:29.
“KHALANI OKONDANA KWAMBIRI”
9. Kodi pa nthawi ina, Petulo analephera bwanji kusonyeza chikondi? (Onaninso chithunzi.)
9 Petulo anaphunzira zimene angachite kuti azikonda ena. Iye analipo pamene Yesu ananena kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana.” (Yoh. 13:34) Ngakhale zinali choncho, pa nthawi ina iye analephera kuchita zimenezi chifukwa choopa anthu ndipo anasiya kudya ndi abale ndi alongo ake a mitundu ina. Mtumwi Paulo ananena kuti zimene anachitazi zinali “zachiphamaso” kapena kuti zachinyengo. (Agal. 2:11-14) Petulo anavomereza malangizowo ndipo anaphunzirapo kanthu. M’makalata ake onse awiri, iye anatsindika kuti sitiyenera kumangomva mumtima kuti timakonda abale athu koma tiyenera kumawasonyezanso chikondicho.
10. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti ‘tizikonda abale mopanda chinyengo’? Fotokozani. (1 Petulo 1:22)
10 Petulo ananena kuti tiyenera kumakonda abale ndi alongo athu “mopanda chinyengo.” (Werengani 1 Petulo 1:22.) Tingakhale ndi chikondi chimenechi ngati ‘timamvera choonadi.’ Choonadi chimenechi chikuphatikizapo mfundo yoti “Mulungu alibe tsankho.” (Mac. 10:34, 35) Sitingamvere lamulo la Yesu lakuti tizikondana ngati timakonda ena mumpingo n’kumalephera kukonda ena. N’zoona kuti tingamagwirizane kwambiri ndi ena kuposa ena, ngati mmenenso Yesu ankachitira. (Yoh. 13:23; 20:2) Koma Petulo akutikumbutsa kuti tiyenera kuyesetsa kuti ‘tizikonda abale’ onse ngati anthu a m’banja lathu.—1 Pet. 2:17.
11. Kodi ‘kukondana kwambiri kuchokera mumtima’ kumatanthauza chiyani?
11 Petulo anatilimbikitsa kuti ‘tizikondana kwambiri kuchokera mumtima.’ Apa mawu akuti ‘kukondana kwambiri’ akutanthauza kukonda winawake ngakhale pamene zili zovuta kutero. Mwachitsanzo, bwanji ngati m’bale watikhumudwitsa m’njira inayake? Mwachibadwa timafuna kumubwezera osati kumusonyeza chikondi. Komatu Petulo anaphunzira kwa Yesu kuti kubwezera sikusangalatsa Mulungu. (Yoh. 18:10, 11) Iye analemba kuti: “Osabwezera choipa pa choipa kapena chipongwe pa chipongwe, koma m’malomwake muzidalitsa.” (1 Pet. 3:9) Muzilola kuti kukonda kwambiri ena, kuzikulimbikitsani kuti muzikomera mtima komanso kuganizira amene akukhumudwitsani.
12. (a) Kodi kukondana kwambiri kungatilimbikitsenso kuchita chiyani? (b) Mogwirizana ndi vidiyo yakuti Tiziteteza Mgwirizano Wathu Wamtengo Wapatali, kodi inuyo mudzayesetsa kuchita chiyani?
12 M’kalata yake yoyamba, Petulo anagwiritsanso ntchito mawu akuti “khalani okondana kwambiri.” Chikondi chimenechi chimakwirira osati machimo ochepa chabe koma “machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) Mwina Petulo ankakumbukira zimene Yesu anamuphunzitsa zaka zingapo m’mbuyomo pa nkhani yokhululuka. Pa nthawiyo, iye ayenera ankakhulupirira kuti ngati atakhululukira m’bale wake “mpaka nthawi 7,” angasonyeze kuti ndi wokoma mtima. Koma Yesu anaphunzitsa Petulo ndiponso ifeyo kuti tiyenera kukhululuka “mpaka nthawi 77,” kutanthauza kuti popanda malire. (Mat. 1 8:21, 22) Ngati nthawi ina zinakuvutani kutsatira malangizowa, musataye mtima. Atumiki onse a Yehova poti si angwiro, nthawi zina zimawavuta kukhululuka. Chofunika kwambiri panopa, ndi kuchita zonse zomwe mungathe kuti mukhululukire m’bale wanu ndi kukhalanso naye pamtendere.c
AKULU, MUZIWETA NKHOSA
13. Kodi n’chiyani chingachititse kuti kukhale kovuta kuti akulu azipeza nthawi yolimbikitsa abale ndi alongo awo?
13 Mosakayikira, Petulo ankakumbukira zimene Yesu anamuuza atangoukitsidwa kumene, kuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:16) Ngati ndinu mkulu, mukudziwa kuti malangizowa akukhudzanso inuyo. Komabe, nthawi zina zingakhale zovuta kuti mkulu apeze nthawi yokwaniritsira udindo wofunikawu. Choyamba akulu amafunika kuonetsetsa kuti akupezera anthu a m’banja lawo zinthu zofunika, kuwathandiza kuti azimva kuti amakondedwa komanso kuwathandiza kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Iwo amatsogoleranso pa ntchito yolalikira, kukonzekera komanso kukamba nkhani pamisonkhano yampingo, yadera ndiponso yachigawo. Enanso amatumikira m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala kapena m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga. Kunena zoona, akulu amakhala otanganidwa kwambiri.
14. Kodi n’chiyani chingalimbikitse akulu kuti azisamalira nkhosa? (1 Petulo 5:1-4)
14 Petulo analimbikitsa akulu anzake kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu.” (Werengani 1 Petulo 5:1-4.) Ngati ndinu mkulu, timadziwa kuti mumakonda abale ndi alongo anu ndipo mumafuna kuwasamalira. Komabe, nthawi zina mungamaone kuti mwatanganidwa kapena mwatopa kwambiri moti simungathe kukwaniritsa udindowu. Zikatere, kodi mungatani? Muzimuuza Yehova nkhawa zanu zonse. Petulo analemba kuti: “Ngati wina akutumikira, atumikire modalira mphamvu imene Mulungu amapereka.” (1 Pet. 4:11) Abale ndi alongo anu angakumane ndi mavuto omwe sangatheretu panopa. Koma muzikumbukira kuti “m’busa wamkulu,” yemwe ndi Yesu Khristu, angawathandize kuposa wina aliyense. Iye angawathandize panopa komanso m’dziko latsopano. Mulungu amangofuna kuti akulu azikonda abale awo, kuwasamalira komanso kukhala “zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”
15. Kodi mkulu wina amatani kuti azilimbikitsa nkhosa? (Onaninso chithunzi.)
15 William, yemwe wakhala mkulu kwa nthawi yaitali, amadziwa kufunika kosamalira nkhosa. Mliri wa COVID-19 utangoyamba, iye ndi akulu anzake anakonza zoti mlungu uliwonse aziimbira foni munthu aliyense wa m’kagulu kawo. Anafotokoza chifukwa chake kuti: “Abale ambiri ankakhala okhaokha pakhomo ndipo akanatha kusokonezeka maganizo mosavuta.” M’bale kapena mlongo akakumana ndi vuto linalake, William ankamvetsera mwatcheru kuti aone zimene akufunikira komanso zomwe zikumudetsa nkhawa. Kenako ankafufuza malangizo omwe angamulimbikitse kuchokera m’mabuku komanso mavidiyo opezeka pa webusaiti yathu. Iye anati: “Kulimbikitsa abale ndi alongo athu n’kofunika kwambiri, makamaka panopa kuposa kale. Mofanana ndi mmene timachitira khama pothandiza anthu kuphunzira za Yehova, tiyeneranso kuchita khama posamalira ndi kuthandiza nkhosa za Yehova kuti zipitirizebe kukhala m’choonadi.”
MUZILOLA KUTI YEHOVA AMALIZITSE KUKUPHUNZITSANI
16. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji zimene taphunzira m’makalata a Petulo?
16 Tangokambirana mfundo zochepa chabe kuchokera m’makalata awiri ouziridwa a Petulo. N’kutheka kuti mwaona mbali ina imene inuyo mukufunika kukonza. Mwachitsanzo, kodi mukufuna kuti nthawi zambiri muziganizira madalitso omwe mudzapeze m’dziko latsopano? Kodi muli ndi cholinga choti muzilalikira kuntchito, kusukulu kapena kugwiritsa ntchito njira zina zolalikirira? Kodi mukuona kuti pali zimene mungachite kuti muzikonda kwambiri abale ndi alongo anu? Akulu, kodi mwatsimikiza kuti muzisamalira nkhosa za Yehova mofunitsitsa komanso ndi mtima wonse? Kudzifufuza moona mtima kungakuthandizeni kuti mudziwe mbali zina zomwe mukufunika kukonza, komabe simuyenera kutaya mtima. “Ambuye ndi wokoma mtima” ndipo adzakuthandizani. (1 Pet. 2:3) Petulo anatitsimikizira kuti: “Mulungu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.”—1 Pet. 5:10.
17. Kodi chingachitike n’chiyani ngati titapitiriza kukhala okhulupirika n’kumalola kuphunzitsidwa ndi Yehova?
17 Pa nthawi ina, Petulo ankadziona kuti sanali woyenera kukhala pafupi ndi Mwana wa Mulungu. (Luka 5:8) Koma mothandizidwa ndi Yehova komanso Yesu, iye anapitirizabe kutsatira Khristu mokhulupirika. Choncho Yehova analola kuti Petulo ‘alowe mwaulemerero mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.’ (2 Pet. 1:11) Umenewutu unali mwayi wamtengo wapatali. Ngati inunso mutapitirizabe kukhala okhulupirika ngati Petulo, n’kumalola kuphunzitsidwa ndi Yehova, mudzalandira moyo wosatha. “Chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti miyoyo yanu ipulumuke.”—1 Pet. 1:9.
NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima
a Munkhaniyi, tiona mmene kuphunzira zomwe zili m’makalata a Petulo kungatithandizire kupirira mayesero. Akulu nawonso aona mmene angakwaniritsire udindo wawo wosamalira nkhosa.
b Mosakayikira, Akhristu okhala ku Palesitina analandira makalata awiri a Petulo, Aroma asanaukire Yerusalemu koyamba mu 66 C.E.