Kupeza Mfungulo ya Chikondi cha pa Abale
“Wonjezerani . . . pakudzipereka kwanu kwaumulungu chikondi cha pa abale.”—2 PETRO 1:5-7, NW.
1. Kodi chimodzi cha zifukwa zazikulu zimene misonkhano ya anthu a Yehova ilili nthaŵi zosangalatsa motero nchiyani?
PANTHAŴI ina dokotala amene sanali mmodzi wa Mboni za Yehova anafika pachochitika cha kumaliza maphunziro a mwana wake wamkazi a Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watch Tower, kumene anachita kosi yaumishonale. Anachita chidwi kwambiri ndi khamu lachimwemwelo kotero kuti ananena kuti payenera kukhala matenda ochepa kwambiri pakati pa anthu ameneŵa. Kodi nchiyani chimene chinachititsa khamulo kukhala lachimwemwe kwambiri? Ndiponso, kodi nchiyani chimene chimachititsa misonkhano yonse ya anthu a Yehova, m’mipingo, pamisonkhano yadera, ndi pamisonkhano yachigawo, kukhala nthaŵi zosangalatsa? Kodi sichikondi cha pa abale chimene amasonyeza kwa wina ndi mnzake? Mosakayikira, chikondi cha pa abale chili chimodzi cha zifukwa zimene zachititsa ena kunena kuti palibe gulu lililonse lachipembedzo limene limapeza chisangalalo, chimwemwe, ndi chikhutiro m’chipembedzo mofanana ndi Mboni za Yehova.
2, 3. Kodi ndimawu aŵiri ati Achigiriki amene amafotokoza mmene tiyenera kulingalirana, ndipo kodi amasiyana motani?
2 Tiyenera kuyembekezera kuona chikondi cha pa abale chotero polingalira mawu a mtumwi Petro pa 1 Petro 1:22: “Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera chowonadi [ndi chikondi cha pa abale, NW] chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima.” Imodzi ya mbali zazikulu za liwu Lachigiriki lomasuliridwa panopo kuti “chikondi cha pa abale” ndiyo phi·liʹa (chikondi). Tanthauzo lake nlofanana kwambiri ndi tanthauzo la a·gaʹpe, liwu limene kaŵirikaŵiri limamasuliridwa kukhala “chikondi.” (1 Yohane 4:8) Ngakhale kuti mawu akuti chikondi cha pa abale ndi chikondi amagwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri mosinthanitsidwa, iwo ali ndi mbali zosiyana. Sitiyenera kuwaona kukhala chinthu chimodzi, monga momwe amachitira otembenuza Mabaibulo ambiri. (M’nkhani ino ndi yotsatirayo, tidzachita ndi lililonse la mawu ameneŵa.)
3 Ponena za kusiyana pakati pa mawu Achigiriki aŵiriwa, katswiri wina ananena kuti phi·liʹa “motsimikiza ndiliwu laubwenzi wapamtima ndi kuyanjana kwathithithi ndi chikondi.” Komabe, a·gaʹpe kwakukulukulu amakhudza maganizo. Chotero pamene timauzidwa kukonda (a·gaʹpe) adani athu, tilibe chikondi chapamtima kwa iwo. Chifukwa ninji? Chifukwa “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Mawu osonyezanso kuti pali kusiyana ali a mtumwi Petro akuti: “Wonjezerani . . . pachikondi cha pa abale chikondi.”—2 Petro 1:5-7, NW; yerekezerani ndi Yohane 21:15-17.a
Zitsanzo za Chikondi cha pa Abale Chapadera Kwambiri
4. Kodi nchifukwa ninji Yesu ndi Yohane anali ndi chikondi chapadera kwa wina ndi mnzake?
4 Mawu a Mulungu amatipatsa zitsanzo zingapo zabwino za chikondi cha pa abale chapadera kwambiri. Chikondi chapadera chimenechi sichimachititsidwa ndi lingaliro longobuka mwadzidzidzi koma nchozikidwa pa kuyamikira mikhalidwe yapadera. Mosakayikira chitsanzo chodziŵika bwino koposa ndicho chikondi chimene Yesu Kristu anali nacho kwa mtumwi Yohane. Mosakayikira, Yesu anali ndi chikondi cha pa abale kwa atumwi ake onse okhulupirika, ndipo anali ndi chifukwa chabwino chochitira zimenezo. (Luka 22:28) Imodzi ya njira zimene anachisonyezera inali mwakusambitsa mapazi awo, motero akumawapatsa phunziro la kudzichepetsa. (Yohane 13:3-16) Koma Yesu anali ndi chikondi chapadera kwa Yohane, chimene Yohane akutchula mobwerezabwereza. (Yohane 13:23; 19:26; 20:2) Monga momwedi Yesu analiri ndi chifukwa chosonyezera chikondi kwa ophunzira ake ndi atumwi ake, mosakayikira Yohane anapereka kwa Yesu chifukwa chomkondera iye mwapadera chifukwa cha chiyamikiro chake chakuya kaamba ka Yesu. Tikhoza kuona zimenezi m’zolembedwa za Yohane, mu Uthenga wake Wabwino ndi makalata ake ouziridwa omwe. Iye amatchula chikondi nthaŵi zochuluka chotani nanga m’zolembedwa zimenezo! Chiyamikiro chakuya cha Yohane kaamba ka mikhalidwe yauzimu ya Yesu chimaoneka m’zimene analemba m’buku la Yohane m’machaputala 1 ndi 13 mpaka 17, limodzinso ndi kutchula kwake mobwerezabwereza kukhalapo kwa Yesu asanakhale munthu.—Yohane 1:1-3; 3:13; 6:38, 42, 58; 17:5; 18:37.
5. Kodi nchiyani chinganenedwe ponena za chikondi chapadera chimene Paulo ndi Timoteo anali nacho kwa wina ndi mnzake?
5 Mofananamo, sitingafune kunyalanyaza chikondi cha pa abale chapadera kwambiri chimene mtumwi Paulo ndi bwenzi lake Lachikristu Timoteo anali nacho kwa wina ndi mnzake, chimene kwenikweni, chinali chozikidwa pakuyamikira mikhalidwe ya wina ndi mnzake. Zolembedwa za Paulo zili ndi ndemanga zabwino zonena za Timoteo, zonga zakuti: “Ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima wowona. . . . Muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine uthenga wabwino.” (Afilipi 2:20-22) Paulo amatchula Timoteo mwachindunji kwa nthaŵi zambiri m’makalata ake opita kwa Timoteo ovumbula chikondi chake chachikulu kwa iye. Mwachitsanzo, taonani lemba la 1 Timoteo 6:20 lomwe limati: “Timoteo iwe, dikira chokusungitsa.” (Onaninso 1 Timoteo 4:12-16; 5:23; 2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.) Kuyerekezera makalata a Paulo kwa Timoteo ndi kalata yake kwa Tito kumagogomezera kwambiri chikondi chapadera cha Paulo kwa mnyamatayu. Timoteo ayenera kukhala analingalira mofananamo zaubwenzi wawowo, monga momwe kungaonedwere m’mawu a Paulo pa 2 Timoteo 1:3, 4 akuti: “Ndikumbukira iwe kosalekeza m’mapemphero anga, pokhumba . . . kukuona iwe, ndi kukumbukira misozi yako, kuti ndidzazidwe nacho chimwemwe.”
6, 7. Kodi nchikondi chotani chimene Davide ndi Jonatani anali nacho kwa wina ndi mnzake, ndipo nchifukwa ninji?
6 Malemba Achihebri amaperekanso zitsanzo zabwino, monga chija cha Davide ndi Jonatani. Timaŵerenga kuti Davide atapha Goliati, “mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.” (1 Samueli 18:1) Kuyamikira kwake chitsanzo cha Davide cha changu kaamba ka dzina la Yehova ndi kulimba mtima kwake pokakumana ndi Goliati chimphonacho mosakayikira kunachititsa Jonatani kukhala ndi chikondi chapadera kwa Davide.
7 Jonatani anali ndi chikondi chachikulu kwa Davide moti anaika moyo wake pachiswe potetezera Davide kwa Mfumu Sauli. Palibe nthaŵi imene Jonatani anaipidwapo pamene Davide anasankhidwa ndi Yehova kukhala mfumu yotsatira ya Israyeli. (1 Samueli 23:17) Davide nayenso anali ndi chikondi chakuya chofananacho kwa Jonatani, chimene chikuonekera m’zimene ananena polira maliro a imfa ya Jonatani: “Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Jonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, . . . chinaposa chikondi cha anthu aakazi.” Ndithudi, unansi wawo unazikidwa pakuyamikirana kozama.—2 Samueli 1:26.
8. Kodi ndiakazi aŵiri ati amene anasonyeza chikondi chapadera kwa wina ndi mnzake, ndipo nchifukwa ninji?
8 Tilinso ndi chitsanzo chabwino m’Malemba Achihebri cha chikondi chapadera kwambiri pakati pa akazi aŵiri, Naomi ndi mpongozi wake wamasiye Rute. Kumbukirani mawu a Rute kwa Naomi akuti: “Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Kodi sitinganene kuti Naomi, mwa khalidwe lake ndi kulankhula kwake za Yehova, anathandizira kuchititsa Rute kuchitapo kanthu moyamikira chotero?—Yerekezerani ndi Luka 6:40.
Chitsanzo cha Mtumwi Paulo
9. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Paulo anapereka chitsanzo chabwino cha chikondi cha pa abale?
9 Monga momwe taonera, mtumwi Paulo anali ndi chikondi cha pa abale chapadera kwa Timoteo. Koma anaperekanso chitsanzo chabwino koposa cha kusonyeza chikondi chachikulu cha pa abale kwa abale ake onse. Iye anauza akulu a ku Efeso kuti “zaka zitatu [sanaleke] usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.” Kodi chimenecho chinali chikondi chachikulu cha pa abale? Mosakayikira konse! Ndipo iwonso anamva mofananamo kulinga kwa Paulo. Pakumva kuti sakamuonanso, “analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona.” (Machitidwe 20:31, 37) Kodi chinali chikondi cha pa abale chozikidwa pa kuyamikira? Inde! Chikondi chake cha pa abale chikuonekanso m’mawu ake pa 2 Akorinto 6:11-13: “M’kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa. Simupsinjika mwa ife, koma mupsinjika mumtima mwanu. Ndipo kukhale chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso.”
10. Kodi ndikupereŵera kotani kwa chikondi cha pa abale kumene kunachititsa Paulo kusimba za ziyeso zake pa 2 Akorinto chaputala 11?
10 Mwachionekere, Akorinto ambiri anali opereŵera pa chikondi cha pa abale choyamikira kwa mtumwi Paulo. Chotero, ena mwa iwo anadandaula kuti: “Akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mawu ake ngachabe.” (2 Akorinto 10:10) Nchifukwa chake Paulo anatchula “atumwi [awo] oposatu” ndipo anasonkhezeredwa kusimba ziyeso zimene anapirira, monga kwalembedwa pa 2 Akorinto 11:5, 22-33.
11. Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wonena za chikondi cha Paulo kwa Akristu a ku Tesalonika?
11 Chikondi chachikulu cha Paulo kwa awo amene anawatumikira chimaonekera kwambiri m’mawu ake pa 1 Atesalonika 2:8 (NW): “Pokhala nacho chikondi chapamtima kwa inu, ife tinakondwera kwambiri kugaŵira kwa inu, osati mbiri yabwino yokha ya Mulungu, komanso miyoyo yathu yomwe, chifukwa munakhala okondedwa kwa ife.” Kunena zowona, anali ndi chikondi chachikulu kwa abale atsopano ameneŵa kwakuti pamene analephera kupirira kuyembekezera kumva za ubwino wawo—ali wofunitsitsa kudziŵa mmene iwo anali kupiririra chizunzo—anatumiza Timoteo, amene anapereka lipoti labwino limene linatsitsimula Paulo kwambiri. (1 Atesalonika 3:1, 2, 6, 7) Ndithudi, Insight on the Scriptures imanena molondola pamene imati: “Unansi wolimba wa chikondi cha pa abale unalipo pakati pa Paulo ndi awo amene anatumikira.”
Chiyamikiro—Mfungulo ya Chikondi cha pa Abale
12. Kodi pali zifukwa zotani zosonyezera chikondi chathu chakuya kwa abale athu?
12 Mosakayikira, mfungulo ya chikondi cha pa abale ndiyo chiyamikiro. Kodi atumiki onse odzipatulira a Yehova sali ndi mikhalidwe imene timayamikira, imene imasonkhezera chikondi chathu, kutichititsa kuwakonda iwo? Tonsefe tikufunafuna choyamba Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake. Tonsefe tikumenya nkhondo zolimba molimbana ndi adani athu atatu amodzimodzi: Satana ndi ziŵanda zake, dziko loipa lolamuliridwa ndi Satana, ndi zikhoterero zadyera za choloŵa cha thupi lochimwa. Kodi nthaŵi zonse sitiyenera kuganiza kuti abale athu akuyesayesa koposa malinga ndi mikhalidweyo? Aliyense padziko lapansi ali kaya kumbali ya Yehova kapena kumbali ya Satana. Abale ndi alongo athu odzipatulira ali kumbali ya Yehova, inde, kumbali yathu, ndipo chotero ayenerera chikondi chathu cha pa abale.
13. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ndi chikondi chakuya kwa akulu?
13 Bwanji za kuyamikira akulu athu? Kodi sitiyenera kuwakonda kwambiri polingalira za njira imene amagwirira ntchito zolimba kaamba ka ubwino wa mpingo? Mofanana ndi aliyense wa ife, afunikira kudzipezera iwo eni ndi mabanja awo zofunika za moyo. Alinso ndi mathayo monga aliyense wa ife akuchita phunziro laumwini, kupezeka pamisonkhano ya mpingo, ndi kukhala ndi phande muutumiki wakumunda. Ndiponso, ali ndi thayo la kukonzekera mbali za programu ya misonkhano, kukamba nkhani zapoyera, ndi kusamalira mavuto amene amabuka mumpingo, amene nthaŵi zina amaphatikizapo maola ochuluka a kuzenga milandu. Ndithudi, tiyenera ‘kuchitira ulemu otereŵa.’—Afilipi 2:29.
Kusonyeza Chikondi cha pa Abale
14. Kodi ndimalemba ati amene amatilamula kusonyeza chikondi cha pa abale?
14 Kuti tikondweretse Yehova, tiyenera kusonyeza lingaliro lamphamvu la chikondi cha pa abale kwa okhulupirira anzathu, monga momwedi anachitira Yesu Kristu ndi Paulo. Timaŵerenga kuti: “[M’chikondi cha pa abale] mukondane ndi chikondi chenicheni.” (Aroma 12:10, Kingdom Interlinear) “Kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake.” (1 Atesalonika 4:9) “Chikondi cha pa abale chikhalebe.” (Ahebri 13:1) Ndithudi Atate wathu wakumwamba amakondwera pamene tisonyeza chikondi cha pa abale kwa ana ake apadziko lapansi!
15. Kodi zina za njira zosonyezera chikondi cha pa abale nziti?
15 M’nthaŵi za atumwi Akristu anali ndi chizoloŵezi cha kupatsana moni mwa “kupsompsona kopatulika” kapena “chipsompsono cha chikondi.” (Aroma 16:16; 1 Petro 5:14) Chinalidi chisonyezero cha chikondi cha pa abale chimenecho! Lerolino, m’mbali zochuluka za dziko lapansi, chisonyezero choyenera kwambiri ndicho kumwetulira kwaubwenzi ndithu ndi kugwirana chanza kwamphamvu. M’maiko a ku Latin America, monga ngati Mexico, kuli mtundu wa kupatsa moni wa kukupatira, chisonyezerodi cha chikondi. Chikondi chakuya chimenechi cha abale ameneŵa chingakhale chimodzi cha zifukwa za kuwonjezeka kwakukulu kochitika m’maiko awo.
16. Kodi ndimipata yotani imene tili nayo yosonyezera chikondi cha pa abale pa Nyumba zathu Zaufumu?
16 Pamene tiloŵa m’Nyumba Yaufumu, kodi timayesayesa zolimba kusonyeza chikondi cha pa abale? Chidzatichititsa kukhala ndi mawu olimbikitsa onena, makamaka kwa awo ooneka kukhala opsinjika. Timauzidwa “kulankhula motonthoza kwa miyoyo yopsinjika.” (1 Atesalonika 5:14, NW) Imeneyi ilidi njira imodzi imene tingasonyezere mphamvu ya chikondi cha pa abale. Njira ina yabwino ndiyo kupereka chiyamikiro kaamba ka nkhani yapoyera yabwino, mbali ya programu yochitidwa bwino lomwe, kuyesayesa kwabwino kochitidwa ndi wophunzira wokamba nkhani m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki, ndi zina zotero.
17. Kodi ndimotani mmene mkulu wina anachititsira mpingo kumkonda?
17 Bwanji za kuitanira anthu osiyanasiyana kunyumba zathu kaamba ka chakudya kapena tiyi pambuyo pa msonkhano ngati sikunade kwambiri? Kodi sitiyenera kulola uphungu wa Yesu pa Luka 14:12-14 kutilamulira? Panthaŵi ina yemwe anali mmishonale anaikidwa kukhala woyang’anira wotsogoza mumpingo kumene onse anali a mafuko osiyana. Iye anazindikira kusoŵeka kwa chikondi cha pa abale, chotero analinganiza mankhwala othetsera vutolo. Motani? Pa Sande iliyonse, anaitanira banja losiyana ku chakudya. Podzafika kumapeto kwa chaka, onse anali kusonyeza chikondi chakuya cha pa abale kwa iye.
18. Kodi ndimotani mmene tingasonyezere chikondi cha pa abale kwa abale ndi alongo athu odwala?
18 Pamene mbale kapena mlongo wadwala, ali panyumba kapena kuchipatala, chikondi cha pa abale chidzatichititsa kumdziŵitsa munthuyo kuti timasamala. Kapena bwanji za awo okhala m’nyumba zosamalira okalamba? Bwanji osapita kukawachezera, kuimba lamya, kapena kutumiza kadi yofotokoza malingaliro achikondi?
19, 20. Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti chikondi chathu cha pa abale chafutukulidwa?
19 Posonyeza chikondi cha pa abale mwanjira yotero, tikhoza kudzifunsa kuti, ‘Kodi chikondi changa cha pa abale nchatsankho? Kodi zinthu zonga maonekedwe a khungu, maphunziro, kapena chuma chakuthupi ndizo zimandisonkhezera kusonyeza chikondi cha pa abale? Kodi ndifunikira kufutukuka m’chikondi changa cha pa abale, monga momwe mtumwi Paulo anafulumizira Akristu ku Korinto?’ Chikondi cha pa abale chidzatichititsa kukhala ndi lingaliro loyenera la abale athu, kuwayamikira pazinthu zawo zabwino. Chikondi cha pa abale chidzatithandizanso kukondwera ndi kupita patsogolo kwa mbale wathu mmalo mokusirira.
20 Chikondi cha pa abale chiyeneranso kutichititsa kukhala atcheru kuthandiza abale athu muutumiki. Ziyenera kukhala monga momwe imodzi ya nyimbo zathu (Nambala 92 [51]) imanenera:
“Thandizani ofoka onse,
Kuti anene molimbika.
Musaiŵale atsopano,
Athandizeni kuchotsa mantha.”
21. Kodi nzotulukapo zotani zimene tingayembekezere pamene tisonyeza chikondi cha pa abale?
21 Chotero tisaiŵaletu kuti posonyeza chikondi cha pa abale, lamulo la mkhalidwe limene Yesu ananena mu Ulaliki wake wa pa Phiri limagwira ntchito: “Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m’manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nawo inu.” (Luka 6:38) Timapindula pamene tisonyeza chikondi cha pa abale, tikumasonyeza ulemu kwa awo amene ali atumiki a Yehova monga mmene ife tilili. Achimwemwedi ali awo amene amakondwera ndi kusonyeza chikondi cha pa abale!
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yotsatira yakuti: “Chikondi (Agape)—Zimene Sichili ndi Zimene Chili.”
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimawu Achigiriki ati amene amafotokoza chikondi chathu, ndipo kodi ngosiyana motani?
◻ Kodi mfungulo ya chikondi cha pa abale nchiyani?
◻ Kodi tili ndi zitsanzo zotani za m’Malemba za chikondi cha pa abale chapadera?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ndi chikondi chakuya kwa abale athu ndi akulu?
[Chithunzi patsamba 15]
Mtumwi Petro anafulumiza abale ake kuwonjezera chikondi cha pa abale pachikhulupiriro chawo ndi pamikhalidwe ina Yachikristu