-
Chipiriro—Nchofunika kwa AkristuNsanja ya Olonda—1993 | September 15
-
-
Chipiriro—Nchofunika kwa Akristu
“Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chipiriro.”—2 PETRO 1:5, 6, NW.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tonsefe tiyenera kupirira kufikira mapeto?
WOYANG’ANIRA woyendayenda wina ndi mkazi wake anali kuchezera Mkristu mnzawo wa m’zaka za m’ma 90. Mkristuyu anali atathera zaka makumi ambiri muutumiki wanthaŵi yonse. Pamene anali kucheza, mbale wokalambayo anasimba za mathayo ena amene anali nawo m’zaka zapita. “Koma,” iye anadandaula pamene misozi inayamba kugwa pamaso pake, “tsopano sindili wokhoza kuchita zambiri.” Woyang’anira woyendayendayo anatsegula Baibulo lake ndi kuŵerenga pa Mateyu 24:13, pamene pali mawu a Yesu Kristu akuti: “Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” Ndiyeno woyang’anira woyendayendayo anayang’ana mbale wokondedwayu nati: “Thayo lomalizira lomwe tonsefe tili nalo, mosasamala kanthu za kuchuluka kapena kuchepa kwa zimene tingachite, ndilo kupirira kufikira mapeto.”
2 Inde, monga Akristu, tonsefe tiyenera kupirira kufikira mapeto a dongosolo lino la zinthu kapena kufikira mapeto a miyoyo yathu. Palibe njira ina yolandirira chivomerezo cha Yehova cha chipulumutso. Tili m’makani a moyo, ndipo tiyenera ‘kuthamanga mwachipiriro’ kufikira mapeto. (Ahebri 12:1) Mtumwi Petro anagogomezera kufunika kwa mkhalidwe umenewu pamene anafulumiza Akristu anzake kuti: “Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chipiriro.” (2 Petro 1:5, 6, NW) Koma kodi kwenikweni chipiriro nchiyani?
Chipiriro—Tanthauzo Lake
3, 4. Kodi kupirira kumatanthauzanji?
3 Kodi kupirira kumatanthauzanji? Verebu Lachigiriki la liwu lakuti “pirira” (hy·po·meʹno) kwenikweni limatanthauza “kukhalabe pansi pa chinthu.” Limaonekera nthaŵi 17 m’Baibulo. Malinga nkunena kwa olemba dikishonale W. Bauer, F. W. Gingrich, ndi F. Danker, limatanthauza “kukhalabe pomwepo mmalo mwa kuthaŵa . . . , kuima nji, kuumirira.” Nauni Lachigiriki la liwu lakuti “chipiriro” (hy·po·mo·neʹ) limaonekera nthaŵi 30. Ponena za liwuli, A New Testament Wordbook, lolembedwa ndi William Barclay, limati: “Ilo ndilo mkhalidwe umene ungapirire zinthu, osati chifukwa cha kulolera molakwa, koma umatero chifukwa cha chiyembekezo chaphamphu . . . Ndiwo mkhalidwe umene umalimbitsa munthu kuyang’anizana ndi mavuto. Ndiwo mkhalidwe waukoma umene ungasinthe chiyeso chovuta kwambiri kukhala chaulemerero chifukwa chakuti m’kupwetekako umayang’ana pamphotho.”
4 Pamenepa, chipiriro chimatikhozetsa kukhala olimba nji ndi kusataya chiyembekezo poyang’anizana ndi zopinga kapena mavuto. (Aroma 5:3-5) Chimaona chonulirapo chimene chili mtsogolo pambuyo pa zopweteka—mphotho, kapena mphatso ya moyo wamuyaya, kaya kumwamba kapena padziko lapansi.—Yakobo 1:12.
Chipiriro—Nchifukwa Ninji Chikufunika?
5. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu onse ‘afunikira chipiriro’? (b) Kodi mayesero athu angagaŵidwe m’magulu aŵiri ati?
5 Monga Akristu, tonsefe “tifunikira chipiriro.” (Ahebri 10:36, NW) Chifukwa ninji? Kwakukulukulu chifukwa chakuti ‘timakumana ndi mayesero a mitundumitundu.’ Lemba Lachigiriki pano pa Yakobo 1:2 limapereka lingaliro la chokumana nacho chosayembekezeredwa kapena chosakondweretsa, monga ngati pamene munthu ayang’anizana ndi wachifwamba. (Yerekezerani ndi Luka 10:30.) Timakumana ndi mayesero amene angagaŵidwe m’magulu aŵiri: awo amene ali ofala kwa anthu chifukwa cha choloŵa cha uchimo, ndi aja amene amabuka chifukwa cha kudzipereka kwathu kwaumulungu. (1 Akorinto 10:13; 2 Timoteo 3:12) Kodi ndiati amene ali ena a mayesero ameneŵa?
6. Kodi ndimotani mmene Mboni ina inapiririra pamene inayang’anizana ndi matenda opweteka?
6 Matenda aakulu. Mofanana ndi Timoteo, Akristu ena ayenera kupirira ‘kudwaladwala.’ (1 Timoteo 5:23, NW) Makamaka pamene tiyang’anizana ndi nthenda yosachiritsika, kapena yopweteka kwambiri mpamene tifunikira kupirira, kuima nji, mwachithandizo cha Mulungu ndi kusataya chiyembekezo chathu Chachikristu. Lingalirani za chitsanzo cha Mboni ina ya zaka za kuchiyambiyambi kwa m’ma 50 imene inamenya nkhondo kwanthaŵi yaitali yolimbana ndi chotupa chomakula mofulumira. Iyo inakhalabe yolimba potsimikiza kukana mwazi m’maopaleshoni aŵiri. (Machitidwe 15:28, 29) Koma chotupacho chinayambanso kutupa m’mimba ndipo chinapitiriza kukula pafupi ndi msana. Pamene chinatero, iyeyu anali kumva ululu waukulu umene panalibe mlingo wa mankhwala uliwonse umene ukanathetsa ululuwo. Komabe, iye anayembekezera mphotho ya moyo m’dziko latsopano kuposa ululu umene anali kumva. Anapitiriza kunena za chiyembekezo chake champhamvu kwa madokotala, anamwino, ndi odzamuona. Anapirira kufikira mapeto—mapeto a moyo wake. Matenda anu sangakhale owopseza moyo kapena opweteka mofanana ndi a mbale wathu wokondedwayo, koma angaperekebe chiyeso chachikulu chofuna chipiriro.
7. Kodi chipiriro chimaloŵetsamo zopweteka zotani kwa ena a abale ndi alongo athu auzimu?
7 Kuvutika mtima. Panthaŵi ndi nthaŵi, anthu ena a Yehova akumana ndi ‘kusweka kwa moyo’ kumene kumachitika chifukwa cha “zowawa za mtima.” (Miyambo 15:13) Kupsinjika maganizo kwakukulu nkofala ‘m’nthaŵi zino zowawitsa.’ (2 Timoteo 3:1) Science News ya December 5, 1992, inasimba kuti: “Kaŵirikaŵiri, milingo yaikulu ya kupsinjika maganizo kofoola yawonjezereka mumbadwo uliwonse wa anthu obadwa chiyambire 1915.” Zochititsa kupsinjika maganizo kumeneko nzosiyanasiyana, zikumayambira pazinthu zochititsa kusapeza bwino kwa thupi mpaka kuzochitika zosasangalatsa. Kwa Akristu ena, chipiriro chimaloŵetsamo kumenya nkhondo kwatsiku ndi tsiku kuti akhalebe olimba poyang’anizana ndi kuvutika mtima. Komabe, iwo samagonja. Amakhalabe okhulupirika kwa Yehova mosasamala kanthu za zisonizo.—Yerekezerani ndi Salmo 126:5, 6.
8. Kodi ndimayesero a zandalama otani amene tingakumane nawo?
8 Mayesero osiyanasiyana amene timakumana nawo angaphatikizepo mavuto aakulu a ndalama. Pamene mbale wina wa ku New Jersey, U.S.A. ntchito inamthera mwadzidzidzi, moyenerera iye anali ndi nkhaŵa ya chimene adzadyetsa banja lake ndi kuti asalandidwe nyumba yake. Komabe, sanacheukitsidwe pachiyembekezo cha Ufumu. Pamene anali kufunafuna ntchito ina, anagwiritsiranso ntchito mwaŵiwo kutumikira monga mpainiya wothandiza. Potsirizira pake, anapeza ntchito.—Mateyu 6:25-34.
9. (a) Kodi ndimotani mmene kutayikiridwa wokondedwa muimfa kungafunikiritse chipiriro? (b) Kodi ndimalemba ati amene amasonyeza kuti kulira chifukwa cha chisoni sikoipa?
9 Ngati mwatayikiridwa wokondwedwa wanu muimfa, mufunikira chipiriro chimene chidzakhalapobe pamene anthu amene anadza kudzakutonthozani abwerera kwawo. Mungakuonedi kukhala kovuta kwambiri kwa inu pofika m’nthaŵiyo chaka chilichonse imene wokondedwa wanuyo anamwalira. Kupirira kutayikiridwa koteroko sikumatanthauza kuti kugwetsa misozi yachisoni nkolakwa. Kulira chifukwa cha imfa ya munthu amene timakonda nkwachibadwa, ndipo kumeneku sikumasonyeza kusakhulupirira chiyembekezo cha chiukiriro. (Genesis 23:2; yerekezerani ndi Ahebri 11:19.) Yesu “analira” Lazaro atamwalira, ngakhale kuti Iye anali atauza Marita motsimikiza kuti: “Mlongo wako adzauka.” Ndipo Lazaro anaukadi!—Yohane 11:23, 32-35, 41-44.
10. Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova afunikira chipiriro mwapadera?
10 Kuwonjezera pakupirira mayesero amene ali ofala kwa anthu onse, anthu a Yehova afunikira chipiriro mwapadera. Yesu anachenjeza kuti: “Anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Iye anatinso: “Ngati anandilondalonda ine, adzakulondalondani inunso.” (Yohane 15:20) Kodi nchifukwa ninji pali udani wonsewu ndi mazunzo? Chifukwa chakuti mosasamala kanthu za kumene timakhala padziko lapansili monga atumiki a Mulungu, Satana akuyesayesa kuswa umphumphu wathu kwa Yehova. (1 Petro 5:8; yerekezerani ndi Chivumbulutso 12:17.) Ali ndi cholinga chimenechi, kaŵirikaŵiri Satana wasonkhezera chizunzo chachikulu, akumaika chipiriro chathu pachiyeso chachikulu.
11, 12. (a) Kodi Mboni za Yehova ndi ana awo zinayang’anizana ndi chiyeso chotani cha chipiriro m’ma 1930 ndi kuchiyambiyambi kwa ma 1940? (b) Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova sizimachitira sawatcha chizindikiro cha dziko?
11 Mwachitsanzo, m’ma 1930 ndi kuchiyambiyambi kwa ma 1940, Mboni za Yehova ndi ana awo mu United States ndi Canada zinakhala chandamale cha chizunzo chifukwa chakuti sizinachitire sawatcha chizindikiro cha dziko chifukwa cha zifukwa za chikumbumtima. Mboni zimalemekeza zizindikiro za dziko limene zimakhala, koma zimagwirizana ndi lamulo loperekedwa m’Chilamulo cha Mulungu pa Eksodo 20:4, 5 lakuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako [ndine Mulungu wofuna kudzipereka kwaumulungu kwapadera, NW].” Pamene ana ena a sukulu a Mboni anathamangitsidwa chifukwa chakuti anafuna kupereka kulambira kwawo kokha kwa Yehova Mulungu, Mboni zinayambitsa Masukulu Aufumu kaamba ka maphunziro awo. Ophunzira ameneŵa anabwereranso kusukulu za boma pamene Bwalo Lalikulu Lamilandu la United States linavomereza mkhalidwe wawo wa chipembedzo, monga momwe maiko opanda tsankho amachitira lerolino. Komabe, kupirira molimba mtima kwa achichepere ameneŵa ndiko chitsanzo cholimbikitsa makamaka kwa Akristu achichepere lerolino amene amayang’anizana ndi zitonzo chifukwa chakuti amayesayesa kukhala mogwirizana ndi miyezo ya Baibulo.—1 Yohane 5:21.
12 Mayesero osiyanasiyana amene timayang’anizana nawo—ponse paŵiri, awo amene ali ofala kwa anthu onse ndi awo amene timayang’anizana nawo chifukwa cha chikhulupiriro chathu Chachikristu—amasonyeza chifukwa chake tifunikira chipiriro. Koma kodi tingapirire motani?
Kupirira Kufikira Mapeto—Motani?
13. Kodi ndimotani mmene Yehova amaperekera chipiriro?
13 Anthu a Mulungu ali ndi mwaŵi wotsimikizirika kuposa anthu amene samalambira Yehova. Kuti tithandizidwe, tikhoza kutembenukira kwa “Mulungu wa chipiriro.” (Aroma 15:5) Komabe, kodi ndimotani mmene Yehova amaperekera chipiriro? Njira imodzi imene amachitira zimenezi ili kupyolera mwa zitsanzo za chipiriro zolembedwa m’Mawu ake, Baibulo. (Aroma 15:4) Pamene tisinkhasinkha za zimenezi, sitimangolimbikitsidwa chabe kupirira, komanso timaphunzira zochuluka ponena za mmene munthu angapiririre. Talingalirani za zitsanzo ziŵiri zapadera—kupirira molimba mtima kwa Yobu ndi kupirira kwa Yesu Kristu kopanda tchimo.—Ahebri 12:1-3; Yakobo 5:11.
14, 15. (a) Kodi ndimayesero otani amene Yobu anapirira? (b) Kodi ndimotani mmene Yobu anakhozera kupirira mayesero amene anakumana nawo?
14 Kodi ndimikhalidwe yotani imene inaika chipiriro cha Yobu pachiyeso? Anasauka pamene anatayikiridwa chuma chake. (Yobu 1:14-17; yerekezerani ndi Yobu 1:3.) Yobu anavutika mtima ndi kutayikiridwako pamene ana ake onse khumi anaphedwa ndi chimphepo. (Yobu 1:18-21) Anadwala matenda aakulu, omvetsa ululu kwambiri. (Yobu 2:7, 8; 7:4, 5) Mkazi wake weniweniyo anamkakamiza kusiya kulambira Mulungu. (Yobu 2:9) Mabwenzi ake apafupi ananena zinthu zimene zinali zopweteka, zankhanza, ndi zonama. (Yerekezerani ndi Yobu 16:1-3 ndi Yobu 42:7.) Komabe, muzonsezi, Yobu anaima nji, akumasunga umphumphu. (Yobu 27:5) Zinthu zimene anapirira nzofanana ndi mayesero amene anthu a Yehova amakumana nawo lerolino.
15 Kodi ndimotani mmene Yobu analiri wokhoza kupirira mayesero amenewo? Chinthu chapadera chimene chinalimbikitsa Yobu chinali chiyembekezo. “Pakuti akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso, ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasoŵa,” iye anatero. (Yobu 14:7) Kodi Yobu anali ndi chiyembekezo chotani? Monga momwe tingaonere m’mavesi angapo pambuyo pake, iye anati: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? . . . Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:14, 15) Inde, Yobu anali kulingalira za zinthu zamtsogolo kuposa mavuto ake. Iye anadziŵa kuti mayesero ake sadzakhalako kosatha. Chifukwa chake iye anafunikira kupirira kufikira imfa. Chiyembekezo chake chachikulu chinali chakuti Yehova, amene mwachikondi amafuna kuukitsa akufa, akampatsanso moyo.—Machitidwe 24:15.
16. (a) Kodi nchiyani chimene timaphunzira ponena za chipiriro m’chitsanzo cha Yobu? (b) Kodi chiyembekezo cha Ufumu chiyenera kukhala chotsimikizirika motani kwa ife, ndipo chifukwa ninji?
16 Kodi timaphunziranji pachipiriro cha Yobu? Kuti tipirire kufikira mapeto, sitiyenera kutaya chiyembekezo chathu. Kumbukiraninso kuti, kutsimikizirika kwa chiyembekezo cha Ufumu kumatanthauza kuti mavuto alionse amene timakumana nawo ‘ngakanthaŵi.’ (2 Akorinto 4:16-18) Chiyembekezo chathu chamtengo wapatali nchozikidwa kwambiri palonjezo la Yehova lonena za nthaŵi imene ili pafupi mtsogolomu pamene ‘adzapukuta misozi yonse kuichotsa pamaso pathu; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.’ (Chivumbulutso 21:3, 4) Chiyembekezo chimenecho, chimene “sichichititsa manyazi,” chiyenera kutetezera maganizo athu. (Aroma 5:4, 5; 1 Atesalonika 5:8) Chiyenera kukhala chenicheni kwa ife—chenicheni kwakuti tikhoza kudziona ife eni m’dziko latsopano ndi maso achikhulupiriro—popanda kulimbananso ndi matenda ndi kupsinjika maganizo koma tsiku lililonse kudzuka tili ndi thanzi labwino ndi omasuka maganizo; popanda kuvutika mumtima ponena za chitsenderezo chachikulu cha ndalama koma kukhala ndi moyo motetezereka; popanda kulira akufa athu okondedwa koma kukhala nacho chisangalalo cha kuwaona akuukitsidwa. (Ahebri 11:1) Popanda chiyembekezo chotero tingakhale othedwa mphamvu ndi mayesero athu atsopano lino kwakuti tikhoza kugonja. Pokhala ndi chiyembekezo chathu, tili ndi chisonkhezero chachikulu chotani nanga choti tipitirizebe kumenya nkhondo, tipitirizebe kupirira kufikira mapeto!
17. (a) Kodi Yesu anapirira mayesero otani? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza ukulu wa zoŵaŵa zimene Yesu anapirira? (Onani mawu amtsinde.)
17 Baibulo limatilimbikitsa “kupenyerera” pa Yesu ndi ‘kulingalira iye.’ Kodi ndimayesero otani amene anapirira? Ena a iwo anadza chifukwa cha uchimo ndi kusalungama kwa ena. Yesu anapirira osati kokha ndi “ochimwa otsutsana naye” komanso mavuto amene anabuka pakati pa ophunzira ake, kuphatikizapo mkangano wawo wobwerezabwereza wonena za wamkulu pakati pawo. Ndiponso, iye analimbana ndi chiyeso chachikulu koposa cha kukhulupirika. “Anapirira [mtengo wozunzirapo, NW].” (Ahebri 12:1-3; Luka 9:46; 22:24) Nkovutadi kuyerekezera za kuvutika kwamaganizo ndi kwakuthupi koloŵetsedwamo paululu wa kukhomeredwa pamtengo wozunzirapo ndi kunyazitsidwa mwa kuphedwa monga munthu wamwano.a
18. Malinga nkunena kwa mtumwi Paulo, kodi nzinthu ziti ziŵiri zimene zinachilikiza Yesu?
18 Kodi nchiyani chimene chinakhozetsa Yesu kupirira kufikira mapeto? Mtumwi Paulo akutchula zinthu ziŵiri zimene zinachilikiza Yesu kuti: ‘mapemphero ndi mapembedzero’ ndiponso “chimwemwe choikidwacho pamaso pake.” Yesu, Mwana wangwiro wa Mulungu, sanachite manyazi kupempha chithandizo. Iye anapemphera “pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi.” (Ahebri 5:7; 12:2) Iye makamaka anaona kukhala kofunika kupempherera nyonga mobwerezabwereza ndi khama pamene mlandu wake wa m’bwalo lapamwambawo unali kuyandikira. (Luka 22:39-44) Poyankha mapemphero a Yesu, Yehova sanachotse chiyesocho, koma analimbikitsa Yesu kupirira. Yesu anapiriranso chifukwa chakuti anali kulingalira za mphotho yake ya mtsogolo koposa mtengo wozunzirapo—chisangalalo chimene akakhala nacho pochilikiza kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi kuwombola mtundu wa anthu kuimfa.—Mateyu 6:9; 20:28.
19, 20. Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha Yesu chimatithandizira kukhala ndi lingaliro labwino la zimene chipiriro chimaloŵetsamo?
19 M’chitsanzo cha Yesu chimenechi, timaphunzira zinthu zingapo zimene zimatithandiza kukhala ndi lingaliro labwino la zimene chipiriro chimaloŵetsamo. Njira ya chipiriro njovuta. Ngati tiona kupirira chiyeso china kukhala kovuta, chitonthozo chili m’kudziŵa kuti zofananazo zinachitikiranso Yesu. Kuti tipirire kufikira mapeto, tiyenera kupempherera nyonga mobwerezabwereza. Pamene tiyesedwa nthaŵi zina tingadzilingalire kukhala osayenerera kupemphera. Koma Yehova amafuna kuti timuuze zakukhosi kwathu ‘pakuti iye atisamalira.’ (1 Petro 5:7) Ndipo chifukwa cha zimene Yehova walonjeza m’Mawu ake, iye amatsimikiza kupereka “mphamvu yoposa yaumunthu” kwa awo amene amamfikira mwachikhulupiriro.—2 Akorinto 4:7-9, NW.
20 Nthaŵi zina tiyenera kupirira ndi misozi. Ululu wa pamtengo wozunzirapo sunali mwa iwo wokha chifukwa chosangalalira kwa Yesu. Mmalomwake, chisangalalo chake chinali pamphotho imene inali patsogolo pake. Kwa ife nkudzinyenga kuyembekezera kuti nthaŵi zonse tidzakhala achimwemwe ndi okondwa pamene tili pamayesero. (Yerekezerani ndi Ahebri 12:11.) Komabe mwakuyembekezera mphothoyo, ‘tingayese mayeserowo chimwemwe’ ngakhale pamene tikumana ndi mikhalidwe yoyesa kwambiri. (Yakobo 1:2-4; Machitidwe 5:41) Chinthu chofunika nchakuti tikhalebe olimba nji—ngakhale pamene mayeserowo angatiliritse. Ndi iko komwe, Yesu sananene kuti, ‘Iye amene agwetsa misozi yochepa adzapulumuka’ koma anati, “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.”—Mateyu 24:13.
21. (a) Kodi pa 2 Petro 1:5, 6 (NW), timalimbikitsidwa kuwonjezera chiyani pachipiriro chathu? (b) Kodi ndimafunso ati amene adzayankhidwa m’nkhani yathu yotsatira?
21 Motero chipiriro nchofunika kaamba ka chipulumutso. Komabe pa 2 Petro 1:5, 6 (NW), tikulimbikitsidwa kuwonjezera kudzipereka kwaumulungu pachipiriro chathu. Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani? Kodi kumagwirizana motani ndi chipiriro, ndipo kodi mungakupeze motani? Mafunso ameneŵa adzayankhidwa m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Kuvutika kwakukulu kumene Yesu anapirira mwinamwake kungaonedwe m’chenicheni chakuti munthu wangwiroyo anamwalira pambuyo pa maola oŵerengeka chabe pamtengo wozunzirapo, pamene kuli kwakuti ochita zoipa amene anapachikidwa pamodzi naye anafunikira kuthyoledwa miyendo yawo kufulumizitsa imfa yawo. (Yohane 19:31-33) Iwo sanamve kuvutika kwa maganizo ndi kwakuthupi kofanana ndi kumene Yesu anali nako mkati mwa zochitika za kuimbidwa mlandu usiku wonse asanapachikidwe, mwinamwake kufikira pamlingo wakuti sakanathanso kunyamula mtengo wake wozunzirapo.—Marko 15:15, 21.
-
-
Wonjezerani Pachipiriro Chanu Kudzipereka KwaumulunguNsanja ya Olonda—1993 | September 15
-
-
Wonjezerani Pachipiriro Chanu Kudzipereka Kwaumulungu
“Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chipiriro, pachipiriro chanu kudzipereka kwaumulungu.”—2 PETRO 1:5, 6, NW.
1, 2. (a) Kuyambira m’ma 1930, kodi nchiyani chimene chinachitikira Mboni za Yehova zokhala m’maiko olamuliridwa ndi Nazi, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi ndimotani mmene anthu a Yehova anachitira pansi pa nkhanza zimenezi?
INALI nthaŵi yamdima m’mbiri ya zaka za zana la 20. Kuyambira m’ma 1930, Mboni za Yehova zikwi zambiri m’maiko olamuliridwa ndi Nazi zinamangidwa mosayenera ndi kuponyedwa m’misasa yachibalo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti zinasunga uchete wawo ndi kukana kutamanda Hitler. Kodi zinachitiridwa motani? “Palibe kagulu kena ka andende . . . kamene kanachitiridwa nkhanza yomkitsa ndi asilikali a SS mofanana ndi Ophunzira Baibulo [Mboni za Yehova]. Inali nkhanza ya kuzunza mwakuthupi ndi maganizo kosatha, kuzunza kosafotokozeka.”—Karl Wittig, yemwe kale anali mkulu wa m’boma la Germany.
2 Kodi Mbonizo zinachita motani? M’buku lake lakuti The Nazi State and the New Religions: Five Case Studies in Non-Conformity, Dr. Christine E. King anati: “Ndi kwa Mboni zokha [mosiyana ndi magulu ena azipembedzo] kumene boma silinapezeko chipambano.” Inde, Mboni za Yehova monga gulu zinachilimika zolimba, ngakhale kuti kwa mazana ambiri a izo, zimenezi zinatanthauza kupirira kufikira imfa.
3. Kodi nchiyani chimene chakhozetsa Mboni za Yehova kupirira mayesero aakulu?
3 Kodi nchiyani chimene chakhozetsa Mboni za Yehova kupirira mayesero otero osati mu Nazi wa Germany yekha koma kuzungulira dziko lonse? Atate wawo wakumwamba wawathandiza kupirira chifukwa cha kudzipereka kwawo kwaumulungu. “Yehova adziŵa kupulumutsa odzipereka mwaumulungu poyesedwa iwo,” amafotokoza motero mtumwi Petro. (2 Petro 2:9, NW) Pachiyambiyambi m’kalata yomweyo, Petro anali atalangiza Akristu kuti: “Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chipiriro, pachipiriro chanu kudzipereka kwaumulungu.” (2 Petro 1:5, 6, NW) Chotero chipiriro nchogwirizanitsidwa kwambiri ndi kudzipereka kwaumulungu. Kwenikweni, kuti tipirire kufikira mapeto, tiyenera ‘kulondola kudzipereka kwaumulungu’ ndi kukusonyeza. (1 Timoteo 6:11) Koma kodi kwenikweni kudzipereka kwaumulungu nchiyani?
Chimene Chili Kudzipereka Kwaumulungu
4, 5. Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani?
4 Nauni Lachigiriki lotembenuzidwa “kudzipereka kwaumulungu” (eu·seʹbei·a) kwenikweni lingatembenuzidwe kukhala “kuchitira ulemu koyenera.”a (2 Petro 1:6, Kingdom Interlinear) Limapereka lingaliro la kukonda Mulungu ndi mtima wonse. Malinga nkunena kwa W. E. Vine ajekitiviyo eu·se·besʹ, kwenikweni kutanthauza “kuchita mantha moyenera,” amasonyeza “nyonga, yolamulidwa ndi mantha oyera kwa Mulungu, osonyezedwa ndi ntchito zodzipereka.”—2 Petro 2:9, Int.
5 Chifukwa chake mawu akuti “kudzipereka kwaumulungu” amanena za ulemu kapena kudzipereka kwa Yehova kumene kumatisonkhezera kuchita chimene chili chomkondweretsa. Zimenezi zimachitidwa ngakhale povutika ndi mayesero aakulu chifukwa chakuti timakonda Mulungu kochokera mumtima. Kumamatirana kokhulupirika ndi Yehova kumeneku, nkumene kumasonyezedwa ndi njira imene timakhalira ndi moyo wathu. Akristu owona akufulumizidwa kupemphera kotero kuti akhale “a moyo wodekha ndi auchete odzazidwa ndi kudzipereka kwaumulungu.” (1 Timoteo 2:1, 2, NW) Malinga nkunena kwa olemba dikishonale J. P. Louw ndi E. A. Nida, “m’zinenero zingapo [eu·seʹbei·a] wa pa 1 Tm 2.2 angatembenuzidwe moyenerera kukhala ‘kukhala ndi moyo monga momwe Mulungu akufunira’ kapena ‘kukhala ndi moyo monga momwe Mulungu watiuzira.’”
6. Kodi kugwirizana kwa chipiriro ndi kudzipereka kwaumulungu nkotani?
6 Tsopano tikhoza kuzindikira bwino kwambiri mgwirizano umene uli pakati pa chipiriro ndi kudzipereka kwaumulungu. Chifukwa chakuti timakhala ndi moyo monga momwe Mulungu afunira—ndi kudzipereka kwaumulungu—timakwiyitsa dziko, limene limadzetsa ziyeso za chikhulupiriro mosalekeza. (2 Timoteo 3:12) Koma palibe njira imene tikanasonkhezeredwa nayo kupirira ziyeso zotero ngati sitikanamamatirana ndi Atate wathu wakumwamba. Ndiponso, Yehova amachitapo kanthu pakusonyezedwa kwa kudzipereka kwamtima wonse kumeneko. Tayerekezerani mmene kumamkhudzira mtima kuyang’ana pansi pano ali kumwamba ndi kuona awo amene, chifukwa cha kudzipereka kwawo kwa iye, akuyesayesa kumkondweretsa mosasamala kanthu za mitundu yosiyanasiyana ya chitsutso. Mposadabwitsa kuti iye ali wofunitsitsa ‘kupulumutsa odzipereka mwaumulungu poyesedwa iwo’!
7. Kodi nchifukwa ninji kudzipereka kwaumulungu kuyenera kukulitsidwa?
7 Komabe, ife sitimabadwa ndi kudzipereka kwaumulungu, ndiponso sitimakupeza chabe chifukwa cha kukhala ndi makolo opembedza Mulungu. (Genesis 8:21) Mmalomwake, kuyenera kukulitsidwa. (1 Timoteo 4:7, 10) Tiyenera kuchitapo kanthu kuti tiwonjezere kudzipereka kwaumulungu pachipiriro ndi pachikhulupiriro chathu. Petro akuti zimenezi zimafunikira “changu chonse.” (2 Petro 1:5) Nangano, kodi ndimotani mmene tingapezere kudzipereka kwaumulungu?
Kodi Ndimotani Mmene Timapezera Kudzipereka Kwaumulungu?
8. Malinga nkunena kwa mtumwi Petro, kodi nchiyani chimene chili mfungulo yopezera kudzipereka kwaumulungu?
8 Mtumwi Petro anafotokoza za mfungulo yopezera kudzipereka kwaumulungu. Iye anati: “Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m’chidziŵitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu. Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi [kudzipereka kwaumulungu, NW], mwa chidziŵitso cha iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa iye yekha.” (2 Petro 1:2, 3) Chotero kuti tiwonjezere kudzipereka kwaumulungu pachikhulupiriro chathu ndi chipiriro, tiyenera kukula m’chidziŵitso cholongosoka, ndiko kuti, kukhala ndi chidziŵitso chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu chodzaza, kapena chokwanira.
9. Kodi ndimotani mmene tingafanizirire za mmene kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Kristu kumaloŵetseramo zoposa kungowadziŵa?
9 Kodi kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu ndi Kristu kumatanthauzanji? Mwachionekere, kumaloŵetsamo zoposa kuwadziŵa chabe. Mwachitsanzo: Inu mungakhale mukudziŵa munthu amene mumakhala naye moyandikana ndipo mungampatsedi moni mwakumtchula dzina. Koma kodi mungamkongoze ndalama zambirimbiri? Kutalitali, pokhapokha ngati munadziŵadi kuti munthuyo ngwotani. (Yerekezerani ndi Miyambo 11:15.) Mofananamo, kudziŵa Yehova ndi Yesu molongosoka, kapena mokwanira, kumatanthauza zoposa kungokhulupirira kuti iwowo aliko ndi kudziŵa maina awo. Kuti tikhale ofunitsitsa kupirira m’mayesero kaamba ka iwo kufikiradi paimfa, tiyenera kuwadziŵa bwino kwenikweni. (Yohane 17:3) Kodi zimenezi zimaphatikizapo chiyani?
10. Kodi kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Yehova ndi Yesu kumaphatikizapo zinthu ziŵiri ziti, ndipo chifukwa ninji?
10 Kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka, kapena chokwanira chonena za Yehova ndi Yesu kumaphatikizapo zinthu ziŵiri: (1) kuwadziŵa monga anthu—mikhalidwe yawo, malingaliro, ndi njira—ndipo (2) kutsanzira chitsanzo chawo. Kudzipereka kwaumulungu kumaphatikizapo kumamatirana ndi Yehova ndi mtima wonse ndipo kumeneku kumasonyezedwa ndi moyo wathu. Chifukwa chake, kuti tichipeze tiyenera kudziŵana ndi Yehova ndi kukhala ozoloŵerana ndi chifuniro chake ndi njira zimene zili zotheka kuchitidwa ndi munthu. Kuti tidziŵedi Yehova, mwa amene tinalengedwa m’chifanizo chake, tiyenera kugwiritsira ntchito chidziŵitso chotero ndi kuyesayesa kufanana naye. (Genesis 1:26-28; Akolose 3:10) Ndipo popeza kuti Yesu anatsanzira Yehova mwangwiro m’zimene ananena ndi kuchita, kudziŵa Yesu molongosoka ndiko chithandizo chamtengo wapatali m’kukulitsa kudzipereka kwaumulungu.—Ahebri 1:3.
11. (a) Kodi tingapeze motani chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Kristu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kusinkhasinkha pazimene timaŵerenga?
11 Komabe, kodi ndimotani mmene tingapezere chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu ndi Kristu? Mwakuphunzira mosamalitsa Baibulo ndi zofalitsidwa zina zofotokoza Baibulo.b Komabe, ngati phunziro lathu laumwini la Baibulo liti litichititse kupeza kudzipereka kwaumulungu, kuli kofunika kuti tipatule nthaŵi ya kusinkhasinkha, ndiko kuti, kupenda, kapena kuganizitsa, pazimene timaŵerenga. (Yerekezerani ndi Yoswa 1:8.) Kodi nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika? Kumbukirani kuti kudzipereka kwaumulungu ndiko kukonda Mulungu kochokera pansi pa mtima. M’Malemba, liwu lakuti kusinkhasinkha, mobwerezabwereza limagwirizanitsidwa ndi mtima wophiphiritsira—munthu wamkati. (Salmo 19:14; 49:3; Miyambo 15:28) Pamene tisinkhasinkha moyamikira zimene timaŵerenga, zinthuzo zimaloŵa m’munthu wathu wamkati, motero zikumasonkhezera mtima wathu, ndi kusonkhezera maganizo athu. Mpokhapo pamene phunzirolo lingalimbitse kumamatirana kwathu ndi Yehova ndi kutisonkhezera kukhala ndi moyo umene umakondweretsa Mulungu ngakhale poyang’anizana ndi mikhalidwe yovuta kapena mayesero ovuta.
Kusonyeza Kudzipereka Kwaumulungu Panyumba
12. (a) Malinga nkunena kwa Paulo, kodi ndimotani mmene Mkristu angachitire kudzipereka kwaumulungu panyumba? (b) Kodi nchifukwa ninji Akristu owona amasamalira makolo okalamba?
12 Choyamba kudzipereka kwaumulungu kuyenera kusonyezedwa panyumba. Mtumwi Paulo akuti: “Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.” (1 Timoteo 5:4) Kusamalira makolo okalamba kuli, monga momwe Paulo akunenera, chisonyezero cha kudzipereka kwaumulungu. Akristu owona amapereka chisamaliro chotero osati kokha chifukwa cha kuzindikira thayolo koma chifukwa cha kukonda makolo awo. Komabe, kuposa zimenezo, iwo amazindikira za kufunika kwa thayo limene Yehova amaika pakusamalira banja la munthu. Amadziŵa bwino lomwe kuti kukana kuthandiza makolo awo m’nthaŵi ya kusoŵa kukakhala kofanana ndi ‘kukana chikhulupiriro Chachikristu.’—1 Timoteo 5:8.
13. Kodi nchifukwa ninji kusonyeza kudzipereka kwaumulungu panyumba kungakhale kopereka vuto, koma kodi ndichikhutiro chotani chimene chimakhalapo chifukwa cha kusamalira makolo a munthuwe?
13 Zowonadi, nthaŵi zina nkovuta kuchita kudzipereka kwaumulungu panyumba. Ziŵalo za banja zingakhale zili zokhalirana patali. Ana achikulire angakhale ali ndi thayo la kusamalira mabanja awo ndipo angakhale akuvutikira kupeza ndalama. Mkhalidwe kapena ukulu wa chisamaliro chofunidwa ndi kholo ungathe kukhala cholemetsa mwakuthupi, mwamaganizo, ndi mwamalingaliro kwa anthu amene akupereka chisamalirocho. Komabe, pangakhale chikhutiro chenicheni m’kudziŵa kuti kusamalira makolo a munthuwe sikumachititsa kokha ‘kubwezeredwa’ komanso kumakondweretsa Uyo “amene kuchokera kwa iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina.”—Aefeso 3:14, 15.
14, 15. Simbani za chitsanzo cha chisamaliro choperekedwa mwaumulungu chochitidwa ndi ana kwa kholo.
14 Talingalirani za chitsanzo chogwira mtima kwambiridi. Ellis ndi abale ndi alongo ake asanu ali ndi thayo lovuta la kusamalira atate wawo panyumba. “Mu 1986 atate anadwala sitiroko, imene inawapangitsa kukhala opuŵala kotheratu,” akufotokoza motero Ellis. Ana asanu ndi mmodziwo amathandizana kusamalira atate wawo, kuyambira pakuwasambitsa kufikira pakutsimikizira kuti akutembenuzidwa nthaŵi ndi nthaŵi pakama kotero kuti asachite zilonda. “Timawaŵerengera mabuku, kulankhula nawo, kuwalizira nyimbo. Sitili otsimikiza ngati amadziŵa zimene zikuchitika kwa iwo, koma timawachitira zinthu monga ngati kuti akuzindikira zonse.”
15 Kodi nchifukwa ninji anawo amasamalira atate wawo monga momwe amachitiramo? Ellis akupitiriza kuti: “Amayi atamwalira mu 1964, Atate anatilera ali okha. Panthaŵiyo, tinali azaka zoyambira pa 5 kufika pa 14. Ndiwo amene anatithandiza panthaŵiyo; tsopano nafenso tiyenera kuwathandiza.” Mwachionekere, kupereka chisamaliro chotero nkovuta, ndipo nthaŵi zina anawo amatopa nazo. “Koma timazindikira kuti mkhalidwe wa atatewo ngwakanthaŵi,” akutero Ellis. “Tikuyembekezera nthaŵiyo pamene thanzi la atate lidzabwezeretsedwa pamkhalidwe wabwino ndipo tidzagwirizanitsidwanso ndi amayi.” (Yesaya 33:24; Yohane 5:28, 29) Ndithudi, chisamaliro choperekedwa ndi mtima wonse chimenecho kwa kholo chiyenera kukondweretsa mtima wa Uyo amene amalamulira ana kulemekeza makolo awo!c—Aefeso 6:1, 2.
Kudzipereka Kwaumulungu ndi Utumiki
16. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chifukwa chachikulu cha zimene timachita muutumiki?
16 Pamene tivomereza chiitano cha Yesu cha ‘kumtsatira mosalekeza,’ timaloŵa ntchito yaumulungu ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 16:24; 24:14; 28:19, 20) Mwachionekere, kukhala ndi phande muutumiki kuli thayo Lachikristu mu “masiku otsiriza” ano. (2 Timoteo 3:1) Komabe, cholinga chathu polalikira ndi kuphunzitsa chiyenera kukhala choposa kukhala ntchito kapena thayo chabe. Kukonda kwathu Yehova mwakuya kuyenera kukhala chifukwa chachikulu cha zimene timachita ndi kuchuluka kwake muutumiki. “Mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.” (Mateyu 12:34) Inde, pamene mitima yathu isefukira ndi kukonda Yehova, timasonkhezereka kuchitira umboni za iye kwa ena. Pamene kukonda kwathu Yehova kuli chisonkhezero chathu, utumiki wathu umakhala chisonyezero chenicheni cha kudzipereka kwathu kwaumulungu.
17. Kodi tingakulitse motani chisonkhezero choyenera cha utumiki?
17 Kodi ndimotani mmene tingakulitsire chisonkhezero chabwino cha utumiki? Sinkhasinkhani moyamikira pazifukwa zitatu zimene Yehova watipatsa za kumkondera. (1) Timakonda Yehova chifukwa cha zimene watichitira. Palibe chikondi choposa chimene anasonyeza popereka dipo. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) (2) Timakonda Yehova chifukwa cha zimene akutichitira tsopano lino. Tili ndi ufulu wa kulankhula ndi Yehova momasuka, amene amayankha mapemphero athu. (Salmo 65:2; Ahebri 4:14-16) Pamene tiika zinthu Zaufumu pamalo oyamba, timalandira zosoŵa zathu zochilikizira moyo. (Mateyu 6:25-33) Timalandira chakudya chauzimu choperekedwa mokhazikika chimene chimatithandiza kulimbana ndi mavuto amene timakumana nawo. (Mateyu 24:45) Ndipo tili ndi dalitso la kukhala mbali ya gulu lonse la abale la padziko lonse limene limatilekanitsa ndi dziko. (1 Petro 2:17) (3) Timakondanso Yehova chifukwa cha zimene adzatichitira. Chifukwa cha chikondi chake, ‘tagwira moyo weniweniwo’—moyo wosatha wamtsogolo. (1 Timoteo 6:12, 19) Pamene tilingalira za mmene Yehova anatikondera, ndithudi mitima yathu idzatisonkhezera kukhala ndi phande lokwanira m’kuuza ena za iye ndi zifuno zake zamtengo wapatali! Sipafunikira ena kutiuza zonse zimene tiyenera kuchita kapena kuchuluka kwa ntchito imene tiyenera kuchita muutumiki. Mitima yathu idzatisonkhezera kuchita zimene tingathe.
18, 19. Kodi ndichopinga chotani chimene mlongo wina anagonjetsa kuti akhale ndi phande muutumiki?
18 Ngakhale poyang’anizana ndi mikhalidwe yovuta, mtima wosonkhezeredwa ndi kudzipereka kwaumulungu udzasonkhezereka kunena. (Yerekezerani ndi Yeremiya 20:9.) Zimenezi zasonyezedwa m’nkhani ya Stella, mkazi Wachikristu wamanyazi kwambiri. Pamene anayamba kuphunzira Baibulo, analingalira kuti, ‘Sindidzatha kumka kunyumba ndi nyumba!’ Iye akufotokoza kuti: “Ndinkakhala chete nthaŵi zonse. Sindinkatha kufikira anthu ndi kuyamba kukambitsirana nawo.” Pamene anapitiriza kuphunzira, kukonda kwake Yehova kunakula, ndipo anakulitsa chikhumbo chachikulu chofuna kuuza ena ponena za iye. “Ndikukumbukira kuti ndinauza mphunzitsi wanga wa Baibulo kuti, ‘Ndimafuna kwambiri kulankhula, koma sindimatha kutero, ndipo zimenezo zimandivutitsa maganizo.’ Sindidzaiŵala zimene anandiuza: ‘Stella, khala woyamikira chifukwa chakuti umafuna kunena ndi ena.’”
19 Posapita nthaŵi, Stella anayamba kuchitira umboni kwa mnansi wake woyandikana naye. Ndiyeno anapanga sitepe limene linali lalikulu kwa iye—anakhala ndi phande muutumiki wa kunyumba ndi nyumba kwanthaŵi yoyamba. (Machitidwe 20:20, 21) Iye akukumbukira kuti: “Ndinalemba ulaliki wanga. Koma ndinkachita mantha kwambiri kwakuti ngakhale kuti ndinali nawo, sindinathe kuyang’ana pazolembedwa zanga!” Tsopano, zaka 35 pambuyo pake, Stella adakali wamanyazi kwambiri mwachibadwa. Komabe, iye amakonda utumiki wakumunda ndipo akupitiriza kukhalamo ndi phande lenileni.
20. Kodi ndichitsanzo chotani chimene chikusonyeza kuti chizunzo ngakhale kuikidwa m’ndende sizingaletse Mboni zodzipatulira za Yehova kunena ndi anthu?
20 Chizunzo kapena ngakhale kuikidwa m’ndende sizingaletse Mboni zodzipereka za Yehova kunena. Talingalirani za chitsanzo cha Ernst ndi Hildegard Seliger a ku Germany. Chifukwa cha chikhulupiriro chawo, iwo anathera zaka zoposa 40 kuphatikiza pamodzi za onse aŵiri, m’misasa ya chibalo ya Nazi ndi ndende za Akomyunizimu. Ngakhale pamene anali m’ndendemo, iwo anapitirizabe kuchitira umboni kwa andende ena. Hildegard akukumbukira kuti: “Akuluakulu andende anandiyesa munthu waupandu koposa, chifukwa chakuti, monga momwe mlonda wina wachikazi ananenera, ndinkanena za Baibulo tsiku lonse. Chotero ndinaikidwa m’ndende yapansi.” Potsirizira pake atamasulidwa, Mbale ndi Mlongo Seliger anadzipereka muntchito yanthaŵi yonse ya utumiki Wachikristu. Onsewo anatumikira mokhulupirika kufikira paimfa zawo, Mbale Seliger mu 1985 ndipo mkazi wake mu 1992.
21. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tiwonjezere kudzipereka kwaumulungu pachipiriro chathu?
21 Mwakuphunzira mosamalitsa Mawu a Mulungu ndi kupatula nthaŵi ya kusinkhasinkha pazimene timaphunzira, tidzawonjezera chidziŵitso chathu cholongosoka chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Zimenezi, nazonso, zidzachititsa kupeza kwathu mlingo wokwanira wa mkhalidwe wamtengo wapatali umenewo—kudzipereka kwaumulungu. Popanda kudzipereka kwaumulungu sitingathe kupirira mayesero osiyanasiyana amene amadza pa ife monga Akristu. Chotero tiyeni titsatire uphungu wa mtumwi Petro, tikumapitiriza ‘kuwonjezera pachikhulupiriro chathu chipiriro ndi pachipiriro chathu kudzipereka kwaumulungu.’—2 Petro 1:5, 6, NW.
-