Tigwiritse Chikhulupiriro Chathu Chamtengo Wapatali!
“Kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife.”—2 PETRO 1:1.
1. Kodi Yesu ananenanji kuchenjeza atumwi ake, nanga Petro anadzitamandira motani?
USIKU imfa ya Yesu isanachitike, iye anati atumwi ake onse adzamthaŵa. Mmodzi wa iwo, Petro, anadzitamandira nati: ‘Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthaŵi zonse.’ (Mateyu 26:33) Koma Yesu anadziŵa kuti sizinali zoona zimenezo. Ndiye chifukwa chake anauza Petro nthaŵi yomweyo kuti: “Ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.”—Luka 22:32.
2. Ngakhale kuti Petro anadzikhulupirira kwambiri, kodi anachita zotani zomwe zinavumbula kuti chikhulupiriro chake chinali chosalimba?
2 Petro, yemwe anadzikhulupirira kwambiri, anakana Yesu usiku womwewo. Katatu konse anati samdziŵa Kristu! (Mateyu 26:69-75) Pamene ‘anatembenuka,’ ayenera kuti anawakumbukira bwino kwambiri mawu a Mbuyake akuti, “ukhazikitse abale ako.” Moyo wake wonse wa Petro unakhudzidwa kwambiri ndi chenjezo limenelo, malinga ndi zomwe akusonyeza makalata ake aŵiri omwe analemba, opezeka m’Baibulo.
Chifukwa Chake Petro Analemba Makalata Ake
3. Kodi Petro analemberanji kalata yake yoyamba?
3 Zaka ngati 30 kuchokera pa imfa ya Yesu, Petro analemba kalata yake yoyamba, kwa abale ake ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya, madera omwe tsopano ali kumpoto ndi kumadzulo kwa Turkey. (1 Petro 1:1) Ayuda, omwe ena a iwo mwina anakhala Akristu pa Pentekoste wa 33 C.E., mosakayikira anali pakati pa omwe Petro anawalemberawo. (Machitidwe 2:1, 7-9) Ambiri anali Akunja omwe otsutsa anawayesa koopsa. (1 Petro 1:6, 7; 2:12, 19, 20; 3:13-17; 4:12-14) Choncho Petro analembera abale ameneŵa kuwalimbikitsa. Cholinga chake chinali kuwathandiza kulandira “chitsiriziro cha chikhulupiriro [chawo], ndicho chipulumutso cha Moyo [wawo].” Chotero, powachenjeza m’mawu ake otsazika, anawalimbikitsa kuti: “Mumkanize [Mdyerekezi] okhazikika m’chikhulupiriro.”—1 Petro 1:9; 5:8-10.
4. Kodi Petro analemberanji kalata yake yachiŵiri?
4 Pambuyo pake, Petro analemba kalata yachiŵiri kwa Akristu ameneŵa. (2 Petro 3:1) Chifukwa ninji? Chifukwa panali ngozi yaikulu koposa. Anthu opanda khalidwe amayesa kulimbikitsa khalidwe lawo lodetsa mwa okhulupirira ndipo amafuna kusokeretsa ena! (2 Petro 2:1-3) Ndiponso, Petro anachenjeza za onyoza. Anali atalemba m’kalata yake yoyamba kuti “chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi,” ndipo tsopano ena mwachionekere anali kuseka lingaliro limenelo. (1 Petro 4:7; 2 Petro 3:3, 4) Tiyeni tipende kalata yachiŵiri ya Petro ndi kuona mmene inalimbitsira abalewo kuchirimika m’chikhulupiriro. M’nkhani ino yoyamba, tidzapenda 2 Petro chaputala 1.
Cholinga cha Chaputala 1
5. Kodi Petro akuwakonzekeretsa motani oŵerenga kalata yake pofuna kukambirana nawo mavuto?
5 Petro sakuyamba nthaŵi yomweyo kusamalira mavuto aakulu. M’malo mwake, akukonza njira yokambirana mavuto ameneŵa mwa kukulitsa chiyamikiro cha oŵerenga kalata yake pa zimene analandira atakhala Akristu. Akuwakumbutsa za malonjezo a Mulungu odabwitsa ndi za kudalirika kwa maulosi a Baibulo. Akutero mwa kusimba za kusandulika, masomphenya omwe iye anaona ndi maso onena za Kristu m’mphamvu ya Ufumu.—Mateyu 17:1-8; 2 Petro 1:3, 4, 11, 16-21.
6, 7. (a) Kodi mawu oyamba a kalata ya Petro angatiphunzitsenji? (b) Ngati tipereka uphungu, kodi ndi kuvomereza chiyani kumene nthaŵi zina kungathandize?
6 Kodi tikhoza kutolapo phunziro lililonse pa mawu oyambawo a Petro? Kodi uphungu sumakhala wolandirika kwambiri ngati choyamba tipenda mbali za chiyembekezo chaulemerero cha Ufumu limodzi ndi omvetsera athu omwenso ali ndi chiyembekezo chimodzimodzi? Ndipo bwanji zosimba zimene zinakuchitikirani? Pambuyo pa imfa ya Yesu, Petro angakhale atasimba kaŵirikaŵiri zakuti anaona masomphenya a Kristu mu ulemerero wa Ufumu.—Mateyu 17:9.
7 Kumbukiraninso kuti nzotheka kwambiri kuti pamene Petro analemba kalata yake yachiŵiri, Uthenga Wabwino wa Mateyu ndi kalata ya mtumwi Paulo kwa Agalatiya zingakhale zitafala kwambiri. Chotero kuphophonya kwa Petro monga munthu ndiponso mbiri ya chikhulupiriro chake angakhale ataidziŵa kwambiri anzake. (Mateyu 16:21-23; Agalatiya 2:11-14) Komabe, zimenezo sizinamlande ufulu wake wa kulankhula. Inde, mwina zinachititsa kalata yake kukhala yokopa kwambiri kwa aja omwe anali kuzindikira zofooka zawo. Chotero, pothandiza amene ali ndi mavuto, kodi sikungathandize kwambiri kuvomera kuti ifenso timalakwa?—Aroma 3:23; Agalatiya 6:1.
Moni Wolimbikitsa
8. Kodi Petro angakhale atagwiritsira ntchito liwu la “chikhulupiriro” ndi tanthauzo lotani?
8 Tsopano talingalirani moni wa Petro. Iye mosataya nthaŵi akhudza nkhani ya chikhulupiriro, akumatcha oŵerenga kalata yake “iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife.” (2 Petro 1:1) Panopa mawuwo “chikhulupiriro” angakhale akutanthauza “malingaliro otsimikizika” ndipo akunena za zikhulupiriro kapena ziphunzitso zonse zachikristu, zimene nthaŵi zina zimatchedwa “choonadi” m’Malemba. (Agalatiya 5:7; 2 Petro 2:2; 2 Yohane 1) Liwu lakuti “chikhulupiriro” nthaŵi zambiri limagwiritsiridwa ntchito ndi tanthauzo limeneli m’malo mwa tanthauzo lofala la kukhulupirira kapena kudalira munthu kapena chinthu.—Machitidwe 6:7; 2 Akorinto 13:5; Agalatiya 6:10; Aefeso 4:5; Yuda 3.
9. Kodi nchifukwa ninji moni wa Petro ungakhale utawakondweretsa kwambiri Akunja?
9 Moni wa Petro ungakhale utawakondweretsa kwambiri oŵerenga Akunja. Ayuda sanali kuyenderana nawo Akunja, ndipo amawayesa onyozeka, ndiponso Ayuda amene anali atakhala Akristu anapitirizabe kukhala atsankhu kwa Akunja. (Luka 10:29-37; Yohane 4:9; Machitidwe 10:28) Komabe, Petro, wobadwa Myuda ndiponso mtumwi wa Yesu Kristu, anatero kuti oŵerenga kalata yake—Ayuda ndi Akunja—anali ndi chikhulupiriro chimodzimodzi ndipo anali ndi mtengo wolingana ndi wake.
10. Kodi ndi maphunziro otani omwe tingatengepo pa moni wa Petro?
10 Talingalirani za maphunziro abwino omwe timatengapo pa moni wa Petro lerolino. Mulungu alibe tsankhu; samakondera fuko lina kapena mtundu wina kuposa wina. (Machitidwe 10:34, 35; 11:1, 17; 15:3-9) Monga Yesu mwiniyo anaphunzitsira, Akristu onse ali abale, ndipo aliyense wa ife sayenera kudziyesa wopambana. Ndiponso, moni wa Petro ukugogomezera kuti tilidi abale dziko lonse, omwe ali ndi “mtengo wake womwewo” wa chikhulupiriro chomwe Petro ndi atumwi anzake anali nacho.—Mateyu 23:8; 1 Petro 5:9.
Chidziŵitso ndi Malonjezo a Mulungu
11. Atatha moni wake, kodi ndi zinthu ziti zofunika kwambiri zomwe Petro akugogomezera?
11 Atatha moni wake, Petro akulemba kuti: “Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe.” Kodi chisomo ndi mtendere zingachulukitsidwe motani kwa ife? “M’chidziŵitso [cholongosoka, NW] cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu,” akuyankha Petro. Kenako akuti: “Mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo.” Koma kodi timazilandira motani zinthu zofunika kwambiri zimenezi? “Mwa chidziŵitso [cholongosoka, NW] cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma.” Chotero kaŵiri Petro akugogomezera kuti chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Mwana wake nchofunika kwambiri.—2 Petro 1:2, 3; Yohane 17:3.
12. (a) Kodi nchifukwa ninji Petro akugogomezera kufunika kwake kwa chidziŵitso cholongosoka? (b) Kuti tilandire malonjezo a Mulungu, kodi choyamba tiyenera kukhala titachitanji?
12 “Aphunzitsi onama” omwe Petro akuchenjeza za iwo m’chaputala 2 amagwiritsira ntchito “mawu onyenga” pofuna kuchenjeretsa Akristu. Mwanjira imeneyi amayesa kuwakopa kubwerera ku makhalidwe oipa omwe anamasukako. Zimene zimachitika kwa aliyense amene anapulumuka mwa “chizindikiritso [“chidziŵitso cholongosoka,” NW] cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu” ndiyeno nkutsata chinyengocho pambuyo pake zimakhala zoopsa. (2 Petro 2:1-3, 20) Mwachionekere poyembekezera kuti adzafotokoza za vuto limeneli pambuyo pake, Petro akugogomezera pachiyambi penipeni pa kalata yake kufunika kwa chidziŵitso cholongosoka kuti munthu akhale ndi kaimidwe koyera kwa Mulungu. Petro akutero kuti Mulungu “adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nawo umulungu wake.” Komabe, kuti tikalandire malonjezo ameneŵa, omwe ali ofunika kwambiri pa chikhulupiriro chathu, akutero Petro, tiyenera choyamba ‘kupulumuka ku chivundi chili padziko lapansi m’chilakolako.’—2 Petro 1:4.
13. Kodi Akristu odzozedwa ndi “nkhosa zina” ali otsimikiza kugwiritsa chiyani?
13 Kodi malonjezo a Mulungu mumawaona motani? Mmene otsalira a Akristu odzozedwa amawaonera? Mu 1991, Frederick Franz, pulezidenti wa panthaŵiyo wa Watch Tower Bible and Tract Society, amene anali mu utumiki wanthaŵi zonse zaka zoposa 75, anafotokoza mwachidule maganizo a aja omwe akuyembekeza kukalamulira ndi Kristu: “Talimbikira mpaka ola lino, ndipo tidzalimbikirabe mpaka Mulungu atasonyezadi kuti ‘malonjezano ake a mtengo wake ndi aakulu ndithu’ ali oona.” Mbale Franz anasunga chidaliro chake m’lonjezo la Mulungu la chiukiriro cha kumwamba, ndipo anagwiritsa chikhulupiriro chake mpaka imfa yake ali ndi zaka 99. (1 Akorinto 15:42-44; Afilipi 3:13, 14; 2 Timoteo 2:10-12) Mofananamo, anthu mamiliyoni ambiri akugwiritsa chikhulupirirocho, kusumika maganizo awo pa lonjezo la Mulungu la dziko lapansi la paradaiso limene anthu adzakhalamo kosatha ndi chimwemwe. Kodi ndinu mmodzi wa iwo?—Luka 23:43; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4.
Kulabadira Malonjezo a Mulungu
14. Kodi nchifukwa ninji Petro akutchula ukoma monga mkhalidwe woyamba kuwonjeza pa chikhulupiriro?
14 Kodi timamyamikira Mulungu pa zimene walonjeza? Ngati timatero, Petro akutilimbikitsa kuti tiyenera kusonyeza zimenezo. “Ndipo mwa ichi chomwe” (chifukwa Mulungu watipatsa malonjezo a mtengo wapatali kwambiri), tiyenera kuchita khama. Sitiyenera kungokhutira ndi kukhala m’chikhulupiriro kapena kungodziŵa choonadi cha Baibulo. Zimenezo nzosakwanira! M’tsiku la Petro mwinamwake ena mumpingo analankhula kwambiri za chikhulupiriro koma nkumachita zoipa. Anafunika kukhala ndi khalidwe lokoma, chotero Petro akulimbikitsa kuti: ‘Muwonjezerepo ukoma pa chikhulupiriro chanu.’—2 Petro 1:5; Yakobo 2:14-17.
15. (a) Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso chikutsatira ukoma monga mkhalidwe wowonjezera pa chikhulupiriro? (b) Kodi ndi mikhalidwe ina iti imene idzatithandiza kugwiritsa chikhulupiriro?
15 Atatchula ukoma, Petro akutchulanso mikhalidwe ina isanu ndi umodzi imene iyenera kuwonjezedwa pa chikhulupiriro chathu. Uliwonse mwa mikhalidwe imeneyi ngwofunika kuti ‘tichirimike m’chikhulupiriro.’ (1 Akorinto 16:13) Chifukwa chakuti ampatuko anali ‘kupotoza Malembo’ ndi kulimbikitsa “ziphunzitso zonama,” Petro kenako akutchula kuti chidziŵitso nchofunika kwambiri, kuti: “Paukoma [muwonjezepo] chizindikiritso [“chidziŵitso,” NW].” Ndiye akupitiriza kuti: “Pachizindikiritso [onjezanipo] chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo; ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.”—2 Petro 1:5-7; 2:12, 13; 3:16.
16. Kodi chidzachitika nchiyani ngati mikhalidwe imene Petro akutchula iwonjezedwa pa chikhulupiriro, nanga chidzachitika nchiyani ngati siiwonjezedwapo?
16 Kodi chidzachitika nchiyani ngati zinthu zisanu ndi ziŵirizi ziwonjezedwa pa chikhulupiriro chathu? “Izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka,” akuyankha Petro, “zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso [“chidziŵitso cholongosoka,” NW] cha Ambuye wathu Yesu Kristu.” (2 Petro 1:8) Komanso, Petro akuti: “Iye wakusoŵa izi ali wakhungu, wa chimbuuzi, woiŵala matsukidwe ake potaya zoipa zake zakale.” (2 Petro 1:9) Onani kuti Petro wasintha, wasiya kugwiritsira ntchito mawu akuti “inu” ndi “wathu” nayamba kunena kuti “iye,” “ali,” ndi “ake.” Ngakhale kuti nzachisoni kuti ena ngakhungu, oiŵala, ndi odetsedwa, Petro panopa sakutanthauza kuti woŵerenga ali mmodzi wa iwo.—2 Petro 2:2.
Alimbitsa Abale Ake
17. Kodi nchiyani mwina chimene chinasonkhezera Petro kuwachonderera mwachifundo kuchita “izi”?
17 Mwinamwake pozindikira kuti atsopano makamaka anganyengeke msanga, Petro mwachifundo akuwalimbikitsa kuti: “Abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthaŵi zonse.” (2 Petro 1:10; 2:18) Akristu odzozedwa omwe amawonjezera zinthu zisanu ndi ziŵiri zimenezi pa chikhulupiriro chawo adzalandira mphotho yaikulu, pakuti Petro akuti: “Kudzawonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakuloŵa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu.” (2 Petro 1:11) A “nkhosa zina” adzalandira choloŵa chosatha m’chigawo cha padziko lapansi cha Ufumu wa Mulungu.—Yohane 10:16; Mateyu 25:33, 34.
18. Kodi nchifukwa ninji Petro akonda ‘kuwakumbutsa nthaŵi zonse’ abale ake?
18 Petro akufunitsitsadi kuti abale ake akalandire mphotho yaikulu imeneyo. “Mwa ichi,” akulemba tero, “sindidzaleka kukukumbutsani inu nthaŵi zonse za izi, mungakhale muzidziŵa nimukhazikika m’choonadi.” (2 Petro 1:12) Petro akugwiritsira ntchito liwu lachigiriki lakuti ste·riʹzo, lotembenuzidwa panopa kuti “nimukhazikika” koma lotembenuzidwa kuti “limbitsa” m’malangizo oyamba a Yesu kwa Petro: “Ukalimbitse abale ako mtima.” (Luka 22:32, Chipangano Chatsopano) Kugwiritsira ntchito kwake liwulo kungasonyeze kuti Petro akukumbukira malangizo amphamvu omwe analandira kwa Ambuye wake. Tsopano Petro akuti: “Ndichiyesa chokoma, pokhala ine m’msasa uwu [thupi laumunthu], kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani; podziŵa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi.”—2 Petro 1:13, 14.
19. Kodi tifunika zothandiza zotani lerolino?
19 Ngakhale kuti Petro akutchula mokoma mtima kuti oŵerenga kalata yake ali ‘okhazikika m’choonadi,’ akudziŵa kuti chikhulupiriro chawo chingatayike. (1 Timoteo 1:19) Popeza akudziŵa kuti adzafa posachedwa, akulimbitsa abale ake mwa kutchula zinthu zomwe iwo angadzazikumbukire pambuyo pake kuti adzakhale olimba mwauzimu. (2 Petro 1:15; 3:12, 13) Momwemonso, ifenso lero tifunika zikumbutso nthaŵi zonse kuti tikhalebe olimba m’chikhulupiriro. Kaya ndife yani kapena takhala zaka zingati m’choonadi, sitikayenera konse kunyalanyaza kuŵerenga Baibulo, phunziro laumwini, ndi kupezeka pamisonkhano ya mpingo. Ena amapereka zifukwa zosapezekera pamsonkhano, kuti amatopa kwambiri kapena kuti misonkhano imakhala yobwerezabwereza kapena yogwetsa ulesi, koma Petro anadziŵa kuti aliyense wa ife angataye chikhulupiriro kamodzinkamodzi ngati tidzikhulupirira kwambiri.—Marko 14:66-72; 1 Akorinto 10:12; Ahebri 10:25.
Maziko Olimba a Chikhulupiriro Chathu
20, 21. Kodi kusandulika kwa Yesu kunalimbitsa motani chikhulupiriro cha Petro ndi oŵerenga makalata ake, kuphatikizapo ife lero?
20 Kodi chikhulupiriro chathu chazikidwa pa nthanthi zopeka mwamachenjera? “Sitinatsata miyambi yachabe,” akuyankha Petro mwamphamvu, “pamene tinakudziŵitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake.” Petro, Yakobo, ndi Yohane anali ndi Yesu pamene anaona masomphenya ake m’mphamvu ya Ufumu. Petro akufotokoza: “Analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mawu otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; ndipo mawu awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.”—2 Petro 1:16-18.
21 Pamene Petro, Yakobo, ndi Yohane anaona masomphenyawo, Ufumu unakhaladi weniweni kwa iwo! “Ndipo,” akutero Petro, “tili nawo mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira.” Inde, oŵerenga kalata ya Petro, kuphatikizapo ife lero, ali ndi chifukwa chabwino chosamalira maulosi a Ufumu wa Mulungu. Kodi tiyenera kuwasamalira motani? Petro akuyankha: “Monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa m[i]tima yanu.”—2 Petro 1:19; Danieli 7:13, 14; Yesaya 9:6, 7.
22. (a) Kodi mitima yathu iyenera kukhala yogalamuka pa chiyani? (b) Kodi tingawasamalire motani mawu a ulosi?
22 Mitima yathu ingakhale ya mdima popanda kuunika kwa mawu a ulosi. Koma mwa kuwasamalira, mitima ya Akristu yakhala yogalamuka pofuna kuona kucha kwa tsiku pamene “nthanda,” Yesu Kristu, adzauka mu ulemerero wa Ufumu. (Chivumbulutso 22:16) Kodi ife lero timawasamalira motani mawu a ulosi? Mwa phunziro la Baibulo, mwa kukonzekera misonkhano ndi kutengamo mbali, ndi mwa ‘kuzisamalitsa izi; ndi kukhala mu izi.’ (1 Timoteo 4:15) Kuti mawu a ulosi akhale monga nyali younikira “m’malo a mdima” (mitima yathu), tiwalole kutikhudza kwambiri—zikhumbo zathu, mtima, maganizo, ndi zolinga. Tiyenera kukhala ophunzira Baibulo, pakuti Petro akumaliza chaputala 1 motere: “Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pachokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.”—2 Petro 1:20, 21.
23. Kodi chaputala choyamba cha 2 Petro chawakonzekeretsa zotani oŵerenga kalata yake?
23 M’chaputala chotsegulira kalata yake yachiŵiri, Petro anatipatsa chifukwa champhamvu chogwirira zolimba chikhulupiriro chathu chamtengo wapatali. Tsopano ndife okonzeka kupenda nkhani zofunika kwambiri zomwe zikutsatira. Nkhani yotsatira idzafotokoza chaputala 2 cha 2 Petro, mmene mtumwiyo akulimbana ndi vuto la makhalidwe oipa amphamvu amene analoŵa mumpingo.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji Petro akugogomezera kufunika kwake kwa chidziŵitso cholongosoka?
◻ Kodi nchiyani chimene chingakhale chifukwa chotchulira ukoma monga mkhalidwe woyamba kuwonjezera pa chikhulupiriro?
◻ Kodi nchifukwa ninji Petro akonda kukumbutsa abale ake nthaŵi zonse?
◻ Kodi ndi maziko ati olimba a chikhulupiriro chathu omwe Petro akutipatsa?
[Chithunzi patsamba 9]
Zophophonya za Petro sizinamtayitse chikhulupiriro chake