Chikondi (Agape)—Zimene Sichili ndi ZImene Chili
‘Muwonjezere . . . pachikondi cha pa abale chikondi.’—2 PETRO 1:5, 7.
1. (a) Kodi ndimkhalidwe uti umene Baibulo limagogomezera kwambiri? (b) Kodi ndimawu anayi ati Achigiriki amene kaŵirikaŵiri amatembenuzidwa kukhala “chikondi,” ndipo kodi ndiliti lotchulidwa pa 1 Yohane 4:8?
NGATI pali mkhalidwe kapena ubwino umodzi umene Mawu a Mulungu, Baibulo, amagogomezera kwambiri, ndiwo chikondi. M’Chigiriki, chinenero choyambirira cha Malemba Achikristu, muli mawu anayi otembenuzidwa kaŵirikaŵiri kukhala “chikondi.” Chikondi chimene tidzakambitsirana tsopano sichija cha eʹros (liwu losapezeka m’Malemba Achigiriki Achikristu), lozikidwa pakukopeka kwa mwamuna ndi mkazi; ndipo sichili stor·geʹ, chikondi chozikidwa paunansi wa achibale; sichili phi·liʹa, chikondi chachikulu chaubwenzi chozikidwa pakulemekezana, chofotokozedwa m’nkhani yapitayo. Mmalomwake, ndicho a·gaʹpe—chikondi chozikidwa palamulo la mkhalidwe, chimene chinganenedwe kukhala chofanana ndi kusadzikonda, chikondi chimene mtumwi Yohane anali kunena pamene anati: “Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.
2. Kodi nchiyani chomwe chanenedwa ponena za chikondi (a·gaʹpe)?
2 Ponena za chikondi chimenechi cha (a·gaʹpe), Profesa William Barclay mu New Testament Words yake amati: “Agapē imasonkhezeredwa ndi maganizo: sichili konse chikondi chimene chimangobuka pachokha m’mitima yathu [monga momwe zimachitikira ndi phi·liʹa]; ndilamulo la mkhalidwe limene timalitsatira modzifunira. Agapē kwakukulukulu imasonkhezeredwa ndi mphamvu zakulingalira. Ndicho chilakiko, chipambano, ndi chigonjetso. Palibe munthu amene mwachibadwa amakondadi adani ake. Kukonda adani athu ndiko kulaka zikhoterero zathu zonse zachibadwa ndi mtima. Kwenikweni agapē imeneyi . . . ndiyo mphamvu ya kukonda osakondeka, kukonda anthu amene sitimafuna.”
3. Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu ndi Paulo anagogomezerera chikondi?
3 Inde, chimodzi cha zinthu zimene zimasiyanitsa kulambira koyera kwa Yehova Mulungu ndi mitundu ina yonse ya kulambira ndiko kugogomezera kwake mtundu umenewu wa chikondi. Yesu Kristu ananenadi molondola pamene anatchula malamulo aŵiri aakulu koposa kuti: “Lamtsogolo ndi ili, . . . Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. Lachiŵiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.” (Marko 12:29-31) Mtumwi Paulo anagogomezera chikondi mofananamo m’chaputala 13 cha 1 Akorinto. Atagogomezera kuti chikondi chinali mkhalidwe wofunika koposa, anamaliza mwakunena kuti: “Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.” (1 Akorinto 13:13) Yesu ananena molondola kuti chikondi chikakhala chizindikiro chodziŵikitsa otsatira ake.—Yohane 13:35.
Zinthu Zimene Chikondi Sichili
4. Kodi ndimbali zingati zimene chikondi sichili ndi zimene chili zomwe Paulo akutchula pa 1 Akorinto 13:4-8?
4 Nsonga yamveketsedwa yakuti nkosavuta kwambiri kufotokoza zimene chikondi sichili kuposa kufotokoza zimene chili. Zimenezo nzowona, pakuti mtumwi Paulo m’chaputala chake chonena za chikondi, 1 Akorinto, m’mavesi 4 mpaka 8, akutchula zinthu zisanu ndi zinayi zimene chikondi sichili ndi zinthu zisanu ndi ziŵiri zimene icho chili.
5. Kodi “nsanje” imamasuliridwa motani, ndipo kodi ndimotani mmene imagwiritsidwira ntchito ndi lingaliro labwino m’Malemba?
5 Chinthu choyamba chimene Paulo akunena kuti chikondi sichili nchakuti “sichichita nsanje.” (NW) Zimenezi zifunikira kufotokoza ndithu chifukwa pali mbali zabwino ndi zoipa za nsanje. Dikishonale imamasulira “nsanje” kukhala “kusalekerera mpikisano” ndipo monga “kudzipereka kotheratu.” Motero, Mose ananena pa Eksodo 34:14 kuti: “Musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje.” Pa Eksodo 20:5, Yehova amati: “Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje [wofuna kudzipereka kotheratu, NW].” Nditanthauzo lofanana, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu.”—2 Akorinto 11:2.
6. Kodi nzitsanzo za m’Malemba ziti zimene zimasonyeza chifukwa chake chikondi sichichita nsanje?
6 Komabe, nthaŵi zambiri, “nsanje” imakhala ndi tanthauzo loipa, nchifukwa chake yandandalikidwa pamodzi ndi ntchito zathupi pa Agalatiya 5:20. Inde, nsanje yotero njadyera ndipo imabutsa chidani, ndipo chidani nchosemphana ndi chikondi. Nsanje inachititsa Kaini kuda Abele kufikira pakumupha, ndipo inachititsa abale a mimba ina khumi a Yosefe kumuda kufikira pakufuna kumupha. Chikondi sichimasirira chuma kapena zabwino za ena, monga momwe Mfumu Ahabu anasirira munda wa mphesa wa Naboti.—1 Mafumu 21:1-19.
7. (a) Kodi nchochitika chotani chimene chimasonyeza kuti Yehova samakondwera ndi kudzitamandira? (b) Nchifukwa ninji chikondi sichimadzitamandira ngakhale mopanda kulingalira?
7 Ndiyeno Paulo akutiuza kuti chikondi ‘sichidziŵa kudzitamandira.’ Kudzitamandira kumasonyeza kusoŵeka kwa chikondi, popeza kumachititsa wina kudziika pamalo oposa a ena. Yehova sakondwera ndi odzitamandira, monga momwe tingaonere ndi mmene anatsitsira Mfumu Nebukadinezara pamene anadzitamandira. (Danieli 4:30-35) Kaŵirikaŵiri kudzitamandira kumachitidwa mopanda kulingalira chifukwa cha kukhala wokondweretsedwa kwambiri ndi zipambano kapena chuma cha munthuwe. Ena angakhale ndi chizoloŵezi cha kudzitama chifukwa cha chipambano chawo muutumiki Wachikristu. Ena ali ngati mkulu wina amene anaimbira lamya mabwenzi ake kungowauza kuti anagula galimoto latsopano la ndalama zokwanira $50,000. Konseko nkupanda chikondi chifukwa kumasonyeza kuti wodzitamandirayo aposa omvetsera ake.
8. (a) Kodi Yehova amawaona motani awo amene ali odzikuza? (b) Nchifukwa ninji chikondi sichimachita mwanjira imeneyo?
8 Ndiyeno tikuuzidwa kuti chikondi “sichidzikuza.” Munthu wodzikuza, kapena wodzitukumula, mopanda chikondi amadzikweza yekha pamwamba pa ena. Mkhalidwe wamaganizo wotero ngwopanda nzeru kwambiri chifukwa “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.” (Yakobo 4:6) Chikondi chimachita mwanjira yosiyana kwambiri; chimaona ena kukhala oposa. Paulo analemba pa Afilipi 2:2, 3 kuti: “Kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi; musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.” Mkhalidwe wamaganizo wotero umachititsa ena kumva bwino, koma munthu wodzitukumula chifukwa cha kutetana amavutitsa ena maganizo.
9. Kodi nchifukwa ninji chikondi sichimachita zosayenera?
9 Ndiponso Paulo akunena kuti chikondi “sichichita zosayenera.” Dikishonale imamasulira liwu lakuti “zosayenera” kukhala “zosavomerezeka konse kapena zopandukira miyezo kapena makhalidwe abwino.” Munthu amene amachita mosayenera (mopanda chikondi) amanyalanyaza malingaliro a ena. Mabaibulo ambiri amatembenuza liwu Lachigiriki limenelo kukhala “chipongwe.” Munthu wotero amanyozera zimene zimaonedwa kukhala zoyenera ndi zabwino. Ndithudi, kulingalira ena mwachikondi kungatanthauze kupeŵa zinthu zonse zimene zili zachipongwe kapena zosayenera, zinthu zimene zimakwiyitsa kapena ngakhale zochititsa kakasi.
Zinthu Zina Zimene Chikondi Sichili
10. Kodi ndimotani mmene chikondi sichimatsatirira za mwini yekha?
10 Tsopano tikuuzidwa kuti chikondi “sichitsata za mwini yekha,” ndiko kuti, pamene pali nkhani yokhudza zokonda zathu ndi zija za ena. Mtumwiyo palemba lina akuti: “Munthu sanadana nalo thupi lake ndi kalelonse; komatu alilera nalisunga.” (Aefeso 5:29) Chotero, pamene zokonda zathu ziwombana ndi zokonda za ena ndipo ngati siziloŵetsamo malamulo a mkhalidwe a Baibulo, tiyenera kuchita monga momwe anachitira Abrahamu kwa Loti, mwachikondi kulola munthu winayo kusankha choyamba.—Genesis 13:8-11.
11. Kodi kunena kuti chikondi sichipsa mtima kumatanthauzanji?
11 Ndiponso chikondi sichikwiya msanga. Chotero Paulo akutiuza kuti chikondi “sichipsa mtima.” Sichamtima wapachala. Chimasonyeza kudziletsa. Makamaka okwatirana ayenera kutenga mosamala chilangizo chimenechi mwakupeŵa kulankhula mozaza kapena kulalatirana. Pamakhala mikhalidwe pamene kuli kosavuta kukwiyitsidwa, nchifukwa chake Paulo anakuona kukhala kofunika kupereka uphungu kwa Timoteo kuti: “Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziŵa kuphunzitsa, woleza”—inde, samapsa mtima—“wolangiza iwo akutsutsana mofatsa.”—2 Timoteo 2:24, 25.
12. (a) Kodi ndimwanjira yotani imene chikondi sichimalingalirira zoipa? (b) Kodi nchifukwa ninji sikuli kwanzeru kulingalira zoipa?
12 Akumapitiriza ndi zinthu zimene chikondi sichili, Paulo akulangiza kuti: “Chikondi . . . sichilingalira zoipa.” Zimenezo sizitanthauza kuti chikondi sichimazindikira zoipa. Yesu anasonyeza mmene tiyenera kuchitira ngati wina watichitira choipa chachikulu. (Mateyu 18:15-17) Koma chikondi sichimatilola kupitiriza kuipidwa, kusunga chakukhosi. Kusalingalira zoipa kumatanthauza kukhululukira ndi kuiŵala nkhaniyo itathetsedwa mwa Malemba. Inde, musadzizunze inu mwini kapena kudzivutitsa mwakupitirizabe kuganiza za choipacho, kulingalira zoipa!
13. Kodi kumatanthauzanji kusakondwera ndi chisalungamo, ndipo kodi nchifukwa ninji chikondi sichimachita motero?
13 Ndiponso, tikuuzidwa kuti chikondi “sichikondwera ndi [chisalungamo, NW].” Dziko limakondwera ndi chisalungamo, monga momwe timaonera ndi kuchuluka kwa mabuku achiwawa ndi umaliseche, mafilimu, ndi maprogramu a pa TV. Kukondwera konseko nkwadyera, kuli kusaŵerengera malamulo olungama a mkhalidwe a Mulungu kapena ubwino wa ena. Kukondwera kwadyera konseko nkufesera kwa thupi ndipo m’kupita kwa nthaŵi kudzatuta chivundi kuchokera m’thupi.—Agalatiya 6:8.
14. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe mwachidaliro kuti chikondi sichitha nthaŵi zonse?
14 Nachi chinthu chomalizira chimene chikondi sichimachita: “Chikondi sichitha nthaŵi zonse.” Kwenikweni, chikondi sichitha kapena kulephera chifukwa Mulungu ndiye chikondi, ndipo ndiye “Mfumu yosatha.” (1 Timoteo 1:17) Pa Aroma 8:38, 39, timatsimikiziridwa kuti chikondi cha Yehova pa ife sichidzatha konse: “Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Ndiponso, chikondi sichitha nthaŵi zonse chifukwa sichimakhala chopereŵera. Chikondi chimakwaniritsa zofunika za panthaŵi iliyonse, chimalimbika pachitokoso chilichonse.
Zinthu Zimene Chikondi Chili
15. Kodi nchifukwa ninji Paulo akuyamba ndi kuleza mtima pondandalika mbali zabwino za chikondi?
15 Tsopano akutembenukira kumbali yabwino, kuzinthu zimene chikondi chili, Paulo akuyamba kuti: “Chikondi chikhala chilezere.” Kwanenedwa kuti sipangakhale unansi Wachikristu popanda kuleza mtima, ndiko kuti, popanda kulekererana moleza mtima. Zimenezi zili choncho chifukwa tonsefe ndife opanda ungwiro, ndipo kupanda kwathu ungwiro ndi zophophonya zathu zimaika ena pachiyeso. Nchifukwa chake mtumwi Paulo akundandalika mbali imeneyi choyamba kukhala zimene chikondi chili!
16. Kodi ndimwanjira zotani zimene ziŵalo za banja zingasonyezere kukoma mtima kwa wina ndi mnzake?
16 Paulo akunena kuti chikondi chilinso “chokoma mtima.” Ndiko kuti, chikondi chimathandiza, chimalingalira ena, chimasamala za ena. Kukoma mtima kumasonyezedwa m’zinthu zazikulu ndi zazing’ono. Mosakayikira, Msamariya waunansi anali kusonyeza kukoma mtima kwa munthu amene anamenyedwa ndi achifwamba. (Luka 10:30-37) Chikondi chimakonda kunena kuti “chonde.” Kunena kuti, “Ndipatsireni mkate” nkulamula. Kuwonjezera mawu akuti “chonde” pazimenezo kumakuchititsa kukhala pempho. Amuna amakhala okoma mtima kwa akazi awo pamene alabadira uphungu wa pa 1 Petro 3:7 wakuti: “Amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.” Akazi amakhala okoma mtima kwa amuna awo pamene awapatsa “ulemu waukulu.” (Aefeso 5:33, NW) Atate amakhala okoma mtima kwa ana awo pamene atsatira uphungu wa pa Aefeso 6:4 wakuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].”
17. Kodi ndinjira ziŵiri ziti zimene chikondi chikondwerera ndi chowonadi?
17 Chikondi sichimakondwera ndi chisalungamo koma “chikondwera ndi chowonadi.” Chikondi ndi chowonadi zimagwirizana kwambiri—Mulungu ndiye chikondi, ndipo panthaŵi imodzimodziyo, iye ali “Mulungu wa chowonadi.” (Salmo 31:5) Chikondi chimakondwera poona chowonadi chikulakika pachinyengo ndi kuchivumbula; zimenezi zili chimodzi cha zochititsa chiwonjezeko chachikulu cha chiŵerengero cha olambira a Yehova lerolino. Komabe, popeza kuti chowonadi chikusiyanitsidwa ndi chisalungamo, lingaliro lingakhalenso lakuti chikondi chikondwera ndi chilungamo. Chikondi chikondwera ndi kulakika kwa chilungamo, monga momwe olambira a Yehova akulamulidwira kuchita pa kugwa kwa Babulo Wamkulu.—Chivumbulutso 18:20.
18. Kodi ndi m’lingaliro lotani limene chikondi chimakwiririra zinthu zonse?
18 Paulo akutiuzanso kuti chikondi “chikwirira zinthu zonse.” Monga momwe Kingdom Interlinear imasonyezera, lingaliro nlakuti chikondi chiphimba zinthu zonse. ‘Sichimaneneza’ mbale, monga momwe oipa amakonda kuchitira. (Salmo 50:20; Miyambo 10:12; 17:9) Inde, lingaliro panopo nlofanana ndi la pa 1 Petro 4:8: “Chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” Ndithudi, kukhulupirika kungaletse munthu kubisa machimo aakulu ochimwira Yehova ndi mpingo Wachikristu.
19. Kodi ndimwanjira yotani imene chikondi chikhulupirira zinthu zonse?
19 Chikondi “chikhulupirira zinthu zonse.” Chikondi nchabwino, sichoipa. Zimenezi sizikutanthauza kuti chikondi chimangokhulupirira zilizonse. Sichimafulumira kukhulupirira nkhani za m’maluwa. Koma kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro mwa Mulungu, ayenera kukhala ndi chifuno cha kukhulupirira. Chotero chikondi sichikayikira, sichisuliza mopambanitsa. Sichimakana kukhulupirira monga momwe amachitira osakhulupirira kukhalako kwa Mulungu, amene motsimikiza amanena kuti kulibe Mulungu, ndipo sichili ngati okayikira kukhalako kwa Mulungu, amene motsimikiza amanena kuti nkosatheka konse kudziŵa kumene tinachokera, chifukwa chake tili pano, ndi mmene mtsogolo mudzakhalira. Mawu a Mulungu amatipatsa chitsimikizo cha zinthu zonsezi. Chikondi nchokonzekera kukhulupirira chifukwa chili ndi chidaliro, sichimanyumwa mopambanitsa.
20. Kodi chikondi chigwirizana motani ndi chiyembekezo?
20 Mtumwi Paulo akutilimbikitsanso kuti chikondi “chiyembekeza zinthu zonse.” Popeza kuti chikondi nchabwino, sichoipa, chili ndi chiyembekezo cholimba cha zinthu zonse zolonjezedwa m’Mawu a Mulungu. Timauzidwa kuti: “Wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugaŵana nawo.” (1 Akorinto 9:10) Monga momwe chikondi chiliri ndi chidaliro, chilinso ndi chiyembekezo, nthaŵi zonse chimayembekeza zabwino koposa.
21. Kodi pali chilimbikitso chotani cha m’Malemba chakuti chikondi chipirira?
21 Pomaliza, tikulimbikitsidwa kuti chikondi “chipirira zinthu zonse.” Chimakhoza kuchita zimenezo chifukwa cha zimene mtumwi Paulo akutiuza pa 1 Akorinto 10:13 kuti: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” Chikondi chidzatichititsa kuyang’ana pazitsanzo zambiri za m’Malemba za atumiki a Mulungu amene anapirira, Yesu Kristu nkukhala chitsanzo chachikulu, monga momwe tikukumbutsidwira pa Ahebri 12:2, 3.
22. Monga ana a Mulungu, kodi ndimkhalidwe wofunika koposa uti umene tiyenera kufunitsitsa kusonyeza nthaŵi zonse?
22 Ndithudi, chikondi (a·gaʹpe) chili mkhalidwe wofunika koposa umene ifeyo monga Akristu, Mboni za Yehova, tifunikira kukulitsa, kudziŵa ponse paŵiri zimene sichili ndi zimene chili. Monga ana a Mulungu, tiyeni tikhale ofunitsitsa nthaŵi zonse kusonyeza chipatso chimenechi cha mzimu wa Mulungu. Kuteroko nkufanana ndi Mulungu, pakuti, kumbukirani, “Mulungu ndiye chikondi.”
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu ndi Paulo amasonyezera kufunika kwa chikondi?
◻ Kodi chikondi sichichita nsanje m’lingaliro lotani?
◻ Kodi ndimotani mmene chikondi ‘chimakwiririra zinthu zonse’?
◻ Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti chikondi sichitha nthaŵi zonse?
◻ Kodi ndimwanjira ziŵiri zotani zimene chikondi chikondwera ndi chowonadi?
[Bokosi patsamba 21]
CHIKONDI (AGAPE)
Zimene Sichili Zimene Chili
1. Sichichita nsanje 1. Chikhala chilezere
2. Sichidzitamandira 2. Nchokoma mtima
3. Sichidzikuza 3. Chikondwera ndi chowonadi
4. Sichichita zosayenera 4. Chikwirira zinthu zonse
5. Sichitsata za mwini yekha 5. Chikhulupirira zinthu zonse
6. Sichipsa mtima 6. Chiyembekeza zinthu zonse
7. Sichilingirira zoipa 7. Chipirira zinthu zonse
8. Sichikondwera ndi chisalungamo
9. Sichitha nthaŵi zonse
[Zithunzi patsamba 18]
Yehova anachepetsa Nebukadinezara chifukwa chodzikuza