Achinyamata, Kodi Mungakonzekere Bwanji Kubatizidwa?
“Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.”—SAL. 40:8.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kubatizidwa ndi nkhani yaikulu? (b) Kodi munthu asanabatizidwe ayenera kutsimikizira zinthu ziti, ndipo n’chifukwa chiyani?
KODI ndinu wachinyamata ndipo mukuganizira zobatizidwa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti kubatizidwa ndi mwayi waukulu kwambiri. M’nkhani yapita ija tinaona kuti kubatizidwa ndi nkhani yaikulu imene muyenera kuiganizira bwino. Munthu amabatizidwa posonyeza kuti wadzipereka kwa Yehova. Amamulonjeza kuti adzamutumikira moyo wake wonse komanso azichita zofuna za Yehovayo osati zake. Choncho munthu asanabatizidwe ayenera kutsimikizira kuti wakonzekadi kudzipereka kwa Yehova, akufunadi kuchita zimenezi komanso akumvetsa tanthauzo la kudzipereka kwa Yehova.
2 Ndiye kodi mungatani ngati mukuona kuti si inu wokonzeka kubatizidwa? Nanga mungatani ngati inuyo mukufuna kubatizidwa koma makolo anu akuona kuti muyenera kuyembekeza kuti muphunzire kaye zinthu zina? Simuyenera kukhumudwa, koma yesetsani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova kuti mubatizidwe pasanapite nthawi yaitali. Pali zinthu zina zimene zingakuthandizeni kuchita zimenezi. Zinthu zake ndi zokhudza (1) zimene mumakhulupirira, (2) zimene mumachita ndiponso (3) kuyamikira zimene Mulungu wakuchitirani.
ZIMENE MUMAKHULUPIRIRA
3, 4. (a) Kodi achinyamata angaphunzire chiyani kwa Timoteyo?
3 Mungachite bwino kudzifunsa mafunso otsatirawa: Kodi ndikudziwa bwanji kuti kuli Mulungu? Nanga ndikudziwa bwanji kuti Baibulo ndi Mawu ake? N’chifukwa chiyani ndimakhulupirira kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo n’kothandiza kusiyana ndi kutsatira makhalidwe a anthu a m’dzikoli? Cholinga cha mafunso amenewa si choti muyambe kukayikira zimene mumakhulupirira. Koma mafunsowa angakuthandizeni kuti mutsatire malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezi?
4 Chitsanzo cha Timoteyo chingakuthandizeni pa nkhaniyi. Iye ankadziwa bwino Malemba. Paja anaphunzitsidwa ndi mayi ake ndiponso agogo ake ‘kuyambira pamene anali wakhanda.’ Komabe Paulo anamuuza kuti: “Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo.” (2 Tim. 3:14, 15) Buku lina limanena kuti mawu achigiriki amene palembali anawamasulira kuti ‘kukhutira nazo,’ amatanthauza ‘kutsimikizira kuti mfundo inayake ndi yoona.’ Choncho Timoteyo anatsimikizira kuti zimene anaphunzira ndi zoona. Iye ankakhulupirira zinthuzo osati chifukwa choti mayi ake ndi agogo ake anamuuza kuchita zimenezi. Koma chifukwa choti anaziganizira n’kufika pokhutira kuti ndi zoona.—Werengani Aroma 12:1.
5, 6. Kodi kutsimikizira kuti zimene mwaphunzira ndi zoona kungakuthandizeni bwanji?
5 Mwina nanunso mwakhala mukudziwa mfundo za m’Baibulo kuyambira muli mwana. Komabe mungachite bwino kufufuza kuti mupeze umboni wakuti zimene mwaphunzirazo ndi zoona. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri mfundo za m’Baibulo. Zingakuthandizeninso kuti musamasokonezeke ndi zochita za anzanu, maganizo a anthu a m’dzikoli ndiponso zofuna zanu.
6 Kutsimikizira kuti zimene mwaphunzira ndi zoona kungakuthandizeni kuti muzitha kuyankha bwino mafunso amene anzanu angakufunseni. Mafunso ake ndi monga akuti, “Kodi ukudziwa bwanji kuti kulidi Mulungu? Ngati Mulungu ndi wachikondi, n’chifukwa chiyani amalola kuti zoipa zizichitika? Kodi zingatheke bwanji kuti Mulungu alibe chiyambi?” Ngati mwakonzekera bwino, mafunso oterewa sangachititse kuti muyambe kukayikira zimene mumakhulupirira. M’malomwake angakuthandizeni kuti mupitirize kuphunzira Baibulo n’cholinga choti mudziwe zambiri.
7-9. Kodi nkhani zapawebusaiti yathu zakuti, “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?” zingakuthandizeni bwanji kulimbitsa chikhulupiriro chanu?
7 Mukamaphunzira Baibulo mwakhama mumatha kuyankha mafunso amene anthu angakufunseni. Komanso simukayikira mfundo za m’Baibulo ndipo mumakhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Mac. 17:11) Achinyamata ambiri amaona kuti mabuku athu amene amafotokoza umboni woti kuli Mulungu amawathandiza kwambiri. (Onani kabuku kakuti, The Origin of Life—Five Questions Worth Asking komanso buku lakuti, Is There a Creator Who Cares About You?) Achinyamata ena amaona kuti nkhani zakuti, “Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?” zimene zimapezeka pawebusaiti yathu ya jw.org/ny ndi zothandizanso. Mungazipeze pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA. Nkhani zimenezi zingakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana.
8 Popeza mukudziwa kale mfundo za m’Baibulo, mwina mungayankhe mosavuta mafunso ena omwe ali m’nkhanizi. Koma kodi mumakhulupiriradi zimenezo kapena mumangoyankha chifukwa choti ndi zimene munaphunzira? Nkhanizi zimakhala ndi malemba oti muwerenge ndi kuwaganizira komanso mafunso okuthandizani kuti mulembe maganizo anu. Nkhani zimenezi zingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu komanso kukonzekera mmene mungafotokozere ena zimene mumakhulupirira. Ngati muli ndi mwayi wogwiritsa ntchito Intaneti, mungachite bwino kuwerenga nkhanizi mukamaphunzira Baibulo panokha.
9 Muyenera kutsimikiza kuti zimene mumaphunzira ndi zoona. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mukhale okonzeka kubatizidwa. Mtsikana wina anati: “Ndisanabatizidwe ndinaphunzira Baibulo n’kutsimikizira kuti chipembedzo chathu ndi choona. Ndipo mpaka pano ndimakhulupirirabe kwambiri zimenezi.”
ZIMENE MUMACHITA
10. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro?
10 Baibulo limati: “Chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.” (Yak. 2:17) Zimene mumachita zimasonyeza ngati chikhulupiriro chanu ndi cholimba kapena ayi. Baibulo limanena kuti ‘muyenera kukhala ndi khalidwe loyera ndiponso kuchita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.’—Werengani 2 Petulo 3:11.
11. Kodi mungasonyeze bwanji kuti muli ndi khalidwe loyera?
11 Kuti musonyeze kuti muli ndi khalidwe loyera, nthawi zonse muyenera kupewa kuchita zoipa. Mwachitsanzo, taganizirani zimene mwachita pa miyezi 6 yapitayi. Ngati munayesedwa kuti muchite zoipa, kodi munaiganizira bwinobwino nkhaniyo n’kuzindikira zoyenera kuchita? (Aheb. 5:14) Kodi mukukumbukira nthawi ina pamene munakana mayesero kapena kutengera zochita za anzanu? Nanga kodi zimene mumachita kusukulu zimathandiza anthu kuti azilemekeza Yehova? Kodi mumakhala okhulupirika kwa Yehova kapena mumachita zofuna za anthu akusukulu kwanu n’cholinga choti asakunyozeni? (1 Pet. 4:3, 4) N’zoona kuti tonsefe timalakwitsa zinthu nthawi zina. Ngakhale anthu amene atumikira Mulungu kwa zaka zambiri, nthawi zina amachita mantha kulalikira kwa ena. Komabe munthu aliyense amene anadzipereka kwa Yehova ayenera kunyadira kuti ndi wa Mboni za Yehova ndipo ayenera kuyesetsa kukhala ndi khalidwe loyera.
12. Kodi “ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu” ndi ziti, nanga muyenera kuziona bwanji?
12 Koma kodi “ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu” ndi ziti? Izi ndi zinthu monga kusonkhana komanso kulalikira. Palinso zinthu zina zomwe anthu ambiri sangaone monga kupemphera komanso kuphunzira Baibulo panokha. Munthu amene anadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse saona zinthu zimenezi ngati zotopetsa. Koma amakhala ndi maganizo ofanana ndi a Mfumu Davide amene anati: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.”—Sal. 40:8.
13, 14. Kodi ndi buku liti limene lingakuthandizeni kuti muzichita “ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu,” ndipo bukuli lathandiza bwanji achinyamata ena?
13 Buku lachiwiri la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, lingakuthandizeni kuti muzichita “ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.” Patsamba 308 ndi 309 m’bukuli, pali mafunso amene mungayankhe. Mafunso ake ndi monga akuti: “Mukamapemphera, kodi mumatchula mwachindunji zimene mukufuna? Nanga mapemphero anuwo amasonyeza kuti mumakondadi Yehova?” “Kodi mumachita zotani paphunziro lanu laumwini?” “Kodi mumalowa mu utumiki ngakhale ngati makolo anu sanalowe?” Ndiyeno patsamba 309 palinso malo amene mungalembepo zimene mukufuna kuchita pa nkhani ya kupemphera, kuphunzira panokha komanso kulalikira.
14 Achinyamata ambiri amene akuganiza zobatizidwa amaona kuti zimene zili pamasambawa n’zothandiza kwambiri. Mtsikana wina dzina lake Tilda ananena kuti: “Ndinkagwiritsa ntchito masamba amenewa kulembapo zimene ndinkafuna kuchita. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono ndinakwaniritsa zimene ndinalembazo. Patangotha chaka chimodzi, ndinali wokonzeka kubatizidwa.” Mnyamata wina dzina lake Patrick ananenanso kuti: “Ndinkadziwa zimene ndinkafuna kuchita, komabe kulemba zinthuzo kunandithandiza kuchita khama kuti ndizikwaniritse.”
15. N’chifukwa chiyani aliyense ayenera kusankha yekha kudzipereka kwa Mulungu?
15 Patsamba 309 pali funso lina lofunika kwambiri lakuti: “Kodi mungapitirize kutumikira Yehova ngakhale makolo anu ndiponso anzanu atasiya kum’tumikira?” Muyenera kukumbukira kuti munthu aliyense adzayankha yekha kwa Mulungu. Choncho aliyense ayenera kusankha yekha kuti adzipereke kwa iye ndiponso kubatizidwa. Sayenera kudalira makolo ake kapenanso anthu ena potumikira Mulungu. Mukakhala ndi khalidwe loyera ndiponso mukamachita zinthu zosonyeza kuti ndinu wodzipereka kwa Yehova, mumasonyeza kuti mumamukonda komanso mumakonda mfundo zake. Komanso mumasonyeza kuti mukhoza kubatizidwa pasanapite nthawi yaitali.
MUZIYAMIKIRA ZIMENE MULUNGU WAKUCHITIRANI
16, 17. (a) N’chiyani chiyenera kuchititsa munthu kuti abatizidwe? (b) Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chingatithandize kuti tiziyamikira dipo?
16 Munthu wina amene ankadziwa bwino Chilamulo cha Mose anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?” Yesu anamuyankha kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mat. 22:35-37) Apatu Yesu anasonyeza kuti munthu ayenera kubatizidwa komanso kutumikira Yehova chifukwa chomukonda ndi mtima wonse. Chinthu chimodzi chimene chingakuthandizeni kuti muzikonda Yehova ndi mtima wonse ndi kuganizira kwambiri dipo limene anapereka. (Werengani 2 Akorinto 5:14, 15; 1 Yohane 4:9, 19.) Izi zingakuthandizeni kuti muzisonyeza kuti mumayamikira zimene Mulungu anachitazi.
17 Tiyerekeze kuti mukumira m’madzi ndiye munthu wina wakupulumutsani. Kodi mungangopita kunyumba kukasintha zovala n’kuiwala zimene munthuyo wakuchitirani? Ayi. N’zodziwikiratu kuti mungathokoze munthuyo chifukwa wapulumutsa moyo wanu. N’chimodzimodzinso zimene Yehova ndi Yesu anatichitira. Dipo limene anapereka linatipulumutsa ku uchimo ndi imfa. Chifukwa cha chikondi chimene anatisonyezachi, tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.
18, 19. (a) N’chifukwa chiyani simuyenera kuchita mantha kuti mudzipereke kwa Yehova? (b) Kodi kutumikira Yehova kungakuthandizeni bwanji?
18 Kodi mumayamikira zimene Yehova wakuchitirani? Ngati ndi choncho ndiye kuti muyenera kudzipereka kwa iye komanso kubatizidwa. Komabe kumbukirani kuti munthu akadzipereka kwa Yehova amamulonjeza kuti azichita zimene Yehovayo amafuna zivute zitani. Ndiye kodi muyenera kuchita mantha ndi zimenezi? Ayi. Musaiwale kuti Yehova amakufunirani zabwino ndipo “amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6) Kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa kudzakuthandizani kukhala osangalala. M’bale wina amene panopo ali ndi zaka 24 ndipo anabatizidwa asanakwanitse zaka 13 anati: “Ndikanadikira kaye, mwina ndikanabatizidwa nditamvetsa bwino zinthu zina. Komabe kubatizidwa ndili wamng’ono kunandithandiza kuti ndisatengeke ndi zinthu za m’dzikoli.”
19 Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi Satana. Paja Satana sakufunirani zabwino ndipo sangakuthandizeni kukhala ndi tsogolo labwino. Sangachite zimenezi chifukwa nayenso alibiretu tsogolo. Choncho mukayamba kuchita zofuna zake nanunso simungakhale ndi tsogolo labwino.—Chiv. 20:10.
20. Kodi wachinyamata angakonzekere bwanji kudzipereka ndiponso kubatizidwa? (Onaninso bokosi lakuti, “Nkhani Zimene Zingakuthandizeni.”)
20 Malinga ndi zimene takambiranazi, ndi nzeru kudzipereka kwa Yehova. Koma kodi mwakonzeka kuchita zimenezi? Ngati ndi choncho musazengereze. Komabe ngati panopa simunakonzeke, muzichita zinthu zimene zatchulidwa m’nkhaniyi zomwe zingakuthandizeni. Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti: “Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenera m’njira yomweyo.” (Afil. 3:16) Mukatsatira malangizowa, pasanapite nthawi yaitali mudzakhala okonzeka kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa.