Mutu 42
Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano
1. Kodi Yohane anafotokoza kuti anaona zotani mngelo uja atabwerera naye m’mbuyo n’kuyamba kumuonetsa zimene zidzachitike kumayambiriro kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000?
YOHANE anapitiriza kuona masomphenya aulemererowa pamene mngelo uja anabwerera naye m’mbuyo n’kuyamba kumuonetsa zimene zidzachitike kumayambiriro kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000. Kodi Yohane anafotokoza kuti anaona zotani? Iye anati: “Tsopano ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, pakuti kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitachoka, ndipo kulibenso nyanja.” (Chivumbulutso 21:1) Apa iye anayamba kuona zinthu zochititsa chidwi kwambiri.
2. (a) Kodi ulosi wa Yesaya wonena za kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano unakwaniritsidwa bwanji pa Ayuda amene anabwerera kwawo mu 537 B.C.E.? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti ulosi wa Yesaya unayenera kudzakwaniritsidwanso mwanjira ina, ndipo lonjezo limeneli likukwaniritsidwa bwanji?
2 Zaka mahandiredi ambiri m’mbuyomo nthawi ya Yohane isanafike, Yehova anauza Yesaya kuti: “Pakuti ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” (Yesaya 65:17; 66:22) Ulosi umenewu unakwaniritsidwa koyamba pamene Ayuda okhulupirika anabwerera ku Yerusalemu mu 537 B.C.E., atakhala zaka 70 mu ukapolo ku Babulo. Iwo atabwerera kwawo, anakhala mtundu woyera, kapena kuti “dziko lapansi latsopano,” ndipo anali ndi ulamuliro watsopano, kapena kuti “kumwamba kwatsopano.” Komabe, mtumwi Petulo anasonyeza kuti ulosiwu udzakwaniritsidwanso mwanjira ina pamene anati: “Koma pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13) Tsopano Yohane anasonyeza kuti lonjezo limeneli likukwaniritsidwa m’tsiku la Ambuye. “Kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale,” zidzachoka. Zimenezi zikuimira dziko la Satanali pamodzi ndi maboma ake olamulira, omwe amachita zinthu motsogoleredwa ndi Satana pamodzi ndi ziwanda zake. “Nyanja” yamafunde, yomwe ikuimira anthu oipa ndiponso osamvera Mulungu, sidzakhalaponso. Zinthu zimenezi zidzalowedwa m’malo ndi “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” zomwe zikuimira mtundu watsopano wa anthu okhala padziko lapansi amene azidzalamuliridwa ndi boma latsopano, lomwe ndi Ufumu wa Mulungu.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 20:11.
3. (a) Kodi Yohane anafotokoza zotani, ndipo Yerusalemu Watsopano n’chiyani? (b) Kodi mfundo yakuti Yerusalemu Watsopano ‘adzatsika kuchokera kumwamba’ ikutanthauza chiyani?
3 Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “Ndinaonanso mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wokongoletsedwera mwamuna wake.” (Chivumbulutso 21:2) Yerusalemu Watsopano ndi mkwatibwi wa Khristu, ndipo wapangidwa ndi Akhristu odzozedwa amene anakhalabe okhulupirika mpaka imfa ndipo anaukitsidwa kuti akakhale mafumu ndi ansembe pamodzi ndi Yesu amene ali mu ulemerero wake. (Chivumbulutso 3:12; 20:6) Yerusalemu wa padziko lapansi anali likulu la ulamuliro wakale ku Isiraeli. Mofanana ndi zimenezi, boma la dziko latsopano lapangidwa ndi Yerusalemu Watsopano, yemwe ndi wokongola kwambiri, pamodzi ndi Mkwati wake. Boma limeneli ndi limene likutchedwa “kumwamba kwatsopano.” Lembali likusonyeza kuti ‘mkwatibwi adzatsika kuchokera kumwamba.’ Zimenezi sizikutanthauza kuti adzachoka kumwamba n’kubwera padziko lapansi, koma kuti adzayamba kuyendetsa zinthu padzikoli. Mkwatibwi wa Mwanawankhosa azidzathandizana ndi Mwanawankhosayo mokhulupirika poyendetsa boma lolungama lomwe lizidzalamulira anthu onse. Zimenezi zidzabweretsa madalitso osaneneka kudziko lapansi latsopano.
4. Kodi Mulungu anachita lonjezo lotani lofanana ndi limene anachita ndi mtundu wa Isiraeli, umene unali watsopano?
4 Yohane akupitiriza kutiuza kuti: “Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: ‘Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.’” (Chivumbulutso 21:3) Pamene Yehova ankachita pangano la Chilamulo ndi mtundu wa Isiraeli umene pa nthawiyo unali watsopano, analonjeza kuti: “Ine ndidzaika chihema changa chopatulika pakati panu, ndipo sindidzanyansidwa nanu. Motero ndidzayendadi pakati panu ndi kukusonyezani kuti ine ndine Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga.” (Levitiko 26:11, 12) Tsopano pa Chivumbulutso 21:3, Yehova akulonjeza anthu okhulupirika zinthu zofanana ndi zimene analonjeza Aisiraeli akale. Pa Tsiku la Chiweruzo la zaka 1,000, iwo adzakhala anthu ake apadera kwambiri.
5. (a) Kodi Mulungu adzakhala bwanji pamodzi ndi anthu mu Ulamuliro wa Zaka 1,000? (b) Nanga kodi Mulungu adzakhala bwanji pamodzi ndi anthu Ulamuliro wa Zaka 1,000 ukadzatha?
5 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yehova “adzakhala pamodzi” ndi anthu mongoyembekezera chabe, moimiridwa ndi Mwana wake yemwenso ndi mfumu, Yesu Khristu. Koma pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu akadzapereka Ufumu kwa Atate wake, sipadzafunikanso mkhalapakati, kapena mfumu yoimira Mulungu. Yehova adzakhala ndi “anthu ake” mpaka kalekale mwauzimu komanso mwachindunji. (Yerekezerani ndi Yohane 4:23, 24.) Umenewu ndi mwayi waukulu zedi umene anthu angwiro adzakhale nawo.
6, 7. (a) Kodi ndi malonjezo ati osangalatsa amene Yohane anafotokoza, ndipo ndani amene adzasangalale ndi madalitso amenewo? (b) Kodi Yesaya anafotokoza bwanji paradaiso wauzimu ndiponso weniweni?
6 Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Apanso tikukumbutsidwa za malonjezo ena ouziridwa a m’mbuyomu. Mwachitsanzo, Yesaya ankayembekezera nthawi imene imfa ndi kulira sizidzakhalaponso, ndiponso chisoni chidzalowedwa m’malo ndi chisangalalo. (Yesaya 25:8; 35:10; 51:11; 65:19) Apa tsopano Yohane akutitsimikizira kuti malonjezo osangalatsawa adzakwaniritsidwa bwino kwambiri pa Tsiku la Chiweruzo la zaka 1,000. Oyamba kulandira madalitsowa adzakhala a khamu lalikulu. “Mwanawankhosa, amene ali pambali pa mpando wachifumu,” adzapitiriza kuwaweta ndi “kuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.” (Chivumbulutso 7:9, 17) Koma m’kupita kwa nthawi, anthu onse amene adzaukitsidwe n’kukhulupirira Yehova adzakhala pamodzi ndi anthu a khamu lalikuluwa ndipo onsewa adzasangalala ndi paradaiso wauzimu komanso weniweni.
7 Yesaya anati: “Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva.” Komanso “pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.” (Yesaya 35:5, 6) Pa nthawi imeneyonso, “iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo, ndipo anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.” (Yesaya 65:21, 22) Choncho, iwo sadzachotsedwa padziko lapansi.
8. Kodi Yehova ananena yekha kuti chiyani posonyeza kuti malonjezo osangalatsawa ndi odalirika?
8 Tikamaganizira malonjezo amenewa, timatha kuona m’maganizo mwathu kuti zinthu zidzakhala zosangalatsa kwambiri m’tsogolomu. Boma labwino kwambiri lakumwamba lidzabweretsa madalitso osaneneka kwa anthu okhulupirika. Koma kodi zinthu zabwino ngati zimenezi zidzachitikadi? Kodi madalitsowa angokhala maloto chabe amene Yohane, yemwe anali wokalamba, ankalota ali mkaidi pachilumba cha Patimo? Yehova akuyankha yekha kuti: “Ndipo wokhala pampando wachifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.’ Ananenanso kuti: ‘Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.’ Anandiuzanso kuti: ‘Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega, chiyambi ndi mapeto.’”—Chivumbulutso 21:5, 6a.
9. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira ngakhale pang’ono kuti madalitso am’tsogolowa adzakwaniritsidwa?
9 Zimenezi zili ngati kuti Yehova akusainira yekha chikalata chotsimikizira kuti anthu okhulupirika adzalandiradi madalitso m’tsogolomu. Kodi munthu angayese dala kutsutsa zinthu zimene Yehova watsimikizira mwanjira imeneyi? Malonjezo amenewa ndi otsimikizirika kwambiri moti Yehova analankhula ngati kuti akwaniritsidwa kale. Iye anati: “Zakwaniritsidwa!” Kodi si paja Yehova ndi “Alefa ndi Omega . . . Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera, Wamphamvuyonse”? (Chivumbulutso 1:8) Zimenezi n’zoonadi, ndipo iye ananena yekha kuti: “Ine ndine woyamba ndi womaliza, ndipo palibenso Mulungu kupatulapo ine.” (Yesaya 44:6) Motero, iye anganene maulosi ndi kuwakwaniritsa ndendende. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri chikhulupiriro. Choncho, iye analonjeza kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” M’malo mochedwa ndi kukayikira ngati malonjezo ochititsa chidwiwa adzachitikedi, ndi bwino kumadzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo pandekha ndiyenera kuchita chiyani kuti ndidzalandire nawo madalitsowa?’
Anthu Omva Ludzu Adzapatsidwa “Madzi”
10. Kodi Yehova amapereka “madzi” otani, ndipo madziwo akuimira chiyani?
10 Yehova ananena yekha kuti: “Aliyense womva ludzu, ndidzamupatsa madzi a m’kasupe wa moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 21:6b) Kuti munthu athetse ludzu limeneli, ayenera kuzindikira zosowa zake zauzimu ndiponso ayenera kufunitsitsa kulandira “madzi” amene Yehova amapereka. (Yesaya 55:1; Mateyu 5:3) Kodi “madzi” amenewa ndi otani? Yesu anayankha funso limeneli pamene ankalalikira kwa mayi wina pachitsime ku Samariya. Iye anamuuza kuti: “Amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu m’pang’ono pomwe. Ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi otuluka mwa iye, opatsa moyo wosatha.” “Madzi a m’kasupe wa moyo” amenewo amachokera kwa Mulungu kudzera mwa Khristu. Madziwo akuimira zinthu zonse zimene Mulungu amapereka zothandiza anthu kuti akhalenso ndi moyo wangwiro. Mofanana ndi mayi wachisamariya uja, tiyenera kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumwa madzi ambiri ochokera m’kasupe wa moyo. Komanso mofanana ndi mayi uja, tiyenera kukhala okonzeka kusiya zinthu zosafunikira kwenikweni n’cholinga choti tiuze anthu ena uthenga wabwino.—Yohane 4:14, 15, 28, 29.
Opambana pa Nkhondo
11. Kodi Yehova anapereka lonjezo lotani, ndipo mawu amenewo choyamba akupita kwa ndani?
11 Anthu amene adzamwe “madzi” otsitsimulawo ayeneranso kupambana pa nkhondo, monga mmene Yehova anapitirizira kunena kuti: “Aliyense wopambana pa nkhondo adzalandira zimenezi monga cholowa. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake, ndipo iye adzakhala mwana wanga.” (Chivumbulutso 21:7) Lonjezo limeneli likufanana ndi malonjezo amene anali m’mauthenga opita kumipingo 7. Choncho, mawu amenewa choyamba ayenera kuti akupita kwa ophunzira a Yesu odzozedwa. (Chivumbulutso 2:7, 11, 17, 26-28; 3:5, 12, 21) Kwa nthawi yaitali, abale auzimu a Khristu akhala akuyembekezera mwachidwi mwayi wapadera wokhala mbali ya Yerusalemu Watsopano. Ngati iwo angapambane pa nkhondo, mofanana ndi mmene Yesu anapambanira, ndiye kuti akhoza kudzakhaladi mbali ya Yerusalemu Watsopano.—Yohane 16:33.
12. Kodi lonjezo la Yehova la pa Chivumbulutso 21:7 lidzakwaniritsidwa bwanji kwa anthu a khamu lalikulu?
12 Anthu a khamu lalikulu ochokera m’mitundu yonse nawonso akuyembekezera kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli. Nawonso akuyenera kupambana pa nkhondo ndi kupitirizabe kutumikira Mulungu mokhulupirika mpaka adzatuluke m’chisautso chachikulu. Kenako adzalandira cholowa chawo padziko lapansi, chomwe ndi ‘ufumu umene anawakonzera kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa dziko.’ (Mateyu 25:34) Anthu a khamu lalikuluwa, komanso atumiki ena a Ambuye apadziko lapansi okhala ngati nkhosa amene adzapambane mayesero omaliza zaka 1,000 zikadzatha, akutchedwa “oyera.” (Chivumbulutso 20:9) Iwo adzakhala pa ubwenzi wopatulika ndi Mlengi wawo, Yehova Mulungu, yemwe azidzawaona ngati ana ake, ndipo adzakhala mbali ya gulu lake la m’chilengedwe chonse.—Yesaya 66:22; Yohane 20:31; Aroma 8:21.
13, 14. Kuti tidzalandire madalitso osangalatsa a Mulungu, kodi tikufunika kupeweratu makhalidwe otani, ndipo n’chifukwa chiyani tikuyenera kutero?
13 Popeza anthu a Mboni za Yehova akuyembekezera madalitso osangalatsawa, iwo ayenera kuyesetsa kukhalabe oyera ndi kupewa kudetsedwa ndi zinthu zonyansa za m’dziko la Satanali. Tiyenera kukhala anthu olimba ndiponso titsimikize ndi mtima wonse kuti Mdyerekezi asatikokere m’gulu la anthu oipa amene Yehova akuwafotokoza tsopano. Iye anati: “Koma amantha, opanda chikhulupiriro, odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa, opha anthu, adama, ochita zamizimu, opembedza mafano, ndi onse abodza, gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto ndi sulufule. Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.” (Chivumbulutso 21:8) Ndithudi, munthu aliyense amene akufuna kudzalandira madalitso ayenera kupewa kuchita zinthu zonyansa zimene zaipitsa dziko lakaleli. Munthu wotere ayenera kupambana pa nkhondo pokhalabe wokhulupirika pamene akukumana ndi mayesero komanso mavuto osiyanasiyana.—Aroma 8:35-39.
14 Matchalitchi Achikhristu, ngakhale kuti amanena kuti ndi mkwatibwi wa Khristu, amachita zinthu zonyansa zimene Yohane wafotokoza palembali. Choncho, matchalitchiwa adzawonongedwa pamodzi ndi Babulo Wamkulu yense ndipo sadzakhalaponso. (Chivumbulutso 18:8, 21) Komanso Mkhristu aliyense wodzozedwa kapena wa m’khamu lalikulu amene angayambe kuchita zinthu zoipazi, kapena kuyamba kulimbikitsa makhalidwe oipawa, nayenso sadzalandira madalitso amene alonjezedwa koma adzawonongedwa kwamuyaya. Ndipo aliyense amene angadzayambe kuchita zinthu zoipazi m’dziko latsopano adzawonongedwa nthawi yomweyo. Imeneyi idzakhala imfa yachiwiri yopanda chiyembekezo choti adzauka.—Yesaya 65:20.
15. Kodi ndani amene ali zitsanzo zabwino kwambiri za opambana pa nkhondo, ndipo buku la Chivumbulutso linafika kumapeto osangalatsa kwambiri ndi masomphenya otani?
15 Mwanawankhosa, Yesu Khristu, pamodzi ndi mkwatibwi wake wa a 144,000, omwe ndi Yerusalemu Watsopano, ndiwo zitsanzo zabwino kwambiri za opambana pa nkhondo. Choncho, m’pake kuti masomphenya a m’buku la Chivumbulutso anafika kumapeto osangalatsa kwambiri, Yohane ataona Yerusalemu Watsopano wokongola kwambiri. Tsopano Yohane atifotokozera masomphenya omaliza amenewa.
[Zithunzi patsamba 302]
M’dziko lapansi latsopano, anthu onse adzakhala pa ubwenzi wabwino ndiponso azidzagwira ntchito yosangalatsa