-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—2003 | December 15
-
-
Tinganene motsimikiza kuti ngakhale zimenezo zisanachitike, pamene angelo oipa anali adakali ndi mwayi wokhala kumwamba, iwo sanalinso mbali ya banja la Mulungu ndipo anali ataletsedwa kuchita zinthu zina. Mwachitsanzo, Yuda 6 amasonyeza kuti m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino anali ‘atawasunga [kale] m’ndende zosatha pansi pa mdima [wauzimu], kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.’ Mofananamo, 2 Petro 2:4 amati: “Mulungu sanalekerera angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende [mkhalidwe wa m’malo otsika kotheratu] nawaika ku maenje a mdima [wauzimu], asungike akaweruzidwe.”b
-
-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—2003 | December 15
-
-
b Mtumwi Petro anafananitsa khalidwe losayanjidwa mwauzimu limeneli ndi kukhala mu ‘ndende.’ Komabe, sanatanthauze “phompho” limene ziwanda zidzaponyedwamo kwa zaka chikwi m’tsogolomu.—1 Petro 3:19, 20; Luka 8:30, 31; Chivumbulutso 20:1-3.
-